Back to Languages

Chichewa - Chapter 3 - Al-Imran

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Imran 3:1

Verse 2 — Surah Al-Imran 3:2

“Allah (ndimmodzi), palibe winanso wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye Yekha, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi kuteteza chilichonse

Verse 3 — Surah Al-Imran 3:3

“Wakuvumbulutsira buku mwachoonadi, lomwe likutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake. Ndipo adavumbulutsa Taurat ndi Injil

Verse 4 — Surah Al-Imran 3:4

“Kale, kuti (mabukuwo) akhale chotsogolera anthu. Ndipo adavumbulutsa (Qur’an) yolekanitsa pakati pa choonadi ndi chonama * Ndithudi, aja amene sadakhulupirire zizindikiro za Allah, adzakhala ndi chilango chaukali. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wobwezera (chilango mwaukali)

Verse 5 — Surah Al-Imran 3:5

“Ndithudi, kwa Allah sikungabisike chilichonse cha pansi ngakhale cha kumwamba

Verse 6 — Surah Al-Imran 3:6

“Iye ndi Yemwe amakulinganizani muli m’mimba mmaonekedwe anu mmene akufunira. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye; Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

Verse 7 — Surah Al-Imran 3:7

“Iye ndi Yemwe wakuvumbulutsira buku (ili la Qur’an), lomwe mkati mwake muli ndime zomveka zomwe ndimaziko a bukuli. Ndipo zilipo zina zokuluwika. Koma amene m’mitima mwawo muli kusokera, akutsata zomwe zili zokuluwika ndi cholinga chofuna kusokoneza anthu, ndi kufuna kudziwa tanthauzo lake lenileni. Palibe amene akudziwa tanthauzo lake lenileni koma Allah basi. Koma amene azama pa maphunziro, amanena: “Tawakhulupirira (ma Ayah amenewa). Onse ngochokera kwa Mbuye wathu.” Ndipo palibe angakumbukire koma eni nzeru basi

Verse 8 — Surah Al-Imran 3:8

“(Anzeruwo amanena): “ E Mbuye wathu! Musaikhotetse mitima yathu pambuyo potiongola. Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu. Ndithudi, Inu Ndinu wopatsa kwambiri

Verse 9 — Surah Al-Imran 3:9

“E Mbuye wathu! Inu ndinu Wosonkhanitsa anthu patsiku lopanda chikaiko, ndithudi, Allah saswa lonjezo

Verse 10 — Surah Al-Imran 3:10

“Ndithu amene sadakhulupirire, chuma chawo sichidzawathandiza chilichonse ngakhalenso ana awo, ku chilango cha Allah. Ndipo iwo ndi nkhuni za ku Moto

Verse 11 — Surah Al-Imran 3:11

“(Khalidwe la awa osakhulupiira, amumbadwo wako iwe mneneri Muhammad {s.a.w}, liri) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi amene adalipo pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa zisonyezo Zathu. Choncho, Allah adawakhaulitsa chifukwa cha machimo awo. Ndipo Allah Ngolanga mwaukali

Verse 12 — Surah Al-Imran 3:12

“Auze amene sadakhulupirire: “Posachedwapa mugonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa ndi kuponyedwa ku Moto. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!”

Verse 13 — Surah Al-Imran 3:13

““Ndithudi, padapezeka chisonyezo chachikulu kwa inu m’magulu awiri omwe adakumana (tsiku la nkhondo ya Badri), pomwe gulu limodzi limamenya (nkhondo) pa njira ya Allah, pamene linalo lokanira, (ndipo gululo) linkawaona (Asilamu) kukhala ochuluka kawiri kuposa ilo, poona ndi maso awo. Ndipo Allah amamlimbikitsira mphamvu ndi chipulumutso chake amene wamfuna. Ndithudi, m’zimenezo muli malingaliro (akulu) kwa eni kupenyetsetsa mwanzeru.”

Verse 14 — Surah Al-Imran 3:14

“Kwakometsedwa kwa anthu kukonda zilakolako (za moyo wawo) monga akazi, ana, milumilu ya chuma cha golide ndi siliva, ndi mahachi oyang’aniridwa bwino, ziweto ndi mbewu. Izo ndi zosangalatsa za moyo wa dziko lapansi (zomwe sizili kanthu). Koma kwa Allah ndiko kuli mabwelero abwino

Verse 15 — Surah Al-Imran 3:15

“Nena: “Kodi ndikuuzeni zomwe zili zabwino kuposa zimenezo? Kwa omwe ali olungama, akapeza kwa Mbuye wawo Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda; adzakhala mmenemo nthawi yaitali ndikulandira akazi oyeretsedwa ndi chiyanjo chochokera kwa Allah. Ndipo Allah akuona akapolo ake onse

Verse 16 — Surah Al-Imran 3:16

“Omwe akunena: “Mbuye wathu! Ndithudi, ife takhulupirira. Choncho tikhululukireni machimo athu ndi kutipewetsa ku chilango cha Moto.”

Verse 17 — Surah Al-Imran 3:17

“Opirira, onena zoona, omvera, opereka chaulere ndi opempha chikhululuko nthawi yam‘bandakucha

Verse 18 — Surah Al-Imran 3:18

“Allah (Mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) angelo ndi eni nzeru (kuti Iye) Ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

Verse 19 — Surah Al-Imran 3:19

“Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Allah ndi Chisilamu. Ndipo amene adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) sadatsutsane koma pambuyo powabwerera kuzindikira. (Adatsutsana) chifukwa cha dumbo lomwe lidali pakati pawo. Ndipo amene akukana zisonyezo za Allah, (Allah akamulanga pa tsiku la chiweruziro). Ndithu Allah Ngwachangu powerengera

Verse 20 — Surah Al-Imran 3:20

“Ngati (osakhulupirira) atsutsana nawe, nena: “Ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Allah (ndadzipereka kwa Iye) pamodzi ndi amene anditsata.” Ndipo nena kwa onse adapatsidwa buku (Ayuda Ndi Akhrisitu) ndi osadziwa kulemba ndi kuwerenga (Arabu): “Kodi mwagonjera (kwa Allah)?” Ngati agonjera ndiye kuti aongoka. Koma ngati atembenukira kumbali, udindo wako ndikufikitsa uthenga basi. Ndipo Allah akuona akapolo Ake onse

Verse 21 — Surah Al-Imran 3:21

“Ndithudi, amene akutsutsa zizindikiro za Allah ndi kupha aneneri popanda choonadi, ndikuphanso anthu omwe akulamula (kuchita) zolungama, auze nkhani ya chilango chopweteka

Verse 22 — Surah Al-Imran 3:22

“Iwowo ndi omwe zochita zawo zaonongeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Ndipo iwo sadzapeza athandizi

Verse 23 — Surah Al-Imran 3:23

“Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la buku (la Allah)? Akuitanidwa ku buku la Allah kuti liwaweruze pakati pawo; kenako gulu lina la iwo likutembenukira kumbali iwo ali onyoza

Verse 24 — Surah Al-Imran 3:24

“Zimenezo (kusalabadira malamulo a Allah) nchifukwa chakuti amanena: “Sudzatikhudza Moto koma masiku ochepa basi.” Ndipo zawanyenga pa chipembedzo chawo zomwe adali kupeka (kuti adzakhululukidwa kapena kulangidwa masiku ochepa okha)

Verse 25 — Surah Al-Imran 3:25

“Kodi zidzakhala zotani pamene tidzawasonkhanitsa tsiku lopanda chikaiko? Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa mokwanira pa zomwe udachita. Ndipo iwo sadzaponderezedwa

Verse 26 — Surah Al-Imran 3:26

“Nena “E Mbuye wanga! Mwini ufumu wonse. Mumapereka ufumu kwa yemwe mwamfuna. Ndipo mumachotsa ufumu kwa yemwe mwamfuna. Mumapereka ulemelero kwa yemwe mwamfuna, ndipo mumamsambula yemwenso mwamfuna. Ubwino wonse uli m’manja Mwanu. Ndithudi, Inu ndinu Wokhonza chilichonse.”

