Back to Languages

Chichewa - Chapter 19 - Maryam

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Maryam 19:1

“Kâf-Hâ-Yâ- ‘Aîn-Sâd

Verse 2 — Surah Maryam 19:2

“Ichi (ndi) chikumbutso cha chifundo cha Mbuye wako pa kapolo Wake Zakariya

Verse 3 — Surah Maryam 19:3

“Pamene adaitana Mbuye wake, kuitana kwa chinsinsi

Verse 4 — Surah Maryam 19:4

“Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu mafupa anga afooka, ndipo mutu wanga wayaka (ukung’anima) ndi imvi; sindidali watsoka pokupemphani Mbuye wanga (koma nthawi iliyonse ndikakupemphani mumandivomereza)

Verse 5 — Surah Maryam 19:5

““Ndipo ndithu ine ndikuopera abale anga (kuononga chipembedzo) pambuyo panga; ndipo mkazi wanga ndi chumba; choncho ndipatseni (mwana) mlowammalo wanga wochokera kwa Inu.”

Verse 6 — Surah Maryam 19:6

““Adzandilowe chokolo (pa nzeru za utsogoleri ndi uneneri) ndikulowanso ufumu wa banja la Ya’qub; ndipo Mbuye wanga nchiteni kukhala woyanjidwa (ndi Inu)”

Verse 7 — Surah Maryam 19:7

“(Adauzidwa): “E iwe Zakariya! Ife tikukuuza nkhani yabwino yakuti ubereka mwana dzina lake Yahya palibe patsogolo pake amene tidamutcha dzina longa lake.”

Verse 8 — Surah Maryam 19:8

“(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingapeze bwanji mwana pomwe mkazi wanga ndi nkhalamba yosabereka ndipo ine ndafikanso pa ukulu wopyola muyeso?”

Verse 9 — Surah Maryam 19:9

“Adati: “Ndimomwemo. Mbuye wako wanena (kuti): ‘Izi nzofewa kwa Ine; ndithu ndidakulenga kale pomwe iwe sudali kanthu.”

Verse 10 — Surah Maryam 19:10

“Adati: “Mbuye wanga ndipatseni chizindikiro (chodziwitsa kuti mkazi wanga ali ndi pakati).” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu pomwe iwe uli bwinobwino.”

Verse 11 — Surah Maryam 19:11

“Ndipo adatuluka kuchipinda chopemphelera ndikuonekera kwa anthu ake, ndipo adawalozera (pomwe sadathe kuyankhula) kuti: “Lemekezani Allah m’mawa ndi madzulo.”

Verse 12 — Surah Maryam 19:12

““E iwe Yahya! Gwira buku ili mwamphamvu (ndi mwachidwi).” Ndipo tidampatsa nzeru ali mwana

Verse 13 — Surah Maryam 19:13

“Ndi chisoni chochokera kwa Ife ndi kumuyeretsa (mwanayo), ndipo adali woopa (Allah)

Verse 14 — Surah Maryam 19:14

“Komanso wochitira zabwino makolo ake ndipo sadali wodzitukumula (kwa anthu) kapena kunyoza (Allah)

Verse 15 — Surah Maryam 19:15

“Ndipo mtendere wa Allah udali pa iye kuyambira tsiku lomwe adabadwa ndi tsiku lomwe adamwalira, ndi tsiku limene adzaukitsidwa ku imfa kukhala wamoyo

Verse 16 — Surah Maryam 19:16

“Ndipo mtchule Mariya m’buku ili pamene adadzipatula ku anthu a kubanja lake (ndikunka) kumalo ambali ya kummawa

Verse 17 — Surah Maryam 19:17

“Ndipo adadzitsekereza kwa iwo (kuti athe kutumikira Allah mokwanira), choncho tidatuma Mzimu Wathu (Mngelo Gabriel) kwa iye ndipo adadzifanizira kwa iye monga munthu weniweni

Verse 18 — Surah Maryam 19:18

“(Mariya) adati: “Ndithu ndikudzichinjiriza ndi (Allah) Mwini chifundo chambiri, kwa iwe ngati umaopa (Allah).”

Verse 19 — Surah Maryam 19:19

“(Mngelo) adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa mbuye wako, (ndadza) kuti ndikupatse mwana woyera.”

Verse 20 — Surah Maryam 19:20

“Adati: “Ndingakhale bwanji ndi mwana pomwe sadandikhudze mwamuna (aliyense), ndipo ine sindili (mkazi) wachiwerewere?”

