Back to Languages

Chichewa - Chapter 20 - Ta-Ha

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Ta-Ha 20:1

Verse 2 — Surah Ta-Ha 20:2

“Sitidakuvumbulutsire iwe Qur’an kuti uvutike (nayo)

Verse 3 — Surah Ta-Ha 20:3

“Koma kuti ikhale ulaliki ndi chikumbutso kwa yemwe akuopa (ndikudzichepetsa kwa Allah)

Verse 4 — Surah Ta-Ha 20:4

“Chovumbulitsidwa chochokera kwa Yemwe adalenga nthaka ndi thambo lotukuka kumwamba

Verse 5 — Surah Ta-Ha 20:5

“(Iye ndi Allah), Wachifundo Chambiri; pa Arsh (Mpando wachifumu) adakhazikika, (kukhazikika koyenerana ndi ulemelero Wake kopanda kukufanizira ndi kukhazikika kwa chilichonse; pakuti Iye salingana ndi chilichonse pa chikhalidwe ndi mbiri Zake)

Verse 6 — Surah Ta-Ha 20:6

“Zonse za kumwamba ndi za pansi ndi za pakati pake ndi za pansi pa nthaka, nza Iye

Verse 7 — Surah Ta-Ha 20:7

“Ndipo ngati ulankhula mokweza mawu, (iwe munthu), ndithu Iye akudziwa zobisika ndi zobisika kwambiri (zomwe mwazibisa mu mtima mwanu)

Verse 8 — Surah Ta-Ha 20:8

“Allah! Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Iye ali ndi maina abwino (ndi mbiri zabwinonso)

Verse 9 — Surah Ta-Ha 20:9

“Ndipo kodi yakufika nkhani ya Mûsa? (Yomwe njododometsa)

Verse 10 — Surah Ta-Ha 20:10

“Pamene adaona moto adauza banja lake: “Yembekezani (pano); ndithu ndaona moto; mwina ndingakakutengereni chikuni chamoto (kuti muothe), kapena ndikapeza ondiongolera njira pa motopo

Verse 11 — Surah Ta-Ha 20:11

“Koma pamene adaudzera motowo Anaitanidwa (kuti), “E, iwe Mûsa

Verse 12 — Surah Ta-Ha 20:12

“Ndithu ine ndine Mbuye wako! Vula nsapato zakozo; ndithu iwe uli pa chigwa chopatulika, chotchedwa Tuwa.”

Verse 13 — Surah Ta-Ha 20:13

“Ndipo Ine ndakusankha (kuti ukhale Mtumiki); choncho mvera zonse zomwe zikuvumbulutsidwa (kwa iwe)

Verse 14 — Surah Ta-Ha 20:14

“Ndithu Ine ndine Allah palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine; choncho ndipembeze, pemphera Swala moyenera pondikumbukira

Verse 15 — Surah Ta-Ha 20:15

“Ndithu nthawi ya tsiku lachimaliziro idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuibisa dala (kwa anthu) kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita

Verse 16 — Surah Ta-Ha 20:16

“Ndipo asakutsekereze (ku khulupirira) zimenezo yemwe saikhulupirira (Kiyamayo), ndipo akungotsata zilakolako za mtima wake; kuopa kuti Ungadzaonongeke.”

Verse 17 — Surah Ta-Ha 20:17

““Kodi nchiyani icho chili kudzanja Lako ladzanjadzanja, iwe Mûsa?”

Verse 18 — Surah Ta-Ha 20:18

“(Mûsa) adati: “Iyi ndi ndodo yanga, ndimaitsamira (poyenda) ndi kuphopholera masamba a mbuzi zanga; ndiponso (m’ndodomo) muli zina zondithandiza.”

Verse 19 — Surah Ta-Ha 20:19

“(Allah) adati: “Iponye iwe Mûsa!”

Verse 20 — Surah Ta-Ha 20:20

“Ndipo adaiponya; pompo idasanduka njoka yoyenda mothamanga

Verse 21 — Surah Ta-Ha 20:21

“(Allah) adati: “Igwire, usaope. Tiibwezera m’chikhalidwe chake Choyamba.”