Verse 27 — Surah Al-Imran 3:27

“(Inu) mumalowetsa usiku mu usana (ndikukhala usana wautali monga m’nyengo yotentha). Ndipo mumalowetsa usana mu usiku (nkukhala usiku wautali monga m’nyengo yachisanu). Mumatulutsa cha moyo m’chakufa; ndipo mumatulutsa chakufa m’chamoyo. Ndipo mumapatsa rizq (chakudya) amene mwamfuna mopanda chiwerengero.”

Verse 28 — Surah Al-Imran 3:28

“Asilamu asapale ubwenzi osakhulupirira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Allah, kupatula (kupalana nawo ubwenzi mwachiphamaso) chifukwa cha kudzitchinjiriza kwa iwo. Ndipo Allah Iye Mwini akukuchenjezani (za chilango Chake). Ndipo kobwerera ndi kwa Allah (basi)

Verse 29 — Surah Al-Imran 3:29

“Nena: “Ngati mubisa zomwe zili m’zifuwa zanu, kapena kuzionetsa (poyera), Allah akuzidziwa. Iye akudziwa zonse zakumwamba ndi zapansi. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.”

Verse 30 — Surah Al-Imran 3:30

“Tsiku lomwe mzimu uliwonse udzapeza zabwino zomwe udachita zitabweretsedwa, ndiponso zoipa zomwe udachita; udzalakalaka kuti pakadakhala ntunda wautali pakati pa machimo ake ndi iye. Ndipo Allah Mwini akukuchenjezani za chilango Chake. Ndipo Allah Ngoleza kwa akapolo Ake

Verse 31 — Surah Al-Imran 3:31

“Nena: (Iwe Mtumiki) “Ngati inu mukumkonda Allah, tsatani ine; Allah akukondani ndikukukhululukirani machimo anu. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.”

Verse 32 — Surah Al-Imran 3:32

“Nena: “Mvereni Allah ndi Mtumiki (wake).” Koma ngati akana, (Allah awakhaulitsa). Ndithudi, Allah sakonda anthu osakhulupirira

Verse 33 — Surah Al-Imran 3:33

“Ndithudi Allah adasankha Adam ndi Nuh ndi banja la Ibrahim ndi banja la Imran pa zolengedwa zonse

Verse 34 — Surah Al-Imran 3:34

“Ana ena kuchokera mwa ena pakati pawo. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa

Verse 35 — Surah Al-Imran 3:35

“(Kumbukirani) pamene adanena mkazi wa Imran (mayi wa Mariya), m’mapemphero ake): “Mbuye wanga! Ndapereka kwa Inu chimene chili m’mimba mwanga monga “waqf” (wotumikira m’kachisi Wanu). Tero landirani ichi kwa ine. Ndithudi, Inu ndinu Akumva, Wodziwa.”

Verse 36 — Surah Al-Imran 3:36

“Choncho pamene adam’bala adati: “Mbuye wanga! Ndabala wamkazi!” Ndipo Allah akudziwa kwambiri chimene wabereka - “Ndipo wamwamuna (yemwe ndimayembekezera kubala) sali ngati wamkazi (amene ndamubala. Sangathe kutumikira moyenera mkachisi Wanu). Ndipo ine ndamutcha Mariya (wotumikira Allah). Ndipo ndikupempha Chitetezo Chanu pa iye ndi ana ake kwa satana wothamangitsidwayo.”

Verse 37 — Surah Al-Imran 3:37

“Choncho Mbuye wake adamulandira, kulandira kwabwino; namkulitsa, kukulitsa kwabwino. Adampatsa Zakariya kuti amulere. Nthawi iliyonse Zakariya akamulowera mchipinda mwake (mwa Mariya) m’kachisimo, amampeza ali ndi chakudya. Amati: “Iwe Mariya! Ukuzipeza kuti izi?” (Iye) amati: “Izi zikuchokera kwa Allah. Ndipo Allah amampatsa yemwe wamfuna popanda chiyembekezo (mwini wakeyo).”

Verse 38 — Surah Al-Imran 3:38

“Pompo Zakariya adapempha Mbuye wake nati: “Mbuye wanga! Ndipatseni kuchokera kwa Inu mwana wabwino. Ndithudi, Inu ndinu Akumva pempho!”

Verse 39 — Surah Al-Imran 3:39

“Mwadzidzidzi, mngelo adamuitana uku iye ataimilira akupemphera mchipinda cha m’kachisi: “Allah akukuuza nkhani yabwino (yakuti ubereka mwana; dzina lake) Yahya yemwe adzakhala wotsimikizira (mneneri yemwe adzabadwa) ndi liwu lochokera kwa Allah, (yemwe ndi mneneri Isa (Yesu) amene adzakhalanso wolemekezeka ndi wolungama ndi mneneri wa mwa anthu abwino.”

Verse 40 — Surah Al-Imran 3:40

“(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndidzakhala bwanji ndi mwana pomwe ukalamba wandifikira, nayenso mkazi wanga ndichumba.” (Mngelo adati): “Ndimomwemo; Allah amachita chimene wafuna.”

Verse 41 — Surah Al-Imran 3:41

“(Iye) adati: “Mbuye wanga! Ndipatseni chizindikiro!” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu koma momangolozera (ndi chala) basi. Ndipo tamanda Mbuye wako, kutamanda kwambiri ndiponso umlemekeze (popemphera) madzulo ndi m’mawa.”

Verse 42 — Surah Al-Imran 3:42

“Ndipo (kumbukira) pamene angelo adati: “E Iwe Mariya! Ndithudi, Allah wakusankha, wakuyeretsa ndipo wakulemekeza, mwa akazi onse amitundu ya anthu.”

Verse 43 — Surah Al-Imran 3:43

““E iwe Mariya, dzichepetse kwa Mbuye wako ndi kumlambira powerama pamodzi ndi owerama.”

Verse 44 — Surah Al-Imran 3:44

“Izi ndizina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuvumbulutsira. Sudali nawo pamene amaponya zolembera zawo (m’madzi m’njira ya mayere) kuti aone ndani mwa iwo alere Mariya. Komanso sudali nawo pamene adali kutsutsana

Verse 45 — Surah Al-Imran 3:45

“(Kumbukira) pamene angelo adati: “E iwe Mariya! Ndithu Allah akukuuza nkhani yabwino (kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu) liwu lochokera kwa Iye (Allah, lakuti: “Bereka,” ndipo nkubereka popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa oyandikitsidwa kwa Allah

Verse 46 — Surah Al-Imran 3:46

“Iye adzayankhula ndi anthu ali mchikuta ndi kuukulu (wake). Ndipo adzakhala mmodzi wa anthu abwino.”

Verse 47 — Surah Al-Imran 3:47

“(Mariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingakhale ndi mwana bwanji pomwe sadandikhudze munthu aliyense (wamwamuna)?” (Mngelo) adati: “Ndi momwemo. Allah amalenga chimene wafuna. Akafuna chinthu amanena kwa icho: ‘Chitika,’ ndipo chimachitikadi.”

Verse 48 — Surah Al-Imran 3:48

““Ndipo Allah adzamphunzitsa kulemba, nzeru, Taurat ndi Injili.”

Verse 49 — Surah Al-Imran 3:49

““Ndipo (adzamchita kukhala) mneneri kwa ana a Israyeli (adzakhala akuwauza kuti): “Ine ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu kuti ndikuumbireni dongo ngati chithunzi chambalame, nkuuzira m’menemo nkukhaladi mbalame mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndichiritsa osapenya chibadwire, ndiwamaangamaanga (chinawa), ndi kuukitsa akufa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndikuuzani zomwe mudye ndi zimene musunge m’nyumba zanu. Ndithudi, m’zimenezi muli zizindikiro kwa inu ngati mulidi okhulupirira.”

