Back to Languages

Chichewa - Chapter 10 - Yunus

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Yunus 10:1

“Alif-Lam-Ra. Izi ndi Ayah za m’buku lanzeru. (Lokamba zanzeru zokhazokha)

Verse 2 — Surah Yunus 10:2

“Kodi nchodabwitsa kwa anthu kuti tamuvumbulutsira (chivumbulutso) munthu wochokera mwa iwo (yemwe ndi Muhammad {s.a.w}) kuti: “Chenjeza anthu ndipo awuze nkhani yabwino amene akhulupirira kuti iwo adzapeza ulemelero waukulu kwa Mbuye wawo?” Osakhulupirira adati: “Ndithudi uyu ndi wa matsenga (mfiti) wowonekera.’’

Verse 3 — Surah Yunus 10:3

“Ndithu Mbuye wanu ndi Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zonse za m’menemo) m’masiku asanu ndi limodzi; (masiku omwe palibe yemwe akuwadziwa kutalika kwake koma Iye Yekha), kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, kukhazikika kwake akukudziwa ndi Iye Yekha basi). Amayendetsa zinthu (za zolengedwa Zake). Palibe muomboli (woombola wina) koma pambuyo pa chilolezo Chake (Allah). Uyo ndiye Allah Mbuye wanu; choncho mupembedzeni Iye. Kodi simungakumbukire (kuti mafanowo si milungu)

Verse 4 — Surah Yunus 10:4

“Kobwerera kwanu nonsenu ndi kwa Iye. Ili ndilonjezo la Allah loona. Ndithu Iye ndi Yemwe adayamba kulenga (zolengedwa), ndiponso ndi Yemwe adzazibwereza (pambuyo pa imfa) kuti adzawalipire amene adakhulupirira ndi kumachita zabwino mwa chilungamo. Ndipo amene sadakhulupirire, akapeza zakumwa za madzi owira ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo

Verse 5 — Surah Yunus 10:5

“Iye (Allah) ndiYemwe adapanga dzuwa kukhala lowala, ndi mwezi kukhala wounika; ndipo adaukonzera mbuto (masitesheni) kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero chake. Allah sadalenge zimenezo koma mwachoonadi (ndi cholinga cha nzeru). Akufotokoza Ayah (Zake) kwa anthu ozindikira

Verse 6 — Surah Yunus 10:6

“Ndithu m’kusinthanasinthana kwa usiku ndi usana, ndi zomwe Allah walenga kumwamba ndi pansi, ndithudi, ndi zisonyezo kwa anthu oopa (Allah)

Verse 7 — Surah Yunus 10:7

“Ndithu amene sayembekeza kukumana Nafe, nakondetsetsa umoyo wapadziko lapansi ndi kukhazikika (mtima) ndi za mmenemo, ndi omwe akunyozera Ayah Zathu

Verse 8 — Surah Yunus 10:8

“Iwowo (onse) malo awo ndi ku Moto chifukwa cha zomwe adazipeza (m’njira zosayenera)

Verse 9 — Surah Yunus 10:9

“Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, Mbuye wawo awaongola chifukwa cha chikhulupiliro chawo. Pansi (ndi patsogolo) pawo mitsinje ikuyenda m’Minda yamtendere

Verse 10 — Surah Yunus 10:10

“Mapemphero awo m’menemo adzakhala kunena: “Subuhanaka Lahuma’ Ulemelero ndi Wanu, E Inu Allah!” Ndipo kulonjerana kwawo m’menemo kudzakhala kunena: “Salaam (alayikum’) Mtendere (ukhale pa inu).” Ndipo duwa yawo yomaliza (idzakhala kuyamika ponena kuti) “Alham’du Lillah Rabil a’lamin’. Kuyamikidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zolengedwa.”

Verse 11 — Surah Yunus 10:11

“Ndipo Allah akadakhala kuti akuwapatsa anthu zoipa mwachangu (zomwe iwo akuzifulumizitsa) monga mmene amawapatsira mwachangu zabwino (akamupemphamo, ndiye kuti) ikadalamulidwa nthawi yawo (yowaonongera koma Allah amawamvera chisoni), koma amene saopa kukumana Nafe tikuwasiya akuyumbayumba m’zoipa zawo

Verse 12 — Surah Yunus 10:12

“Ndipo vuto likamkhuza munthu amatipempha (m’kakhalidwe kake konse), chogona, chokhala kapena choimilira. Koma tikamchotsera vuto lomwe lidampeza, amayenda ngati sanatipempheko pa vuto Iomwe Iidamkhudza. Momwemo ndimo zakometseredwa kwa opyola malire zomwe ankachita

