Back to Languages

Chichewa - Chapter 33 - Al-Ahzab

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Ahzab 33:1

“E iwe Mneneri! Muope Allah, ndipo usamvere osakhulupirira ndi achiphamaso. Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri; Wanzeru zakuya (m’zoyankhula ndi m’zochita Zake)

Verse 2 — Surah Al-Ahzab 33:2

“Ndipo tsata zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako (pozigwiritsa ntchito). Ndithu Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita

Verse 3 — Surah Al-Ahzab 33:3

“Ndipo yadzamira kwa Allah; ndipo Allah akukwana kukhala Msungi ndi Mtetezi (wako)

Verse 4 — Surah Al-Ahzab 33:4

“Allah sadaike m’chifuwa cha munthu mitima iwiri. Ndipo sadachite akazi anu amene mukuwayesa ena mwa iwo monga amayi anu, kukhala mayi anu enieni. Ndipo sadachite ana anu ongowalera kukhala ana anu enieni (monga inu mukuwatchulira). Zimenezo ndi zolankhula zanu za pakamwa panu chabe. Koma Allah akunena choona; Iye akuongolera ku njira yoongoka

Verse 5 — Surah Al-Ahzab 33:5

“Aitaneni ndi maina a atate awo. Kutero ndichilungamo kwa Allah. Koma ngati simukuwadziwa atate awo, (aitaneni ngati) ndiabale anu pachipembedzo; ndiponso ndi anzanu. Palibe uchimo kwa inu pa zimene mwazichita molakwitsa (mosazindikira). Koma (pali uchimo) pa zimene mitima yanu yachita mwadala. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

Verse 6 — Surah Al-Ahzab 33:6

“Mneneri ngofunika kwambiri kwa okhulupirira kuposa moyo wawo, (matupi awo ndi chuma chawo); ndipo akazi ake ndi amayi awo (amayi a Asilamu; nkoletsedwa kuwakwatira pambuyo pa imfa yake). Ndipo achibale pakati pawo ngoyenera (kulandira zamasiye pamalamulo a) m’buku la Allah kuposa Asilamu ena ngakhalenso Amuhajirina (amene adasamuka ku Makka kupita ku Madina chifukwa cha chipembedzo cha Chisilamu). Kupatula ngati mutachita zabwino kwa anzanu (sikolakwika). Izi zidalembedwa kale m’buku

Verse 7 — Surah Al-Ahzab 33:7

“Ndipo (akumbutse) pamene tidalandira kuchokera kwa Aneneri onse pangano lawo. Ndi kwa iwe, ndi kwa Nuh, Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Ndipo tidatenga kwa iwo pangano lamphamvu (kuti adzafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu ndi kuitanira anthu ku chipembedzo cha Allah)

Verse 8 — Surah Al-Ahzab 33:8

“Kuti (Allah) adzafunse owona (aneneri) (tsiku la chimaliziro) pa zimene adanena (kwa anthu awo zakufikitsa uthenga woonadi kwa iwo). Ndipo Allah wawakonzera (osakhulupirira) chilango chopweteka

Verse 9 — Surah Al-Ahzab 33:9

“E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani chisomo cha Allah chimene chili pa inu, pamene adakudzerani magulu a nkhondo. Ndipo tidawatumizira mphepo ndi magulu a nkhondo (a angelo) amene simudawaone. Ndipo Allah akuona (zonse) zimene mukuchita

Verse 10 — Surah Al-Ahzab 33:10

“Pamene adakudzerani cha kumtunda kwanu, ndi kunsi kwanu (kumtunda kwa dambo ndi kumunsi kwake), pamene maso adangoti tong’oo chammbali ndipo mitima idafika kum’mero (chifukwa cha mantha ndi kunjenjemera) uku mukumganizira Allah maganizo osiyanasiyana

Verse 11 — Surah Al-Ahzab 33:11

“Panthawi imeneyo okhulupirira adayesedwa mayeso aakulu. Adanjenjemeretsedwa kunjenjemera kwambiri

Verse 12 — Surah Al-Ahzab 33:12

“Ndipo pamene ankanena achiphamaso (achinyengo) ndi omwe m’mitima mwawo muli matenda: “Palibe chomwe adatilonjeza Allah ndi Mtumiki Wake koma chinyengo basi.”