Verse 50 — Surah Al-Imran 3:50

““Ndipo (ndikhala) wotsimikizira zomwe zidalipo patsogolo panga (rn’buku la) Taurat. Ndipo ndadza kuti ndikulolezeni zina mwa zomwe zidaletsedwa kwa inu. Ndipo ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu (zotsimikizira uthenga wanga). Choncho, opani Allah ndi kundimvera (ine).”

Verse 51 — Surah Al-Imran 3:51

““Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu; choncho mupembedzeni. Iyi ndiyo njira yoongoka.”

Verse 52 — Surah Al-Imran 3:52

“Koma pamene Isa (Yesu) adazindikira mwa iwo kusakhulupirira adati: “Ndani akhale athandizi anga kwa Allah (popitiriza kufalitsa Chipembedzo Chake)?” Ophunzira ake adati: “Ife ndife athandizi a Allah (pofalitsa Chipembedzo Chake). Takhulupirira Allah; ndipo ikira umboni kuti ife ndithu ndi odzipereka kwa Allah (Asilamu).”

Verse 53 — Surah Al-Imran 3:53

““Mbuye wathu! Tazikhulupirira zimene mwavumbulutsa, ndipo tamtsata Mtumikiyo. Choncho tilembeni pamodzi ndi oikira umboniwo.”

Verse 54 — Surah Al-Imran 3:54

“Ndipo (Ayuda) adakonza chiwembu (chofuna kupha Isa (Yesu), koma Allah adachiwononga chiwembu chawocho. Allah Ngokhoza bwino zedi poononga ziwembu za anthu a chiwembu

Verse 55 — Surah Al-Imran 3:55

“(Kumbukirani) pamene Allah adati: “Iwe Isa (Yesu)! Ine ndikukwaniritsira nyengo yako yokhala ndi moyo (Ayuda sachita kanthu kwa iwe). Ndipo ndikunyamulira kwa Ine ndiponso ndikuyeretsa kwa anthu osakhulupirira (omwe ndi adani ako). Ndipo amene akutsata (iwe) ndiwasankha kukhala apamwamba pa amene sadakhulupirire kufikira tsiku lachimaliziro. Kenako kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo ndidzaweruza pakati panu pa zomwe mudali kusiyana

Verse 56 — Surah Al-Imran 3:56

“Tsono amene sadakhulupirire, ndiwakhaulitsa ndi chilango chaukali pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro, ndipo sadzapeza athandizi

Verse 57 — Surah Al-Imran 3:57

“Koma amene akhulupirira nachita zabwino, (Allah) adzawalipira malipiro awo (mokwanira). Ndipo Allah sakonda anthu ochita zoipa

Verse 58 — Surah Al-Imran 3:58

“Izi tikukuwerengera iwezi ndi zivumbulutso ndi ulaliki waluntha

Verse 59 — Surah Al-Imran 3:59

“Ndithudi, fanizo la Isa (Yesu) kwa Allah lili ngati fanizo la Adam; adamulenga ndi dothi namuuza kuti: “Khala munthu.” Ndipo adakhaladi

Verse 60 — Surah Al-Imran 3:60

“(Ichi ndi) choona chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale mwa okaikira

Verse 61 — Surah Al-Imran 3:61

“Tsopano amene akutsutsana nawe (iwe Mtumiki s.a.w) pa ichi pambuyo pokudzera kuzindikira, auze: “Bwerani tiitane ana athu ndi ana anu, akazi athu ndi akazi anu, ife ndi inu; kenako modzichepetsa tipemphe tembelero la Allah kuti likhale pa amene ali abodza (mwa ife).”

Verse 62 — Surah Al-Imran 3:62

“Ndithu iyi ndinkhani yoona; ndipo palibe woyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Allah. Ndithudi, Iye Allah Ngwamphamvu Zoposa, Ngwanzeru Zakuya

Verse 63 — Surah Al-Imran 3:63

“Ngati atembenuka (monyoza, Allah awalanga); ndithudi Allah Ngodziwa za oononga

Verse 64 — Surah Al-Imran 3:64

“Nena: “Inu eni buku (la Allah, Ayuda ndi Akhrisitu!) Idzani ku liwu lolingana pakati pathu ndi inu (lakuti) tisapembedze aliyense koma Allah (Mmodzi Yekha), ndiponso tisamphatikize ndi chilichonse ndipo ena mwa ife asawasandutse anzawo kukhala milungu m’malo mwa Allah.” Ngati atembenuka ndi kunyoza, nenani: “Ikirani umboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera malamulo a Allah).”

Verse 65 — Surah Al-Imran 3:65

“E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukutsutsana za Ibrahim pomwe Taurat ndi Injili sizidavumbulutsidwe koma pambuyo pake. Kodi simuzindikira

Verse 66 — Surah Al-Imran 3:66

“Taonani! Inu mudatsutsana pa zomwe mudazidziwa, nanga bwanji mukutsutsana pa zomwe simuzidziwa? Allah ndi Yemwe akudziwa. Pomwe inu simudziwa

Verse 67 — Surah Al-Imran 3:67

“Ibrahim sadali Myuda ndipo sadali Mkhrisitu, koma adali wolungama Msilamu (wodzipereka); ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina)

Verse 68 — Surah Al-Imran 3:68

“Ndithu anthu omwe ali oyenera kudzilumikiza ndi Ibrahim ndi amene adamutsata (m’nyengo yake) ndi Mtumiki uyu (Muhammad {s.a.w}) ndi amene amkhulupirira (Mtumikiyu). Ndipo Allah ndi Mtetezi wa okhulupirira

Verse 69 — Surah Al-Imran 3:69

“Gulu lina la anthu amene adapatsidwa buku likufuna kukusokeretsani; ndipo sasokeretsa aliyense koma iwo wokha, pomwe (iwo eni) sakuzindikira

Verse 70 — Surah Al-Imran 3:70

“E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukuzikana zizindikiro za Allah (Qur’an) pomwe mukudziwa

Verse 71 — Surah Al-Imran 3:71

“E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukusakaniza choona ndi chabodza, ndipo mukubisa choona uku mukudziwa

Verse 72 — Surah Al-Imran 3:72

“Ndipo gulu lina la amene adapatsidwa buku lidati (kwa anzawo): “Khulupirirani chomwe chavumbulutsidwa kwa Asilamu kumayambiliro kwa usana, ndipo chikaneni kumalekezero kwake (kwa usana) mwina angabwelere (kusiya Chisilamu)

Verse 73 — Surah Al-Imran 3:73

“Ndipo musakhulupirire aliyense kupatula yekhayo yemwe watsata chipembedzo chanu. (Allah adauza Mtumiki {s.a.w}), nena: “Ndithudi, chiongoko chenicheni ndi chiongoko cha Allah basi.” (Amene adapatsidwa buku Adanena kwa anzawo: “Musakhulupirire) kuti angapatsidwe aliyense zofanana ndi zomwe mwapatsidwa inu (Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti angakutsutseni kwa Mbuye wanu.” (Allah adati kwa mtumiki{s.a.w}), nena: “Ndithu zabwino zonse zili m’manja mwa Allah; amazipereka kwa yemwe wamfuna. Allah ndi Mataya, Ngodziwa.”

