Back to Languages

Chichewa - Chapter 31 - Luqman

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Luqman 31:1

Verse 2 — Surah Luqman 31:2

“Izi ndi Ayah za buku lodzadza ndi nzeru

Verse 3 — Surah Luqman 31:3

“(Lomwe ndi) chiongoko ndi chifundo kwa ochita zabwino

Verse 4 — Surah Luqman 31:4

“Amene akupemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat) omwenso akutsimikiza za tsiku lachimaliziro

Verse 5 — Surah Luqman 31:5

“Iwowo ali pa chiongoko chochokera kwa Mbuye wawo; ndipo iwowo ndiwo opambana

Verse 6 — Surah Luqman 31:6

“Koma alipo ena mwa anthu amene akusankha nkhani ya bodza (ndi kumaifotokoza kwa anthu) ndi cholinga choti awasokeretse ku njira ya Allah popanda kuzindikira. Ndipo akuichitira zachipongwe (njira ya Allah yi). Iwo adzapeza chilango chowasambula

Verse 7 — Surah Luqman 31:7

“Ndipo pamene Ayah Zathu zilakatulidwa kwa iye, akuzitembenuzira msana modzikuza ngati kuti sanazimve, ngati kutinso m’makutu mwake muli ugonthi. Choncho muuze nkhani ya chilango chopweteka

Verse 8 — Surah Luqman 31:8

“Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere

Verse 9 — Surah Luqman 31:9

“Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ili nlonjezo la Allah lomwe lili loona. Ndipo Iye Ngwamphamvu, Ngwanzeru zakuya

Verse 10 — Surah Luqman 31:10

“Adalenga thambo popanda mizati yomwe mukuiona. Ndipo adaika mapiri m’nthaka kuti isakugwedezeni. Ndipo (Iye) adafalitsa nyama m’menemo zamitundu yosiyanasiyana. Ndipo tidatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, choncho tidameretsa m’menemo (m’nthaka) mmera wokongola wamitundu yosiyanasiyana

Verse 11 — Surah Luqman 31:11

“Izi (zonse) nzolengedwa za Allah. Choncho, tandisonyezani, nchiyani adalenga amene sali Allah. Koma odzichitira okha zoipa ali mkusokera koonekera

Verse 12 — Surah Luqman 31:12

“Ndipo ndithu tidampatsa Luqmân nzeru (ndipo tidati kwa iye): “Thokoza Allah (pazimene wakupatsa).” Ndipo, amene athokoze, ndithu kuthokozako kumthandiza yekha, ndiponso amene akana (mtendere wa Allah pakusiya kuthokoza), ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa

Verse 13 — Surah Luqman 31:13

“Ndipo (akumbutse) pamene Luqmân adauza mwana wake akumulangiza: “E iwe mwana wanga! Usaphatikize Allah ndi mafano. Ndithu kumuphatikiza (Allah), ndi kuipitsa kwakukulu.”

Verse 14 — Surah Luqman 31:14

“Ndipo tamulangiza munthu kwa makolo ake (kuwachitira zabwino), mayi wake adatenga pathupi pake mofooka pamwamba pakufooka. (Adamuyamwitsa) ndi kumusiyitsa patapita zaka ziwiri, kuti: “Ndithokoze Ine ndi makolo ako, kwa Ine nkobwerera.”

Verse 15 — Surah Luqman 31:15

“Ndipo (makolo ako) ngati atakukakamiza kuti undiphatikize Ine ndi zomwe iwe sukuzidziwa, usawamvere; koma khala nawo pa dziko mwaubwino; ndipo tsatira njira ya amene atembenukira kwa Ine. Ndipo kenako kobwerera kwanu nkwa Ine. Choncho ndidzakuuzani zimene mudali kuchita

Verse 16 — Surah Luqman 31:16

““E iwe mwana wanga! Ndithu icho (chabwino ndi choipa cha munthu) ngakhale chitakhala cholemera ngati njere ya mpiru ndi kukhala mkati mwa thanthwe kapena m’kati mwa thambo, kapena mkati mwa nthaka, Allah adzachibweretsa (ndi kumulipira amene adachita). Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika, (ndiponso) Ngodziwa zinthu zoonekera.”

Verse 17 — Surah Luqman 31:17

““E iwe mwana wanga! Pemphera Swala moyenera, lamula zabwino, letsa zoipa, ndipo pirira ndi masautso amene akukhudza. Ndithu zimenezo ndizinthu zofunika kuziikirapo mtima (munthu aliyense).”

Verse 18 — Surah Luqman 31:18

““Ndipo usatembenuze tsaya lako kwa anthu monyogodola, ndipo usayende pa dziko monyada. Ndithu Allah sakonda yense wodzitukumula, wonyada.”

