“Amuna m’chuma chimene makolo ndi achibale asiya ali ndi gawo. Naonso akazi ali ndigawo m’chuma chimene asiya makolo ndi achibale (chapafupi), ngakhale chitakhala chochepa kapena chochuluka ndigawo logawidwa (ndi Allah)
“Koma amene anganyoze Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kulumpha malire ake, (Allah) adzamulowetsa ku Moto; nadzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ndipo adzapeza chilango chosambula
“Ndipo omwe achite cha uve (chigololo) mwa akazi anu, afunireni mboni zinayi za mwa inu zoikira umboni pa iwo. Ngati ataikira umboni (kuti achitadi cha uvecho), atsekereni m’nyumba kufikira imfa idzawapeze, kapena Allah adzawaikire njira ina (monga kuphedwa)
“Kulapa sikungalandiridwe pa omwe akuchita zoipa mpaka imfa kumfikira m’modzi wa iwo (pamenepo) nkunena: “Ndithudi ine ndikulapa tsopano.” Ngakhalenso pa omwe akufa ali osakhulupirira. Iwo tawakonzera chilango chopweteka
“Kwaletsedwa kwa inu kukwatira amayi anu, ana anu, alongo anu, azakhali anu, amayi anu aang’ono kapena aakulu, ana achikazi am’bale wanu, ana achikazi a mlongo wanu, amayi anu amene adakuyamwitsani, alongo anu oberekedwa ndi amene adakuyamwitsanipo. Mayi a akazi anu, ana achikazi owapeza amene mukuwasunga woberekedwa ndi akazi anu omwe mwalowana nawo. Koma ngati simudalowane nawo, nkosaletsedwa kwa inu kukwatira ana awowo; ndi akazi a ana amuna omwe ngochokera kumisana yanu. Ndiponso nkoletsedwa kwa inu kukwatira mophatikiza mkazi ndi mchemwali wake obadwa naye, kupatula zomwe zidapita. Ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni zedi
“۞ Ndiponso (nkoletsedwa kwa inu kukwatira) akazi okwatiwa kupatula chimene manja anu akumanja apeza (mdzakazi). Ili ndi lamulo la Allah lomwe lili pa inu. Ndipo kwalolezedwa kwa inu (kukwatira akazi) omwe sali m’gulu ili. Afunefuneni ndi chuma chanu m’njira ya ukwati, osati chiwerewere. Choncho, amene mwawakwatira mwa iwo nkusangalala nawo, apatseni chiwongo chawo chomwe chakakamizidwa. Palibe kuipa kwa inu (kupereka) chomwe mwagwirizana m’malo mwa chomwe chidatchulidwa. Ndithudi, Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya (pokhazikitsa malamulo Ake)
“Ndipo musazilakelake (mwadumbo) zomwe Allah wawadalitsa nazo ena mwa inu. Amuna ali ndi gawo (lokwanira) la zomwe apeza. Nawonso akazi ali ndi gawo (lokwanira) la zomwe apeza. Ndipo mpempheni Allah zabwino zake. Ndithudi, Allah Ngodziwa chilichonse
“Ndipo anthu tawaikira alowa mmalo pa zomwe asiya makolo awiri ndi achibale. Ndipo amene mudagwirizana nawo chipangano, apatseni gawo lawo. Ndithudi, Allah Ndimboni pa chilichonse
“Amuna ndiayang’aniri pa akazi chifukwa choti Allah watukula ena pa ulemelero pamwamba pa ena, chifukwa cha chuma chawo chimene apereka. Choncho, akazi abwino ndi omwe ali omvera, odzisunga ngakhale amuna awo palibe pakuti Allah wawalamula kudzisunga. Ndipo akazi omwe mukuopa mnyozo wawo, achenjezeni; ndipo kenako achokereni pamphasa, (apo ayi), akwapuleni (kukwapula kosavulaza), koma ngati akukumverani, musawafunire njira yowavutitsira. Ndithu Allah ndi yemwe ali Wapamwamba, Wamkulu (kuposa inu nonse)