Verse 13 — Surah Al-Ahzab 33:13

“Ndipo pamene gulu lina mwa iwo lidanena: “E inu nzika za mu Yathiriba (Madina)! Palibe njira kwa inu yokhalira (pa nkhondo yogonjayi). Choncho bwererani (ku nyumba zanu; msiyeni Muhammad alimbane yekha ndi adani ake).” Ndipo gulu lina la nkhondo lochokera mwa iwo limapempha chilolezo kwa Mneneri (s.a.w) ( chobwelera ku Madina) ponena (kuti): “Ndithu nyumba zathu nzamaliseche (zopanda chitetezo).” Koma izo sizamaliseche. Sakufuna china, koma kuthawa basi

Verse 14 — Surah Al-Ahzab 33:14

“Ndipo akadawalowera (magulu ankhondo a adaniwo), mbali zonse (za Mzindawo), kenako nkupemphedwa kuti atuluke m’Chisilamu ndi kumenyana ndi Asilamu, akadachita zimenezo; ndipo sakadayembekezera koma nthawi yochepa basi

Verse 15 — Surah Al-Ahzab 33:15

“Ndipo ndithu (awa amene adathawa pabwalo la nkhondo), adali atamulonjeza kale Allah (kuti iwo) sadzatembenuza misana (kuthawa). Ndipo lonjezo la Allah nlofunsidwa. (Choncho iwo adzafunsidwa pa zomwe adalonjeza kwa Allah)

Verse 16 — Surah Al-Ahzab 33:16

“Nena: “Kuthawa sikungakuthandizeni ngati mukuthawa imfa kapena kuphedwa; choncho (kuthawa kwanuku) simusangalatsidwa (nako) koma pang’ono basi. (Kenako ikatha nthawi ya moyo wanu, mukufa).”

Verse 17 — Surah Al-Ahzab 33:17

“Nena: “Kodi ndani amene angakutetezeni kwa Allah, ngati atafuna kukuchitirani choipa; kapena atafuna kukuchitirani chifundo?” Ndipo sadzapeza mthandizi ndi mtetezi kupatula Allah

Verse 18 — Surah Al-Ahzab 33:18

“Ndithu Allah akuwadziwa amene akudziletsa mwa inu (kupita ku nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) ndi kuletsanso anthu ena), ndi amene akuuza abale awo: “Bwerani kwa ife; (m’thaweni Muhammad {s.a.w}).” Ndiponso sapita ku nkhondo koma pang’ono pokha

Verse 19 — Surah Al-Ahzab 33:19

“Okuchitirani inu umbombo (pa chikondi ndi pa chifundo; sakufunirani zabwino). Koma mantha akadza uwaona akukuyang’ana, uku maso awo akutembenuka (mophethiraphethira) monga a amene wakomoledwa ndi imfa. Koma mantha akachoka, akukupatsani masautso ndi malirime awo akuthwa; mbombo pa chabwino chilichonse. Iwowo sadakhulupirire ndipo choncho Allah wagwetsa malipiro a zochita zawo. Zimenezo nzosavuta kwa Allah

Verse 20 — Surah Al-Ahzab 33:20

“(Kufikira tsopano chifukwa cha mantha awo) akuganiza kuti magulu a nkhondo (adani) sadapitebe; ndipo magulu amenewo akadadzanso, akadalakalaka akadakhala kuchipululu pamodzi ndi arabu a kuchimidzi ndi kuti azikangofunsa za nkhani zanu. Akadakhala pamodzi ndi inu sadakamenyana (ndi adani) koma pang’ono pokha