Verse 21 — Surah Maryam 19:21

“(Mngelo) adati: “Ndimomwemo.” Mbuye Wako akuti: “Zimenezi kwa Ine nzosavuta. Ndipo timchita kukhala chozizwitsa kwa anthu ndi chifundo chochokera kwa Ife. (Nchifukwa chake tachita izi;) ndipo ichi ndi chinthu chimene chidalamulidwa kale. (Chichitika monga momwe Allah adafunira).”

Verse 22 — Surah Maryam 19:22

“Choncho adatenga pakati pake, ndipo adachoka ndi pakatipo kunka kumalo akutali

Verse 23 — Surah Maryam 19:23

“Ndipo matenda auchembere (atakwana), adampititsa ku thunthu la mtengo wa kanjedza (wouma kuti awutsamire pomubala mwanayo) adati: “Kalanga ine! Ndiponi ndikadafa izi zisanachitike ndikadakhala nditaiwalidwa ndithu.”

Verse 24 — Surah Maryam 19:24

“Kenaka (Mngelo) adamuitana kuchokera chapansi pake (kumuuza kuti): “Usadandaule. Ndithu Mbuye wako wakupangira kamtsinje pansi pako.”

Verse 25 — Surah Maryam 19:25

“Ndipo ligwedezere kumbali yako thunthu la mtengo wakanjedza (woumawo), zipatso zabwino zakupsa zikugwera.”

Verse 26 — Surah Maryam 19:26

“Choncho udye ndi kumwa ndikutonthoza diso lako, (khala ndi mpumulo wabwino). Ndipo ukaona munthu aliyense (akafunsa za mwanayo), nena: “Ndithu ine ndalonjeza kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri kusala kuti lero sindiyankhula ndi munthu aliyense.”

Verse 27 — Surah Maryam 19:27

“Ndipo adadza naye (mwanayo) kwa anthu ake atamnyamula. (Anthu) adati: “E iwe Mariya! Ndithu wabwera ndi chinthu chachikulu; (chododometsa).”

Verse 28 — Surah Maryam 19:28

““E iwe mlongo wa Harun! Bambo wako sadali munthu woipa, ngakhalenso mayi wako sadali wachiwerewere.”

Verse 29 — Surah Maryam 19:29

“(Mariya sadawayankhe) koma adaloza kwa iye (mwanayo kuti ayankhule naye). Ndipo iwo adati: “Timuyankhula chotani mwana yemwe ali m’chikuta?”

Verse 30 — Surah Maryam 19:30

“(Mwanayo) adanena: “Ine ndine kapolo wa Allah. Wandipatsa buku ndikundichita kukhala Mneneri.”

Verse 31 — Surah Maryam 19:31

““Ndipo wandichita kukhala wodala paliponse pomwe ndili, ndipo wandilamula kuswali ndi kupereka Zakaat pomwe ndili moyo.”

Verse 32 — Surah Maryam 19:32

““Ndipo wandilangiza kuchitira mayi wanga zabwino, ndipo sadandichite kukhala wodzikuza, watsoka (woipa).”

Verse 33 — Surah Maryam 19:33

““Ndipo mtendere uli pa ine kuyambira tsiku lomwe ndidabadwa ndi tsiku limene ndidzamwalira, ndi tsiku limene ndidzaukitsidwa (kwa akufa tsiku la chiweruziro) ndikukhala ndi moyo.”

Verse 34 — Surah Maryam 19:34

“Uyu ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya; (awa ndi) mau owona omwe (Akhrisitu) akuwakaikira

Verse 35 — Surah Maryam 19:35

“Sikoyenera kwa Allah kudzipangira mwana. Iye (Allah) wapatukana ndi zimenezi. Akafuna chinthu, amangonena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo icho chimachitikadi

Verse 36 — Surah Maryam 19:36

“(Isa (Yesu) adati:) “Ndipo ndithu Allah ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu. Choncho mpembedzeni; iyi ndinjira yolunjika (yokufikitsani ku mtendere)

Verse 37 — Surah Maryam 19:37

“Koma magulu (a Akhrisitu ndi Ayuda) adapatukana pakati pawo; (ena adamuyesa Isa (Yesu) kuti ndimwana wa Mulungu, ndipo ena adamuyesa Mulungu weniweni, pomwe Ayuda ankati ndi mwana wobadwa m’njira ya chiwerewere), choncho chilango chaukali chidzatsimikizika pa amene sadakhulupirire pokaonekera tsiku lalikululo (kwa Allah)

Verse 38 — Surah Maryam 19:38

“Taona kumvetsetsa kwawo ndi kupenyetsetsa kwawo tsiku lodzatidzera, (kudzanenedwa kuti:) “Koma osalungama lero ali m’kusokera koonekera.”