Verse 13 — Surah Yunus 10:13

“Ndipo ndithu tidaiononga mibadwo yambiri patsogolo panu pamene idachita zoipa. Komatu atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera, koma sadali oti nkukhulupirira. Umo ndi momwenso tidzawalipire anthu ochita zoipa

Verse 14 — Surah Yunus 10:14

“Kenako takupangani inu (Asilamu) kukhala olowa m’malo mwawo pa dziko pambuyo pawo kuti tione mmene mungachitire (zabwino kapena zoipa)

Verse 15 — Surah Yunus 10:15

“Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, akunena amene sayembekezera kukumana ndi Ife: “Bwera ndi Qur’an (yogwirizana ndi zofuna zathu) osati iyi, kapena uyisinthe (pang’ono).” Nena: “Nkosatheka kwa ine kuisintha mwachifuniro changa. Sinditsata koma zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine. Ndithu ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.”

Verse 16 — Surah Yunus 10:16

“Nena: “Allah akadafuna, sindikadakuwerengerani Qur’aniyi ndiponso sakadakudziwitsani Qur’aniyo, ndidakhala pakati panu moyo wanga (zaka zambiri) isadavumbulutsidwe, (simudandimve ndikunena chilichonse cha utumiki). Kodi mulibe nzeru?”

Verse 17 — Surah Yunus 10:17

“Ndani woipitsitsa woposa yemwe akumpekera Allah bodza, ndi yemwe akutsutsa Ayah Zake? Ndithudi, sangapambane wochita zoipa

Verse 18 — Surah Yunus 10:18

“Ndipo iwo akupembedza milungu yina kusiya Allah, yomwe singathe kuwapatsa masautso (ngati atasiya kuipembedza) ndiponso siyingathe kuwapatsa chithandizo (ngati atalimbika kuipembedza) ndipo akunena: “Iwo (mafanowo) ndi aomboli athu kwa Allah.” Nena: “Kodi mukumuuza Allah zomwe sakudziwa kumwamba ndi pansi? Wapatukana Allah Ndipo watukuka kuzimene akum’phatikiza nazo.”

Verse 19 — Surah Yunus 10:19

“Ndipo ndithudi anthu kalero (m’nthawi ya Adam) adali mpingo umodzi (opembedza Allah), koma adasiyana (pambuyo pake). Ndipo pakadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako, lomwe lidatsogola (lakuti adzawalanga tsiku la Qiyâma), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo m’zomwe adali kusiyana

Verse 20 — Surah Yunus 10:20

“Ndipo akunena: “Kukadakhala kuti chinatsitsidwa kwa iye chizindikiro (chotsimikizira uneneri wake) chochokera kwa Mbuye wake (chomwe takhala tikuchipempha nthawi ndi nthawi).” Nena (kwa iwo): “Ndithu kudziwa zobisika nkwa Allah Yekha. Choncho dikirani (chiweruzo cha Allah) inenso pamodzi nanu ndine mmodzi wa odikira.”

Verse 21 — Surah Yunus 10:21

“Ndipo tikawalawitsa anthu mtendere pambuyo pa masautso omwe adawakhudza, pompo iwo amayamba kuzichitira ndale Ayah Zathu. Nena: “Allah ngwachangu kwambiri poononga ndale (zawo).” Ndithu amithenga athu (angelo) akulemba ziwembu zanu (zonse) zimene mukuchita

Verse 22 — Surah Yunus 10:22

“Iye ndi Yemwe amakuyendetsani pa ntunda ndi pa nyanja; kufikira pomwe mumakhala m’zombo; ndipo zimayenda nawo (zombozo) ndi mphepo yabwino, naisangalalira. (Mwadzidzidzi) namondwe nkuzidzera (zombozo) ndipo mafunde nkuwadzera mbali zonse natsimikiza kuti azingidwa (ndi chionongeko); amampempha Allah modzipereka kwa Iye mukupempha kwawo (uku akunena): “Ngati mutipulumutsa pa ichi, tidzakhala m’gulu la oyamika (nthawi zonse)!”

