Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 21 - Al-Anbiya
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Anbiya 21:1
“۞ Chiwerengero chayandikira kwa anthu pomwe iwo ali m’kusalabadira ndi M’kunyozera
Verse 2 — Surah Al-Anbiya 21:2
“Palibe pamene ukuwadzera ulaliki watsopano wochokera kwa Mbuye wawo koma amaumvetsera uku akuchita zachibwana
Verse 3 — Surah Al-Anbiya 21:3
“Mitima yawo ikunyozera (osalabadira za kudza kwa Qiyâma). Ndipo akunenezana mobisa amene adzichitira zoipa; (akuuzana motere): “Kodi uyu (Muhammadiyu) ndi ndani, simunthu monga inu? Kodi mukuudzera ufiti pomwe mukuuona?”
Verse 4 — Surah Al-Anbiya 21:4
“(Mneneri Muhammad{s.a.w}) adati: “Mbuye wanga akudziwa zimene zikunenedwa kumwamba ndi pansi; ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa
Verse 5 — Surah Al-Anbiya 21:5
“Koma (osakhulupirira) adati: “(Izi zimene akufotokozazi) ndi maloto opanda pake.” (Ndipo nthawi zina amati:) “Koma zimenezi wazipeka.” (Penanso amati:) “Koma iyeyu ndi mlakatuli. Chonchotu, atibweretsere chizizwa monga mmene adatumiziridwa (aneneri) oyamba.”
Verse 6 — Surah Al-Anbiya 21:6
“Sadakhulupirire apatsogolo pawo, eni midzi imene tidaiononga (ngakhale kuti zozizwitsa adaziona); nanga iwo akhulupirira
Verse 7 — Surah Al-Anbiya 21:7
“Ndipo sitidawatume patsogolo pako, (iwe Mtumiki,) koma anthu, (osati angelo); tidawavumbulutsira (chivumbulutso Chathu.) Choncho, afunseni eni kudziwa ngati inu simukudziwa (nkhani zakale)
Verse 8 — Surah Al-Anbiya 21:8
“Ndipo sitidawachite (aneneriwo) kukhala matupi osadya chakudya ndipo sadalinso okhala nthawi yaitali
Verse 9 — Surah Al-Anbiya 21:9
“Kenako tidawatsimikizira lonjezo (la kuwathangata pa adani awo), ndipo tidawapulumutsa iwo ndi amene tidawafuna (mwa omwe adawatsata), ndipo olumpha malire (a Allah) Tidawaononga
Verse 10 — Surah Al-Anbiya 21:10
“Ndithu tatumiza kwa inu buku lomwe m’kati mwake muli ulaliki wanu (malangizo kwa inu). Kodi simukuzindikira
Verse 11 — Surah Al-Anbiya 21:11
“Ndi ambiri mwa eni midzi yomwe idali yosalungama, tidawaononga; ndipo pambuyo pake tidalenga anthu ena
Verse 12 — Surah Al-Anbiya 21:12
“Pamene adazindikira za chilango chathu, pompo adayamba kuchithawa
Verse 13 — Surah Al-Anbiya 21:13
“Musathawe, (kuthawa sikukupulumutsani), koma bwererani ku zimene mwasangalatsidwa nazo ndi m’malo mwanu, kuti mufunsidwe
Verse 14 — Surah Al-Anbiya 21:14
“Adanena: “Tsoka lathu ndithu! Tidali ochita zoipa.”
