Back to Languages

Chichewa - Chapter 16 - An-Nahl

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah An-Nahl 16:1

“Lamulo la Allah lidzafika, (ndithu) choncho, musalifulumizitse; (ndipo khulupirirani kuti Iye ndi Allah) Woyera Wopatukana ndi mbiri zopunguka, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo

Verse 2 — Surah An-Nahl 16:2

“Amatumiza angelo pansi pamodzi ndi chivumbulutso mwa lamulo Lake (Allah), kwa omwe wawafuna mwa akapolo Ake (powauza) kuti: “Achenjezeni (anthu zakuti): ‘Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha, choncho ndiopeni.”

Verse 3 — Surah An-Nahl 16:3

“Adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi (osati mwakungoseweretsa chabe) ndipo watukuka kuzimene akumphatikiza nazo (ophatikiza Allah ndi mafano)

Verse 4 — Surah An-Nahl 16:4

“Adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna. Ha! kenaka iye (munthuyo) wakhala wotsutsana naye (Allah) woonekera

Verse 5 — Surah An-Nahl 16:5

“Ndipo adalenga ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi) mwa izo mukupeza zofunda, ndi zothandiza (zina zambiri), ndipo zina mwa izo mumazidya

Verse 6 — Surah An-Nahl 16:6

“Ndipo mumakondwa ndi kunyadira chifukwa cha kukongola kwa izo mukamabwera nazo (kuchokera kubusa mimba zitakhuta), ndi popita nazo (kubusa zikuyenda mwandawala)

Verse 7 — Surah An-Nahl 16:7

“Ndipo zimasenza mitolo yanu (yolemera) kukafika nayo ku midzi yakutali komwe simumatha kukafikako popanda kuvutika kwambiri. Ndithu Mbuye wanu Ngodekha kwabasi, Ngwachisoni zedi

Verse 8 — Surah An-Nahl 16:8

“(Adalenganso) akavalo, nyumbu ndi abulu kuti muzizikwera ndi kutinso zizikhala chokometsera chanu (cholowetsa chisangalalo m’mitima yanu); ndipo adzalenga (zokwera zina) zomwe simukuzidziwa

Verse 9 — Surah An-Nahl 16:9

“Ndipo ndi udindo wa Allah kusonyeza njira yolungama (yomwe ingakufikitseni ku Munda wamtendere), koma zilipo njira zina zokhota (zomwe sizifikitsa ku choonadi). Ndipo Allah akadafuna, akadakuongolani nonsenu (mwa chifuniro chanu ndi mopanda chifuniro chanu. Koma Iye adakupatsani nzeru kuti musankhe nokha njira imene mufuna)

Verse 10 — Surah An-Nahl 16:10

“Iye ndi Amene akukutsitsirani madzi kuchokera ku mitambo, madziwo mumamwa (pothetsa ludzu lanu), ndipo ndi madziwo mitengo imamera; mitengo yomwe mumadyetsera ziweto (zanu)

Verse 11 — Surah An-Nahl 16:11

“Ndi madzi omwewo amakumeretserani mmera, (mitengo ya) mzitona, kanjedza, mphesa, ndi mitundu ina yonse ya zipatso. Ndithu kupezeka kwa zimenezi ndi chisonyezo (chosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu olingalira

Verse 12 — Surah An-Nahl 16:12

“Ndipo chifukwa cha inu adagonjetsa usiku ndi usana; dzuwa ndi mwezi; (zonse zidalengedwa kuti zibwere ndi zokomera inu). Nazo nyenyezi zidagonjetsedwa mwa lamulo Lake. Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu anzeru

Verse 13 — Surah An-Nahl 16:13

“Ndiponso ndi zimene adakulengerani m’nthaka (zinthu zododornetsa monga nyama, mmera, miyala yamtengo wapatali, zamoyo ndi zopanda moyo), zautoto wosiyanasiyana ndi maonekedwe osiyanasiyana; ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa anthu olalikika

Verse 14 — Surah An-Nahl 16:14

“Ndipo Iye ndi Yemwe adagonjetsa nyanja kuti mudye nyama yamatumbi (ya) m’menemo (nsomba) ndikuti mutulutse m’menemo zodzikongoletsera zomwe mumavala; ndipo uona zombo zikuluzikulu zikung’amba (mafunde) m’menemo kuti mufunefune zabwino zake (njira ya malonda), ndi kuti muthokoze (Mbuye wanu Allah)

Verse 15 — Surah An-Nahl 16:15

“Ndipo adaika panthaka mapiri ataliatali kuti (nthaka) isagwedezeke nanu; ndipo (adaika) mitsinje ndi misewu kuti muongoke (potsata njira yeniyeni ndikukafika komwe mukufuna)

Verse 16 — Surah An-Nahl 16:16

“Ndipo (adaikanso) zizindikiro zina, ndiponso kupyolera m’nyenyezi, iwo amalondola njira

