Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 26 - Ash-Shuara
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Ash-Shuara 26:1
“Tâ-Sîn-Mîm
Verse 2 — Surah Ash-Shuara 26:2
“Izi ndi Ayah (ndime) za buku (la Qur’an) lofotokoza chilichonse (chofunika m’chipembedzo)
Verse 3 — Surah Ash-Shuara 26:3
“Mwina iwe (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) udziononga wekha (ndi madandaulo) chifukwa chakuti (iwo) sadakhale okhulupirira
Verse 4 — Surah Ash-Shuara 26:4
“Tikadafuna, tikadawatsitsira chizizwa kuchokera kumwamba; kotero kuti makosi awo akadadzichepetsa ndi chizizwacho, (sakadatha kucheukira kwina koma sitifuna kukakamiza anthu kuti akhale Asilamu)
Verse 5 — Surah Ash-Shuara 26:5
“Ndipo palibe pamene chikuwadzera chivumbulutso chatsopano chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri koma amazipatula ku icho (chivumbulutso)
Verse 6 — Surah Ash-Shuara 26:6
“Ndithu atsutsa; choncho posachedwapa ziwadzera nkhani zomwe adali kuzichitira chipongwe
Verse 7 — Surah Ash-Shuara 26:7
“Kodi sadaone nthaka? Ndimmera ungati taumeretsa m’menemo kuchokera mu mtundu ulionse, wokongola
Verse 8 — Surah Ash-Shuara 26:8
“Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro (zosonyeza mphamvu za Allah). Koma ambiri a iwo sali okhulupirira
Verse 9 — Surah Ash-Shuara 26:9
“Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha
Verse 10 — Surah Ash-Shuara 26:10
“Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako adaitana (m’neneri) Mûsa; adamuuza: “Pita kwa anthu ochita zoipa.”
Verse 11 — Surah Ash-Shuara 26:11
“Anthu a Farawo; (auze): “Kodi sawopa (Allah)?”
Verse 12 — Surah Ash-Shuara 26:12
“(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ine ndikuopa kuti anganditsutse
Verse 13 — Surah Ash-Shuara 26:13
“Ndipo chingabanike chifuwa changa (ndi maganizo, chifukwa chakunditsutsa kwawo); ndiponso lirime langa siliyankhula momveka bwino. Choncho tumizaninso uthengawu kwa Harun (kuti tikhale awiri ndipo azikandithangata pantchito yangayi)
Verse 14 — Surah Ash-Shuara 26:14
“Ndipo iwowo ndili nawo mlandu ndipo ndikuopa kuti angandiphe (pobwezera chimene ndidawalakwira powaphera munthu wawo)
Verse 15 — Surah Ash-Shuara 26:15
“(Allah) adati: “Iyayi! Pitani pamodzi ndi zozizwa Zathu; ndithu Ife tikakhala nanu limodzi (pokuthangatani) uku tikumvetsera (zimene azikanena).”
Verse 16 — Surah Ash-Shuara 26:16
““Choncho mpitireni Farawo, ndipo kamuuzeni kuti: “Ife ndi atumiki a Mbuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 17 — Surah Ash-Shuara 26:17
““(Tatumidwa) kuti uwapereke kwa ife ana a Israyeli (kuti tinke nawo ku Sham).”
Verse 18 — Surah Ash-Shuara 26:18
“(Farawo) adati (kwa Mûsa): “Kodi sitidakulere kwathu uli mwana, ndi kukhala nafe pa moyo wako zaka zambiri?”
Verse 19 — Surah Ash-Shuara 26:19
““Ndipo udachita chochita chako chimene udachichita, ndipo iwe ndiwe mmodzi wa osathokoza!”
Verse 20 — Surah Ash-Shuara 26:20
“(Mûsa) adati: “Ndidachita zimenezo pomwe ine ndidali mmodzi wa osazindikira zinthu.”
Verse 21 — Surah Ash-Shuara 26:21
““Choncho ndidakuthawani pomwe ndidakuopani; tsono Mbuye wanga wandipatsa nzeru zoweruzira (zinthu), ndi kundisankha kukhala mmodzi wa atumiki.”
Verse 22 — Surah Ash-Shuara 26:22
““Ndipo kodi umenewu ndimtendere wonditonzera pomwe mudawaika muukapolo ana a Israyeli!”
Verse 23 — Surah Ash-Shuara 26:23
“Farawo adati: “Kodi ndani Mbuye wa zolengedwayo?”
Verse 24 — Surah Ash-Shuara 26:24
“(Mûsa) adati: “Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli ndi chitsimikizo. (Amachita chilichonse m’menemo mmene wafunira; kupereka moyo ndi imfa).”