Verse 21 — Surah Al-Ahzab 33:21

“Ndithu muli nacho chitsanzo chabwino mwa Mthenga wa Allah (m’kudzipereka kwake ndi khama lake pa njira ya Allah, ndi kupirira kwake ndi masautso) kwa yemwe akuopa Allah ndi tsiku lachimaliziro, namatchula Allah kwambiri

Verse 22 — Surah Al-Ahzab 33:22

“Ndipo pamene okhulupirira adaona magulu a nkhondo (a adani atawazinga mbali zonse), adati: “Ichi ndichimene Allah ndi Mtumiki Wake adatilonjeza (kuti tidzapeza masautso, kenako nkupambana), ndipo Allah ndi Mtumiki Wake adanena zoona.” Ndipo (ichi) sichidawaonjezere china, koma chikhulupiliro (mwa Allah) ndi kudzipereka

Verse 23 — Surah Al-Ahzab 33:23

“Mwa okhulupirira alipo amuna ena amene adakwaniritsa zomwe adamlonjeza Allah (kuti sadzathawa pa nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w), ena mwa iwo adamaliza moyo wawo (nakwaniritsa lonjezo lawo pofera pa njira ya Allah). Ndipo ena mwa iwo akuyembekezerabe (kufera pa njira ya Allah). Ndipo sadasinthe konse (lonjezo lawo)

Verse 24 — Surah Al-Ahzab 33:24

“Kuti Allah awalipire owona chifukwa cha kuona kwawo; ndi kuti awalange achiphamaso ngati atafuna, kapena kuwalandira kulapa kwawo (ngati atalapa). Ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha

Verse 25 — Surah Al-Ahzab 33:25

“Ndipo Allah adawabweza amene sadakhulupirire uku ali odzazidwa ndi mkwiyo m’mitima mwawo; sadapeze chabwino; (sadagonjetse Asilamu ndi kupeza zimene ankaziyembekezera monga zotola za pa nkhondo). Ndipo Allah adawakwaniritsira okhulupirira nkhondo (powatumizira adani mphepo yamkuntho ndi angelo). Ndipo, Allah Ngwamphamvu, Ngopambana, (sapambanidwa ndi chilichonse)

Verse 26 — Surah Al-Ahzab 33:26

“Ndipo adawatsitsa m’malinga mwawo amene adathandiza adaniwo mwa anthu a buku (Ayuda). Ndipo adathira mantha m’mitima mwawo. Ena mumawapha; ndipo ena mumawagwira

Verse 27 — Surah Al-Ahzab 33:27

“Ndipo adakupatsani dziko lawo, nyumba zawo, chuma chawo, ndi nthaka imene simudaipondepo. Allah Ngokhoza chilichonse

Verse 28 — Surah Al-Ahzab 33:28

“E iwe Mneneri! Nena kwa akazi ako (m’njira yowalangiza): “Ngati mufuna moyo wa dziko lapansi ndi zosangalatsa zake (ine ndilibe zosangalatsa za m’dziko, ndipo sindingakukakamizeni kuti mukhale ndi ine mu moyo wa umphawi; ngati mufuna) bwerani ndikupatsani cholekanira, chokusangalatsani, kenako ndikusiyeni kusiyana kwabwino (kopanda masautso).”

Verse 29 — Surah Al-Ahzab 33:29

““Ndipo ngati mukufuna Allah ndi Mtumiki Wake, ndi nyumba yomaliza, ndithu Allah wawakonzera ochita zabwino mwa inu malipiro aakulu.”

