Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 27 - An-Naml
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah An-Naml 27:1
“Tâ-Sîn. Izi ndi Ayah (ndime) (za Qur’an buku lodzazidwa ndi zothandiza), ndiponso buku lofotokoza (chilichonse chauzimu ndi chamoyo wadziko)
Verse 2 — Surah An-Naml 27:2
“(Qur’an) nchiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira
Verse 3 — Surah An-Naml 27:3
“Amene akupemphera Swala (zisanu, modzichepetsa ndi mokwaniritsa malamulo ake) ndi kumapereka Zakaat (m’nthawi yake), ndipo iwo ali ndi chitsimikizo champhamvu cha (moyo wa) tsiku la chimaliziro
Verse 4 — Surah An-Naml 27:4
“Ndithu amene sakhulupirira za (moyo wa) tsiku la chimaliziro, tawakometsera zochita zoipa kukhala ngati zabwino; choncho iwo akungoyumbayumba (m’kusokera kwawo)
Verse 5 — Surah An-Naml 27:5
“Iwowo ndiamene adzapeza chilango choipa; iwo tsiku lachimaliziro ngotayika zedi, (adzaonongeka ku Moto motheratu)
Verse 6 — Surah An-Naml 27:6
“Ndipo ndithu iwe ukuphunzitsidwa Qur’an kuchokera kwa mwini nzeru zakuya, Wodziwa kwambiri
Verse 7 — Surah An-Naml 27:7
“(Kumbuka) Mûsa pamene adauza banja lake (mkazi wake): “Ndithu ine ndaona moto; posachedwapa ndikubweretserani nkhani za kumeneko, kapena ndikubweretserani chikuni cha moto kuti inu muothe
Verse 8 — Surah An-Naml 27:8
“Choncho pamene adaudzera (motowo) kudaitanidwa: “Wadalitsidwa yemwe ali m’moto ndi yemwe ali m’mphepete mwake; ndipo walemekezeka Allah Mbuye wa zolengedwa
Verse 9 — Surah An-Naml 27:9
“E iwe Mûsa! Ndithu ine ndine Allah, Wamphamvu zoposa; Wanzeru zakuya
Verse 10 — Surah An-Naml 27:10
“Ndipo ponya (pansi) ndodo yako! (Pamene adaiponya idasanduka njoka), tero pamene adaiwona ikugwedezeka (ndodo ija) ngati njoka, adatembenuka kuthawa, ndipo sadacheuke (kapena kudikira kuti amve mawu omvekawo): “E iwe Mûsa! Usaope. Ndithu Ine, saopa kwa Ine atumiki.”
Verse 11 — Surah An-Naml 27:11
““Koma amene wadzichitira yekha zoipa, kenako nkusintha (pochita) zabwino pambuyo pa zoipa, (ndimkhululukira) pakuti Ine ndine Wokhululuka kwabasi, Wachifundo chambiri.”
Verse 12 — Surah An-Naml 27:12
““Ndipo lowetsa dzanja lako palisani la mkanjo wako, ndipo lituluka lili loyera, (kuyera) kopanda matenda. (Ziwirizi) zili m’gulu la zododometsa zisanu ndi zinayi. Pita nazo kwa Farawo ndi anthu ake; ndithu iwo ndianthu otuluka m’chilamulo cha Allah.”
Verse 13 — Surah An-Naml 27:13
“Tero pamene zidawadzera zizindikiro Zathu zosonyeza (kuti iye ndimtumiki wa Allah) adati: “Awa ndimatsenga woonekera.”
Verse 14 — Surah An-Naml 27:14
“Ndipo adazitsutsa (zisonyezozo) mwachinyengo ndi modzikuza chikhalirecho mitima yawo idatsimikiza (kuti ndizoona zochokera kwa Allah); choncho, yang’ana adali bwanji malekezero a oononga
Verse 15 — Surah An-Naml 27:15
“Ndipo ndithu Daud ndi Sulaiman tidawapatsa nzeru (zazikulu; adayamika Allah) adati: “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah Yemwe watichitira ubwino kuposa ambiri mwa akapolo ake okhulupirira.”
