Back to Languages

Chichewa - Chapter 22 - Al-Hajj

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Hajj 22:1

“E inu anthu! Opani Mbuye wanu (ndipo kumbukirani tsiku la Kiyâma). Ndithu kugwedezeka kwa Kiyâma ndichinthu chachikulu (kwabasi)

Verse 2 — Surah Al-Hajj 22:2

“Tsiku limene mudzaione (Qiyâmayo), mkazi aliyense woyamwitsa adzaiwala (mwana wake) womuyamwitsa, ndipo (mkazi) aliyense wapakati adzataya pakati pake; ndipo udzawaona anthu ataledzera, pomwe sadaledzere; koma ndi chilango chaukali cha Allah (chimene chawapeza)

Verse 3 — Surah Al-Hajj 22:3

“Ndipo alipo ena mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ndipo akutsatira satana aliyense wolakwa

Verse 4 — Surah Al-Hajj 22:4

“(Za satana), kwalembedwa kuti amene amsankhe kukhala bwenzi lake, ndithu iye amsokeretsa ndi kumtsogolera ku chilango cha Moto

Verse 5 — Surah Al-Hajj 22:5

“E inu anthu! Ngati muli m’chikaiko za kuuka ku imfa, (ndipo mukuona kuti nzosatheka, yang’anani mmene tidakulengerani). Ndithu Ife tidakulengani ndi dothi, ndipo (timakulengani) ndi dontho la umuna, komanso (umunawo udasanduka) gawo lamagazi, kenako gawo la mnofti woumbidwa (chithunzi cha munthu) ndi wosaumbidwa, kuti tikulongosolereni (kukhoza Kwathu;) ndipo Ife timachikhazikitsa mchiberekero; chimene tifuna kufikira nthawi yake yoyikidwa kenako timakutulutsani muli khanda, (tsono timakulerani) kuti mufike pa nsinkhu wanu. Ndipo ena mwa inu amamwalira (asanakule), pomwe ena mwa inu amabwezedwa ku moyo wofooka (waukalamba) kotero kuti asadziwe chilichonse pambuyo pakuti adali wodziwa. Ndipo umaiona nthaka ili chetee, koma tikatsitsa madzi pamwamba pake, imagwedezeka ndi kufufuma, ndi kumeretsa mtundu uliwonse wa mmera wokongola

Verse 6 — Surah Al-Hajj 22:6

“Zimenezo (monga kulenga munthu ndi kumeretsa mmera, ndi umboni wosonyeza) kuti Allah Woona alipo; ndikuti Iye amaukitsa akufa, ndiponso Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse

Verse 7 — Surah Al-Hajj 22:7

“Ndipo, ndithu Qiyâma idza; palibe chikaiko pa zimenezi, ndipo ndithu Allah adzawatulutsa amene ali m’manda

Verse 8 — Surah Al-Hajj 22:8

“Ndipo alipo mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika, (koma makani basi ndi kungotsata zimene akuziganizira)

Verse 9 — Surah Al-Hajj 22:9

“(Yemwe) akupinda khosi lake (chifukwa chodzikuza) kuti asokereze (anthu powachotsa) kunjira ya Allah; pa iye pali chilango choyalutsa pa moyo uno, ndipo patsiku la Qiyâma tikamulawitsa chilango cha Moto wotentha

Verse 10 — Surah Al-Hajj 22:10

“(Tidzamuuza kuti): “Izi ndi zomwe manja ako adatsogoza; ndithu Allah siwachinyengo kwa akapolo (Ake).”

