Back to Languages

Chichewa - Chapter 36 - Ya-Sin

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Ya-Sin 36:1

Verse 2 — Surah Ya-Sin 36:2

“Ndikulumbira Qur’an (iyi yomwe yakonzedwa mwaluso) yodzazidwa ndi mawu anzeru

Verse 3 — Surah Ya-Sin 36:3

“Ndithu iwe (Muhammad {s.a.w}) ndimmodzi wa atumiki (amene Allah adawatuma kwa anthu kuti akawasonyeze chiongoko)

Verse 4 — Surah Ya-Sin 36:4

“(Uli) panjira yolunjika

Verse 5 — Surah Ya-Sin 36:5

“(Qur’an iyi) nchivumbulutso cha Mwini Mphamvu zoposa; (palibe chokanika kwa Iye) Wachisoni chosatha

Verse 6 — Surah Ya-Sin 36:6

“Kuti uwachenjeze anthu omwe makolo awo sadachenjezedwe; choncho iwo ngoiwala (zomwe zili zofunika kuchitira Allah ndi kudzichitira okha pamodzi ndi anthu ena)

Verse 7 — Surah Ya-Sin 36:7

“Ndithu mawu (onena za chilango) atsimikizika pa ambiri a iwo; poti iwo sakhulupirira

Verse 8 — Surah Ya-Sin 36:8

“Ndithu Ife taika magoli m’makosi mwawo ofika kuzibwano, kotero kuti mitu yawo yayang’ana mmwamba; (siingathe kutembenuka ndi kuyang’ana)

Verse 9 — Surah Ya-Sin 36:9

“Ndipo tawaikira chotsekereza patsogolo pawo ndi chotsekereza pambuyo pawo, ndipo (maso awo) tawaphimba, tero iwo saona (zapatsogolo ndi pambuyo pawo)

Verse 10 — Surah Ya-Sin 36:10

“Ndipo kwa iwo nchimodzimodzi, uwachenjeze ngakhale usawachenjeze sangakhulupirire

Verse 11 — Surah Ya-Sin 36:11

“Ndithu kuchenjeza kwako kupindulira amene watsatira Qur’an ndi kumuopa (Allah) Wachifundo chambiri ngakhale sakumuona. Wotere muuze nkhani yabwino ya chikhululuko (chochokera kwa Allah pa machimo ake) ndi malipiro aulemu

Verse 12 — Surah Ya-Sin 36:12

“Ndithu Ife tidzaukitsa akufa, ndipo tikulemba zimene atsogoza (m’dziko lapansi m’zochita zawo) ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, zonkerankera mtsogolo), ndipo chinthu chilichonse tachilemba m’kaundula wopenyeka (wofotokoza chilichonse)

Verse 13 — Surah Ya-Sin 36:13

“Ndipo pereka kwa iwo (iwe Mneneri) fanizo la (nkhani ya) eni mudzi pamene atumiki (a Allah) adaudzera mudziwo (kuti akaaongole eni mudziwo)

Verse 14 — Surah Ya-Sin 36:14

“Pamene tidatumiza atumiki awiri kwa iwo adawatsutsa; ndipo tidawalimbitsa iwo (awiriwo) potumiza wachitatu. (Atumiki atatuwo) adati: “Ife tatumidwa kwa inu.”

Verse 15 — Surah Ya-Sin 36:15

“(Eni mudzi) adati: “Inu ndi anthu ngati ife; (Allah) Wachifundo chambiri sadavumbulutse chilichonse (kwa munthu); inu simuli kanthu koma mukunena bodza.”

Verse 16 — Surah Ya-Sin 36:16

“(Atumiki) adati: “Mbuye wathu (Amene watituma kwa inu) akudziwa kuti ife ndi otumidwadi kwa inu.”

Verse 17 — Surah Ya-Sin 36:17

““Ndipo palibe china pa ife, koma kufikitsa mwachimvekere (uthenga wa Allah).”

Verse 18 — Surah Ya-Sin 36:18

“(Eni mudzi) adati: “Ife tapeza tsoka chifukwa cha inu; ngati simusiya (ulaliki wanuwo wofuna kutichotsa ku chipembedzo chathu) tikugendani ndi miyala; ndipo kuchokera kwa ife chikukhudzani chilango chowawa.”

Verse 19 — Surah Ya-Sin 36:19

“(Atumiki) adati: “Tsoka lanu lili ndi inu (chifukwa cha kukana kwanu ndi kupitiriza kupembedza mafano). Kodi mukakumbutsidwa (ndi mawu omwe m’kati mwake muli mtendere wanu mukuti takudzetserani masoka; ndi kumatiopseza ndi chilango chowawa)? Koma inu ndi anthu olumpha malire.”