Verse 15 — Surah Al-Anbiya 21:15
“Kukuwa kwawoko sikudathe, kufikira tidawapanga ngati (mbewu) zokololedwa, mpaka kupuma kwawo kudazima (adafa)
Verse 16 — Surah Al-Anbiya 21:16
“Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, mwamasewera
Verse 17 — Surah Al-Anbiya 21:17
“Tikadafuna kupanga choti tiziseweretsa (sitidakapanga zomwe mukuzionazi) tikadapanga mwazomwe tili nazo, tikadakhala oti tichite (zachibwana)
Verse 18 — Surah Al-Anbiya 21:18
“Koma (chimene timachita ndi ichi), timachiponya choona pa chachabe ndi kuchiswa bongo bwake, ndipo chachabecho chimachoka. Ndipo chilango chili pa inu chifukwa cha zomwe mukunena (kumnamizira Allah)
Verse 19 — Surah Al-Anbiya 21:19
“Onse akumwamba ndi pansi, Ngake (Allah); ndipo amene ali kwa Iye (angelo), sadzitukumula pakumulambira, ndiponso satopa (ndi mapemphero)
Verse 20 — Surah Al-Anbiya 21:20
“Amamlemekeza usiku ndi usana, ndipo sagwidwa ndi ulesi
Verse 21 — Surah Al-Anbiya 21:21
“Kapena adzipangira milungu yochokera m’nthaka youkitsa akufa, (kotero kuti aichita kukhala milungu yawo mmalo mwa Allah)
Verse 22 — Surah Al-Anbiya 21:22
“Kukadakhala kuti ilipo m’menemo milungu ina (kuthambo ndi pansi) kupatula Allah, (ziwirizi) zikadawonongeka, wapatukana Allah Mbuye wa Arsh (Mpando Wachifumu) ndi zimene akunena (osakhulupirira)
Verse 23 — Surah Al-Anbiya 21:23
“Safunsidwa pa zimene akuchita, koma iwo adzafunsidwa
Verse 24 — Surah Al-Anbiya 21:24
“Kapena adzipangira milungu ina m’malo mwa Iye? Nena: ‘“Bweretsani umboni wanu (pa zimenezi), (izi ndikuuzani) ndichikumbutso kwa awa ali pamodzi ndi ine, ndiponso ndichikumbutso kwa amene adalipo patsogolo panga.” Koma ambiri a iwo sadziwa za choonadi, tero iwo akunyozera
Verse 25 — Surah Al-Anbiya 21:25
“Ndipo sitidatume patsogolo pako mtumiki aliyense koma tidali kumzindikiritsa kuti palibe mulungu wina wompembedza mwachoonadi, koma Ine; choncho ndilambireni
Verse 26 — Surah Al-Anbiya 21:26
“Ndipo (osakhulupirira) akuti: “(Allah) Wachifundo chambiri wadzipangira mwana.” Allah wapatukana (ndi zimenezo) koma (awa angelo) ndi akapolo (a Allah) amene alemekezedwa
Verse 27 — Surah Al-Anbiya 21:27
“Samutsogolera kuyankhula, ndipo iwo amachita molingana ndi malamulo Ake
Verse 28 — Surah Al-Anbiya 21:28
“(Allah) akudziwa zapatsogolo pawo (angelowo) ndi zapambuyo pawo, ndipo (angelowo) sangaombole (aliyense) koma yekhayo (Allah) wamuyanja, ndipo iwo, chifukwa chomuopa, amanjenjemera
Verse 29 — Surah Al-Anbiya 21:29
“Ndipo mwa iwo amene anganene kuti: “Ine ndi mulungu mmalo mwa Iye,” ndiye kuti timulipira Jahannam; umo ndi momwe timawalipirira ochita zoipa
Verse 30 — Surah Al-Anbiya 21:30
“Kodi osakhulupirira sadaone kuti thambo ndi nthaka zidali zophatikizana, ndipo tidazilekanitsa? Ndipo ndi madzi tidalenga chilichonse chamoyo. Kodi sakhulupirira
Verse 31 — Surah Al-Anbiya 21:31
