Back to Languages

Chichewa - Chapter 111 - Al-Masad

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Masad 111:1

“Aonongeka manja a Abi Lahab (omwe adali kuwagwiritsa ntchito pozunza Asilamu). Nayenso wawonongeka

Verse 2 — Surah Al-Masad 111:2

“Chuma chake ndi ulemelero wake (umene adaupeza) sizidamthandize ku chilango cha Allah

Verse 3 — Surah Al-Masad 111:3

“Adzalowa ku Moto wa malawi

Verse 4 — Surah Al-Masad 111:4

“Nayenso mkazi wake (adzalowa ku Moto) yemwe adali kusenza nkhuni (za minga pomutchera Mtumiki (s.a.w) komanso amanka nadanitsa pakati pa anthu

Verse 5 — Surah Al-Masad 111:5

“Mkhosi mwake mdzamangidwa chingwe chopiringidwa bwino cha mlaza (chomlanga nacho)