Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 28 - Al-Qasas
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Qasas 28:1
“Tâ-Sîn-Mîm
Verse 2 — Surah Al-Qasas 28:2
“Izi ndi Ayah (ndime) za m’buku (la Qur’an) lofotokoza (chilichonse chofunika pa Chipembedzo)
Verse 3 — Surah Al-Qasas 28:3
“Tikukulakatulira (iwe Mtumiki) nkhani za Mûsa ndi Farawo m’njira yoona kwa anthu okhulupirira. (Koma osakhulupirira sangapindule kanthu ndi nkhanizi)
Verse 4 — Surah Al-Qasas 28:4
“Ndithu Farawo adadzikuza pa dziko, ndipo adawakhazika (anthu a m’dzikolo) m’magulumagulu; gulu lina la mwa iwo adalifooketsa (poliyesa akapolo) ndi kupha ana awo achimuna, ndi kuwasiya a moyo ana awo achikazi. Ndithu iye adali mmodzi wa oononga kwambiri
Verse 5 — Surah Al-Qasas 28:5
“Ndipo tidafuna kuwachitira zabwino amene adafooketsedwa m’dziko (la Iguputo), ndi kuwachita kukhala atsogoleri ndi kuwachitanso kukhala amlowa mmalo ( a Baiti Al-Makadasi)
Verse 6 — Surah Al-Qasas 28:6
“Ndi kuwapatsa mphamvu za pa dziko (kuti azichita mmene angafunire) ndi kuti timuonetse Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo kuchokera kwa iwo (ana a Israel), zomwe amaziwopa (kuti zingawathetsere ufumu wawo)
Verse 7 — Surah Al-Qasas 28:7
“Ndipo tidamzindikiritsa mayi wa Mûsa (tinati): “Muyamwitse (mwana wako), ndipo ukamuopera (chiwembu cha Farawo), mponye mu mtsinje usaope, ndipo usadandaule ndithu Ife tidzamubwezera kwa iwe, ndipo tidzamchita kukhala mmodzi wa atumiki.”
Verse 8 — Surah Al-Qasas 28:8
“Choncho adamtola anthu a Farawo kuti mapeto ake adzakhale m’dani kwa iwo ndi odandaulitsa. Ndithu Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo adali olakwa
Verse 9 — Surah Al-Qasas 28:9
“Ndipo mkazi wa Farawo adati: “(Musamuphe, akhale) chosangalatsa diso langa ndi lako; musamuphe mwina angatithandize, kapena tingam’chite kukhala mwana (wathu.” Adanena izi) iwo asakudziwa (kuti adzakhala m’dani wawo)
Verse 10 — Surah Al-Qasas 28:10
“Ndipo mu mtima mwa mayi wa Mûsa mudali mopanda kanthu (mudalibe maganizo ena koma maganizo a mwana wake). Padatsala pang’ono kuti aonetse (chinsinsi cha mwanayo ponena kuti adali mwana wake), tikadapanda kulimbitsa mtima wake, kuti akhale mmodzi mwa okhulupirira (lonjezo la Allah)
Verse 11 — Surah Al-Qasas 28:11
“Ndipo (mayi wa Musayo) adauza mlongo wake (wa Mûsa): “Mtsatire, (komwe madzi akupita naye).” Choncho iye ankamuyang’ana chapatali pomwe iwo samadziwa (za ichi)
Verse 12 — Surah Al-Qasas 28:12
“Ndipo poyamba tidamuletsa kuti asayamwe mawere a woyamwitsa, (kufikira pomwe mlongo wake) adati: “Kodi ndikusonyezeni eni nyumba omwe angakulelereni ndi kukhala naye momteteza bwino mwanayo?”