Verse 16 — Surah An-Naml 27:16
“Ndipo Sulaiman adalowa mmalo mwa Daud pa nzeru ndi uneneri ndipo (Sulaiman) adati: “E inu anthu! Ndithu taphunzitsidwa (mpaka tikudziwa) chiyankhulo cha mbalame, ndiponso tapatsidwa chilichonse; ndithu umenewu ndiubwino wopenyeka
Verse 17 — Surah An-Naml 27:17
“Ndipo adasonkhanitsidwa kwa Sulaiman ankhondo ake ochokera m’ziwanda, anthu ndi mbalame, ndipo adawandandika m’magulumagulu
Verse 18 — Surah An-Naml 27:18
“Kufikira pamene adadza pachigwa chanyelere, nyelere idanena (kuuza zinzake): “E inu nyelere, lowani m’nyumba zanu poopa kuti angakupondeni Sulaiman ndi magulu ake ankhondo pomwe iwo sakudziwa (za inu).”
Verse 19 — Surah An-Naml 27:19
“Choncho adamwetulira, mosekelera chifukwa cha mawu ake aja (mawu a nyelere); ndipo (Sulaiman) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nyonga zakuti ndizithokozera mtendere wanu umene mwandidalitsa nawo pamodzi ndi makolo anga, ndi kuti ndizichita zabwino (zomwe) mukuziyanja; Kupyolera m’chifundo chanu, ndiponso ndilowetseni m’gulu la akapolo anu abwino.”
Verse 20 — Surah An-Naml 27:20
“Ndipo adayamba kuyendera mbalame, adati: “Kodi bwanji sindikumuona Huduhudu? Kapena ali m’gulu la amene pano palibe?”
Verse 21 — Surah An-Naml 27:21
““Ndithu ndimulanga chilango chokhwima, kapena ndimzinga (ndimdula khosi) pokhapokha andibweletsere umboni womveka (wosonyeza kuti adachoka pazifukwa zomveka).”
Verse 22 — Surah An-Naml 27:22
“Choncho (Hudhud) sadakhalitse nthawi yaitali; ndipo adati (kwa Sulaiman): “Ndatulukira zomwe iwe sudazitulukire, ndipo ndakubweletsera nkhani yotsimikizika kuchokera ku Saba.”
Verse 23 — Surah An-Naml 27:23
““Ndithu ine ndapeza mkazi akuwalamulira (anthu a ku dziko la Saba), ndipo wapatsidwa chilichonse; ndiponso ali ndi chimpando chachifumu chachikulu.”
Verse 24 — Surah An-Naml 27:24
““Ndampeza iye ndi anthu ake akulambira dzuwa kusiya Allah; ndipo satana wawakometsera zochita zawo zoipa; choncho wawatsekereza ku njira yolungama, tero sadaongoke.”
Verse 25 — Surah An-Naml 27:25
““Kuti asamlambire Allah yemwe amatulutsa zobisika kumwamba ndi pansi; ndipo akudziwa zimene mukubisa ndi zimene muonetsa poyera.”
Verse 26 — Surah An-Naml 27:26
““Allah! Palibe wina wopembedzedwa mwachoona koma Iye basi; Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) waukulu.”
Verse 27 — Surah An-Naml 27:27
“(Sulaiman) adati “Tiona ngati wanena zoona kapena ngati) uli m’gulu la onama.”
Verse 28 — Surah An-Naml 27:28
““Pita ndi kalata yangayi, kaiponye kwa iwo; kenako ukadzipatule kwa iwo (ukakhale pambali) ndi kuona momwe azikayankhira.”
Verse 29 — Surah An-Naml 27:29
“(Mfumukazi) idati; “E inu nduna! Ndithu kalata yolemekezeka yaponyedwa kwa ine.”
Verse 30 — Surah An-Naml 27:30
““Yachokera kwa Sulaiman, ndipo mawu ake ndi awa: ‘Mdzina la Allah, Wachifundo chambiri, Wachisoni.’
Verse 31 — Surah An-Naml 27:31
“‘Musadzikweze kwa ine, ndipo idzani kwa ine muli ogonjera malamulo anga.”
Verse 32 — Surah An-Naml 27:32
“(Mfumukazi idaonjezera) kunena: “E inu nduna! ndilangizeni pankhani yangayi; sindilamula kanthu mpaka inu mutandibwerera.”
