Back to Languages

Chichewa - Chapter 29 - Al-Ankabut

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Ankabut 29:1

Verse 2 — Surah Al-Ankabut 29:2

“Kodi anthu akuganiza kuti adzasiyidwa popanda kuyesedwa ndi masautso pakungonena kuti: “Takhulupirira?” (Iyayi, ayenera kuyesedwa ndithu ndi masautso osiyanasiyana pa matupi pawo ndi pachuma chawo kuti adziwike woona ndi wachiphamaso)

Verse 3 — Surah Al-Ankabut 29:3

“Ndipo ndithu tidawayesa amene adalipo patsogolo pawo. Ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zoona, ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zabodza

Verse 4 — Surah Al-Ankabut 29:4

“Kodi amene akuchita zoipa akuganiza kuti atipambana (kotero kuti sitingawalange)? Ndichiweruzo choipa chimene akuweruzacho

Verse 5 — Surah Al-Ankabut 29:5

“Amene akuyembekezera kukumana ndi Allah, (agwire ntchito yabwino pamoyo wake kuti akakumane Naye ndi zabwino), pakuti ndithu nthawi ya Allah (tsiku la chimaliziro) ikudza (popanda chikaiko). Ndipo Iye Ngwakumva (zonena za akapolo Ake), Ngodziwa (zachinsinsi chawo)

Verse 6 — Surah Al-Ankabut 29:6

“Ndipo amene akuchita khama (polimbana ndi Akafiri, kapena pogonjetsa mtima wake kuti utsatire malamulo a Allah), ndithu zabwino za khamalo zili pa iye mwini. Ndithu Allah siwosaukira chilichonse kwa zolengedwa Zake

Verse 7 — Surah Al-Ankabut 29:7

“Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, Tidzawafafanizira zoipa zawo, ndipo tidzawalipira zabwino kuposa zomwe amachita

Verse 8 — Surah Al-Ankabut 29:8

“Ndipo tamulamula munthu kuchitira zabwino makolo ake. Koma ngati atakukakamiza (makolo ako) kuti undiphatikize Ine ndi (zinthu zina) zomwe iwe sukuzidziwa, usawamvere. Kwa Ine ndiko kobwerera kwanu, ndipo ndidzakuuzani zimene mumachita

Verse 9 — Surah Al-Ankabut 29:9

“Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, tidzawalowetsa m’gulu la anthu abwino

Verse 10 — Surah Al-Ankabut 29:10

“Ndipo alipo ena mwa anthu omwe akunena: “Takhulupirira mwa Allah.” Koma akavutitsidwa chifukwa cha Allah, amawachita masautso a anthu monga chilango cha Allah, (sapirira; iwowa ndi achinyengo (achiphamaso). Ndipo chikadza chipulumutso chochokera kwa Mbuye wako amanena: “Ndithu ife tidali pamodzi ndi inu.” (Koma chikhalirecho akunena zonama). Kodi Allah sadziwa zomwe zili m’zifuwa za zolengedwa

Verse 11 — Surah Al-Ankabut 29:11

“Ndipo ndithu Allah awaonetsera poyera amene akhulupirira (moona), ndiponso awaonetsera poyera achiphamaso (achinyengo)

Verse 12 — Surah Al-Ankabut 29:12

“Ndipo amene sadakhulupirire adanena kwa okhulupirira: “Tsatani njira yathu; (musatsate njira ya Muhammad). Ife tidzakusenzerani machimo anu (kuti chilichonse chisakupezeni). Koma sadzasenza chilichonse cha machimo awo, ndithu iwo ngabodza

Verse 13 — Surah Al-Ankabut 29:13

“Ndipo ndithudi, adzasenza mitolo ya machimo ndi mitolo yina yamachimo (ya omwe adawasokeretsa) poiphatikiza ku mitolo yawo ya machimo. (Nawonso osokezedwa, adzasenzanso mitolo ya machimo chifukwa cha kutsatira kwawo anthu owasokezawo). Ndipo pa tsiku la Qiyâma (chimaliziro,) ndithu adzafunsidwa pa zimene amapeka