Verse 39 — Surah Maryam 19:39

“Ndipo achenjeze (anthu) za tsiku la madandaulo, pamene chiweruzo chidzagamulidwa, (abwino kulowa ku munda wamtendere, oipa kulowa ku Moto); koma iwo (pano pa dziko lapansi) ali m’kusalabadira ndipo sakhulupirira

Verse 40 — Surah Maryam 19:40

“Ndithu Ife Tidzaitenga nthaka ndi amene ali pamenepo; (zonse zidzakhala za Ife) ndipo kwa Ife adzabwerera

Verse 41 — Surah Maryam 19:41

“Ndipo mtchule m’buku ili, Ibrahim. Ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri

Verse 42 — Surah Maryam 19:42

“(Akumbutse) pamene iye adauza bambo wake: “E inu bambo wanga! Bwanji mukupembedza zomwe sizimva ndiponso sizipenya, ndiponso Zosakupindulitsani chilichonse?”

Verse 43 — Surah Maryam 19:43

““E inu bambo wanga! Ndithu ine zandidzera nzeru (zomuzindikira Allah) zomwe sizidakudzereni; choncho nditsateni. Ndikutsogolereni ku njira yolungama.”

Verse 44 — Surah Maryam 19:44

““E bambo wanga! Musapembedze satana (potsatira malangizo ake). Ndithu satana ngopandukira (Allah) Mwini chifundo chambiri.”

Verse 45 — Surah Maryam 19:45

“E bambo wanga! Ndithu ine ndikuopa kuti chilango chingakukhudzeni chochokera kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri, ndipo potero mdzakhala bwenzi la satana.”

Verse 46 — Surah Maryam 19:46

“(Bambo wake) adati: “Kodi iwe ukuda milungu yanga, E iwe Ibrahim? Ngati susiya (kunyoza milungu yanga) ndikugenda ndi miyala; choncho ndichokere kwa nthawi yaitali (tisaonanenso).”

Verse 47 — Surah Maryam 19:47

“(Ibrahim) adati: “Mtendere ukhale pa inu! Ndikupempherani chikhululuko kwa Mbuye wanga (ngakhale mwandipirikitsa). Ndithu iye amandichitira chisoni kwambiri.”

Verse 48 — Surah Maryam 19:48

““Ndipo ine ndikupatukirani ku zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah ndipo ndipempha Mbuye wanga; ndithu sindikhala watsoka popempha Mbuye wanga.”

Verse 49 — Surah Maryam 19:49

“Ndipo pamene adawapatukira ndi zimene adali kuzipembedza kusiya Allah, tidampatsa iye Ishaq, ndi Ya’qub, ndipo aliyense wa iwo tidampanga kukhala m’neneri

Verse 50 — Surah Maryam 19:50

“Ndipo tidawapatsa iwo chifundo Chathu, ndi kuwayikira iwo kutchulidwa kwabwino, kwapamwamba (pakati pa zolengedwa)

Verse 51 — Surah Maryam 19:51

“Ndipo mtchule Mûsa m’buku (ili). Ndithu iye adali wosankhidwa ndi woyeretsedwa: ndipo adali Mtumiki M’neneri

Verse 52 — Surah Maryam 19:52

“Ndipo tidamuitana kumbali yakudzanjadzanja la phiri la Turi, ndipo tidamuyandikitsa ndi kuyankhula Nafe momunong’ oneza

Verse 53 — Surah Maryam 19:53

“Ndipo mwachifundo Chathu tidampatsa (Mûsa) m’bale wake Harun kukhala mneneri (womuthangata)

Verse 54 — Surah Maryam 19:54

“Mtchulenso m’buku (ili) Ismaila; ndithu iye adali woona palonjezo, ndipo adali Mtumiki Mneneri

Verse 55 — Surah Maryam 19:55

“Adali kulamula anthu ake Swala ndi Zakaat, ndipo kwa Mbuye wake adali woyanjidwa

Verse 56 — Surah Maryam 19:56

“Mtchulenso m’buku (ili) Idris, ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri

Verse 57 — Surah Maryam 19:57

“Ndipo tidamunyamula (kumuika pa) malo apamwamba

Verse 58 — Surah Maryam 19:58

“Iwowo ndi omwe adawadalitsa Allah, mwa aneneri mu ana a Adam, ndi (m’mbumba ya) amene tidawatenga pamodzi ndi Nuh (m’chombo), ndi m’mbumba ya Ibrahim ndi Israyeli, ndi amene tidawaongola ndi kuwasankha. Ndipo zikawerengedwa kwa iwo Ayah za (Allah) Mwini chifundo chambiri, amagwa ndi kulambira uku akulira