Verse 30 — Surah Al-Ahzab 33:30

“E inu akazi a Mneneri! Amene achite choipa choonekera mwa inu, amuonjezera chilango kawiri; ndipo zimenezi nzosavuta kwa Allah

Verse 31 — Surah Al-Ahzab 33:31

“۞ Koma yense mwa inu amene amvere Allah ndi Mneneri Wake, ndi kumachita zabwino, timpatsa malipiro ake kawiri ndi kumkonzera rizq laulemu

Verse 32 — Surah Al-Ahzab 33:32

“E inu akazi a Mneneri! Inu simuli monga mmodzi wa akazi ena (omwe siakazi a Mtumiki, paulemelero) ngati muopa Allah. Choncho musalobodole mawu (mowakometsa poyankhulana ndi amuna,) kuti asalakelake (kuchita zoipa ndi inu) yemwe mu mtima mwake muli matenda (achiwerewere). Koma nenani zonena zabwino

Verse 33 — Surah Al-Ahzab 33:33

“Ndipo khalani mnyumba zanu, ndipo musadzionetsere (kwa amuna) uku mutadzikongoletsa monga mmene ankaonetsera zokongoletsa zawo (akazi) a m’nthawi ya umbuli wakale. Ndipo pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat, mverani Allah ndi Mtumiki Wake. Ndithu Allah akufuna kukuchotserani uve e, inu a kunyumba (ya Mneneri)! Ndi kuti akuyeretseni ndithu

Verse 34 — Surah Al-Ahzab 33:34

“Ndipo lowezani pamtima zimene zikunenedwa m’nyumba zanu; ndime za mawu a Allah ndi (zonena za Mtumiki) zanzeru. Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika kwambiri, ndi zapoyera

Verse 35 — Surah Al-Ahzab 33:35

“Ndithu Asilamu achimuna ndi Asilamu achikazi; okhulupirira achimuna ndi okhulupirira achikazi; omvera achimuna ndi omvera achikazi; owona achimuna ndi owona achikazi; opirira achimuna ndi opirira achikazi; odzichepetsa achimuna ndi odzichepetsa achikazi; opereka sadaka achimuna ndi opereka sadaka achikazi; osala achimuna ndi osala achikazi; osunga umaliseche wawo (kuchiwerewere) achimuna ndi osunga umaliseche wawo achikazi; otamanda Allah kwambiri achimuna ndi otamanda Allah kwambiri achikazi, Allah wawakonzera chikhululuko ndi malipiro aakulu

Verse 36 — Surah Al-Ahzab 33:36

“Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira wachimuna ndi wokhulupirira wachikazi, Allah ndi Mtumiki Wake akalamula chinthu, iwo nkukhala ndi chisankho pa zinthu zawo. Ndipo amene akunyoza Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu wasokera; kusokera koonekera

Verse 37 — Surah Al-Ahzab 33:37

“Ndipo (kumbuka) pamene udamuuza yemwe Allah adampatsa mtendere (pomuongolera ku Chisilamu, ndipo) iwenso udampatsa mtendere (pomulera ndi kumpatsa ufulu, yemwe ndi Zaid Bun Haritha, udati kwa iye): “Gwirizana ndi mkazi wako, ndipo wopa Allah.” Ukubisa mu mtima mwako chimene Allah afuna kuchisonyeza poyera (chomwe ndi kuti Allah akulamula kumkwatira mkazi ameneyo akamuleka Zaid Bun Haritha kuti chichoke chizolowezi choti mwana wongomulera chabe nkumuyesa mwana wako weniweni). Ndipo ukuopa anthu (kuti akudzudzula pa zimenezo), pomwe woyenera kumuopa ndi Allah. Choncho pamene Zaid adamaliza chilakolako chake pa mkazi ameneyo, tidakukwatitsa iwe kuti pasakhale masautso pa okhulupirira pokwatira akazi a ana awo akungowalera chabe ngati (anawo) atamaliza zilakolako zawo pa akaziwo, ndipo lamulo la Allah ndilochitika, (palibe chingalepheretse kuti lisachitike)

Verse 38 — Surah Al-Ahzab 33:38

“Palibe tchimo pa Mneneri pa zimene Allah wamulamula. Chimenechi ndichizolowezi cha Allah (njira ya Allah) pa amene adanka kale. Ndipo lamulo la Allah ndi chikonzero (chomwe) chidakonzedwa. (Ndipo sichisinthidwa)