Verse 25 — Surah Ash-Shuara 26:25
“(Farawo) adauza omwe adali m’mphepete mwake (mwachipongwe): “Kodi simukumva (mawu achibwanawa)?”
Verse 26 — Surah Ash-Shuara 26:26
“(Mûsa adapitiriza kunena) adati: “Allah ndi Mbuye wanu komanso Mbuye wamakolo anu oyamba.”
Verse 27 — Surah Ash-Shuara 26:27
“(Farawo) adati (kwa anthu ake pofuna kuwakwiitsa): “Ndithu Mtumiki wanu amene watumidwa kwa inu, ngwamisala.”
Verse 28 — Surah Ash-Shuara 26:28
“(Mûsa) adati: “Mbuye wakuvuma ndi kuzambwe, ndi zomwe ziri pakati pake ngati mumazindikira (zinthu, muzindikira izi).”
Verse 29 — Surah Ash-Shuara 26:29
“(Farawo) adati: “Ngati udzipangira mulungu wina kusiya ine, ndikuchita kukhala mmodzi wa omangidwa kundende.”
Verse 30 — Surah Ash-Shuara 26:30
“(Mûsa) adati: “Kodi ngakhale nditakubweretsera chinthu choonekera poyera (chosonyeza kuti zimene ndikunenazi ndizoona ndatumidwa ndi Allah)?”
Verse 31 — Surah Ash-Shuara 26:31
“(Farawo) adati: “Chibweretse, ngati uli mwa onena zoona.”
Verse 32 — Surah Ash-Shuara 26:32
“Ndipo (Mûsa) adaponya (pansi) ndodo yake, mwadzidzidzi idasanduka njoka yopenyeka
Verse 33 — Surah Ash-Shuara 26:33
“Ndipo adatulutsa dzanja lake; pompo lidali loyera (kwambiri) kwa (onse) openya
Verse 34 — Surah Ash-Shuara 26:34
“(Farawo) adauza akuluakulu omwe adali m’mphepete mwake: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa kwambiri.”
Verse 35 — Surah Ash-Shuara 26:35
““Akufuna kukutulutsani m’dziko lanu ndi matsenga ake; kodi nanga mukuti chiyani?”
Verse 36 — Surah Ash-Shuara 26:36
“(Anthu) adati (kwa Farawo): “Mpatse nthawi ndi m’bale wakeyo, ndipo tumiza (amithenga) m’mizinda yonse osonkhanitsa anthu.”
Verse 37 — Surah Ash-Shuara 26:37
““Ndipo akubweretsera amatsenga onse odziwa kwabasi (kotero kuti adzampambana Mûsa).”
Verse 38 — Surah Ash-Shuara 26:38
“Choncho amatsenga adasonkhanitsidwa mu nthawi ya tsiku lodziwika
Verse 39 — Surah Ash-Shuara 26:39
“Ndipo anthu adauzidwa: “Kodi inu musonkhana? (Choncho, sonkhanani).”
Verse 40 — Surah Ash-Shuara 26:40
““Mwina tingawatsatire amatsenga ngati iwo ndiamene apambane.”
Verse 41 — Surah Ash-Shuara 26:41
“Ndipo pamene amatsenga adadza, adati kwa Farawo: “Kodi tidzakhala ndi mphoto ngati ife ndife tipambane?”
Verse 42 — Surah Ash-Shuara 26:42
“(Farawo) adati: “Inde, (ndipo kuonjezera apo) ndithu inu mudzakhala mwa amene amakhala pafupi (ndi ine, monga nduna zanga).”
Verse 43 — Surah Ash-Shuara 26:43
“Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zimene mufuna kuponya (zosonyeza kuya kwa matsenga anu).”
Verse 44 — Surah Ash-Shuara 26:44
“Choncho adaponya zingwe zawo ndi ndodo zawo, ndipo adati: “Kupyolera mu mphamvu za Farawo, ndithu ife ndife opambana.”
Verse 45 — Surah Ash-Shuara 26:45
“Kenako Mûsa adaponya ndodo yake; mwadzidzidzi iyo idameza zabodza zomwe iwo adakonza
Verse 46 — Surah Ash-Shuara 26:46
“Pamenepo amatsenga adadzigwetsa pansi molambira
Verse 47 — Surah Ash-Shuara 26:47
“Adati: “Tamkhulupirira Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 48 — Surah Ash-Shuara 26:48
““Mbuye wa Mûsa ndi Harun.”