Verse 14 — Surah Al-Ankabut 29:14

“Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake ndipo adakhala nawo zaka chikwi chimodzi kupatulapo zaka makumi asanu. (Koma m’nthawi yonseyi sadatsatire ulaliki wake). Choncho chigumula chidawapeza (ndipo adamira onse), uku ali odzichitira zoipa

Verse 15 — Surah Al-Ankabut 29:15

“Tidampulumutsa iye (ndi anthu ake) a m’chombo; ndipo tidachita ichi kuti likhale phunziro kwa zolengedwa

Verse 16 — Surah Al-Ankabut 29:16

“Ndipo (akumbutse nkhani ya) Ibrahim pamene adawauza anthu ake: “Mpembedzeni Allah ndi kumuopa. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati mukudziwa (kusiyana kwa chabwino ndi choipa).”

Verse 17 — Surah Al-Ankabut 29:17

“Ndithu inu mukupembedza mafano kusiya (kupembedza) Allah ndipo mwadzipangira chonama. Ndithu amene mukuwapembedzawo kusiya Allah, sangakupatseni rizq (madalitso) choncho funani rizq (madalitso) kwa Allah, ndipo mpembedzeni Iye Yekha ndi kumthokoza. Kwa Iye ndikomwe mudzabwerera (tsiku la chimaliziro)

Verse 18 — Surah Al-Ankabut 29:18

“Ndipo ngati mutsutsa, ndithu mibadwo ya omwe adalipo patsogolo panu idatsutsanso. Ndipo kwa Mtumiki kulibe udindo wina koma kufikitsa uthenga woonekera poyera, (womveka bwino)

Verse 19 — Surah Al-Ankabut 29:19

“Kodi saona momwe Allah ayambitsira zolengedwa, kenako nkuzibwerezanso? Ndithu kwa Allah zimenezo nzosavuta

Verse 20 — Surah Al-Ankabut 29:20

“Nena: “Yendani pa dziko ndi kuona momwe Allah adayambitsira chilengedwe; kenako Allah adzaumba, kuumba kwina. Ndithu Allah Ndiwokhoza chilichonse.”

Verse 21 — Surah Al-Ankabut 29:21

““Amamlanga yemwe wamfuna ndipo amamchitira chifundo amene wamfuna, ndipo kwa Iye nonse mudzabwezedwa.”

Verse 22 — Surah Al-Ankabut 29:22

““Ndipo inu simungampambane (Allah) pa dziko ngakhale kumwamba (pomuzemba kuti asakulangeni). Inu mulibe mtetezi kapena mpulumutsi kupatula Allah.”

Verse 23 — Surah Al-Ankabut 29:23

“Ndipo amene akana Ayah (ndime) za Allah ndi kukumana Naye amenewo ndiwo ataya mtima pa zakupeza chifundo Changa, ndipo iwowo ndiwo adzapeza chilango chowawa

Verse 24 — Surah Al-Ankabut 29:24

“Choncho yankho la anthu ake silidali lina koma adangoti: “Mupheni kapena mtentheni ndi moto.” Koma Allah adampulumutsa ku moto. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu okhulupirira

Verse 25 — Surah Al-Ankabut 29:25

“Ndipo adanena: “Ndithu inu mwasankha mafano kukhala milungu kusiya Allah, ndipo mukukondana pakati panu m’moyo wa pa dziko; (pokhalirana pamodzi ndi kupitiriza kupembedza mafanowo mwachimvano). Koma tsiku la Qiyâma, mudzakanana wina ndi mnzake, komanso mudzatembelerana wina ndi mnzake, malo anu adzakhala ku Moto, ndipo simudzapeza okupulumutsani.”