Verse 17 — Surah An-Nahl 16:17

“Kodi Yemwe amalenga angalingane ndi omwe salenga? Kodi simungakumbukire (ndikudziwa kulakwa kwanu pomuyerekeza Allah ndi mafano)

Verse 18 — Surah An-Nahl 16:18

“Ngati mutayesera kuwerengera mtendere wa Allah simungathe kuuwerengera (wonse); ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

Verse 19 — Surah An-Nahl 16:19

“Ndipo Allah akuzidziwa zimene mukuzibisa, ndi zomwe mukuwonetsera

Verse 20 — Surah An-Nahl 16:20

“Ndipo zomwe mukuzipembedza kusiya Allah, sizilenga chilichonse, ndipo izo nzolengedwa

Verse 21 — Surah An-Nahl 16:21

“Zakufa zopanda moyo; ndipo sizizindikira kuti nliti akufa adzaukitsidwa (m’manda mwawo)

Verse 22 — Surah An-Nahl 16:22

“Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi Yekha; koma amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, mitima yawo ikukana (kukhulupirira umodzi wa Allah), ndipo iwo akudzitukumula

Verse 23 — Surah An-Nahl 16:23

“Palibe chikaiko, Allah akudziwa zomwe akubisa, ndi zomwe akuzilengeza. Ndithudi, Iye sakonda odzikuza

Verse 24 — Surah An-Nahl 16:24

“Ndipo (osakhulupirira) akafunsidwa: “Kodi Mbuye wanu watumizanji (kwa Mneneri Muhammad {s.a.w})?” Akunena: “(Sadatumize chilichonse koma) nthano zabodza za anthu akale.”

Verse 25 — Surah An-Nahl 16:25

“(Motero akuwasokeretsa anthu) kuti akasenze mitolo yawo (ya machimo) yokwanira pa tsiku la Qiyâma, ndiponso gawo lamitolo ya omwe akuwasokeretsa popanda kuzindikira (osokerawo). Tamverani! Ndi yoipa kwabasi mitolo yomwe azikaisenza

Verse 26 — Surah An-Nahl 16:26

“Adachita ndale omwe adalipo patsogolo pawo; choncho Allah adagumula maziko anyumba zawo. Ndipo madenga adawagwera pamwamba pawo; ndipo chilango chidawadzera kuchokera komwe sadali kukudziwa

Verse 27 — Surah An-Nahl 16:27

“Kenako tsiku la Qiyâma adzawayalutsa ndi kunena: “Ali kuti omwe mudali kundiphatikiza nawo, omwe chifukwa cha iwo mudali kukangana (ndi Mtumiki)?” Adzanena omwe apatsidwa nzeru: “Ndithu kuyaluka ndi tsoka loipa zili pa osakhulupirira lero.”

Verse 28 — Surah An-Nahl 16:28

“Omwe angelo akutenga miyoyo yawo atadzichitira okha zoipa (ponyoza Allah). Choncho adzadzipereka (kwa angelowa, kuti atenge miyoyo yawo akunena:) “Sitidali kuchita choipa chilichonse.” (Angelo adzati:) “Zoona, palibe chikaiko, Allah akudziwa kwambiri zomwe munkachita.”

Verse 29 — Surah An-Nahl 16:29

““Choncho, lowani makomo a ku Jahannam; mukakhala m’menemo nthawi yaitali.” Taonani kuipitsitsa kwa malo a anthu odzikweza

Verse 30 — Surah An-Nahl 16:30

“Ndipo kukanenedwa kwa omwe akuopa Allah (kuti): “Kodi nchiyani watumiza Mbuye wanu?” Amati: “Zabwino.” Kwa omwe achita zabwino padziko ili lapansi, awapatsanso zabwino, ndipo Nyumba ya tsiku la chimaliziro njabwino kwambiri, ndipo taonani ubwino wa Nyumba ya oopa (Allah)

Verse 31 — Surah An-Nahl 16:31

“Minda yamuyaya adzailowa, pansi pake padzakhala pakuyenda mitsinje (ndi patsogolo pake), chokhumba chilichonse akachipeza mmenemo (popanda kuchivutikira); umo ndi momwe Allah amawalipirira omuopa (iye)

Verse 32 — Surah An-Nahl 16:32

“Amene miyoyo yawo angelo amaitenga iwo ali abwino, uku akuwauza: “Mtendere uli pa inu, lowani ku Munda wamtendere chifukwa cha (zabwino) zija zomwe mudali kuzichita.”