Verse 13 — Surah Al-Qasas 28:13
“Choncho tidamubwezera kwa mayi wake kuti maso ake atonthole, (mtima wake ukhazikike) ndi kuti asadandaule; ndi kuti adziwe kuti lonjezo la Allah ndi loona. Koma ambiri a iwo sadziwa
Verse 14 — Surah Al-Qasas 28:14
“Ndipo (Mûsa) pamene adakula nsinkhu wake ndi kulingana bwino tidampatsa nzeru ndi maphunziro. Ndipo umo ndimomwe timawalipirira ochita zabwino
Verse 15 — Surah Al-Qasas 28:15
“Ndipo (tsiku lina) adalowa mu mzinda mozemba, eni m’zindawo osadziwa. Ndipo adapeza m’menemo anthu awiri akumenyana, mmodzi wochokera ku gulu lake, ndipo winayo wochokera kwa adani ake. Tsono wa kugulu lake uja adampempha chithandizo pa mdani wake uja, ndipo Mûsa adammenya chibagera mpaka kumupha (mdaniyo). Adanena: “Iyi (ndachitayi) ndintchito ya satana; ndithu iye ndimdani wosokeretsa, woonekera.”
Verse 16 — Surah Al-Qasas 28:16
“Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ndadzichitira zoipa ndekha! Choncho ndikhululukireni!” Tero (Allah) adamkhululukira (chifukwa sadalinge kupha). Ndithu Iye (Allah) Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha
Verse 17 — Surah Al-Qasas 28:17
“Adati: “E Mbuye wanga! Chifukwa cha kuti mwandidalitsa, sindidzakhala mthangati wa oipa.”
Verse 18 — Surah Al-Qasas 28:18
“Choncho kudamuchera mu mzindamo (m’mawa mwake) uku ali wodzazidwa ndi mantha akuyembekezera (kuti chiyani chimpeze pa zimene zidachitika); pompo munthu uja adampempha dzulo chithandizo ankamuitana (kuti amthandize kumenyana ndi m’dani wake wina). Mûsa adamuuza: “Ndithudi ndiwe wopotoka owonekera.”
Verse 19 — Surah Al-Qasas 28:19
“Choncho pamene adafuna kumpanda, yemwe ndi mdani wa awiriwo, (uja wofuna chithandizo kwa Mûsa adaganiza kuti Mûsa afuna kuti ampande iye), ndipo adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukufuna kundipha monga momwe udaphera munthu uja dzulo? Iwe sufuna china koma kukhala wodzitukumula (wankhanza) pa dziko, ndipo sukufuna kukhala mmodzi mwa ochita zabwino (oyanjanitsa okangana ndi kukonza zinthu).”
Verse 20 — Surah Al-Qasas 28:20
“(Farawo zitamfika mphekesera kuti Mûsa wapha munthu pothangata mu Israyeli, adalamula kuti Mûsa paliponse pomwe angapezeke, agwidwe ndi kuphedwa). Choncho munthu adadza akuthamanga kuchokera kumalekezero a m’zindawo. Adati: “E iwe Mûsa! Akuluakulu akukuchitira upo kuti akuphe choncho choka (m’dziko muno). Ndithu ine ndine mmodzi mwa okufunira iwe zabwino.”
Verse 21 — Surah Al-Qasas 28:21
“Ndipo adachoka mu mzindawo ali woopa uku akuyembekezera (kumpeza choipa kuchokera kwa adani ake). Adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu ochita zoipa.”
Verse 22 — Surah Al-Qasas 28:22
“Ndipo pamene adalunjika (kumka) ku Madiyan adati: “Mwina Mbuye wanga andiongolera kunjira yoyenera.”
Verse 23 — Surah Al-Qasas 28:23
“Ndipo pamene adawafika madzi a ku Madiyan (pomwe anthu kumeneko ankatungapo madzi), adapeza gulu la anthu likumwetsa (ziweto zawo), ndipo pambali (pa gululo) adapeza akazi awiri akuletsa (ziweto zawo kuti zisapite kukamwa ndi ziweto zinazo). (Mûsa) adati: “Kodi mwatani? (Bwanji simukuzimwetsa ziweto zanu?)” Iwo Adati: “Sitingamwetse (ziweto zathu) mpaka abusa atachotsa (ziweto zawo, chifukwa sitingathe kulimbana nawo). Ndipo bambo wathu ndinkhalamba yaikulu kwabasi.”
Verse 24 — Surah Al-Qasas 28:24
“Choncho (Mûsa) adawamwetsera (ziweto zawo); kenako adapita pamthunzi, ndipo adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndiwosaukira chabwino chimene munditsitsire.”
