Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 18 - Al-Kahf
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Kahf 18:1
“Kutamandidwa konse kwabwino nkwa Allah, Yemwe adavumbulutsa kwa kapolo Wake (Mtumiki Muhammad{s.a.w}), buku (ili lopatulika), ndipo sadalikhotetse (koma m’menemo muli zoona zokhazokha)
Verse 2 — Surah Al-Kahf 18:2
“(Walichita kukhala) loongoka kuti lichenjeze anthu za chilango chokhwima chochokera kwa Iye (Allah), ndikuti liwasangalatse okhulupirira omwe akuchita zabwino, kuti adzapeza malipiro abwino
Verse 3 — Surah Al-Kahf 18:3
“Adzakhalamo (mumtendere wosathawo) muyaya
Verse 4 — Surah Al-Kahf 18:4
“Ndikuti liwachenjeze amene akunena (kuti): “Allah wadzipangira Mwana.”
Verse 5 — Surah Al-Kahf 18:5
“Iwo pabodza lawolo alibe kuzindikira chinthu chilichonse chanzeru ngakhale makolo awo. Lakula kwabasi liwu lomwe likutuluka mkamwa mwawo. Sanena china koma bodza basi
Verse 6 — Surah Al-Kahf 18:6
“Mwina udziwononga wekha pakuwadandaulira chikhalidwe chawo kuti sakhulupirira nkhani iyi. (Iyayi! Usakhale wodandaula ndi zimenezo)
Verse 7 — Surah Al-Kahf 18:7
“Ndithu Ife tazichita zomwe zili pamwamba pa nthaka kukhala zokometsera nthakayo, ndikuti (mwa izo) tiwayese mayeso kuti (ndani) mwa iwo ali wochita zabwino kwambiri
Verse 8 — Surah Al-Kahf 18:8
“Ndipo ndithu Ife ndi Amene tidzazichita zomwe zili pamenepo kukhala monga nthaka yoguga (yopanda mmera)
Verse 9 — Surah Al-Kahf 18:9
“Kodi ukuganiza kuti eni phanga ndi eni nkhani zomwe zidalembedwa m’mabuku, adali mwa zizindikiro zathu zododometsa kwambiri? (Iyayi, zilipo zododometsa kwabasi kuposa zimenezo)
Verse 10 — Surah Al-Kahf 18:10
“Pamene anyamata adathawira kuphanga nati: “Mbuye wathu! Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu, ndipo tikonzereni chiongoko m’zochita zathu.”
Verse 11 — Surah Al-Kahf 18:11
“Tidagonthetsa makutu awo, (ndikugona kosamva nako kanthu) kwa zaka zambirimbiri m’phanga
Verse 12 — Surah Al-Kahf 18:12
“Kenako tidawautsa, kuti tiwayese (kuti) ndani mwa magulu awiriwa amadziwa kuwerengera nthawi imene (anyamatawa) adakhala (m’phangamo)
Verse 13 — Surah Al-Kahf 18:13
“Ife tikusimbira (iwe mtumiki{s.a.w}) nkhani zawo mwachoonadi; ndithu iwo adali anyamata amene adakhulupirira Mbuye wawo, ndipo tidawaonjezera chiongoko
Verse 14 — Surah Al-Kahf 18:14
“Ndipo tidalimbikitsa mitima yawo pa chikhulupiliro pamene adaimilira (pamaso pa mfumu yawo yosakhulupirira) ndikunena: “Mbuye wathu ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka. Sitipembedza mulungu wina m’malo mwa Iye. Ngati titatero ndiye kuti tanena zoipa zopyola muyeso
Verse 15 — Surah Al-Kahf 18:15
“Awa anthu athu adzipangira milungu ina kusiya Allah, nanga bwanji sakubweretsa pa za iyo (milunguyo) umboni woonekera (wosonyeza kuti iyo ndi milungudi)? Kodi ndani wachinyengo wamkulu woposa yemwe akupekera bodza Allah
Verse 16 — Surah Al-Kahf 18:16
“(Adauzana pakati pawo): “Ndipo ngati muwapatuka ndizimene akuzipembedza kusiya Allah, thawirani kuphanga; Mbuye wanu akutambasulirani chifundo Chake ndikukufewetserani zinthu zanu zonse.”
