Back to Languages

Chichewa - Chapter 39 - Az-Zumar

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Az-Zumar 39:1

“Kuvumbulutsidwa kwa Buku ili kwachokera kwa Allah, Mwini mphamvu zoposa; Mwini nzeru zakuya

Verse 2 — Surah Az-Zumar 39:2

“Ndithu Ife takuvumbulutsira iwe buku ili mwamtheradi; choncho mpembedze Allah momyeretsera mapemphero Iye yekha

Verse 3 — Surah Az-Zumar 39:3

“Dziwani kuti Allah Ngolandira mapemphero oyera, (opanda kuphatikizidwa ndi zina). Koma amene adzipangira athandizi kusiya Allah, (akumanena kuti): “Ife sitikuwapembedza awa, koma tikutero ndi cholinga choti atifikitse pafupi ndi Allah.” Ndithu Allah, adzaweruza pakati pawo (pakati pa okhulupirira Allah, ndi okana) pa zimene akusiyana. Ndithu Allah saongola amene ali wabodza; wokanira zedi (Allah)

Verse 4 — Surah Az-Zumar 39:4

“Allah akadafuna kupeza mwana, akadasankha yemwe akum’funa mzomwe adalenga. Wapatukana ndi zimenezo! Iye ndi Allah Mmodzi; Wogonjetsa; (Wochita zimene wafuna)

Verse 5 — Surah Az-Zumar 39:5

“Adalenga thambo ndi nthaka mwamtheradi. Amakulunga usiku mu usana; ndipo amakulunga usana mu usiku. Ndipo dzuwa ndi mwezi wazichita kuti zitumikire monga momwe afunira. Zonsezi zikuyenda kufikira pa nthawi yake imene yaikidwa. Dziwani kuti Iye (Allah) Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri

Verse 6 — Surah Az-Zumar 39:6

“Adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi (womwe ndi Adam; tate wa anthu). Ndipo kenako adalenga kuchokera mu mzimu umenewo mnzake, (mkazi wake, Hawa); ndipo adakutsitsirani mitundu isanu ndi itatu ya nyama ziwiriziwiri (zomwe ndi: Ngamira yaimuna ndi yaikazi, ng’ombe yaimuna ndi yaikazi, mbuzi yaimuna ndi yaikazi ndi nkhosa yaimuna ndi yaikazi. Zonse pamodzi, zisanu ndi zitatu, zomwe mumathandizidwa nazo kwambiri). Amakuumbani m’mimba mwa mayi anu mkaumbidwe kosiyanasiyana, mu mdima utatu; (mu mdima wa mimba, chiberekero ndi mdima wa nembanemba). Ameneyo (adakuchitirani zonsezi), ndi Allah, Mleri wanu; ufumu ngwa Iye. Palibe wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Kodi nanga mukutembunuzidwa bwanji (kusiya Allah)

Verse 7 — Surah Az-Zumar 39:7

“Ngati mukana ndithu Allah Ngodzikwaniritsa sasaukira kwa inu (chikhulupiliro chanu ndi kuthokoza kwanu); koma sakonda kukanira kwa anthu Ake. Ngati mumthokoza (pa mtendere Wake umene uli pa inu) akuyanja kuthokoza kwanuko. Ndipo mzimu wochimwa sungasenze machimo a mzimu wina. Kenako kobwerera kwanu nkwa Mbuye wanu, ndipo adzakuuzani zimene mudali kuchita. Ndithu Iye Ngodziwa (zinsinsi) za m’mitima

Verse 8 — Surah Az-Zumar 39:8

“Ndipo masautso akampeza munthu, amapempha Mbuye wake ndi kutembenukira kwa Iye (pomwe chikhalirecho adali kumnyoza). Kenako (Mbuye wake) akampatsa mtendere wochokera kwa Iye (waukulu), amaiwala (masautso aja) omwe adali kumpempha Allah kuti amchotsere asadampatse mtenderewo, ndipo kenako ndikumpangira Allah milungu inzake kuti asokeretse ku njira Yake. Nena (iwe Mtumiki kwa yemwe ali ndi chikhalidwe chotere): “Sangalala ndi kukanira kwako (mtendere wa Allah) kwa nthawi yochepa. Ndithu iwe ndi mmodzi wa anthu aku Moto.”