Verse 39 — Surah Al-Ahzab 33:39

“(Aneneri) amene amafikitsa uthenga wa Allah (kwa anthu) uku akumuopa Iye, ndipo samamuopa aliyense koma Allah (yekha). Ndipo Allah Akukwana kukhala wowerengera (zochita za akapolo Ake)

Verse 40 — Surah Al-Ahzab 33:40

“Muhammad (s.a.w) sali tate wa aliyense mwa amuna anu, koma iye ndi Mtumiki wa Allah, ndiponso wotsiriza mwa Aneneri. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

Verse 41 — Surah Al-Ahzab 33:41

“E inu amene mwakhulupirira! Mkumbukireni Allah; kumkumbukira kwambiri

Verse 42 — Surah Al-Ahzab 33:42

“Ndipo mulemekezeni m’mawa ndi madzulo

Verse 43 — Surah Al-Ahzab 33:43

“Iye ndi Amene akukuchitirani chifundo (ndi kukufunirani zabwino) nawonso Angelo Ake (akukupemphelerani kwa Allah) kuti akutulutseni mu mdima ndi kukuikani m’kuunika. Ndipo (Iye) Ngwachisoni zedi kwa okhulupirira

Verse 44 — Surah Al-Ahzab 33:44

“Kulonjerana kwawo tsiku lokumana Naye, kudzakhala koti: “Mtendere!” Ndipo wawakonzera malipiro a ulemu

Verse 45 — Surah Al-Ahzab 33:45

“E iwe Mneneri (wa Allah)! Ndithu Ife takutuma (kuti ukhale) mboni (pa anthu ako ndi pa mibadwo yonse). Wonena nkhani zabwino (kwa oopa Allah), ndi mchenjezi (kwa onyoza Allah)

Verse 46 — Surah Al-Ahzab 33:46

“Ndi kuti ukhale woitanira (anthu) kwa Allah kupyolera m’chifuniro Chake. Ndi (kutinso ukhale) nyali younikira (anthu)

Verse 47 — Surah Al-Ahzab 33:47

“Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira kuti iwo ali ndi zabwino zazikulu kwa Allah

Verse 48 — Surah Al-Ahzab 33:48

“Ndipo usawamvere osakhulupirira ndi achiphamaso (pa zimene akufuna kuti uwapeputsire malamulo a Allah), usalabadire masautso awo, ndipo tsamira kwa Allah. Ndipo Allah akukwanira kukhala Mtetezi

Verse 49 — Surah Al-Ahzab 33:49

“E inu amene mwakhulupirira! Mukakwatira akazi okhulupirira, kenako ndikulekana nawo musadawakhudze, inu mulibe chiwerengero cha ‘Edda’ pa iwo choti nkuchiwerengera. Asangalatseni powapatsa cholekanira. siyananawoni; kusiyana kwabwino

Verse 50 — Surah Al-Ahzab 33:50

“E iwe Mneneri! Ndithu Ife takuloleza (kukhala nawo pamodzi) akazi ako amene wawapatsa chiwongo chawo, ndi chimene dzanja lako lamanja lapeza (omwe ndi akazi ogwidwa pa nkhondo) chomwe Allah wakupatsa, ndi ana achikazi a m’bale wa atate ako, ndi ana achikazi a mlongo wa atate ako, ndi ana achikazi a atsibweni ako, ndi ana achikazi a m’bale wa mayi ako amene adasamuka pamodzi ndi iwe, ndi mkazi wokhulupirira atadzipereka yekha kwa Mneneri ngati Mneneri akufuna kumkwatira, chilolezo ichi ncha iwe wekha, osati okhulupirira onse. Ndithu tikudziwa malamulo amene tawakhazikitsa kwa iwo pa akazi awo, ndi chimene manja awo akumanja apeza; (takuchitira zimenezi iwe wekha Mneneri Muhammad {s.a.w}) kuti pasakhale masautso pa iwe (ngati ukufuna kukwatira mkazi wina chifukwa chofalitsa chipembedzo) ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni chosatha