Verse 22 — Surah Ta-Ha 20:22

““Ndipo lipane dzanja lako m’khwapa mwako lituluka lili loyera (ngati kuwala kwadzuwa ndi mwezi). Osati mwamatenda, (ichi chikhala) chozizwitsa china.”

Verse 23 — Surah Ta-Ha 20:23

““Kuti tikusonyeze zina mwa zozizwitsa zathu, zazikuluzikulu.”

Verse 24 — Surah Ta-Ha 20:24

““Pita kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire.”

Verse 25 — Surah Ta-Ha 20:25

“(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Nditsakulireni chifuwa changa.”

Verse 26 — Surah Ta-Ha 20:26

““Ndi kundifewetsera ntchito yangayi (imene mwandipatsa kuti uthengawu ndikaufalitse m’njira yoyenera).”

Verse 27 — Surah Ta-Ha 20:27

““Ndipo masulani mfundo yomwe ili ku lirime kwanga, (ndimasulireni kumangika kwa lirime langa kuti mawu anga akakhale opanda chibwibwi).”

Verse 28 — Surah Ta-Ha 20:28

““Kuti (anthu) akamvetse mawu anga.”

Verse 29 — Surah Ta-Ha 20:29

““Ndipo ndipatseni nduna (mthandizi) yochokera kubanja langa.”

Verse 30 — Surah Ta-Ha 20:30

““M’bale wanga Harun.”

Verse 31 — Surah Ta-Ha 20:31

““Limbitsani nyonga zanga ndi iye.”

Verse 32 — Surah Ta-Ha 20:32

““Ndipo mphatikeni ku ntchito yangayi.”

Verse 33 — Surah Ta-Ha 20:33

““Kuti tikulemekezeni kwambiri.”

Verse 34 — Surah Ta-Ha 20:34

““Ndi kukutamandani kwabasi.”

Verse 35 — Surah Ta-Ha 20:35

““Ndithu inu (nthawi zonse) mumationa (ndi kutisunga).”

Verse 36 — Surah Ta-Ha 20:36

“(Allah) adati: “Ndithu wapatsidwa zomwe wapempha, E, iwe Mûsa.”

Verse 37 — Surah Ta-Ha 20:37

““Ndipo ndithu tidakuchitira ubwino nthawi ina (popanda iwe kutipempha).”

Verse 38 — Surah Ta-Ha 20:38

““Pamene mayi wako tidamuzindikiritsa zimene tidamzindikiritsa (kuti azichite).”

Verse 39 — Surah Ta-Ha 20:39

“(Kuti): “Mponye (mwanayo) m’bokosi ndipo ponya bokosilo mu mtsinje; ndipo mtsinje umponya m’mbali kuti amtenge mdani wanga ndi mdani wake (ndi kuti aleredwe mwaubwino ndi Farawo); ndipo ndidaika kukondeka pa iwe kochokera kwa Ine (kuti ukhale wokondedwa ndi anthu onse) ndikuti uleredwe moyang’aniridwa ndi Ine.”

Verse 40 — Surah Ta-Ha 20:40

“(Kumbuka) pomwe mlongo wako ankayenda (kunka kubanja la Farawo) Ndipo adati: “Kodi ndikulondolereni munthu amene angathe kumlera?” Ndipo tidakubwezera kwa mayi wako kuti maso ake atonthole, ndipo asadandaule. Ndipo kenaka udapha munthu (mwangozi), ndipo tidakupulumutsa ku madandaulo; tidakuyesa ndi mayeso ambiri. Udakhala zaka zambiri ndi anthu a ku Madiyan. Kenaka wabwera (apa) monga mwachikonzero, E, iwe Mûsa

Verse 41 — Surah Ta-Ha 20:41

“Ndipo ndakusankha ndekha (kuti ukhale Mtumiki Wanga)

Verse 42 — Surah Ta-Ha 20:42

“Pita iwe ndi m’bale wako ndi zozizwitsa Zanga, ndipo musatope (musasiye) kundikumbukira

Verse 43 — Surah Ta-Ha 20:43

“Pitani kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire

Verse 44 — Surah Ta-Ha 20:44

“Kamuuzeni mawu ofewa mwina akalingalira (uthengawo) kapena akaopa

Verse 45 — Surah Ta-Ha 20:45

“(Iwo) adati: “Mbuye wathu ndithu ife tikuopa kuti angatimbwandire kapena kutipyolera malire (tisananene kanthu).”