Verse 25 — Surah Al-Qasas 28:25
“Kenako mmodzi mwa asungwana aja adadza kwa iye uku akuyenda mwa manyazi. (Msungwanayo) adati: “Ndithu tate wanga akukuitana kuti akakupatse malipiro pakutimwetsera (ziweto zathu).” Choncho pamene adamdzera, (mneneri Shuaib) ndikumulongosolera nkhani, adati: “Usaope; wapulumuka kwa anthu oipa.”
Verse 26 — Surah Al-Qasas 28:26
“Mmodzi wa iwo (asungwana aja) adanena: “E bambo wanga mulembeni ntchito (kuti akhale woweta ziweto m’malo mwa ife). Ndithu amene alibwino kuti mumulembe ntchito ndi yemwe ali wamphamvu wokhulupirika (zonse ziwiri mwa iyeyu zirimo)
Verse 27 — Surah Al-Qasas 28:27
“(Shuaib) adati (kwa iye): “Ine ndikufuna kukukwatitsa mmodzi mwa asungwana anga awiriwa, chiongo chake ndikundigwilira ntchito zaka zisanu ndi zitatu; ngati utakwaniritsa zaka khumi ndiye kuti nkufuna kwako. Sindikufuna kukuvutitsa (pokuchulukitsira zaka); undipeza, Allah akafuna, kuti ndine mmodzi wa anthu abwino, (wokwaniritsa lonjezo).”
Verse 28 — Surah Al-Qasas 28:28
“(Mûsa) adati: “Zimene mwandilonjezazi zili pakati pa ine ndi inu. Nyengo iriyonse imene ndikwaniritse pa ziwirizi (pogwira ntchitoyo, ndiye kuti ndakwaniritsa lonjezo lanu) musandichitire mtopola. Ndipo Allah ndiye Muyang’aniri pa zomwe tikukambazi.”
Verse 29 — Surah Al-Qasas 28:29
“Mûsa pamene adakwaniritsa nyengoyo, adanyamuka ndi banja lake (kubwerera kwao) adaona moto kumbali ya phiri. Adauza banja lake: “Dikirani ndithudi ine ndaona moto mwina mwake ndingakutengereni nkhani za kumeneko kapena chikuni cha moto kuti muothe.”
Verse 30 — Surah Al-Qasas 28:30
“Tsono pamene adaudzera, adaitanidwa kuchokera mbali ya kumanja ya chigwacho, pa malo wodalitsidwa kuchokera mu mtengo, ankati: “E iwe Mûsa! Ndithudi Ine ndi Allah Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 31 — Surah Al-Qasas 28:31
““Ndipo ponya (pansi) ndodo yakoyo.” Choncho pamene adayiona ikugwedezeka monga kuti iyo ndi njoka, adatembenuka kuthawa ndipo sadachewuke. (Adauzidwa): “E iwe Mûsa! Bwera kuno, usaope. Ndithu iwe ndiwe mmodzi wokhala ndi mtendere.”
Verse 32 — Surah Al-Qasas 28:32
“Lowetsa dzanja lako m’thumba mwako (palisani la mkanjo wako), lituluka lili loyera, popanda choipa. Ukachita mantha, fumbata dzanja lako chakukhwapa; (ukatero mantha akuchokera). Izi zidzakhala zizindikiro ziwiri zochokera kwa Mbuye wako kwa Farawo ndi nduna zake. Ndithu iwo ndianthu olakwa.”
Verse 33 — Surah Al-Qasas 28:33
“(Mûsa) adanena (moopa) “E Mbuye wanga! Ine ndidapha munthu mwa iwo, ndipo ndikuopa kuti akandipha.”
Verse 34 — Surah Al-Qasas 28:34
““Ndipo m’bale wanga (Haaruni) ndikatswiri pakuyankhula kuposa ine. Mutumizeni pamodzi ndi ine monga mnthandizi, azikandivomereza (pa zimene ndizikanena). Ndithu ine ndikuopa kuti akanditsutsa.”
Verse 35 — Surah Al-Qasas 28:35
“(Allah) adati: “Tilimbitsa dzanja lako ndi m’bale wakoyo ndipo tikupatsani kupambana, iwo sangafikitse masautso pa inu; chifukwa cha zozizwitsa zathuzo inu awiri ndi amene akutsatireni, ndinu opambana.”