Verse 51 — Surah Al-Ahzab 33:51

“Ukhoza kumchedwetsa (posagona m’nyumba mwake) amene wam’funa pakati pa iwo ndi kumuyandikitsa kwa iwe amene wam’funa. Ndipo amene wam’funa mwa amene udawapatuka, palibe tchimo pa iwe. Kuchita izi kuchititsa kuti maso awo atonthole (mitima yawo ikondwe) ndipo asadandaule; ndi kuyanjana nacho chimene wawapatsa onse. Ndipo Allah akudziwa zimene zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Ngoleza, (salanga mwachangu)

Verse 52 — Surah Al-Ahzab 33:52

“Pambuyo (pa akazi awa amene uli nawo) nkosaloledwa kwa iwe kukwatira akazi ena, (poonjezera pa chiwerengero cha akazi amene uli nawo). Ndiponso usasinthe (ofanana ndi chiwerengero chawo), (zonsezi nzoletsedwa kwa iwe) ngakhale kuti ubwino wawo utakusangalatsa, kupatula chimene dzanja lako lakumanja lapeza; ndipo Allah ndi M’yang’aniri wa chinthu chilichonse

Verse 53 — Surah Al-Ahzab 33:53

“E inu amene mwakhulupirira! Musalowe m’nyumba za Mneneri pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kukadya, osati kukhala nkuyembekezera kupsa kwa chakudya. Koma mukaitanidwa, lowani. Ndipo mukamaliza kudya, balalikani; ndiponso musakambe nkhani zocheza. Chifukwa kutero kumavutitsa Mneneri. Ndipo iye amakuchitirani manyazi (kuti akutulutseni); koma Allah alibe manyazi ponena choona. Ndipo inu mukamawafunsa (akazi ake) za ziwiya, afunseni uku muli kuseri kwa Chotsekereza. Zimenezo ndi zoyera zedi ku mitima yanu ndi mitima yawo. Sikoyenera kwa inu kumvutitsa Mtumiki wa Allah, ndiponso nkosayenera kwa inu kukwatira akazi ake pambuyo pa imfa yake mpaka muyaya. Ndithu kutero ndi tchimo lalikulu kwa Allah

Verse 54 — Surah Al-Ahzab 33:54

“Chilichonse chimene mungachionetse kapena kuchibisa Allah achidziwa. Ndithu chifukwa chakuti Allah Ngodziwa chilichonse

Verse 55 — Surah Al-Ahzab 33:55

“Palibe tchimo pa iwo (akazi) kuonana ndi atate awo ngakhale ana awo, alongo awo, ana amuna alongo awo, ana a amuna a abale awo, akazi anzawo, ndi amene manja awo akumanja apeza. Ndipo opani Allah (inu akazi). Ndithu Allah ndimboni pa chilichonse

Verse 56 — Surah Al-Ahzab 33:56

“Ndithu Allah akumtsitsira madalitso Mneneri; nawonso angelo Ake (akumpemphelera chifukwa cha zochita zake zabwino). E inu amene mwakhulupirira! Mpemphereni madalitso ndi kumpemphera mtendere (chifukwa chokusonyezani njira yolungama)

Verse 57 — Surah Al-Ahzab 33:57

“Ndithu amene akumukwiyitsa Allah ndi kumuvutitsa Mtumiki Wake (ponyozera malamulo ake) Allah wawatembelera pa dziko lapansi (mpaka) pa tsiku la chimaliziro, ndipo wawakonzera chilango chosambula

Verse 58 — Surah Al-Ahzab 33:58

“Ndipo amene akuvutitsa okhulupirira aamuna ndi okhulupirira aakazi popanda kuchimwa kulikonse, ndithu asenza chinyengo ndi tchimo loonekera