Verse 46 — Surah Ta-Ha 20:46

“(Allah) adati: “Musaope. Ndithu Ine ndili nanu pamodzi. ndikumva, ndiponso ndikuona.”

Verse 47 — Surah Ta-Ha 20:47

“Choncho mpitireni, ndikumuuza (kuti): “Ndithu ife ndife atumiki a Mbuye wako. Asiye ana a Israyeli achoke ndi ife, ndipo usawazunze; ndithu takudzera ndi chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wako (chomwe ndi mboni yathu pa zomwe tikukuuzazi), ndipo mtendere ukhala pa yemwe atsate chiwongoko.”

Verse 48 — Surah Ta-Ha 20:48

““Ndithu zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chiwapeza amene akutsutsa (zimenezi) ndikuzitembenukira kumbali.”

Verse 49 — Surah Ta-Ha 20:49

“(Farawo) adati: “Kodi Mbuye wanu ndani, iwe Mûsa?”

Verse 50 — Surah Ta-Ha 20:50

“(Mûsa) adati: “Mbuye wathu ndi yemwe adapatsa chinthu chilichonse chilengedwe chake, kenako adachiongolera (kutsata chimene chikulingana ndi chilengedwe chake).”

Verse 51 — Surah Ta-Ha 20:51

“(Farawo) adati: “Nanga mibadwo yakale ili bwanji, (imene idapita iwe usadadze?”)

Verse 52 — Surah Ta-Ha 20:52

“(Mûsa) adati: “Kudziwa kwa zimenezo nkwa Mbuye wanga, m’kaundula (Wake momwe mwasonkhanitsidwa chilichonse), Mbuye wanga sasokera, ndipo saiwala

Verse 53 — Surah Ta-Ha 20:53

“Yemwe adakupangirani nthaka monga choyala, ndipo m’menemo adakuikirani njira ndikutsitsa madzi kuchokera kumwamba.” Ndipo kupyolera m’madziwo tidameretsa mmera wosiyanasiyana

Verse 54 — Surah Ta-Ha 20:54

“Idyani ndikudyetsa ziweto zanu. Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru

Verse 55 — Surah Ta-Ha 20:55

“Kuchokera (m’nthaka) umu tidakulengani, ndipo momwemo tidzakubwezani, ndipo kuchokera m’menemo tidzakutulutsani nthawi ina (muli moyo)

Verse 56 — Surah Ta-Ha 20:56

“Ndipo, ndithu tidamuonetsa (Farawo) zozizwitsa zathu zonse, koma adatsutsa ndipo adakana

Verse 57 — Surah Ta-Ha 20:57

“Adati: “Kodi watidzera kuti utitulutse m’dziko lathu, ndi matsenga ako, E, iwe Mûsa

Verse 58 — Surah Ta-Ha 20:58

“Choncho nafe tikubweretsera matsenga onga amenewo! Choncho ika lonjezo (la msonkhano) pakati pathu ndi iwe; lonjezo lomwe tisaliswe ife ndi iwe, (tidzakumane) pamalo poyenera.”

Verse 59 — Surah Ta-Ha 20:59

“(Mûsa) adati: “Lonjezo lanu likhale pa tsiku lodzikongoletsa (tsiku la chikondwelero), ndipo anthu adzasonkhanitsidwe m’mawa.”

Verse 60 — Surah Ta-Ha 20:60

“Ndipo Farawo adabwerera ndikusonkhanitsa matsenga ake, ndipo kenako adabwera (ndi amatsenga ake pa tsiku la chipanganolo)

Verse 61 — Surah Ta-Ha 20:61

“Mûsa adawauza: “Tsoka kwa inu! Musampekere bodza Allah, kuopera kuti angakuphwasuleni ndi chilango. Ndipo, ndithu wataika amene akupeka bodza.”