Verse 33 — Surah An-Nahl 16:33

“Kodi akuyembekezera china, awa osakhulupirira, posakhala kuti angelo awadzere ndikuwaononga; kapena kuti liwadzere lamulo la Mbuye wako (lakuwalanga)? Momwemo ndi m’mene adachitiranso omwe adalipo patsogolo pawo. Koma Allah sadawachitire choipa koma adadzichitira okha choipa

Verse 34 — Surah An-Nahl 16:34

“Choncho, zoipa za zomwe adachita zidawapeza, ndipo chilango chidawazinga pa zomwe ankazichita mwachipongwe

Verse 35 — Surah An-Nahl 16:35

“Ndipo aja amapembedza mafano akuti: “Allah akadafuna, sitikadapembedza chilichonse kusiya Iye, ife ngakhale makolo athu; ndiponso palibe chomwe tikadachiyesa choletsedwa popanda lamulo Lake.” Momwemo ndimo adachitiranso aja omwe adalipo patsogolo pawo. Kodi atumiki ali ndi udindo winanso, osati kufikitsa uthenga woonekera (womveka)

Verse 36 — Surah An-Nahl 16:36

“Ndipo ndithu ku mtundu uliwonse tidatumiza mtumiki (amene amawauza kuti): “Pembedzani Allah, ndi kumpewa (Iblis) woipa.” Choncho alipo ena mwa iwo omwe Allah adawaongola, ndipo alipo ena mwa iwo omwe kusokera kudatsimikizika pa iwo. Choncho yendani pa dziko ndikuyang’ana (kuti) kodi adali bwanji mathero a otsutsa

Verse 37 — Surah An-Nahl 16:37

“Ngati uwumilira kwambiri kuti uwaongole, komatu Allah saongola yemwe akusokeretsa (ena), ndipo sadzapeza wowathangata

Verse 38 — Surah An-Nahl 16:38

“Ndipo iwo adalumbilira m’dzina la Allah, kulumbilira kwawo kwamphamvu (kuti) Allah sadzaukitsa amene afa; nchotani (kuti asawaukitse?) Ili ndi lonjezo lokakamizika kwa Iye, (kuwaukitsa ndi kuwalipira); koma anthu ambiri sadziwa

Verse 39 — Surah An-Nahl 16:39

“(Adzawaukitsa) kuti awafotokozere za zomwe adali kusiyana ndi kuti amene sadakhulupirire adziwe kuti ndithu iwo adali abodza

Verse 40 — Surah An-Nahl 16:40

“Ndithu liwu Lathu pa chinthu chimene tikuchifuna kuti chichitike ndikuchiuza basi kuti: “Chitika,” ndipo chimachitikadi

Verse 41 — Surah An-Nahl 16:41

“Ndipo omwe adasamuka chifukwa cha Allah (kusiya midzi yawo) pambuyo poponderezedwa (kumeneko,) ndithu tiwakhazika mwaubwino pa dziko lapansi; ndipo malipiro a tsiku la chimaliziro (omwe akuwayembekezera), ngakulu zedi, akadakhala akudziwa (awa oipa)

Verse 42 — Surah An-Nahl 16:42

“(Amene adzapeza zimenezi, ndi) omwe adapirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo

Verse 43 — Surah An-Nahl 16:43

“Ndipo patsogolo pako (aneneri) omwe tidawatuma adalinso amuna, omwe tidawavumbulutsira chivumbulutso. Choncho afunseni eni chikumbumtima (za m’mabuku a Allah akale) ngati inu simukudziwa

Verse 44 — Surah An-Nahl 16:44

“(Tidabwera) ndi zisonyezo zoonekera pamodzi ndi mabuku; ndipo takuvumbulutsira ulaliki kuti uwafotokozere anthu zomwe zavumbulutsidwa kwa iwo kuti aganizire

Verse 45 — Surah An-Nahl 16:45

“Kodi adziika pachitetezo, amene akuchita ndale zoipa, kuti Allah sangawakwilire ndi nthaka, kapena chilango kuwadzera kuchokera komwe sadali kukudziwa (sadali kukuyembekezera)

Verse 46 — Surah An-Nahl 16:46

“Kapena (Allah) kuwalanga mkuyenda kwawo kwa uku ndi uko? Pomwe iwo sangathe kumulepheretsa Allah kuchita chomwe wafuna pa iwo

Verse 47 — Surah An-Nahl 16:47

“Kapena kuwalanga uku ali ndi mantha oyembekezera chilango (pakulanga m’modzim’modzi kufikira onse atatha)? Ndithu Mbuye wanu Ngodekha Ngwachisoni chosatha

Verse 48 — Surah An-Nahl 16:48

“Kodi sadaone chinthu chilichonse (molingalira) m’zimene Allah adalenga zomwe zithuzi zake zimazungulira kudzanjadzanja ndi kumanzere, kulambira Allah uku zili zodzichepetsa kwa Iye? (Nanga iwo osakhulupirira akudzikweza chotani pamaso pa Allah)

Verse 49 — Surah An-Nahl 16:49

“Ndipo zimalambira Allah zonse za kumwamba ndi zapansi, nyama ndi angelo; iwo sadzikuza (pa mapemphero)

Verse 50 — Surah An-Nahl 16:50

“Amaopa Mbuye wawo Yemwe ali pamwamba pawo; ndipo amachita zokhazo zomwe alamulidwa

Verse 51 — Surah An-Nahl 16:51

“Ndipo Allah wanena: “Musadzipangire milungu ina iwiri. Ndithudi, Iye ndi Mulungu Mmodzi. Choncho opani Ine ndekha.”