Verse 17 — Surah Al-Kahf 18:17
“(Zidali tere) ukadakhala ukuliona dzuwa pamene linkatuluka (ndikuyamba kukwera), ukadaliona likulambalala kumbali kwa phanga lawo mbali yakudzanjadzanja, ndipo pamene linkalowa limawadutsa mbali yakumanzere (popanda kuwalunjika) pomwe iwo adali pamtetete mmenemo. Zimenezo ndi zina mwa zisonyezo za Allah (zosonyeza kukhoza Kwake). Amene Allah wamuongola iyeyo ndiye woongoka; ndipo amene wamulekelera kuti asokere, simungampezere mtetezi kapena muongoli
Verse 18 — Surah Al-Kahf 18:18
“Ndipo ungawaganizire kuti ali maso pomwe iwo ali mtulo, uku tikuwatembenuzira mbali yakumanja ndi yakumanzere (kuti nthaka isadye matupi awo), ukunso galu wawo atatambasula miyendo yake (yakutsogolo) pakhomo. Ngati ukadawaona ukadatembenuka kuwathawa; ndipo ndithu ukadadzadzidwa mantha ndi iwo
Verse 19 — Surah Al-Kahf 18:19
“Ndipo momwemonso tidawautsa kuti afunsane pakati pawo (zanthawi imene akhala ali chigonere). Adanena wonena mwa iwo: “Kodi mwakhala nthawi yotani muli mtulo?” Adati: “Takhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku.” (Ena) adati: “Mbuye wanu akudziwa kwambiri za nyengo imene mwakhala. Choncho mtumeni mmodzi wa inu ndindalama zanuzi za siliva kumudzi ndipo akayang’ane chakudya chake nchotani chomwe chili choyera bwino, ndikubwerera nacho chakudyacho; koma izi akachite mochenjera ndipo asamzindikiritse aliyense za inu.”
Verse 20 — Surah Al-Kahf 18:20
““Ndithu iwo akakudziwani (pamene mulipa), akugendani ndi miyala; apo ai akubwezerani ku chipeinbedzo chawo (chopotoka), zikatero ndiye kuti simudzapambananso mpaka kalekale.”
Verse 21 — Surah Al-Kahf 18:21
“(Koma anthu anazindikira pamene adaona ndalama yakale), momwemonso tidawazindikiritsa (kwa anthu) kuti adziwe kuti lonjezo la Allah (loukitsa ku imfa zolengedwa) nloona, ndikuti nthawi ya chimaliziro njosakaikitsa, (ndipo kumbukani) pamene adakangana pakati pawo pa chinthu chaochi, ena adati: “Mangani chomanga pa iwo (kuti anthu asamadze kudzawasuzumira), Mbuye wawo za iwo akudziwa bwino, koma amene adapambana paganizo lawolo adanena: “Ndithu ife timanga Msikiti wa iwowa (pa phanga lawoli).”
Verse 22 — Surah Al-Kahf 18:22
“(Ena) akhala akunena (kuti) adali anthu atatu, wachinayi ndi galu wawo; ndipo (ena) akuti adali asanu, wachisanu ndichimodzi ndigalu wawo. (Akunena) mwakungoganizira chabe zomwe sakuzidziwa; ndipo (ena) akuti adali asanu ndi awiri, ndipo wachisanu ndi chitatu ndi galu wawo. Nena: “Mbuye wanga ndiye akudziwa bwinobwino za chiwerengero chawo. Palibe amene akudziwa (za iwo) koma ndi ochepa chabe.” Choncho usatsutsane nawo za iwo, kupatula kutsutsana kwa pa zinthu zodziwika, ndipo usamfunse aliyense mwa iwo za iwo
Verse 23 — Surah Al-Kahf 18:23
“Ndipo usanene ngakhale pang’ono zachilichonse kuti: “Ndichita mawa.”
Verse 24 — Surah Al-Kahf 18:24
““Koma (utsogoze liwu lakuti): Insha Allah, (Allah akafuna!)” Ndipo mukumbuke Mbuye wako ukaiwala ponena kuti: “Mwina Mbuye wanga anditsogolera pa njira yapafupi pachiongoko kuposa iyi.”