“Ndipo tidaika mapiri panthaka molimbika kuti isagwedezeke ndi iwo, ndipo m’menemo tidaikamo misewu kuti alondole njira (ndikufika komwe afuna)
Verse 32 — Surah Al-Anbiya 21:32
“Ndipo thambo tidalipanga monga tsindwi losungidwa (kuti lisagwe). Koma iwo akuzitembenukira kumbali zizindikiro zake
Verse 33 — Surah Al-Anbiya 21:33
“Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi; chilichonse mwa izo chikusambira mozungulira m’njira mwake
Verse 34 — Surah Al-Anbiya 21:34
“Ife sitidawachite anthu amene adalipo patsogolo pako kukhala okhala nthawi yaitali. Nanga ukafa, kodi iwo adzakhala okhala nthawi yaitali
Verse 35 — Surah Al-Anbiya 21:35
“Chamoyo chilichonse chidzalawa imfa; ndipo tikukuyesani mayeso ndi zinthu zoipa ndi zabwino. Ndipo nonsenu mudzabwerera kwa Ife
Verse 36 — Surah Al-Anbiya 21:36
“Ndipo amene sadakhulupirire akakuona, akungokuchitira chipongwe. “Kodi ndi uyu yemwe akutchula milungu yanu (mwachipongwe)?” Pomwe iwo ndi amene akukana zakutchula (Allah) Wachifundo chambiri
Verse 37 — Surah Al-Anbiya 21:37
“Munthu walengedwa ndi chikhalidwe chokonda zinthu (zake zonse) mwachangu. Posachedwapa ndikusonyezani zisonyezo Zanga; choncho musandifulumizitse (kukubweretserani chilango changa)
Verse 38 — Surah Al-Anbiya 21:38
“Ndipo (osakhulupirira) akuti: “Kodi malonjezo awa adzakwaniritsidwa liti, ngati mukunena zoona?”
Verse 39 — Surah Al-Anbiya 21:39
“Chikhala kuti amene sadakhulupirire akudziwa chilango chimene chidzawapeza panthawi yomwe sangathe kutchinjiriza Moto kunkhope zawo ndi kumisana yawo ndipo kuti sadzathandizidwa, (sakadanena zimenezi)
Verse 40 — Surah Al-Anbiya 21:40
“Koma (Qiyâma) idzawadzera mwadzidzidzi ndi kuwadzidzimutsa; kenako sadzatha kuibweza kapena kupatsidwa danga (kuti achite zomwe sadachite)
Verse 41 — Surah Al-Anbiya 21:41
“Ndipo ndithu atumiki adachitidwa chipongwe patsogolo pako; choncho amene adachita chipongwe mwa iwo, zidawadzera zomwe adali kuzichita chipongwe
Verse 42 — Surah Al-Anbiya 21:42
“Nena: “Kodi ndani angakutetezeni usiku ndi usana ku masautso a (Allah) Wachifundo Chambiri?” Koma iwo akunyozera kukumbuka Mbuye wawo
Verse 43 — Surah Al-Anbiya 21:43
“Kapena ali nayo milungu yowatchinjiriza m’malo mwa Ife? (Milunguyo) siingathe kudzithandiza yokha (nanga ndiye ingathe kuthandiza ena?) Ndipo (milungu) imeneyo siidzasamalidwa ndi Ife
Verse 44 — Surah Al-Anbiya 21:44
“Koma awa (osakhulupirira) tidawasangalatsa ndi makolo awo kufikira nthawi ya moyo wawo idatalika; kodi saona kuti tikulidzera dziko lawo ndikulichepetsa malire ake?. Nanga kodi iwo ndiwo opambana
Verse 45 — Surah Al-Anbiya 21:45
“Nena: “Ndithu ndikukuchenjezani ndi chivumbulutso (cha Allah). Koma agonthi samva kuitana pamene akuchenjezedwa.”
Verse 46 — Surah Al-Anbiya 21:46
“Ndipo kukadawakhudza kumenya kumodzi kwa chilango cha Mbuye wako, ndithudi, (akadadzichepetsa nthawi yomweyo). Akadanena: “Tsoka kwa ife ndithu tidali osalungama.”