Verse 9 — Surah Az-Zumar 39:9

“Kodi yemwe akudzichepetsa (kwa Allah ndi kumpembedza) pakati pa usiku uku akugwetsa nkhope pansi ndi kuimilira, kuopa tsiku la chimaliziro ndi kuyembekezera chifundo cha Mbuye wake, (kodi angafanane ndi yemwe amapempha Allah akakhala pa mavuto pokha, akakhala pa mtendere ndikumuiwala?) Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki {s.a.w}): “Kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa, ngofanana?” Ndithu ndi eni nzeru amene amalingalira

Verse 10 — Surah Az-Zumar 39:10

“Nena (kwa iwo mau Anga akuti): “E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Muopeni Mbuye wanu. Ndithu amene achita zabwino zotsatira zake nzabwino padziko lapansi, ndipo dziko la Allah ndilophanuka. (Pirirani chifukwa chosiya midzi yanu ndi abale). Ndithu opirira adzalipidwa malipiro awo mokwana mopanda mulingo.”

Verse 11 — Surah Az-Zumar 39:11

“Nena: “Ine ndalamulidwa kuti ndimpembedze Allah momuyeretsera mapemphero Ake (posamphatikiza ndi aliyense pa mapemphero, kapena kupemphera mwa chiphamaso).”

Verse 12 — Surah Az-Zumar 39:12

““Ndalamulidwanso kuti ndikhale woyamba mwa ogonjera (malamulo Ake).”

Verse 13 — Surah Az-Zumar 39:13

“Nena: “Ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu, (loopsa), ngati ndinyoza Mbuye wanga.”

Verse 14 — Surah Az-Zumar 39:14

“Nena (kwa iwo, iwe Mneneri {s.a.w}): “Ndi Allah Yekha ndikumpembedza pomuyeretsera Iye mapemphero anga.”

Verse 15 — Surah Az-Zumar 39:15

““Choncho pembedzani zimene mwafuna, kumsiya Iye.” Nena (kwa iwo): “Ndithu otaika ndi kuonongeka kwakukulu, ndi amene adzitaya okha, (adziluzitsa okha), ndi maanja awo, patsiku la Qiyâma. Dziwa, ndithu kumeneko ndiko kuluza koonekera.”

Verse 16 — Surah Az-Zumar 39:16

“Pa iwo padzakhala misanjikosanjiko ya moto ndiponso pansi pawo. Ndi (chilango) chimenechi, Allah akuwaopseza nacho akapolo Ake. “E inu akapolo Anga! Ndiopeni!”

Verse 17 — Surah Az-Zumar 39:17

“Ndipo amene apatukana nawo mafano ndi satana posiya kuzipembedza, ndikusiya kuziyandikira, ndipo mmalo mwake nkutembenukira kwa Allah (pa zochita zawo zonse), nkhani yabwino njawo (ponseponse). Auze nkhani yabwino akapolo Anga

Verse 18 — Surah Az-Zumar 39:18

“Amene akumvetsera mawu ndi kutsatira amene ali abwino kwambiri. Iwowo ndi amene Allah wawaongola. Ndipo iwowo ndiwo eni nzeru

Verse 19 — Surah Az-Zumar 39:19

“Kodi yemwe chiweruzo cha chilango chatsimikizika pa iye, (mungamteteze)? Kodi iwe ungampulumutse yemwe ali m’Moto

Verse 20 — Surah Az-Zumar 39:20

“Koma amene aopa Mbuye wawo, iwo adzakhala nazo Nyumba zikuluzikulu zimene zamangidwa mosanjikizana, mitsinje ikuyenda pansi pake. Ili ndi lonjezo lochokera kwa Allah. Allah saphwanya lonjezo