Verse 25 — Surah Al-Kahf 18:25
“Ndipo adakhala m’phanga lawolo (ali mtulo) zaka zikwi zitatu ndikuonjezera zisanu ndi zinayi
Verse 26 — Surah Al-Kahf 18:26
“Nena: “Allah akudziwa bwinobwino nyengo imene (iwo) adakhala; zobisika za kumwamba ndi za pansi nza Iye (Allah basi); taona Allah kuonetsetsa! Taona Allah kumvetsetsa! (Allah Ngoona chilichonse, ndipo Ngwakumva chilichonse). Ndipo iwo alibe mtetezi popanda Iye (Allah); ndipo Iye sagawira aliyense udindo Wake wakulamula
Verse 27 — Surah Al-Kahf 18:27
“Ndipo werenga zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe za m’buku la Mbuye wako, palibe amene angathe kusintha mau Ake, ndipo nawe sungapeze potsamira ndi pothawira (kuti Allah asakupeze)
Verse 28 — Surah Al-Kahf 18:28
“Ndipo dzikakamize kukhala pamodzi ndi amene akupempha Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo uku akufunafuna nkhope Yake (chiyanjo Chake), ndipo maso ako asachoke pa iwo ndi (kuyang’ana ena) ncholinga chofuna zokongoletsa za moyo wa dziko lapansi; ndipo usamumvere amene mtima wake tauiwalitsa kutikumbukira ndikumangotsatira zilakolako zake, ndipo zinthu zake nkukhala zotaika (zosalongosoka)
Verse 29 — Surah Al-Kahf 18:29
“Ndipo nena (kwa osakhulupirirawo, kuti): “Ichi ndi choonadi chimene chachokera kwa Mbuye wanu.” Choncho amene afuna, akhulupirire; ndipo amene afuna (kusachikhulupirira) asakhulupirire. Ndithu achinyengo tawakonzera Moto, womwe mipanda yake ikawazinga. Ndipo akakapempha chithandizo (chifukwa cha ludzu loopsya lomwe likawapeza), akathandizidwa popatsidwa madzi (otentha kwambiri) monga madzi a chitsulo chosungunuka, omwe adzasupula nkhope zawo. Taona kuipa chakumwa! ndi kuipa malo wotsamira
Verse 30 — Surah Al-Kahf 18:30
“Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, (tidzawalipira pa ubwino wawowo), ndithu Ife sitisokoneza malipiro a amene wagwira ntchito yabwino
Verse 31 — Surah Al-Kahf 18:31
“Iwo adzapeza minda yamuyaya; yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; m’menemo adzawakongoletsa powaveka zibangiri za golide, ndipo adzavala nsalu zobiriwira; zasilika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atatsamira makhushoni mmenemo. Taonani kukhala bwino malipiro! Ndi pamalo potsamira pokongola (popeza mpumulo wabwino)
Verse 32 — Surah Al-Kahf 18:32
“Ndipo apatse fanizo la anthu awiri mmodzi wa iwo tidampangira minda iwiri ya mphesa ndi kuizunguliza ndi mitengo ya kanjedza; ndipo pakati pa iyo tidaikapo mbewu (zina)
Verse 33 — Surah Al-Kahf 18:33
“Minda yonse iwiriyi idapatsa zipatso zake ndipo siidapungule chilichonse mzipatso zake. Ndipo pakati pake tidapititsapo mitsinje
Verse 34 — Surah Al-Kahf 18:34
“Ndipo iye adali ndi chuma (china) nati kwa mnzakeyo mokambirana naye: “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe, (ndilinso) ndi mphamvu zambiri chifukwa cha onditsatira (omwe ndili nawo).”
Verse 35 — Surah Al-Kahf 18:35
“Ndipo adalowa m’munda mwake uku akudzichitira yekha zoipa. Adati: “Sindiganiza ngakhale mpang’ono pomwe kuti (munda) uwu udzaonongeka.”
Verse 36 — Surah Al-Kahf 18:36
““Ndiponso sindiganiza kuti Qiyâma (chimaliziro) idzachitikadi. Ngati (itapezekadi Kiyamayo), ine nkubwezedwa kwa Mbuye wanga, ndithu ndikapeza malo abwino wobwererako kuposa awa. (Monga momwe ndapezera mwayi kuno, ukonso ndikapeza, ngati Kiyamayo ilikodi).”