Verse 47 — Surah Al-Anbiya 21:47
“Ndipo tsiku la Qiyâma tidzaika masikero achilungamo, choncho mzimu uliwonse sudzachitidwa chinyengo pa chilichonse. Ngakhale (chinthucho) chili cholemera ngati njere ya mpiru, tidzachibweretsa; ndipo tikukwana (kukhala akatswiri) pa chiwerengero
Verse 48 — Surah Al-Anbiya 21:48
“Ndipo ndithu Mûsa ndi Harun tidawapatsa (buku) losiyanitsa pakati pa choonadi ndi chonama, ndiponso muuni ndi ulaliki kwa anthu oopa (Allah)
Verse 49 — Surah Al-Anbiya 21:49
“Omwe akumuopa Mbuye wawo ngakhale ali paokha, omwenso amaopa Qiyâma
Verse 50 — Surah Al-Anbiya 21:50
“Ndipo iyi (Qur’an) ndi ulaliki wodalitsika umene tauvumbulutsa (kwa inu); kodi inu mukuikana
Verse 51 — Surah Al-Anbiya 21:51
“Ndipo ndithu Ibrahim tidampatsa kulungama kwake kuyambira kale (kuubwana), ndipo tinkamudziwa (bwinobwino)
Verse 52 — Surah Al-Anbiya 21:52
“(Akumbutse anthu) pamene adauza bambo wake ndi anthu ake, “Nchiyani mafano awa omwe inu nthawi zonse mukupitiriza kuwapembedza.”
Verse 53 — Surah Al-Anbiya 21:53
“Adati: “Tidapeza makolo athu akuwapembedza. (Choncho nafenso Tikuwapembedza).”
Verse 54 — Surah Al-Anbiya 21:54
“(Iye) adati: “Ndithu inu ndi makolo anu mudali mkusokera koonekera.”
Verse 55 — Surah Al-Anbiya 21:55
“(Iwo) adati: “Kodi watibweretsera choonadi, kapena iwe ndi m’modzi mwa osereula?”
Verse 56 — Surah Al-Anbiya 21:56
“(Iye) adati: (“Iyayi, ine siwosereula), koma Mbuye wanu, ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka amene adalenga zimenezi; ine pa zimenezi, ndine m’modzi wochitira umboni.”
Verse 57 — Surah Al-Anbiya 21:57
““Ndipo ndikulumbilira Allah, ndiwachitira chiwembu mafano anuwo pambuyo ponditembenukira misana kupita komwe mukupita.”
Verse 58 — Surah Al-Anbiya 21:58
“Choncho adawaphwanya (mafanowo) zidutswazidutswa kupatula lalikulu lawo (sadaliswe) kuti iwo alibwelere (ndi kulifunsa zimene zachitika)
Verse 59 — Surah Al-Anbiya 21:59
“(Iwo parnene adafika kumafano awo) adati: “Ndani wachita ichi pa milungu yathu? Ndithu iye ndi m’modzi wa ochita zoipa.”
Verse 60 — Surah Al-Anbiya 21:60
“Adati: “Tidamumva m’nyamata wina akuitchula (moipa); amatchedwa Ibrahim.”
Verse 61 — Surah Al-Anbiya 21:61
“Adati: “Mubweretseni pamaso pa anthu kuti amuone.”
Verse 62 — Surah Al-Anbiya 21:62
“Adati: “Kodi ndiwedi wachita ichi ku milungu yathu, E, iwe Ibrahim?”
Verse 63 — Surah Al-Anbiya 21:63
“(Iye) adati: “(Iyayi), koma wachita ichi ndi mkulu wawoyu. Choncho afunseni (kuti akuuzeni zenizeni) ngati amatha kuyankhula.”
Verse 64 — Surah Al-Anbiya 21:64
“Ndipo adadzitembenukira okha ndikunena kuti: “Ndithu inu ndinu oipa.”
Verse 65 — Surah Al-Anbiya 21:65
“Kenako adazyolitsa mitu yawo (ndikubwerera kuumbuli wawo) nanena kuti: “Ndithu iwe ukudziwa kuti izi siziyankhula (nchifukwa ninji ukutichita chipongwe)?”