Verse 52 — Surah An-Nahl 16:52

“Zonse zakumwamba ndi pansi nza Iye, ndipo kumumvera ndi kumugonjera nkwake nthawi zonse. Kodi muopa wina amene sali Allah

Verse 53 — Surah An-Nahl 16:53

“Ndipo mtendere wonse umene muli nawo udachokera kwa Allah (koma inu simuthokoza), ndipo masautso akakukhudzani Iye ndi amene mumamulilira

Verse 54 — Surah An-Nahl 16:54

“Koma akakuchotserani masautso, pompo gulu lina la mwa inu limamphatikiza Mbuye wake (ndi mafano)

Verse 55 — Surah An-Nahl 16:55

“Ncholinga choti akane mtendere umene tawapatsa, choncho sangalalani pang’ono, posachedwapa mudziwa (mapeto a zochita zanu)

Verse 56 — Surah An-Nahl 16:56

“Ndipo gawo la zomwe tawapatsa akuliikira (milungu yawo yabodza) yomwe siizindikira chilichonse. Tallahi, (ndikulumbira Allah,) ndithudi, mudzafunsidwa pa zimene munkapeka

Verse 57 — Surah An-Nahl 16:57

“Ndipo (mwaumbuli) akumuikira Allah ana aakazi (ponena kuti adabereka ana aakazi) Subuhana! (Wayera Allah kuzimenezi!) Ndipo iwo (eni) amadzifunira amene amawakonda (omwe ndi ana achimuna)

Verse 58 — Surah An-Nahl 16:58

“Ndipo mmodzi wawo akauzidwa nkhani ya (kuti wabereka) mwana wamkazi nkhope yake imada, ndipo amadzala ndi madandaulo

Verse 59 — Surah An-Nahl 16:59

“Amadzibisa kwa anthu chifukwa chankhani yoipa imene wauzidwa (nayamba kulingalira): Kodi akhale naye pamodzi ndikuyaluka (pamaso pa anthu), kapena angomkwilira m’dothi (ali moyo)? Mverani! Ndi choipa kwabasi chiweruzo chawo

Verse 60 — Surah An-Nahl 16:60

“Kwa awo amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, ali ndi mbiri yoipa; koma Allah ali ndi mbiri zapamwamba; ndipo Iye Ngwanyonga, Ngwanzeru zakuya

Verse 61 — Surah An-Nahl 16:61

“Ndipo Allah akadakhala akulanga anthu (mwachangu) pa zolakwa zawo, sakadasiya ngakhale nyama imodzi pamwamba pa nthaka; koma akuwachedwetsera (chilangocho) mpaka panthawi yoikidwa; ndipo ikadzadza nthawi yawoyo, sangathe kuichedwetsa ngakhale ola limodzi; ndiponso sangathe kuifulumizitsa (ngakhale ola limodzi)

Verse 62 — Surah An-Nahl 16:62

“Ndipo akumuikira Allah zimene (iwo) akuzida (omwe ndi ana aakazi pomati Allah adabala ana aakazi), ndipo malirime awo akunena bodza kuti iwo adzapeza zabwino (kwa Allah); palibe chikaiko, ndithu Moto ndi wawo, ndipo iwo adzasiidwa (mmenemo)

Verse 63 — Surah An-Nahl 16:63

“Pali Mulungu! Ndithudi tidatumiza (atumiki) kumitundu yomwe idalipo patsogolo pako, koma satana adawakometsera zochita zawo (zoipa ankaziona kuti nzabwino napitiriza kuzichita). Choncho iye (satana) ndi bwenzi wawo lero, (koma pa tsiku la chimaliziro, adzadana naye kwambiri), ndipo iwo adzapata chilango chowawa

Verse 64 — Surah An-Nahl 16:64

“Ndipo sitidakutumizire buku (ili) koma kuti uwafotokozere zomwe akusiyana pa izo ndi kuti (likhale) chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira

Verse 65 — Surah An-Nahl 16:65

“Ndipo Allah watsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo akuipatsa moyo nthaka ndi madziwo (pomeretsa mbewu) pambuyo poti nthakayo idali yakufa; ndithu m’zimenezo muli chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah) kwa anthu amene amamva

Verse 66 — Surah An-Nahl 16:66

“Palibe chikaiko, m’ziweto muli phunziro ndi lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwa izo, (zomwe zimatuluka) pakati pa ndowe ndi magazi, (omwe ndi) mkaka woyera, wabwino wokoma kwa oumwa

Verse 67 — Surah An-Nahl 16:67

“Ndipo kuchokera ku zipatso za tende ndi mphesa, mumakonza zakumwa zoledzeretsa (zomwe nzoletsedwa) ndikupezanso rizq labwino (m’zipatsozo); ndithudi m’zimenezo muli lingaliro kwa anthu oganiza mwanzeru

Verse 68 — Surah An-Nahl 16:68

“Ndipo Mbuye wako adaizindikiritsa njuchi kuti: “Dzikonzere nyumba m’mapiri, m’mitengo, ndi (m’ming’oma) imene (anthu) amakonza.”

