Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 108 - Al-Kawthar
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Kawthar 108:1
“Ndithu takupatsa zabwino zambiri (zina mwa izo ndi mtsinje wotchedwa Kauthar)
Verse 2 — Surah Al-Kawthar 108:2
“(Pakuti ndakupatsa zimenezo), pitiriza kupembedza Mbuye wako (moyera mtima) ndipo ipha nsembe yako (chifukwa chakuthokoza Allah pa zimene wakupatsa, monga ulemelero ndikukusankhira zabwino zambiri)
Verse 3 — Surah Al-Kawthar 108:3
“Ndithu mdani wako ndiye ali wopanda mwawi