Verse 20 — Surah Ya-Sin 36:20

“Kenako munthu adadza akuthamanga kuchokera ku malekezero a mzindawo (ndipo) adati: “E inu anthu anga! Atsateni atumikiwa.”

Verse 21 — Surah Ya-Sin 36:21

““Atsateni omwe sakupemphani malipiro (pa kukulangizani kwawo), ndipo iwo ngoongoka.”

Verse 22 — Surah Ya-Sin 36:22

““Kodi nchiyani chingandiletse ine kupembedza Yemwe adandilenga? Ndipo kwa Iye ndi komwe inu nonse mudzabwerera.”

Verse 23 — Surah Ya-Sin 36:23

““Kodi ndidzipangire milungu kusiya Iye (Allah)? Chipulumutso chawo sichingandipindulire chilichonse ngati (Allah) Wachifundo Chambiri atafuna kundichitira zoipa; ndipo siingandipulumutse.”

Verse 24 — Surah Ya-Sin 36:24

““Ndithu ine ngati nditatero ndiye kuti ndili mchisokero choonekera poyera”

Verse 25 — Surah Ya-Sin 36:25

““Ndithu ine ndakhulupirira Mbuye wanu choncho ndimvereni.”

Verse 26 — Surah Ya-Sin 36:26

“Kudanenedwa (kwa iye): “Lowa m’Munda wamtendere.” Iye adati: “Ha! Anthu anga akadadziwa!”

Verse 27 — Surah Ya-Sin 36:27

““Momwe Mbuye wanga wandikhululukira ndikundichita kukhala mmodzi wa opatsidwa ulemu (akadakhulupirira).”

Verse 28 — Surah Ya-Sin 36:28

“Ndipo anthu ake sitidawatsitsire ankhondo ochokera kumwamba pambuyo pake (kuti awaononge). Ndipo pachizolowezi chathu sititsitsa (ankhondo kumwamba tikafuna kuononga, koma Mngelo mmodzi amakwanira)

Verse 29 — Surah Ya-Sin 36:29

“(Kuonongeka kwawo) kudali mkuwe umodzi, ndipo nthawi yomweyo adali akufa (izi zidachitika pamene mngelo Gabuliyele adawakuwira mkuwe wamphamvu)

Verse 30 — Surah Ya-Sin 36:30

“Ha! Nzodandaulitsa kwa akapolo! Palibe pamene mtumiki adawadzera popanda kumchitira chipongwe (ndi kukana kumtsata)

Verse 31 — Surah Ya-Sin 36:31

“Kodi sadalingalire za mibadwo yambirimbiri imene tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo iwo sangabwelerenso kwa iwo

Verse 32 — Surah Ya-Sin 36:32

“Ndipo zolengedwa zonse zidzaonekera kwa Ife

Verse 33 — Surah Ya-Sin 36:33

“Ndipo chisonyezo chawo ndi nthaka yakufa; timaiukitsa (ndi madzi) ndi kutulutsa m’menemo njere, zomwe zina mwa izo amadya

Verse 34 — Surah Ya-Sin 36:34

“Ndipo tapanga m’menemo minda ya kanjedza ndi mphesa; ndipo tatulutsa m’menemo akasupe

Verse 35 — Surah Ya-Sin 36:35

“Kuti azidya zipatso zake pomwe sizidapangidwe ndi manja awo. Kodi bwanji sathokoza (Allah)

Verse 36 — Surah Ya-Sin 36:36

“Alemekezeke (Allah), Amene adalenga zinthu zonse, chachimuna ndi chachikazi, kuchokera m’zimene nthaka ikutulutsa, ndi iwo omwe ndi zina zimene (anthu) sakudziwa

Verse 37 — Surah Ya-Sin 36:37

“Ndiponso chisonyezo chawo ndiusiku. M’menemo timachotsamo usana (womwe umabisa usiku), ndipo (anthu) amangozindikira ali mu mdima

Verse 38 — Surah Ya-Sin 36:38

“۞ Ndipo dzuwa; limayenda m’njira ndi m’nthawi yake imene idakonzedwa kwa ilo. Chikonzero chimenecho ncha (Allah) Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri

Verse 39 — Surah Ya-Sin 36:39

“Ndiponso mwezi; tidaukonzera malo oimirapo mpaka kukafika pomwe umabwerera ndi kukhala wochepa ndi wokhota monga nthambi ya mtengo wa kanjedza, youma komanso yokhota