Verse 62 — Surah Ta-Ha 20:62

“Choncho (amatsengawo) adakangana pakati pawo pa zinthu zawo ndipo adakambirana mwachinsinsi

Verse 63 — Surah Ta-Ha 20:63

“(Iwo) adati (mkunong’onezana kwawo): “Ndithu anthu awiriwa ndi amatsenga; kupyolera mmatsenga awo akufuna kukutulutsani m’dziko mwanu, ndikuchotsa chikhalidwe chanu chomwe chili chabwino.”

Verse 64 — Surah Ta-Ha 20:64

““Choncho sonkhanitsani matsenga anu (onse), kenako mudze (kwa iwo) mutandanda pamzere; ndithu lero, apambana amene akhale wapamwamba.”

Verse 65 — Surah Ta-Ha 20:65

“(Iwo) adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukhale ndiwe woyamba kuponya (matsenga ako), kapena tikhale oyamba ndife kuponya?”

Verse 66 — Surah Ta-Ha 20:66

“(Mûsa) adati: “Koma inu ndinu muponye!” (Choncho adaponya matsengawo). Mwadzidzidzi zingwe zawo ndi ndodo zawo zamatsenga awo, zimaoneka pamaso pake (Mûsa) kuti zikuyenda mothamanga

Verse 67 — Surah Ta-Ha 20:67

“Ndipo Mûsa adadzazidwa ndi mantha mu mtima mwake

Verse 68 — Surah Ta-Ha 20:68

“Tidati: “Usaope (zomwe ukuzionazi), ndithu iwe ukhala wopambana.”

Verse 69 — Surah Ta-Ha 20:69

““Ndipo ponya chimene chili kudzanja lako ladzanjadzanja (ndodo); chimeza zomwe apanga; ndithu iwo apanga matsenga a mfiti ndipo mfiti siingapambane paliponse pamene yadza.”

Verse 70 — Surah Ta-Ha 20:70

“Choncho amatsenga adagwa molambira uku akuti: “Tamkhulupirira Mbuye wa Harun ndi Mûsa.”

Verse 71 — Surah Ta-Ha 20:71

“(Farawo) adanena: “Ha! Mwamkhulupirira ndisadakupatseni chilolezo? Ndithu iye ndi mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga! Choncho ndikudulani manja anu ndi miyendo yanu, mosemphanitsa:; (dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wakumanzere. Pomwe wina, mkono wakumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja), ndipo kenako ndikupachikani pa mathunthu a mitengo ya kanjeza; ndithu mudziwa (panthawiyo) kuti ndani mwa ife, (ine kapena Mulungu wa Mûsa), wachilango chaukali ndi chopitilira.”

Verse 72 — Surah Ta-Ha 20:72

“(Amatsenga) adati: “Sitisankha iwe kusiya zomwe zatidzera; zisonyezo zachoonadi zoonekera poyera! Ndipo tikumlumbilira Yemwe adatilenga, (sitikusankha iwe), chita zomwe ufuna kuchita; ndithu iwe utha kupititsa chiweruzo chokhudzana ndi moyo uno wapansi, basi.”

Verse 73 — Surah Ta-Ha 20:73

““Ndithu takhulupirira Mbuye wathu kuti atikhululukire zolakwa zathu ndi matsenga amene watikakamiza (kuchita); ndipo Allah ndi Yemwe ali Wabwino ndi Wamuyaya (osati iwe).”

Verse 74 — Surah Ta-Ha 20:74

“Ndithu amene adzadze kwa Mbuye wake uku ali wamachimo, adzapeza moto wa Jahannam; sadzafa m’menemo, ndipo sadzakhalanso ndi moyo wabwino

Verse 75 — Surah Ta-Ha 20:75

“Koma amene adzamdzera uku ali wokhulupirira, yemwe adachita ntchito zabwino, iwo ndi amene adzapeze ulemewero wapamwamba

Verse 76 — Surah Ta-Ha 20:76

“Minda yamuyaya, yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) pakuyenda mitsinje. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali. Ndipo zimenezo ndi mphoto za yemwe wadziyeretsa

Verse 77 — Surah Ta-Ha 20:77

“Ndipo ndithu Mûsa tidamtumizira chivumbulutso, (tidamzindikiritsa kuti): “Yenda usiku ndi akapolo Anga (kutuluka m’dziko la Iguputo,) ndipo ukawapangire panyanja njira youma, ndipo usaope kukupeza adani ndiponso usaope (kumira).”