Verse 21 — Surah Az-Zumar 39:21

“Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera kumwamba, ndipo amawalowetsa mu akasupe mkati mwa nthaka, kenako amatulutsa ndi madziwo mbewu zosiyana mitundu: (chimanga, mpunga, tirigu, ndi zina zotere). Ndipo kenako zimauma (pambuyo pokhala zobiriwira); umaziona zili zachikasu. Kenako amazichita kukhala zidutswazidutswa? Ndithu muzimenezo muli chikumbutso kwa eni nzeru (zofufuzira zinthu)

Verse 22 — Surah Az-Zumar 39:22

“Kodi amene Allah watsekula chifuwa chake povomereza Chisilamu, kotero kuti iye akuyenda mkuunika kwa Mbuye wake, (angafanane ndi yemwe akunyozera kupenyetsetsa zisonyezo za Allah?) Kuonongeka kwakukulu kuli pa ouma mitima yawo posakumbukira Allah (ndi kulabadira Qur’an). Iwo ali m’kusokera koonekera

Verse 23 — Surah Az-Zumar 39:23

“Allah wavumbulutsa nkhani yabwino zedi yomwe ndi buku logwirizana nkhani zake; (losasemphana). Lobwerezabwereza (malamulo ake). Makungu a omwe amaopa Mbuye wawo amanjenjemera ndi ilo. Kenako makungu awo ndi mitima yawo zimakhazikika pokumbukira Allah. Buku limeneli ndi chiongoko cha Allah; ndi ilo, akumuongola amene wamfuna. Ndipo amene Allah wamulekelera kuti asokere (chifukwa chonyozera kwake choona), sangakhale ndi womuongola (ndi ompulumutsa ku chionongeko)

Verse 24 — Surah Az-Zumar 39:24

“Kodi yemwe adzakhala akudzitchinjiriza ndi nkhope yake (uku manja atanjatidwa) ku chilango choipa pa tsiku la Qiyâma, (angafanane ndi yemwe adzakhala mchisangalalo mminda ya mtendere?” Ndipo kudzanenedwa kwa oipa: “Lawani zoipa za zochita zanu.”)

Verse 25 — Surah Az-Zumar 39:25

“Amene adalipo patsogolo pawo, adatsutsa. Ndipo chilango chidawadzera kuchokera komwe sadali kuyembekezera

Verse 26 — Surah Az-Zumar 39:26

“Choncho Allah adawalawitsa kunyozeka pa moyo wa pa dziko lapansi; koma ndithu chilango cha tsiku la chimaliziro nchachikulu zedi (kuposa chilango cha m’dziko lapansi) akadakhala akudziwa

Verse 27 — Surah Az-Zumar 39:27

“Ndithu m’buku ili la Qur’an taperekamo mafanizo osiyanasiyana kwa anthu kuti akumbukire

Verse 28 — Surah Az-Zumar 39:28

“Qur’an ya Chiarabu yopanda zokhota, kuti iwo aope (Allah)

Verse 29 — Surah Az-Zumar 39:29

“Allah wapereka fanizo la munthu wotumikira mabwana awiri omwe ngokangana pa za iye, ndi munthu yemwe akutumikira bwana mmodzi. Kodi awiriwa ngofanana? Kuyamikidwa konse nkwa Allah! Koma ambiri a iwo sadziwa

Verse 30 — Surah Az-Zumar 39:30

“Ndithu iwe udzafa; naonso adzafa

Verse 31 — Surah Az-Zumar 39:31

“(Ndipo) kenako, inu patsiku la Qiyâma mudzakangana pamaso pa Mbuye wanu

Verse 32 — Surah Az-Zumar 39:32

“۞ Kodi ndiyani wachinyengo wamkulu woposa yemwe akumnamizira Allah zabodza, ndi kutsutsa choona chikamdzera? Kodi Jahannam simalo a okanira

Verse 33 — Surah Az-Zumar 39:33

“Ndipo amene wadza ndi choona, naachikhulupirira, iwowo ndiwo oopa Allah

Verse 34 — Surah Az-Zumar 39:34

“Adzapeza zomwe adzakhumba kwa Mbuye wawo. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino

Verse 35 — Surah Az-Zumar 39:35

“Kuti Allah awafafanizire zoipa za zochita zawo, ndi kuti awalipire malipiro awo chifukwa cha zabwino zomwe adali kuchita

Verse 36 — Surah Az-Zumar 39:36

“Kodi Allah sali Wokwanira kwa kapolo Wake? Koma akukuopseza ndi zina zosakhala Iye! Ndipo yemwe Allah wam’lekelera kuti asokere, ndithu alibe womuongola

Verse 37 — Surah Az-Zumar 39:37

“Ndipo amene Allah wamuongola, palibe amene angathe kumsokeretsa. Kodi Allah sali Mwini mphamvu zoposa; Wokhoza kubwezera chilango

Verse 38 — Surah Az-Zumar 39:38

“Ndipo ukawafunsa (kuti) ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndithu anena (kuti ndi) “Allah.” Nena: “Kodi mukuona bwanji, amene mukuwapembedza kusiya Allah angandichotsere masautso ake ngati Allah atafuna kundipatsa masautso? Kapena Allah atafuna kundichitira chifundo, kodi iwo angatsekereze chifundo Chakecho?” Nena: “Allah akundikwanira! Kwa Iye, atsamire otsamira.”

Verse 39 — Surah Az-Zumar 39:39

“Nena: “E inu anthu anga! Chitani zochita zanu mmene mungathere. Nanenso ndichita (mmene ndingathere). Koma posachedwa mudziwa

Verse 40 — Surah Az-Zumar 39:40

“Amene chim’dzere chilango chomuyalutsa, ndi kum’fikira iye chilango chamuyaya.”

Verse 41 — Surah Az-Zumar 39:41

“Ndithu ife takuvumbulutsira buku ili chifukwa cha anthu (onse) kuti Tiwafotokozere choona. Choncho amene waongoka, zabwino zake nza iye mwini. Koma amene wakhota, ndiye kuti akudzikhotetsa yekha. (Ndipo zoipa za kukhotako zidzakhala pa iye yekha). Ndipo iwe si muyang’anili wawo

Verse 42 — Surah Az-Zumar 39:42

“Allah ndiye amatenga mizimu pa nthawi ya imfa yake ndipo amatenga mizimu yomwe siidafe panthawi yogona tulo. Ndipo amaigwira mizimu imene wailamula kufa, (osaibwezera ku matupi awo). Koma inayo amaitumiza (kumatupi awo, yomwe nthawi yake siidakwane) kuti ikwaniritse nthawi yake imene idaikidwa. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo kwa anthu olingalira

Verse 43 — Surah Az-Zumar 39:43

“Kodi adzipangira awomboli kusiya Allah? Nena: “Ngakhale kuti (awombolio) alibe mphamvu ndi kuzindikira pa chilichonse?”

Verse 44 — Surah Az-Zumar 39:44

“Nena: “Chiombolo chonse chili kwa Allah; ufumu wa kumwamba ndi pansi Ngwake; kenako kwa Iye m’dzabwezedwa.”

Verse 45 — Surah Az-Zumar 39:45

“Ndipo pamene Allah Yekha akutchulidwa, mitima ya amene sakhulupirira tsiku la chimaliziro imanyansidwa; koma akatchulidwa amene sali Iye, iwo amakondwa

Verse 46 — Surah Az-Zumar 39:46

“Nena: “E Allah! Mlengi wa thambo ndi nthaka! Wodziwa zobisika ndi zooneka! Inu mudzaweruza pakati pa akapolo Anu pa zimene adali kusemphana.”

