Back to Languages

Chichewa - Chapter 23 - Al-Muminun

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Muminun 23:1

“۞ Ndithu apambana okhulupirira (mwa Allah)

Verse 2 — Surah Al-Muminun 23:2

“Amene amakhudzumuka pa mapemphero awo (poipereka mitima yawo kwa Allah modzichepetsa)

Verse 3 — Surah Al-Muminun 23:3

“Ndi omwe amapewa zinthu zopanda pake (zachabe)

Verse 4 — Surah Al-Muminun 23:4

“Ndi omwe amakwaniritsa (nsanamira ya) chopereka (Zakaat)

Verse 5 — Surah Al-Muminun 23:5

“Ndi omwe amasunga umaliseche wawo

Verse 6 — Surah Al-Muminun 23:6

“Kupatula kwa akazi awo ndi adzakazi omwe manja awo akumanja apeza. Choncho iwo (pakukumana ndi amenewo) saali odzudzulidwa

Verse 7 — Surah Al-Muminun 23:7

“Koma omwe angafune zosemphana ndi izi (kulumikizana ndi mkazi posiya njira ziwirizi) iwowo ndiwo opyola malire (a Allah)

Verse 8 — Surah Al-Muminun 23:8

“Ndi amene amasunga malonjezo awo ndi zomwe akhulupirika nazo

Verse 9 — Surah Al-Muminun 23:9

“Ndi omwe akusunga mapemphero awo (popemphera mu nthawi zake ndi kutsata malamulo ake uku ali odzichepetsa)

Verse 10 — Surah Al-Muminun 23:10

“Iwo ndi olandira (zabwino tsiku la Qiyâma)

Verse 11 — Surah Al-Muminun 23:11

“Amene adzalandira Munda wamtendere (wotchedwa) Fir’dausi (Munda wapamwamba kwambiri). M’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali

Verse 12 — Surah Al-Muminun 23:12

“Ndipo ndithu tidamlenga munthu kuchokera ku dongo labwino

Verse 13 — Surah Al-Muminun 23:13

“Kenako tidalenga ana ake ndi dontho lamadzi (ambewu ya munthu) lomwe lidaikidwa pamalo osungidwa

Verse 14 — Surah Al-Muminun 23:14

“Kenako tidalisintha dontholo kukhala magazi oundana; ndipo kenako magaziwo tidawasintha kukhala m’nofu; ndipo kenako m’nofu tidausintha kukhala mafupa; ndipo mafupawo tidawaveka minofu, kenako tidamsintha kukhala cholengedwa china. Choncho watukuka Allah, Wabwino polenga

Verse 15 — Surah Al-Muminun 23:15

“Kenako ndithu inu pambuyo pa zimenezo mudzamwalira

Verse 16 — Surah Al-Muminun 23:16

“Ndithu inu, kenako mudzaukitsidwa pa tsiku la Qiyâma

Verse 17 — Surah Al-Muminun 23:17

“Ndipo ndithu tapanga njira zisanu ndi ziwiri (mitambo) pamwamba panu, ndipo ndithu (Ife) sitisiya kulabadira zolengedwa

Verse 18 — Surah Al-Muminun 23:18

“Ndipo tatsitsa madzi mwamuyeso kuchokera kumwamba, ndi kuwakhazikitsa m’nthaka; ndipo ndithu Ife ndi okhoza kuwachotsa (kuti musathandizike nawo, koma sitidachite zimenezo chifukwa chokuchitirani chifundo)

Verse 19 — Surah Al-Muminun 23:19

“Ndi madzi amenewo, tidakupangirani minda ya kanjedza ndi mpesa, m’menemo inu mulinazo zipatso zambiri; ndipo mwazimenezo mumadya

Verse 20 — Surah Al-Muminun 23:20

“Ndipo (tidakupangirani) mtengo womera pa phiri la Sinai, womwe umatulutsa mafuta; ndipo ndindiwo kwa amene amadya. (Mtengo wake ndi mzitona)

Verse 21 — Surah Al-Muminun 23:21

“Ndipo ndithu m’ziweto muli lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwake; ndipo m’zimenezo mukupeza zothandiza zambiri; ndipo zina mwa izo mumadya

