Back to Languages

Chichewa - Chapter 101 - Al-Qariah

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Qariah 101:1

“Kugunda kwa phokoso (la Qiyâma)

Verse 2 — Surah Al-Qariah 101:2

“Kodi kugunda kwa phokosolo ndi chiyani

Verse 3 — Surah Al-Qariah 101:3

“Ndichiyani chingakudziwitse za kugunda kwa phokoso (la Qiyâma komwe kudzawakomole anthu)

Verse 4 — Surah Al-Qariah 101:4

“Limenelo ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika

Verse 5 — Surah Al-Qariah 101:5

“Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya womwazidwa (wongouluka uku ndi uku mumlengalenga)

Verse 6 — Surah Al-Qariah 101:6

“Tsono amene muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzalemere (ndikupepuka zoipa)

Verse 7 — Surah Al-Qariah 101:7

“Ndiye kuti iye adzakhala mu umoyo wosangalatsa (patsiku la chiweruziro)

Verse 8 — Surah Al-Qariah 101:8

“Ndipo yemwe muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzapepuka (ndi kulemera zoipa)

Verse 9 — Surah Al-Qariah 101:9

“Ndiye kuti mbuto yake ndi ku Hawiya

Verse 10 — Surah Al-Qariah 101:10

“Kodi ndi chiyani chingakudziwitse za Hawiya

Verse 11 — Surah Al-Qariah 101:11

“Umenewo ndi Moto woyaka mwa ukali