Verse 23 — Surah Yunus 10:23

“Koma akawapulumutsa, pompo akuyamba kudzitukumula ndi kuononga pa dziko popanda chowayenereza (kutero). E inu anthu! Ndithu kuononga kwanu kukubweretserani masautso inu nokha. Ndipo chisangalalo (chake) cha moyo wa dziko lapansi (nchochepa). Kenako kobwerera kwanu ndi kwa Ife, ndipo tidzakuuzani zomwe munkachita

Verse 24 — Surah Yunus 10:24

“Ndithu fanizo la moyo wadziko lapansi lili ngati madzi amvula, tawatsitsa kuchokera ku mitambo nkusakanikirana ndi zomera za m’nthaka zomwe anthu ndi nyama amadya; kufikira nthaka ikakwaniritsa kukongola kwake ndi kudzikometsa ndipo eni (nthaka) nkuganiza kuti iwo ali ndi mphamvu pa nthakayo (pokolola zomwe zili pamenepo). Mwadzidzidzi nkuzidzera lamulo Lathu (za pa nthakazo), usiku kapena masana, nkuzichita kukhala ngati zokololedwa ngati kuti sizidalipo dzulo (lake). Motere tikufotokoza Ayah kwa anthu olingalira

Verse 25 — Surah Yunus 10:25

“Ndipo Allah akuitanira (anthu Ake) ku Nyumba yamtendere. Ndipo amamuongolera kunjira yolungama amene wamfuna (ngati ali wotheka kuongoka)

Verse 26 — Surah Yunus 10:26

“Ndipo omwe achita zabwino, adzapata (malipiro) abwino ndi zoonjezera. Ndipo fumbi silikavindikira nkhope zawo. Ndiponso kunyozeka sikukawapeza. Iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere; mmenemo akakhala nthawi yaitali

Verse 27 — Surah Yunus 10:27

“Ndipo amene akolola zoipa (kuchokera m’zochita zawo zoipa) mphoto ya choipa ndiyofanana ndi icho; ndipo kunyozeka kudzawapeza; sadzakhala ndi aliyense wotha kuwateteza ku chilango cha Allah. Nkhope zawo zidzakhala ngati zaphimbidwa ndi zidutswa za usiku wa m’dima, (zidzakhala zakuda kwambiri); awo ndiwo anthu a ku Moto. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali

Verse 28 — Surah Yunus 10:28

“Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse. Kenako tidzawauza amene ankaphatikiza (Allah ndi mafano kuti): “Imani pompo inu pamodzi ndi aphatikizi anuwo.” Ndipo tidzawasiyanitsa pakati pawo; koma aphatikizi awowo adzati: “Simudali kutipembedza ife (koma mudali kupembedza zilakolako zanu).”

Verse 29 — Surah Yunus 10:29

““Allah akukwanira kukhala mboni pakati pathu ndi pakati panu. Ndithu ife sitidali kuzindikira za mapemphero anu. (Sitinkazindikira kuti inu mukutipembedza).”

Verse 30 — Surah Yunus 10:30

“Kumeneko munthu aliyense adzadziwa zimene adatsogoza; ndipo adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona ndipo zidzawasowa zimene adali kupeka

Verse 31 — Surah Yunus 10:31

“Nena: “Kodi ndani akukupatsani (zopatsa) kuchokera kumwamba (povumbwitsa mvula), ndi pansi (pomeretsa mmera)? Nanga ndani amakupatsani kumva ndi kupenya? Nanga ndani amene akutulutsa chamoyo kuchokera m’chakufa, ndi kutulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo? Nanga ndani akukonza zinthu zonse?” Anena: “Ndi Allah.” Choncho, nena: “Kodi bwanji simukumuopa?”

Verse 32 — Surah Yunus 10:32

“Uyo ndi Allah, Mbuye wanu Woona; nanga pali chiyani pambuyo poleka choonadi, sikusokera basi? Kodi nanga mukutembenuzidwa chotani (kusiya choonadi)

Verse 33 — Surah Yunus 10:33

“Momwemo liwu la Mbuye wako latsimikizika kwa amene adatuluka m’chilamulo cha Allah kuti iwo sadzakhulupirira

Verse 34 — Surah Yunus 10:34

“Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) amene angayambitse kulenga zolengedwa; kenako (zitafa) ndikuzibweza?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuyambitsa zolengedwa kenaka ndi kuzibweza (pambuyo poonongeka). Nanga mukunamizidwa chotani (kusiya chikhulupiliro)?”