Verse 37 — Surah Al-Kahf 18:37
“Mnzake adanena kwa iye mokambirana naye: “Kodi ukumukana yemwe adakulenga ndi dongo, kenako ndi dontho lamadzi a umuna ndiponso adakupanga kukhala munthu wolingana?”
Verse 38 — Surah Al-Kahf 18:38
““Koma ine ndikukhulupirira kuti Iye ndi Mulungu Mbuye wanga, ndipo sindiphatikiza aliyense ndi Mbuye wanga.”
Verse 39 — Surah Al-Kahf 18:39
““Ndipo pamene umalowa m’munda wako ukadanena kuti izi ndi zimene wandifunira Allah, mphamvu sizikadapezeka koma kupyolera mwa Allah (zikadakhala zabwino kwa iwe). Ngati ukundiona ine kuti ndili ndi chuma chochepa ndi ana ochepa kuposa iwe (koma sindisiya kutamanda Allah).”
Verse 40 — Surah Al-Kahf 18:40
““Mwina Mbuye wanga angandipatse zabwino kuposa munda wakowo ndi kuutumizira mliri wachiphaliwali kuchokera kumwamba, ndipo ndikusanduka nthaka yotelera (yoguga).”
Verse 41 — Surah Al-Kahf 18:41
““Kapena madzi ake nkumangophwa kotero kuti sungathe kuwapeza.”
Verse 42 — Surah Al-Kahf 18:42
“Tsono mliri unagwa pa zipatso zakezo (ndikuziononga motheratu), ndipo adayamba kutembenuza manja modandaulira zomwe adaonongera m’menemo; (mindayo) mitengo yake itagwera pansi. Ndipo adati: “Kalanga ine! Ndikadapanda kumphatikiza Mbuye wanga ndi aliyense (zoterezi sizikadachitika.)”
Verse 43 — Surah Al-Kahf 18:43
“Ndipo sadakhale ndi anthu omthangata pamene Allah adamtaya, ngakhale iye mwini sadadzithandize
Verse 44 — Surah Al-Kahf 18:44
“Pamalo potere chitetezo chimakhala cha Allah Yekha Woona. Iye Ngolipira bwino, ndiponso Wabwino (pakudza) ndi malekezero abwino
Verse 45 — Surah Al-Kahf 18:45
“Ndipo apatse fanizo la moyo wadziko lapansi, uli ngati madzi amene tikutsitsa kuchokera kumitambo kenako (madziwo) amasakanikirana ndi mmera wa m’nthaka (ndikuyamba kumera mokongola), kenako (mmerawo) nkukhala masamba ouma odukaduka omwe mphepo ikuwaulutsa uku ndi uku. Ndipo Allah ali ndi mphamvu pachilichonse
Verse 46 — Surah Al-Kahf 18:46
“Chuma ndi ana ndizokometsera za moyo wa dziko lapansi, koma ntchito zabwino zopitirira ndizo zabwino kwa Mbuye wako, monga mphoto ndi chiyembekezo chabwino
Verse 47 — Surah Al-Kahf 18:47
“Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzayendetsa mapiri (powaulutsa ngati ubweya mu mlengalenga), ndipo udzaiona nthaka ili tetetee, (itatambasuka yosakhwinyata ndi mapiri kapena zitunda), ndipo tidzawasonkhanitsa (tsiku limenelo), ndipo sitidzasiya aliyense mwa iwo (oyamba ndi omaliza)
Verse 48 — Surah Al-Kahf 18:48
“Ndipo adzabwera nawo kwa Mbuye wako atandanda m’mizere (ndikuuzidwa): “Ndithu mwatidzera monga tidakulengerani pachiyambi (opanda nsapato, amaliseche ndiponso opanda chilichonse chuma ndi ana). Koma mumaganiza kuti sitikuikirani lonjezo (ili louka ku imfa ndi kuweruzidwa).”