Verse 74 — Surah Al-Imran 3:74

“Amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino wawukulu

Verse 75 — Surah Al-Imran 3:75

“Ndipo mwa iwo muli anthu ena oti ukawasungitsa milumilu ya chuma, akubwezera. Ndipo mwa iwo muli ena oti ukawasungitsa “dinar” (ndalama imodzi) sangakubwezere pokhapokha upitirize kwa iye kuimilira (kulonjelera). Izi nchifukwa chakuti amanena: “Palibe njira pa ife (yotidzudzulira) chifukwa chozibera mbulizi.” Koma akumnamizira Allah uku iwo akudziwa

Verse 76 — Surah Al-Imran 3:76

“Sichoncho (monga momwe akunenera)! Koma amene akukwaniritsa lonjezo lake napewa machimo (ndiyemwe ayenera kukhala wokondedwa kwa Allah). Ndithudi, Allah amakonda opewa machimo

Verse 77 — Surah Al-Imran 3:77

“Ndithu anthu amene akusinthanitsa chipangano cha Allah ndi malumbiliro awo, (ndi zinthu za) mtengo wochepa, iwo alibe gawo labwino pa tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah sadzawayankhula (ndi mawu abwino); ndipo sadzawayang’ana (ndi diso la chifundo) pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso sadzawayeretsa (kumachimo awo); ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka

Verse 78 — Surah Al-Imran 3:78

“Ndipo ndithu mwa iwo muli gulu lomwe likukhotetsa malirime awo (powerenga) buku kuti muwaganizire (mawu awowo) kuti ndi a m’buku la Allah); pomwe si a m’buku (la Allah). Ndipo akunena: “Izi zachokera kwa Allah.” Pomwe zimenezo sizinachokere kwa Allah; ndipo akumnamizira Allah uku akudziwa

Verse 79 — Surah Al-Imran 3:79

“Sikoyenera kwa munthu yemwe Allah wampatsa buku ndi chiweruzo ndi uneneri, kenako nanena kwa anthu: “Khalani opembedza ine, mmalo mwa Allah.” Koma (awauze): “Khalani opembedza Allah, anzeru, aluntha chifukwa choti mukuphunzitsa buku ndi chifukwanso cha zomwe mukaphunzira.”

Verse 80 — Surah Al-Imran 3:80

“Ndipo sangakulamulireni kuwasandutsa angelo ndi aneneri kukhala milungu. Kodi angakulamulireni kusakhulupirira pambuyo poti muli Asilamu (ogonjera)

Verse 81 — Surah Al-Imran 3:81

“Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adatenga lonjezo kwa aneneri, (n’kuwauza): “Ndikakupatsani buku ndi nzeru, nakudzerani Mtumiki wotsimikizira zomwe zili pamodzi ndi inu, mudzamkhulupirire ndi kumthangata.” (Allah) adatinso: “Kodi mwavomereza ndi kulandira pa zimenezi pangano langali?” (Iwo) adati: “Tavomereza.” (Iye) adati: “Tsono chitirani umboni, ine ndili pamodzi nanu mwa oikira umboni.”

Verse 82 — Surah Al-Imran 3:82

“Ndipo amene adzatembenuke pambuyo pa lonjezoli, (Allah adzawalanga chifukwa chakuti) iwo ngopandukiradi chilamulo cha Allah

Verse 83 — Surah Al-Imran 3:83

“Kodi akufuna chipembedzo chomwe si cha Allah pomwe chinthu chilichonse chili kumwamba ndi pansi chikugonjera Iye, mofuna kapena mosafuna? Ndipo onse adzabwezedwa kwa Iye

Verse 84 — Surah Al-Imran 3:84

“Nena: “Takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa pa ife, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, ndi Ismail, Ishâq ndi Yaqub ndi zidzukulu (zake), ndi zimene adapatsidwa Mûsa ndi Isa (Yesu), ndi aneneri (ena) zochokera kwa Mbuye wawo. Sitisiyanitsa aliyense pakati pawo, ndipo ife kwa Iye ndi Asilamu (odzipereka kwathunthu).”

Verse 85 — Surah Al-Imran 3:85

“Ndipo amene angafune chipembedzo chosakhala Chisilamu, sichidzalandiridwa kwa iye. Ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mmodzi mwa (anthu) otaika

Verse 86 — Surah Al-Imran 3:86

“Kodi Allah angawaongole bwanji anthu omwe atuluka m’chikhulupiliro pambuyo pakukhulupirira natsimikiza kuti Mtumiki (uyu Muhammad{s.a.w}) ngoona, nkuwafikiranso zisonyezo zoonekera? Koma Allah saongola anthu ochita zoipa

Verse 87 — Surah Al-Imran 3:87

“Ndithu mphoto yawo ndiyakuti pa iwo pali matembelero a Allah, a angelo ndi anthu onse

Verse 88 — Surah Al-Imran 3:88

“M’menemo adzakhala nthawi yaitali; ndipo sichidzapeputsidwa chilango kwa iwo, ndiponso sadzapatsidwa danga

Verse 89 — Surah Al-Imran 3:89

“Kupatula anthu amene alapa, pambuyo pa zimenezo nachita zabwino. ndithudi, Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

Verse 90 — Surah Al-Imran 3:90

“Ndithudi, amene atuluka m’chikhulupiliro pambuyo pokhulupirira, kenako naonjezera kusakhulupirira, kulapa kwawo sikudzavomerezedwa konse. Ndipo iwo ndiosekera

Verse 91 — Surah Al-Imran 3:91

“Ndithudi amene sadakhulupirire, nkumwalira pamene ali osakhulupirira, sikudzalandiridwa kwa aliyense wa iwo ngakhale atapereka dipo la golide lodzadza dziko lonse. Iwo ndi omwe adzalandire chilango chopweteka, ndipo sadzakhala ndi athandizi

Verse 92 — Surah Al-Imran 3:92

“۞ Simudzapeza ubwino (weniweni) kufikira mutapereka m’zimene mukuzikonda. Ndipo chilichonse chimene mupereka, ndithudi, Allah akuchidziwa

Verse 93 — Surah Al-Imran 3:93

“Zakudya zonse zidali zololedwa kwa ana a Israyeli kupatula chimene adadziretsa Israyeli mwini wake Taurat isadavumbulutsidwe. Nena: “Bwerani ndi Tauratiyo ndipo iwerengeni ngati mukunena zoona.”

Verse 94 — Surah Al-Imran 3:94

“Choncho aliyense amene adzapekera bodza Allah pambuyo pa izi iwo ndiwochita zoipa

Verse 95 — Surah Al-Imran 3:95

“Nena: “Allah wanena zoona. Choncho tsatirani chipembedzo cha Ibrahim yemwe adali wolungama; sadali mwa ophatikiza Allah ndi mafano.”

Verse 96 — Surah Al-Imran 3:96

“Ndithudi, nyumba yoyamba yomwe idakhazikitsidwa chifukwa cha anthu (kuti azipempheramo) ndiyomwe ili pa Bakka (ku Makka); yodalitsidwa ndiponso ndichiongolo kwa anthu onse

Verse 97 — Surah Al-Imran 3:97

“M’menemo muli zizindikiro zoonekera (zozindikiritsa kupatulika kwake ndi ukale wake); ndi pamalo pomwe Ibrahim adali kuimilira; ndipo amene akulowamo amakhala m’chitetezo; ndipo Allah walamula anthu kuti akachite Hajj ku nyumbayo amene angathe kukonzekera ulendo wonka kumeneko. Ndipo yemwe angakane, (osapitako pomwe ali nazo zomuyenereza), ndithudi, Allah Ngwachikwanekwane pa zolengedwa Zake

Verse 98 — Surah Al-Imran 3:98

“Nena: “E inu amene mudapatsidwa buku! chifukwa chiyani mukuzikana zizindikiro za Allah pomwe Allah ndi Mboni wa zonse zimene mukuchita?”

Verse 99 — Surah Al-Imran 3:99

“Nena: “ E inu amene mudapatsidwa buku! Chifukwa chani mukutsekereza anthu amene akhulupirira kuyenda pa njira ya Allah? Mukufuna kuti ikhote pomwe inu ndinu mboni (kuti ndi njira ya Allah yopanda choipa)? Komatu Allah sanyalanyaza zomwe mukuchita.”

