Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 32 - As-Sajdah
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah As-Sajdah 32:1
“Alif-Lâm-Mîm
Verse 2 — Surah As-Sajdah 32:2
“Chivumbulutso cha buku (la Qur’an) chilibe chikaiko mkati mwake chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa
Verse 3 — Surah As-Sajdah 32:3
“Kapena akunena kuti: “Walipeka yekha (bukulo)?” Iyayi, ichi nchoona chimene chachokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu ndi chimenechi, amene sadawadzere mchenjezi iwe usadadze. Kuti aongoke (ndi kutsatira njira yolungama)
Verse 4 — Surah As-Sajdah 32:4
“Allah ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu); (kukhazikika kolingana ndi ulemelero Wake, kumene Iye Mwini wake akukudziwa). Inu mulibe mtetezi ngakhale muomboli kupatula Iye. Nanga kodi bwanji simulingalira
Verse 5 — Surah As-Sajdah 32:5
“(Iye) akuyendetsa zinthu (zonse) kuchokera kumwamba kupita pansi. Kenako zidzakwera kubwerera kwa Iye, pa tsiku lolingana ndi zaka chikwi chimodzi (poyerekeza ndi zaka zadziko lapansi) mzomwe inu mumawerengera
Verse 6 — Surah As-Sajdah 32:6
“Ameneyo (ndi Allah), Wodziwa zobisika ndi zoonekera; Mwini mphamvu zoposa Wachisoni chosatha
Verse 7 — Surah As-Sajdah 32:7
“Yemwe adakonza bwino chilichonse (chomwe) adalenga. Ndipo adayambitsa chilengedwe cha munthu (Adam) kuchokera ku dongo
Verse 8 — Surah As-Sajdah 32:8
“Kenako adachita mbumba yake kuti ipangike kuchokera m’madzi enieni onyozeka
Verse 9 — Surah As-Sajdah 32:9
“Kenako adamkonza ndi kuuziramo mzimu Wake. Ndipo adakuikirani kumva, kupenya ndi mitima. Kuthokoza kwanu mpang’ono ndithu
Verse 10 — Surah As-Sajdah 32:10
“Ndipo (otsutsa kuuka ku imfa) akunena: “Kodi tikadzatayika m’nthaka (ndi kusakanikirana ndi dothi), tidzakhalanso mkalengedwe katsopano?” (Iyayi), koma iwo sakhulupirira za kukumana ndi Mbuye wawo
Verse 11 — Surah As-Sajdah 32:11
“Nena: “Adzachotsa mizimu yanu Mngelo wa imfa yemwe wapatsidwa udindo umenewu pa inu. Kenako mudzabwerera kwa Mbuye wanu.”
Verse 12 — Surah As-Sajdah 32:12
“Ndipo ukadawaona oipa atazolikitsa mitu yawo kwa Mbuye wawo (uku akunena): “E Mbuye wathu! Taona, ndipo tamva. Choncho tibwezeni tikachita ntchito zabwino. Ndithu tsopano tatsimikiza (kukhulupirira).”
Verse 13 — Surah As-Sajdah 32:13
“Ndipo tikadafuna, tikadaupatsa mzimu ulionse chiongoko chake (moukakamiza monga momwe tidawachitira angelo, koma mzimu udapatsidwa mphamvu ndi ufulu wodzisankhira chimene ufuna; chabwino kapena choipa). Koma mawu atsimikizika ochokera kwa Ine: “Ndithu ndizadzazitsa Jahannam ziwanda ndi anthu; onse pamodzi (amene ali oipa).”
Verse 14 — Surah As-Sajdah 32:14
““Choncho, lawani chifukwa cha kuyiwala (kusalabadila) kwanu kukumana ndi tsiku lanu ili. Ifenso tikusiyani (ku chilango monga ngati takuiwalani). Tero lawani chilango chamuyaya, chifukwa cha zomwe munkachita.”