Verse 26 — Surah Al-Ankabut 29:26

“Choncho (Mneneri) Luti adamkhulupirira iye. Ndipo (Mneneri Ibrahim) adanena: “Ndithu ine ndikusamukira kwa Mbuye wanga (ku dziko lomwe wandilamulira). Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.”

Verse 27 — Surah Al-Ankabut 29:27

“Ndipo tidampatsa (Mneneri Ibrahim) Ishâq ndi Ya’qub, ndipo tidaika uneneri ndi buku pa mbumba yake, ndipo tidampatsa malipiro ake pa dziko lapansi; ndithu iye pa tsiku la chimaliziro adzakhala mwa anthu abwino

Verse 28 — Surah Al-Ankabut 29:28

“Ndipo (akumbutse nkhani ya Mneneri) Luti pamene adawauza anthu ake: “Ndithu inu mukuchita zadama; palibe amene adakutsogolerani kuzichita (zadamazo) mwa zolengedwa.”

Verse 29 — Surah Al-Ankabut 29:29

““Kodi inu mukuchita amuna anzanu ukwati ndi kutseka njira (pakuchita chifwamba) ndi kuchita zoipa m’mabwalo anu osonkhanirana?” Koma yankho la anthu ake silidali lina koma kunena kuti: “Tidzere ndi chilango cha Allah cho ngati uli mmodzi wa owona.”

Verse 30 — Surah Al-Ankabut 29:30

“Iye adati: “Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu oononga.”

Verse 31 — Surah Al-Ankabut 29:31

“Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Ibrahim ndi nkhani yabwino (yoti abereka Mneneri Ishaq), adanenanso: “Ndithu tiwaononga eni mudzi uwu (wa Sodom); ndithu iwowo ngochimwa.”

Verse 32 — Surah Al-Ankabut 29:32

“(Mneneri Ibrahim) adati: “Koma mmenemo muli Luti.” Iwo adati: “Ife ndife odziwa kwambiri za omwe ali m’menemo; ndithu timpulumutsa iye ndi banja lake kupatula mkazi wake; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”

Verse 33 — Surah Al-Ankabut 29:33

“Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Luti, adawadandaulira ndi kuwadera nkhawa; (ndipo iwo) adati: “Usaope ndipo usadandaule. Ndithu ife tikupulumutsa ndi banja lako kupatula mkazi wako; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”

Verse 34 — Surah Al-Ankabut 29:34

““Ndithu ife tiwatsitsira chilango choipa kuchokera kumwamba eni mudzi uwu chifukwa cha kuchimwa kwawo (ndi kuukira malamulo a Allah).”

Verse 35 — Surah Al-Ankabut 29:35

“Ndipo ndithu tidasiya chizindikiro mmenemo choonekera kwa anthu anzeru

Verse 36 — Surah Al-Ankabut 29:36

“Ndipo ku Madiyan (tidatumako) m’bale wawo Shuaib, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah ndipo opani tsiku lachimaliziro musanke mu ononga pa dziko.”

Verse 37 — Surah Al-Ankabut 29:37

“Koma adamutsutsa. Ndipo kugwedezeka kwa nthaka kudawachotsa moyo wawo, ndipo kudawachera ali gwadegwade m’nyumba zawo (atafa)

Verse 38 — Surah Al-Ankabut 29:38

“Nawonso Âdi ndi Asamudu (tidawaononga). Ndipo mokhala mwawo mukudziwika kwa inu. Ndipo satana adawakometsera zochita zawo (zoipa), ndipo adawatsekereza ku njira (zabwino) chikhalirecho adali openya (anzeru zawo)

Verse 39 — Surah Al-Ankabut 29:39

“Momwemonso Kaaruni, Farawo ndi Hamana (adaonongedwa). Ndithu adawadzera Mûsa ndi zozizwitsa (zooneka), koma adadzikweza pa dziko. Komatu sadathe kumpambana (Allah pomulepheretsa kuwalanga)