Verse 33 — Surah An-Naml 27:33
“(Nduna) zidati: “Ife ndife eni nyonga ndi eni kumenya nkhondo mwaukali; koma zonse zili ndi inu; choncho yang’anani mmene mungalamulire.”
Verse 34 — Surah An-Naml 27:34
“(Mfumukazi) idati: “Ndithu mafumu akamalowa m’mudzi (wa anthu), amauononga motheratu, ndi kuwachita olemekezeka a m’menemo kukhala onyozeka. Mmenemo ndimomwe amachitira (nthawi zonse).”
Verse 35 — Surah An-Naml 27:35
““Koma ine nditumiza mitulo kwa iwo ndi kuyembekezera zimene abwere nazo otumidwawo.”
Verse 36 — Surah An-Naml 27:36
“Choncho pamene adafika (wamthenga wamkulu) kwa Sulaiman (ndi kupereka mphatso zija, Sulaiman adazikana) nati: “Mukundithandiza ndi chuma? zimene Allah wandipatsa ndizabwino kuposa zimene wakupatsani. Koma inu mukusangalala ndi mphatso zanu.”
Verse 37 — Surah An-Naml 27:37
“Bwerera (nazo) kwa iwo; ndithu tiwadzera ndi gulu lankhondo lomwe iwo sangathe kulimbana nalo; mtheradi, tikawatulutsa m’menemo ali onyozeka ndi oyaluka.”
Verse 38 — Surah An-Naml 27:38
“(Sulaiman adasonkhanitsa nduna zake) nati: “E inu nduna! Ndani abwere ndi mpando wake wachifumuwo kwa ine asadandidzere ali ogonja?”
Verse 39 — Surah An-Naml 27:39
“Chiwanda chotchedwa Ifrit chidati: “Ine ndikubweletsera chimenecho usadaimilire pamalo ako (oweruzira). Ndipo ndithu ine pa icho (chimpando) ndine wanyonga, wokhulupirika.”
Verse 40 — Surah An-Naml 27:40
“Yemwe adali ndi maphunziro (akuya) a m’buku adati: “Ine ndikubweletsera (chimpandocho) maso ako asadaphetire (usadatsinzine ndi kupenya).” Pamene adachiona chitakhazikitsidwa patsogolo pake, adati: “Izi nchifukwa cha ufulu wa Mbuye wanga kuti andiyese mayeso kodi ndithokoza kapena ndiusuliza (ufulu Wake). Ndipo amene akuthokoza ndithu ubwino wa kuthokozako udzakhala pa iye mwini. Ndipo amene akukana (mtendere wa Allah posathokoza), ndithu Mbuye wanga Ngokhupuka; Waulemu, (sasaukira chilichonse kwa anthu).”
Verse 41 — Surah An-Naml 27:41
“(Sulaiman) adati: “Msinthireni (maonekedwe a) mpando wake wachifumuwo kuti tione kodi auzindikira kapena akhala mwa omwe sazindikira (chinthu)
Verse 42 — Surah An-Naml 27:42
“Choncho pamene (mfumukazi) idadza, kudanenedwa: “Kodi mpando wako wachifumu uli ngati uwu?” Idati: “Uli ngati umenewu, ndithu ndipo ife tidapatsidwa kuzindikira (za uneneri wanu) tisadaone chozizwitsa ichi; ndipo, ndithu tidadzipereka (kwa Allah).”
Verse 43 — Surah An-Naml 27:43
“Ndipo (Sulaiman) adamuletsa zomwe amazipembedza kusiya Allah. Ndithu (mfumukaziyo) idali mwa anthu osakhulupirira (Allah)
Verse 44 — Surah An-Naml 27:44
“(Mfumukazi ija) idauzidwa kuti: “Lowa mkhonde la nyumba.” Koma pamene adaliona adaliganizira kuti ndidziwe; adakweza nsalu kumiyendo yake. (Sulaiman) adati: “Ndithu limeneli ndikhonde lomwe laziridwa ndi magalasi.” (Mfumukazi) idati: “E Mbuye wanga! Ndadzichitira ndekha chinyengo; choncho, ndagonjera kwa Allah, Mbuye wazolengedwa pamodzi ndi Sulaiman.”