Verse 36 — Surah Al-Qasas 28:36
“Pamene Mûsa adawadzera ndi zizindikiro zathu zoonekera poyera, adati: “Ichi sichina koma ndi matsenga wopeka; sitidamvepo zimenezi kumakolo athu akale.”
Verse 37 — Surah Al-Qasas 28:37
“Ndipo Mûsa adanena: “Mbuye wanga akumudziwa yemwe wadza ndi chiongoko kuchokera kwa Iye ndi yemwe adzakhala ndi mathero a pokhala pabwino. Ndithu ochita zoipa sakapambana.”
Verse 38 — Surah Al-Qasas 28:38
“Ndipo Farawo adati: “E inu nduna (zanga)! Sindidziwa kuti inu muli ndi mulungu (wina) kupatula ine. Choncho, iwe Haamana! Ndiwotchere njerwa tero undimangire chipilala kuti mwina mwake ndingamsuzumire Mulungu wa Mûsa. Ndithu ine ndikumganizira kuti ndi mmodzi wa abodza.”
Verse 39 — Surah Al-Qasas 28:39
“Ndipo iye pamodzi ndi makamu ake ankhondo adadzitukumula pa dziko popanda chilungamo ndipo ankaganiza kuti iwo sadzabwelere kwa Ife
Verse 40 — Surah Al-Qasas 28:40
“Koma tidamulanga ndi magulu ake ankhondo ndi kuwaponya m’nyanja; yang’ana, kodi adali bwanji mathero a ochita zoipa
Verse 41 — Surah Al-Qasas 28:41
“Ndipo tidawachita kukhala atsogoleri oitanira (anthu) ku Moto; ndipo tsiku la chiweruziro (Qiyâma) sadzathandizidwa
Verse 42 — Surah Al-Qasas 28:42
“Tidawatsatiziranso matembelero padziko lino lapansi. Ndipo tsiku la chimaliziro iwo adzakhala oyipitsitsa (ndi kuthamangitsidwa ku chifundo cha Allah)
Verse 43 — Surah Al-Qasas 28:43
“Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku pambuyo powononga mibadwo yoyamba kuti likhale chiphanulamaso cha anthu (kuti liwaunikire ku njira yolungama), ndi kuti likhale chiongoko ndi chifundo kuti iwo akumbukire
Verse 44 — Surah Al-Qasas 28:44
“Ndipo iwe sudali mbali ya kuzambwe (kwa phiri limenelo) pamene tidampatsa Mûsa lamulo; sudalinso mwa amene adalipo (pamalopo)
Verse 45 — Surah Al-Qasas 28:45
“Koma ife tidaumba mibadwo yambiri (pambuyo pa Mneneri Mûsa) kotero kuti zaka zidapitapo zambiri pakati pawo. Ndipo sudakhale nawo anthu a Madiyan ndi kumawawerengera Ayah (ndime) Zathu; koma Ife tidali kutuma (atumiki ndi kuwafotokozera zomwe zidachitika patsogolo ndi pambuyo pawo, monga momwe takutumira iwe ndi kukudziwitsa nkhani zakale ndi zimene zikudza pambuyo)
Verse 46 — Surah Al-Qasas 28:46
“Ndipo sudali kumbali kwa phiri pamene tidamuitana (Mneneri Mûsa). Koma (kutumidwa kwako) ndimtendere wochokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu omwe mchenjezi sadawadzere (mnthawi yaitali) iwe usadadze, kuti akumbukire
Verse 47 — Surah Al-Qasas 28:47
“(Ndipo sitikadatuma) koma kuti mavuto akawapeza ochokera (ku zoipa) zomwe atsogoza manja awo, amanena: “Mbuye wathu! Bwanji wosatitumizira Mtumiki kuti titsate mawu anu ndi kukhala mwa okhulupirira.”
Verse 48 — Surah Al-Qasas 28:48
“Koma choona pamene chidawadzera kuchokera kwa Ife, adati: “Bwanji sadapatsidwe zonga zomwe adapatsidwa Mûsa? (Monga kutembenuza ndodo kukhala njoka, ndi zina zotero).” Kodi kalelo sadazikane zomwe adapatsidwa Mûsa? Nkunena (za Taurati ndi Qur’an): “Ndimatsenga awiri amene akuthandizana.” Ndipo adati: “Ndithu ife tikuwakana onse.”
