Back to Languages

Chichewa - Chapter 38 - Sad

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Sad 38:1

“Sad, ndikulumbira Qur’an (iyi) ya ulaliki (wothandiza)

Verse 2 — Surah Sad 38:2

“Koma amene sadakhulupirire ali mkudzitukumula ndi makani

Verse 3 — Surah Sad 38:3

“Kodi ndimibadwo ingati taiwononga patsogolo pawo? Adakuwa kuitana (panthawi imeneyo), koma nthawi yopulumuka idali itatha

Verse 4 — Surah Sad 38:4

“Ndipo anadabwa atawadzera mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adati: “Uyu ndiwamatsenga; ngwabodza lamkunkhuniza!”

Verse 5 — Surah Sad 38:5

“Ha! Waichita milungu yambirimbiri ija kuti ikhale Mulungu Mmodzi Yekha? Ndithu ichi nchinthu chodabwitsa.”

Verse 6 — Surah Sad 38:6

“Ndipo adanyamuka akuluakulu a mwa iwo nati: “Nyamukani muzikapitiriza kupembedza milungu yanu. Ndithu chinthu ichi (nchoipa); chikulinga ife (kuti tisiyane ndi milungu yathu).”

Verse 7 — Surah Sad 38:7

““Sitidamve zimenezi (zakuti Mulungu Ndimmodzi ngakhale) m’chipembedzo chakale (Chikhrisitu). Ichi sikanthu, koma ndibodza lopeka.”

Verse 8 — Surah Sad 38:8

““Kodi uthengawo (wakuti Mulungu Ndimmodzi) wavumbulutsidwa kwa iye pakati pathu?” Koma iwo akukaika ndi ulaliki Wanga. Koma sadalawebe chilango Changa

Verse 9 — Surah Sad 38:9

“Kodi iwo ali nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wako, Wamphamvu zoposa, Wopatsa mochuluka

Verse 10 — Surah Sad 38:10

“Kapena ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake, ngwawo. Ngati zili choncho atakwera makwelero (kuti akafike pamalo poti akalamulire zimene akufuna, ngati angathe kutero)

Verse 11 — Surah Sad 38:11

“Awa (Aquraish kuonjezera pa kudzitama kwawo), nkagulu kochepa ndi kofooka. Kagonjetsedwa monga makamu ankhondo (omwe adagonjetsedwa kale omwe amatsutsana ndi aneneri akale)

Verse 12 — Surah Sad 38:12

“Patsogolo pawo, anthu a Nuh, Âdi ndi Farawo, mwini nyumba zitalizitali (Pyramid), adatsutsa (aneneri awo)

Verse 13 — Surah Sad 38:13

“Ndi Asamudu, ndi anthu a Luti ndi (anthu a Shuaib) eni mitengo yambiri yothothana, amenewo ndiwo makamu

Verse 14 — Surah Sad 38:14

“Onsewa adatsutsa atumiki; basi chilango Changa chidatsimikizika (pa iwo)

Verse 15 — Surah Sad 38:15

“Ndipo awa (Aquraish), sayembekeza china koma mkuwe umodzi wosabwereza. (Ndipo ukadzachitika, onse adzafa)

Verse 16 — Surah Sad 38:16

“Ndipo akunena (mwachipongwe): “E Mbuye wathu! Tipatsirenitu gawo la chilango chathu lisanafike tsiku lachiwerengero.”

Verse 17 — Surah Sad 38:17

“Pirira (iwe Mtumiki) ku zimene akunena (kwa iwe), ndipo kumbuka kapolo wathu Daud, wamphamvu (pa chipembedzo ndi za m’dziko lapansi). Ndithu iye ngotembenukira kwa Allah kwambiri

Verse 18 — Surah Sad 38:18

“Ndithu Ife tidawagonjetsa mapiri kuti pamodzi ndi iye alemekeze (Allah) mmawa ndi madzulo

Verse 19 — Surah Sad 38:19

“Ndi mbalame zomwe zidasonkhanitsidwa zonse zimamvera iye

Verse 20 — Surah Sad 38:20

“Ndipo tidaulimbikitsa ufumu wake ndi kumpatsa uneneri ndi kuyankhula kwa luntha (kosiyanitsira choona ndi chonama)

Verse 21 — Surah Sad 38:21

“Kodi yakufika nkhani ya okangana pamene adakwera chipupa mpaka kuchipinda (cha Daud chochitira mapemphero)

Verse 22 — Surah Sad 38:22

“Pamene adamulowera Daud, adachita nawo mantha adati: “Usaope; (ife) ndife okangana awiri, mmodzi wathu wamchenjelera wina. Weruza pakati pathu mwachilungamo, usakondere, ndipo tisonyeze njira yoongoka.”

