Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 15 - Al-Hijr
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Hijr 15:1
“۞ Alif-Lâm-Râ. Izi ndi Aaya (ndime) za m’buku (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika,) ndi Qur’an yomveka bwino
Verse 2 — Surah Al-Hijr 15:2
“Nthawi zambiri omwe sadakhulupirire (pamene adzakhala m’Moto) adzalakalaka kuti akadakhala okhulupirira (pamoyo wa pa dziko lapansi)
Verse 3 — Surah Al-Hijr 15:3
“Asiye azidya (chakudya monga momwe zidyera nyama) ndi kusangalala; ndipo chiyembekezo chiziwatangwanitsa ndi kuwanyenga; posachedwa adziwa (kuti zimene amaziyembekezerazo nzabodza)
Verse 4 — Surah Al-Hijr 15:4
“Ndipo sitidaononge mudzi uliwonse (m’midzi yochita zoipa) koma udali ndi nthawi yake (youwonongera) yodziwika
Verse 5 — Surah Al-Hijr 15:5
“Ndipo palibe mtundu wa anthu umene ungaitsogolere nthawi yake (yofera) kapena kuichedwetsa (itakwana kale)
Verse 6 — Surah Al-Hijr 15:6
“Ndipo (osakhulupirira) akunena (mwachipongwe) “E iwe amene wavumbulutsiridwa ulaliki! Ndithudi ndiwe wamisala.”
Verse 7 — Surah Al-Hijr 15:7
““Bwanji iwe osatibweretsera angelo (kuti akuchitire umboni) ngati uli mmodzi waonena zoona?”
Verse 8 — Surah Al-Hijr 15:8
“(Allah akuwauza:) “Ife sititsitsa angelo pokhapokha kutatsimikizika (tikawatuma kukapereka chilango kwa anthu). Ndipo pamenepo sangapatsidwe nthawi.”
Verse 9 — Surah Al-Hijr 15:9
“Ndithu Ife ndife omwe tavumbulutsa Qur’an, ndipo ndithudi, tiisunga
Verse 10 — Surah Al-Hijr 15:10
“Ndithudi tidatuma (atumiki) patsogolo pako m’magulu (a anthu) akale, oyamba
Verse 11 — Surah Al-Hijr 15:11
“Ndipo sadali kuwadzera mtumiki aliyense, koma ankamchitira chipongwe
Verse 12 — Surah Al-Hijr 15:12
“Momwemo tikuupititsa (mkhalidwe wachipongwewu) m’mitima mwa oipa
Verse 13 — Surah Al-Hijr 15:13
“Koma saikhulupirira Qur’aniyi chikhalirecho mafanizo a anthu oyamba awadutsa (ndipo aona momwe tidawaonongera)
Verse 14 — Surah Al-Hijr 15:14
“Ndipo tikadawatsekulira (awa osakhulupirira) khomo lakumwamba ndipo nkukhala akukwera m’menemo (ndi kutsika monga momwe amafunira kuti zimenezo zikhale chozizwitsa cha Mtumiki)
Verse 15 — Surah Al-Hijr 15:15
“Akadati: “Ndithu maso athu aledzera; (iyayi) koma ndife anthu olodzedwa (tikuona zomwe sindizo).”
