Back to Languages

Chichewa - Chapter 11 - Hud

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Hud 11:1

“Alif-Lam-Ra. Ili ndi buku lomwe ndime zake zakonzedwa bwino ndipo zafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera kwa Allah Mwini nzeru zakuya Wodziwa chilichonse

Verse 2 — Surah Hud 11:2

“(Wachita zimenezi) kuti musampembedze wina wake koma Allah yekha. Ndithudi ine kwa inu ndimchenjezi wochokera kwa Iye ndiponso wokuuzani nkhani zabwino

Verse 3 — Surah Hud 11:3

“Ndikuti mupemphe chikhululuko kwa Mbuye wanu ndipo mulape kwa Iye. Akupatsani chisangalalo chabwino mpakana m’nthawi yoikidwa. Ndipo adzampatsa (tsiku lachimaliziro) aliyense wochita zabwino ubwino wake. Koma, ngati mupotoka ine kwanga nkukuoperani za chilango cha tsiku lalikulu

Verse 4 — Surah Hud 11:4

“Kobwerera kwanu nkwa Allah basi. Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse

Verse 5 — Surah Hud 11:5

“Tamverani! Iwo akubisa zimene zili m’mitima yawo kuti amubise Iye (Allah). Mverani! Ndithudi pamene akuzifunda nsalu zawo Iye akudziwa zimene akuzibisa ndi zimene akuzionetsa. Ndithudi Iye ndiwodziwa za mzifuwa

Verse 6 — Surah Hud 11:6

“۞ Ndipo palibe nyama iliyonse panthaka koma rizq lake lili kwa Allah; ndipo (Iye) akudziwa mbuto yake yamuyaya ndi mbuto yake yakungodutsapo (yomwe ndi pano padziko lapansi). Zonse zili m’buku lofotokoza chilichonse

Verse 7 — Surah Hud 11:7

“Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo Arsh Yake (Mpando Wake wachifumu) idali pa madzi. (Adakulengani) kuti akuyeseni mayeso, ndani mwa inu ali wochita zabwino. Koma ukanena (kwa iwo kuti): “Inu mudzaukitsidwa pambuyo pa imfa,” amene sadakhulupirire akuti: “Izi sikanthu koma ndi matsenga oonekera.”

Verse 8 — Surah Hud 11:8

“Ndipo ngati titawachedwetsera chilango mpaka m’nthawi yodziwika (ndi kukhazikitsidwa ndi Ife), akunena (mwamwano): “Nchiyani chikumanga chilangocho (kuti chidze)? “Tamverani! Tsiku lomwe chidzawadzera, sichidzachotsedwa kwa iwo ndipo zomwe adali kuzichita mwachibwana zidzawazinga

Verse 9 — Surah Hud 11:9

“Ndipo munthu tikamulawitsa mtendere wochokera kwa Ife, kenako nkuuchotsa kwa iye, ndithu amakhala wotaya mtima kwambiri ndikukhala wosathokoza

Verse 10 — Surah Hud 11:10

“Koma ngati titamulawitsa mtendere pambuyo pa masautso omwe adamkhudza, amati: “Masautso andichoka,”(ndipo sakhala wotanganidwa ndi ntchito zabwino zosonyeza kuyamika Allah), ndithudi iye amakhala wosangalala, wodzitukumula

Verse 11 — Surah Hud 11:11

“Koma amene apirira ndi kumachita ntchito zabwino, iwowo ndiwo adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa Allah)

Verse 12 — Surah Hud 11:12

“Mwina usiya zina mwa zomwe zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndikubanika nazo mchifuwa mwako chifukwa chakuti akunena: “Bwanji sizidatsitsidwe kwa iye nkhokwe za chuma kapena bwanji mngelo osadza pamodzi ndi iye?” Koma ndithu iwe ndiwe mchenjezi basi ndipo Allah ndiye muyang’aniri wa chinthu chilichonse

Verse 13 — Surah Hud 11:13

“Kapena akunena kuti: “Waipeka Qur’an?” Nena: “Tabweretsani sura khumi zopekedwa zomwe zingafanane ndi iyi (Qur’an) ndipo aitaneni amene mungathe (kuwaitana) kupatula Allah. (Adze akuthandizeni kulemba bukulo) ngati mukunena zoona!”

Verse 14 — Surah Hud 11:14

““Ngati sakuyankhani, choncho, dziwani kuti yavumbulutsidwa (Qur’aniyo) m’kudziwa kwa Allah, ndikuti kulibe mulungu wina koma Iye. Nanga kodi inu simugonjera (Iye)?”