Verse 35 — Surah Yunus 10:35

“Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) woongolera kuchoonadi?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuongolera ku choonadi. Kodi amene akutsogolera ku choonadi sindiye woyenera kwambiri kutsatidwa kapena (woyenera kutsatidwa ndi) yemwe sakutha kudziongola pokhapokha atawongoledwa ndi wina wake? Nanga mwatani kodi, kodi mukuweruza bwanji?”

Verse 36 — Surah Yunus 10:36

“Ndipo ambiri a iwo satsatira (china) koma zoganizira basi, (osati chomwe afufuza ndikuchizindikira ndi nzeru zawo). Ndithu choganizira sichithandiza ngakhale pang’ono ku choonadi. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene akuchita

Verse 37 — Surah Yunus 10:37

“Ndipo sikotheka Qur’an iyi kukhala yopekedwa, yosachokera kwa Allah (monga momwe munenera). Koma (yachokera kwa Allah) kutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake, ndi kulongosola za buku (lakale). Palibe chikaiko m’menemo (kuti) yachokera kwa Mbuye wa zolengedwa

Verse 38 — Surah Yunus 10:38

“Kapena akunena kuti waipeka? Nena: “Tabwerani ndi sura (imodzi) yofanana ndi iyo, ndipo itanani amene mungathe (kuwaitana kuti akuthandizeni) kupatula Allah, ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’aniyi waipeka Muhammad {s.a.w}).”

Verse 39 — Surah Yunus 10:39

“Koma atsutsa zomwe sakuzizindikira (m’mene zilili) ngakhale tanthauzo lake (la kuona kwake kapena kunama kwake) lisanawafike. Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo. Choncho, taona momwe mathero a anthu ochimwa adalili

Verse 40 — Surah Yunus 10:40

“Ndipo mwa iwo pali ena omwe akuikhulupirira (Qur’an), ndipo ena mwa iwo sakuikhulupirira. Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino oononga

Verse 41 — Surah Yunus 10:41

“Ndipo ngati apitiriza kukutsutsa, nena: “Ine ndili ndi ntchito yanga, inunso muli ndi ntchito yanu. Inu mwatalikirana nazo zimene ndikuchita, inenso ndatalikirana nazo zimene mukuchita!”

Verse 42 — Surah Yunus 10:42

“Ndipo mwa iwo alipo ena amene akumvetsera kwa iwe, (koma osati ndi cholinga choti adziwe). Kodi iwe ungathe kuwamveretsa agonthi, chikhalirecho nzeru alibe

Verse 43 — Surah Yunus 10:43

“Ndipo alipo ena mwa iwo amene akukutong’olera maso (kukuyang’ana monyoza). Kodi iwe ungathe kuwatsogolera akhungu, chikhalirecho sali openya

Verse 44 — Surah Yunus 10:44

“Ndithu Allah sachitira anthu choipa chilichonse. Koma anthu akudzichitira okha zoipa. (Adapatsidwa nzeru, koma sazigwiritsa ntchito)

Verse 45 — Surah Yunus 10:45

“Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe adzawasonkhanitsa (onse) ngati kuti sadakhale (pa dziko lapansi) koma ola limodzi la usana (atathedwa nzeru). Adzazindikirana pakati pawo; (koma aliyense sadzalabadira mnzake). Ndithu aonongeka amene adatsutsa za kukumana ndi Allah ndipo sadali oongoka

Verse 46 — Surah Yunus 10:46

“Ndipo ngati tingakusonyeze (pompano pa dziko lapansi) zina mwa zomwe tikuwalonjeza ndikuwachenjeza nazo, kapena kukubweretsera imfa (usadazione zimenezo), kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kenako Allah ndi mboni pa zomwe akuchita

Verse 47 — Surah Yunus 10:47

“Ndipo fuko lililonse lili ndi Mtumiki ndipo akazabwera Mtumiki wawo (tsiku la chiweruziro), kudzaweruzidwa pakati pawo mwa chilungamo ndipo sadzaponderezedwa

Verse 48 — Surah Yunus 10:48

“Ndipo akunena (osakhulupirira): “Kodi lonjezo ili lidzachitika liti ngati mukunena zoona?”

Verse 49 — Surah Yunus 10:49

“Nena: “Ndilibe mphamvu mwandekha pa (kudzichotsera) vuto ngakhale (kudzibweretsera) thandizo. (Nanga za zimenezo ndingadziweponji)? Koma chimene Allah wafuna (ndi chomwe chimachitika). M’badwo uli wonse uli ndi nthawi yake (yofera). Nthawi yawo (yofera) ikadza sangathe kuichedwetsa ola limodzi ngakhale kuifulumizitsa.”