Verse 23 — Surah Sad 38:23

““Ndithu uyu m’bale wanga ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi , pomwe ine ndili ndi imodzi.” Ndipo akuti: “Ndipatse nkhosa imodziyo kuti ndizikusungira.” Ndipo wandiposa pakuyankhula

Verse 24 — Surah Sad 38:24

“(Daud) adati: “Zoona, wakuchitira zosalungama pokupempha nkhosa yako imodzi kuti aiphatikize ndi nkhosa zake. Ndithu ambiri mwa ophatikizana nawo zinthu, ena amachenjelera ena kupatula amene akhulupirira ndi kumachita zabwino; ndipo iwo ngochepa.” Basi pamenepo Daud adaona kuti tamuyesa mayeso (ndipo sadapambane). Choncho adapempha chikhululuko kwa Mbuye wake; adagwa ndi kulambira ndi kubwerera kwa Mbuye wake

Verse 25 — Surah Sad 38:25

“Choncho tidamkhululukira iye zimenezo; ndithu iye ali nawo ulemelero kwa Ife ndi mabwelero abwino

Verse 26 — Surah Sad 38:26

““E iwe Daud! Ndithu ife takuchita iwe kukhala woyang’anira pa dziko; choncho weruza pakati pa anthuwa mwachilungamo; ndipo usatsatire zilakolako kuopa kuti zingakusokeretse ku njira ya Allah.” Ndithu amene akusokera ku njira ya Allah (potsatira zilakolako zawo), chilango chaukali chili pa iwo chifukwa cha kuiwala kwawo tsiku la chiwerengero

Verse 27 — Surah Sad 38:27

“Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake popanda cholinga. Zoterezo ndi maganizo a amene sadakhulupirire. Choncho kuonongeka kwakukulu ku Moto kuli kwa iwo amene sadakhulupirire

Verse 28 — Surah Sad 38:28

“Kodi tingawachite amene akhulupirira (Allah) ndi kuchita zabwino kukhala monga oononga pa dziko? Kapena tiwachite oopa (Allah) monga oipa

Verse 29 — Surah Sad 38:29

“(Ili), ndibuku lochuluka madalitso lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti (anthu) azame kwambiri pomvetsetsa ndime zake; ndi kuti apeze nalo phunziro eni nzeru

Verse 30 — Surah Sad 38:30

“Ndipo Daud tidampatsa (dalitso lobereka) Sulaiman, amene adali munthu wabwino. Ndithu iye adali wochulukitsa kutembenukira kwa Allah (ndi kudzichepetsa m’chikhalidwe chake chonse)

Verse 31 — Surah Sad 38:31

“(Kumbuka) pamene adasonyezedwa kwa iye nthawi yamadzulo akavalo ofatsa akaima; othamanga kwambiri, akayenda

Verse 32 — Surah Sad 38:32

“Ndipo adati: “Ndikukonda zinthu zabwino chifukwa chokumbukira Mbuye wanga,” kufikira pomwe (akavalowo) adabisika kuseri kwa chotsekereza (poikidwa m’makola mwawo pomwe iye amafunitsitsa kumawaonabe)

Verse 33 — Surah Sad 38:33

“(Ndipo adati): “Abwezeni kwa ine.” Kenako adayamba kuwasisita m’miyendo ndi m’makosi (mwawo)

Verse 34 — Surah Sad 38:34

“Ndithu Sulaiman tidamuyesa (mayeso); ndipo tidaika thupi pa mpando wake wachifumu; kenako adabwerera kwa Allah

Verse 35 — Surah Sad 38:35

“Adati: “E Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndipo ndipatseni ufumu (umene) sangaupeze aliyense pambuyo panga; ndithu inu ndiwopatsa mochulukitsa.”

Verse 36 — Surah Sad 38:36

“Kenako tidaichita mphepo yoomba moleza kuti imgonjere, yomwe imayenda mwachifuniro chake (Sulaiman), paliponse pomwe wafuna

Verse 37 — Surah Sad 38:37

“Ndiponso (tidamgonjetsera) asatana; ena mwa iwo omanga zomangamanga ndi obira m’nyanja zakuya

Verse 38 — Surah Sad 38:38

“Ndi ena (mwa asatana) onjatidwa mmagoli ndi unyolo, (kuti asiye kusokoneza ena)

Verse 39 — Surah Sad 38:39

“(Ndipo adauzidwa iye): “Izi (zomwc takudalitsa nazo) ndi zopatsa Zathu; choncho mpatse kapena mmane (amene wamfuna). Popanda kuwerengeredwa.”

Verse 40 — Surah Sad 38:40

“Ndithu (Sulaiman) ali nawo ulemelero waukulu woyandikira kwa Ife, ndi mabwelero abwino

Verse 41 — Surah Sad 38:41

“Kumbuka, (iwe Mtumiki {s.a.w}) kapolo Wathu Ayubu, pamene adaitana Mbuye wake: “Ine wandikhudza satana ndi masautso ndi zowawa!”