Verse 66 — Surah Al-Anbiya 21:66
“(Iye) adati: “Kodi mukupembedza zomwe sizingakuthandizeni chilichonse, kusiya Allah, zomwenso sizingakupatseni masautso?”
Verse 67 — Surah Al-Anbiya 21:67
““Kuyaluka nkwanu ndi zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah. Kodi simuganizira?”
Verse 68 — Surah Al-Anbiya 21:68
“(Iwo) adati: “Mtentheni; ndipo pulumutsani milungu yanu, ngati inu mungathe kuchita zimenezi.”
Verse 69 — Surah Al-Anbiya 21:69
“Tidati: “E iwe Moto! Khala kuzizira ndiponso mtendere kwa Ibrahim.”
Verse 70 — Surah Al-Anbiya 21:70
“Ndipo adamfunira chiwembu; koma tidawachita kukhala otaika zedi
Verse 71 — Surah Al-Anbiya 21:71
“Ndipo tidampulumutsa iye ndi Luti kupita ku dziko lomwe tidalidalitsa ku zolengedwa
Verse 72 — Surah Al-Anbiya 21:72
“Ndipo (Ibrahim) tidampatsa Ishaq ndi kuonjezera Ya’qub, ndipo tidawachita onse kukhala abwino
Verse 73 — Surah Al-Anbiya 21:73
“Ndipo tidawasankha kukhala atsogoleri, owongolera mwa lamulo Lathu, ndipo tidawazindikiritsa kuchita zabwino ndi kupemphera Swala moyenera, ndi kupereka Zakaat; ndipo kwa Ife adali opembeza
Verse 74 — Surah Al-Anbiya 21:74
“Ndipo Luti tidampatsa luntha ndi kuzindikira, ndipo tidampulumutsa ku mudzi womwe anthu ake ankachita zoipa; ndithu iwo adali anthu oipa otuluka m’chilamulo (cha Allah)
Verse 75 — Surah Al-Anbiya 21:75
“Ndipo tidamulowetsa mu chifundo Chathu; ndithu iye adali m’modzi wa ochita zabwino
Verse 76 — Surah Al-Anbiya 21:76
“Ndipo (akumbutse za) Nuh, pamene adatiitana kale (kutipempha). Ndipo Ife tidamuyankha ndi kupulumutsa iye ndi anthu ake ku sautso Ialikulu
Verse 77 — Surah Al-Anbiya 21:77
“Ndipo tidampulumutsa pa anthu amene adatsutsa Ayah Zathu; ndithu iwo adali anthu oipa. Ndipo onse tidawamiza (ndi chigumula chamadzi)
Verse 78 — Surah Al-Anbiya 21:78
“Ndipo (akumbutse za) Daud ndi Sulaiman, pamene ankaweruza mlandu wa munda, pomwe mbuzi za anthu zidadya ndi kuonongaononga usiku mmenemo ndipo Ife tidali mboni pa kuweruza kwawo
Verse 79 — Surah Al-Anbiya 21:79
“Tero tidamzindikiritsa za mlanduwo Sulaiman (kuposa tate wake Daud). Yense wa iwo tidampatsa kuweruza ndi kudziwa; ndipo tidagonjetsa mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Daud zikulemekeza (Allah); ndipo Ife ndi ochita chimene tafuna
Verse 80 — Surah Al-Anbiya 21:80
“Ndipo tidamphunzitsa (Daud) kapangidwe ka chovala chapankhondo chifukwa cha inu kuti chikutetezeni mkumenyana kwanu; kodi simungakhale othokoza
Verse 81 — Surah Al-Anbiya 21:81
“Nayenso Sulaiman tidamugonjetsera mphepo yamphamvu; inkayenda mwa lamulo lake kunka ku dziko lomwe talidalitsa (dziko la Sham); ndipo Ife pa chilichonse Ngodziwa
Verse 82 — Surah Al-Anbiya 21:82
“Ndipo (tidamugonjetseranso) asatana omwe ankamubilira m’madzi (ndikumtolera ngale), ndipo ankachita ntchito zina kuonjezera pa zimenezi; ndipo Ife tidali owasunga (owateteza)
Verse 83 — Surah Al-Anbiya 21:83
“Ndipo akumbutsenso za Ayubu pamene adakuwira Mbuye wake (kuti): “Ndithu mavuto andikhudza, pomwe Inu ndi Achifundo kuposa achifundo!”