Verse 49 — Surah Al-Qasas 28:49
“Nena: “Bwerani nalo buku lochokera kwa Allah lomwe lili ndi chiongoko chabwino kuposa awiriwa (Taurati ya Mneneri Mûsa, ndi iyi Qur’an), kuti ndilitsate ngati inu mukunena zoona.”
Verse 50 — Surah Al-Qasas 28:50
“Koma ngati sadakuyankhe, dziwa kuti akutsatira zilakolako zawo. Kodi ndani wasokera kwambiri kuposa yemwe akutsatira zilakolako zake popanda chiongoko chochokera kwa Allah? Ndithu Allah saongola anthu odzichitira zoipa
Verse 51 — Surah Al-Qasas 28:51
“Ndipo ndithu tafikitsa mawu kwa iwo mochulukitsa, mwatsatanetsatane kuti iwo akumbukire
Verse 52 — Surah Al-Qasas 28:52
“Amene tidawapatsa buku kale ili lisadadze, akulikhulupirira ili (buku la Qur’an)
Verse 53 — Surah Al-Qasas 28:53
“Ndipo likawerengedwa kwa iwo, akuti: “Talikhulupirira; ndithu ichi nchoona chochokera kwa Mbuye wathu; ndithu ilo lisanadze ife tidali Asilamu (ogonjera Allah).”
Verse 54 — Surah Al-Qasas 28:54
“Iwo adzapatsidwa malipiro awo kawiri (chifukwa chotsatira Mneneri Mûsa Ndi Mneneri Isa (Yesu), kale; ndipo tsopano ndikumtsatira Mneneri Muhammad{s.a.w}) nchifukwa chakuti adapirira; amachotsa choipa (pochita) chabwino, ndipo m’zimene tawapatsa akupereka chopereka (Sadaka)
Verse 55 — Surah Al-Qasas 28:55
“Ndipo akamva zopanda pake amazipewa, ndipo amati (kwa achibwanawo): “Ife tili ndi zochita zathu inunso muli ndi zochita zanu, mtendere ukhale pa inu. Ife sitifuna (kutsutsana) ndi mbuli.”
Verse 56 — Surah Al-Qasas 28:56
“Ndithu iwe sungathe kumuongola amene ukumfuna, koma Allah amamuongola amene wamfuna. Ndipo Iye akudziwa za amene ali oongoka
Verse 57 — Surah Al-Qasas 28:57
“Ndipo akunena (akafiri a m’ Makka, kuuza Mtumiki): “Ngati titsatira chiongoko (ichi chimene wadza nacho) pamodzi ndi iwe, tifwambidwa m’dziko lathu (potimenya nkhondo mafuko ena a Arabu).” Kodi sitidawakhazike pamalo opatulika ndi pa mtendere pomwe zipatso za mitundumitundu zikudza pamenepo mwaulere (monga rizq) zochokera kwa Ife? Koma ambiri a iwo sadziwa
Verse 58 — Surah Al-Qasas 28:58
“Kodi ndimidzi ingati imene tidaiononga yomwe inkanyadira za moyo wawo (wosavutika ndi wodya bwino)! Umo m’malo mwawo simudakhalidwebe pambuyo pawo koma mochepa basi; ndipo ife tidalowa chokolo m’zimenezi
Verse 59 — Surah Al-Qasas 28:59
“Ndipo Mbuye wako sali owononga midzi pokhapokha akatuma mtumiki mu mzinda wawo waukulu ndi kuwawerengera mawu a m’ndime Zathu, (akakana ndi pamene timawaononga); ndiponso sitili owononga midzi pokhapokha anthu ake atakhala achinyengo
Verse 60 — Surah Al-Qasas 28:60
“Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa nchosangalatsa cha moyo wa pa dziko, ndiponso chokometsera chake (chomwe sichikhalira kutha); koma chomwe chili kwa Allah ndicho chabwino, chamuyaya; kodi bwanji simukuzindikira
Verse 61 — Surah Al-Qasas 28:61
“Kodi munthu yemwe tamulonjeza lonjezo labwino (kuti akalowa ku Munda wamtendere) kotero kuti iye akakumana nalo (lonjezolo), angafanane ndi yemwe tamsangalatsa ndi zosangalatsa za moyo wa pa dziko basi, kenako iye nkukhala mmodzi okaponyedwa (ku Moto) tsiku la chiweruziro (Qiyâma)
Verse 62 — Surah Al-Qasas 28:62
“Ndipo (akumbutse) tsiku limene (Allah) adzawaitana, adzati: “Ali kuti anzanga aja omwe mumanena (kuti ndianzananga)?”