Verse 69 — Surah An-Nahl 16:69

““Tsono idya zipatso zamtundu uliwonse ndikuyenda m’njira za Mbuye wako zimene wazifewetsa (kuziyenda).” Chimatuluka m’mimba mwake chakumwa cha utoto wosiyanasiyana (uchi), mwa icho muli kuchilitsa kwa anthu (kumatenda ochuluka), ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu oganiza (zinthu) mwakuya

Verse 70 — Surah An-Nahl 16:70

“Ndipo Allah adakulengani, kenako akukupatsani imfa (nthawi ya moyo wanu ikatha); ndipo mwa inu alipo ena amene akubwezedwa ku moyo wonyozeka (waukalamba wogwa nkumina) kotero kuti asadziwe kanthu pambuyo pakudziwa (zambiri); ndithudi Allah Ngodziwa kwambiri Wokhoza (chilichonse chimene wafuna kuti chichitike)

Verse 71 — Surah An-Nahl 16:71

“Ndipo Allah wapereka zopereka Zake mochuluka kwa ena kuposa ena; ndipo amene apatsidwa mochulukawo sangagawire zopatsidwa zawo omwe manja awo adzanjadzanja apeza (akapolo awo) kuti akhale ofanana pa zopatsidwazo, (nanga bwanji inu mukuti Allah ngofanana ndi akapolo Ake pomwe inu simufuna kufanana ndi akapolo anu?) Nanga kodi mtendere wa Allah akuukana

Verse 72 — Surah An-Nahl 16:72

“Ndiponso Allah adakulengerani akazi a mtundu wanu, ndipo adakupangirani ana ndi zidzukulu kuchokera mwa akazi anuwo; ndipo adakupatsani zinthu zabwinozabwino, kodi akukhulupirira zachabe, ndi kuchikana chisomo cha Allah

Verse 73 — Surah An-Nahl 16:73

“Ndipo akumusiya Allah ndikupembedza zomwe sizingawapezere zopatsa ngakhale pang’ono, zochokera kumwamba ndi pansi ndipo sizikhoza chilichonse

Verse 74 — Surah An-Nahl 16:74

“Choncho, musaponyere mafanizo Allah. Ndithudi Allah akudziwa, pomwe inu simudziwa (chinsinsi cha zinthu)

Verse 75 — Surah An-Nahl 16:75

“Allah akuponya fanizo la (anthu awiri: Wina ndi) kapolo wopatidwa (wokhala pansi pa ulamuliro wa munthu wina); yemwe alibe mphamvu pa chilichonse; ndi (munthu) yemwe tampatsa zabwino zochokera kwa Ife, ndipo iye nkupereka rizqlo mobisa ndi moonekera; kodi angafanane (awiriwa? Nanga bwanji mukufananitsa Allah ndi mafano?) Kuyamikidwa konse nkwa Allah. Koma ambiri aiwo sadziwa (kuyamika Allah)

Verse 76 — Surah An-Nahl 16:76

“Ndipo Allah waponyanso fanizo la anthu (ena) awiri: Mmodzi ndi bubu (wosatha kuyankhula), alibe mphamvu pa chilichonse; ndipo iye ndi mtolo wolemetsa chabe bwana wake; kulikonse kumene wamulunjikitsa, sabwerako ndi chabwino (chifukwa cha umbutuma wake). Kodi iye angafanane ndi yemwe akulamula mwa chilungamo, yemwenso ali pa njira yolunjika

Verse 77 — Surah An-Nahl 16:77

“Ndipo chinsinsi cha (za) kumwamba ndi (za) pansi ncha Allah Yekha, (Iye ndiye amene akudziwa zochitika m’menemo, osati wina wake). Ndipo kuchitika kwa Qiyâma kuli ngati kuphetira kwa diso, kapena kufulumilirapo. Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse

Verse 78 — Surah An-Nahl 16:78

“Ndipo Allah adakutulutsani m’mimba mwa amayi anu pomwe simudali kudziwa chilichonse; ndipo adakupatsani kumva, kuona ndi mitima kuti muthokoze

Verse 79 — Surah An-Nahl 16:79

“Kodi saona mbalame mu mlengalenga zikugonjera (Allah)? Palibe amene akuzigwira (kuti zisagwe) koma Allah Yekha. Ndithudi m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

Verse 80 — Surah An-Nahl 16:80

“Ndipo Allah adakuikirani nyumba zanu kuti zikhale mokhala (mwanu), ndiponso adakupangirani zikopa za ziweto (kukhala zotheka kuzikonza) kukhala nyumba, zomwe mumaziona kuti nzopepuka kuzitenga panthawi Ya ulendo wanu ndi panthawi ya kukhazikika kwanu (pamalo); ndipo kuchokera ku bweya wake wautaliutali ndi bweya wake wa manyunyu (ung’onoung’ono), ndi tsitsi lake (la ziwetozo,) mumakonza ziwiya (zovala) zosangalatsa, kwa kanthawi