Verse 49 — Surah Ash-Shuara 26:49
“(Farawo) adati: “Ha! Mwamkhulupirira chotani ndisanakulolezeni? Ndithu iyeyu ndimkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Choncho posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni) ndithu ndidula manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa (podula mkono wakumanja ndi mwendo wakumanzere; kapena kudula mkono wakumanzere ndi mwendo wakumanja), ndipo kenako ndikupachikani nonsenu.”
Verse 50 — Surah Ash-Shuara 26:50
“(Amatsenga) adati: “Palibe vuto, ndithu ife (tonse) tibwerera kwa Mbuye wathu.”
Verse 51 — Surah Ash-Shuara 26:51
““Ndithu ife tikuyembekezera kuti Mbuye wathu atikhululukire zolakwa zathu; pokhala oyamba mwa okhulupirira.”
Verse 52 — Surah Ash-Shuara 26:52
“Ndipo tidamvumbulutsira Mûsa (kuti): “Pita ndi anthu anga m’nthawi yausiku (musamuke m’dziko la Iguputo); ndithu inu mutsatidwa.”
Verse 53 — Surah Ash-Shuara 26:53
“Choncho Farawo adatuma (owatuma) kuti asonkhanitse anthu m’mizinda (kuti aletse ana a Israyeli kutuluka)
Verse 54 — Surah Ash-Shuara 26:54
“(Adawauza otumidwa aja kuti auze anthu kuti): “Ndithu awa (ana a Israyeli) ndikagulu kochepa
Verse 55 — Surah Ash-Shuara 26:55
“Ndipo ndithu iwo akutikwiitsa
Verse 56 — Surah Ash-Shuara 26:56
“Koma ndithu ife tonse (ndife ochuluka komabe ngakhale zili choncho) tikuwaopa.”
Verse 57 — Surah Ash-Shuara 26:57
“Choncho tidawatulutsa m’minda ndi mwa akasupe
Verse 58 — Surah Ash-Shuara 26:58
“Ndi m’nkhokwe za chuma ndi m’malo okongola
Verse 59 — Surah Ash-Shuara 26:59
“Momwemo ndi mmene tidawachitira ndipo tidawalowetsera chokolo zinthu zawo zonse kwa ana a Israyeli
Verse 60 — Surah Ash-Shuara 26:60
“Choncho (anthu a Farawo ndi iye mwini) adawatsatira (ana a Israyeli) dzuwa litatuluka
Verse 61 — Surah Ash-Shuara 26:61
“Ndipo pamene magulu awiri adaonana (anthu a Farawo ndi anthu a Mûsa), anthu a Mûsa adati: “Ndithu ife tigwidwa.”
Verse 62 — Surah Ash-Shuara 26:62
“(Mûsa) adati: “Iyayi! Ndithu Mbuye wanga ali nane pamodzi. Andiongolera (kuti ife tonse tipulumuke).”
Verse 63 — Surah Ash-Shuara 26:63
“Ndipo tidam’vumbulutsira mawu Mûsa (akuti): “Menya nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo idagawikana, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu
Verse 64 — Surah Ash-Shuara 26:64
“Ndipo tidawayandikitsa pamenepo anthu enawo, (Farawo ndi anthu ake nalowa pa njira yomweyo pambuyo pa Mûsa ndi anthu ake)
Verse 65 — Surah Ash-Shuara 26:65
“Ndipo tidapulumutsa Mûsa ndi onse amene adali nawo (mpaka adaoloka nyanjayo, madzi ali chiimire mbali iyi ndi iyi)
Verse 66 — Surah Ash-Shuara 26:66
“Kenako tidawamiza enawo, (Farawo ndi anthu ake)
Verse 67 — Surah Ash-Shuara 26:67
“Ndithu pa zimenezi pali lingaliro. Koma ambiri a iwo sali okhulupirira
Verse 68 — Surah Ash-Shuara 26:68
“Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa (amalanga ndi chilango choopsa omwe amunyoza); Wachisoni (kwa omkhulupirira ndi kumumvera)
Verse 69 — Surah Ash-Shuara 26:69
“Ndipo awerengere (osakhulupirira) nkhani ya (M’neneri) Ibrahim
Verse 70 — Surah Ash-Shuara 26:70
“Pamene adafunsa bambo wake ndi anthu ake (kuti); “Kodi mukupembedza chiyani?”
Verse 71 — Surah Ash-Shuara 26:71
“Adati: “Tikupembedza mafano; ndipo tipitiriza kuwapembedza.”
Verse 72 — Surah Ash-Shuara 26:72
“(Ibrahim) adati: “Kodi amakumvani mukawaitana?”