Verse 84 — Surah Al-Anbiya 21:84
“Choncho tidavomera (pempho lake); ndipo tidamchotsera mavuto omwe adali nawo, ndipo tidampatsa ana ake ofanana ndi omwe adali nawo kale ndikuonjezeranso ena onga iwo, (zonsezi monga) chifundo chochokera kwa Ife, (ndikuti zikhale) chikumbutso kwa ochita mapemphero
Verse 85 — Surah Al-Anbiya 21:85
“Ndipo (mutchule) Isimaila ndi Idrisa ndi Zul Kifli, onsewa adali mwa opirira
Verse 86 — Surah Al-Anbiya 21:86
“Tidawalowetsanso ku chifundo Chathu, ndithu iwo adali mwa anthu abwino
Verse 87 — Surah Al-Anbiya 21:87
“Ndipo (mtchulenso) Thun-Nun (Yunusu), pamene adachoka uku atakwiya, ndipo ankaganiza (kuti tamuloleza kusamuka) ndikuti sititha kumchita kanthu. Choncho adaitana mu mdima (mammimba mwa nsomba imene idamumeza, kuti): “Ndithu palibe mulungu wina wopembezedwa mwachoonadi koma Inu; mwayeretsedwa; ndithu ine ndidali m’modzi wa odzichitira zoipa.”
Verse 88 — Surah Al-Anbiya 21:88
“Choncho tidavomereza (pempho lake) ndi kumpulumutsa ku madandaulo; umo ndi m’mene timawapulumutsira okhulupirira
Verse 89 — Surah Al-Anbiya 21:89
“Ndipo (akumbutse za) Zakariya pamene adaitana Mbuye wake (kuti): “Mbuye wanga! Musandisiye ndekha; ndithu Inu ndinu wabwino kuposa alowa mmalo onse.”
Verse 90 — Surah Al-Anbiya 21:90
“Choncho tidamuvomera (pempho), ndikumpatsa Yahya ndikumkonzera mkazi wake. Ndithu iwo adali achangu pochita zabwino; ankatipempha mwakhumbo ndi mwamantha, ndipo adali odzichepetsa kwa Ife
Verse 91 — Surah Al-Anbiya 21:91
“Ndipo (atchulire za Mariya) yemwe adauteteza umaliseche wake (podzisunga); ndipo tidauzira mwa iye Mzimu Wathu, ndipo tidamchita iye ndi mwana wake kukhala chizizwa (cha Allah) kwa zolengedwa zonse
Verse 92 — Surah Al-Anbiya 21:92
“Ndithu uwu mpingo wanu, ndimpingo umodzi, ndipo Ine ndine Mbuye wanu; choncho ndipembedzeni
Verse 93 — Surah Al-Anbiya 21:93
“Koma iwo adaswa chinthu chawochi pakati pawo (tero adakhala mipingo yosiyanasiyana). Onse adzabwerera kwa Ife
Verse 94 — Surah Al-Anbiya 21:94
“Ndipo amene achite ntchito zabwino uku ali wokhulupirira, khama lake silidzakanidwa; ndithunso Ife tikumlembera zonse zimene akuchita
Verse 95 — Surah Al-Anbiya 21:95
“Ndipo nkosatheka kwa eni mudzi umene tidauononga chifukwa cha machimo awo kuti asabwelere kwa Ife; (koma ndithu abwerera)
Verse 96 — Surah Al-Anbiya 21:96
“Kufikira pamene Yaajuju ndi Maajuju adzatsekulilidwa (mpanda wawo), ndipo iwo adzakhala akuthamanga kuchokera m’phiri lililonse
Verse 97 — Surah Al-Anbiya 21:97
“Ndipo lonjezo la choonadi lidzafika; pamenepo maso a omwe sadakhulupirire, adzatong’oka uku akunena: “Tsoka pa ife! Ndithu tidali osalabadira (za chinthu) ichi; koma tidali oipa, (odzichitira tokha zoipa.)”