Verse 15 — Surah Hud 11:15

“Amene akufuna moyo wa dziko lapansi ndi zokometsera zake, tiwapatsa pompo pa dziko lapansi (malipiro a) zochita zawo mokwanira, ndipo iwo m’menemo sachepetseredwa chilichonse

Verse 16 — Surah Hud 11:16

“Iwo ndi omwe sadzakhala ndi kanthu tsiku lachimaliziro koma Moto basi. Ndipo zimene adachita m’menemo zidzaonongeka, ndiponso nzopanda phindu zimene ankachita

Verse 17 — Surah Hud 11:17

“Nanga kodi munthu yemwe ali ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wake (kotero kuti m’moyo mwake akuyenda molungama; yemwe ndi mneneri Muhammad {s.a.w}), ndipo Mboni ili naye pamodzi ikumtsata yochokera kwa Iye (Mbuye wake yomwe ndi Qur’an kapena Gaburiel), ndipo patsogolo pake padali buku la Mûsa lomwe lidali chitsanzo chabwino ndi mtendere, (wotereyu angafanane ndi yemwe ali mum’dima wa umbuli yemwenso sadziwa cholinga chakulengedwa kwake?) Awa (amene aongoka) akulikhulupirira (buku ili la Qur’an), ndipo amene ati asalikhulupirire m’magulu (a adani), Moto ndiwo malo awo alonjezo. Choncho, usakhale ndi chipeneko pa ichi; ndithudi ichi ndi choona chochokera kwa Mbuye Wako koma anthu ambiri sakhulupirira

Verse 18 — Surah Hud 11:18

“Ndipo palibe oipitsitsa kuposa yemwe wapeka bodza pakumnamizira Allah (kuti ali ndi mwana ndi athandizi). Iwo adzabweretsedwa kwa Mbuye wawo (tsiku la Qiyâma) ndipo mboni (zomwe ndi angelo) zidzanena: “Awa ndi omwe adapekera Mbuye wawo bodza. Mverani! Tembelero la Allah lili pa ochita zoipa.”

Verse 19 — Surah Hud 11:19

“Omwe akutsekereza anthu kutsata njira ya Allah ndi kufuna kuikhotetsa (njirayo). Ndiponso iwo sakhulupirira za tsiku lachimaliziro

Verse 20 — Surah Hud 11:20

“Iwowa sangathe kumulepheretsa (Allah) m’dziko, ndiponso alibe atetezi pambuyo pa Allah. Chilango chawo chidzaonjezeredwa (chifukwa cha zoipa zawo). Sadali kutha kumva ngakhale kuona (chifukwa cha mkwiyo umene udali m’mitima mwawo wokwiira choonadi)

Verse 21 — Surah Hud 11:21

“Awa ndi omwe adziononga okha ndipo zomwe adali kuzipeka zidzawataika

Verse 22 — Surah Hud 11:22

“Zoonadi, iwo ndiotaika kwakukulu pa tsiku lachimaliziro

Verse 23 — Surah Hud 11:23

“Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi kumadzichepetsa kwa Mbuye wawo, iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo adzakhala nthawi yaitali

Verse 24 — Surah Hud 11:24

“Fanizo la magulu awiriwa (okhulupirira ndi osakhulupirira), lili ngati (munthu) wakhungu ndi gonthi, ndi (munthu) wopenya ndi wakumva. Kodi awiriwa angakhale ofanana (pa chikhalidwe chawo)? Bwanji simukuganiza

Verse 25 — Surah Hud 11:25

“Ndipo ndithu Ife tidamtuma Nuh (monga Mtumiki) kwa anthu ake (kuti akawauze): “Ine kwa inu ndine mchenjezi owonekera poyera.”

Verse 26 — Surah Hud 11:26

““Ndikuti musapembedze aliyense koma Allah basi. Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lopweteka.”

Verse 27 — Surah Hud 11:27

“Ndipo pompo akuluakulu mwa omwe sadakhulupirire mwa anthu ake, adati: “Sitikukuona koma ndiwe munthu monga ife, ndipo sitikukuona koma kuti akutsata anthu a pansi pathu ofooka pa nzeru (omwe sadalingalire mozama za iwe). Ndipo sitikukuonani kuti muli ndi ulemelero ndi ubwino wochuluka kuposa ife. Koma tikukuganizirani kuti ndinu onama.”

Verse 28 — Surah Hud 11:28

“(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi muona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo chowonekera chochokera kwa Mbuye wanga ndipo wandipatsa chifundo chochokera kwa Iye (monga uneneri), ndipo chabisika kwa inu, kodi tingakukakamizeni kuvomereza pomwe simukuchifuna?”

Verse 29 — Surah Hud 11:29

““Ndipo E inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma pa uthengawu. Palibe malipiro anga, koma ali kwa Allah basi. Ndipo ine sindingathamangitse amene akhulupirira (monga momwe mudandipemphera kuti ndiwathamangitse anthu ofooka kuti inu mulowe m’malo mwawo), ndithu iwo adzakumana ndi Mbuye wawo, ndipo ine ndikukuonani monga anthu osazindikira (mbuli).”

Verse 30 — Surah Hud 11:30

““Ndipo E inu anthu anga! Ndani angandithandize kwa Allah ngati nditawathamangitsa? Kodi simuganiza?”