Verse 81 — Surah An-Nahl 16:81

“Ndipo mwa zina zomwe Allah adapanga, adakupangirani zodzetsa mthunzi; ndipo adakupangirani mokhala kumapiri (monga mapanga akuluakulu). Adakupangiraninso nsalu (zathonje ndi ubweya) zokutetezani ku kutentha (ndi kuzizira), ndiponso (adakupangirani) zovala (za chitsulo) zokutetezani pankhondo zanu. Umo ndi momwe akukukwaniritsirani chisomo Chake kuti mugonjere (Iye)

Verse 82 — Surah An-Nahl 16:82

“Koma ngati anyoza, basi palibe udindo wina pa iwe koma kufikitsa uthenga womveka (popanda kubisapo kalikonse)

Verse 83 — Surah An-Nahl 16:83

“Akuchidziwa chisomo cha Allah; koma akuchikana, ndipo ambiri a iwo ngosakhulupirira

Verse 84 — Surah An-Nahl 16:84

“Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse; kenako sikudzaloledwa, kwa amene sadakhulupirire, (kupereka madandaulo) ndipo iwo sadzauzidwa kuti afunefune chiyanjo cha Allah (koma chilango basi)

Verse 85 — Surah An-Nahl 16:85

“Ndipo amene achita zoipa akadzachiona chilango (ndikuyamba kudandaula ndi kulira), sichidzachepetsedwa kwa iwo (chilangocho), ndipo sadzapatsidwa mwayi wina

Verse 86 — Surah An-Nahl 16:86

“Ndipo amene ankam’phatikiza Allah akadzawaona aphatikizi awowo adzati: “Mbuye wathu! Awa ndiaphatikizi athu omwe tidali kuwapembedza m’malo mwa Inu.” Ndipo (aphatikiziwo akadzamva mawu awa) adzawaponyera mawu awo (nkunena kuti): “Ndithu inu ndi abodza.”

Verse 87 — Surah An-Nahl 16:87

“Ndipo tsiku limenelo onse adzadzitula kwa Allah; ndipo zidzawataika zomwe adali kuzipeka

Verse 88 — Surah An-Nahl 16:88

“Tsono amene sadakhulupirire ndi kumaletsa anthu kunjira ya Allah tidzawaonjezera chilango pamwamba pa chilango chifukwa chakuononga kwawo

Verse 89 — Surah An-Nahl 16:89

“Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse zochokera mwa iwo omwe adzawachitira umboni (pa zomwe zinkachitika ndi iwo); ndipo tidzakubweretsa iwe kukhala mboni pa awa (anthu ako); ndiponso takuvumbulutsira buku ili lomwe likufotokoza za chinthu chilichonse lomwenso ndi chiongoko ndi mtendere ndiponso ndinkhani yosangalatsa kwa ogonjera (Allah)

Verse 90 — Surah An-Nahl 16:90

“Ndithudi, Allah akulamula (kuchita) chilungamo, ndikuchita zabwino, ndi kupatsa achinansi, ndipo akuletsa zauve ndi zoipa ndi kupyola malire; akukulangizani kuti muzindikire ndi kukumbukira

Verse 91 — Surah An-Nahl 16:91

“Ndipo kwaniritsani lonjezo (limene mukupereka mdzina) la Allah pamene mulonjeza, ndipo musaswe malonjezowo pambuyo pakuwalimbikitsa; pomwe mwasankha Allah kukhala mboni yanu; ndithu Allah akudziwa (zonse) zimene mukuchita

Verse 92 — Surah An-Nahl 16:92

“Ndipo musakhale monga mkazi yemwe adakhulula ulusi wake pambuyo pouluka mwamphamvu, mukukuchita kulumbira kwanu pakati panu kukhala kwa chinyengo, chifukwa chakuti gulu la mtundu wina nlochuluka kwambiri kuposa gulu la mtundu wina (powasiya omwe mudalonjezana nawo chifukwa chakuwaona kuchepa, ndi kukagwirizana ndi omwe simudalonjezane nawo chifukwa chakuwaona kuchuluka); ndithu Allah akukuyesani mayeso pa njira yotere; ndipo ndithu pa tsiku la Qiyâma adzakufotokozerani za zomwe mudali kusiyana

Verse 93 — Surah An-Nahl 16:93

“Ndipo Allah akadafuna, ndithu akadakuchitani kukhala gulu limodzi, (nonsenu mukadamumvera monga momwe adawachitira angelo, koma adakupatsani ufulu kuti muchite chimene mufuna); komatu amamulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo amamuongola wamfuna; ndipo, ndithu mudzafunsidwa pa zomwe munkachita