Verse 16 — Surah Al-Hijr 15:16
“Ndithudi, kumwamba tidaikako “Buruji” (njira momwe zikuyendamo nyenyezi) ndipo tidakukongoletsa kwa okuwona
Verse 17 — Surah Al-Hijr 15:17
“Ndipo tidakuteteza kwa satana aliyense wopirikitsidwa (kumwambako akafuna kukamvetsera zimene zikunenedwa kumeneko)
Verse 18 — Surah Al-Hijr 15:18
“Kupatula amene amamvetsera mobera; ndipo pompo chinsakali chamoto choonekera chimamtsata
Verse 19 — Surah Al-Hijr 15:19
“Ndipo nthaka tidaiyala ndi kuikamo mapiri ndipo tameretsa mmera wa chinthu chilichonse m’menemo mwamlingo (wake)
Verse 20 — Surah Al-Hijr 15:20
“Ndipo mmenemo takupangirani zinthu zoyendetsa moyo (wanu zakudya ndi zakumwa ndi zina zotere) ndiponso (tidakupatsani ana ndi ziweto) zomwe inu simungathe kuzidyetsa. (Ife ndife amene tikuzikonzera chakudya chawo, osati inu)
Verse 21 — Surah Al-Hijr 15:21
“Ndipo palibe chinthu chilichonse koma gwero lake likuchokera kwa Ife; ndipo sitichitsitsa koma mwamlingo wodziwika (osati mwachisawawa)
Verse 22 — Surah Al-Hijr 15:22
“Ndipo timazitumiza mphepo zitasenza madzi, ndipo madziwo tikuwatsitsa kuchokera kumitamboyo; kenako tikukumwetsani madziwo (tikukumwetseraninso ziweto zanu, mitengo yanu ndi zina), ndipo inu si amene mukuwasunga (madziwo)
Verse 23 — Surah Al-Hijr 15:23
“Ndipo ndithudi, Ife ndife omwe timapereka moyo, ndi kupereka imfa. Ndiponso Ife ndi Amlowam’malo (a chinthu chilichonse chimene chikusiidwa chopanda mwini)
Verse 24 — Surah Al-Hijr 15:24
“Ndipo ndithu tikuwadziwa mwa inu amene atsogola (amene adafa kale), ndipo ndithu tikuwadziwanso amene atsalira (ali ndi moyobe ndi amene sanabadwe)
Verse 25 — Surah Al-Hijr 15:25
“Ndipo ndithu palibe chikaiko, Mbuye wako ndi Yemwe adzawasonkhanitsa (pambuyo pa imfa kuti adzawaweruze). Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa chilichonse
Verse 26 — Surah Al-Hijr 15:26
“Ndipo ndithu tidamlenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera, osinthika mtundu
Verse 27 — Surah Al-Hijr 15:27
“Ndipo ziwanda tidazilenga kale ndi moto wamphepo yotentha kwambiri
Verse 28 — Surah Al-Hijr 15:28
“Ndipo (kumbuka) pamene Mbuye wako adauza angelo (kuti): “Ndithu Ine ndilenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
Verse 29 — Surah Al-Hijr 15:29
““Choncho ndikamkwaniritsa ndikumuuzira mzimu wolengedwa ndi Ine, muweramireni momulemekeza.’’
Verse 30 — Surah Al-Hijr 15:30
“Choncho angelo onse adamuweramira
Verse 31 — Surah Al-Hijr 15:31
“Kupatula Iblis; adakana kukhala mmodzi mwa owerama
Verse 32 — Surah Al-Hijr 15:32
“Allah adati: “E iwe Iblis! Chifukwa ninji sudakhale pamodzi ndi owerama?”
Verse 33 — Surah Al-Hijr 15:33
“Adati: “Sindingamuweramire munthu yemwe mwam’lenga ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
Verse 34 — Surah Al-Hijr 15:34
“(Allah) adati: “Choncho choka m’menemo; ndithu iwe ndiwe wopirikitsidwa (ku chifundo Changa).”
Verse 35 — Surah Al-Hijr 15:35
““Ndipo ndithu matembelero ali pa iwe mpaka tsiku lamalipiro.”
Verse 36 — Surah Al-Hijr 15:36
“(Iblis) adati: “Mbuye wanga choncho ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwe kwa akufa.”
Verse 37 — Surah Al-Hijr 15:37
“(Allah) adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi mwa opatsidwa nthawi (danga).”
Verse 38 — Surah Al-Hijr 15:38
“Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (ikadzafika nthawi imeneyo, udzafa).”