“Ndipo mpembedzeni Allah, ndipo musamphatikize ndi chilichonse; ndipo achitireni zabwino makolo awiri, ndi achibale, ndi ana amasiye ndi masikini ndi mnansi woyandikana naye nyumba, ndi wapadera wogundizana naye nyumba, ndi mnzako wokhala naye limodzi, ndi wapaulendo yemwe alibe choyendera, ndi omwe manja anu akumanja apeza (adzakazi). Ndithudi, Allah sakonda wodzitukumula ndi wodzitama
“Ndi omwe akupereka chuma chawo modzionetsera kwa anthu ndipo sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndiponso yemwe satana angakhale bwenzi lake, ndithudi ali ndi bwenzi loipa
“Kodi pakadakhala vuto lanji kwa iwo ngati akadakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro napereka zina mwa zomwe Allah wawapatsa? Ndipo Allah ali Wodziwa bwino za iwo
“Ndithudi, Allah sachitira (anthu) zosalungama ngakhale kanthu kolemera ngati kanyelere; ngati kanthuko kali kabwino amakachulukitsa ndi kupereka malipiro aakulu kuchokera kwa Iye
“Kodi sukuwaona omwe adapatsidwa gawo la (nzeru zozindikira) buku (la Allah, omwe ndi Ayuda ndi Akhrisitu), akudzisankhira kusokera ndiponso akufuna mutasokera kusiya njira (yabwino)
“Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la nzeru zozindikira buku (la Allah)? Amakhulupirira mafano ndi asatana, ndipo akumati kwa amene sadakhulupirire: “Awa ali panjira yoongoka kwabasi kuposa okhulupirira (Asilamu).”
“Kodi akuchitira anthu dumbo pa zomwe Allah wawapatsa ndi ufulu wake? Choncho tidalipatsa banja la Ibrahim buku ndi nzeru. Ndipo tidawapatsa ufumu waukulu
“Ndithudi, Allah akukulamulani kubweza kwa eni zomwe mwakhulupirika nazo. Ndipo pamene mukuweruza pakati pa anthu, weruzani mwachilungamo. Ndithu malangizo amene Allah akukulangizani, ngabwino kwambiri. Ndithudi, Allah Ngwakumva, Ngoona
“E inu amene mwakhulupirira! Mumvereni Allah ndiponso mumvereni Mtumiki, ndi omwe ali ndi udindo pa inu. Ngati Mutatsutsana pa chinthu chilichonse, chibwezeni kwa Allah ndi Mtumiki Wake, ngatidi mukukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, kutero ndibwino; ndipo zotere zili ndi zotsatira zabwino
“Ndipo sitidamtumize mtumiki aliyense koma kuti azimveredwa mwa lamulo la Allah. Ngati akadakudzera pamene adadzichitira okha zoipa, (chifukwa chokafuna chiweruzo cha satana) napempha chikhululuko kwa Allah (naye) Mtumiki nkuwapempheranso chikhululuko, ndithudi, akadampeza Allah ali Wolandira kulapa kwawo ali Wachisoni chosatha
“Ndipo amene angamvere Allah ndi Mtumiki wake, iwowo ndi omwe adzakhale pamodzi ndi omwe Allah adawadalitsa, kuyambira aneneri, olungama, mashahidi (asilamu ofela ku nkhondo) ndi anthu abwino. Taonani ubwino wokhala nawo pamodzi iwowo
“Mwatani inu osamenyana pa njira ya Allah, ndi (kuwapulumutsa) omwe ali ofooka, aamuna ndi aakazi ndi ana, omwe akunena: “Mbuye wathu! Titulutseni m’mudzi uwu omwe anthu ake ndiopondereza; ndipo tipatseni mtetezi wochokera kwa Inu; ndiponso tipatseni mthandizi wochokera kwa Inu.”