Verse 63 — Surah Al-Qasas 28:63
“Adzanena amene mawu (onena za chilango) atsimikizika pa iwo: “Mbuye wathu! Awa ndiamene tidawasokeretsa; tidawasokeretsa monga momwe Tidasokelera. tikudzipatula ndi iwo kwa inu; samatilambira ife.”
Verse 64 — Surah Al-Qasas 28:64
“Ndipo kudzanenedwa: “Itanani aphatikizi anu.” Choncho adzawaitana koma sadzawayankha. Ndipo azawawona mavuto (pa nthawiyo azakhumba) akadakhala oongoka (pa dziko lapansi kotero kuti akadapeza mtendere pa tsiku la chimaliziro)
Verse 65 — Surah Al-Qasas 28:65
“Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawaitana, nkudzati: “Kodi mudawayankha chiyani Atumiki?”
Verse 66 — Surah Al-Qasas 28:66
“Basi tsiku limenelo nkhani zidzawasowa choncho iwo sadzatha kufunsana
Verse 67 — Surah Al-Qasas 28:67
“Koma amene walapa ndi kukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala mwa opambana
Verse 68 — Surah Al-Qasas 28:68
“Ndipo Mbuye wako amalenga chimene wafuna ndi kuchisankha (chimene wafuna). Iwo alibe chifuniro. Allah wapatukana ndi zonse zochepetsa ulemelero Wake, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo
Verse 69 — Surah Al-Qasas 28:69
“Ndiponso Mbuye wako akudziwa zimene zifuwa zawo zikubisa (maganizo awo) ndi zimene akuwonetsera (poyera)
Verse 70 — Surah Al-Qasas 28:70
“Ndipo Iye ndi Allah; palibe wopembedzedwa m’choonadi koma Iye. Kuyamikidwa konse (kwabwino) pachiyambi ndi kumapeto nkwake; ndipo kulamulanso nkwake, ndipo inu mudzabwerera kwa Iye
Verse 71 — Surah Al-Qasas 28:71
“Nena: “Tandiuzani ngati Allah atakupangirani usiku kuti usachoke mpaka tsiku la chiweruziro (Qiyâma), kodi ndimulungu wanji osati Allah amene angakudzetsereni kuunika? Kodi simumva?”
Verse 72 — Surah Al-Qasas 28:72
“Nena: “Tandiuzani ngati Allah ataupanga usana kuti usachoke mpaka tsiku la chiweruziro (Qiyâma), kodi ndimulungu wanji osati Allah amene angakudzetsereni usiku m’mene mumapumulamo? Kodi simuona (chifundo cha Allah)?”
Verse 73 — Surah Al-Qasas 28:73
“Ndipo mu chifundo Chake, adakupangirani usiku ndi usana kuti muzipumulamo ndi kufunafuna zabwino Zake (masana) kuti muthokoze
Verse 74 — Surah Al-Qasas 28:74
“Ndipo tsiku limene (Allah) adzawaitana, adzati: “Ali kuti anzanga aja amene mumati ndimilungu inzanga?”
Verse 75 — Surah Al-Qasas 28:75
“Ndipo mumpingo uliwonse tidzatulutsa mboni (yawo yowaikira umboni), ndipo tidzawauza: “Bwerani ndi umboni wanu.” Pamenepo adzadziwa kuti choonadi ncha Allah, ndipo zidzawasowa zimene amapeka
Verse 76 — Surah Al-Qasas 28:76
“Ndithu Qaruni adali mwa anthu a Mûsa; koma adazikweza kwa iwo, ndipo tidampatsa nkhokwe za chuma zomwe makiyi ake ngolemetsa kagulu ka anthu anyonga (kuwasenza). Anthu ake adamuuza: “Usanyade; ndithu Allah sakonda onyada.”