Verse 39 — Surah Al-Hijr 15:39
“(Satana) adati: “Mbuye wanga! Pakuti mwanena kuti ndine wosokera, choncho ndikawakometsera za m’dziko (kufikira kuti akakulakwireni), ndithu ndikawasokeretsa onse.”
Verse 40 — Surah Al-Hijr 15:40
““Kupatula akapolo anu oyeretsedwa, mwa iwo.”
Verse 41 — Surah Al-Hijr 15:41
“(Allah) adati: “Iyi ndinjira yoongoka yobwerera kwa Ine (ndipo adzandidzera akadzafuna).”
Verse 42 — Surah Al-Hijr 15:42
“Ndithudi akapolo Anga pa iwo sudzakhala ndi mphamvu kupatula okutsata (mwachifuniro chawo) mwa opotoka.”
Verse 43 — Surah Al-Hijr 15:43
“Ndithu Jahannam ndiwo malo awo olonjezedwa kwa onse
Verse 44 — Surah Al-Hijr 15:44
“Ili ndi makomo asanu ndi awiri; khomo lililonse lili ndi gawo logawidwa mwa iwo
Verse 45 — Surah Al-Hijr 15:45
“Ndithudi owopa Allah adzakhala m’minda ndi akasupe (omwe adzakhala patsogolo pawo)
Verse 46 — Surah Al-Hijr 15:46
“(Ndipo tidzawauza) “Lowani m’menemo mwamtendere, mosatekeseka.”
Verse 47 — Surah Al-Hijr 15:47
“Ndipo tidzawachotsera mfundo za chidani zomwe zidali m’mitima mwawo; (adzakhala) mwachibale, (mokondana,) atakhala pa mipando yachifumu atayang’anizana nkhope
Verse 48 — Surah Al-Hijr 15:48
“Mmenemo masautso sakawakhudza, ndiponso sadzatulutsidwamo
Verse 49 — Surah Al-Hijr 15:49
“Auze akapolo anga kuti ndithu Ine ndine Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha
Verse 50 — Surah Al-Hijr 15:50
“Ndipo ndithu chilango Changa ndi chilango chopweteka zedi
Verse 51 — Surah Al-Hijr 15:51
“Ndipo auze nkhani ya alendo a (Mneneri) Ibrahim
Verse 52 — Surah Al-Hijr 15:52
“Pamene adalowa kwa iye ndikunena: “Salaman (Mtendere!)” (Iyenso adawayankha: “Mtendere ukhalenso pa inu.” Ndipo Pamene adaona kuti akana chakudya) Adati: “Ndithu ife tikukuopani.”
Verse 53 — Surah Al-Hijr 15:53
“Iwo adati: “Usaope! Ife tikukuuza nkhani yabwino ya (kuti ubala) mwana wanzeru kwambiri.”
Verse 54 — Surah Al-Hijr 15:54
“Iye adati: “Ha! Mukundiuza nkhani iyi pomwe ukalamba wandifikira? Kodi nkhani yabwinoyi mukundiuza mnjira yotani?”
Verse 55 — Surah Al-Hijr 15:55
“Iwo adati: “Takuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi; choncho, usakhale mwa otaya mtima.”
Verse 56 — Surah Al-Hijr 15:56
“Iye adati: “(Ine sinditaya mtima ndi chifundo cha Allah. Ndipo) palibe angataye mtima ndi chifundo cha Allah, koma wosokera basi (yemwe sazindikira ukulu wa Allah).”
Verse 57 — Surah Al-Hijr 15:57
“Iye adati: “Nanga cholinga chanu china nchiyani, E inu otumidwa?”
Verse 58 — Surah Al-Hijr 15:58
“Iwo adati: “Ife tatumidwanso kwa anthu aja oipa (kuti tikawaononge).”
Verse 59 — Surah Al-Hijr 15:59
““Kupatula akubanja la Luti, ndithu ife tikawapulumutsa onse.”