Verse 11 — Surah Al-Hajj 22:11

“Ndipo alipo wina mwa anthu amene akupembedza Allah cham’mphepete (mwachipembedzo). Chabwino chikampeza amatonthola nacho; koma masautso akamufika, amatembenuka ndi nkhope yake (posiya chikhulupiliro mwa Allah. Choncho) waluza moyo wa dziko lapansi ndi moyo wa tsiku la chimaliziro; kumeneko ndiko kuluza koonekera

Verse 12 — Surah Al-Hajj 22:12

“M’malo mwa Allah, amapembedza zomwe sizingampatse masautso (ngati ataleka kuzipembedza), ndiponso zomwe sizingampatse chithandizo (akamazipembedza), ndipo kumeneko ndiko kusokera konka nako kutali

Verse 13 — Surah Al-Hajj 22:13

“Akupembedza omwe masautso awo ali pafupi zedi poyerekeza ndi zabwino zawo, taonani kuipa atetezi ndiponso ndi abwenzi oipa

Verse 14 — Surah Al-Hajj 22:14

“Ndithu Allah adzawalowetsa ku Minda yamtendere amene akhulupirira ndikuchita zabwino, mitsinje ikuyenda pansi (pa mindayo). Ndithu Allah amachita chimene wafuna

Verse 15 — Surah Al-Hajj 22:15

“Amene akuganiza kuti Allah samthangata (Mtumiki Wake) pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro, amange chingwe kudenga, kenako adzipachike (ngati safuna kuona Chisilamu chikufala); ndipo aone kuti kodi ndale zakezo zichotsa zimene zamkwiitsazo

Verse 16 — Surah Al-Hajj 22:16

“Momwemonso taivumbulutsa (Qur’an) kuti ikhale mawu omveka; ndipo ndithu Allah amaongola amene wamfuna

Verse 17 — Surah Al-Hajj 22:17

“Ndithu amene akhulupirira, ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi chipembedzo cha Sabia; ndi Akhrisitu, ndi Maajusi (opembedza moto), ndi ophatikiza Allah ndi mafano, ndithu Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chiweruziro (Qiyâma). (Osokera adzaponyedwa ku Moto ndipo olungama adzawalowetsa ku Munda wamtendere). Ndithu Allah ndi Mboni pa chinthu chilichonse

Verse 18 — Surah Al-Hajj 22:18

“Kodi suona kuti Allah zikumulambira zimene zili kumwamba ndi zimene zili m’nthaka, kudzanso dzuwa, mwezi, nyenyezi mapiri, mitengo, nyama ndi anthu ambiri. Koma ambirinso chilango chatsimikizika pa iwo. Ndipo amene Allah wamuyalutsa, palibe amene angampatse ulemelero; ndithu Allah amachita chimene wafuna

Verse 19 — Surah Al-Hajj 22:19

“Awa ndi magulu awiri amene akangana pa za Mbuye wawo (pa zomwe zili zomuyenera, ndi zosamuyenera, ndipo ena sadakhulupirire.) Choncho amene sadakhulupirire, adzawadulira nsalu za ku Moto ndi kuwaveka; ndipo pamwamba pa mitu yawo padzathiridwa madzi otentha

Verse 20 — Surah Al-Hajj 22:20

“Chifukwa cha madziwo zidzasungunuka zomwe zili m’mimba mwawo ndiponso makungu (awo)

Verse 21 — Surah Al-Hajj 22:21

“Ndipo (kuonjezera pa zimenezi) adzakhala nazo nyundo zachitsulo (zowamenyera)

Verse 22 — Surah Al-Hajj 22:22

“Nthawi iliyonse akafuna kutuluka m’menemo, chifukwa chakumva kupweteka, adzabwezedwa momwemo (ndipo angelo uku akuwamenya ndi nyundo), ndi (kuwauza): “Chilaweni chilango chootcha.”

Verse 23 — Surah Al-Hajj 22:23

“Ndithu Allah adzalowetsa amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, ku Minda ya mtendere komwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi pasogolo) pake; m’menemo akavekedwa (ndi angelo) zibangili za golide ndi ngale; ndipo zovala zawo m’menemo zidzakhala za silika

Verse 24 — Surah Al-Hajj 22:24

“Ndipo adzatsogozedwa (kupita kumalo) kokamba mawu abwino okhaokha; ndiponso adzatsogozedwa ku njira ya Mwini kutamandidwa (kunjira yonkera ku Jannah)

Verse 25 — Surah Al-Hajj 22:25

“Ndithu. amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndipo nkumatsekereza ena ku njira ya Allah, (ndiponso nkumatsekereza kulowa) mu Msikiti Wopatulika umene tidauchita kuti ukhale wa anthu onse mofanana kwa amene akukhala m’menemo ndi kwa alendo, (anthu otere tidzawalanga ndi chilango chaukali), ndipo aliyense wofuna kuchita zopotoka m’menemo mosalungama, timulawitsa chilango chowawa zedi