Verse 73 — Surah Ash-Shuara 26:73
““Kapena amakuthandizani (mukawapembedza) kapena amapereka masautso kwa inu (mukasiya kuwapembedza)?”
Verse 74 — Surah Ash-Shuara 26:74
“(Iwo) adati: “Koma tidapeza makolo athu akuchita zimenezi.”
Verse 75 — Surah Ash-Shuara 26:75
“(Ibrahim) adati: “Kodi mukuwaona awa amene mwakhala mukuwapembedza,”
Verse 76 — Surah Ash-Shuara 26:76
““Inu ndi makolo anu amene adatsogola?”
Verse 77 — Surah Ash-Shuara 26:77
““Ndithu iwo ndiadani anga, kupatula Mbuye wa zolengedwa zonse;”
Verse 78 — Surah Ash-Shuara 26:78
““Yemwe adandilenga, ndiponso Yemwe akundiongolera (kunjira yolungama);”
Verse 79 — Surah Ash-Shuara 26:79
““Ndiyemwe akundidyetsa ndi kundimwetsa.”
Verse 80 — Surah Ash-Shuara 26:80
““Ndipo ndikadwala ndiyemwe amandichiritsa.”
Verse 81 — Surah Ash-Shuara 26:81
““Ndi Amene adzandipatsa imfa, ndipo (tsiku la Qiyâma) adzandidzutsa;”
Verse 82 — Surah Ash-Shuara 26:82
““Ndi Yemwe ndikuyembekezera kuti adzandikhululukira zolakwa zanga tsiku la malipiro.”
Verse 83 — Surah Ash-Shuara 26:83
““E Mbuye wanga! Ndipatseni nzeru zoweruzira (zinthu), ndikundilumikiza ndi anthu abwino;”
Verse 84 — Surah Ash-Shuara 26:84
““Ndipatseni kutchulidwa kwabwino kwa anthu ena odza pambuyo;”
Verse 85 — Surah Ash-Shuara 26:85
““Ndichiteni kukhala mmodzi mwa olandira Munda wamtendere;”
Verse 86 — Surah Ash-Shuara 26:86
““Ndipo khululukirani bambo wanga; ndithu iye adali mmodzi wa osokera;”
Verse 87 — Surah Ash-Shuara 26:87
““Ndipo musadzandiyalutse pa tsiku loukitsidwa anthu (ku imfa);”
Verse 88 — Surah Ash-Shuara 26:88
““Tsiku lomwe chuma ndi ana sizidzathandiza (aliyense).”
Verse 89 — Surah Ash-Shuara 26:89
““Kupatula yemwe adzadza kwa Allah ndi mtima woyera (iye ndiamene adzathandizidwa patsikulo).”
Verse 90 — Surah Ash-Shuara 26:90
“Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa kwa oopa (Allah)
Verse 91 — Surah Ash-Shuara 26:91
“Ndipo Jahannam idzaonetsedwa kwa opotoka
Verse 92 — Surah Ash-Shuara 26:92
“Ndipo kudzanenedwa kwa iwo: “Ali kuti amene mudali kuwapembedza aja
Verse 93 — Surah Ash-Shuara 26:93
“M’malo mwa Allah? Kodi angathe kukuthandizani kapena kudzithandiza okha?”
Verse 94 — Surah Ash-Shuara 26:94
“Ndipo iwo ndi opotoka ena adzaponyedwa ndi nkhope zawo m’menemo (mu Jahannam)
Verse 95 — Surah Ash-Shuara 26:95
“Ndi magulu onse ankhondo a Iblis (omwe adali kukometsa kwa anthu zoipa ndi machimo)
Verse 96 — Surah Ash-Shuara 26:96
“Adzanena (movomereza kulakwa kwawo) uku naonso ali m’menemo, akukangana (ndi anzawo omwe adawasokeretsa)
Verse 97 — Surah Ash-Shuara 26:97
““Ndikulumbira Allah, ndithu tidali m’kusokera kowonekera
Verse 98 — Surah Ash-Shuara 26:98
“Pamene timakufananitsani ndi Mbuye wa zolengedwa
Verse 99 — Surah Ash-Shuara 26:99
“Ndipo sadatisokeretse, koma oipa okha basi
Verse 100 — Surah Ash-Shuara 26:100
“Choncho ife tilibe aomboli (otiombola)
Verse 101 — Surah Ash-Shuara 26:101
“Ngakhalenso bwenzi wapamtima (woti angatipulumutse kumasautsowa)
Verse 102 — Surah Ash-Shuara 26:102
“Tikadapeza mwayi wobwerera (ku moyo wa padziko), tikadakhala mwa okhulupirira.”