Verse 31 — Surah Hud 11:31

““Ndipo ine sindikukuuzani kuti ndili ndi nkhokwe za chuma cha Allah kapena kuti ine ndikudziwa zinthu zamseli, ndiponso sindikunena kuti ndine m’ngelo. Ndiponso sindikunena kwa omwe maso anu akuwachepetsa kuti Allah sadzawapatsa chabwino. Allah akudziwa zam’mitima mwawo. (Ngati nditatero) ndiye kuti ine pamenepo ndili m’gulu la oipa.”

Verse 32 — Surah Hud 11:32

“(Iwo) adati: “E iwe Nuh! Watsutsana nafe, ndipo wachulukitsa kutsutsana nafe. Choncho bweretsa kwa ife chimene ukutilonjezacho, ngati ulidi mwa onena zoona

Verse 33 — Surah Hud 11:33

“Adati: “Ndithu Allah achibweretsa kwa inu ngati afuna, ndipo inu simungathe kumulepheretsa (chimene wafuna).”

Verse 34 — Surah Hud 11:34

““Ndipo kulangiza kwanga sikungakuthandizeni ngati ntafuna kukulangizani, ngati Allah akufuna kukulekelerani kusokera. Iye ndiye Mbuye wanu. Ndipo kwa Iye mudzabwezedwa.”

Verse 35 — Surah Hud 11:35

“Kapena akunena (osakhulupirira a m’Makka kuti: “Muhammad) waipeka (Qur’an mwa iye yekha)?” Nena: “ngati ndayipeka ndiye kuti machimo ake (akupekawo) ali pa ine. Ndipo ine ndili kutali ndi zoipa zimene mukuchita.”

Verse 36 — Surah Hud 11:36

“Ndipo tidamuululira Nuh kuti: “(Tsopano) sakhulupirira aliyense mwa anthu ako kupatula okhawo akhulupirira kale. Choncho, usadandaule pa zimene adali kuchita.”

Verse 37 — Surah Hud 11:37

““Ndipo khoma chombo moyang’aniridwa ndi Ife, ndi ulangizi wathu (satha kukuchitira choipa), ndipo usandiyankhulitse za iwo amene achita zoipa (kuti ndiwakhululukire). Ndithudi, iwo amizidwa.”

Verse 38 — Surah Hud 11:38

“Ndipo adayamba kukhoma chombo. Nthawi iliyonse akamdutsa akuluakulu a mwa anthu ake, adali kumchitira chipongwe. Naye ankanena (kuti): “Ngati inu Mukutichitira chipongwe, nafenso tidzakuchitirani chipongwe monga momwe mukutichitira chipongwe.”

Verse 39 — Surah Hud 11:39

““Posachedwa mudziwa kuti ndani chimdzere chilango chomuyalutsa ndi kumtsikira chilango chopitilira.”

Verse 40 — Surah Hud 11:40

“Kufikira pamene lidadza lamulo lathu, madzi naphulika mu uvuni, (chomwe chidali chisonyezo cha Nuh chosonyeza kudza kwa lamulo loona kwa anthu ake) tidamuuza (kuti): “Kweza m’menemo (m’chombo) mtundu uliwonse (wa nyama), ziwiriziwiri, (yaikazi ndi yaimuna), ndi anthu a kubanja lako kupatula omwe chiweruzo (cha Allah) chatsimikizidwa pa iwo (kuti aonongeke), ndipo (atengenso onse) amene akhulupirira.” Komatu ndi ochepa kwambiri amene adakhulupirira pamodzi ndi iye

Verse 41 — Surah Hud 11:41

“Ndipo (Nuh) adati: “Kwerani m’menemo mwadzina la Allah mkuyenda kwake ndi mkukocheza kwake. Ndithu Mbuye wanga Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.”

Verse 42 — Surah Hud 11:42

“Ndipo (chombocho) chidali kuyenda nawo m’mafunde onga mapiri, ndipo Nuh adaitana mwana wake yemwe adali patali (atakana kulowa m’chombo): “Mwana wanga! Kwera pamodzi ndi ife usakhale pamodzi ndi osakhulupirira.”

Verse 43 — Surah Hud 11:43

“(Iye) adati: “Ndithawira kuphiri likanditeteza ku madziwa.” Nuh adati: “Lero palibe otetezedwa ku lamulo la Allah kupatula yemwe Allah wamchitira chifundo.” Pompo mafunde adatchinga pakati pawo. Choncho adali mgulu la omizidwa

Verse 44 — Surah Hud 11:44

“Ndipo (pambuyo poonongeka onse ndi zonse zomwe Allah adafuna kuti zionongeke), kudanenedwa: “E iwe nthaka! Meza madzi ako. Ndipo iwe thambo! Amange (madzi ako amvula).” Choncho, madzi adaphwa ndipo lamulo lidakwaniritsidwa (loononga anthu oipa). Ndipo (chombo) chidaima pamwamba pa (phiri lotchedwa) Judi, ndipo kudanenedwa: “Aonongeke onse ochita zoipa.”