“Amene akhulupirira, akumenya nkhondo pa njira ya Allah. Koma amene sadakhulupirire, akumenya nkhondo panjira ya satana. Choncho menyanani ndi abwenzi a satana. Ndithudi, ndale za satana nzofooka
“Amati: “Tikumvera.” Koma akachoka kwa iwe, gulu lina la iwo limapangana usiku zosagwirizana ndi zomwe ukunena (pamaso pawo). Koma Allah akulemba zonse zomwe akupangana. Choncho apatukire ndipo yadzamira kwa Allah. Ndipo Allah wakwanira kukhala Mtetezi
“Ndipo chikawadzera chinthu chilichonse chokhuza chitetezo kapena mantha, amachifalitsa. Koma akadachibwezera kwa Mtumiki ndi kwa omwe ali ndi udindo pa iwo, akadachidziwa omwe amafufuzafufuza zinthu mwa iwo (kuti kodi nzoyenera kuzifalitsa kapena ayi). Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, ndithudi, mukadamtsatira satana kupatula ochepa
“Choncho menya nkhondo pa njira ya Allah, suukukakamizidwa (za anthu ena) koma iwe mwini, ndipo akhwirizire Asilamu. Ndithu Allah angatsekereze mtopola wa omwe sadakhulupirire. Ndipo Allah Ngwaukali kwambiri pomenya nkhondo ndiponso Wolanga kwabasi
“Allah! Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi. Ndithudi, adzakusonkhanitsani tsiku la chiweruziro lopanda chikaiko mwa ilo. Kodi ndani ali onena zoona kuposa Allah
“Muzawapeza ena omwe akufuna kupeza chitetezo kwa inu ndi kupeza chitetezo kwa anthu awo. Nthawi iliyonse akabwezedwa ku ukafiri (ndi anzawo osakhulupirira), amagweramo mwamtheradi (nkuyamba kumenyananso ndi inu), ngati sadzipatula kwa inu ndipo osakupatsani mtendere ndi kutsekereza manja awo, agwireni ndi kuwapha paliponse pamene mwawapeza (monga momwe iwo akuchitira kwa inu) ndipo takupangirani chisonyezo choonekera pa iwo
“Ndipo amene angaphe wokhulupilila mwadala, mphoto yake ndi Jahannam; mmenemo adzakhala nthawi yaitali. Ndipo Allah amkwiira ndi kumtembelera ndi kumkonzera chilango chachikulu
“Sangafanane okhulupirira omwe akukhala osapita kunkhondo pomwe sali ovutika, ndi amene akumenya nkhondo yoyera pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo. Allah wawatukula pa ubwino ndi pa nyota amene akuchita Jihâd ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo kuposa okhala. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino. Koma wawapambanitsa ochita Jihâd malipiro aakulu kuposa ongokhala
“Ndipo amene angasamuke pa njira ya Allah (chifukwa cha chipembedzo chake,) apeza malo ambiri m’dzikomo othawira ndikupeza bwino. Ndipo amene angatuluke m’nyumba mwake kuti asamuke chifukwa cha Allah ndi Mtumiki Wake, kenako nkumpeza imfa (m’njira), ndithu malipiro ake atsimikizika kwa Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha
“Akudzibisa kwa anthu (pochita za machimo) koma sakuzibisa kwa Allah pomwe Iye adali nawo pamodzi pamene adali kupangana usiku mawu osakondweretsa. Allah akudziwa bwinobwino zimene akuchita
“Taonani! Inu ndi amene mwaayikira kumbuyo pa moyo wa pa dziko lapansi. Kodi ndani amene adzatsutsana ndi Allah pa iwo tsiku lachimaliziro, kapena ndani adzakhale mtetezi wawo
“Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chisoni chake pa iwe, ndithudi, gulu limodzi la iwo likadalinga kukusokeretsa. Ndipo iwo palibe yemwe akadamsokeretsa koma iwo okha basi. Ndipo sangathe kukuvutitsa ndi chilichonse. Ndipo Allah wakuvumbulutsira buku, kudzanso luntha. Ndipo wakuphunzitsa zomwe sudali kuzidziwa. Ndipo ubwino wa Allah umene uli pa iwe ngwaukulu zedi