Verse 45 — Surah An-Naml 27:45
“Ndipo ndithu Asamudu tidawatumizira m’bale wawo Swalih kuti awauze: “Mpembedzeni Allah.” Choncho adali magulu awiri omwe amakangana. (Ena adam’tsata pomwe ena adam’kana)
Verse 46 — Surah An-Naml 27:46
“(Swaleh) adati: “E inu anthu anga chifukwa ninji inu mukufulumizitsa choipa (kuti chidze) musanachite chabwino? Bwanji simukupempha chikhululuko kwa Allah kuti muchitiridwe chifundo?”
Verse 47 — Surah An-Naml 27:47
“(Iwo) adati: “Tapeza masoka oipa chifukwa cha iwe ndi omwe uli nawo.” (Iye) adati: “Tsoka lanu lili kwa Allah (chifukwa cha zolakwa zanu); koma inu ndinu anthu amene mukuyesedwa (ndi Allah kuti aone ngati mutsatire Mtumiki Wake kapena simutsatira).”
Verse 48 — Surah An-Naml 27:48
“Ndipo m’mudzimo adalipo anthu asanu ndi anayi omwe amaononga pa dziko, ndipo samakonza (chilichonse koma kuchiononga)
Verse 49 — Surah An-Naml 27:49
“(Iwo) adati: “Aliyense wa ife alumbire kwa Allah (kuti) iye (Swaleh) ndi banja lake timthira nkhondo usiku, ndipo kenako Timuuza mlowam’malo wake (kuti): “Sitidaone kuonongeka kwa m’bale wake; ndithu ife tikunena zoona.”
Verse 50 — Surah An-Naml 27:50
“Ndipo adakonza chiwembu ndi kutchera misampha yamphamvu, nafenso tidawatchera misampha yowaononga, iwo asakudziwa
Verse 51 — Surah An-Naml 27:51
“Tsono tayang’ana, kodi malekezero a chiwembu chawo adali otani! Tidawaononga iwo ndi anthu awo onse
Verse 52 — Surah An-Naml 27:52
“Izo ndinyumba zawo (zomwe zasanduka) mabwinja chifukwa cha chinyengo chawo. Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa odziwa
Verse 53 — Surah An-Naml 27:53
“Ndipo tidawapulumutsa amene adakhulupirira pakuti amamuopa (Allah)
Verse 54 — Surah An-Naml 27:54
“Ndipo (akumbutse nkhani ya) Luti pamene adanena kwa anthu ake: “Kodi mukuchita zadama uku inu mukuziona?”
Verse 55 — Surah An-Naml 27:55
““Kodi inu mukugona ndi amuna pokwaniritsa chilakolako (cha chilengedwe) kusiya akazi? koma inu ndinu mbuli.”
Verse 56 — Surah An-Naml 27:56
“۞ Koma anthu ake sadayankhe yankho lina koma ili (lakuti): “Apirikitseni otsatira Luti m’mudzi mwanumu; ndithu iwo ndianthu odziyeretsa (asakhale pamodzi ndi ife adama).”
Verse 57 — Surah An-Naml 27:57
“Choncho tidampulumutsa iye ndi otsatira kupatula mkazi wake; tidamkozera kukhala mmodzi mwa otsalira (kuti aonongedwe pamodzi ndi oonongedwa, chifukwa cha ntchito zake zoipa ngakhale kuti adali mkazi wa mneneri)
Verse 58 — Surah An-Naml 27:58
“Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji mvula ya ochenjezedwa (koma osachenjezeka)
Verse 59 — Surah An-Naml 27:59
“Nena: “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, ndipo mtendere ukhale pa akapolo Ake omwe adawasankha. Kodi wabwino ndi Allah kapena zimene akumphatikiza nazozo?”