Verse 77 — Surah Al-Qasas 28:77
““Ndipo uyifunefune kupyolera m’zomwe Allah wakupatsa, nyumba yabwino yomaliza, usaiwale gawo lako la m’dziko; chita zabwino monga momwe Allah wakuchitira zabwino, ndipo usafune kuononga pa dziko; ndithu Allah sakonda oononga.”
Verse 78 — Surah Al-Qasas 28:78
“Adati: “Ndithu ndapatsidwa izi chifukwa cha kudziwa kwanga komwe ndili nako.” Kodi iye sadadziwe kuti Allah adawaononga anthu patsogolo pake omwe adali anyonga kwambiri kuposa iye, komanso osonkhanitsa chuma chambiri? Ndipo oipa sadzafunsidwa zolakwa zawo. (Allah akudziwa zonse za iwo)
Verse 79 — Surah Al-Qasas 28:79
“Choncho, adatulukira kwa anthu ake (monyada) uku atadzikongoletsa. Amene akufuna moyo wa pa dziko adanena (mokhumbira): “Kalanga ife! Tikadapatsidwa monga wapatsidwa Qaruna! Ndithu iye ngodala kwakukulu.”
Verse 80 — Surah Al-Qasas 28:80
“Ndipo amene adapatsidwa kuzindikira adanena: “Tsoka lanu! Malipiro a Allah ngabwino kwa yemwe wakhulupirira ndi kuchita zabwino, (kuposa izi ali nazo Qaruni); ndipo sadzapatsidwa zimenezi koma okhawo ali opirira.”
Verse 81 — Surah Al-Qasas 28:81
“Kenako tidamdidimiza m’nthaka iye ndi nyumba yake; ndipo adalibe gulu lililonse lomuthangata popikisana ndi Allah, ndipo sadali mwa odzipulumutsa okha
Verse 82 — Surah Al-Qasas 28:82
“Ndipo amene ankalakalaka ulemelero wake dzulo adayamba kunena: “E zoonadi Allah amamuonjezera chuma amene akumfuna mwa akapolo Ake (chingakhale ali oipa wosayanjidwa ndi Iye), ndipo amamuchepetsera chuma (amene wamfuna kotero ngakhale ali woyanjidwa ndi Iye.) Pakadapanda Allah kutimvera chisoni. (Mkukhumbira kwathu pa zimene adampatsa Qaruna akadatikwilira m’nthaka. Ha! Zoonadi osakhulupirira sangapambane.”)
Verse 83 — Surah Al-Qasas 28:83
“Nyumba yomalizirayo tikawapangira amene sakufuna kudzikweza pa dziko ndi kuononga. Ndipo malekezero abwino adzakhala a wanthu owopa (Allah)
Verse 84 — Surah Al-Qasas 28:84
“Amene achite chabwino, adzapeza mphoto yoposa chimene adachitacho ndipo amene achite choipa sadzalipidwa (china chake) koma zoipa zomwezo zimene adali kuzichita
Verse 85 — Surah Al-Qasas 28:85
“Ndithudi yemwe wakulamula kuitsata Qur’an, mwachoonadi adzakubwezera pa malo pobwerera. Nena! “Mbuye wanga ndi yemwe akudziwa amene wadza ndi chiongoko ndi yemwe ali m’kusokera koonekera poyera.’’
Verse 86 — Surah Al-Qasas 28:86
“Ndipo iwe sudali kulakalaka kuti ungapatsidwe buku (pamodzi ndi uneneri) koma izi zidachitika pa chifundo chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale m’thandizi wa anthu osakhulupirira (Allah)
Verse 87 — Surah Al-Qasas 28:87
“Ndipo asakutsekereze kutsatira ndime za (mawu a) Allah pa mbuyo povumbulutsidwa pa iwe, ndipo aitanire anthu kwa Mbuye wako, komatu usakhale m’gulu la anthu omphatikiza Allah ndi mafano
Verse 88 — Surah Al-Qasas 28:88
“Ndipo usapemphe mulungu wina pa modzi ndi Allah. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye Yekha. Chinthu chilichonse chidzaonongeka kupatula Nkhope Yake. Ulamuliro (wazinthu zonse) uli kwa Iye ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera nonsenu