Verse 45 — Surah Hud 11:45

“Ndipo Nuh adafuulira Mbuye wake nati. “E Mbuye wanga! Ndithu mwana wanga ali mgulu la akubanja langa (akuonongedwa). Ndipo ndithu lonjezo lanu ndiloona, ndipo Inu Ndinu Woweruza mwachoonadi kuposa aweruzi onse.”

Verse 46 — Surah Hud 11:46

“(Allah) adati: “E iwe Nuh! Ndithu iyeyo si (mwana) wa m’banja lako. Iye zochita zake sizili zabwino. Choncho usandipemphe zomwe siukuzidziwa, Ine ndikukulangiza kuti usakhale m’gulu la osazindikira (mbuli).”

Verse 47 — Surah Hud 11:47

“(Nuh) adati: “E Mbuye wanga! Ndikudziteteza mwa Inu kuti ndisakupempheninso zomwe sindikuzidziwa. Ngati simundikhululukira ndi kundichitira chifundo, ndikhala mwa anthu otaika.”

Verse 48 — Surah Hud 11:48

“Kudanenedwa: “E iwe Nuh! Tsika (pa nthaka youma) mwamtendere wochokera kwa Ife, ndipo madalitso ambiri akhale pa iwe ndi pa anthu omwe ali nawe; ndipo kudzakhala mibadwo ina (yoipa pambuyo pako) yomwe tidzaisangalatsa, ndipo kenako chidzaikhudza chilango chowawa chochokera kwa Ife.”

Verse 49 — Surah Hud 11:49

“Izi ndi zina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuululira iwe. Siudali kuzidziwa, iwe ngakhale anthu ako, patsogolo pa ichi, (Qur’an isadadze). Choncho, pirira. Ndithu mathero abwino adzakhala kwa anthu oopa Allah

Verse 50 — Surah Hud 11:50

“Ndipo anthu (amtundu) wa Âdi, tidawatumizira m’bale wawo Hûd. Adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah! (Siyani kupembedza mafano). Mulibe mulungu wina koma Iye. Inu simuli kanthu koma ndinu opeka bodza (m’kunena kwanu kwakuti mafano ndi anzake a Allah).”

Verse 51 — Surah Hud 11:51

““E inu anthu anga! Sindikukupemphani malipiro pa ichi (uthengawu). Palibe Malipiro anga koma ali kwaYemwe adandilenga. Kodi mulibe nzeru?”

Verse 52 — Surah Hud 11:52

““Ndipo E inu anthu anga! Pemphani chikhululuko kwa Mbuye wanu, (pa machimo omwe mwakhala mukuchita), kenako lapani kwa Iye. Akutumizirani mitambo yodzetsa mvula yambiri, ndipo akuonjezerani mphamvu pa mphamvu zanu (zomwe muli nazo). Choncho, musatembenuke kukhala oipa.”

Verse 53 — Surah Hud 11:53

“(Iwo) adati: “E iwe Hûd! Sudatibweretsere chisonyezo chooneka (chosonyeza kuti ndiwe Mneneri), ndipo ife sitisiya (kupembedza) milungu yathu chifukwa cha zoyankhula zakozo. Ndipo ife sitikukhulupirira.”

Verse 54 — Surah Hud 11:54

““Sitinena kanthu, koma kuti (mwina) milungu yathu ina yakulodza misala.” (Iye) adati: “Ndithu ine ndikupereka umboni kwa Allah ndipo inunso perekani umboni kuti ine ndili kutali ndi zimene mukumphatikiza nazo (Allah pomazipembedza).”

Verse 55 — Surah Hud 11:55

““Kusiya Iye; (milungu yanuyo sindikuiopa ngati ili ndi mphamvu pamodzi ndi inu), tero ndichitireni chiwembu nonsenu, ndipo kenako musandiyembekezere (musandipatse nthawi).”

Verse 56 — Surah Hud 11:56

““Ndithu ine ndatsamira kwa Allah, Mbuye wanga yemwenso ali Mbuye wanu. Palibe chinyama chilichonse koma Allah wachigwira tsumba lake (ndikuchiyendetsa mmene akufunira). Ndithudi, Mbuye wanga Ngwachilungamo.”

Verse 57 — Surah Hud 11:57

““Ngati munyoza (kulandira chimene ndakuuzani palibe vuto kwa ine); ndithu ndafikitsa kwa inu chimene ndatumidwa. Ndipo Mbuye wanga (awaononga osakhulupirira, ndipo) abweretsa anthu ena m’malo mwanu, ndipo inu simungamusautse konse. Ndithu Mbuye wanga ndi Msungi wa chilichonse.”