Verse 26 — Surah Al-Hajj 22:26

“Ndipo (kumbukira) pamene tidamkhazika Ibrahim (ndi kumlondolera) pamalo pa Nyumba (yopatulikayo; tidamuuza kuti): “Usandiphatikize ndi chilichonse; ndipo iyeretse nyumba yanga chifukwa cha amene akuizungulira ndi kumakhala pompo (pochita mapemphero awo); ndi omwe amawerama ndi kugwetsa nkhope zawo pansi

Verse 27 — Surah Al-Hajj 22:27

“Ndipo (tidamuuza): “Lengeza kwa anthu za Hajj; akudzera (ena) oyenda ndi mapazi, ndipo (ena ali) pamwamba pa chiweto choonda (chifukwa chamasautso a paulendo); adza kuchokera kunjira zamtalimtali

Verse 28 — Surah Al-Hajj 22:28

“Kuti adzaone zabwino zawo, ndikuti (achulukitse) kutchula dzina la Allah m’masiku odziwika (ubwino wake), kupyolera m’zimene wawapatsa monga ziweto za miyendo inayi. Ndipo idyani ina mwa nyamayo ndi kum’dyetsa wovutika, wosauka

Verse 29 — Surah Al-Hajj 22:29

“Kenako adziyeretse kuzitakataka zawo, ndipo akwaniritse naziri (malonjezo) zawo ndikuzungulira nyumba yakale

Verse 30 — Surah Al-Hajj 22:30

“Umo ndi momwe zikhalire; ndipo amene alemekeze zinthu zopatulika za Allah kutero ndi bwino kwa iyeyo pamaso pa Mbuye wake. Ndipo ziweto za miyendo inayi nzovomerezeka kwa inu kuzidya, kupatula zomwe zatchulidwa kwa inu (m’Qur’an kuti nzoletsedwa); choncho upeweni uve wa mafano, ndiponso pewani mawu abodza

Verse 31 — Surah Al-Hajj 22:31

“Uku mutapendekera kwa Allah Yekha, osati kum’phatikiza (Allah). Ndipo amene akuphatikiza Allah ndi mafano, ali ngati wogwa kuchokera kumwamba, kenako mbalame nkumuwakha, kapena mphepo kukamtaya malo akutali

Verse 32 — Surah Al-Hajj 22:32

“Zimenezo ndikuti amene alemekeze zizindikiro za chipembedzo cha Allah, kutero ndichinthu choonetsa kuopa Allah m’mitima

Verse 33 — Surah Al-Hajj 22:33

“(Ziweto zimene mukutumiza ku Makka monga nsembe) muli nazo zithandizo mmenemo (monga kukwera ndi kukama mkaka) kufikira nthawi yodziwika, (yomwe ndi nthawi yozizingira); kenako malo ozizingira ndi pafupi ndi Nyumba yakalekaleyo

Verse 34 — Surah Al-Hajj 22:34

“Ndipo mpingo uliwonse tidaupangira malo ozingira nsembe zamapemphero kuti atchule dzina la Allah pa zomwe wawapatsa monga ziweto zamiyendo inayi. Choncho mulungu wanu ndi Mulungu m’modzi Yekha; gonjerani kwa Iye; ndipo odzichepetsa auze nkhani yabwino

Verse 35 — Surah Al-Hajj 22:35

“Omwe Allah akatchulidwa, mitima yawo imanjenjemera ndiponso amapirira pa zomwe zawapeza, ndipo amapemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka kuchokera m’zomwe tawapatsa

Verse 36 — Surah Al-Hajj 22:36

“Ndipo ngamira (ng’ombe, mbuzi ndi mbelere) tadzichita kwa inu kuti zikhale mwa zizindikiro za chipembedzo cha Allah; m’zimenezo muli zabwino kwa inu; choncho litchuleni dzina la Allah pa izo pamene zikuima mondanda (uku mukuzizinga,) ndipo zikagwa cham’nthiti, idyani (nyama yake) ndikumdyetsa yemwe akungozungulirazungulira, wosapempha ndi wopempha yemwe. Momwemo tazigonjetsa kwa inu (pochita kuti zikugonjereni) kuti muthokoze