Verse 40 — Surah Ya-Sin 36:40

“Nkosatheka kwa dzuwa kukumana ndi mwezi (njira yake); nawonso usiku sungathe kupambana usana (pakudza nthawi yausana isadathe, koma zimasinthana). Ndipo chilichonse mwa izo chimasambira m’njira yake (imene Allah adachikonzera)

Verse 41 — Surah Ya-Sin 36:41

“Ndiponso pali chisonyezo kwa iwo (chosonyeza madalitso Athu pa iwo). Ndithu tidaukweza mtundu wawo mchombo chodzazidwa (ndi zonse zamoyo)

Verse 42 — Surah Ya-Sin 36:42

“Ndipo tidawapangira chonga icho chomwe akuchikwera

Verse 43 — Surah Ya-Sin 36:43

“Ndipo ngati titafuna tikhoza kuwamiza m’madzi, ndipo sangapezeke wowathandiza, ndiponso sangapulumutsidwe

Verse 44 — Surah Ya-Sin 36:44

“Koma (sitikuwamiza) chifukwa cha chifundo Chathu pa iwo ndi kuti asangalale kufikira nthawi yawo (yofera)

Verse 45 — Surah Ya-Sin 36:45

“Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Opani zomwe ziri patsogolo panu ndi zomwe ziri pambuyo panu kuti muchitiridwe chifundo.” (Iwo akunyoza malangizowo)

Verse 46 — Surah Ya-Sin 36:46

“Ndipo palibe chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo (zosonyeza umodzi Wake ndi kukhoza Kwake) chomwe chidawadzera popanda kuchinyoza (ndi kuchikana)

Verse 47 — Surah Ya-Sin 36:47

“Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Patsani (amphawi) zimene Allah wakupatsani.” Osakhulupirira amanena kwa okhulupirira: “Kodi tidyetse yemwe Allah akadafuna akadamdyetsa; (titsutsane ndi cholinga cha Allah)? Ndithu inu simuli kanthu koma muli m’kusokera koonekeratu.”

Verse 48 — Surah Ya-Sin 36:48

“Ndipo akunena (mwachipongwe kwa okhulupirira): “Kodi lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro), lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”

Verse 49 — Surah Ya-Sin 36:49

“Palibe chimene akuyembekeza, koma ndi mkuwe umodzi womwe udzawamaliza mwadzidzidzi uku iwo akukangana

Verse 50 — Surah Ya-Sin 36:50

“Ndipo sangathe kuuza wina mawu pa chinthu, ndiponso sangathe kubwerera ku maanja awo

Verse 51 — Surah Ya-Sin 36:51

“Ndipo lipenga lidzaimbidwa (loukitsa akufa); iwo adzangozindikira akutuluka m’manda kunka kwa Mbuye wawo uku akuthamanga

Verse 52 — Surah Ya-Sin 36:52

“Adzati: “Kalanga ife! Kodi ndani watidzutsa pogona pathu?” (Adzawauza): “Izi ndi zimene adalonjeza (Allah), Wachifundo chambiri ndi zimene adanena atumiki moona.”

Verse 53 — Surah Ya-Sin 36:53

“Sipadzakhala (china) koma mkuwe umodzi basi; adzangozindikira iwo onse atabweretsedwa patsogolo Pathu

Verse 54 — Surah Ya-Sin 36:54

““Ndipo mzimu uliwonse lero suponderezedwa pa chilichonse. Ndipo mulipidwa pa zokhazo munkachita.”

Verse 55 — Surah Ya-Sin 36:55

“Ndithu anthu aku Jannah (Munda wamtendere) lero akhala wotanganidwa ndi chisangalalo

Verse 56 — Surah Ya-Sin 36:56

“Iwo ndi akazi awo ali m’mithunzi uku atatsamira mipando (ya mtengo wapamwamba)

Verse 57 — Surah Ya-Sin 36:57

“M’menemo apeza (mtundu uliwonse) wa zipatso ndiponso apeza chilichonse chimene akuchifuna

Verse 58 — Surah Ya-Sin 36:58

““Mtendere (pa iwo)!” Limeneli ndi liwu lochokera kwa Mbuye (wawo), Wachisoni chosatha

Verse 59 — Surah Ya-Sin 36:59

“Ndipo dzipatuleni lero, inu oipa

Verse 60 — Surah Ya-Sin 36:60

“Kodi sindidakulangizeni, E inu ana a Adam kuti musapembedze satana? Ndithu, iye ndi mdani woonekera kwa inu