Verse 50 — Surah Yunus 10:50

“Nena: “Kodi mukuona bwanji, ngati chilango chakecho chitakudzerani usiku kapena usana (mungathe kuthawa)? Nanga bwanji ochimwa akuchifulumizitsa (kuti chidze mwachangu)?”

Verse 51 — Surah Yunus 10:51

(““Kodi chikadza ndipamene mudzachikhulupirire?” Panthawiyo mudzauzidwa): “Kodi tsopano (ndi pamene mukukhulupirira), chikhalirecho mudali kuchifulumizitsa (kale)?”

Verse 52 — Surah Yunus 10:52

“Kenako kudzanenedwa kwa amene adachita zoipa: “Lawani chilango chamuyaya! Kodi mungalipidwe zina osakhala zomwe mudazipata (kuchokera m’zochita zanu zoipa)?”

Verse 53 — Surah Yunus 10:53

“Eti akukufunsa: “Kodi nzoona izo (zimene ukunena)?” Nena: “Inde! Ndikulumbira kwa Mbuye wanga, zimenezo ndi zoona. Ndipo inu simuli olepheretsa (Allah).”

Verse 54 — Surah Yunus 10:54

“Ndipo kukadakhala kuti munthu aliyense amene adachita zoipa, nkukhala nazo zonse zam’dziko akadapereka zonse kuti adziombole nazo (pamene adzaona kuopsa kwa chilango cha tsikulo). Ndipo akadzachiona chilango, adzayesetsa kubisa madandaulo (awo; koma adzaonekera poyera). Ndipo kudzaweruzidwa mwachilungamo pakati pawo, ndipo iwo sadzaponderezedwa

Verse 55 — Surah Yunus 10:55

“Tamverani! Ndithu zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Tamverani! Ndithu lonjezo la Allah ndi loona, koma ambiri a iwo sadziwa

Verse 56 — Surah Yunus 10:56

“Iye (Allah ndi amene) amapereka moyo ndi imfa. Ndipo kwa Iye (nonsenu) mudzabwezedwa

Verse 57 — Surah Yunus 10:57

“E inu anthu! Ndithu ulaliki wakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu ndi machiritso a matenda omwe ali m’mitima mwanu, ndiponso nchiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira

Verse 58 — Surah Yunus 10:58

“Nena: “Chifukwa cha ubwino wa Allah ndi chifundo Chake (mwapeza zimenezi), choncho asangalalire zimenezi.” Izi ndizabwino kwambiri kuposa zimene akusonkhanitsa (m’zinthu za dziko lapansi)

Verse 59 — Surah Yunus 10:59

“Nena: “Kodi mukuona bwanji, rizq lomwe Allah wakutsitsirani? Kenako inu lina mwa ilo mwalichita kukhala loletsedwa (la haramu), ndipo lina mwa ilo kukhala lololedwa (la halali).” Nena: “Kodi Allah adakulolezani (kuchita zimenezo), kapena mukumpekera Allah bodza?”

Verse 60 — Surah Yunus 10:60

“Kodi ali ndi ganizo lotani amene akumpekera Allah bodza pa za tsiku la Qiyâma? Ndithu Allah Ndi mwini ubwino wochuluka kwa anthu. Koma ambiri a iwo sathokoza

Verse 61 — Surah Yunus 10:61

“Ndipo siutanganidwa ndi ntchito iliyonse, ndiponso simuwerenga m’menemo (chinthu chilichonse) cha m’Qur’an ndipo simuchita ntchito ina iliyonse (inu anthu) koma Ife timakhala mboni pa inu pamene mukutanganidwa nayo. Ndipo sichibisika kwa Mbuye wako chinthu chilichonse ngakhale cholemera ngati nyelere, m’nthaka ngakhale kumwamba. Ndipo ngakhale chocheperapo zedi kuposa pamenepo kapena chokulirapo koma chili m’kuku (la Allah) lofotokoza chilichonse

Verse 62 — Surah Yunus 10:62

“Tamverani! Ndithu okondedwa a Allah sadzakhala ndi mantha (pa tsiku la Qiyâma), ndipo sadzadandaula

Verse 63 — Surah Yunus 10:63

“(Amenewo ndi) amene adakhulupirira ndi kumuopa (Allah)

Verse 64 — Surah Yunus 10:64

“Iwo ali ndi zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Palibe kusintha pa mawu a Allah. Uku ndiko kupambana kwakukulu

