Back to Languages

Chichewa - Chapter 25 - Al-Furqan

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Furqan 25:1

“Watukuka Mwini kupereka madalitso, Yemwe wavumbulutsa Qur’an kwa kapolo Wake kuti ikhale mchenjezi kwa zolengedwa zonse

Verse 2 — Surah Al-Furqan 25:2

“(Allah) Yemwe Ngwake ufumu wa kumwamba ndi wa pansi. Ndipo sadabale mwana ndipo alibenso wothandizana naye pa ufumu (Wake). Adalenga chinthu chilichonse ndikuchilinga mlingo wake

Verse 3 — Surah Al-Furqan 25:3

“Ndipo m’malo mwa Iye (Mulungu weniweni, osakhulupirira) adzipangira milungu yomwe siilenga chilichonse koma iyo ndiyomwe idalengedwa; ndiponso ilibe mphamvu yodzichotsera masautso ngakhale kudzidzetsera zothandiza. Ndiponso ilibe mphamvu zoperekera irnfa ndi moyo, ngakhale kuukitsa akufa

Verse 4 — Surah Al-Furqan 25:4

“Ndipo osakhulupirira akunena: “Ichi sikanthu (Qur’an imene Muhammad {s.a.w} wadza nayo) koma ndi chonama chimene wachipeka, ndipo pachimenechi amthandiza anthu ena (eni mabuku).” Kunena zoona, iwo (osakhulupirira) adza ndi chinyengo ndi bodza (pazonena zawozi)

Verse 5 — Surah Al-Furqan 25:5

“Ndipo (osakhulupirira) akunena: “Iyi (Qur’an) ndi nthano za anthu akale zomwe (Muhammad {s.a.w}) adazilembetsa. Choncho zikulakatulidwa kwa iye m’mawa ndi madzulo (kuti aloweze).”

Verse 6 — Surah Al-Furqan 25:6

“Nena: “Adaivumbulutsa Yemwe akudziwa zobisika za m’thambo ndi m’nthaka. Ndithu Iye ali Wokhululuka; Wachisoni, (nchifukwa chake sakukulangani mwachangu pazimene mukunenazi).”

Verse 7 — Surah Al-Furqan 25:7

“Ndipo akunena: “Ndi Mtumiki wanji uyu, womadya chakudya nkumayenda m’misika? Kodi bwanji sadatumizidwe mngelo kwa iye kuti azikhala naye limodzi uku akuchenjeza?”

Verse 8 — Surah Al-Furqan 25:8

““Kapena kuponyeredwa nkhokwe (za chuma), kapena kukhala ndi munda ndikumadya m’menemo?” Ndipo osalungama akuti: “Ndithudi, mukutsatira munthu wolodzedwa.”

Verse 9 — Surah Al-Furqan 25:9

“Ona momwe akukuponyera mafanizo (omwe sali oyenerana nawe, nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa wamisala, wabodza, wophunzitsidwa ndi anthu ena) choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yoongoka yokunenera)

Verse 10 — Surah Al-Furqan 25:10

“Watukuka Mwini kupereka madalitso ambiri, Yemwe akafuna, akuchitira zabwino kuposa zimenezi, (adzakupatsa pa tsiku lachimaliziro) Minda yamtendere yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; ndipo adzakupangira nyumba zikuluzikulu zachifumu

Verse 11 — Surah Al-Furqan 25:11

“Koma akutsutsa zanthawi ya Qiyâma. ndipo tawakonzera Moto woyaka (iwo) amene akutsutsa zanthawi ya Qiyâma (ya chimaliziro)

Verse 12 — Surah Al-Furqan 25:12

“(Motowo) ukadzawaona (naonso nkuuona) kuchokera pa malo apatali, (iwo) adzamva mkwiyo wa Motowo ndi mkokomo wake

Verse 13 — Surah Al-Furqan 25:13

“Ndipo akadzaponyedwa m’menemo, pamalo opanika uku manja atanjatidwa chakukhosi, pamenepo adzaitana imfa (kuti iwafike, afe apumule ku masautsowo)

Verse 14 — Surah Al-Furqan 25:14

“(Tidzawauza): “Lero musaitane imfa imodzi, koma itanani imfa zambiri (ndipo simupeza mpumulo koma mazunzo okhaokha).”