Verse 58 — Surah Hud 11:58

“Ndipo pamene lamulo lathu lidafika (lakuwaononga), tidampulumutsa Hûd ndi amene adakhulupirira pamodzi naye, mwachifundo Chathu, ndipo tidawapulumutsa kuchilango chokhwima

Verse 59 — Surah Hud 11:59

“Ndipo awa ndi Âdi. Adatsutsa Ayah (ndime) za Mbuye wawo ndi kunyoza atumiki Ake; ndipo adatsata lamulo la yense wodzikweza, wamakani

Verse 60 — Surah Hud 11:60

“Ndipo adatsatizidwa ndi tembelero pa moyo wapano padziko lapansi ndi tsiku la Qiyâma (tsiku la chiweruziro). Dziwani! Ndithu Âdi adakana Mbuye wawo. Ha! Adaonongeka Âdi, anthu a Hûd

Verse 61 — Surah Hud 11:61

“Ndipo kwa anthu (a mtundu) wa Samud, (tidatuma) m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Lambirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye Yekha. Iye adakuumbani ndi nthaka ndi kukukhazikani m’menemo. Ndipo mpempheni chikhululuko (pa zolakwa zanu), kenako tembenukirani kwa Iye. Ndithu Mbuye wanga ali pafupi (ndi akapolo Ake). Ndipo Ngovomera mapempho (aopempha).”

Verse 62 — Surah Hud 11:62

“Iwo adati: “E iwe Swaleh! Ndithudi, udali woyembekezeka (kukhala mfumu kwa ife) patsogolo pa izi (usanabwere ndi izi). Ha! Kodi ukutiletsa kulambira zomwe makolo athu adali kulambira? Ndithu ife tili m’chikaiko chokaikira zomwe ukutiitanirazo.”

Verse 63 — Surah Hud 11:63

“(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wanga (chosonyeza kuona kwa zimenezi), nandipatsanso chifundo chochokera kwa Iye. Nanga ndi yani angandipulumutse ku chilango cha Allah ngati nditamunyoza? Choncho, simungandionjezere china chake koma kutaika basi.”

Verse 64 — Surah Hud 11:64

““Ndipo E inu anthu anga! Iyi ngamira ya Allah ndi chisonyezo kwa inu. Ilekeni izidya panthaka ya Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopa kuti chilango chomwe chili pafupi chingakuonongeni.”

Verse 65 — Surah Hud 11:65

“Koma adaipha. Choncho (Swaleh) adati: “Sangalalani m’midzi yanuyi pamasiku atatu. (Kenako mulangidwa). Limenelo ndi lonjezo osati labodza.”

Verse 66 — Surah Hud 11:66

“Choncho pamene lamulo Lathu lidadza (lakuononga midziyo), tidampulumutsa Swalih ndi anthu amene adakhulupirira naye, kukuyaluka kwa tsiku limenelo, mwa chifundo Chathu. Ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu, Ngopambana

Verse 67 — Surah Hud 11:67

“Ndipo amene adadzichitira okha zoipa phokoso lalikulu lidawaononga, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa)

Verse 68 — Surah Hud 11:68

“Ngati kuti iwo mudalibemo m’menemo. Mverani! Ndithu Asamudu adamkana Mbuye wawo. Choncho Asamudu adaonongeka

Verse 69 — Surah Hud 11:69

“Ndipo ndithu atumiki athu (angelo) adadza kwa Ibrahim ndi uthenga wabwino. (Iwo) adati: “Mtendere!” (Iye) adayankha: “Mtendere (ukhale pa inu!)” Ndipo (Ibrahim) sadakhalitse (adafulumira) kudza nayo nyama yootcha ya thole (mwana wa ng’ombe)

Verse 70 — Surah Hud 11:70

“Koma pamene adaona kuti manja awo sakuwatambasula kuchakudya adawadodoma, nadzadzidwa nawo mantha. (Iwo) Adati: “Usaope; ndithu ife tatumidwa kwa anthu a Luti (kuti tikawaononge ndiponso kukupatsa nkhani yabwino).”

Verse 71 — Surah Hud 11:71

“Ndipo (m’menemo nkuti) mkazi wake (wa Ibrahim) ali chiimire, ndipo adaseka. Kenaka tidamuuza uthenga wabwino (wakubadwa kwa) Ishaq ndipo pambuyo pa Ishaq, Ya’qub

Verse 72 — Surah Hud 11:72

“(Iye) adati: “Kalanga ine! Ndibereka pomwe ine ndili nkhalamba, ndiponso uyu mwamuna wanga ndi nkhalamba? Ndithudi, ichi ndi chinthu chododometsa.”

Verse 73 — Surah Hud 11:73

“(Angelowo) adati: “Ukudabwa ndi lamulo la Allah? Chisomo cha Allah ndi madalitso ake zili pa inu, E inu eni nyumba iyi! Iye Ngoyamikidwa, Mwini ulemelero!”