Verse 49 — Surah Al-Kahf 18:49
“Ndipo kaundula adzaikidwa (pamaso pawo), ndipo udzaaona oipa ali oopa chifukwa cha zomwe zili m’menemo, ndipo adzanena: “Kalanga ife taonongeka! Ngotani kaundula uyu, sasiya chaching’ono ngakhale chachikulu, koma zonse kuzilemba.” Ndipo adzapeza zonse zimene adazichita zitalembedwa m’menemo. Ndipo Mbuye wako sapondereza aliyense (pomusenzetsa zomwe sizake, kapena kumchitira zomwe sizikumuyenera)
Verse 50 — Surah Al-Kahf 18:50
“Ndipo (kumbuka) pamene tidawauza angelo: “Mchitireni sijida Adam (mugwadireni momulemekeza).” Onse adachitadi sijida kupatula Iblis. Iye adali mmodzi wa ziwanda, ndipo adatuluka m’chilamulo cha Mbuye wake. Kodi iye ndi mbumba yake mukuwalola kukhala abwenzi (anu) kusiya Ine, pomwe iwo ndiadani anu? Taonani kuipa kusintha kwa anthu oipa
Verse 51 — Surah Al-Kahf 18:51
“Sindidawachite (iwo) kukhala mboni nkulenga kwa thambo ndi nthaka, ngakhale kuwalenga kwawo ndipo sindidawalole osokeretsa kukhala athandizi (Anga)
Verse 52 — Surah Al-Kahf 18:52
“Ndipo (kumbukani) tsiku lomwe (Allah) adzanena: “Aitaneni aja omwe munkandiphatikiza nawo omwe munkati (ndi milungu inzanga).” Choncho, adzaiitana koma siidzawayankha; ndipo tidzaika chionongeko pakati pawo (ndipo sadzakumananso)
Verse 53 — Surah Al-Kahf 18:53
“Ndipo woipa adzauona moto (panthawi imeneyo) ndikutsimikiza kuti iwo alowa m’menemo. Ndipo sadzapeza pouzembera
Verse 54 — Surah Al-Kahf 18:54
“Ndipo ndithu tawafotokozera anthu mwatsatanetsatane m’Qur’aniyi fanizo la mtundu uliwonse; koma munthu wapambana chinthu chilichonse pa makani
Verse 55 — Surah Al-Kahf 18:55
“Ndipo palibe chimene chaletsa anthu kukhulupirira (tsopano) pamene chiongoko choonadi chawadzera ndikupempha chikhululuko kwa Mbuye wawo, koma akuyembekezera kuti chiwadzere chikhalidwe cha anthu oyamba, kapena chiwadzere chilango masomphenya
Verse 56 — Surah Al-Kahf 18:56
“Ndiponso sitituma atumiki (ndi cholinga choti adzetse chilango), koma kuti akhale onena nkhani zabwino ndi ochenjeza. Ndipo amene sadakhulupirire, akuchita makani ndi chabodza kuti kupyolera m’chabodzacho achotse choonadi, ndipo Ayah Zanga ndi zomwe achenjezedwa nazo, akuzichitira chipongwe
Verse 57 — Surah Al-Kahf 18:57
“Ndindani woipitsitsa kwabasi woposa yemwe akukumbutsidwa ndi Ayah za Mbuye wake, koma iye nkuzinyoza, ndipo nkuiwala (zoipa) zimene manja ake adatsogoza? Ndithu Ife taika m’mitima mwawo zitsekelero kuti asazizindikire. Ndiponso m’makutu mwawo mwalemedwa ndi ugonthi. Ndipo ukawaitanira kuchiongoko (choonadi), salola kuongoka ngakhale pang’ono
Verse 58 — Surah Al-Kahf 18:58
“Ndipo Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri mwini chifundo. Ndipo akadawathira m’dzanja pa zoipa zomwe akhala akuchita, ndiye kuti ndithu akadawapatsa chilango mwachangu; koma iwo ali nalo lonjezo ndipo sadzapeza pothawira paliponse ndikulipewa
Verse 59 — Surah Al-Kahf 18:59
“Ndipo imeneyo ndi midzi tidawaononga (okhalamo) pamene adadzichitira zoipa; ndipo tidawaikira lonjezo la nthawi yoikidwa la kuonongeka kwawo
Verse 60 — Surah Al-Kahf 18:60
“Ndipo (kumbukani) pamene Mûsa adanena kwa mnyamata wake (Yusha’ Ibn Nun): “Ndipitiriza kuyenda kufikira ndikafike pamajiga pa nyanja ziwiri, kapena ndizingoyenda zaka ndi zaka (kufikira nditakumana naye amene ndikumfunayo).”