Verse 37 — Surah Al-Hajj 22:37

“(Nyamazo) Allah siimfika minofu yake ngakhale magazi ake, koma kuopa kuchokera mwa inu ndiko kumene kumamfika; momwemo wazichita (nyamazo) kukhala zogonjera inu kuti mumlemekeze Allah chifukwa cha kukuongolaniku. Auze nkhani yabwino ochita zabwino

Verse 38 — Surah Al-Hajj 22:38

“Ndithu Allah amawateteza amene akhulupilira, ndithu Allah sakonda aliyense wachinyengo, wosathokoza

Verse 39 — Surah Al-Hajj 22:39

“Chaperekedwa chilolezo kwa (Asilamu) amene akuputidwa (ndi adani awo kuti abwezere) chifukwa chakuti iwo achitiridwa zoipa; ndipo ndithu Allah ngokhoza kuwathandiza

Verse 40 — Surah Al-Hajj 22:40

“Omwe atulutsidwa m’nyumba zawo popanda chilungamo, koma pachifukwa chakuti akunena: “Mbuye wathu ndi Allah.” Ndipo pakapanda Allah kukankha anthu ena kupyolera mwa ena, (popatsa ena mphamvu kuti agonjetse ena), ndiye kuti Masinagogi, Matchalitchi, nyumba zina zopempheleramo ndi Misikiti momwe dzina la Allah likutchulidwa mochuluka zikadagumulidwa. Ndithu Allah am’thangata amene akuthangata chipembedzo Chake; ndithu Allah Ngwanyonga, Wogonjetsa chilichonse

Verse 41 — Surah Al-Hajj 22:41

“Omwe akuti tikawakhazika pa dziko mwa ubwino, amachita mapemphero a Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, ndi kulamula zabwino ndi kuletsa zoipa; ndipo mabwelero a zinthu nkwa Allah basi

Verse 42 — Surah Al-Hajj 22:42

“Ndipo ngati akukuyesa wabodza, (awa Akafiri, sizachilendo), ndithu adatsutsanso (aneneri awo) patsogolo pawo anthu a Nuh, Aadi, a Samudu

Verse 43 — Surah Al-Hajj 22:43

“Anthu a Ibrahim, anthu a Luti

Verse 44 — Surah Al-Hajj 22:44

“Ndi anthu a ku Madiyan; nayenso Mûsa adayesedwa wabodza (adamkana). Ndipo osakhulupirira ndidawapatsa nthawi, kenako ndidawathira m’dzanja. Nanga chidali bwanji chilango changa

Verse 45 — Surah Al-Hajj 22:45

“Ndi midzi ingati tidaiononga yomwe inkachita zoipa? Zipupa zitagwera pa madenga ake. Ndipo ndi zitsime (zingati) zomwe zidasiidwa, ndi nyumba zikuluzikulu zomwe zidali zolimba

Verse 46 — Surah Al-Hajj 22:46

“Kodi sayendayenda pa dziko kuti akhale ndi mitima (yanzeru) yowazindikiritsa ndi makutu omvera? Ndithu maso sagwidwa khungu, (khungu loononga chipembedzo), koma mitima yomwe ili m’zifuwa ndi imene imagwidwa khungu (loononga chipembedzo)

Verse 47 — Surah Al-Hajj 22:47

“Ndipo akukufulumizitsa kuti udzetse chilango. Komatu Allah sadzaswa lonjezo Lake (limene adaliika lakuti chilango chenicheni chidzakhala patsiku la chimaliziro). Ndipo ndithu tsiku limodzi kwa Mbuye wako lili ngati zaka chikwi chimodzi mukawerengedwe kanu

Verse 48 — Surah Al-Hajj 22:48

“Kodi ndi (anthu a) midzi ingati amene ndidawapatsa nthawi pomwe ankachita zoipa? Kenako ndidawathira m’dzanja. Ndipo kwa Iye nkobwerera

Verse 49 — Surah Al-Hajj 22:49

“Nena: “E inu anthu! Ndithu ine kwa inu ndine Mchenjezi woonekera.”