Verse 103 — Surah Ash-Shuara 26:103
“Ndithu m’zimenezi, muli malingaliro akulu, koma ambiri a iwo sali okhulupirira
Verse 104 — Surah Ash-Shuara 26:104
“Ndipo ndithu Mbuye wako, ndiye Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha
Verse 105 — Surah Ash-Shuara 26:105
“Anthu a Nuh adatsutsa atumiki
Verse 106 — Surah Ash-Shuara 26:106
“Pamene adawauza Nuh m’bale wawo kuti: “Kodi simukuopa (Allah ngakhale nditakuuzani zoopsa zimene zikukudikirani)?”
Verse 107 — Surah Ash-Shuara 26:107
““Ndithu ine kwa inu ndine Mtumiki wokhulupirika;”
Verse 108 — Surah Ash-Shuara 26:108
““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
Verse 109 — Surah Ash-Shuara 26:109
““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 110 — Surah Ash-Shuara 26:110
““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
Verse 111 — Surah Ash-Shuara 26:111
“(Iwo) adati: “Nchotani kuti tikukhulupirire iwe chikhalirecho anthu wamba ndi amene akukutsatira?”
Verse 112 — Surah Ash-Shuara 26:112
“(Nuh) adati: “Sindikudziwa zimene adali kuchita (zomwe zachititsa kuti Allah awaongolere kunjira yoongoka).”
Verse 113 — Surah Ash-Shuara 26:113
““Chiwerengero chawo sichili kwina koma kwa Mbuye wanga, mukadakhala mukuzindikira.”
Verse 114 — Surah Ash-Shuara 26:114
““Ndipo sindine wopirikitsa okhulupirira (ku chipembedzo cha Allah kuti inu olemekezeka muchikhulupirire).”
Verse 115 — Surah Ash-Shuara 26:115
““Ine sikanthu , koma ndine mchenjezi woonekera.”
Verse 116 — Surah Ash-Shuara 26:116
“(Iwo) adati: “Ngati susiya, iwe Nuh, (zonena zakozi) ndithu ukhala mmodzi mwa ogendedwa (miyala mpaka ufe).”
Verse 117 — Surah Ash-Shuara 26:117
“(Nuh) adati (kwa Allah): “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga anditsutsa.”
Verse 118 — Surah Ash-Shuara 26:118
“Choncho weruzani pakati panga ndi pakati pa iwo (chiweruzo chabwino), ndipo ndipulumutseni pamodzi ndi amene alinane mwa okhulupirira.”
Verse 119 — Surah Ash-Shuara 26:119
“Choncho, tidampulumutsa pamodzi ndi omwe adali naye m’chombo chodzadza (ndi chilichonse chamoyo chomwe chidalipo m’dziko, chachimuna ndi chachikazi chidaikidwa m’menemo)
Verse 120 — Surah Ash-Shuara 26:120
“Pambuyo pake tidawamiza otsalawo
Verse 121 — Surah Ash-Shuara 26:121
“Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira
Verse 122 — Surah Ash-Shuara 26:122
“Ndipo ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha
Verse 123 — Surah Ash-Shuara 26:123
“Naonso Âdi adatsutsa atumiki
Verse 124 — Surah Ash-Shuara 26:124
“Pamene m’bale wawo (Mneneri) Hûd adawafunsa kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”
Verse 125 — Surah Ash-Shuara 26:125
““Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu;”
Verse 126 — Surah Ash-Shuara 26:126
““Choncho, muopeni Allah ndipo mverani ine.”
Verse 127 — Surah Ash-Shuara 26:127
““Ndipo pazimenezi sindikukupemphani malipiro; ndithu malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 128 — Surah Ash-Shuara 26:128
““Kodi mukudzimangira nyumba pamalo paliponse pachitunda pokongola, moseweretsa?”
Verse 129 — Surah Ash-Shuara 26:129
““Ndipo mukudzimangira (nyumba zonga) linga ngati kuti mukuona kuti mudzakhala muyaya?”
Verse 130 — Surah Ash-Shuara 26:130
““Ndipo mukamamenya nkhondo mumamenya modzitukumula.”
Verse 131 — Surah Ash-Shuara 26:131
““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
Verse 132 — Surah Ash-Shuara 26:132
““Ndipo muopeni Yemwe adakupatsani zimene mukuzidziwa.”
Verse 133 — Surah Ash-Shuara 26:133
““Adakupatsani ziweto ndi ana.”
Verse 134 — Surah Ash-Shuara 26:134
““Ndi minda ndi akasupe.”