Verse 65 — Surah Yunus 10:65

“Ndipo (iwe, Mtumiki) zisakudandaulitse zonena zawo (zomwe akukunenera monyoza). Ndithu ulemelero ndi mphamvu zonse nza Allah. Iye Ngwakumva, Ngodziwa

Verse 66 — Surah Yunus 10:66

“Tamverani! Ndithu (zonse) za kumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndipo amene akupembedza zina kusiya Allah, satsatira aphatikizi (a Allah). Akungotsatira zoganizira, ndipo iwo sanena china koma bodza basi

Verse 67 — Surah Yunus 10:67

“Iye (Allah) ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti muzipumamo, ndi (adakupangirani) usana kukhala wowala (kuti mupenye). Ndithu m’zimene muli zisonyezo (zosonyeza chifundo cha Allah pa zolengedwa Zake) kwa anthu akumva

Verse 68 — Surah Yunus 10:68

“Akunena: “Allah wadzipangira mwana.” Wapatukana ndi zimenezo! Iye Ngokwanira, (salakalaka mwana ngakhale mthangati aliyense). NdiZake (zonse) za kumwamba ndi za pansi. Inu mulibe umboni pa zimenezi. Kodi mukumnenera Allah zomwe simukuzidziwa

Verse 69 — Surah Yunus 10:69

“Nena: “Ndithu amene akumpekera Allah bodza, sadzapambana.”

Verse 70 — Surah Yunus 10:70

“Ndichisangalalo chochepa basi m’dziko lapansi. Kenako kwa Ife ndiwo mabwelero awo. Kenako tidzawalawitsa chilango chaukali chifukwa cha kusakhulupirira kwawo

Verse 71 — Surah Yunus 10:71

“Ndipo awerengere (molakatula) nkhani za Nuh pamene adanena kwa anthu ake: “E inu anthu anga! Ngati kukhala kwanga pamodzi ndi inu ndi kukumbutsa kwanga Ayah za Allah kukukukulirani, ine ndatsamira kwa Allah (sindisiya ntchito yangayi). Choncho sonkhanitsani zinthu zanu pamodzi ndi milungu yanuyo; (sonkhanani kuti mundichitire choipa, ine sindilabadira chilichonse). Ndipo chinthu chanucho chisabisike kwa inu, (chitani moonekera. Ine sinditekeseka ndi chilichonse). Kenako chitani pa ine (chimene mufuna kuchita) ndipo musandipatse danga

Verse 72 — Surah Yunus 10:72

“Ngati mutembenuka ndikunyoza, (ndikufuna kwanu). Ine sindinakupempheni malipiro. Malipiro anga kulibe kulikonse (kumene ndingalandire) koma kwa Allah, ndipo ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi mwa Asilamu (ogonjera Iye).”

Verse 73 — Surah Yunus 10:73

“Koma adamutsutsa. Choncho tidampulumutsa pamodzi ndi amene adali naye m’chombo. Ndipo tidawasankha iwo kukhala otsala (pa dziko anzawo ataonongeka). Ndipo tidawamiza amene adatsutsa Ayah Zathu. Choncho taona momwe mapeto a ochenjezedwa adalili

Verse 74 — Surah Yunus 10:74

“Pambuyo pake tidawatumiza atumiki (ambiri) kwa anthu awo. Adawadzera ndi zisonyezo zoonekera poyera koma sadali okhulupirira zimene ena adazitsutsa kale, (adatsatira njira zomwezo za anzawo). Umo ndi momwe tikudindira zidindo m’mitima ya anthu opyola malire

Verse 75 — Surah Yunus 10:75

“Kenako pambuyo pawo tidamtuma Mûsa ndi Haarun pamodzi ndi zizindikiro zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adadzikweza. Tero adali anthu ochita zoipa

Verse 76 — Surah Yunus 10:76

“Ndipo pamene choonadi chidawadzera kuchokera kwa Ife, adanena: “Ndithu awa ndimatsenga oonekera.”

Verse 77 — Surah Yunus 10:77

“Mûsa adati: “Mukutero pa choonadi pamene chakudzerani? Kodi matsenga ali chonchi? Ndipo amatsenga sangapambane (ngakhale zitatani).”

Verse 78 — Surah Yunus 10:78

“(Iwo) adati: “Kodi watidzera kuti utichotse ku zimene tidawapeza nazo makolo athu kuti ukulu ukhale wa inu awiri m’dzikoli? Koma ife sitingakukhulupirireni awirinu.”