Verse 74 — Surah Hud 11:74

“Ndipo pamene Ibrahim mantha adamchokera ndikumufikira uthenga wabwino, adayamba kutidandaulira za anthu a Luti (kuti tisawaononge)

Verse 75 — Surah Hud 11:75

“Ndithu Ibrahim adali wodekha, wodandaulira Allah komanso wobwerera kwa Iye mwachangu (polapa)

Verse 76 — Surah Hud 11:76

“(Tidamuuza): “E iwe Ibrahim! Siya ichi. Lamulo la Mbuye wako, ndithu ladza. Ndipo ndithu iwo chiwadzera chilango chosabwezedwa.”

Verse 77 — Surah Hud 11:77

“Ndipo atumiki athu pamene adafika kwa Luti, iye anadandaula za iwo ndi kubanika nao mu mtima (chifukwa chosowa njira yowatetezera kwa anthu oipa pomwe iye sadadziwe kuti alendowo ndi angelo), nati: “Lino ndi tsiku lovuta.”

Verse 78 — Surah Hud 11:78

“Ndipo anthu ake adadza akuthamangira kwa iye (ku nyumba kwake kuti adzachite zauve ndi alendowo). Ndipo kalenso ankachita zoipa zokhazokhazi, (Luti) adati: “E anthu anga! Nawa asungwana anga; ngoyenera kwa inu (kuwakwatira, osati amuna anzanu) choncho, opani Allah, ndipo musandiyalutse pamaso pa alendo anga. Kodi mwa inu mulibe munthu woongoka?”

Verse 79 — Surah Hud 11:79

“(Iwo) adati: “Ndithu ukudziwa bwino kuti tilibe khumbo ndi atsikana ako. Ndipo ndithu iwe ukudziwa bwino chimene tifuna.”

Verse 80 — Surah Hud 11:80

“(Iye) adati: “Ndikadakhala nayo mphamvu (yomenyana nanu) kapena kotsamira kolimba kwamphamvu (ndikadalimbana nanu kuti musachite zauve ndi alendowa).”

Verse 81 — Surah Hud 11:81

“(Athengawa) adati: “E iwe Luti! Ife ndi athenga a Mbuye wako. Safika kwa iwe (ndi chilichonse choipa). Ndipo choka pamodzi ndi banja lako m’gawo la usiku, ndipo aliyense wa inu asatembenuke (kuyang’ana m’mbuyo akamva mkokomo wa kudza kwa chilangocho), kupatula mkazi wako; iye chimpeza chimene chiwapeze anthu enawo. Ndithu lonjezo lawo ndi m’mawa. Kodi m’mawa suudayandikire?”

Verse 82 — Surah Hud 11:82

“Choncho, pamene lidadza lamulo lathu, tidaugadabula (m’zindawo) kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, ndipo tidawavumbwitsira mvula ya sangalawe zopangika ndi dongo lotentheka ndi moto, zogwirana kwambiri

Verse 83 — Surah Hud 11:83

“(Sangalawezo) zokhala ndi zizindikiro kwa Mbuye wako. (Sangalawe iliyonse idali ndi mwini wake); ndipo chilango chimenechi sichili kutali ndi anthu oipa

Verse 84 — Surah Hud 11:84

“Ndipo, ku Madiyan tidamtuma m’bale wawo Shuaib, iye adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah; mulibe mulungu wina koma Iye. Ndipo musachepetse mulingo wa mbale ndi wasikelo (powapimira anthu), ine ndikukuonani kuti ndinu opeza bwino, ndipo ndikukuoperani chilango cha tsiku (lalikulu) lomwe lidzakuzingani.”

Verse 85 — Surah Hud 11:85

““Ndipo E inu anthu anga! Kwaniritsani mulingo wa mbale ndi wasikelo mwachilungamo, ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo (mwachinyengo). Ndipo musafalitse zoipa pa dziko ndi cholinga chodzetsa chisokonezo.”

Verse 86 — Surah Hud 11:86

““Chuma chimene wakusiirani Allah (m’njira yovomerezeka) ndicho chabwino kwa inu ngati muli okhulupirira. Ndipo ine sindine msungi wanu.”

Verse 87 — Surah Hud 11:87

“Adati: “E iwe Shuaib! Kodi mapemphero ako akukulamula (kuti utilamule) kuti tisiye zimene makolo athu ankapembedza, kapena kuti tisiye kuchita zimene tifuna pachuma chathu? (Adati mwachipongwe) ndithudi, iwe ndiwe wanzeru, ndi wolungama.”

Verse 88 — Surah Hud 11:88

“(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi umboni wowonekera wochokera kwa Mbuye wanga, ndipo nkundipatsa rizq labwino (lahalali) lochokera kwa Iye, (ndisiye zimenezi ndi kusankha njira yokhota)? Ndipo sindifuna kusiyana nanu pochita chimene ndakuletsani. Sindifuna china, koma kukonza mmene ndingathere; ndipo kupambana kwanga (pazimenezi) kuli kwa Allah. Kwa Iye ndatsamira, ndipo kwa Iye ndikutembenukira.”