Verse 50 — Surah Al-Hajj 22:50

““Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, chikhululuko ndi rizq laulemu zili pa iwo.”

Verse 51 — Surah Al-Hajj 22:51

““Ndipo amene akulimbikira kulimbana ndi Ayah Zathu, iwowo ndi anthu a ku Moto.”

Verse 52 — Surah Al-Hajj 22:52

“Ndipo palibe pamene tidatuma mtumiki ngakhale m’neneri patsogolo pako, koma akamawerenga, satana amaponya (zosokoneza) m’kuwerenga kwakeko; koma Allah amachotsa zomwe satana akuponya; kenako nkuzilongosola Ayah Zake. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Wanzeru zakuya

Verse 53 — Surah Al-Hajj 22:53

“(Izi zimachitika) kuti achichite chimene satana akuponya kukhala mayeso kwa omwe m’mitima mwawo muli matenda ndi ouma mitima yawo; ndithu osalungama ali m’kusiyana komwe kuli kutali (ndi choonadi)

Verse 54 — Surah Al-Hajj 22:54

“Ndipo kuti adziwe amene apatsidwa kuzindikira kuti chimenechi n’choonadi chochokera kwa Mbuye wako ndi kuchikhulupirira ndikuti mitima yawo idzichepetse kwa Iye; ndithu Allah ndi Woongolera ku njira yolunjika amene akhulupirira

Verse 55 — Surah Al-Hajj 22:55

“Ndipo amene sadakhulupirire apitilira kukhala m’chikaiko ndi chimenecho (wadza nachocho) kufikira tsiku la chimaliziro liwadzera mowatutumutsa, kapena chiwadzera chilango pa tsiku lopanda chabwino (kwa iwo)

Verse 56 — Surah Al-Hajj 22:56

“Ufumu tsiku limenelo ngwa Allah; adzaweruza (mwachilungamo) pakati pawo; choncho amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala m’Minda yamtendere

Verse 57 — Surah Al-Hajj 22:57

“Ndipo amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndikutsutsa Ayah Zathu, iwo adzapeza chilango choyalutsa

Verse 58 — Surah Al-Hajj 22:58

“Ndipo amene asamuka chifukwa cha chipembedzo cha Allah, kenako ndikuphedwa kapena kufa, ndithu Allah adzawapatsa (patsiku la chiweruziro) zopatsa zabwino. Ndithu Allah Ngwabwino popatsa kuposa opatsa

Verse 59 — Surah Al-Hajj 22:59

“Ndithu adzawalowetsa pamalo pomwe adzapayanja. Ndithu Allah Ngodziwa; Ngodekha

Verse 60 — Surah Al-Hajj 22:60

“Zimenezi zili chonchi, ndipo yemwe akubwezera kulanga molingana ndi momwe iye adalangidwira; kenakonso nkuchitidwa mtopola, ndithu Allah amthangata; Allah Ngofufuta uchimo; Wokhululuka kwambiri

Verse 61 — Surah Al-Hajj 22:61

“Zimenezo nchifukwa chakuti Allah amalowetsa usiku mu usana ndikulowetsa usana mu usiku, ndi chifukwanso chakuti ndithu Allah Ngwakumva Ngopenya

Verse 62 — Surah Al-Hajj 22:62

“Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Wowona (alipo;) ndipo zimene akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo Allah Ngwapamwambamwamba Ngwamkulu

Verse 63 — Surah Al-Hajj 22:63

“Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo nthaka imakhala yobiriwira? Ndithu Allah Ngodziwa zobisika ndiponso Ngodziwa zoonekera

Verse 64 — Surah Al-Hajj 22:64

“Zakumwamba ndi zapansi zonse ndizake; ndithu Allah Ngwachikwanekwane; Wotamandidwa