Verse 15 — Surah Al-Furqan 25:15

“Nena (kwa osakhulupirira): “Kodi izi ndizo zabwino, kapena munda wamuyaya umene alonjezedwa oopa Allah kuti udzakhale mphoto (yabwino) kwa iwo ndi kobwerera (kotamandika)?”

Verse 16 — Surah Al-Furqan 25:16

““M’menemo adzapeza chilichonse chomwe adzafune. Adzakhala nthawi yaitali. Mtenderewu ndi lonjezo lochokera kwa Mbuye wako pa iwo lomwe adampempha kuti adzawakwaniritsire.”

Verse 17 — Surah Al-Furqan 25:17

“Ndipo (kumbuka) tsiku limene adzawasonkhanitse (awa osakhulupirira) ndi omwe adali kuwapembedza (monga Isa (Yesu), Uzairi ndi angelo) kusiya Allah; adzanena (Allah kuuza amene ankalambiridwawo): “Kodi ndinu mudasokeretsa anthu angawa, kapena ndi okha adasokera njira.”

Verse 18 — Surah Al-Furqan 25:18

“Adzanena: “E ulemelero ukhale kwa inu! Sizidali zoyenera kwa ife kudzikonzera atetezi mmalo mwa Inu, (nanji kuuza anthu kuti azitipembedza). Koma mudawasangalatsa iwo ndi makolo awo kufikira adaiwala malangizo (Anu). Ndipo adali anthu oonongeka.”

Verse 19 — Surah Al-Furqan 25:19

“(Allah adzati): “Ndithu yakutsutsani (milungu yanuyo) pa zimene mwanena (kuti iwo adakusokeretsani). Ndipo simutha kudzichotsera (chilango) ngakhale (kupeza) chithandizo.” Ndipo, ndithudi amene achite zoipa mwa inu, tidzamulawitsa chilango chachikulu

Verse 20 — Surah Al-Furqan 25:20

“Ndipo palibe pamene tidatuma atumiki patsogolo pako koma ndithu iwo, adali kudya chakudya; ankayendanso m’misika. Ndipo tawasankha ena mwa inu kuti akhale mayeso kwa ena (popereka masautso kwa olungama). kodi mupirira? Ndipo, Mbuye wako ali Wopenya (chilichonse)

Verse 21 — Surah Al-Furqan 25:21

“۞ Ndipo amene alibe chiyembekezo chakukumana Nafe akunena: “Bwanji angelo satumidwa kwa ife? Kapena timuone Mbuye wathu (kuti atitsimikizire kuti ndiwedi Mtumiki wake”? Ndipo Allah akunena): “Ndithu adzitukumula mmitima mwawo ndipo anyoza; kunyoza kwakukulu.”

Verse 22 — Surah Al-Furqan 25:22

“Tsiku lowaona angelo, sikudzakhala chisangalalo tsiku limenelo kwa ochimwa, (koma lidzakhala tsiku lochoka moyo wawo). Ndipo adzanena (tsiku limenelo): “Ha! Allah atitchinjirize kwambiri.” (Koma mawu awa, sadzathandiza chilichonse)

Verse 23 — Surah Al-Furqan 25:23

“Ndipo tidzaidzera ntchito iliyonse (yabwino) imene adachita, ndipo tizaichita monga fumbi louluka (ponseponse, yopanda phindu chifukwa cha kusakhulupirira Allah kwawo)

Verse 24 — Surah Al-Furqan 25:24

“Anthu a ku Munda wamtendere tsiku limenelo adzakhala ndi mokhala mwabwino, ndi pamalo pampumulo wabwino

Verse 25 — Surah Al-Furqan 25:25

“Ndipo akumbutse za tsikulo pomwe thambo lidzang’ambika ndikudzetsa mitambo (yomwe idzachititsa chimdima ponseponse). Ndipo angelo adzatsika ambirimbiri

Verse 26 — Surah Al-Furqan 25:26

“Tsiku limenelo ufumu wachoonadi ngwa (Allah) Wachifundo chambiri. Ndipo lidzakhala tsiku lovuta kwa osakhulupirira

Verse 27 — Surah Al-Furqan 25:27

“Ndipo tsiku (limenelo), wosalungama adzakukuta zala zake uku akunena: “Kalanga ine! Ndikadatsata njira ya Mtumiki.”