Verse 100 — Surah Al-Imran 3:100

“E inu amene mwakhulupirira! Ngati muwamvera ena mwa amene apatsidwa buku, akubwezani kuti mukhale osakhulupirira pambuyo pa chikhulupiliro chanu

Verse 101 — Surah Al-Imran 3:101

“Kodi mukukanira bwanji pomwe ndime za Allah zikuwerengedwa kwa inu, pomwenso Mtumiki Wake ali pamodzi nanu? Ndipo amene agwiritse mwa Allah (bwinobwino), ndithudi iye wawongoleredwa kunjira yoongoka

Verse 102 — Surah Al-Imran 3:102

“E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah; kuopa kwenikweni. Ndipo musafe pokhapokha mutakhala Asilamu (ogonjera)

Verse 103 — Surah Al-Imran 3:103

“Ndipo gwiritsani chingwe (chipembedzo) cha Allah nonsenu, ndipo musagawikane. Kumbukirani mtendere wa Allah womwe uli pa inu; pamene mudali odana ndipo Iye adalunzanitsa pakati pa mitima yanu, tero mwa mtendere Wake mudakhala abale; ndipo mudali m’mphepete mwa dzenje la moto (wa Jahanama), ndipo Iye adakupulumutsanimo. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah Ake (ndime Zake) kuti muongoke

Verse 104 — Surah Al-Imran 3:104

“Ndipo mwa inu lipezeke gulu la anthu oitanira ku zabwino (Chisilamu) ndipo alamule (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa. Iwo ndiwo opambana

Verse 105 — Surah Al-Imran 3:105

“Ndipo musakhale monga aja amene adagawikana nasiyana pambuyo powadzera zisonyezo zoonekera poyera (zowaletsa kutero). Ndipo iwo adzakhala ndichilango chachikulu

Verse 106 — Surah Al-Imran 3:106

“Patsikulo nkhope zina zidzakhala zowala pomwe nkhope zina zidzakhala zakuda. Tsono amene nkhope zawo zidzakhala zakuda, (adzauzidwa): “Kodi mudakana ( Allah) pambuyo pa chikhulupiliro chanu? Choncho, lawani chilango (chopweteka) chifukwa cha zomwe mudali kuzikana.”

Verse 107 — Surah Al-Imran 3:107

“Tsono (anthu odala) omwe nkhope zawo zidzawale, adzakhala m’chifundo cha Allah. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali

Verse 108 — Surah Al-Imran 3:108

“Awo ndi ma Ayah (ndime) a Allah; tikukuwerengera mwa choonadi. Ndipo Allah safuna kupondereza zolengedwa (Zake)

Verse 109 — Surah Al-Imran 3:109

“Chilichonse cha kumwamba ndipansi ncha Allah. ndipo zinthu zonse zidzabwezedwa kwa Allah

Verse 110 — Surah Al-Imran 3:110

“Inu (Asilamu) ndinu gulu labwino limene lasankhidwa kwa anthu. Mukulamula (kuchita) zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa Allah. Ndipo aja adapatsidwa buku akadakhulupirira monga momwe (adawalamulira) kukadakhala kwabwino kwa iwo. (Koma) mwa iwo alipo okhulupirira pomwe ambiri mwa iwo ngopandukira (chilamulo cha Allah)

Verse 111 — Surah Al-Imran 3:111

“Sangakuvutitseni (adani anuwo, makamaka Ayuda) koma ndi timasautso (tochepa); ngati (atayesera) kukuthirani nkhondo, akufulatirani (kuthawa); ndipo kenako sangapulumutsidwe

Verse 112 — Surah Al-Imran 3:112

“Adindidwa chidindo chakunyozeka paliponse pamene angapezeke kupatula (akagwira) chingwe (cha chipembedzo) cha Allah, kapena chingwe cha anthu (pothandizidwa ndi anthu ena. Koma paokha sangakhale ndi nyonga). Abwerera ndi mkwiyo wa Allah; ndipo chidindo chaumphawi chadindidwa pa iwo. Izi nchifukwa chakuti iwo sadali kukhulupirira mawu a Allah, ndipo amapha aneneri popanda choonadi. Izi nchifukwa chakutinso adanyoza ndi kulumpha malire

Verse 113 — Surah Al-Imran 3:113

“Iwo amene adapatsidwa buku sali ofanana. Mwa iwo muli anthu olungama omwe akuwerenga ma Ayah (ndime) a Allah nthawi za usiku uku akumulambira

Verse 114 — Surah Al-Imran 3:114

“Amakhulupirira Allah ndi lsiku lomaliza; ndipo amalamulira (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa; ndipo amachita changu pa zinthu zabwino. Ndipo iwo ndi omwe ali mwa anthu abwino

Verse 115 — Surah Al-Imran 3:115

“Ndipo chabwino chilichonse chimene angachite sadzakanidwa nacho, (koma adzawalipira malipiro abwino). Ndipo Allah Ngodziwa za amene akuopa Iye

Verse 116 — Surah Al-Imran 3:116

“Ndithudi, amene sakhulupirira, chuma chawo ngakhale ana awo, sizidzawathandiza chilichonse kwa Allah. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto basi; adzakhala mmenemo nthawi yaitali

Verse 117 — Surah Al-Imran 3:117

“Fanizo la chimene akupereka mwaulere pa moyo uwu wa dziko lapansi, chili ngati mphepo yomwe mkati mwake muli chisanu chaukali, chagwera pa munda wa anthu omwe adadzichitira okha zoipa, n’kuuonongeratu. Si Allah amene adawachitira zoipa, koma iwo okha adadzichitira zoipa

Verse 118 — Surah Al-Imran 3:118

“E inu amene mwakhulupirira! Musawachite omwe sali mwa inu kukhala abwenzi; owauza chinsinsi, iwo sasiya kukuchitirani choipa. Amakonda zimene zikukuvutitsani. Chidani chawo (pa inu) chaonekera m’milomo yawo. Ndipo zimene zikubisa zifuwa zawo, nzazikulu zedi. Ndithudi, takufotokozerani zizindikiro zonse ngati inu muli anthu ozindikira

Verse 119 — Surah Al-Imran 3:119

“Ha! Inu ndinu amene muwakonda (adani anu) pomwe iwo sakukondani ngakhale inu mukukhulupirira mabuku onse! Akakumana nanu amanena (mwachiphamaso): “Takhulupirira.” Koma akakhala kwa okha, amakulumirani nsonga za zala chifukwa chaukali. Nena: “Mwalirani ndiukali wanuwo ndithudi, Allah akudziwa za m’zifuwa (mwanu).”

Verse 120 — Surah Al-Imran 3:120

“Ngati chabwino chikakufikirani, amaipidwa nacho; koma choipa chikakugwerani amachikondwelera. Koma ngati inu mupirira ndi kuopa Allah, ndale zawo sizingakuvutitseni chilichonse. Ndithu Allah akudziwa bwino zonse zimene iwo akuchita

Verse 121 — Surah Al-Imran 3:121

“(Kumbukira) pamene unachoka m’mawa kusiya banja lako kuti uwakonzere Asilamu malo omenyanira (nkhondo). Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa

Verse 122 — Surah Al-Imran 3:122

“(Kumbukira) pamene magulu awiri mwa inu anafunitsitsa kuti athawe (chifukwa cha mantha monga momwe adathawira achinyengo). Koma Allah adali Mtetezi wa magulu awiriwo. (Choncho adawasunga kuti asathawe). Ndipo okhulupirira ayadzamire kwa Allah Yekha basi

Verse 123 — Surah Al-Imran 3:123

“Allah adakupulumutsani pa (nkhondo) ya Badri pomwe inu munali ofooka (chifukwa chakuchepa ndi kusakhala ndi zida zokwanira). Choncho opani Allah kuti mumthokoze (nthawi zonse pa zomwe akukuchitirani)

Verse 124 — Surah Al-Imran 3:124

“(Kumbukira) pamene umauza okhulupirira: “Kodi sizikukukwanirani pokuonjezerani Mbuye wanu zikwi zitatu za angelo otsitsidwa

Verse 125 — Surah Al-Imran 3:125

“Inde, ngati mupirira ndi kudziteteza ku machimo, ndipo (adani anu) nakudzerani mwachangu chawo chimenechi, pamenepo Mbuye wanu adzakuonjezerani ndi zikwi zisanu za angelo odziwa kumenya nkhondo.”