Verse 94 — Surah An-Nahl 16:94

“Ndipo musakuchite kulumbira kwanu kukhala njira yonyengelerana pakati panu, kuopera kuti mwendo ungatelere (pa njira yolungama nkukagwera ku Moto) pambuyo pokhazikika mwendowo (pa njirapo) ndi kukazilawa zoipa chifukwa chakutsekereza kwanu (anthu) ku njira ya Allah, ndipo nkupeza chilango chachikulu (tsiku lachimaliziro)

Verse 95 — Surah An-Nahl 16:95

“Ndipo musagulitse mapangano a Allah ndi mtengo wochepa (wa zomwe mukupeza pano pa dziko lapansi). Chimene chili kwa Allah, ndicho chabwino kwa inu ngati mukudziwa

Verse 96 — Surah An-Nahl 16:96

“Zomwe mulinazo nzakutha ndipo zili kwa Allah ndizo zosatha. Ndithudi Ife tidzawapatsa malipiro (aakulu zedi) amene adapirira oposera zabwino zimene ankachita

Verse 97 — Surah An-Nahl 16:97

“Amene akuchita zabwino, wamwamuna kapena wamkazi uku ali wokhulupirira timkhazika ndi moyo wabwino (pano pa dziko, ndi tsiku la Qiyâma) tidzawalipira malipiro awo mochuluka kwambiri chifukwa cha zabwino zomwe ankachita

Verse 98 — Surah An-Nahl 16:98

“Ndipo ukafuna kuwerenga Qur’an dzitchinjirize ndi Allah kwa satana wopirikitsidwa (ponena kuti Awudhu Billahi mina Shaitwani Rajim)

Verse 99 — Surah An-Nahl 16:99

“Ndithu iye (satana) alibe mphamvu pa amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo

Verse 100 — Surah An-Nahl 16:100

“Ndithudi mphamvu zake zili pa amene akumusankha (amulola) kukhala bwenzi lawo (mlangizi wawo) ndiponso ndi omwe akumphatikiza iye (ndi Allah)

Verse 101 — Surah An-Nahl 16:101

“Ndipo tikasintha Ayah (ndime) ndikubwera ndi Ina pamalopo, pomwe Allah akudziwa zimene akuvumbulutsa, akunena: “Ndithu iwe ndiwe wopeka.” Koma ambiri a iwo sadziwa (chilichonse)

Verse 102 — Surah An-Nahl 16:102

“Nena: “Mzimu woyera (Gabriel) waitsitsa (Qur’an) kuchokera kwa Mbuye wako mwachoonadi kuti awalimbikitse nayo amene akhulupirira ndi kuti ikhale chiongoko ndi nkhani yabwino kwa amene alowa m’Chisilamu (amene agonjera Allah)

Verse 103 — Surah An-Nahl 16:103

“Ndithu tikudziwa kuti iwo akunena: “Pali munthu amene akumphunzitsa.” (Koma) chiyankhulo cha amene akumganizirayo nchachilendo, ndipo ichi (chiyankhulo cha Qur’an) ndi chiyankhulo cha Chiarabu chomveka

Verse 104 — Surah An-Nahl 16:104

“Ndithudi amene sakhulupirira Ayah (ndime) za Allah, Allah sawaongolera (kunjira ya choonadi), choncho adzapeza chilango chowawa

Verse 105 — Surah An-Nahl 16:105

“Ndithudi amene sakhulupirira Ayah (ndime) za Allah ndi amene amapeka bodza (ndi kumalifalitsa kwa anthu) ndipo iwowo ndiwo onama

Verse 106 — Surah An-Nahl 16:106

“Amene akukana Allah, pambuyo pomukhulupirira, (chilango chachikulu chikumuyembekezera), kupatula yemwe adakakamizidwa, uku mtima wake utakhazikika pa chikhulupiliro; koma amene akutsekulira mtima wake kusakhulupirira, mkwiyo wa Allah uli pa iwo (ndipo anthu otere) adzapata chilango chachikulu

Verse 107 — Surah An-Nahl 16:107

“Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adakonda moyo wa dziko lapansi kwambiri kuposa wa pambuyo pa imfa; ndi kutinso Allah saongola anthu osakhulupirira

Verse 108 — Surah An-Nahl 16:108

“Iwo ndi omwe Allah adawadinda m’mitima mwawo, m’makutu mwawo, ndi m’maso mwawo (chifukwa cha kusimbwa kwawo). Ndipo iwo ngonyalanyaza (malamulo a Allah) kwambiri

Verse 109 — Surah An-Nahl 16:109

“Palibe chikaiko chakuti iwo ngotaika kwambiri pa tsiku la chimaliziro

Verse 110 — Surah An-Nahl 16:110

“Ndithudi kenako Mbuye wako, kwa amene adasamuka pambuyo pakusautsidwa (kufikira adanena zosayenera) komanso nkuchita Jihâd ndikupirira (chifukwa cha chipembedzo), ndithu Mbuye wako pambuyo pa zimenezo, Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosantha

Verse 111 — Surah An-Nahl 16:111

“(Akumbutse za) tsiku lomwe mzimu uliwonse udzadza ukudziteteza wokha (wosalabadira za mwana wake, mkazi wake ndi abale ake), ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa molingana ndi zochita zake zimene unkachita, ndipo iwo sadzachitidwa chinyengo (pochepetsedwa mphoto yawo yoti alandire)

Verse 112 — Surah An-Nahl 16:112

“Ndipo Allah waponya fanizo lamudzi womwe udakhala mwa mtendere mokhazikika, rizq lake (madalitso) linkaudzera mochuluka kuchokera malo aliwonse; koma (mudziwo) udakana mtendere wa Allah (pakusathokoza); choncho Allah adaulawitsa chovala cha njala ndi mantha chifukwa cha (zoipa) zomwe (anthu ake) adali kuchita

Verse 113 — Surah An-Nahl 16:113

“Ndipo adawadzera mtumiki wochokera mwa iwo, koma adamtsutsa; choncho chilango chidawafika uku ali odzichitira okha zoipa

Verse 114 — Surah An-Nahl 16:114

“Choncho idyani zimene Allah wakupatsani zomwe zili zahalali, zabwino; ndipo yamikani mtendere wa Allah ngatidi mukupembedza Iye

Verse 115 — Surah An-Nahl 16:115

“Ndithu wakuletsani (kudya) zakufa zokha, magazi (liwende), nyama ya nkhumba ndi chimene chazingidwa posatchula dzina la Allah. Koma amene wasimidwa (nadya choletsedwa) mosafuna kapena kupyoza muyeso (Allah amkhululukira), ndithudi Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni

Verse 116 — Surah An-Nahl 16:116

“Ndipo musanene chifukwa chabodza lomwe malirime anu akunena (kuti) “Ichi nchololedwa; ichi ncholetsedwa; (popanda umboni).” Kuopera kuti mungampekere bodza Allah. Ndithu amene akupekera bodza Allah, sangapambane

Verse 117 — Surah An-Nahl 16:117

“Ndichisangalalo chochepa (cha m’dziko lapansi chimene chikuwachititsa zimenezo); ndipo iwo adzapata chilango chowawa

Verse 118 — Surah An-Nahl 16:118

“Ndipo kwa Ayuda tidawaletsa kale zimene takusimbira. Ndipo sitidawachitire chinyengo (pakuwaletsa zimenezo), koma iwo okha adali kudzichitira chinyengo

Verse 119 — Surah An-Nahl 16:119

“Kenako ndithu Mbuye wako, kwa amene achita zoipa mwaumbuli ndipo nkulapa pambuyo pazimenezo nachita zabwino, ndithudi Mbuye wako pambuyo pa zimenezo Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

Verse 120 — Surah An-Nahl 16:120

“Ndithu Ibrahim adali mtsogoleri (chitsanzo chabwino kwa anthu), womvera Allah, wopendekera ku choonadi ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano)

Verse 121 — Surah An-Nahl 16:121

“(Adali) wothokoza mtendere Wake (Allah); adamsankha ndipo adamuongolera ku njira yolunjika

Verse 122 — Surah An-Nahl 16:122

“Ndipo tidampatsa zabwino padziko lapansi, ndipo ndithudi, iye pa tsiku la chimaliziro adzakhala m’gulu la anthu abwino

Verse 123 — Surah An-Nahl 16:123

“Kenako takuvumbulutsira (iwe Muhammad{s.a.w} mawu) akuti: “Tsatira njira (chipembedzo) ya Ibrahim (yemwe adali) wokwanira mkulungama, ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano.)”

Verse 124 — Surah An-Nahl 16:124

“Ndithudi Sabata idaikidwa kwa amene adatsutsana pa za iyo (Sabatayo); ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zomwe adali kusiyana

Verse 125 — Surah An-Nahl 16:125

“Itanira (anthu) ku njira ya Mbuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino; ndipo tsutsana nawo mkutsutsana kwabwino (osati motukwanana kapena monyozana). Ndithu Mbuye wako Iye Ngodziwa kwambiri za amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye Ngodziwa kwambiri za amene aongoka

Verse 126 — Surah An-Nahl 16:126

“Ndipo ngati mukubwezera (choipa chimene mwachitiridwa), bwezerani cholingana ndi chimene mwachitiridwacho, koma ngati mutapirira (posiya kubwezera), ndithu kutero ndi ubwino kwa opirira

Verse 127 — Surah An-Nahl 16:127

“Ndipo pirira. Kupirira kwakoko kusakhale pa china chake koma Allah basi. Ndipo usadandaule chifukwa cha iwo, (iwo akudzisokeretsa okha). Ndipo usakhale wobanika chifukwa cha chiwembu chomwe akuchita

Verse 128 — Surah An-Nahl 16:128

“Ndithu Allah ali pamodzi ndi amene akumuopa ndi amenenso akuchita zabwino