Verse 60 — Surah Al-Hijr 15:60
““Koma mkazi wake (wa Luti), tamkonzera kukhala mmodzi wa otsalira pambuyo.”
Verse 61 — Surah Al-Hijr 15:61
“Ndipo pamene atumikiwo adawadzera anthu a Luti (ali mmaonokedwe amunthu)
Verse 62 — Surah Al-Hijr 15:62
“(Luti) adati: “Ndithudi, inu ndi anthu osadziwika (sitikudziwani).”
Verse 63 — Surah Al-Hijr 15:63
“Iwo adati: “Inde, ife takudzera ndi zomwe (iwo) adali kuzikaikira, (zomwe ndi chilango chawo).”
Verse 64 — Surah Al-Hijr 15:64
““Ndipo tadza kwa iwe ndi (chinthu) choonadicho, ndithu ife ndi owona (pazimene tinenazi).”
Verse 65 — Surah Al-Hijr 15:65
““Choncho, choka ndi banja lako mkati mwa usiku; ndipo iwe udziwatsata pambuyo pawo; tsono aliyense wa inu asayang’ane kumbuyo (akamva mkokomo wachilango chochokera kumwamba, kuopa kuti angafe), ndipo yendani (mwachangu) kunka komwe mukulamulidwa.”
Verse 66 — Surah Al-Hijr 15:66
“Ndipo tidamudziwitsa iyeyo (Luti) lamulo lathu lakuti ndithu phata lawo anthu (ochimwawo) lidzadulidwa kum’banda kucha
Verse 67 — Surah Al-Hijr 15:67
“Ndipo adadza (kwa Luti) anthu a m’mudziwo akusangalala (poona kuti kwadza alendo okongola kuti achite nawo zadama)
Verse 68 — Surah Al-Hijr 15:68
“(Mneneri Luti) adati: “Ndithu awa ndialendo anga; choncho musandiyalutse (pochita nawo zadama).”
Verse 69 — Surah Al-Hijr 15:69
““Muopeninso Allah, ndipo musandichititse manyazi (pamaso pawo).”
Verse 70 — Surah Al-Hijr 15:70
“Iwo adati (kwa Mneneri Luti): “Kodi sitidakuletse kulandira anthu (achilendo)?”
Verse 71 — Surah Al-Hijr 15:71
“Iye adati: “Awa (akazi onsewa ali ngati) ana anga. Ngati inu ndinu ochita (chimene chalamulidwa, akwatireni; musachite zauve ndi alendowa).”
Verse 72 — Surah Al-Hijr 15:72
“Ndikulumbira moyo wako, ndithu iwo m’kuledzera kwawo (ndi zoipa) akungoyumbayumba
Verse 73 — Surah Al-Hijr 15:73
“Choncho mkuwe wa chilango udawagwira pamene dzuwa linkatuluka
Verse 74 — Surah Al-Hijr 15:74
“Choncho (midziyo) tidaigadabula kumwamba kukhala pansi, (pansi kukhala kumwamba); ndipo tidawavumbwitsira mvula yamiyala (yotentha) ya moto
Verse 75 — Surah Al-Hijr 15:75
“Ndithudi, (m’nkhani iyi) muli malingaliro (aakulu) kwa anthu olingalira zinthu
Verse 76 — Surah Al-Hijr 15:76
“Ndipo (midzi) iyi (yomwe tidaiwononga chotereyi), ili chikhalire m’njira moyenda anthu (ndipo iwo akuona zizindikiro zake)
Verse 77 — Surah Al-Hijr 15:77
“Ndithudi, mzimenezi muli phunziro (lalikulu) kwa okhulupirira
Verse 78 — Surah Al-Hijr 15:78
“Ndipo ndithu anthu a m’nkhalango (anthu a Mneneri Shuaib) adali ochita zoipa kwabasi
Verse 79 — Surah Al-Hijr 15:79