Verse 47 — Surah Az-Zumar 39:47

“Ndipo amene adzichitira zoipa, ngakhale kukadakhala kuti ali nazo zonse za mnthaka pamodzi ndi zina zonga izo, akadadziombola nazo ku chilango choipa cha tsiku la Qiyâma (koma sizikanatheka). Ndipo zidzawaonekera kuchokera kwa Allah, zomwe sadali kuziyembekezera

Verse 48 — Surah Az-Zumar 39:48

“Kukawaonekera kuipa kwa zimene adazichita, ndipo zikawazinga zimene adali kuzichitira chipongwe

Verse 49 — Surah Az-Zumar 39:49

“Pamene munthu mavuto amkhudza, amatipempha (uku ali wodzichepetsa); koma tikampatsa mtendere wochokera kwa Ife, amanena kuti: “Ndapatsidwa mtendere uwu chifukwa chakudziwa kwanga (njira zoupezera).” (Sichoncho) koma mtendere umenewu ndi mayeso; koma ambiri a iwo sadziwa

Verse 50 — Surah Az-Zumar 39:50

“Ndithu adanenanso zonga zimenezi omwe adalipo patsogolo pawo, koma sizidawathandize zimene adali kuchita

Verse 51 — Surah Az-Zumar 39:51

“Choncho, zidawapeza zoipa za zomwe adazichita. Ndipo amene achita chinyengo mwa awa, posachedwa kuwapeza kuipa kwa zomwe achita, ndipo iwo sangamlempheretse (Allah)

Verse 52 — Surah Az-Zumar 39:52

“Kodi iwo sadziwa kuti Allah amamtambasulira zopatsa zake yemwe wamfuna, ndi kumchepetsera (amene wamfuna)? Ndithu m’zimenezi muli malingaliro kwa anthu okhulupirira

Verse 53 — Surah Az-Zumar 39:53

“Nena (kwa iwo mau anga akuti): “E inu akapolo anga! Amene mwadzichitira chinyengo, musataye mtima ndi chifundo cha Allah. Ndithu Allah amakhululuka machimo onse. Ndithu Iye Ngokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.”

Verse 54 — Surah Az-Zumar 39:54

“Ndipo tembenukirani kwa Mbuye wanu, ndipo m’gonjereni chilango chisadakudzereni. Ndipo zitatero, sim’dzapulumutsidwa

Verse 55 — Surah Az-Zumar 39:55

“Ndipo tsatirani zabwino, zimene zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu chisadakufikeni chilango mwadzidzidzi pomwe inu simukudziwa!”

Verse 56 — Surah Az-Zumar 39:56

“Kuti mzimu usadzanene: “Kalanga ine! Mzomwe sindidalabadire kumbali ya Allah; ndithu ndidali mmodzi wa ochitira chibwana (zinthu za chipembedzo).”

Verse 57 — Surah Az-Zumar 39:57

“Kapena ungadzanene: “Allah akadandiongola, ndithu ndikadakhala mwa oopa (Allah).”

Verse 58 — Surah Az-Zumar 39:58

“Kapena kunena utaona chilango: “Ndikadatha kubwerera (pa dziko lapansi), ndikadakhala mmodzi wa ochita zabwino.”

Verse 59 — Surah Az-Zumar 39:59

“(Adzauzidwa: “Nchiyani iwe?) Ndithu zidakufika zisonyezo Zanga, ndipo udazitsutsa ndi kudzitukumula; ndipo udali mmodzi wa okanira.”

Verse 60 — Surah Az-Zumar 39:60

“Ndipo tsiku la Qiyâma udzawaona omwe adamnamizira Allah, nkhope zawo zili zakuda. Kodi Jahannam simalo a odzitukumula

Verse 61 — Surah Az-Zumar 39:61

“Ndipo Allah adzawapulumutsa amene adamuopa, chifukwa cha kupambana kwawo. Zoipa sizikawakhudza, ndipo iwo sakadandaula

Verse 62 — Surah Az-Zumar 39:62

“Allah ndiye Mlengi wa chilichonse, ndipo Iye ndi Myang’aniri wa chilichonse

Verse 63 — Surah Az-Zumar 39:63

“Makiyi a kumwamba ndi pansi ali kwa Iye. Ndipo amene akanira zisonyezo za Allah, iwo ndiwo oluza, (otaika)

Verse 64 — Surah Az-Zumar 39:64

“Nena: “Kodi mukundilamula kuti ndipembedze yemwe sali Allah, E inu mbuli?”