Verse 28 — Surah Al-Furqan 25:28

““E tsoka langa! Ndikadapanda kumchita uje kukhala bwenzi wanga. (nkadapulumuka lero).”

Verse 29 — Surah Al-Furqan 25:29

““Ndithu adandisokeretsa kufikira ndidasiya ulaliki (wa Allah) utandidzera. Zoonadi, satana amataya munthu (akaona kuti wamgwetsa m’chionongeko).”

Verse 30 — Surah Al-Furqan 25:30

“Ndipo Mtumiki (adasuma kwa Mbuye wake) adati: “E Mbuye wanga! Ndithu anthu anga aisandutsa Qur’aniyi kukhala chinthu chosiidwa, (sakuiwerenga. Ndiponso sakutsata ziphunzitso zake).”

Verse 31 — Surah Al-Furqan 25:31

“Momwemonso mneneri aliyense tidamkonzera mdani wochokera mwa (anthu) oipa. Ndipo Mbuye wako wakwana kukhala muongoli ndi mthandizi (wako)

Verse 32 — Surah Al-Furqan 25:32

“Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji Qur’an yonse siidavumbulutsidwe nthawi imodzi kwa iye? Momwemo (ukuoneramo, tikuitumiza pang’onopang’ono) kuti tiulimbikitse mtima wako ndi iyo, ndipo taiyala, mkayalidwe kabwino

Verse 33 — Surah Al-Furqan 25:33

“Ndipo sangakubweretsere fanizo lililonse koma tikubweretsera choonadi (choyankha fanizolo ndi kukudziwitsa) ndi kumasulira kwabwino

Verse 34 — Surah Al-Furqan 25:34

“Amene adzasonkhanitsidwe akukokedwa ndi nkhope zawo kunka ku Jahanama, iwowo adzakhala pamalo oipa ndipo ngosokera njira (yachoonadi)

Verse 35 — Surah Al-Furqan 25:35

“Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Ndipo m’bale wake Harun (Aroni) tidamsankha kukhala nduna (yake)

Verse 36 — Surah Al-Furqan 25:36

“Choncho tidati: “Pitani kwa anthu omwe atsutsa zisonyezo Zathu. Tero, tidawaononga kotheratu.”

Verse 37 — Surah Al-Furqan 25:37

“Naonso anthu a Nuh, pamene adatsutsa atumiki, tidawamiza, ndipo tidawachita kukhala phunziro kwa anthu, ndipo anthu osalungama tawakonzera chilango chowawa

Verse 38 — Surah Al-Furqan 25:38

“Nawonso Âdi, Asamudu ndi eni chitsime ndi mibadwo yambiri pakati pa iwo

Verse 39 — Surah Al-Furqan 25:39

“Ndipo onse tidawaponyera mafanizo; ndiponso onse tidawaononga motheratu (pamene adakana kutsatira malamulo athu)

Verse 40 — Surah Al-Furqan 25:40

“Ndipo ndithu iwo (Aquraish, m’maulendo awo) adafika pa mudzi (Sodomu ndi Gomora) womwe mvula yoipa (ya sangalabwi) idawavumbwa. Kodi sadali kuuona? Koma sadali kuyembekezera zakuuka ku imfa

Verse 41 — Surah Al-Furqan 25:41

“Ndipo akakuona (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}), amangokuchitira chipongwe: “Kodi uyu ndi yemwe Allah wamtuma kuti akhale mtumiki?”