Verse 59 — Surah Al-Ahzab 33:59

“E iwe Mneneri! Uza akazi ako, ndi ana ako aakazi, ndi akazi a okhulupirira, kuti adziphimbe ndi nsalu zawo (akamatuluka m’nyumba), kutero kuchititsa kuti adziwike, asazunzidwe (ndi anthu achipongwe). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni

Verse 60 — Surah Al-Ahzab 33:60

“Ngati sasiya (machitidwe awo oipa) achiphamaso (achinyengo), ndi amene m’mitima mwawo muli matenda (a chiwerewere), ndi ofalitsa mbiri zoipa mu mzinda, tikukhwirizira kwa iwo (kuti uwathire nkhondo). Kenako sadzakhala m’menemo pamodzi ndi iwe, koma nthawi yochepa

Verse 61 — Surah Al-Ahzab 33:61

“(Iwo) ngotembeleredwa; paliponse pamene apezeke, agwidwe ndi kuphedwa ndithu

Verse 62 — Surah Al-Ahzab 33:62

“(Awa ndi) machitidwe a Allah omwe adalipo pa omwe adamka kale. sungapeze kusintha pa machitidwe a Allah

Verse 63 — Surah Al-Ahzab 33:63

“Anthu akukufunsa za (kudza kwa) nthawi (ya tsiku la chitsiriziro). Nena: “Kuzindikira kwa nthawiyo kuli ndi Allah (Yekha). Nanga nchiyani chikudziwitse kuti nthawi ya chimaliziro iri pafupi?”

Verse 64 — Surah Al-Ahzab 33:64

“Ndithu Allah wawatembelera osakhulupirira ndi kuwakonzera Moto woyaka kwambiri

Verse 65 — Surah Al-Ahzab 33:65

“Adzakhala nrmenemo nthawi yaitali. Sadzapeza bwenzi ngakhale mthandizi

Verse 66 — Surah Al-Ahzab 33:66

“Tsiku limene nkhope zawo zikatembenuzidwa ku Moto (zikutenthedwa), uku akunena: “Kalanga ife! Tikadamumvera Allah ndi kumveranso Mtumiki (s.a.w), (sibwenzi tili m’chilangomu).”

Verse 67 — Surah Al-Ahzab 33:67

“Ndipo adzanena: “E Mbuye wathu! Ndithu ife tidamvera olemekezeka athu ndi akuluakulu athu, choncho adatisokeza njira.”

Verse 68 — Surah Al-Ahzab 33:68

“Mbuye wathu! Apatseni chilango pamwamba pa chilango ndipo atembelereni, kutembelera kwakukulu.”

Verse 69 — Surah Al-Ahzab 33:69

“E inu amene mwakhulupirira! Musakhale monga amene adamvutitsa Mûsa; koma Allah adamuyeretsa kuzimene ankamnenera. Ndipo iye kwa Allah adali wolemekezeka

Verse 70 — Surah Al-Ahzab 33:70

“E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah (pokwaniritsa malamulo Ake, ndi kusiya zoletsedwa), ndipo nenani mawu olungama

Verse 71 — Surah Al-Ahzab 33:71

“Akukonzerani bwino zochita zanu ndi kukukhululukirani machimo anu. ndipo amene akumvera Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu apambana; kupambana kwakukulu

Verse 72 — Surah Al-Ahzab 33:72

“Ndithu Ife tidapereka udindo (otsatira malamulo) ku thambo ndi nthaka ndi mapiri; koma zidakana kuwusenza (udindowo); ndipo zidauopa. Koma munthu adawusenza; ndithu iye ngwachinyengo kwambiri ndiponso mbuli

Verse 73 — Surah Al-Ahzab 33:73

“Kuti Allah adzawalange achiphamaso aamuna ndi aakazi, ndi opembedza mafano achimuna ndi achikazi ndi kuti adzawakhululukire okhulupirira achimuna ndi achikazi. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha