Back to Languages

Chichewa - Chapter 109 - Al-Kafirun

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Kafirun 109:1

“Nena (iwe Mtumiki) (s.a.w): E inu anthu osakhulupirira

Verse 2 — Surah Al-Kafirun 109:2

“Sindipembedza chimene inu mukuchipembedza (kusiya Allah)

Verse 3 — Surah Al-Kafirun 109:3

“Inunso simumpembedza amene ine ndikumpembedza (yemwe ndi Allah)

Verse 4 — Surah Al-Kafirun 109:4

“Ndiponso ine sindidzapembedza chimene inu mwakhala mukuchipembedza (chifukwa inu ndinu ophatikiza Allah ndi zinthu zina)

Verse 5 — Surah Al-Kafirun 109:5

“Ndipo inu simudzampembedza amene ine ndikumpembedza (yemwe ndi Allah)

Verse 6 — Surah Al-Kafirun 109:6

“Inu muli ndi chipembedzo chanu (chimene mukuchikhulupirira), inenso ndili ndi chipembedzo changa (chimene Allah wandisankhira)