Verse 22 — Surah Al-Muminun 23:22

“Ndipo pa msana pa izo ndi pamwamba pa zombo, mumanyamulidwa

Verse 23 — Surah Al-Muminun 23:23

“Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah! Mulibe mulungu wina woti nkumpembedza kupatula Iye. Kodi simuopa (chilango Chake)

Verse 24 — Surah Al-Muminun 23:24

“Akuluakulu mwa anthu ake amene sadakhulupirire, adati: “Uyu sali kanthu, koma ndi munthu ngati inu; akufuna kuti adzipezere ubwino pa inu; ndipo Allah akadafuna (kukuphunzitsani) akadatuma angelo. Zoterezi sitidamvepo kumakolo athu akale.”

Verse 25 — Surah Al-Muminun 23:25

““Uyu sali kanthu, koma ndi munthu wamisala; choncho muyembekezereni mpaka nthawi (yofera.”)

Verse 26 — Surah Al-Muminun 23:26

“(Nuh) adati: “Mbuye wanga ndipulumutseni pazomwe anditsutsa!”

Verse 27 — Surah Al-Muminun 23:27

“Choncho tidamuvumbulutsira (mawu akuti): “Panga chombo moyang’aniridwa ndi kudziwitsidwa ndi Ife.” Ndipo lamulo Lathu likadza ndi kufwamphuka madzi mu uvuni, lowetsa mkati mwake (mwa chombocho) chilichonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi ndi banja lako, kupatula yemwe liwu latsogola pa iye kuti aonongeke mwa iwo. Ndipo usandilankhule za omwe adzichitira (okha) zoipa ndithu iwo amizidwa (m’madzi)

Verse 28 — Surah Al-Muminun 23:28

“Ndipo ukakhazikika m’chombocho, iwe ndi amene uli nawo, nena: “Tikuthokoza Allah, amene watipulumutsa ku anthu osalungama.”

Verse 29 — Surah Al-Muminun 23:29

“Ndipo (potsika), nena: “E Mbuye wanga! Nditsitseni; kutsitsa kwa madalitso, pakuti Inu ndinu wotsitsa bwino kwambiri kuposa otsitsa.”

Verse 30 — Surah Al-Muminun 23:30

“Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo. Ndithu Ife tili (ndi udindo) wowayesa ndi mayeso osiyanasiyana

Verse 31 — Surah Al-Muminun 23:31

“Kenako tidabweretsa m’badwo wina pambuyo pawo (omwe ndi Âdi)

Verse 32 — Surah Al-Muminun 23:32

“Ndipo tidatuma kwa iwo mtumiki (Hûd) wochokera mwa iwo, (yemwe ankati): “Pembedzani Allah! Mulibe mulungu wina kupatula Iye. Kodi simuopa

Verse 33 — Surah Al-Muminun 23:33

“Ndipo akuluakulu a mwa anthu ake amene adali osakhulupirira, ndikutsutsa za kukumana ndi tsiku la chimaliziro, omwe tidawapatsa kulemera pa moyo wa padziko lapansi, adati: “Uyu saali kanthu, koma ndi munthu monga inu; amadya zimene inu mumadya, ndi kumwa zomwe inu mumamwa

Verse 34 — Surah Al-Muminun 23:34

“Koma ngati mumvera munthu wonga inu, ndiye kuti mukhala otaika (oluza)

Verse 35 — Surah Al-Muminun 23:35

“Kodi akukulonjezani kuti mukadzafa ndikusanduka dothi ndi mafupa, mudzaukitsidwanso (m’manda)

Verse 36 — Surah Al-Muminun 23:36

“Sizingachitike, sizingachitike, zimene mukulonjezedwazi

Verse 37 — Surah Al-Muminun 23:37

“Palibe (moyo wina) koma moyo wathu wapadziko lapansiwu basi! Tikufa ndiponso kukhala ndi moyo! Ndipo sitidzaukitsidwa m’manda

Verse 38 — Surah Al-Muminun 23:38

“Uyu saali kanthu (amene akudzitcha kuti ndi Mtumiki) koma ndi munthu basi, akupekera Allah bodza, ndipo ife sitimkhulupirira.”