“Choncho, tidawalanga. Ndipo (maiko) awiriwa ali m’njira zoonekera, (momwe Aquraish amadutsa pa maulendo awo)
Verse 80 — Surah Al-Hijr 15:80
“Ndipo ndithu okhala m’chigwa cha Hijr (Asamuda), Adatsutsa atumiki
Verse 81 — Surah Al-Hijr 15:81
“Tidawapatsa zisonyezo zathu, koma sadazilabadire
Verse 82 — Surah Al-Hijr 15:82
“Iwo adali kujoba nyumba m’mapiri mwamtendere (ankaboola mapiri kuwasandutsa nyumba zawo)
Verse 83 — Surah Al-Hijr 15:83
“Choncho, chiphokoso cha chilango chidawapeza m’mawa
Verse 84 — Surah Al-Hijr 15:84
“Sichidawathandize (chuma) chomwe ankachipeza (ngakhalenso zimene ankazichita)
Verse 85 — Surah Al-Hijr 15:85
“Sitidalenge thambo ndi nthaka ndi (zonse) zapakati pake koma (kulimbikitsa) choonadi. Ndipo palibe chikaiko, Qiyâma idza. Choncho mkhululukire kukhululuka kwabwino (aliyense wokuchitira zoipa)
Verse 86 — Surah Al-Hijr 15:86
“Ndithudi, Mbuye wako, Iye ndi Mlengi wa zonse, Wodziwa kwambiri
Verse 87 — Surah Al-Hijr 15:87
“Ndipo ndithu takupatsa (Ayah izi) zisanu ndi ziwiri zomawerenga kawirikawiri, (Sûrat Al-Fatihah), ndi Qur’an yolemekezeka
Verse 88 — Surah Al-Hijr 15:88
“Usatong’olere maso ako (kuyang’ana) zimene tawasangalatsa nazo mitundumitundu ya mwa iwo (monga chuma cha anthu osakhulupirira). Usawadandaulirenso iwo ndipo tsitsa phiko lako kwa okhululupirira, (uwafungatire)
Verse 89 — Surah Al-Hijr 15:89
“Ndipo nena: “Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera (sindikubisa chilichonse kuopera kuti chingakutsikireni chilango).”
Verse 90 — Surah Al-Hijr 15:90
“Monga momwe tidatsitsira (chilango) kwa amene adadzigawa m’magulu
Verse 91 — Surah Al-Hijr 15:91
“Omwe aichita Qur’an kukhala magawomagawo; (zina nkuzikhulupirira, zina nkuzitsutsa)
Verse 92 — Surah Al-Hijr 15:92
“(Allah akudzilumbilira kuti:) Pali Mbuye wako, tidzawafunsa onse (tsiku la Qiyâma)
Verse 93 — Surah Al-Hijr 15:93
“Pazimene ankachita (padziko lapansi)
Verse 94 — Surah Al-Hijr 15:94
“Choncho, lengeza zimene ukulamulidwa, ndipo uwapewe opembedza mafano, (usaope chilichonse kwa iwo)
Verse 95 — Surah Al-Hijr 15:95
“Ndithu Ife tikukwanira kukuteteza ku (zoipa za) achipongwe
Verse 96 — Surah Al-Hijr 15:96
“Omwe akupanga milungu ina ndi kuiphatikiza ndi Allah, posachedwapa adziwa (zotsatira zake)
Verse 97 — Surah Al-Hijr 15:97
“Ndithu Ife tikudziwa kuti chifuwa chako chikubanika ndi zimene akunenazo
Verse 98 — Surah Al-Hijr 15:98
“(Koma pirira), lemekeza Mbuye wako pamodzi ndi kumtamanda (ndi rnbiri Zake zabwino) ndipo khala mwa olambira (Allah)
Verse 99 — Surah Al-Hijr 15:99
“Ndipo mpembedze Mbuye wako mpaka chikufike chitsimikizo (imfa)