Verse 40 — Surah Al-Ankabut 29:40

“Choncho aliyense wa iwo tidamlanga ndi machimo ake. Ena a iwo tidawatumizira chimphepo chamiyala; ena a iwo udawaononga mkuwe; ena a iwo tidawadidimiza m’nthaka, ndipo ena a iwo tidawamiza (m’madzi). Si Allah amene adawachitira zoipa, koma adadzichitira okha zoipa

Verse 41 — Surah Al-Ankabut 29:41

“Fanizo la amene adzipangira milungu yabodza kusiya Allah, lili ngati fanizo la kangaude (yemwe) wadzipangira nyumba (kuti imsunge, pomwe nyumbayo siingathe kumsunga m’nyengo yozizira kapena yotentha), ndithu nyumba yomwe ili yofooka kwambiri ndi nyumba ya kangaude, akadakhala akudziwa

Verse 42 — Surah Al-Ankabut 29:42

“Ndithu Allah akudziwa kupembedza kwawo zinthu zina kusiya Iye, Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

Verse 43 — Surah Al-Ankabut 29:43

“Ndipo amenewa ndimafanizo (omwe) tikuwaponyera anthu. Sangawazindikire kupatula odziwa

Verse 44 — Surah Al-Ankabut 29:44

“Allah adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi; ndithu; m’menemo muli zizindikiro kwa okhulupirira

Verse 45 — Surah Al-Ankabut 29:45

“Werenga zimene zavumbulutsidwa kwa iwe (za) m’buku, ndipo pemphera Swala moyenera; ndithu Swala (ikapempheredwa moyenera) imamtchinjiriza (woipempherayo) ku zinthu zauve ndi zoipa. Ndipo kukumbukira Allah, ndi chinthu chachikulu. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita

Verse 46 — Surah Al-Ankabut 29:46

“۞ Ndipo musatsutsane ndi anthu a buku koma kutsutsana kwabwino kupatula amene achita zoipa mwa iwo. Ndipo nenani: “Takhulupirira zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa inu, ndipo Mulungu wathu ndi Mulungu wanu ndi Mmodzi; ndipo ife ndife ogonjera Iye.”

Verse 47 — Surah Al-Ankabut 29:47

“Ndipo umo ndimomwe takuvumbulutsira buku (ili la Qur’an). Choncho amene tidawapatsa buku, (ili lisadadze, monga Taurat ndi Injili), akulikhulupirira; akulikhulupiriranso ena mwa awa (Arabu omwe sitidawapatse buku). Ndipo sangawakane ma Ayah Athu kupatula osakhulupirira

Verse 48 — Surah Al-Ankabut 29:48

“Ndipo iwe sumawerenga buku lililonse, ili lisanadze; ndipo sudalilembe ndi dzanja lako lakumanja. Zikadatero ndiye kuti anthu achabe akadakaikira

Verse 49 — Surah Al-Ankabut 29:49

“Koma izi ndi Ayah zoonekera poyera zomwe zili m’zifuwa za amene apatsidwa nzeru. Ndipo sangazikane Ayah (ndime) zathu koma achinyengo

Verse 50 — Surah Al-Ankabut 29:50

“Ndipo akunena: “Kodi bwanji sizinatsitsidwe kwa iye zozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah; ndipo ine ndine mchenjezi woonekera, (ndilibe mphamvu zokudzetserani zozizwitsa koma pokhapo Allah atafuna).”

Verse 51 — Surah Al-Ankabut 29:51

“Kodi sizidawakwanire kuti takuvumbulutsira buku (ili) lomwe likuwerengedwa kwa iwo? Ndithu mmenemo muli chifundo ndi phunziro kwa anthu okhulupirira

Verse 52 — Surah Al-Ankabut 29:52

“Nena: “Allah akukwana kukhala mboni pakati panga ndi inu; akudziwa za kumwamba ndi zapansi ndipo amene akukhulupirira zachabe ndi kukana Allah, iwowo ndiwo otayika.”