Verse 39 — Surah Al-Muminun 23:39

“(Mtumikiyo) adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni pachifukwa chakuti anditsutsa.”

Verse 40 — Surah Al-Muminun 23:40

“(Allah) adati: “Posachedwapa akhala odzinena.”

Verse 41 — Surah Al-Muminun 23:41

“Choncho, mkuwe wa (chilango) choonadi udawaononga, ndipo tidawachita ngati zinyalala (zongotengedwa ndi madzi). Choncho, kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osalungama

Verse 42 — Surah Al-Muminun 23:42

“Ndipo titatero tidalenga mibadwo ina pambuyo pawo

Verse 43 — Surah Al-Muminun 23:43

“Palibe mtundu ungaifulumizitse kapena kuichedwetsa nthawi yake yofera

Verse 44 — Surah Al-Muminun 23:44

“Kenaka tidatuma atumiki Athu motsatizana; (wina pambuyo pa mnzake). Ndipo mbadwo uliwonse pamene adaufikira mtumiki wake, udamtsutsa; ndipo tidawaononga motsatana; ndipo tidawachita kukhala nkhani (za anthu.) Ndipo kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osakhulupirira

Verse 45 — Surah Al-Muminun 23:45

“Zitatero tidatuma Mûsa ndi m’bale wake Harun ndi zozizwitsa Zathu, ndi umboni woonekera poyera

Verse 46 — Surah Al-Muminun 23:46

“Kwa Farawo ndi nduna zake. Koma onse adadzitukumula; ndipo adali anthu odzikweza

Verse 47 — Surah Al-Muminun 23:47

“Ndipo adati: “Ha! Tikhulupirire anthu awiri onga ife, omwe mtundu wawo ndi akapolo athu!”

Verse 48 — Surah Al-Muminun 23:48

“Choncho adawatsutsa onse awiri, ndipo adali m’gulu la oonongedwa

Verse 49 — Surah Al-Muminun 23:49

“Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku kuti iwo aongoke

Verse 50 — Surah Al-Muminun 23:50

“Ndipo tidamchita mwana wa Mariya ndi mayi wake kukhala chisonyezo (choonetsa kukhoza kwathu). Ndipo tidawapatsa malo othawirapo, pachikweza, chokhazikika pomwenso padali akasupe

Verse 51 — Surah Al-Muminun 23:51

“E inu Atumiki! Idyani zakudya zabwino, ndipo chitani zabwino. Ndithu Ine ndi Wodziwa zonse zimene muchita

Verse 52 — Surah Al-Muminun 23:52

“(Tidauza mibadwo yawo): “Ndithu mpingo wanuwu ndi mpingo umodzi, ndipo Ine Ndine Mbuye wanu; choncho ndiopeni.”

Verse 53 — Surah Al-Muminun 23:53

“Koma adadula chinthu chawochi (chipembedzo chawo) pakati pawo mipatukomipatuko; gulu lililonse limasangalalira chimene lili nacho

Verse 54 — Surah Al-Muminun 23:54

“Choncho, asiye mu umbuli wawo kufikira nthawi (yakufa kwawo)

Verse 55 — Surah Al-Muminun 23:55

“Kodi akuganiza kuti tikamawapatsa chuma ndi ana

Verse 56 — Surah Al-Muminun 23:56

“Tikuwafulumizitsira zabwino? Sichoncho, koma iwo sakuzindikira

Verse 57 — Surah Al-Muminun 23:57

“Ndithu amene amakhala amantha chifukwa choopa Mbuye wawo, (ndi m’mene mathero awo adzakhalire)

Verse 58 — Surah Al-Muminun 23:58

“Ndi omwe amakhulupirira Ayah za Mbuye wawo

Verse 59 — Surah Al-Muminun 23:59

“Ndi omwenso saphatikiza Mbuye wawo ndi mafano

Verse 60 — Surah Al-Muminun 23:60

“Ndi omwenso amapereka (Zakaat ndi sadaka kuchokera m’chuma) chimene apatsidwa, uku mitima yawo ili yoopa kuti adzabwerera kwa Mbuye wawo