Verse 135 — Surah Ash-Shuara 26:135
““Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”
Verse 136 — Surah Ash-Shuara 26:136
“Iwo adati: “Kwa ife nchimodzimodzi, utichenjeze kapena iwe usakhale mmodzi mwa ochenjeza.”
Verse 137 — Surah Ash-Shuara 26:137
““Ndithu kutero (anthu ena kudzitcha atumiki a Allah), sikanthu koma ndi machitidwe a anthu akale.”
Verse 138 — Surah Ash-Shuara 26:138
““Ndipo ife sitidzalangidwa (monga momwe ukunenera).”
Verse 139 — Surah Ash-Shuara 26:139
“Choncho adamtsutsa, ndipo tidawaononga. Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira
Verse 140 — Surah Ash-Shuara 26:140
“Ndipo ndithu Mbuye wako ndiye Wamphamvu zoposa; Wachisoni chosatha
Verse 141 — Surah Ash-Shuara 26:141
“A Samudu (naonso) adatsutsa atumiki
Verse 142 — Surah Ash-Shuara 26:142
“Pamene m’bale wawo Swalih adawauza kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”
Verse 143 — Surah Ash-Shuara 26:143
““Ndithu ine ndimtumiki wokhulupirika kwa inu.”
Verse 144 — Surah Ash-Shuara 26:144
““Choncho muopeni Allah ndipo mverani ine.”
Verse 145 — Surah Ash-Shuara 26:145
““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi. Palibe kumene kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 146 — Surah Ash-Shuara 26:146
““Kodi (mukuganizira kuti) mudzasiidwa mwamtendere pa izi zili pano (popanda imfa kukudzerani?)”
Verse 147 — Surah Ash-Shuara 26:147
““M’minda ndi mu akasupe?”
Verse 148 — Surah Ash-Shuara 26:148
““Ndi (m’minda) yammera ndi mitengo yakanjedza yamikoko yakupsa yofewa?”
Verse 149 — Surah Ash-Shuara 26:149
““Ndipo mukugoba nyumba m’mapiri mwaluso.”
Verse 150 — Surah Ash-Shuara 26:150
““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
Verse 151 — Surah Ash-Shuara 26:151
““Ndipo musamvere za awo opyola malire.”
Verse 152 — Surah Ash-Shuara 26:152
““Amene akuononga pa dziko, ndipo sakonza.”
Verse 153 — Surah Ash-Shuara 26:153
“Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”
Verse 154 — Surah Ash-Shuara 26:154
““Iwe suli kanthu, koma munthu ngati ife; tabwera ndi chozizwitsa, ngati ndiwedi mmodzi wa onena zoona!”
Verse 155 — Surah Ash-Shuara 26:155
“Iye adati: “(Ndakubweretserani) ngamira iyi yaikazi; (koma) ili ndi gawo lake lakumwa, ndipo inu muli ndi gawo lanu lakutunga (madzi) patsiku lodziwika. (Tsiku lina lotunga rnadzi anthu).”
Verse 156 — Surah Ash-Shuara 26:156
““Ndipo musaikhudze ndi choipa chilichonse kuopera kuti chingakupezeni chilango cha tsiku lalikulu.”
Verse 157 — Surah Ash-Shuara 26:157
“Koma iwo adaipha; ndipo adali odzinena (pamene chidadza chilango cha Allah)
Verse 158 — Surah Ash-Shuara 26:158
“Choncho chilango (cha Allah) chidawaononga, ndithu pa zimenezi pali phunziro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira
Verse 159 — Surah Ash-Shuara 26:159
“Ndipo, ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; wachisoni chosatha
Verse 160 — Surah Ash-Shuara 26:160
“Anthu a Luti adatsutsa atumiki
Verse 161 — Surah Ash-Shuara 26:161
“Pamene m’bale wawo Luti adanena kwa iwo (kuti): “Kodi simuopa (Allah)?”
Verse 162 — Surah Ash-Shuara 26:162
““Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”
Verse 163 — Surah Ash-Shuara 26:163
““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
Verse 164 — Surah Ash-Shuara 26:164
““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; palibe komwe kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wazolengedwa.”
Verse 165 — Surah Ash-Shuara 26:165
““Kodi mukugonana ndi amuna (anzanu) muzolengedwa (za Allah)
Verse 166 — Surah Ash-Shuara 26:166
““Ndikusiya amene Mbuye wanu adakulengerani kuti akhale akazi anu? Ndithu inu ndinu anthu olumpha malire.”
Verse 167 — Surah Ash-Shuara 26:167
“Iwo adati: “Ngati susiya (izi), E iwe Luti! ndithu ukhala mmodzi wa opirikitsidwa.”