Verse 78 — Surah Ta-Ha 20:78

“Choncho Farawo pamodzi ndi ankhondo ake, adawatsata, ndipo m’nyanjamo chidawaphimba chimene chidawaphimba

Verse 79 — Surah Ta-Ha 20:79

“Ndipo Farawo adawasokeretsa anthu ake, ndipo sadawaongolere

Verse 80 — Surah Ta-Ha 20:80

“E inu ana a Israyeli! Ndithu tidakupulumutsani kwa mdani wanu, ndipo tidakulonjezani (kuti mudze) mbali yakudzanjadzanja ya phiri (kuti tikupatseni malamulo ndi zina), ndipo tidakutsitsirani Manna ndi Saluwa

Verse 81 — Surah Ta-Ha 20:81

“Idyani zinthu zabwino zomwe takupatsani, ndipo musapyole malire pa zimenezo kuti mkwiyo Wanga usakutsikireni; ndipo amene mkwiyo Wanga wamtsikira, ndiye kuti ameneyo waonongeka

Verse 82 — Surah Ta-Ha 20:82

“Ndipo ndithu Ine ndi Wokhululuka kwambiri kwa amene walapa ndi kukhulupirira, ndikuchita ntchito zabwino, kenako ndikutsata chiongoko mwaubwino

Verse 83 — Surah Ta-Ha 20:83

““Nchiyani chakufulumizitsa (kudza kuno) kusiya anthu ako, E, iwe Mûsa?”

Verse 84 — Surah Ta-Ha 20:84

“Adati: “Iwo ali pambuyo panga akunditsata. Ndachita changu kudza kwa Inu, Mbuye wanga, kuti mundiyanje kwambiri.”

Verse 85 — Surah Ta-Ha 20:85

“(Allah) adati: “Ndithu Ife tawayesa Mmayeso anthu ako pambuyo pako; tero Samiriyyu wawasokeretsa.”

Verse 86 — Surah Ta-Ha 20:86

“Mûsa adabwerera kwa anthu ake ali wokwiya ndi wodandaula. Adati: “E inu anthu anga! Kodi Mbuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kapena nyengo yalonjezolo idatalika kwa inu? Kapena mudafuna kuti mkwiyo ukutsikireni kuchokera kwa Mbuye wanu; tero mwaswa lonjezo langa”

Verse 87 — Surah Ta-Ha 20:87

“(Iwo) adati: “Sitidaswe lonjezo lako mwachifuniro chathu; koma tidasenzetsedwa mitolo ya zodzikometsera za anthu (ziwiya zagolide zomwe tidabwereka kwa akazi a chimisiri), ndipo tidaziponya (pa moto, ndipo zidasungunuka ndikupangidwa mwana wang’ombe.) Ndipo momwemonso Samiriyyu adaponya.”

Verse 88 — Surah Ta-Ha 20:88

“Ndipo adawatulutsira (kuchokera m’golide wosungunukayo) mwana wang’ombe wokhala ndi thupi lokwanira, yemwe amatulutsa mawu (ngati kulira kwa ng’ombe), (iwo) adati: “Uyu ndi mulungu wanu ndiponso mulungu wa Mûsa, koma (Mûsa) wamuiwala, (choncho wapita kukamfuna ku phiri)!”

Verse 89 — Surah Ta-Ha 20:89

“Kodi sadaone kuti (mwana wang’ombe) sabweza mawu kwa iwo, ndiponso sangathe kudzetsa matsautso kwa iwo ngakhale zothandiza

Verse 90 — Surah Ta-Ha 20:90

“Ndipo ndithu Harun adawauza kale (kuti): “E inu anthu anga! Ndithu inu mwasokonezeka ndi (chinthu) ichi. Ndithu Mbuye wanu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; choncho nditsateni, ndipo mverani lamulo langa, (siyani kupembedza fano ili).”

Verse 91 — Surah Ta-Ha 20:91

“(Iwo) adati: “Sitisiya ngakhale pang’ono kumpembedza. Kufikira Mûsa abwelere kwa ife.”

Verse 92 — Surah Ta-Ha 20:92

“(Pamene Mûsa adabwerera) adati: “E iwe Harun! Nchiyani chidakuletsa pamene udawaona atasokera,”

Verse 93 — Surah Ta-Ha 20:93

“Kuti usanditsate? Udanyozera lamulo langa?”

Verse 94 — Surah Ta-Ha 20:94

“(Harun) adati: E iwe mwana wa mayi anga! Usagwire ndevu zanga, ngakhale mutu wanga (poukoka chifukwa cha mkwiyo). Ndithu ine ndidaopa (kuchoka ndi ena, kusiya ena) kuti ungati: “Wawagawa ana a Israyeli, ndipo sudayembekezere mawu anga.”

Verse 95 — Surah Ta-Ha 20:95

“(Mûsa) adati: “E iwe Samiriyyu! Nchiyani wachita?”

Verse 96 — Surah Ta-Ha 20:96

“(Iye adati:) “Ndidaona zomwe sadazione (ena) ndipo ndidatapa pang’ono mapazi a Mtumiki (Gabriele) ndikuwaponya (mu fano la mwana wa ng’ombe). Ndipo zimenezi ndi zomwe zidakomera mtima wanga.”

Verse 97 — Surah Ta-Ha 20:97

“(Mûsa) adati: “ Choka, ndithu pa iwe (pali chilango) pa moyo (wako) choti uzingonena (kuti): “Musandikhudze musandikhudze.” (Ndipo palibe amene adzakuyandikira ndipo iwe sudzayandikira aliyense). Ndithu pa iwe pali lonjezo la (Allah) losaswedwa; ndipo muyang’ane mulungu wako, yemwe wakhala ukupitiriza kumpembedza. Timtentha, kenako chipala chakecho tichimwaza m’nyanja

Verse 98 — Surah Ta-Ha 20:98

“Ndithu wompembedza wanu, ndi Allah Yekha, Yemwe, palibe woti nkupembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo wakwanira pa chilichonse kuchidziwa ndi nzeru (Zake zopanda malire)

Verse 99 — Surah Ta-Ha 20:99

“Umo ndi momwe tikukusimbira nkhani za (zinthu) zomwe zidatsogola (za aneneri). Ndithu takupatsa uthenga waukulu kuchokera kwa Ife (omwe ndi Qur’an)

Verse 100 — Surah Ta-Ha 20:100

“Amene aunyozere, ndithu iye tsiku la Qiyâma adzasenza mitolo (ya machimo)

Verse 101 — Surah Ta-Ha 20:101

“Adzakhala m’menemo m’chilango. Ndipo ndi zoipa zedi (kwa anthu) kusenza mitolo (imeneyo) tsiku la Qiyâma

Verse 102 — Surah Ta-Ha 20:102

“(Kumbuka Mtumiki Muhammad {s.a.w}), tsiku lomwe lipenga lidzaimbidwa. Ndipo tidzasonkhanitsa oipa tsiku limenelo maso awo ali a buluu (blue, chifukwa cha mantha)

Verse 103 — Surah Ta-Ha 20:103

“Adzanong’onezana pakati pawo (ponena kuti): “Simudakhalitse pa dziko lapansi koma masiku khumi okha basi.”

Verse 104 — Surah Ta-Ha 20:104

“Ife tikudziwa kwambiri zimene azidzanena pamene abwino awo pamayendedwe azidzanena: “Inu simudakhale koma tsiku limodzi basi (poyerekeza ndi kuchuluka kwa masiku a ku Moto).”

Verse 105 — Surah Ta-Ha 20:105

“Ndipo akukufunsa zamapiri (kuti adzatani tsiku la Qiyâma); auze: “Mbuye wanga adzawagumulagumula ndikuwaululutsa (ngati fumbi).”

Verse 106 — Surah Ta-Ha 20:106

““Ndipo adzaisiya (nthaka yonse) ngati bwalo losalazidwa myaa!”

Verse 107 — Surah Ta-Ha 20:107

““Sudzaona kukhota m’menemo ngakhale chitunda (chikweza).”

Verse 108 — Surah Ta-Ha 20:108

“Tsiku limenelo adzamtsatira woitana; sadzatha kumpatuka, ndipo mawu (azolengedwa) adzatonthola (kuti chete) kwa (Allah) Wachifundo chambiri; ndipo sudzamva, koma kunong’ona basi (ndi mididi ya mapazi)

Verse 109 — Surah Ta-Ha 20:109

“Tsiku limenelo chiombolo (cha aliyense) sichidzathandiza, kupatula yemwe wapatsidwa chilolezo ndi (Allah) Wachifundo chambiri, ndi kumuyanja kuti alankhule

Verse 110 — Surah Ta-Ha 20:110

“(Allah) akudziwa za patsogolo pawo ndi zapambuyo pawo. Ndipo iwo sangathe kumzindikira (Allah) mmene alili

Verse 111 — Surah Ta-Ha 20:111

“Ndipo nkhope (tsiku limenelo) zidzalobodoka pamaso pa (Allah) Wamoyo wamuyaya, Wochita chilichonse. Ndithu adzataika kwathunthu yense wochita zosalungama

Verse 112 — Surah Ta-Ha 20:112

“Ndipo amene achite zabwino uku ali wokhulupirira, sadzaopa kuchitiridwa zoipa kapena kumchepetsera (choyenera chake)

Verse 113 — Surah Ta-Ha 20:113

“Ndipo momwemo taivumbulutsa (Qur’an) m’Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mwatsatanetsatane za machenjezo (amtundu uliwonse), kuti aope (Allah), ndikuti nthawi iliyonse (Qur’aniyo), iwapatse chikumbutso chatsopano

Verse 114 — Surah Ta-Ha 20:114

“Chomwecho watukuka Allah, Mfumu ya choonadi, ndipo usaifulumizitse Qur’an (powerenga) chivumbulutso chake chisanamalizike kwa iwe, ndipo nena (popempha) kuti: “Mbuye wanga! Ndionjezereni nzeru (kuzindikira).”

Verse 115 — Surah Ta-Ha 20:115

“Ndipo tidamulangiza (Mneneri) Adam kale, koma adaiwala. Ndipo sitidapeze Mwa iye kulimba mtima (potsatira lamulo Lathu loti asadye zipatso za mtengo woletsedwa)

Verse 116 — Surah Ta-Ha 20:116

“Ndipo (kumbukirani) pamene tidauza angelo: “Muchitireni sajida (mugwadireni momulemekeza) Adam,” dipo adachita Sajida kupatula Iblis, adakana

Verse 117 — Surah Ta-Ha 20:117

“Tsono tidati: “E iwe Adam! Ndithu uyu ndi mdani wako iwe ndi mkazi wako; choncho asakutulutseni m’Munda wamtendere, mungadzavutike.”

Verse 118 — Surah Ta-Ha 20:118

““Ndithu iwe sumva njala m’menemo ndipo sukhala wamaliseche.”

Verse 119 — Surah Ta-Ha 20:119

““Ndipo iwe sumva ludzu m’menemo, ndiponso sumva kutentha (kwa dzuwa).”

Verse 120 — Surah Ta-Ha 20:120

“Koma satana (adamsokoneza) pomunong’oneza (zoipa) adati: “E iwe Adam! Kodi ndikusonyeze mtengo wamuyaya ndi (wopatsa) ufumu wosatha?”

Verse 121 — Surah Ta-Ha 20:121

“Ndipo (onse awiri) adaudya, ndipo umaliseche wawo awiriwo udaonekera poyera; ndipo adayamba kudziphatika masamba a m’mundamo; ndipo Adam adalakwira Mbuye wake, choncho adasokera

Verse 122 — Surah Ta-Ha 20:122

“Kenako Mbuye wake adamsankha pomulandira kulapa kwake ndikumuongola

Verse 123 — Surah Ta-Ha 20:123

“(Allah) adati: “Chokani nonsenu m’menemo, uku pali chidani pakati pa wina ndi mnzake, (padzakhala chidani pakati pa ana anu); koma chikadzakudzerani chiongoko kuchokera kwa Ine, tero amene adzachitsate chiongoko changacho, sadzasokera ndiponso sadzavutika.”

Verse 124 — Surah Ta-Ha 20:124

“Ndipo amene anyozere ulaliki wanga, ndithu moyo wamavuto udzakhala pa iye ndipo tidzamuukitsa m’manda tsiku la chimaliziro ali wakhungu.”

Verse 125 — Surah Ta-Ha 20:125

“Adzanena: “Mbuye wanga! Chifukwa ninji mwandiukitsa ndili wakhungu, pomwe ndidali wopenya?”

Verse 126 — Surah Ta-Ha 20:126

“(Allah) adzanena: “Zimenezo nchifukwa chakuti zidakudzera Ayah zathu koma udaziiwala (chifukwa chosalabadira), momwemo lero uiwalidwa, (salabadilidwa).”

Verse 127 — Surah Ta-Ha 20:127

“Ndipo umo ndimomwe tidzamulipirire aliyense wopyola malire, wosakhulupirira Ayah za Mbuye wake. Ndipo chilango cha tsiku la chimaliziro nchaukali, ndiponso chamuyaya

Verse 128 — Surah Ta-Ha 20:128

“Kodi sizidadziwikebe kwa iwo kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo awa (osakhulupirira atsopano) akuyenda m’malo awo, (kodi saona zizindikiro zakuonongeka kwawo)? Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru

Verse 129 — Surah Ta-Ha 20:129

“Ndipo pakadapanda liwu lomwe lidatsogola kuchokera kwa Mbuye wako (lochedwetsera chilango) ndi nthawi yomwe idaikidwa, ndithu (chilango) chikadawafika (tsopano lomwe lino)

Verse 130 — Surah Ta-Ha 20:130

“Choncho pirira pa zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda, dzuwa lisanatuluke (popemphera swala ya Fajr), ndiponso lisanalowe (popemphera swala ya Asr); ndiponso nthawi za usiku umulemekeze (popemphera swala ya Magrib ndi Isha), ndi pansonga za masana (pakatikati pa usana popemphera swala ya Dhuhr); kuti udzakhale wokondwa (ndi malipilo amene azakupatse tsiku la Qiyâma)

Verse 131 — Surah Ta-Ha 20:131

“Ndipo usazitong’olere maso ako (mozidololokera zinthu) zimene tawasangalatsa nazo ena mwa anthu pakati pawo; zimenezo nzokongoletsa za moyo wa pa dziko basi, kuti tiwayese mayeso pazimenezo; koma chopatsa cha Mbuye wako (chomwe nchololedwa ngakhale chikhale chochepa) nchabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa

Verse 132 — Surah Ta-Ha 20:132

“Ndipo lamula banja lako kupemphera Swala ndi kuipirira iwe mwini Swalayo. Sitikukupempha rizq, (chakudya) koma Ife ndi amene tikukudyetsa ndipo malekezero abwino ali mukuopa (Allah)

Verse 133 — Surah Ta-Ha 20:133

“Ndipo (osakhulupirira) adanena: “Chifukwa ninji sakutibweretsera chizizwa kuchokera kwa Mbuye wake?” Kodi sudawafike umboni woonekera wa zomwe zili m’mabuku akale? (Kodi sadakhutitsidwe ndi Qur’an chomwe ndi chizizwa chachikulu).”

Verse 134 — Surah Ta-Ha 20:134

“Ndipo ngati tikadawaononga ndi chilango, asanadze uyo (Mtumiki), akadanena: “Mbuye wathu! Bwanji osatitumizira mtumiki kuti titsate Ayah Zanu tisanayaluke ndi kunyozeka?”

Verse 135 — Surah Ta-Ha 20:135

“Nena: “Aliyense (wa ife) akuyembekezera (mphoto yake); choncho yembekezerani. Posachedwapa mudziwa kuti kodi ndani mwini njira yolingana, ndipo ndani amene waongoka.”