Verse 79 — Surah Yunus 10:79

“Ndipo Farawo adati: “Ndibweretsereni wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri (zamatsenga).”

Verse 80 — Surah Yunus 10:80

“Ndipo pamene amatsenga adadza, Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zomwe mufuna kuponya (kuti musonyeze ukatswiri wanu kwa anthu).”

Verse 81 — Surah Yunus 10:81

“Pamene adaponya, Mûsa adati: “Zomwe mwabweretsa ndi matsenga. Allah awaononga pompano. Ndithu Allah sakonza ntchito za oononga.”

Verse 82 — Surah Yunus 10:82

““Ndipo Allah achilimbikitsa choonadi ndi mau Ake, ngakhale oipa anyansidwe nazo.”

Verse 83 — Surah Yunus 10:83

“Sadamkhulupirire Mûsa kupatula achinyamata a mwa anthu ake, chifukwa choopa Farawo ndi nduna zake kuti angawazunze. Ndithu Farawo adali wodzikuza pa dziko, ndithudi, adali m’modzi mwa opyola malire

Verse 84 — Surah Yunus 10:84

“Ndipo Mûsa adati: “E inu anthu anga! Ngati inu mwakhulupirira Allah, choncho tsamirani kwa Iye ngati mulidi Asilamu (owona)

Verse 85 — Surah Yunus 10:85

“Choncho (iwo) adati: “Tayadzamira kwa Allah. E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayetsero kwa anthu oipa.”

Verse 86 — Surah Yunus 10:86

““Ndipo tipulumutseni mwa chifundo Chanu ku anthu osakhulupirira.”

Verse 87 — Surah Yunus 10:87

“Ndipo tidavumbulutsa kwa Mûsa ndi m’bale wake mawu Athu (oti): “Apangireni nyumba anthu anu mu Eguputo ndipo nyumba zanu zichiteni kukhala misikiti (pakuti simungathe kukhala ndi misikiti yoonekera), ndipo pempherani Swala. Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira (kuti Allah awapatsa zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro).”

Verse 88 — Surah Yunus 10:88

“Ndipo Mûsa adati: “Mbuye wathu! Inu mwampatsa Farawo ndi nduna zake zodzikometsera, ndi chuma chambirimbiri pa moyo wa pa dziko. Mbuye wathu, (iwo akugwiritsa ntchito zimenezi) kuti asokeretse anthu pa njira Yanu. Mbuye wathu, wonongani chuma chawo ndipo iumitseni mitima yawo popeza sakhulupirira kufikira ataona chilango chowawa.”

Verse 89 — Surah Yunus 10:89

“(Allah) adati: “Pempho lanu lavomerezedwa! Choncho lungamani mwaubwino, ndipo musatsate njira za omwe sadziwa.”

Verse 90 — Surah Yunus 10:90

“Ndipo tidawaolotsa pa nyanja ana a Israyeli. Ndipo Farawo ndi asilikali ake ankhondo adawatsata moipitsa ndi mwamtopola, kufikira pamene kumira kudampeza; (iye) adati: “Ndakhulupirira kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Yemwe ana a Israyeli amkhulupirira. Ndipo ine ndine mmodzi mwa Asilamu (omugonjera monga iwo akumgonjera).”

Verse 91 — Surah Yunus 10:91

“(Angelo adamuuza kuti:) “Tsopano (ndipamene ukukhulupirira), pomwe kale udanyoza ndikukhala mmodzi wa oononga!”

Verse 92 — Surah Yunus 10:92

““Choncho lero tikupulumutsa (polisunga) thupi lako, kuti ukhale chisonyezo kwa amene akudza m’mbuyo mwako (kuti adziwe kuti sudali mulungu). Koma ndithu anthu ambiri salabadira zisonyezo Zathu.”