Verse 42 — Surah Sad 38:42

“(Tidamuyankha kuitana kwake, ndipo tidamuuza): “Menyetsa miyendo yako (panthaka; patuluka madzi) ozizira osamba ndi kumwa (zikuchokera zomwe uli nazo).”

Verse 43 — Surah Sad 38:43

“Ndipo tidamubwezera anthu ake, ndi kumpatsanso ena onga iwo (m’kuchuluka kwawo) powaphatikiza ndi omwe adali nawo; (tidachita zimenezi) chifukwa cha chifundo chochokera kwa Ife ndi kuti chikhale chikumbutso kwa eni nzeru

Verse 44 — Surah Sad 38:44

““Ndipo gwira m’dzanja lako mtolo wa zikoti; menya ndi mtolowo ndipo usaswe lonjezo.” Ndithu Ife tidampeza ali wopirira. Taonani kukhala bwino kapolo! Ndithu iye ngotembenukira kwambiri kwa Allah

Verse 45 — Surah Sad 38:45

“Kumbukira, (iwe Mtumiki {s.a.w}) akapolo athu Ibrahim, Ishâq ndi Ya’qub, eni mphamvu (pa ntchito yachipembedzo) ndi kuyang’ana kozindikira

Verse 46 — Surah Sad 38:46

“Ndithu Ife tidawasankha powapatsa chikhalidwe chabwino (chomwe) ndi kukumbukira Nyumba yomaliza (nthawi zonse)

Verse 47 — Surah Sad 38:47

“Ndithu kwa Ife iwo adali mwa anthu abwino omwe adasankhidwa

Verse 48 — Surah Sad 38:48

“Ndipo kumbuka Ismail, Alyasa’ (Eliya), ndi Thulkifl (Yesaya); ndipo onsewo adali mwa anthu abwino

Verse 49 — Surah Sad 38:49

“Ichi ndichikumbutso (kwa iwe ndi anthu ako). Ndipo ndithu oopa Allah ali ndi mabwelero abwino

Verse 50 — Surah Sad 38:50

“(Awakonzera iwo) minda yamuyaya yotsekulidwa makomo ake kwa iwo

Verse 51 — Surah Sad 38:51

“(Azidzakhala m’menemo) uku atatsamira (makama amtengo wapatali, ndipo adzakhala akusangalala) akuitanitsa mmenemo zipatso ndi zakumwa zambiri

Verse 52 — Surah Sad 38:52

“Ndipo (ku Munda wamtenderewo) adzakhala ndi akazi oyang’ana amuna awo okha basi, ofanana misinkhu

Verse 53 — Surah Sad 38:53

“Izi ndi zomwe mukulonjezedwa pa tsiku la chiweruziro

Verse 54 — Surah Sad 38:54

“Ndithu izi ndizopatsa Zathu zosatha

Verse 55 — Surah Sad 38:55

“Awa ndimalipiro (a oopa Allah)! Koma opyola malire (ndi kunyoza aneneri awo), ali ndi mabwelero oipa

Verse 56 — Surah Sad 38:56

“(Omwe ndi) Jahannam adzailowa (ndi kupseleramo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo

Verse 57 — Surah Sad 38:57

“Awa ndimadzi wotentha kwambiri, ndi mafinya (a anthu a ku Moto). Choncho awalaweko

Verse 58 — Surah Sad 38:58

“Ndi zilango zina zambiri zonga zimenezi zamitundumitundu

Verse 59 — Surah Sad 38:59

“(Kudzanenedwa kwa opyola malire, omwe ndiatsogoleri a opembedza mafano): “Gulu ili lalikulu, lilowa nanu ku Moto; (omwe adali okutsatirani. Ndipo atsogoleri adzati): Siolandiridwa (mwamtendere). Ndithu iwo ngolowa ku Moto.”

Verse 60 — Surah Sad 38:60

“(Otsatira adzanena): “Ndithu tembeleroli likuyenera inu, (limene mukutitembelera ife) chifukwa inu ndiamene mudadzetsa chilangochi potinyenga ife (ndi kutiitanira kunjira yopotoka), taonani kuipa malo okhazikikamo (Jahannam)!”

Verse 61 — Surah Sad 38:61

“(Otsatira) adzanena: “E Mbuye wathu! Muonjezereni chilango ku Moto pamwamba pa chilango amene watidzetsera chilangochi.”