Verse 126 — Surah Al-Imran 3:126

“Ndipo Allah sadachite izi (potumiza angelo) koma kuti ukhale uthenga wabwino kwa inu ndi kuti pakutero mitima yanu ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo chithandizo sichichokera (kwa wina aliyense) koma kwa Allah basi, Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

Verse 127 — Surah Al-Imran 3:127

“(Kuchita izi) nkuti adule gawo la osakhulupirira (kuti ena a iwo aphedwe) kapena awasambule ndi kuti abwelere ali olephera

Verse 128 — Surah Al-Imran 3:128

“Iwe ulibe chako pa izi. Mwina (Allah) angalandire kulapa kwawo kapena kuwalanga pakuti ndithu iwo ndi anthu oipa

Verse 129 — Surah Al-Imran 3:129

“Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah; amamkhululukira amene wamfuna, ndikumulanga amene wamfuna. Komatu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

Verse 130 — Surah Al-Imran 3:130

“E inu amene mwakhulupirira! Musadye Riba (chuma cha katapira), kumangoonjezeraonjezera. Ndipo opani Allah kuti mupambane

Verse 131 — Surah Al-Imran 3:131

“Ndipo opani Moto umene wakonzedwa kwa (anthu) osakhulupirira

Verse 132 — Surah Al-Imran 3:132

“Ndipo mverani Allah ndi Mtumiki kuti mumveredwe chisoni

Verse 133 — Surah Al-Imran 3:133

“Ndipo chimkereni mwachangu chikhululuko cha Mbuye wanu (kupyolera m’zochita zanu zabwino), ndi Munda (Wake) umene Kutambasuka kwake (mulifupi) kuli ngati kumwamba ndi pansi, (womwe) wakonzedwa kuti ukhale wa oopa Allah

Verse 134 — Surah Al-Imran 3:134

“Omwe amapereka (zopereka zawo mwaulere) pamene akupeza bwino ngakhale pamene akuvutika; amenenso amabisa ukali wawo ndi okhululukira anthu. Ndipo Allah amakonda ochita zabwino

Verse 135 — Surah Al-Imran 3:135

“Ndi amene amati akachita uve (wamachimo), kapena kudzichitira okha zoipa, amakumbukira Allah nampempha chikhululuko pa machimo awo. Kodi ndindani angakhululuke machimo kupatula Allah; ndipo napanda kupitiriza machimo omwe achita uku akudziwa

Verse 136 — Surah Al-Imran 3:136

“Iwowo mphoto yawo ndi chikhululuko chochokera kwa Mbuye wawo, ndi minda yoyenda mitsinje pansi pake (ndi patsogolo pake), momwe akakhalamo nthawi yaitali. Taonani kukoma malipiro a ochita zabwino

Verse 137 — Surah Al-Imran 3:137

“Zidapita njira za zilango zambiri zosiyanasiyana zomwe adapatsidwa amene adalipo patsogolo panu. Tero tayendani pa dziko ndi kuona momwe adalili mapeto a anthu otsutsa

Verse 138 — Surah Al-Imran 3:138

“Uku ndi kulengeza poyera kwa anthu (onse); komanso chiongoko ndi ulaliki kwa (anthu) oopa Allah

Verse 139 — Surah Al-Imran 3:139

“Ndipo musafooke (pomenya nkhondo), ndiponso musadandaule (ndi mavuto amene akupezani) pakuti ndinu apamwamba, ngati mulidi okhulupirira

Verse 140 — Surah Al-Imran 3:140

“Ngati mwavulazidwa, naonso anthuwo avulazidwanso molingana. Ndipo amenewo ndimasiku, timawapatsa anthu mosinthanasinthana. (Ichi chachitika) kuti Allah aonetse poyera amene akhulupirira (moona; choncho sadathawe konse); ndi kuti awachite ena mwa inu kukhala Shuhadaa (ofera pankhondo yoyera). Komatu Allah sakonda anthu ochita zoipa

Verse 141 — Surah Al-Imran 3:141

“(Izi) nkuti Allah awayeretse amene akhulupirira ndikuwathetseratu osakhulupirira

Verse 142 — Surah Al-Imran 3:142

“Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe Allah asadawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo cha Allah mwa inu ndi kuwaonetseranso poyera opirira (pa nkhondo ya Allah)

Verse 143 — Surah Al-Imran 3:143

“Ndithudi, mudali kuilakalaka imfa musanakumane nayo. Ndithudi tsopano mwaiona (ndikuphedwa kwa abale anu) inu mukupenya

Verse 144 — Surah Al-Imran 3:144

“Muhammad (s.a.w) sali chinthu china koma Mtumiki chabe. Patsogolo pake adamuka atumiki ambiri. Kodi ngati atamwalira kapena kuphedwa, mungabwelerenso m’mbuyo? Ndipo amene abwelere m’mbuyo mwake savutitsa Allah ndi chilichonse; koma Allah adzalipira othokoza

Verse 145 — Surah Al-Imran 3:145

“Munthu aliyense sangafe pokhapokha mwa chilolezo cha Allah, (ndi kukwanira) nthawi yake yolembedwa. Ndipo amene akufuna mphoto ya pa dziko la pansi, timpatsa pompo; ndipo amene akufuna Mphoto ya tsiku lachimaliziro tidzampatsa konko. Ndipo, tidzawalipira (zabwino) othokoza

Verse 146 — Surah Al-Imran 3:146

“Ndi Aneneri angati adamenyana (ndi adani) pamodzi ndi anthu olungama ambiri, komatu sadataye mtima pa mavuto omwe adawagwera pa njira ya Allah; sadafooke ndipo sadagonjere (adani awo), ndipo Allah amakonda opirira

Verse 147 — Surah Al-Imran 3:147

“(Anthu olungamawa) kunena kwawo sikudali kwina koma ankati: “Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kupyola malire kwathu m’zinthu zathu. Ndipo limbikitsani mapazi athu (panjira Yanu) ndipo tithandizeni ku anthu osakhulupirira.”

Verse 148 — Surah Al-Imran 3:148

“Choncho Allah adawapatsa mphoto ya pa dziko lapansi ndi mphoto yabwino ya tsiku lachimaliziro. Allah amakonda ochita zabwino

Verse 149 — Surah Al-Imran 3:149

“E inu amene mwakhulupirira! Ngati muwamvere amene sadakhulupirire, akubwezerani kumbuyo kwanu (kumachitidwe achikunja) tero mudzakhala otaika

Verse 150 — Surah Al-Imran 3:150

“Komatu Allah ndiye Mbuye wanu. Iye Ngwabwino kwabasi kuposa athandizi (ena onse)

Verse 151 — Surah Al-Imran 3:151

“Tiponya mantha m’mitima mwa amene sadakhulupirire chifukwa chakumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadatsitsire umboni (wosonyeza umulungu wawo) ndipo malo awo adzakhala ku Moto. Taonani kuipitsitsa malo a anthu ochita zoipa

Verse 152 — Surah Al-Imran 3:152

“Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira

Verse 153 — Surah Al-Imran 3:153

“Kumbukirani pamene mudali kuthawa mwa liwiro popanda kumvera aliyense; pomwe Mtumiki adali kukuitanani, ali pambuyo panu. Ndipo (Allah) Adakupatsani madandaulo pa madandaulo. (Motero wakukhululukirani) kuti musadandaule pa zomwe zakudutsani, ngakhalenso (pa masautso) omwe akupezani. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita

Verse 154 — Surah Al-Imran 3:154

“Kenako pambuyo pa kudandaula, adakutsitsirani mpumulo - tulo tomwe tidaphimba gulu lina mwa inu. Padali gulu lina lomwe maganizo awo adawatangwanitsa namuganizira Allah ndizoganizira zopanda choonadi, zoganizira zaumbuli; ankati: “Ha! Kodi tili ndi chiyani ife pa chinthu ichi?” Nena: “Zinthu zonse nza Allah.” Akubisa m’mitima mwawo zomwe sakuzionetsa kwa iwe. Akunena: “Tidakakhala ndi chilichonse pa chinthu ichi, sitikadaphedwa apa.” Nena: “Ngakhale mukadakhala m’nyumba zanu, ndithudi kwa iwo amene imfa idalembedwa (kuti amwalire) akadapita kumalo omwalilirawo, koma Allah (adachita izi) kuti awonetse poyera zomwe zili m’zifuwa zanu. Ndikuyeretsa zomwe zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa za mzifuwa.”