Verse 61 — Surah Al-Muminun 23:61

“Amenewa ndiamene akuchita changu pa zinthu zabwino, ndipo iwo akutsogolera (ena) pa zimenezo

Verse 62 — Surah Al-Muminun 23:62

“Ndipo sitikakamiza munthu, koma chimene angathe (kuchichita). Ndipo tili naye kaundula (wosunga chilichonse) yemwe adzayankhula choonadi ndipo iwo sadzaponderezedwa

Verse 63 — Surah Al-Muminun 23:63

“Koma mitima yawo ili m’kusalabadira mu ichi; ndipo iwo ali ndi ntchito zimene akuchita, osati izi

Verse 64 — Surah Al-Muminun 23:64

“Kufikira tikadzawaika m’chilango amene ali opeza bwino awo, pompo adzakuwa (ndi kupempha chipulumutso)

Verse 65 — Surah Al-Muminun 23:65

“(Kudzanenedwa kwa iwo): “Musalire lero (ndi kupempha chipulumutso)! Ndithu inu simupulumutsidwa ndi Ife.”

Verse 66 — Surah Al-Muminun 23:66

““Ndipo Ayah Zanga zinkawerengedwa kwa inu koma munkadzibwezera kumbuyo ndi zidendene zanu

Verse 67 — Surah Al-Muminun 23:67

“Uku mukudzikweza; nkumakambirana usiku za chabechabe zoinyoza (Qur’an).”

Verse 68 — Surah Al-Muminun 23:68

“Kodi sadaganizire liwu (ili limene wadza nalo Mtumiki{s.a.w}), kapena zawadzera zomwe sizidawadzerepo makolo awo akale

Verse 69 — Surah Al-Muminun 23:69

“Kodi kapena sadam’dziwe Mtumiki wawoyu (makhalidwe ake) kotero kuti iwo akum’kana

Verse 70 — Surah Al-Muminun 23:70

“Kapena akunena kuti: “Ngwamisala?” Koma wawadzera ndi choonadi, ndipo ambiri a iwo amachida choonadi

Verse 71 — Surah Al-Muminun 23:71

“Ndipo choonadi chikadatsatira zofuna zawo, ndiye kuti thambo ndi nthaka ndi za m’menemo zikadaonongeka! Koma tawabweretsera chikumbutso chawo, koma iwo akuchipewa chikumbutso chawocho

Verse 72 — Surah Al-Muminun 23:72

“Kodi kapena ukuwapempha malipiro (nchifukwa chake akuchikana chipembedzochi)? Koma malipiro a Mbuye wako ndiwo abwino; ndipo Iye ndi Wopereka Wabwino kuposa opereka

Verse 73 — Surah Al-Muminun 23:73

“Ndipo ndithu iwe ukuwaitanira ku njira yolunjika; (supempha malipiro kwa iwo pa kuitanako)

Verse 74 — Surah Al-Muminun 23:74

“Ndipo ndithu amene sakhulupirira tsiku la chimaliziro, ali kutali ndi njira ya choonadi

Verse 75 — Surah Al-Muminun 23:75

“Ndipo tikadawachitira chifundo ndi kuwachotsera masautso omwe ali nawo, ndithu akadapitiriza kuyumbayumba m’kuchita kwawo zoipa

Verse 76 — Surah Al-Muminun 23:76

“Ndipo ndithu tidawalanga ndi chilango (chaukali), koma sadacheukire kwa Mbuye wawo ndikudzichepetsa

Verse 77 — Surah Al-Muminun 23:77

“Kufikira pamene tidawatsekulira khomo la chilango chaukali; pamenepo ndipo adataya mtima

Verse 78 — Surah Al-Muminun 23:78

“Ndipo Iye ndi Yemwe adakupangirani makutu, maso ndi mitima; nzochepa zimene mukuthokoza

Verse 79 — Surah Al-Muminun 23:79

“Iyenso ndi Yemwe wakufalitsani pa dziko; kenako mudzasonkhanitsidwa kwa Iye

Verse 80 — Surah Al-Muminun 23:80

“Ndipo Iye ndi Yemwe amapatsa moyo ndi imfa, ndipo kusinthana kwa usiku ndi usana Nkwake. Kodi simuzindikira

Verse 81 — Surah Al-Muminun 23:81

“Koma akunena monga (anthu) oyamba adanenera

Verse 82 — Surah Al-Muminun 23:82

“Akunena: “Kodi tikadzafa ndikukhala dothi ndi mafupa, tidzaukitsidwanso?”