Verse 15 — Surah As-Sajdah 32:15
“Ndithu amene akukhulupirira Ayah Zathu, ndiamene akuti pamene akukumbutsidwa ndi Ayazo, amagwetsa nkhope zawo pansi (kusujudu) ndi kulemekeza Mbuye wawo pamodzi ndi kumthokoza. Ndipo iwo sadzitukumula
Verse 16 — Surah As-Sajdah 32:16
“Nthiti zawo zimalekana ndi malo ogona (usiku), uku akumpempha Mbuye wawo, moopa ndi mwachiyembekezo. Ndipo amapereka (Zakaat ndi sadaka) mzimene tawapatsa
Verse 17 — Surah As-Sajdah 32:17
“Mzimu uliwonse sudziwa zimene aubisira zotonthoza diso (zosangalatsa moyo ku Munda wa mtendere) monga mphoto pa zimene unkachita
Verse 18 — Surah As-Sajdah 32:18
“Kodi yemwe ali okhulupirira angafanane ndi wotuluka m’chilamulo cha Allah? Sangafanane
Verse 19 — Surah As-Sajdah 32:19
“Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzalandira Minda yokhalamo yokongola, monga phwando lawo pa zimene ankachita
Verse 20 — Surah As-Sajdah 32:20
“Koma kwa amene adachita zoipa potuluka m’chilamulo cha Allah, malo awo ndi ku Moto. Nthawi iliyonse akafuna kutulukamo, azikabwezedwamo ndipo azidzauzidwa: “Lawani chilango cha Moto, chomwe munkachitsutsa.”
Verse 21 — Surah As-Sajdah 32:21
“Ndipo ndithudi, tiwalawitsa chilango chocheperapo (pa dziko lapansi) chisanafike chilango chachikulu (cha tsiku lachimaliziro), kuti atembenuke, (alape)
Verse 22 — Surah As-Sajdah 32:22
“Kodi ndani wachinyengo kwambiri, woposa yemwe akukumbutsidwa Ayah za Mbuye wake, kenako nkuzikana? Ndithu Ife, tidzawabwezera zoipa anthu oipa
Verse 23 — Surah As-Sajdah 32:23
“Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Choncho usakhale ndi chikaiko pa zakukumana Naye (Allah). Ndipo tidalichita (bukulo) kukhala chiongoko cha ana a Israyeli
Verse 24 — Surah As-Sajdah 32:24
“Ndipo ena mwa iwo tidawachita kukhala atsogoleri oongola (anthu) mwa lamulo lathu, pamene adapirira; ndipo adali kuvomereza motsimikiza Ayah Zathu
Verse 25 — Surah As-Sajdah 32:25
“Ndithudi Mbuye wako ndi Yemwe adzaweruze pakati pawo tsiku la Qiyâma pazimene amatsutsana
Verse 26 — Surah As-Sajdah 32:26
“Kodi sizidadziwike kwa iwo kuti ndimibadwo ingati imene tidaiononga patsogolo pawo; (chikhalirecho iwo) akudutsa mokhala mwawo? Ndithu m’zimenezo, muli zizindikiro, kodi sakumva
Verse 27 — Surah As-Sajdah 32:27
“Kodi sakuona kuti timapereka madzi ku nthaka youma; ndipo ndi madziwo tikumeretsa mrnera umene ziweto zawo zimadya ndi iwo omwe; kodi sakupenya
Verse 28 — Surah As-Sajdah 32:28
“Ndipo akunena: “Kulamulidwa kumeneku (kwa tsiku la chimaliziro) kudzachitika liti, ngati mukunenadi zoona?”
Verse 29 — Surah As-Sajdah 32:29
“Nena: “Tsiku la chiweruzirolo, amene sadakhulupirire, chikhulupiriro chawo sichidzawathandiza. Ndipo sadzapatsidwa nthawi yoyembekezera (kuti mizimu yawo isachoke ayambe akhulupirira kaye, mngero wa imfa akadzawadzera).”
Verse 30 — Surah As-Sajdah 32:30
“Choncho apatuke; ndipo yembekezera (zimene Allah wakulonjeza). Ndithu nawonso akuyembekezera (zimene Allah wawalonjeza)