Verse 61 — Surah Al-Kahf 18:61
“Choncho pamene adafika pamajiga (pa nyanja ziwirizo) adaiwala nsomba yawo yomwe idatenga njira yake kunka m’nyanja ngati una (Mûsa adaiwala kumfunsa mnyamata wake za nsombayo; naye mnyamata adaiwala kumfotokozera Mûsa zomwe zidachitika ndi nsoinbayo)
Verse 62 — Surah Al-Kahf 18:62
“Pamene adapita patsogolo, adauza mnyamata wake, (kuti): “Tipatseni chakudya chathu chammawa; ndithu pa ulendo wathuwu takumana ndi zotopetsa.”
Verse 63 — Surah Al-Kahf 18:63
“(Mnyamata) adati: “Kodi mwaona pamene tidapumula paja, pathanthwe ndipomwe ndidaiwala (kuti ndikuuzeni) za nsombayo ndipo palibe wandiiwalitsa koma satana basi, kuti ndisaikumbukire. Iyo idatenga njira yake kunka m’nyanja, mododometsa.”
Verse 64 — Surah Al-Kahf 18:64
“(Mûsa) adati : “Pamenepo ndi pomwe timafuna.” Choncho adabwerera m’mbuyo potsatira njira yawo (yomweyo)
Verse 65 — Surah Al-Kahf 18:65
“Ndipo adampeza kapolo (Khidwiri) yemwe ndi m’modzi wa akapolo athu amene tidampatsa chifundo chochokera kwa Ife, (yemwenso) tidamphunzitsa maphunziro ambiri kuchokera kwa Ife
Verse 66 — Surah Al-Kahf 18:66
“Mûsa adati kwa iye: “Kodi ndingakutsate kuti undiphunzitse chiongoko chomwe waphunzitsidwa?”
Verse 67 — Surah Al-Kahf 18:67
“Adati: “Ndithu iwe siutha kupirira nane! (Uwona zomwe sungathe kupirira nazo).”
Verse 68 — Surah Al-Kahf 18:68
““Kodi ungapirire bwanji ndi zinthu zomwe sukuzidziwa chinsinsi chake?”
Verse 69 — Surah Al-Kahf 18:69
“(Mûsa) adati: “Ngati Allah afuna, undipeza ndili wopirira; ndipo sindinyoza lamulo lako.”
Verse 70 — Surah Al-Kahf 18:70
“Adati: “Ngati unditsata usandifunse za chilichonse (chimene uchione) kufikira ine nditakuuza.”
Verse 71 — Surah Al-Kahf 18:71
“Choncho onse awiri adanyamuka kufikira pamene adakakwera m’chombo adachiboola. (Mûsa) adati: “Kodi wachiboola kuti uwamize ali m’menemo? Ndithu wachita chinthu chachikulu choipa.”
Verse 72 — Surah Al-Kahf 18:72
“Adati: “Kodi sindidanene kuti iwe sutha kupirira nane?”
Verse 73 — Surah Al-Kahf 18:73
“(Mûsa) adati: “Usandidzudzule chifukwa chakuiwala kwanga, ndipo usandipatse zovuta kwambiri pa khumbo langali (lofuna kukutsata).”
Verse 74 — Surah Al-Kahf 18:74
“Ndipo adanyamuka; mpaka pomwe adakumana ndi mnyamata wochepa, ndipo (mneneri Khidir) adamupha. Mûsa adati: “Ha! Wapha munthu wopanda cholakwa, pomwe sadaphe munthu mnzake? Ndithu wachita chinthu choipitsitsa.”
Verse 75 — Surah Al-Kahf 18:75
“۞ Adati: “Kodi sindidakuuze (kuti) ndithu iwe sutha kupirira nane?”
Verse 76 — Surah Al-Kahf 18:76
“(Mûsa) adati: “Ngati ndikufunsanso chilichonse pambuyo pa ichi, usandilole kutsagana nawe. Ndiye kuti wakwaniritsa dandaulo lako pa ine.”
Verse 77 — Surah Al-Kahf 18:77
“Choncho adamuka; kufikira pamene adawapeza eni mudzi ndipo adawapempha eni mudziwo chakudya, koma adakana kuwalandira monga alendo. Ndipo adapezamo khoma lili pafupi kugwa, (ndipo Khidhiriyo) adaliimika. (Mûsa) adati: “Ngati ukadafuna, ukadalandira malipiro (pa ntchitoyi kuti tigulire chakudya).”
Verse 78 — Surah Al-Kahf 18:78
“(Khidhiri) adati: “Awa ndiwo malekano pakati pa ine ndi iwe. Tsopano ndikuuza tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”
Verse 79 — Surah Al-Kahf 18:79
““Tsopano chombo chija, chidali cha masikini ogwira ntchito pa nyanja, ndipo ndidafuna kuchiononga (mwadala) chifukwa patsogolo pawo padali mfumu yomwe imatenga chombo chilichonse (chabwino) molanda.”
Verse 80 — Surah Al-Kahf 18:80
““Ndipo mnyamata uja, makolo ake adali okhulupirira, ndipo tidaopera kuti angawachititse zoipa (makolo akewo) ndi za kusakhulupirira (mwa Allah)
Verse 81 — Surah Al-Kahf 18:81
“Choncho tidafuna kuti Mbuye wawo awasinthire ndi wabwino kuposa iye pa kuyera, ndi wachifundo chapafupi (kwa makolo ake.)”
Verse 82 — Surah Al-Kahf 18:82
““Tsopano chipupa chija, chidali cha ana awiri amasiye mu mzindamo; ndipo pansi pake padali chuma chawo (chimene adawasiira bambo wawo) ndipo tate wawo adali munthu wabwino choncho Mbuye wako adafuna kuti akule misinkhu yawo ndipo adzadzitulutsire chuma chawocho; ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo ine sindidachite zinthu zimenezi mwandekha. Limenelo ndilo tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”
Verse 83 — Surah Al-Kahf 18:83
“Ndipo akukufunsa nkhani za Thul-Qarnain. Auze: “Ndikulakatulirani zina mwa nkhani zake.”
Verse 84 — Surah Al-Kahf 18:84
“Ndithu tidampatsa mphamvu zokhalira pa dziko ndikumpatsa njira yopezera chilichonse
Verse 85 — Surah Al-Kahf 18:85
“Choncho adatsata njira
Verse 86 — Surah Al-Kahf 18:86
“Mpaka pomwe adafika kumlowero kwa dzuwa (ku maiko a kuzambwe), adaliona (ngati) likulowa pa dziwe la matope ambiri. Ndipo pompo adapeza anthu; tidati: “E iwe Thul-Qarnain! Alange, kapena achitire zabwino.”
Verse 87 — Surah Al-Kahf 18:87
“Adati: “Koma amene achita zosalungama timulanga; ndipo kenako adzabwezedwa kwa Mbuye wake; ndipo akamukhaulitsa ndi chilango choipa
Verse 88 — Surah Al-Kahf 18:88
“Koma amene akhulupirire ndikuchita ntchito zabwino, apeza mphoto yabwino; ndipo timuuza zomwe zili zofewa m’zinthu zathu.”
Verse 89 — Surah Al-Kahf 18:89
“Kenako adatsata njira
Verse 90 — Surah Al-Kahf 18:90
“Mpaka adafika ku mtulukiro kwa dzuwa (ku maiko akuvuma). Adalipeza (dzuwalo) likuwatulukira anthu omwe sitidawaikire chowatchinga ku ilo
Verse 91 — Surah Al-Kahf 18:91
“Momwemo, tidali kudziwa bwino nkhani zonse zomwe zidali ndi iye
Verse 92 — Surah Al-Kahf 18:92
“Kenako adatsata njira
Verse 93 — Surah Al-Kahf 18:93
“Mpaka pomwe adafika pakatikati pa mapiri awiri adapeza pafupi ndi mapiriwo anthu omwe sikudali kwapafupi kumva chiyankhulo
Verse 94 — Surah Al-Kahf 18:94
“Adati: “E iwe Zul-Qarnain! Ndithu Yaajuju ndi Maajuju akuononga pa dziko. Kodi sikungatheke kuti tikupatse malipiro kuti uike pakati pathu ndi pakati pawo, chotchinga (mpanda)?”
Verse 95 — Surah Al-Kahf 18:95
“(Iye) adati: “Zomwe Mbuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi mphamvu zanu (zonse pantchito imeneyi) ndiika chotchinga cholimba pakati panu ndi pakati pawo.”
Verse 96 — Surah Al-Kahf 18:96
““Ndipatseni zidutswa za zitsulo.” Kufikira pamene adadzaza ndi zitsulozo mpata umene udalipo pakati pa mapiri awiriwo, adati: “Pemelerani (moto).” Mpaka (chitsulocho) chidafiira monga moto, adati: “Ndibweretsereni mtovu wosungunuka ndiuthire pamwamba pake (pa chitsulocho).”
Verse 97 — Surah Al-Kahf 18:97
“Choncho (Yaajuju ndi Maajuju) sadathe kukwera pamwamba pake, ndiponso sadathe kuchiboola
Verse 98 — Surah Al-Kahf 18:98
“(Iye) adati: “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wanga; koma likadzafika lonjezo la Mbuye wanga (kudza kwa Qiyâma), adzachiswanyaswanya; ndipo lonjezo la Mbuye wanga nloona.”
Verse 99 — Surah Al-Kahf 18:99
“Ndipo patsiku limenelo tidzawasiya ena a iwo (oipa) akuchita chipolowe pa ena; ndipo lidzaimbidwa lipenga. Pamenepo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi
Verse 100 — Surah Al-Kahf 18:100
“Ndipo tsiku limenelo, tidzayionetsa poyera Jahannam kwa osakhulupirira
Verse 101 — Surah Al-Kahf 18:101
“(Osakhulupirira) omwe maso awo adali ophimbidwa pakusalabadira ulaliki Wanga, ndipo sadali kutha kumva (zimene akuuzidwa)
Verse 102 — Surah Al-Kahf 18:102
“Kodi osakhulupirira akuganiza kuti angawasandutse akapolo Anga kukhala atetezi kusiya Ine? Ndithu taikonza Jahannam kukhala malo ofikirapo osakhulupirira
Verse 103 — Surah Al-Kahf 18:103
“Nena: “Kodi tikudziwitseni eni kuluza (kulephera) pa zochita zawo?”
Verse 104 — Surah Al-Kahf 18:104
““Iwo ndi omwe khama lawo lataika m’moyo wa pa dziko lapansi, pomwe iwowo akuganiza kuti akuchita zabwino”
Verse 105 — Surah Al-Kahf 18:105
“Iwowo ndi amene sadakhulupirire zisonyezo za Mbuye wawo, ndipo (sadakhulupirire) zakukumana Naye. Choncho zochita zawo zaonongeka (zapita pachabe), ndipo pa tsiku la chiweruziro sitidzawaikira sikelo
Verse 106 — Surah Al-Kahf 18:106
“Zimenezo, mphoto yawo ndi Jahannam chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, ndipo Ayah Zanga ndi atumiki Anga adazichitira chipongwe
Verse 107 — Surah Al-Kahf 18:107
“Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, malo awo ofikira adzakhala ku minda ya “Firdaus.”
Verse 108 — Surah Al-Kahf 18:108
“Adzakhalamo nthawi yaitali. Ndipo sadzafuna kuchokamo
Verse 109 — Surah Al-Kahf 18:109
“Nena: “Ngakhale nyanja ikadakhala inki yolembera mawu a Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha mawu a Mbuye wanga asadathe, ngakhale tikadabweretsa nyanja ina ndikuionjezera pa iyo (nyanjazo zikadatha, mawu a Allah akalipobe).”
Verse 110 — Surah Al-Kahf 18:110
“Nena: “Ndithu ine ndi munthu monga inu, (chosiyana nchakuti) ine ndikupatsidwa chivumbulutso (chonena kuti) ndithu Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi Yekha. Ndipo amene afuna kukumana ndi Mbuye wake, achite zochita zabwino ndipo asaphatikizepo aliyense pa mapemphero a Mbuye wake.”