Verse 155 — Surah Al-Imran 3:155

“Ndithudi, mwa inu amene adabwerera m’mbuyo (kuthawa) tsiku lomwe magulu awiri a nkhondo adakumana (pa nkhondo ya Uhudi; gulu la osakhulupirira ndi gulu lankhondo la Asilamu), satana ndiyemwe adawaterezetsa chifukwa cha zina (zolakwa) zomwe adachita; ndipo Allah (tsopano) wawakhululukira. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngoleza koposa

Verse 156 — Surah Al-Imran 3:156

“E inu amene mwakhulupirira! Musakhale ngati amene sadakhulupirire, nanena za anzawo pamene akuyenda pa dziko kapena pomwe akumenyana nkhondo (ndikufera konko): “Akadakhala ndi ife sakadafa, ndiponso sakadaphedwa.” Allah (adawathira maganizo amenewa) kuti azipange zimenezo kukhala zodandaulitsa m’mitima mwawo. Komatu Allah ndi amene amapereka moyo ndi imfa. Ndipo Allah akuona zonse zomwe mukuchita

Verse 157 — Surah Al-Imran 3:157

“Ndipo ngati mwaphedwa pa njira ya Allah, kapena kufa, (palibe chotaika kwa inu) pakuti chikhululuko ndi chisoni zochokera kwa Allah nzabwino kuposa zomwe akuzisonkhanitsa (pa moyo wa pa dziko lapansi)

Verse 158 — Surah Al-Imran 3:158

“Ndipo ngati mumwalira kapena kuphedwa (n’chimodzimodzi), ndithudi nonsenu mudzasonkhanitsidwa kwa Allah

Verse 159 — Surah Al-Imran 3:159

“Chifukwa cha chifundo chochokera kwa Allah, uli woleza mtima kwa iwo, (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}). Ndipo ukadakhala waukali, wouma mtima, ndithudi, akadakuthawa pamaso pako. Choncho akhululukire ndi kuwapemphera chikhululuko (kwa Allah); ndipo chita nawo upo pa zinthu. Ndipo ngati watsimikiza, tsamira kwa Allah (basi, ndi kuchita chimene watsimikiza kuchichita). Ndithudi, Allah amakonda oyadzamira Kwake (odalira Iye)

Verse 160 — Surah Al-Imran 3:160

“Ngati Allah akupulumutsani, palibe amene angathe kukugonjetsani. Ndipo ngati akulekani, ndaninso angakupulumutseni pambuyo pake. Choncho, okhulupirira ayadzamire kwa Allah basi

Verse 161 — Surah Al-Imran 3:161

“Nkosatheka kwa Mtumiki kuchita chinyengo. Ndipo amene achite chinyengo adzadza pa tsiku lachimaliziro ndi zomwe adazichitira chinyengo. Kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zomwe adachita. Ndipo sadzaponderezedwa

Verse 162 — Surah Al-Imran 3:162

“Kodi amene akutsata chokondweretsa Allah angalingane ndi yemwe wabwerera ndi mkwiyo wochokera kwa Allah, ndipo Jahannam nkukhala malo ake? Taonani kuipa kumalo obwerera

Verse 163 — Surah Al-Imran 3:163

“Iwo ali ndi maulemelero (osiyanasiyana) kwa Allah. Ndipo Allah akuona zonse zomwe akuchita

Verse 164 — Surah Al-Imran 3:164

“Ndithudi, Allah adawachitira ubwino waukulu okhulupirira powatumizira Mtumiki wochokera mwa iwo yemwe akuwawerengera ma Ayah ake (ndime zake) ndikuwayeretsa ndikuwaphunzitsa buku ndi (mawu a) nzeru. Ndithudi, kale adali mkusokera koonekera

Verse 165 — Surah Al-Imran 3:165

“Pamene sautso lidakupezani lomwe inu mudawathira nalo (adani anu) lochulukirapo kawiri, mudanena: “Lachokera kuti (sautso) ili?” Nena: “Ilo lachokera kwa inu eni (chifukwa cha kunyoza lamulo lomwe adakuuzani). Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse.”

Verse 166 — Surah Al-Imran 3:166

“Ndipo sautso lomwe lidakupezani tsiku lomwe adakumana magulu awiri ankhondo, lidali mwa chilolezo cha Allah ndikutinso awaonetsere poyera okhulupirira

Verse 167 — Surah Al-Imran 3:167

“Ndi kuwadziwitsa amene adachita uchiphamaso. Iwo adauzidwa: “Bwerani, menyani (nkhondo) pa njira ya Allah kapena mwatsekereze (adani kwa ife).” Adati: “Tikadadziwa kuti pali kumenyana, ndithudi, tikadakutsatani (koma kumeneko kuli kuphedwa kokhakokha basi).” Iwo tsiku limenelo adali pafupi ndikusakhulupirira kuposa chikhulupiliro (ngakhale kuti masiku onse amasonyeza Chisilamu mwa chiphamaso). Akunena ndi milomo yawo zomwe sizili m’mitima mwawo. Koma Allah akudziwa bwinobwino (zonse) zomwe akubisa

Verse 168 — Surah Al-Imran 3:168

“Iwo ndi amene adanena za abale awo pomwe iwo adakhala osapita ku nkhondo: “Akadatimvera, sibwenzi ataphedwa.” Nena: “Dzichotsereni imfa nokha, (kuti musafe) ngati mukunenadi zoona.”

Verse 169 — Surah Al-Imran 3:169

“Ndipo musawaganizire omwe adaphedwa pa njira ya Allah kuti ndi akufa, koma iwo ngamoyo, akudyetsedwa kwa Mbuye wawo

Verse 170 — Surah Al-Imran 3:170

“Akukondwera pa zimene wawapatsa Allah kuchokera m’zabwino Zake. Ndipo akufunira mafuno abwino amene sadakumane nawo omwe ali pambuyo pawo, (omwe alipobe pa dziko lapansi) ponena kuti pa iwo sipadzakhala mantha kapena kudandaula

Verse 171 — Surah Al-Imran 3:171

“Akukondwelera chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah, ndi kuti Allah sasokoneza malipiro a okhulupirira

Verse 172 — Surah Al-Imran 3:172

“(Awa ndi) amene adavomera Allah ndi Mtumiki pambuyo povulazidwa; kwa amene achita zabwino mwa iwo ndi kuopa Allah, adzakhala ndi malipiro aakulu

Verse 173 — Surah Al-Imran 3:173

“Omwenso adauzidwa ndi anthu (olembedwa ganyu ndi Akafiri aku Makka) kuti: “Anthu Akusonkhanirani. Choncho aopeni.” Koma (zonenazo) zidawaonjezera chikhulupiliro (Asilamu). Ndipo adati: “Allah akutikwanira, ndipo Iye ndi Mtetezi wabwino koposa.”