Verse 65 — Surah Al-Hajj 22:65

“Kodi sudaone kuti Allah wakufewetserani zonse zam’nthaka ndi zombo zomwe zikuyenda panyanja mwa lamulo Lake? Ndipo wagwira thambo kuti lisagwe panthaka koma kupyolera m’chilolezo Chake; ndithu Allah Ngodekha kwa anthu Ngwachifundo

Verse 66 — Surah Al-Hajj 22:66

“Ndipo Iye ndi Amene adakupatsani moyo; kenako adzakupatsani imfa, ndipo kenako adzakuukitsani; ndithu munthu ngosathokoza

Verse 67 — Surah Al-Hajj 22:67

“Mpingo uliwonse tidauikira machitidwe amapemphero omwe akuwatsata; choncho asatsutsane nawe pachinthu ichi, ndipo itanira anthu ku chipembedzo cha Mbuye wako. Ndithu iwe uli pachiongoko changwilo

Verse 68 — Surah Al-Hajj 22:68

“Ndipo ngati atsutsana nawe, nena: “Allah Ngodziwa koposa zimene mukuchita.”

Verse 69 — Surah Al-Hajj 22:69

““Allah adzaweruza pakati panu tsiku la Qiyâma pa zimene mudali kusiyana.”

Verse 70 — Surah Al-Hajj 22:70

“Kodi sudziwa kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zapansi? Ndithu zonsezo zili m’kaundula (Wake), ndithu (kudziwika kwa) zimenezo kwa Allah nzosavuta

Verse 71 — Surah Al-Hajj 22:71

“Ndipo akupembedza milungu yabodza, kusiya Allah, yomwe (Allah) sadaitumizire umboni wakuti (ipembedzedwe) yomwenso iwo sakuidziwa bwino. Ndipo anthu osalungama sadzakhala ndi owathandiza

Verse 72 — Surah Al-Hajj 22:72

“Koma Ayah Zathu zomveka zikawerengedwa kwa iwo, uona kunyansidwa pankhope za amene sadakhulupirire. Ndipo amakhala pafupi kuwamenya amene amawawerengera Ayah Zathu. Nena: “Kodi ndikuuzeni zoipa kwambiri kuposa izi? Ndi Moto (wa Allah) umene wawalonjeza amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) amenewo ndi mabwelero oipa zedi.”

Verse 73 — Surah Al-Hajj 22:73

“E inu anthu! Fanizo laperekedwa; choncho limvereni. Ndithu amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah, sangathe kulenga ntchentche ngakhale Atasonkhana (kuti athandizane) pachimenechi. Ndipo ngati ntchenche itawalanda chinthu, sangathe kuchilanda kuntchentcheyo. Wafooka kwenikweni wopempha ndi wopemphedwa

Verse 74 — Surah Al-Hajj 22:74

“Sadamlemekeze Allah, kulemekeza komuyenera. Ndithu Allah Ngwamphamvu Ngogonjetsa chilichonse

Verse 75 — Surah Al-Hajj 22:75

“Allah amasankha atumiki mwa angelo ndi mwa anthu. Ndithu Allah Ngwakumva; Ngopenya

Verse 76 — Surah Al-Hajj 22:76

“Akudziwa zimene zili patsogolo pawo ndi zimene zili pambuyo pawo; kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu

Verse 77 — Surah Al-Hajj 22:77

“E inu amene mwakhulupirira! Weramani ndikugwetsa nkhope zanu pansi ndipo mpembedzeni Mbuye wanu ndikuchita zabwino kuti mupambane

Verse 78 — Surah Al-Hajj 22:78

“Ndipo menyerani chipembedzo cha Allah, kumenyera kwa choonadi; Iye ndi Amene adakusankhani (kuti mukhale mpingo wabwino;) ndipo sadaike pa inu zinthu zolemera pa chipembedzo, ndi chipembedzo cha tate wanu Ibrahim. Iye (Allah) adakutchani Asilamu kuyambira kale (m’mabuku akale) ndi mu iyi, (Qur’an) kuti Mtumiki akhale mboni pa inu, inunso kuti mukhale mboni pa anthu. Choncho pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat ndipo gwirizanani chifukwa cha Allah. Iye ndiye Mbuye wanu, Mbuye wabwino zedi, ndi Mthandizi wabwino zedi