Verse 60 — Surah An-Naml 27:60
“(E iwe Mtumiki! Pitiriza kuwafunsa) kodi kapena (wabwino) ndiamene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zam’menemo) ndi kukutsitsirani madzi (mvula yothandiza) kuchokera kumwamba, choncho ndi madziwo timameretsa madimba okongola. Inu simungathe kumeretsa mitengo yake. Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu (wina)? Koma iwo (Akafiri) ndi anthu opotoka
Verse 61 — Surah An-Naml 27:61
“Kodi kapena (wabwino) ndiamene adapanga nthaka kukhala malo okhazikika ndi kuika mitsinje pakati pake ndi kuipangira mapiri, ndi kuika chitsekerezo pakati pa nyanja ziwiri (nyanja ya madzi amchere, ndi yamadzi ozizira)? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Koma ambiri a iwo sadziwa
Verse 62 — Surah An-Naml 27:62
“Kapena (wabwino) ndiyemwe amamuyankha wozunzika akamampempha ndi kumchotsera masautso ake ndi kukuchitani inu kukhala oyendetsa dziko lapansi? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Ndithu kulangizika kwanu nkochepa
Verse 63 — Surah An-Naml 27:63
“Kapena (wabwino) ndiyemwe amakuongolerani mu mdima wa pamtunda ndi panyanja ndi kutumiza mphepo kuti ikudzetsereni nkhani yabwino patsogolo pa chifundo chake (mvula isanagwe)? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Allah watukuka ku zimene akumuphatikiza nazo
Verse 64 — Surah An-Naml 27:64
“Kapena (wabwino) ndiamene adayambitsa zolengedwa, (ndipo) kenako adzazibweza, kapenanso amene amakupatsani rizq (chakudya) kuchokera kumwamba ndi m’nthaka? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu winanso? Nena: “Bweretsani umboni wanu ngati mukunena zoona (wotsimikizira kuti Allah ali ndi mnzake).”
Verse 65 — Surah An-Naml 27:65
“Nena: “Palibe amene alipo kumwamba ndi pansi akudziwa zam’seri (zomwe zisanadze) kupatula Allah basi. Ndipo (amene akuwapembedza) sadziwa kuti ndiliti adzaukitsidwa ku imfa.”
Verse 66 — Surah An-Naml 27:66
“Kwakhwima liti kudziwa kwawo (za kudza) kwa tsiku la chimaliziro? Koma iwo ali mchikaiko ndi za tsikulo; koma iwo ngakhungu pa zatsikulo
Verse 67 — Surah An-Naml 27:67
“Ndipo adanena omwe adatsutsa (za Allah): “Kodi tikadzakhala dothi, ife ndi makolo athu akale, (nzoona) tidzatulutsidwanso (m’manda tili amoyo)?”
Verse 68 — Surah An-Naml 27:68
“Ndithu tidalonjezedwa izi, ife ndi makolo athu kale, izi sichina koma ndi nthano (zabodza) za anthu akale.”
Verse 69 — Surah An-Naml 27:69
“Nena: “Yendani pa dziko ndi kuona momwe adalili mapeto a oipa.”
Verse 70 — Surah An-Naml 27:70
“Ndipo usawadandaulire, ndiponso usakhale wobanika chifukwa cha ziwembu zomwe akuchita
Verse 71 — Surah An-Naml 27:71
“Ndipo (iwo) akuti: “Kodi lonjezoli lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”
Verse 72 — Surah An-Naml 27:72
“Nena: “Kapena zina mwa zomwe mukuzifulumizitsa zili pafupi kukupezani.”