Verse 42 — Surah Al-Furqan 25:42

““Ndithu adatsala pang’ono kutisokeretsa ku milungu yathu, tikadapanda kupirira pa milunguyo.” Posachedwapa adziwa, pamene adzaona chilango, (kuti) ndani wosokera zedi njira

Verse 43 — Surah Al-Furqan 25:43

“Kodi wamuona yemwe wachichita chilakolako chake (chimene akuchikonda) kukhala mulungu wake? Kodi iweyo ungathe kukhala muyang’aniri wa iye (kotero kuti ungamkakamize chomwe safuna)

Verse 44 — Surah Al-Furqan 25:44

“Kapena ukuganiza kuti ambiri a iwo akumva kapena kuzindikira? Iwo sali kanthu kena koma ali ngati ziweto. Ndipo iwo asokera kwambiri njira

Verse 45 — Surah Al-Furqan 25:45

“Kodi sudaone momwe Mbuye wako wautambasulira mthunzi? Akadafuna, akadauchita kuti ukhale wokhazikika (wosasinthasintha). Ndipo talichita dzuwa kukhala chisonyezo chake

Verse 46 — Surah Al-Furqan 25:46

“Kenaka tikuufumbata kwa Ife m’kufumbata kwapang’onopang’ono (kufikira wonse wutachoka)

Verse 47 — Surah Al-Furqan 25:47

“Ndipo Iye ndi amene wakuchitirani usiku kukhala monga chovala, ndipo tulo monga mpumulo, ndipo usana wauchita kukhala monga nthawi youka (kuimfa)

Verse 48 — Surah Al-Furqan 25:48

“Iye ndi Yemwe amatumiza mphepo kukhala nkhani yabwino patsogolo pa chifundo chake (mvula), ndipo kuchokera kumitambo tikutsitsa madzi oyera

Verse 49 — Surah Al-Furqan 25:49

“Kuti ndi madziwo tiukitse dziko lakufa (lachilala), ndikumwetsa zina mwa zimene tidazilenga monga ziweto ndi anthu ochuluka

Verse 50 — Surah Al-Furqan 25:50

“Ndiponso ndithu tikuigawa (mvulayi) pakati pawo kuti akumbukire, ndipo anthu ambiri akukana (kuthokoza Allah) koma kupitiriza kusakhulupirira

Verse 51 — Surah Al-Furqan 25:51

“Ndipo tikadafuna, tikadatuma mchenjezi wawowawo m’mudzi uliwonse, (koma tatuma Muhammad {s.a.w} kuti akhale mchenjezi wa onse

Verse 52 — Surah Al-Furqan 25:52

“Choncho usawamvere osakhulupirira koma limbana nawo ndi iyo (Qur’an); kulimbana kwakukulu

Verse 53 — Surah Al-Furqan 25:53

“Ndipo Iye (Allah) ndi Yemwe wazikumanitsa nyanja ziwiri, iyi yamadzi okoma othetsa ludzu ndi iyi yamadzi amchere owawa. Ndipo waika malire ndi chitsekerezo chotsekereza pakati pa izo

Verse 54 — Surah Al-Furqan 25:54

“Ndipo Iye ndiye adalenga munthu ndi madzi ndiponso adamchitira chibale cha magazi ndi chibale cha ukwati. Ndipo Mbuye wako ali Wokhoza chilichonse

Verse 55 — Surah Al-Furqan 25:55

“Ndipo (ena mwa anthu) akupembedza zina zake kusiya Allah, zomwe sizingawathandize ndiponso sizingawadzetsere masautso (atasiya kuzipembedza). Ndipo wosakhulupirira ndi mthandizi wa zoipa poukira Mbuye wake

Verse 56 — Surah Al-Furqan 25:56

“Ndipo Ife sitidakutume koma kuti ukhale wouza nkhani zabwino (okhulupirira); ndi wochenjeza (osakhulupirira)

Verse 57 — Surah Al-Furqan 25:57

“Nena: “Sindikupemphani malipiro pa zimenezi (zomwe ndikukuphunzitsani) koma amene afuna ayende pa njira yopita kwa Mbuye wake, (popanda chopereka).”

Verse 58 — Surah Al-Furqan 25:58

“Ndipo tsamira kwa (Allah) Wamoyo, Wamuyaya Yemwe saafa. Ndipo mulemekeze pomtamanda ndi mbiri Zake. Ndipo Iye akukwana kudziwa bwinobwino machimo a akapolo Ake

Verse 59 — Surah Al-Furqan 25:59

“Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zimene zikupezeka mkati mwake. (Adazilenga) m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, m’kukhazikika kodziwa Yekha). Iye Ngwachifundo chambiri; mufunseni wodziwa za Iye

