Verse 1 — Surah An-Nas 114:1
“Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye (Mleri) wa anthu (Yemwe akulinganiza zinthu zawo)
Verse 2 — Surah An-Nas 114:2
“Mfumu ya anthu ( Imene iri ndi mphamvu yochita chirichonse pa iwo)
Verse 3 — Surah An-Nas 114:3
“Wopembedzedwa wa anthu
Verse 4 — Surah An-Nas 114:4
“Kuzoipa za mnong’onezi (yemwe amathira unong’onezi wake m’mitimaya anthu) yemwenso amabisala (posiya unong’onezi wake ngati mwini mtimawo atankumbukira Allah)
Verse 5 — Surah An-Nas 114:5
“Yemwe amanong’oneza mzifuwa za anthu
Verse 6 — Surah An-Nas 114:6
“Wochokera m’ziwanda ndi mwa anthu.”