Verse 59 — Surah Maryam 19:59

“Koma pambuyo pa iwo padadza anthu oipa. Adasokoneza Swala (adasiya kupemphera) natsatira zilakolako zoipa; choncho adzakumana ndi chilango choipa

Verse 60 — Surah Maryam 19:60

“Kupatula amene ati alape ndikukhulupirira ndikuchita zabwino; iwowo adzalowa ku Munda wamtendere ndipo sadzachitidwa chinyengo pa chilichonse

Verse 61 — Surah Maryam 19:61

“Munda wamuyaya umene (Allah) Wachifundo chambiri walonjeza akapolo Ake mobisika, ndithu lonjezo Lake ndilakudza

Verse 62 — Surah Maryam 19:62

“Sakamva m’menemo mawu achibwana, koma mawu a mtendere; ndipo akapeza rizq (chakudya) lawo m’menemo m’mawa ndi madzulo

Verse 63 — Surah Maryam 19:63

“Umenewo ndiwo Munda wamtendere umene tikawapatsa ena mwa akapolo athu omwe adali oopa Allah

Verse 64 — Surah Maryam 19:64

“(Mtumiki adapempha Gabriel kuti akhale akum’bwerera pafupipafupi. Ndipo Gabriel adamuuza kuti): “Ndipo sitimatsika koma mwa lamulo la Mbuye wako. Zapatsogolo pathu ndi zapambuyo pathu ndi zapakati pa zimenezi zonse Nzake (akuzidziwa bwinobwino). Ndipo Mbuye wako sali woiwala.”

Verse 65 — Surah Maryam 19:65

““Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pa izo: Choncho mpembedze Iye basi. Ndipo pitiriza ndikupirira popembedza Iye. Kodi ukumudziwa (wina) yemwe ali wofanana Naye (Allah)?”

Verse 66 — Surah Maryam 19:66

“Ndipo munthu (wokanira) amanena: “Kodi ndikadzafa nzoonadi kuti Ndidzatulutsidwa (m’manda) nkukhala wamoyo?”

Verse 67 — Surah Maryam 19:67

“Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga kale pomwe sadali chilichonse

Verse 68 — Surah Maryam 19:68

“Choncho ndikulumbira Mbuye wako, ndithu tidzawasonkhanitsa iwo pamodzi ndi asatana; ndipo tidzawafikitsa m’mphepete mwa Jahannam uku atagwada

Verse 69 — Surah Maryam 19:69

“Kenako, m’gulu lililonse tidzachotsamo yemwe adali wopyola malire polakwira (Allah) Mwini chifundo chambiri

Verse 70 — Surah Maryam 19:70

“Ndipo Ife tikuwazindikira kwambiri amene ali oyenera kulowa m’Moto

Verse 71 — Surah Maryam 19:71

“Ndipo palibe aliyense mwa inu koma adzaifika (Jahannamyo). Ndithu ili ndi lamulo la Mbuye wako lomwe lidalamulidwa kale

Verse 72 — Surah Maryam 19:72

“Ndipo kenako tidzawapulumutsa amene ankaopa Allah, ndipo osalungama tidzawasiya m’menemo atagwada

Verse 73 — Surah Maryam 19:73

“Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, omwe sadakhulupirire amanena kwa omwe akhulupirira: “Ndi gulu liti pa magulu awiri awa, (lanu ndi lathu) lomwe lili ndi pokhala pabwino ndikukhalanso ndi anthu olemekezeka?”

Verse 74 — Surah Maryam 19:74

“Ndipo mibadwo yambiri tidaiononga patsogolo pawo, yomwe idali ndi ziwiya zabwino ndi maonekedwe abwino

Verse 75 — Surah Maryam 19:75

“Nena: “Amene ali mkusokera, (Allah) Mwini chifundo chambiri amuonjezera nthawi yamoyo kufikira azione zomwe akulonjezedwa - kapena chilango kapena kudza nthawi (ya Qiyâma) - pamenepo ndipomwe adzadziwa kuti ndani mwini kukhala pamalo poipa, ndi mwini wa ankhondo ofooka (iwo kapena Asilamu)?”