Verse 53 — Surah Al-Ankabut 29:53

“Ndipo akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; kukadapanda kuti kudaikidwa nthawi yodziwika, chilango chikadawadzera. Ndipo ndithu chidzawadzera mwadzidzidzi asakudziwa

Verse 54 — Surah Al-Ankabut 29:54

“Akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; ndithu Jahannam idzawazinga osakhuiupirira

Verse 55 — Surah Al-Ankabut 29:55

“Tsiku limene chidzawavindikira chilango kuchokera pamwamba pawo ndi pansi pa miyendo yawo; ndipo adzanena: “Lawani (chilango cha) zomwe munkachita.”

Verse 56 — Surah Al-Ankabut 29:56

“E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Ndithu nthaka Yanga njophanuka; (mukhoza kupita dziko lina ngati m’dziko lanulo simukupeza mwayi wopembedza Allah mokwanira); ndipo Ine ndekha ndipembedzeni

Verse 57 — Surah Al-Ankabut 29:57

“Chamoyo chilichonse chidzalawa imfa. Kenako mudzabwezedwa kwa Ife

Verse 58 — Surah Al-Ankabut 29:58

“Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndithudi tidzawakhazika m’zipinda za ku Munda wamtendere, momwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Taonani kukhala bwino malipiro a ochita zabwino

Verse 59 — Surah Al-Ankabut 29:59

“Amene adapirira ndipo kwa Mbuye wawo amatsamira

Verse 60 — Surah Al-Ankabut 29:60

“Ndinyama zingati zomwe sizidzipezera rizq lake. Allah akuzipatsa izo pamodzi ndi inunso. Ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa

Verse 61 — Surah Al-Ankabut 29:61

“Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndi kugonjetsa dzuwa ndi mwezi?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nanga akutembenuzidwira kuti

Verse 62 — Surah Al-Ankabut 29:62

“Allah amamtambasulira rizq amene wamfuna mwa akapolo Ake, ndi kumchepetsera (amene wamfunanso). Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri za chilichonse

Verse 63 — Surah Al-Ankabut 29:63

“Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani amene akutsitsa madzi kuchokera ku mitambo ndi kuiukitsa nthaka ndi madziwo pambuyo pakufa kwake?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sazindikira

Verse 64 — Surah Al-Ankabut 29:64

“Ndipo moyo uwu wa pa dziko lapansi suli kanthu, koma chibwana ndi masewera. Ndipo ndithu nyumba ya tsiku la chimaliziro, ndiwo moyo weniweni, akadakhala akudziwa

Verse 65 — Surah Al-Ankabut 29:65

“Ndipo akakwera m’chombo (ndi kukumana ndi zoopsa), amampempha Allah modzipereka ndikumuyeretsera pempho. Koma akawapulumutsa ndi kuwafikitsa ku ntunda, iwo amayambanso kumuphatikiza ndi mafano

Verse 66 — Surah Al-Ankabut 29:66

“Posathokoza zimene tawapatsa. Aleke asangalale (ndi zoipa zawozo); posachedwa adzadziwa

Verse 67 — Surah Al-Ankabut 29:67

“Kodi saona kuti dziko lawo (mzinda wa Makka) talichita kukhala lopatulika, lamtendere pomwe anthu ena akutsompholedwa m’mphepete mwawo? Kodi akukhulupirira zachabe ndi kuukana mtendere wa Allah

Verse 68 — Surah Al-Ankabut 29:68

“Kodi wachinyengo wamkulu ndani woposa amene akupekera bodza Allah, kapena kutsutsa choona chikamdzera? Kodi si mu Jahannam momwe mudzakhala malo a osakhulupirira

Verse 69 — Surah Al-Ankabut 29:69

“Ndipo amene akulimbikira m’njira yathu, (polimbana ndi satana, ndi mzimu woipa ndi zilakolako zoipa zam’thupi, ndi cholinga chofuna kukondweretsa Allah) ndithu tiwaongolera ku njira Zathu. Ndipo ndithu Allah ali pamodzi ndi ochita zabwino