Verse 65 — Surah Az-Zumar 39:65

“Ndipo ndithu kwavumbulutsidwa kwa iwe, ndi kwa amene adalipo patsogolo pako (mawu awa:) “Ngati umphatikiza (Allah ndi milungu yabodza), ndithu ntchito zako zionongeka, ndipo ukhala mwa oluza (otaika).”

Verse 66 — Surah Az-Zumar 39:66

“Koma pembedza Allah yekha, ndipo khala mwa othokoza

Verse 67 — Surah Az-Zumar 39:67

“Koma sadamlemekeze Allah, kulemekeza koyenerana Naye, pomwe pa tsiku la Qiyâma nthaka yonse (idzakhala) chofumbata Chake mmanja; ndipo thambo lidzakulungidwa ndi dzanja Lake lamanja. Walemekezeka Allah. Ndipo watukuka ku zimene akum’phatikiza nazozi

Verse 68 — Surah Az-Zumar 39:68

“Ndipo (pamene) lipenga lidzaimbidwa, onse a kumwamba ndi pansi adzakomoka kupatula amene Allah wamfuna. Kenako lidzaimbidwa lachiwiri; pamenepo (onse) adzauka; adzakhala akuyang’ana (modabwa: “Nchiyani chachitika!”)

Verse 69 — Surah Az-Zumar 39:69

“Ndipo nthaka (tsiku limenelo) idzawala ndi kuunika kwa Mbuye wake; ndipo akaundula a zochita, adzaikidwa. Ndipo adzabweretsedwa aneneri ndi mboni (kuti aikire umboni pa anthu). Ndipo padzaweruzidwa pakati pawo mwachoonadi; ndipo iwo sadzaponderezedwa

Verse 70 — Surah Az-Zumar 39:70

“Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa zimene udachita; ndipo Iye (Allah) Ngodziwa kwambiri zimene akuchita

Verse 71 — Surah Az-Zumar 39:71

“Ndipo amene adakanira, adzakusidwa kunka ku Jahannam ali magulumagulu kufikira pomwe adzaifikira, makomo ake adzatsekulidwa, ndipo alonda ake adzawauza: “Kodi sadakudzereni aneneri ochokera mwa inu okulakatulirani zisonyezo za Mbuye wanu, ndi kukuchenjezani za kukumana kwanu ndi tsiku lanuli?” Adzayankha (nati): “Inde, adatidzera; koma lidatsimikizika liwu la chilango pa okanira.”

Verse 72 — Surah Az-Zumar 39:72

“Kudzanenedwa: “Lowani makomo a ku Jahannam; mukakhalitse mmenemo (nthawi yaitali).” Taonani kuipa malo a odzitukumula

Verse 73 — Surah Az-Zumar 39:73

“Ndipo amene adamuopa Mbuye wawo, adzakusidwa kunka ku Munda wamtendere ali magulumagulu, mpaka kufikira pomwe adzaufika. (Adzapeza kuti) makomo ake atsekulidwa. Alonda ake adzanena kwa iwo: “Mtendere ukhale pa inu mwachita bwino! Lowani mmenemo, khalani nthawi yaitali.”

Verse 74 — Surah Az-Zumar 39:74

“Ndipo iwo adzanena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Amene watitsimikizira lonjezo Lake, ndipo watipatsa dziko (kuti n’lathulathu). Tikukhala m’Minda yamtendereyi paliponse tafuna.” Taonani kukoma malipiro aochita zabwino

Verse 75 — Surah Az-Zumar 39:75

“Ndipo udzaona angelo atazungulira mphepete mwa Arsh (Mpando wachifumu) uku akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo. Ndipo padzaweruzidwa pakati pawo mwachoonadi, ndipo kudzanenedwa (ndi zolengedwa zonse): “Kuyamikidwa nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa!”