Verse 89 — Surah Hud 11:89

““Ndipo E inu anthu anga! Kutsutsana nane kusakuchimwitseni kuopera kuti chingakupezeni chonga chimene chidawapeza anthu a Nuh kapena anthu a Hûd kapenanso anthu a Swaleh; ndipo anthu a Luti sali kutali ndi inu.”

Verse 90 — Surah Hud 11:90

““Ndipo mpempheni chikhululuko Mbuye wanu ndipo lapani kwa Iye (posiya machimo ndikuchita zabwino). Ndithu Mbuye wanga Ngwachisoni Ngwachikondi chochuluka (kwa anthu Ake).”

Verse 91 — Surah Hud 11:91

“(Iwo) adati: “E iwe Shuaib! Sitikumvetsa zambiri mwa zomwe ukunena. Ndipo ife tikukuona wofooka mwa ife. Pakadapanda akubanja lako, tikadakugenda ndi miyala. Ndipo ulibe ulemelero pa ife (koma tikusunga ulemu wa anthu akubanja lako).”

Verse 92 — Surah Hud 11:92

“(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi anthu akubanja kwanga ndiwo olemekezeka kwambiri kwa inu kuposa Allah? Ndipo mwamuyika Iye (Allah) kukhala kumbuyo kwa misana yanu. Ndithu Mbuye wanga zonse zimene mukuchita akuzidziwa bwinobwino.”

Verse 93 — Surah Hud 11:93

““Ndipo E anthu anga! Chitani (zimene mufuna) mmene mungathere; inenso ndichita chimodzimodzi (mmene ndingathere). Posachedwapa mudziwa ndani chimufike chilango chomsambula, ndipo ndani wabodza. Ndipo dikirani inenso ndidikira pamodzi ndi inu.”

Verse 94 — Surah Hud 11:94

“Ndipo pamene lamulo Lathu lidadza, tidampulumutsa Shuaib pamodzi ndi amene adakhulupirira naye, mwachifundo Chathu. Ndipo amene adachita zoipa, phokoso lidawachotsa moyo, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa)

Verse 95 — Surah Hud 11:95

“Ndiye ngati sadakhalemo. Tamverani! Adaonongeka (anthu) a ku Madiyan monga momwe adaonongekera Asamudu

Verse 96 — Surah Hud 11:96

“Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa zathu ndi umboni woonekera

Verse 97 — Surah Hud 11:97

“Kwa Farawo ndi nduna zake. Koma iwo adatsata lamulo la Farawo, ndipo lamulo la Farawo siloongoka

Verse 98 — Surah Hud 11:98

“Tsiku la Qiyâma, (Farawo) adzawatsogolera anthu ake ndi kuwafikitsa ku Moto. Ndipo taonani pamalo poipa kufikirapo

Verse 99 — Surah Hud 11:99

“Iwo adatsatizidwa ndi tembelero pano pa dziko lapansi ndipo pa tsiku la Qiyâma (adzatsatizidwanso). Taonani kuipa mphoto (yawo) yopatsidwa

Verse 100 — Surah Hud 11:100

“Izi ndi zina mwa nkhani za m’mizinda (zomwe) tikukusimbira. Ina mwa iyo ikadalipobe, ndipo ina idatha

Verse 101 — Surah Hud 11:101

“Ndipo sitidawachitire choipa (powaononga). Koma adadzichitira okha zoipa (pakusakhulupirira Allah ndi kupembedza mafano ndikuipitsa pa dziko), milungu yawo yomwe ankaipembedza kusiya Allah siidawathandize chilichonse pamene lidadza lamulo la Mbuye wako (la kuwaononga). Ndipo (milunguyo) siidawaonjezere (china chake) koma chionongeko basi

Verse 102 — Surah Hud 11:102

“Ndipo mmenemo ndi momwe kumakhalira kulanga kwa Mbuye wako pamene alanga anthu a m’mizinda akakhala oipa (pa makhalidwe). Ndithu kulanga kwake (Allah) nkowawa, nkwaukali

Verse 103 — Surah Hud 11:103

“Ndithu m’zimenezi muli lingaliro kwa yemwe akuopa chilango cha tsiku lachimaliziro. Limenelo ndi tsiku losonkhanitsidwa anthu. Ndipo limenelo ndi tsiku lochitiridwa umboni (ndi zolengedwa zonse)

Verse 104 — Surah Hud 11:104

“Ndipo sitikulichedwetsa koma m’nthawi yowerengeka (kwa Allah, ngakhale kuti kwa anthu likuoneka kuti lili kutali)

Verse 105 — Surah Hud 11:105

“Tsiku lakudza (zoopsa zake), sadzayankhula aliyense koma mwachilolezo Chake (Allah). Ena adzakhala oipa, ndipo (ena) adzakhala abwino