Verse 83 — Surah Al-Muminun 23:83

““Ndithudi ife ndi makolo athu kale tidalonjezedwa zimenezi, izi sikanthu koma nkhambakamwa za anthu akale.”

Verse 84 — Surah Al-Muminun 23:84

“Nena: “Kodi nthaka njayani ndi zomwe zili m’menemo, ngati inu mukudziwa (kanthu)!”

Verse 85 — Surah Al-Muminun 23:85

“Adzanena kuti: “Nza Allah!” Nena: “Nanga bwanji simukumkumbukira (kuti Iye Ngokhoza chilichonse)

Verse 86 — Surah Al-Muminun 23:86

“Nena: “Kodi ndani Mbuye wa thambo zisanu ndi ziwiri, ndi Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) yaikulu?”

Verse 87 — Surah Al-Muminun 23:87

“Anena (kuti): “Nza Allah.” Nena: “Nanga bwanji simukumuopa?”

Verse 88 — Surah Al-Muminun 23:88

“Nena: “Kodi ndani yemwe m’manja mwake muli mphamvu yolamulira chinthu chilichonse? Ndipo Iye amateteza zonse. Ndipo palibe chimene chingatetezedwe kuchilango Chake. Ngati inu mukudziwa.”

Verse 89 — Surah Al-Muminun 23:89

“Anena (kuti): “Ndi Allah.” Nena: “Nanga mukulodzedwa bwanji (ndi satana)?”

Verse 90 — Surah Al-Muminun 23:90

“Koma tawabweretsera choonadi; ndithu iwo ngabodza (potsutsana ndi choonadicho)

Verse 91 — Surah Al-Muminun 23:91

“Allah sadadzipangire mwana, ndipo padalibe pamodzi ndi Iye mulungu (wina), ngati zikadakhala choncho ndiye kuti mulungu aliyense akadatenga zimene adalenga, ndipo milungu ina ikadaipambana milungu inzawo (polimbanirana ufumu), Allah wapatukana nazo kwambiri zimene akusimbazo

Verse 92 — Surah Al-Muminun 23:92

“Wodziwa zamseri ndi zapoyera; watukuka ku zimene akumphatikiza nazozo

Verse 93 — Surah Al-Muminun 23:93

“Nena: “E Mbuye wanga! Ngati mungandionetse zomwe akulonjezedwa (ndikadali ndi moyo)

Verse 94 — Surah Al-Muminun 23:94

“E Mbuye wanga! Musandiyike m’gulu la anthu osalungama.”

Verse 95 — Surah Al-Muminun 23:95

“Ndipo ndithu Ife ndi Wokhoza kukuonetsa (chilango) chimene tikuwalonjeza

Verse 96 — Surah Al-Muminun 23:96

“Chotsa zoipa (zimene akukuchitira) powabwezera zabwino; Ife tikudziwa zimene akunena

Verse 97 — Surah Al-Muminun 23:97

“Ndipo nena: “E Mbuye wanga! Ndikudzitchinjiriza ndi Inu kumanong’onong’o a satana.”

Verse 98 — Surah Al-Muminun 23:98

““Ndiponso ndikudzitchinjiriza ndi inu Mbuye wanga kuti asandidzere.”