Verse 19 — Surah Luqman 31:19

““Ndipo lingana m’kuyenda kwako (popanda kufulumira kwambiri kapena kuyenda pang’onopang’ono); ndipo tsitsa mawu ako, ndithu mawu oyipitsitsa ndi mawu a bulu.”

Verse 20 — Surah Luqman 31:20

“Kodi simuona kuti Allah adakugonjetserani zakumwamba ndi zapansi ndi kukukwaniritsirani chisomo Chake, choonekera ndi chobisika? Ndipo alipo ena mwa anthu amene akukangana pa za Allah popanda kuzindikira ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika

Verse 21 — Surah Luqman 31:21

“Ndipo akauzidwa kuti: “Tsatani zimene Allah watsitsa.” Akunena: “Koma tikutsata zimene tidawapeza nazo makolo athu.” Kodi ngakhale kuti satana akuwaitanira ku chilango cha Moto (woyaka, adzatsatirabe)

Verse 22 — Surah Luqman 31:22

“Ndipo amene akupereka nkhope yake kwa Allah (amene akugonjera Allah kwatunthu) ali ochita zabwino, ndiye kuti wagwira chogwilira cholimba. Ndipo mapeto a zinthu zonse nkwa Allah basi

Verse 23 — Surah Luqman 31:23

“Koma amene sadakhulupirire (Allah ndi mtima wake) choncho kusakudandaulitse kusakhulupirira kwake. Kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kumeneko tidzawauza zimene adachita. Ndithu Allah Ngodziwa zonse zam’zifuwa

Verse 24 — Surah Luqman 31:24

“Tikuwasangalatsa pang’ono (apo pa dziko lapansi). Kenako tidzawakankhira ku chilango chokhwima

Verse 25 — Surah Luqman 31:25

“Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kutamandidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sadziwa

Verse 26 — Surah Luqman 31:26

“Zonse zakumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa

Verse 27 — Surah Luqman 31:27

“Ndipo ndithu ngakhale mitengo yonse ili m’nthaka ikadakhala zolembera, ndipo nyanja (nkukhala inki), ndipo pambuyo pake ndikuionjezeranso (madzi ake) ndi nyanja zisanu ndi ziwiri, mawu a Allah sakadatha. Ndithu Allah Ngwamphamvu, Wanzeru zakuya

Verse 28 — Surah Luqman 31:28

“Kulengedwa kwanu, ngakhale kuukitsidwa kwanu m’manda sikuli kanthu koma kuli ngati (kulenga kapena kuukitsa kwa) munthu mmodzi. (Palibe chokanika kwa Allah). Ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya chilichonse

Verse 29 — Surah Luqman 31:29

“Kodi suona (kuona kolingalira) kuti Allah amalowetsa nthawi ya usiku mu usana, ndipo amalowetsa nthawi ya usana mu usiku; ndipo adagonjetsa dzuwa ndi mwezi. Chilichonse chikuyenda mwa nthawi imene idaikidwa? Ndithu Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

Verse 30 — Surah Luqman 31:30

“Izi nchifukwa chakuti Allah, Iye Ngoona; ndipo zomwe akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo ndithu Allah ndiye Wotukuka, Wamkulu

Verse 31 — Surah Luqman 31:31

“Kodi suona kuti zombo zikuyenda pa nyanja mwachisomo cha Allah kuti akusonyezeni zisonyezo Zake (zamtendere Wake)? Ndithu M’zimenezo muli zisonyezo kwa yense wopirira, wothokoza

Verse 32 — Surah Luqman 31:32

“Ndipo mafunde onga mitambo akawavindikira, amampempha Allah modzipereka kwambiri. Koma akawapulumutsira ku ntunda, ena a iwo amachita zolungama (koma ena a iwo amakana mtendere wa Allah). Ndipo sangazikane zisonyezo zathu koma yense wachinyengo wosathokoza

Verse 33 — Surah Luqman 31:33

“E inu anthu! Muopeni Mbuye wanu (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa); ndipo liopeni tsiku limene kholo silidzathandiza mwana wake, ngakhalenso mwana sadzathandiza kholo lake chilichonse. Ndithu lonjezo la Allah ndiloona; choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ndiponso asakunyengeni mdyerekezi pa za Allah

Verse 34 — Surah Luqman 31:34

“Ndithu kudziwa kwa nthawi (yakutha kwa dziko) kuli ndi Allah (Yekha). Iye ndiamene amavumbitsa mvula (nthawi imene wafuna); ndipo akudziwa zimene zili m’ziberekero. Ndipo aliyense sadziwa chomwe apeze mawa; (chabwino kapena choipa); ndiponso sadziwa aliyense kuti ndi dziko liti adzafera. Ndithu Allah Ngodziwa zedi, Ngozindikira kwambiri