Verse 106 — Surah Hud 11:106

“Tsono amene adzakhala oipa kobwerera kwawo nkumoto. Iwo adzakhala m’menemo akufuula potulutsa mawu ndi kuwabweza (monga kulira kwa bulu)

Verse 107 — Surah Hud 11:107

“Adzakhala m’menemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna. Ndithu Mbuye wako Ngochita chimene wafuna

Verse 108 — Surah Hud 11:108

“Tsono amene adzakhale abwino adzakhala m’Munda wamtendere. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna; zopatsa (za Mbuye wako ndizo zopatsa) zosatha

Verse 109 — Surah Hud 11:109

“Choncho, usakhale ndi chipeneko pa zimene awa akuzipembedza (kuti ndimilungu yabodza). Sapembedza koma momwe amapembedzera makolo awo kale. Ndipo ndithu Ife tiwapatsa gawo lawo (la chilango) mokwanira popanda kuchepetsa

Verse 110 — Surah Hud 11:110

“Ndipo ndithu tidampatsa buku Mûsa, koma kusiyana kudabuka mmenemo (pakatanthauzidwe ka bukulo pambuyo pa Mûsa). Pakadapanda mawu a Mbuye wako omwe adatsogola (oti sadzawalanga nthawi isanafike), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo. Ndipo ndithu iwo ali m’kukaika ndi kupeneka (kwakukulu) pa zimenezo

Verse 111 — Surah Hud 11:111

“Ndipo ndithu Mbuye wako adzawapatsa onsewo mphoto ya zochita zawo mokwanira. Ndithu Iye Ngodziwa (zonse) zimene akuchita

Verse 112 — Surah Hud 11:112

“Choncho (E iwe Mtumiki!) Pitiriza kulungama monga momwe akulamulira (iwe) pamodzi ndi omwe atembenukira (kwa Allah), ndipo musapyole malire. Ndithu Iye akuona zonse zimene muchita

Verse 113 — Surah Hud 11:113

“Ndipo musapendekere kwa amene sali olungama kuopa kuti chilango cha Moto chingakukhudzeni; ndipo simudzakhala ndi atetezi kwa Allah, ndipo potero simudzathandizidwa (chilichonse)

Verse 114 — Surah Hud 11:114

“Ndipo pemphera Swala nsonga ziwiri za usana ndi nthawi za usiku zomwe zili pafupi ndi usana. Ndithu zabwino zimachotsa zoipa. Ichi ndi chikumbutso kwa okumbukira

Verse 115 — Surah Hud 11:115

“Ndipo pirira (E iwe Mtumiki! Pokwaniritsa malamulo a Mbuye wako)! Ndithu Allah sataya malipiro a ochita zabwino

Verse 116 — Surah Hud 11:116

“Kodi bwanji sadakhalepo, mu mibadwo ya anthu akale, eni nzeru (omvera akalangizidwa), oletsa kuononga pa dziko kupatula ochepa amene tidawapulumutsa mwa iwo? Ndipo amene adadzichitira okha zoipa adatsata zomwe adasangalatsidwa nazo, choncho, adali ochita zoipa

Verse 117 — Surah Hud 11:117

“Ndipo Mbuye wako sali woononga midzi mopanda chilungamo pomwe eni ake (midziyo) ali ochita zabwino

Verse 118 — Surah Hud 11:118

“Ndipo Mbuye wako akadafuna, anthu onse akadawachita kukhala mpingo umodzi. Choncho saleka kukhala osiyana (maganizo)

Verse 119 — Surah Hud 11:119

“Kupatula omwe Mbuye wako wawachitira chifundo; ndipo chifukwa cha chifundocho, adawalenga (koma okha akusankha zoipa). Ndipo mawu a Mbuye wako akwaniritsidwa (akuti): “Ndithudi, ndizadzadzitsa Jahannam ndi ziwanda ndi anthu onse pamodzi (omwe adali oipa).”

Verse 120 — Surah Hud 11:120

“Ndipo tikukusimbira zonse mwa nkhani za atumiki zomwe tikukulimbikitsa nazo mtima. Ndipo m’zimenezi choonadi chakufika ndi ulaliki ndiponso chikumbutso kwa okhulupirira

Verse 121 — Surah Hud 11:121

“Ndipo auze amene sadakhulupirire (kuti): “Chitani mmene mungathere; nafenso tichita (mmene tingathere).”

Verse 122 — Surah Hud 11:122

““Ndipo dikirani (chiweruzo cha Allah) nafenso tikudikira.”

Verse 123 — Surah Hud 11:123

“Zonse zobisika za kumwamba ndi pansi nza Allah ndipo zidzabwezedwa kwa Iye. Choncho, mpembedzeni ndi kutsamira kwa Iye. Ndithu Mbuye wako siwonyalanyaza zimene mukuchita