Verse 168 — Surah Ash-Shuara 26:168
“Iye adati: “Ndithu ine ndine m’modzi wakuzida izi zochita zanu (choncho Sindisiya kuzidzudzula).”
Verse 169 — Surah Ash-Shuara 26:169
““E Mbuye wanga! Ndipulumutseni ine ndi banja langa ku (matsoka a) zimene akuchita.”
Verse 170 — Surah Ash-Shuara 26:170
“Ndipo tidampulumutsa iye ndi onse a pa banja lake
Verse 171 — Surah Ash-Shuara 26:171
“Kupatula nkhalamba yaikazi idali mwa otsalira m’mbuyo
Verse 172 — Surah Ash-Shuara 26:172
“Titatero tidawaononga enawo
Verse 173 — Surah Ash-Shuara 26:173
“Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji, mvula ya ochenjezedwa
Verse 174 — Surah Ash-Shuara 26:174
“Ndithu pazimenezi pali malingaliro. Koma ambiri a iwo sadali okhulupirira
Verse 175 — Surah Ash-Shuara 26:175
“Ndipo, ndithu Mbuye wako, Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha
Verse 176 — Surah Ash-Shuara 26:176
“Anthu a m’dziko lamitengo yambiri (Madiana) adatsutsa atumiki
Verse 177 — Surah Ash-Shuara 26:177
“(Akumbutse) pamene (Mneneri) Shuaib adati kwa iwo: “Kodi simuopa (Allah)?”
Verse 178 — Surah Ash-Shuara 26:178
““Ndithu ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”
Verse 179 — Surah Ash-Shuara 26:179
““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”
Verse 180 — Surah Ash-Shuara 26:180
““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; kulibe malipiro anga koma kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 181 — Surah Ash-Shuara 26:181
““Kwaniritsani mulingo (pamalonda pamene mukupima), ndipo musakhale mwaopungula (mulingo).”
Verse 182 — Surah Ash-Shuara 26:182
““Ndipo yesani ndi sikelo yolungama (yolondola).”
Verse 183 — Surah Ash-Shuara 26:183
““Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo, ndiponso musayende padziko uku mukuononga.”
Verse 184 — Surah Ash-Shuara 26:184
““Ndipo muopeni amene adalenga inu ndiponso zolengedwa zoyamba (zimene zidanka kale).”
Verse 185 — Surah Ash-Shuara 26:185
“Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”
Verse 186 — Surah Ash-Shuara 26:186
““Ndipo iwe suli kanthu koma munthu ngati ife, ndipo ndithu tikukutsimikizira kuti ndiwe mmodzi wa abodza.”
Verse 187 — Surah Ash-Shuara 26:187
““Choncho tigwetsere zidutswa za thambo (kuti zitiononge) ngati uli mmodzi wa onena zoona.”
Verse 188 — Surah Ash-Shuara 26:188
“(Shuaib) adati: “Mbuye wanga Ngodziwa kwambiri zimene mukuchita. (Akadzaona kuti inu ngoyenera kulangidwa ndizidutswa za thambo, adzakulangani).”
Verse 189 — Surah Ash-Shuara 26:189
“Koma adamutsutsa. Ndipo chidawagwera chilango chatsiku la mthunzi; ndithu chimenecho chidali chilango cha tsiku lalikulu
Verse 190 — Surah Ash-Shuara 26:190
“Ndithu pa zimenezi pali lingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira
Verse 191 — Surah Ash-Shuara 26:191
“Ndipo, ndithu Mbuye wako Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha
Verse 192 — Surah Ash-Shuara 26:192
“Ndipo, ndithu iyi (Qur’an) ndiyo chivumbulutso cha Mbuye wazolengedwa zonse
Verse 193 — Surah Ash-Shuara 26:193
“Mzimu Wokhulupirika (Jiburil) udaivumbulutsa
Verse 194 — Surah Ash-Shuara 26:194
“Pa mtima wako kuti ukhale mmodzi wa achenjezi
Verse 195 — Surah Ash-Shuara 26:195
“M’chiyankhulo cha Chiarabu chomveka bwino
Verse 196 — Surah Ash-Shuara 26:196
“Ndipo ndithu izi (zomwe zili m’Qur’an) zilipo m’mabuku akale
Verse 197 — Surah Ash-Shuara 26:197
“Kodi sipadapezeke chisonyezo kwa iwo kuti akuidziwa (Qur’an) odziwa mwa ana a Israyeli (kotero kuti ena alowa m’Chisilamu)
Verse 198 — Surah Ash-Shuara 26:198
“Ndipo tikadaivumbulutsa kwa wina amene sali Muarabu
Verse 199 — Surah Ash-Shuara 26:199
“Kotero kuti nkuwawerengera momveka bwino, sakadaikhulupirira
Verse 200 — Surah Ash-Shuara 26:200
“Momwemo ndimo tidalowetsera kuitsutsa (Qur’an) m’mitima ya oipa
Verse 201 — Surah Ash-Shuara 26:201
“Sangaikhulupirire kufikira ataona chilango chowawa
Verse 202 — Surah Ash-Shuara 26:202
“Choncho chidzawadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira
Verse 203 — Surah Ash-Shuara 26:203
“Tero adzayamba kunena: “Kodi ife tipatsidwa nthawi (yoti tilape)?”
Verse 204 — Surah Ash-Shuara 26:204
“Kodi akuchifulumizitsa chilango Chathu
Verse 205 — Surah Ash-Shuara 26:205
“Kodi ukuona bwanji, ngati titawasangalatsa zaka (zankhaninkhani)
Verse 206 — Surah Ash-Shuara 26:206
“Kenako nkuwadzera (chilango) chomwe adalonjezedwa
Verse 207 — Surah Ash-Shuara 26:207
“Sizidawathandize zomwe adali kusangalatsidwa nazozo
Verse 208 — Surah Ash-Shuara 26:208
“Ndipo sitidauononge mudzi uliwonse koma udali ndi achenjezi
Verse 209 — Surah Ash-Shuara 26:209
“(Kuti akhale) chikumbutso. Ndipo sitidali osalungama (powaononga popanda kuwachenjeza)
Verse 210 — Surah Ash-Shuara 26:210
“Ndipo asatana sadaivumbulutse (iyi Qur’an monga osakhulupirira akunenera monyoza)
Verse 211 — Surah Ash-Shuara 26:211
“Ndipo sikoyenera kwa iwo (kuivumbulutsa Qur’an) ndiponso sangathe
Verse 212 — Surah Ash-Shuara 26:212
“Ndithu iwo ngotsekerezedwa kumvetsera (zimene angelo amalankhula kumwamba)
Verse 213 — Surah Ash-Shuara 26:213
“Choncho usapembedze mulungu wina pamodzi ndi Allah, kuti ungakhale mwa olangidwa
Verse 214 — Surah Ash-Shuara 26:214
“Ndipo achenjeze abale ako a pafupi
Verse 215 — Surah Ash-Shuara 26:215
“Ndipo fungatira ndi phiko lako amene akutsata mwa okhulupirira. (Ukhale wachifundo kwa iwo)
Verse 216 — Surah Ash-Shuara 26:216
“Ngati atakunyoza, nena: “Ine ndili kutali ndi zimene mukuchitazo.”
Verse 217 — Surah Ash-Shuara 26:217
“Ndipo tsamira kwa (Mbuye wako) Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha
Verse 218 — Surah Ash-Shuara 26:218
“Yemwe akukuona pamene ukuimilira (pamapemphero)
Verse 219 — Surah Ash-Shuara 26:219
“Ndikutembenukatembenuka kwako (pogwetsa mphumi yako pansi ndi kudzuka ndi kuimilira) pamodzi ndi ogwetsa mphumi pansi (polambira Allah)
Verse 220 — Surah Ash-Shuara 26:220
“Ndithu Iye Ngwakumva; Ngodziwa chilichonse
Verse 221 — Surah Ash-Shuara 26:221
“Kodi ndikuuzeni amene asatana amawatsikira
Verse 222 — Surah Ash-Shuara 26:222
“Amamtsikira yense wabodza lamkunkhuniza; wamachimo
Verse 223 — Surah Ash-Shuara 26:223
“Amawaponyera (asatana anzawo a mu anthu) zimene azimva. Koma ambiri a iwo ngabodza
Verse 224 — Surah Ash-Shuara 26:224
“Ndipo alakatuli (olakatula zopanda phindu) amatsatidwa ndi (anthu) opotoka
Verse 225 — Surah Ash-Shuara 26:225
“Kodi suona kuti iwo akungoyumbayumba m’chigwa chilichonse (chamawu)
Verse 226 — Surah Ash-Shuara 26:226
“Ndithunso iwo akunena zomwe sachita
Verse 227 — Surah Ash-Shuara 26:227
“Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, ndikumamtchula Allah mowirikiza, ndikuzipulumutsa okha pambuyo pochitiridwa zoipa. Ndipo posachedwa amene adzichitira okha zoipa adziwa kotembenukira komwe adzatembenukire