Verse 99 — Surah Al-Muminun 23:99

“Kufikira m’modzi wawo ikam’dzera imfa, amanena: “Mbuye wanga! Ndibwezereni (ku moyo wa pa dziko),”

Verse 100 — Surah Al-Muminun 23:100

““Kuti ndikachite zabwino pa zimene ndidasiya.” (Angelo amayankha kuti): “Iyayi! Ndithu awa ndi mawu basi amene iye akuyankhula (imfa ikamfika).” Ndipo patsogolo pawo pali chiyembekezo; (moyo wamasautso kwa oipa; ndipo wamtendere kwa abwino) kufikira tsiku limene adzaukitsidwa

Verse 101 — Surah Al-Muminun 23:101

“Choncho, lipenga likadzaimbidwa, sipadzakhala chibale pakati pawo tsiku limenelo, ndipo sadzafunsana

Verse 102 — Surah Al-Muminun 23:102

“Tsono omwe mlingo (wa zochita zawo zabwino) udzalemere, iwowo ndiwo opambana

Verse 103 — Surah Al-Muminun 23:103

“Ndipo omwe miyeso yawo (ya zochita zabwino) idzatsike, iwowo ndi omwe adadziluzitsa okha; adzakhala ku Jahannam nthawi yaitali

Verse 104 — Surah Al-Muminun 23:104

“Moto ukawawula nkhope zawo, ndipo adzakhala m’menemo uku mano ali pamtunda

Verse 105 — Surah Al-Muminun 23:105

“(Adzauzidwa): “Kodi Ayah Zanga sizidali kuwerengedwa kwa inu ndipo inu nkumazitsutsa?”

Verse 106 — Surah Al-Muminun 23:106

“Adzati: “Mbuye wathu! Zoipa zathu zidatigonjetsa, choncho tidali anthu osokera.”

Verse 107 — Surah Al-Muminun 23:107

“Mbuye wathu! Titulutseni umu (m’moto ndikutibwezera ku dziko lapansi kuti tikachite ntchito yabwino); ngati titabwerezanso kuchita zoipa, ndiye kuti tidzakhaladi oipa (odziononga tokha).”

Verse 108 — Surah Al-Muminun 23:108

“(Allah) adzati: “Khalani chete m’menemo, monyozeka! Ndipo musandilankhule!”

Verse 109 — Surah Al-Muminun 23:109

“Ndithu mwa akapolo anga lidalipo gulu lomwe linkanena: “Mbuye wathu! Takhulupirira; choncho tikhululukireni ndi kutichitira chifundo; ndipo inu Ngabwino kwambiri kuposa (ena onse) ochita chifundo.”

Verse 110 — Surah Al-Muminun 23:110

““Koma inu mudawachita chipongwe kufikira adakuiwalitsani kundikumbuka uku muli kuwaseka.”

Verse 111 — Surah Al-Muminun 23:111

““Ndithu Ine lero ndawalipira (Munda wamtendere) chifukwa cha kupirira kwawo; kuti ndithu iwo ndiwo opambana.”

Verse 112 — Surah Al-Muminun 23:112

“Adzanena: “Kodi mudakhala nthawi yotani padziko pa chiwerengero cha zaka?”

Verse 113 — Surah Al-Muminun 23:113

“Adzayankha: “Tidakhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku; afunse owerengera.” (Adzatero poyerekeza ndi kutalika kwa moyo wamasautso ku Moto)

Verse 114 — Surah Al-Muminun 23:114

“Adzanena: “Inu simudakhale (kudzikoko) koma pang’ono basi, mukadakhala mukudziwa (chilango chomwe chakufikanichi, sibwenzi mukuchita zoipa).”

Verse 115 — Surah Al-Muminun 23:115

“Kodi mumaganiza kuti tidakulengani chabe, ndikuti simudzabwerera kwa Ife

Verse 116 — Surah Al-Muminun 23:116

“Watukuka Allah, Mfumu ya choonadi; palibe wompembedza mwachoonadi koma Iye, Bwana wa Arsh (Mpando wachifumu) yolemekezeka (kwambiri)

Verse 117 — Surah Al-Muminun 23:117

“Ndipo amene apembedza mulungu wina pomphatikiza ndi Allah, chikhalirecho iye alibe umboni pa zimenezo; basi chiwerengero chake chili kwa Mbuye wake. Ndithu osakhulupirira sangapambane

Verse 118 — Surah Al-Muminun 23:118

“Choncho nena: “Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndikundichitira Chifundo! Inu Ngabwino kuposa achifundo.”