Verse 60 — Surah Al-Furqan 25:60

“Ndipo akauzidwa (kuti): “Mulambireni (Allah) Wachifundo chambiri.” Amati: “Ndani Wachifundo chambiri? Kodi tilambire Yemwe iwe ukutilamula?” (Mawu amenewa) adawaonjezera iwo mwano

Verse 61 — Surah Al-Furqan 25:61

“Watukuka Mwini kupereka madalitso Yemwe adakhazikitsa nyenyezi ku thambo, ndipo m’menemo adaika nyali (dzuwa) ndi mwezi wounika

Verse 62 — Surah Al-Furqan 25:62

“Ndipo Iye ndi Yemwe adapanga usiku ndi usana kuti zizitsatana (ndikusinthana). (Izi zingapindulitse) kwa amene afuna kukumbukira kapena (amene) afuna kuthokoza

Verse 63 — Surah Al-Furqan 25:63

“Ndipo akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri ndi omwe akuyenda pa dziko modzichepetsa, ndipo mbuli zikanena kwa iwo (mawu amwano), amaziyankha mawu abwino

Verse 64 — Surah Al-Furqan 25:64

“Ndi omwe amapititsa nthawi ina ya usiku uku akulambira ndi kuimilira chifukwa cha kulemekeza Mbuye wawo

Verse 65 — Surah Al-Furqan 25:65

“Ndi omwe akunena: “E Mbuye wathu tipewetsereni chilango cha Jahannam; ndithu chilango chake nchosasiyana nacho.”

Verse 66 — Surah Al-Furqan 25:66

““Ndithu iyo ndi malo woipa; ndiponso pokhala poipa.”

Verse 67 — Surah Al-Furqan 25:67

“Ndi omwe amati akamagawira anthu ena chuma chawo, samwaza pachabe ndiponso sachita umbombo, koma amachita mwapakatikati

Verse 68 — Surah Al-Furqan 25:68

“Ndi omwe sapembedza milungu ina poiphatikiza ndi Allah, ndiponso saapha munthu yemwe Allah adaletsa kumupha kupatula pakakhala choonadi ndiponso saachita chigololo. Ndipo amene achite zimenezi, apeza masautso (pompano pa dziko lapansi)

Verse 69 — Surah Al-Furqan 25:69

“Chilango chidzawonjezeredwa kwa iye tsiku la Qiyâma, ndipo adzakhala m’chilango muyaya uku ali wonyozeka

Verse 70 — Surah Al-Furqan 25:70

“Kupatula amene walapa, naakhulupirira, ndikuchita ntchito yabwino. Tsono iwowo, Allah adzawasinthira zoipa zawo kukhala zabwino. Ndipo Allah ali Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha

Verse 71 — Surah Al-Furqan 25:71

“Ndipo amene akulapa ndikuchita zabwino, ndithu iye akulapa mwachoonadi kwa Allah

Verse 72 — Surah Al-Furqan 25:72

“Omwenso sachitira umboni za bodza, ndipo akadutsa pamalo pa zachibwana, amadutsa mwaulemu

Verse 73 — Surah Al-Furqan 25:73

“Ndiponso omwe amati akakumbutsidwa Ayah za Mbuye wawo, samazigwera mwa ugonthi ndi mwakhungu

Verse 74 — Surah Al-Furqan 25:74

“Ndi omwenso akunena: “E Mbuye wathu! Tipatseni mwa akazi athu ndi ana athu chotonthoza maso, ndipo tichiteni kukhala atsogoleri a oopa Allah.”

Verse 75 — Surah Al-Furqan 25:75

“Iwo adzalipidwa zipinda (za pamwamba ku Jannah) chifukwa cha mavuto omwe adawapirira. Ndipo akalandira m’menemo ulemu ndi mtendere

Verse 76 — Surah Al-Furqan 25:76

“Akakhala m’menemo nthawi yaitali; akongolerenji malo okhazikika ndi kukhalamo

Verse 77 — Surah Al-Furqan 25:77

“Nena: “Ndithu Mbuye wanga sakadalabadira chilichonse pa inu pakadapanda mapemphero anu, (akadakulangani pompano pa dziko lapansi.) Komabe inu mwatsutsa (uthenga wa aneneri). Choncho chilango chidzakugweranibe.”