Verse 93 — Surah Yunus 10:93

“Ndipo ndithu (pambuyo pake) tidawakonzera mokhala mwabwino ana a Israyeli, ndikuwapatsa zabwino. Sadasiyane kufikira pamene kuzindikira kudawadzera. Ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsutsana

Verse 94 — Surah Yunus 10:94

“Ngati uli ndi chipeneko pa zimene takuvumbulutsira, afunse amene akuwerenga mabuku akale (Ayuda ndi Akhrisitu amene alowa m’Chisilamu). Ndithu choonadi chakufika kuchokera kwa Mbuye wako. Choncho usakhale mwa amene akukaikira

Verse 95 — Surah Yunus 10:95

“Ndiponso usakhale mwa omwe akutsutsa zizindikiro za Allah, kuopa kuti ungadzakhale m’gulu la otaika

Verse 96 — Surah Yunus 10:96

“Ndithu aja amene liwu la Mbuye wako latsimikizika pa iwo, sakhulupirira

Verse 97 — Surah Yunus 10:97

“Ndipo ngakhale kuti chisonyezo chamtundu uliwonse chiwadzere (sangakhulupirirebe), mpaka aone chilango chopweteka

Verse 98 — Surah Yunus 10:98

“Kodi udalipo mudzi (ndi umodzi womwe pakati pa midzi mwa yomwe tidaiwononga), umene udalapa ndi kukhulupirira (pambuyo poona chilango kotero kuti) chikhulupiliro chake nkuuthandiza pa nthawi imeneyo, osati kupatula anthu a Yunus okha? Pamene adakhulupirira, tidawachotsera chilango choyalutsa m’moyo wa padziko lapansi, ndipo tidawasangalatsa kufikira nthawi yawo (yofera)

Verse 99 — Surah Yunus 10:99

“Ndipo Mbuye wako akadafuna (kuwakakamiza anthu mwamphamvu kuti akhulupirire), onse ali m’dziko lapansi akadakhulupirira (sipakadatsala ndi mmodzi yemwe. Koma Allah safuna kukakamiza anthu mwamphamvu). Nanga kodi iwe uwakakamiza anthu kuti akhale okhulupirira

Verse 100 — Surah Yunus 10:100

“Ndipo palibe munthu angakhulupirire popanda chilolezo cha Allah. Iye amaachitira ukali amene alibe nzeru (amene sagwiritsa ntchito nzeru zawo)

Verse 101 — Surah Yunus 10:101

“Nena: “Yang’anani nchiyani chikupezeka kumwamba ndi pansi!” Ndipo zisonyezo zonsezi ndi machenjezo onsewa sangawakwanire (ndi kuwapindulira kanthu) anthu osakhulupirira

Verse 102 — Surah Yunus 10:102

“Kodi chiliponso chimene akudikira posakhala (kuwadzera) monga masiku (azilango zomwe zidawapeza) amene adapita kale (iwo asadafike)? Nena: “Dikirani nanenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.”

Verse 103 — Surah Yunus 10:103

“Kenako tidzawapulumutsa atumiki Athu ndi amene adakhulupirira. Chotere nkoyenera kwa Ife kuwapulumutsa okhulupirira

Verse 104 — Surah Yunus 10:104

“Nena: “E inu anthu! Ngati inu muli ndi chipeneko pa chipembedzo changa, (dziwani kuti) sindingapembedze zimene mukuzipembedza kusiya Allah; koma ine ndipembedza Allah (Mmodzi yekha) Yemwe amakupatsani imfa (ndi moyo). Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa okhulupirira.”

Verse 105 — Surah Yunus 10:105

““Ndiponso (ndauzidwa kuti): ‘Lungamitsa nkhope yako kuchipembedzo momuyeretsera Allah mapemphero Ake, ndipo usakhale mmodzi mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).’

Verse 106 — Surah Yunus 10:106

“‘Ndipo (kuti), usapembedze chimene sichingakupindulitsire zabwino, kapena kukubweretsera masautso, kusiya Allah. Ngati utero ndiye kuti iwe ndi mmodzi wa oipa.”

Verse 107 — Surah Yunus 10:107

“Ndipo ngati Allah atakukhudza ndi masautso, palibe aliyense owachotsa kupatula Iye. Ngatinso atakufunira zabwino, palibe amene angaubweze ubwino Wake. (Iye) amadza ndi ubwinowo kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Iye Ngokhululuka Ngwachisoni zedi

Verse 108 — Surah Yunus 10:108

“Nena: “E inu anthu! Choonadi chakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho amene waongoka, (zabwino zake) zili pa iye mwini. Ndipo amene wasokera, ndithu zotsatira za kusokera zili pa iye mwini. Ndipo ine sindili muyang’aniri pa inu, (udindo wanga ndi kuchenjeza basi).”

Verse 109 — Surah Yunus 10:109

“Ndipo (andiuza kuti): “Tsatira zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndipo pirira kufikira Allah adzaweruze. Iye Ngoweruza bwino kuposa aweruzi onse.”