Verse 61 — Surah Ya-Sin 36:61

“Ndikuti ndipembedzeni Ine? Imeneyi ndi njira yolunjika

Verse 62 — Surah Ya-Sin 36:62

“Ndithu (satana) adasokeretsa anthu ambiri mwa inu. Kodi simumaganizira mwanzeru

Verse 63 — Surah Ya-Sin 36:63

“Iyi ndi Jahena yomwe mumalonjezedwa

Verse 64 — Surah Ya-Sin 36:64

“Iloweni lero, chifukwa cha kunkana kwanu (Allah)

Verse 65 — Surah Ya-Sin 36:65

“Lero titseka kukamwa kwawo. Ndipo manja awo atiyankhula ndipo miyendo yawo ichitira umboni pa zomwe amachita

Verse 66 — Surah Ya-Sin 36:66

“Ndipo tikadafuna, tikadafafaniza maso awo; ndipo akadakhala akuthamangira njira; koma akadapenya chotani

Verse 67 — Surah Ya-Sin 36:67

“Ndipo tikadafuna, tikadawasintha kukhala ndi maonekedwe a nyama pamalo pawo pomwepo (pamene adali), kotero kuti sakadatha kuyenda (kunka patsogolo) ngakhale kubwerera pambuyo

Verse 68 — Surah Ya-Sin 36:68

“Ndipo amene tikumtalikitsira moyo wake, timam’bwezeranso pambuyo m’kalengedwe kake (ndi kukhala ngati mwana). Kodi bwanji saganizira mwanzeru

Verse 69 — Surah Ya-Sin 36:69

“Ndipo sitidamphunzitse (Mtumiki {s.a.w}) ndakatulo, ndipo nkosayenera kwa iye (kukhala mlakatuli). Qur’an sichina, koma ndichikumbutso ndi buku lomwe likulongosola chilichonse

Verse 70 — Surah Ya-Sin 36:70

“Kuti liwachenjeze amene ali moyo, ndi kuti litsimikizike liwu (la chilango) pa osakhulupirira

Verse 71 — Surah Ya-Sin 36:71

“Kodi saona kuti Ife tawalengera nyama, m’zimene manja Athu akonza, zomwe iwo akuti nzawo

Verse 72 — Surah Ya-Sin 36:72

“Ndi kuti tazichita kukhala zowatumikira? Zina mwa izo amazikwerapo; ndipo zina mwa izo amazidya

Verse 73 — Surah Ya-Sin 36:73

“Ndipo m’menemo (m’nyama) muli zowathandiza (zambiri) ndiponso zakumwa. Nanga bwanji sathokoza

Verse 74 — Surah Ya-Sin 36:74

“Ndipo adzipangira milungu (yabodza) kusiya Allah kuti athandizidwe nayo

Verse 75 — Surah Ya-Sin 36:75

“(Koma) siingathe kuwathandiza; ndipo iwo (kwa milunguyo) ndi asilikali amene akonzedwa kulondera (mafanowo ndi kuwatumikira)

Verse 76 — Surah Ya-Sin 36:76

“Mawu awo (onyoza Allah ndi okutsutsa iwe) asakudandaulitse. Ndithu Ife tikudziwa zimene akubisa ndi zimene akuzionetsera poyera

Verse 77 — Surah Ya-Sin 36:77

“Kodi munthu sazindikira kuti Ife tidamulenga ndi dontho la umuna? Koma iye wakhala wotsutsa woonekera

Verse 78 — Surah Ya-Sin 36:78

“Ndipo akutiponyera fanizo (lotsutsa kukhoza Kwathu kuukitsa akufa) ndi kuiwala chilengedwe chake (chochokera kumadzi opanda pake). Akunena: “Ndani angaukitse mafupa pomwe ali ofumbwa?”

Verse 79 — Surah Ya-Sin 36:79

“Nena: “Adzawaukitsa Yemwe adawalenga panthawi yoyamba. Ndipo Iye Ngodziwa kalengedwe ka mtundu uliwonse

Verse 80 — Surah Ya-Sin 36:80

“Yemwe adakupangirani moto kuchokera mu mtengo wauwisi; kenako inu mumakoleza moto m’menemo

Verse 81 — Surah Ya-Sin 36:81

“Kodi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka (mukuganiza kuti) siwokhoza kuwalenga (iwo kachiwiri) monga momwe alili? Inde! Iye ndi Mlengi Wamkulu, Wodziwa kwambiri

Verse 82 — Surah Ya-Sin 36:82

“Ndithu machitidwe Ake akafuna kuti chinthu chichitike, amangonena kwa icho: “Chitika!” Ndipo chimachitika (nthawi yomweyo)

Verse 83 — Surah Ya-Sin 36:83

“Kotero alemekezeke Yemwe m’manja Mwake muli ulamuliro pa chinthu chilichonse; ndipo kwa Iye (ndiko) mudzabweerera nonse