Verse 98 — Surah Al-Anbiya 21:98
“Ndithu inu ndi amene mukuwapembedza kusiya Allah, ndinu nkhuni za ku Jahannam. Ndipo inu (Jahannamyo) mudzalowa
Verse 99 — Surah Al-Anbiya 21:99
“Ngati awa akadakhala milungu yeniyeni, ndiye kuti sakadailowa, mmenemo onse adzakhala nthawi yaitali
Verse 100 — Surah Al-Anbiya 21:100
“Mmenemo iwo adzakhala akubuula ndipo iwo mmenemo sadzamva (chifukwa makutu adzagontha)
Verse 101 — Surah Al-Anbiya 21:101
“Ndithu amene ubwino wathu udawafika, iwo adzatalikitsidwa nawo (motowo)
Verse 102 — Surah Al-Anbiya 21:102
“Sadzamva mavume ake, ndipo iwo adzakhala nthawi yaitali m’zomwe ikukhumba mitima yawo
Verse 103 — Surah Al-Anbiya 21:103
“Kugwedezeka kwakukulu sikudzawadandaulitsa; ndipo angelo adzawalandira (ndikuwauza): “Ili ndi tsiku lanu lomwe mudali kulonjezedwa.”
Verse 104 — Surah Al-Anbiya 21:104
“(Kumbukirani) tsiku lomwe tidzakulunga thambo monga momwe amakulungira makalata okhala ndi malembo m’kati mwake; monga tidayamba kulenga zolengedwa poyamba, tidzabwerezanso (kuzilenga kachiwiri. Ndipo aliyense adzalipidwa pa zomwe adali kuchita) ili ndilonjezo lomwe lili pa Ife. Ndithu Ife ndi Ochita (zomwe tikunena)
Verse 105 — Surah Al-Anbiya 21:105
“Ndipo ndithu tidalemba m’zaburi (mu Masalimo buku la Daud) pambuyo polemba mu chikumbutso (Lauhil-Mahafudh) kuti: “Dziko (lapansi) adzalilowa akapolo Anga abwino.”
Verse 106 — Surah Al-Anbiya 21:106
“Ndithu pazimenezi (nkhani za aneneri), pali miyambo kwa anthu, opembedza (Allah)
Verse 107 — Surah Al-Anbiya 21:107
“Ndipo sitidakutume koma kuti ukhale mtendere kwa zolengedwa zonse
Verse 108 — Surah Al-Anbiya 21:108
“Nena: “Ndithu kukuvumbulutsidwa kwa ine kuti mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi; nanga inu mudzagonjera (zofuna Zake polowa m’Chisilamu)?”
Verse 109 — Surah Al-Anbiya 21:109
“Koma ngati anyozera, nena: “Ndalengeza (uthenga) kwa inu mofanana (popanda tsankho); sindidziwa kuti zomwe mukulonjezedwa zili pafupi kapena zili kutali.”
Verse 110 — Surah Al-Anbiya 21:110
““Ndithu Iye akudziwa mawu okweza, ndiponso akudziwa zomwe mukubisa.”
Verse 111 — Surah Al-Anbiya 21:111
““Ndipo sindikudziwa, mwina kuchedwetsa chilango chanu ndi mayeso akukuyesani ndikukusangalatsani ndi zokoma (za m’dziko) mpaka Idzakwane nthawi yoikidwayo.”
Verse 112 — Surah Al-Anbiya 21:112
“Adati: “E Mbuye wanga! Weruzani moona.” “Ndipo Mbuye wathu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; Wopemphedwa chithandizo pa zimene mukusimbazo.”