Verse 76 — Surah Maryam 19:76

“Ndipo Allah amawaonjezera chiongoko amene aongoka. Ndipo zochita zabwino zonkerankera (mpaka tsiku lachimaliziro), ndizo zili zabwino kwa Mbuye wako monga mphoto, ndiponso ndiko kobwerera kwabwino, (osati za mdziko zomwe anthu osalungama akunyadira)

Verse 77 — Surah Maryam 19:77

“Kodi wamuona yemwe watsutsa Ayah Zathu ndikunena kuti: “Ndithu ndidzapatsidwa chuma ndi ana (pa tsiku lachimaliziro monga momwe andipatsira pano pa dziko?)”

Verse 78 — Surah Maryam 19:78

“Kodi adadziwa zamseri, kapena adalandira lonjezo kwa Allah mwini chifundo Chambiri (kotero kuti ali ndi chikhulupiliro pa zimene akunenazo)

Verse 79 — Surah Maryam 19:79

“Sichoncho, ndithu tikulemba zonse zomwe akunena, ndipo tidzamuonjezera nyengo yotalika m’chilango

Verse 80 — Surah Maryam 19:80

“Ndipo tidzamlowa mmalo zimene akunenazi, (chuma ndi anawo), nadzatidzera ali yekhayekha (wopanda chuma ndi zonse zomwe ankanyadira)

Verse 81 — Surah Maryam 19:81

“Eti adzipangira milungu ina m’malo mwa Allah kuti milunguyo iwapatse mphamvu (ndi ulemelero)

Verse 82 — Surah Maryam 19:82

“Iyayi! Idzawakanira mapemphero awo ndikuwaukira

Verse 83 — Surah Maryam 19:83

“Kodi suona kuti Ife timawatuma asatana kwa osakhulupirira ndipo akuwakhwirizira kwambiri (kuchita zoipa)

Verse 84 — Surah Maryam 19:84

“Choncho, usawachitire changu (kuti alangidwe tsopano), ndithu Ife tikuwawerengera chiwerengero (cha masiku awo; masiku akakwana, tiwalanga)

Verse 85 — Surah Maryam 19:85

“(Kumbukira iwe Mtumiki) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa oopa (Allah) kunka nawo kwa Mwini chifundo Chambiri ali m’magulumagulu monga nthumwi (Zake kuti apatsidwe ulemu)

Verse 86 — Surah Maryam 19:86

“Ndipo oipa tidzawakusa kunka nawo ku Moto ali ndi ludzu lalikulu monga momwe ziweto zimathamangira kupita kumadzi zikakhala ndi ludzu lalikulu

Verse 87 — Surah Maryam 19:87

“Sadzakhala ndi mphamvu yoombolera (ena) koma kupatula omwe adagwiritsa lonjezo la (Allah) Mwini chifundo chambiri

Verse 88 — Surah Maryam 19:88

“Ndipo (osakhulupirira omwe ndi Ayuda ndi Akhirisitu) akuti: “(Allah) Mwini chifundo chambiri wadzipangira mwana!”

Verse 89 — Surah Maryam 19:89

“Ndithu mwadza ndi chinthu choipitsitsa (pazimene mukunenazi)

Verse 90 — Surah Maryam 19:90

“Thambo layandikira kusweka ndi mawuwo, ndipo nthaka kuphwasuka, ndipo mapiri kugwa ndikudukaduka

Verse 91 — Surah Maryam 19:91

“Chifukwa chakumunamizira (Allah) Mwini chifundo chambiri kuti ali ndi mwana

Verse 92 — Surah Maryam 19:92

“Ndipo nkosayenera kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri kudzipangira mwana

Verse 93 — Surah Maryam 19:93

“Palibe aliyense yemwe ali kumwamba ndi pansi koma adzadza kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri ali kapolo (Wake)

Verse 94 — Surah Maryam 19:94

“Ndithu (Allah) wawadziwa mokwanira ndipo adzawawerenga aliyense payekhapayekha

Verse 95 — Surah Maryam 19:95

“Ndipo, aliyense wa iwo adzadza kwa Iye (Allah) ali payekhapayekha

Verse 96 — Surah Maryam 19:96

“Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, (Allah) Mwini chifundo chambiri adzaika chikondi pakati pawo

Verse 97 — Surah Maryam 19:97

“Ndithu taifewetsa (Qur’an) m’chiyankhulo chako kuti ndi iyo uwawuze nkhani zabwino oopa Allah ndipo ndi iyo uwachenjeze anthu amakani

Verse 98 — Surah Maryam 19:98

“Kodi ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Kodi ukumuona mmodzi wa iwo, kapena ukumva mgugu wawo