Verse 62 — Surah Sad 38:62

“Ndipo (anthu a ku Moto) adzanena: “Kodi nchifukwa ninji sitikuwaona anthu aja omwe timawawerengera kuti ngoipa (pa dziko lapansi)

Verse 63 — Surah Sad 38:63

“Kodi tidawachitira chipongwe (pa dziko lapansi koma taonani sadalowe nafe ku Moto). Kapena kuti maso athu sakuwaona?”

Verse 64 — Surah Sad 38:64

“Ndithu zimenezo, zokangana anthu a ku Moto nzoona

Verse 65 — Surah Sad 38:65

“Nena (kwa iwo): “Ndithu ine ndine mchenjezi (wochenjeza za chilango cha Allah). Palibe wopembedzedwa mwachoonadi, koma Allah Mmodzi Yekha Wopambana

Verse 66 — Surah Sad 38:66

“Mbuye wathambo ndi nthaka, ndi zapakati pake; wamphamvu zoposa; Wokhululuka machimo kwambiri (kwa yemwe walapa ndi kumkhulupirira).”

Verse 67 — Surah Sad 38:67

“Nena (kwa iwo iwe Mtumiki {s.a.w}): “Ichi (chimene ndakuchenjezani nachochi) ndinkhani yaikulu.”

Verse 68 — Surah Sad 38:68

““Inu, za chimenechi, mukunyozera!”

Verse 69 — Surah Sad 38:69

““Sindimadziwa chilichonse za akuluakulu a pamwamba (angelo) pamene amakangana (za kulengedwa kwa Adam).”

Verse 70 — Surah Sad 38:70

“Palibe china chimene chavumbulutsidwa kwa ine, koma (kuti ndikuuzeni mawu awa oti): “Ine ndine mchenjezi (wanu) woonekera.”

Verse 71 — Surah Sad 38:71

“(Akumbutse) pamene Mbuye wako adanena kwa angelo: “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi, (yemwe ndi Adam).”

Verse 72 — Surah Sad 38:72

““Ndikammaliza ndi kumuuzira mzimu wochokera kwa Ine, igwani pansi momulemekeza.”

Verse 73 — Surah Sad 38:73

“Choncho angelo onse anagwa pansi momulemekeza

Verse 74 — Surah Sad 38:74

“Kupatula Iblis; adadzikweza, ndipo adali mmodzi mwa okana

Verse 75 — Surah Sad 38:75

“(Allah) adati: “E iwe Iblis! Nchiyani chakuletsa kugwa pansi ndi kuchilemekeza chimene ndachilenga ndi manja Anga (popanda kutuma wina)? Kodi wadzikweza kapena uli mmodzi wa odziika pamwamba?”

Verse 76 — Surah Sad 38:76

“(Iblis) adanena: “Ine ndine wabwino kuposa iye (Adam); chifukwa ine mudandilenga kuchokera ku Moto, ndipo iye mudamulenga kuchokera kudongo.”

Verse 77 — Surah Sad 38:77

“(Allah) adanena (kwa Iblis): “Tuluka m’menemo (m’gulu la angelo apamwamba); ndithu iwe ngopirikitsidwa (ku chifundo cha Allah).”

Verse 78 — Surah Sad 38:78

““Ndipo ndithu matembelero Anga akhala pa iwe kufikira tsiku lamalipiro.”

Verse 79 — Surah Sad 38:79

“(Iblis) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nthawi kufikira tsiku louka ku imfa.”

Verse 80 — Surah Sad 38:80

“(Allah) adati: “Ndithu iwe ndiwe mmodzi wa wopatsidwa nthawi.”

Verse 81 — Surah Sad 38:81

““Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (imene yaikidwa).”

Verse 82 — Surah Sad 38:82

“(Iblis) adati: “Choncho kupyolera mu ulemelero Wanu ndikulumbira kuti ndiwasokoneza onse.”

Verse 83 — Surah Sad 38:83

““Kupatula akapolo Anu omwe ali osankhidwa (oyeretsedwa) mwa iwo. (Pa iwo ndilibe nyonga zilizonse).”

Verse 84 — Surah Sad 38:84

“(Allah) adati: “Ndikulumbira mwachoonadi ndipo ndikunena choona.”

Verse 85 — Surah Sad 38:85

““Ndithudi, ndidzazadzitsa Jahannam ndi ochokera ku mtundu wako ndi omwe adzakutsate mwa iwo (ana a Adam) onse.”

Verse 86 — Surah Sad 38:86

“Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}, kwa anthu ako): “Sindikukupemphani malipiro pa zimenezi ndiponso ine simmodzi wa odzikakamiza (pa zinthu zosandiyenera)

Verse 87 — Surah Sad 38:87

“(Qur’an) sichina koma ndichikumbutso ndi chiphunzitso kwa zolengedwa zonse

Verse 88 — Surah Sad 38:88

“Ndipo posachedwa mudziwa, (inu otsutsa, kuona kwa) nkhani zake.”