Verse 73 — Surah An-Naml 27:73
“Ndipo ndithu Mbuye wako ndi mwini kupereka ubwino (waukulu) kwa anthu; koma ambiri a iwo sathokoza
Verse 74 — Surah An-Naml 27:74
“Ndipo ndithu Mbuye wako akudziwa zomwe zikubisa zifuwa zawo ndi zomwe akuonetsera poyera
Verse 75 — Surah An-Naml 27:75
“Ndiponso palibe chobisika kumwamba ndi m’nthaka koma chili m’buku lofotokoza chilichonse
Verse 76 — Surah An-Naml 27:76
“Ndithu Qur’an iyi, ikufotokoza kwambiri za ana a Israyeli pa zambiri zomwe iwo akutsutsana
Verse 77 — Surah An-Naml 27:77
“Ndipo ndithu iyi (Qur’an) ndichiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira
Verse 78 — Surah An-Naml 27:78
“Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo ndi chiweruzo chake (choona); ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa Ngodziwa chilichonse
Verse 79 — Surah An-Naml 27:79
“Choncho tsamira kwa Allah; ndithu iwe uli pa njira yachoonadi yoonekera
Verse 80 — Surah An-Naml 27:80
“Ndithu iwe sungathe kuwachititsa kuti amve kuitana kwako akufa, ndiponso sungathe kuwachititsa kuti agonthi amve kuitanako, pamene akucheuka kutembenuza misana (osafuna kumva ulaliki wako)
Verse 81 — Surah An-Naml 27:81
“Ndiponso suli owaongola akhungu m’kusokera kwawo, ndipo sungachititse kuti amve (uthenga wako) kupatula yemwe akukhulupirira Ayah (ndime) Zathu; iwowo ndiwo Asilamu (ogonjera malamulo Athu)
Verse 82 — Surah An-Naml 27:82
“Ndipo mawu (onena kudza kwa Qiyâma) akadzatsimikizika pa iwo, tidzawatulutsira chinyama m’nthaka chimene chidzawayankhula kuti ndithu anthu adalibe chitsimikizo pa Ayah (ndime) Zathu
Verse 83 — Surah An-Naml 27:83
“Ndipo (akumbutse za) tsiku lormwe tidzasonkhanitsa magulumagulu mu m’badwo uliwonse omwe amatsutsa Ayah (ndime) Zathu. Ndipo iwo adzakhala magulumagulu
Verse 84 — Surah An-Naml 27:84
“Kufikira pomwe adzaza; (Allah) adzati: “Kodi inu mudazitsutsa Ayah (ndime) Zanga popanda kuzidziwa bwinobwino, nanga mumachita chiyani?”
Verse 85 — Surah An-Naml 27:85
“Ndipo mawu onena za kuonongeka adzatsimikizika pa iwo, chifukwa cha chinyengo chawo (chodzichitira okha) ndipo iwo sadzawiringula
Verse 86 — Surah An-Naml 27:86
“Kodi saona kuti Ife tapanga usiku ndi cholinga chakuti apumule m’menemo, ndinso usana woyera (kuti aone)? Ndithu mu zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira
Verse 87 — Surah An-Naml 27:87
“Ndipo (akumbutse za) tsiku limene lipenga (la chiweruziro) lidzaimbidwa, adzadzidzimuka amene ali kumwamba ndi amene ali pansi kupatula yemwe Allah wamfuna (kuti adzadzidzimuke); ndipo onse adzamdzera (Allah) ali odzichepetsa (ofooka)
Verse 88 — Surah An-Naml 27:88
“Ndipo udzawaona mapiri ndi kuwaganizira kuti akhazikika pomwe akuyenda kuyenda kwa mitambo. Chimenecho ndichikonzero cha Allah chimene adakonzera chinthu chilichonse. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene muchita
Verse 89 — Surah An-Naml 27:89
“Amene adzadza ndi chabwino, adzalandira mphoto yoposa chabwinocho; ndikuopsa kwa tsiku limenelo, iwo adzakhala nako mwamtendere
Verse 90 — Surah An-Naml 27:90
“Koma amene adzadza ndi choipa, adzaponyedwa ku Moto champhumi (ndipo kudzanenedwa kwa iwo): “Kodi mungalipidwe (zina) osati zomwe mumachita?”
Verse 91 — Surah An-Naml 27:91
“(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu ndalamulidwa kumpembedza Mbuye wa mzinda uwu, Yemwe adaukhazika wopatulika. Ndipo zinthu zonse nza Iye (Allah), ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa ogonjera (Allah).”
Verse 92 — Surah An-Naml 27:92
““Ndiponso (ndalamulidwa) kuti ndiwerenge Qur’an.” Ndipo amene waongoka, ubwino wa kuongokako uli pa iye; ndipo amene wasokera, (wadzisokeretsa yekha). Nena: “Ndithu ine sikanthu koma ndine mmodzi wa achenjezi. (Ndilibe udindo wina woposa uwu).”
Verse 93 — Surah An-Naml 27:93
“Ndipo nena: “Kuyamikidwa konse (kwabwino) nkwa Allah; posachedwapa akusonyezani zizindikiro Zake, ndipo muzizindikira.” Ndipo Mbuye wako sali woiwala zimene mukuchita