Verse 174 — Surah Al-Imran 3:174

“Choncho adabwerera ndi chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah. Sichidawakhudze choipa chilichonse; adatsatira zokondweretsa Allah. Ndipo Allah ndimwini ubwino waukulu

Verse 175 — Surah Al-Imran 3:175

“Ndithudi uyo (anakuopsezani) ndi satana yemwe amaopseza anzake. Choncho musawaope, ndiopeni Ine ngati inu mulidi okhulupirira

Verse 176 — Surah Al-Imran 3:176

“Ndipo asakudandaulitse omwe akuthamangira kuchita zinthu zachikunja. Ndithu iwo sangapereke sautso lililonse kwa Allah. Allah akufuna kuti asawaikire gawo lililonse la (zabwino) tsiku lachimaliziro, ndipo pa iwo padzakhala chilango chachikulu

Verse 177 — Surah Al-Imran 3:177

“Ndithudi, amene asinthanitsa kusakhulupirira ndi chikhulupiliro, sangathe kumvutitsa Allah ndi chilichonse. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chopweteka

Verse 178 — Surah Al-Imran 3:178

“Ndipo amene sadakhulupirire asaganize kuti nthawi yaitali imene tikuwapatsayi njabwino kwa iwo. Ndithudi, tikuwapatsa nthawiyi kuti aonjezere kuchita uchimo. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chosambula

Verse 179 — Surah Al-Imran 3:179

“Nkosatheka kwa Allah kusiya okhulupirira momwe mulilimu, mpaka atalekanitsa (pakati pawo) oipa ndi abwino. Ndipo nkosatheka kwa Allah kukudziwitsani zinthu zamseri, koma Allah amasankha mwa atumiki ake amene wamfuna (nkumdziwitsa zina mwa zimenezo). Choncho khulupirirani Allah ndi atumiki ake. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kuopa (Allah), pa inu padzakhala malipiro aakulu

Verse 180 — Surah Al-Imran 3:180

“Ndipo asaganize amene akuchitira umbombo zimene Allah wawapatsa kuchokera m’zabwino Zake kuti kutero ndibwino kwa iwo, koma kutero nkoipa kwa iwo. Adzanjatidwa magoli pa zomwe adazichitira umbombo pa tsiku lachimaliziro. Ndipo um’lowam’malo wa zakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

Verse 181 — Surah Al-Imran 3:181

“Ndithu Allah wamva liwu (lonyogodola) la omwe (Ayuda) anena kuti: “Allah ngosauka, ndipo ife ndife olemera.” Tazilemba zimene anena, ndipo (talembanso) kupha kwawo aneneri popanda choonadi. Ndipo tidzawauza (tsiku la chiweruziro): “Lawani chilango cha Moto owotcha.”

Verse 182 — Surah Al-Imran 3:182

““Izi nchifukwa cha zomwe manja anu adatsogoza. Ndithudi, Allah sali opondereza akapolo Ake.”

Verse 183 — Surah Al-Imran 3:183

“Amene anenanso: “Allah Adatilamula ife kuti tisakhulupirire mtumiki aliyense mpaka atabwera ndi nsembe yopserezedwa ndi moto.” Nena: “Adakudzerani atumiki ndisanadze ndi zisonyezo zooneka ndi chimene mukunenachi. Nanga bwanji mudawapha, ngati mukunenadi zoona?”

Verse 184 — Surah Al-Imran 3:184

Ndipo ngati akutsutsa iwe (Mtumiki Muhammad (s.a.w}, sichachilendo) adatsutsidwanso atumiki patsogolo pako omwe adadza ndi zisonyezo zoonekera ndi mabuku anzeru, ndi mabukunso ounika

Verse 185 — Surah Al-Imran 3:185

“Munthu aliyense adzalawa imfa. Ndithudi, mudzalipidwa malipiro anu mokwanira tsiku lachimaliziro. Ndipo amene adzatalikitsidwe ndi Moto nalowetsedwa ku Munda wamtendere, ndiye kuti wapambana, (kupambana kwakukulu), ndipo moyo wapadziko lapansi sulikanthu koma ndichisangalalo chonyenga basi

Verse 186 — Surah Al-Imran 3:186

“Ndithu mudzayesedwa m’chuma chanu ndi miyoyo yanu; ndipo mudzamva masautso ambiri kuchokera kwa omwe adapatsidwa mabuku kale ndiponso kuchokera kwa omwe akuphatikiza Allah ndi zinthu zina (Arab), koma ngati mupirira ndi kudzisunga ku zomwe mwaletsedwa ndi Allah, (ndiye kuti mwachita chinthu chabwino kwambiri) pakuti zinthu izi (ndi zinthu zazikulu) zofunika munthu kuikirapo mtima

Verse 187 — Surah Al-Imran 3:187

“Ndipo (akumbutse) pamene Allah adamanga chipangano ndi amene adapatsidwa buku (ndi kuwauza) kuti ndithudi mudzalifotokoze mwatsatanetsatane (bukulo) kwa anthu, ndipo musadzalibise. Koma Adaliponya kumbuyo kwa misana yawo naligulitsa ndi mtengo wochepa. Taonani kuipa chimene adagula (chimene adasankha)

Verse 188 — Surah Al-Imran 3:188

“Musaganize kuti amene akukondwera ndi zinthu (zoipa) zomwe achita nakonda kutamandidwa ndi zomwe sadachite, musawaganizire kuti akapulumuka. (Koma kuti) pa iwo padzakhala chilango chopweteka

Verse 189 — Surah Al-Imran 3:189

“Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah; ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

Verse 190 — Surah Al-Imran 3:190

“Ndithudi, m’kulenga kwa kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, muli zisonyezo kwa eni nzeru

Verse 191 — Surah Al-Imran 3:191

“Omwe amakumbukira Allah, ali chiimire, ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; namalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (mmene Allah adazilengera, uku akuti): “E Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe. Ulemelero Ngwanu. Tichinjirizeni ku chilango cha Moto.”

Verse 192 — Surah Al-Imran 3:192

““E Mbuye wathu! Ndithudi, yemwe mudzamulowetse ku Moto ndiye kuti mwamuyalutsa, ndipo sipadzakhala athandizi kwa ochita zoipa.”

Verse 193 — Surah Al-Imran 3:193

““E Mbuye wathu! Ndithudi, ife tamva woitana akuitanira ku chikhulupiliro kuti: ‘Khulupirirani Mbuye wanu,’ ndipo takhulupirira. E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kutifafanizira zoipa zathu, ndipo mutenge mizimu yathu tili pamodzi ndi anthu abwino.”

Verse 194 — Surah Al-Imran 3:194

““E, Mbuye wathu! Tipatseni zimene mudatilonjeza kupyolera mwa atumiki anu ndipo musadzatisambule tsiku lachimaliziro. Ndithudi, inu simuswa lonjezo.”

Verse 195 — Surah Al-Imran 3:195

“Choncho Mbuye wawo adawavomereza (zopempha zawo ponena kuti): “Ndithudi, ine sindidzasokoneza (khama la) ntchito yabwino kwa ochita ntchito mwa inu, kaya atakhala mwamuna kapena mkazi, (pakuti) inu ndinu amodzi. Choncho amene asamuka (kumidzi yawo mwachifuniro chawo), naapirikitsidwa m’midzi yawo navutitsidwa pa njira Yanga, namenya nkhondo ndikuphedwa, ndithudi, ndiwafafanizira zolakwa zawo. Ndipo ndidzawalowetsa m’Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda. Amenewo ndimalipiro ochokera kwa Allah, ndipo kwa Allah kuli malipiro abwino.”

Verse 196 — Surah Al-Imran 3:196

“Ndithu kusakunyenge kuyendayenda pa dziko kwa amene sadakhulupirire

Verse 197 — Surah Al-Imran 3:197

“Ndichisangalalo chochepa; kenako malo awo ndi kumoto wa Jahannam. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo

Verse 198 — Surah Al-Imran 3:198

“Koma amene aopa Mbuye wawo (potsatira zolamulidwa ndi kuleka zoletsedwa) adzapeza Minda yamtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi patsogolo pake). Adzakhala m’menemo nthawi yaitali, ndi phwando lochokera kwa Allah. Ndipo zomwe zili kwa Allah nzabwino kwa anthu abwino (kuposa zosangalatsa za dziko lapansi)

Verse 199 — Surah Al-Imran 3:199

“Ndithudi mwa amene adapatsidwa buku, alipo amene akukhulupirira Allah ndi zimene zavumbulutsidwa kwa inu, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa iwo, uku akudzichepetsa kwa Allah; sagulitsa ndime za Allah ndi mtengo wochepa (wa pa dziko lapansi). Iwo adzalandira malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndithudi, Allah Ngwachangu pakuwerengera

Verse 200 — Surah Al-Imran 3:200

“E inu amene mwakhulupirira! Pirirani, ndipo agonjetseni adani anu ndikupirirako; ndipo tetezani malire anu ndipo muopeni Allah kuti mukhale opambana