Back to Languages

Chichewa - Chapter 107 - Al-Maun

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Maun 107:1

“Kodi wamuona yemwe akutsutsa za mphoto (ndi chiwerengero cha tsiku lachimaliziro)

Verse 2 — Surah Al-Maun 107:2

“Iye ndi yemwe akukankha wamasiye (mwankhanza)

Verse 3 — Surah Al-Maun 107:3

“Ndipo salimbikitsa (ena pamodzi ndi iye mwini) kudyetsa osauka

Verse 4 — Surah Al-Maun 107:4

“Choncho kuonongeka kuli pa ena mwa opemphera swala (amene ali ndi mbiri izi)

Verse 5 — Surah Al-Maun 107:5

“Omwe amachitira mphwayi mapemphero awo

Verse 6 — Surah Al-Maun 107:6

“Amenenso (akamachita mapemphero awo) amadzionetsera (kwa anthu mwachipha maso kuti apeze ulemelero ndi kutamandidwa mmitima mwa anthu)

Verse 7 — Surah Al-Maun 107:7

“Ndipo amamana ziwiya (zawo posabwereka anzawo zinthu zofunika pa moyo wa aliyense monga nkhwangwa, mpeni, mtondo ndi zina zotere)