“Ndithudi, Allah sakhululuka (uchimo) womphatikiza ndi chinthu china, (pochiyesa kuti ndi mnzake wa Allah). Koma Iye amakhululukira machimo ena omwe sali amenewo kwa yemwe wamfuna. Ndipo yemwe angamphatikize Allah (ndi milungu yabodza), ndithudi, wasokera kusokera konka nako kutali (ndi njira yachoonadi)
“Ndipo omwe akhulupirira ndi kumachita zabwino, tidzawalowetsa ku Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. Adzakhala m’menemo muyaya. Ili ndilonjezo loona la Allah. Kodi ndani woona ponena kuposa Allah
“(Kulowa ku Munda wamtendere) sikuli pa kukhumba kwanu ngakhalenso pa kukhumba kwa anthu a buku (Ayuda ndi Akhrisitu). Amene angachite choipa, adzalipidwa (nacho), ndipo sadzapeza mtetezi ngakhale mpulumutsi kupatula Allah
“Kodi ndani yemwe ali ndi chipembedzo chabwino choposa yemwe walunjika nkhope yake kwa Allah, iye ali wochita zabwino ndipo akutsata njira ya Ibrahim woona pa chikhulupiliro. Ndipo Allah adasankha Ibrahim kukhala bwenzi
“Ndipo akukufunsa zomwe zikukhudza azimayi nena: “Allah akukuuzani nkhani za iwo ndi zomwe zikuwerengedwa kwa inu m’buku (ili) za akazi amasiye omwe simukuwapatsa (chiwongo chawo) chomwe chidalamulidwa kwa iwo, komabe mukufuna kuwakwatira, ndi za ana omwe ali ofooka ndi oponderezedwa; ndipo (akukuuzani) kuti limbikirani kuwayang’anira ana amasiye mwachilungamo. Ndipo chabwino chilichonse chimene muchita, Allah akuchidziwa
“Zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndithudi, tidawalangiza omwe adapatsidwa buku patsogolo panu ndi inunso kuti muopeni Allah. Koma ngati mungakane, ndithudi, zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndipo Allah Ngokhupuka kwabasi Wotamandidwa
“Amene afuna mphoto ya dziko lapansi, (afunefune kwa Allah). Kwa Allah ndikumene kuli mphoto ya pa dziko lapansi ndi ya tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngopenya
“Ndithudi Iye wakuvumbulutsirani m’buku (ili) kuti mukamva ma Ayah (ndime) a Allah akukanidwa ndi kuchitiridwa chipongwe, musakhale pamodzi nawo mpaka alowe m’zokamba zina. (Ngati mutakhala nawo) ndiye kuti mukhala chimodzimodzi ndi iwo. Ndithudi, Allah adzawasonkhanitsa achiphamaso ndi osakhulupirira onse m’moto wa Jahannam
“Ndithu achiphamaso akufuna kunyenga Allah koma Iye awalanga (chifukwa cha chinyengo chawocho). Ndipo akaimilira kupemphera Swala, amaimilira mwaulesi ndikungoonetsa anthu (kuti akupemphera). Ndipo satchula Allah koma pang’ono pokha
“Akungoyendayenda pakati pa awa ndi awa (pakati pa Asilamu ndi osakhulupirira). Iwo sali mbali iyi kapena mbali inayo. Ndipo amene Allah wamlekelera kuti asokere sungampezere njira yolungama
“Kupatula amene alapa (pambuyo pa uchiphamaso wawo); nakonza (makhalidwe awo) nadziphatika kwa Allah; namuyeretseranso Allah chipembedzo chawo. Choncho iwo ali pamodzi ndi okhulupirira. Ndipo Allah adzapatsa okhulupirira malipiro akulu
“Ndithudi amene sakhulupirira Allah ndi atumiki Ake, ndikumafuna kulekanitsa pakati pa Allah ndi atumiki Ake, ndikumanena kuti: “Ena tikuwakhulupirira, koma ena tikuwakana,” ndikumafunanso kukhonza njira yapakati pa zimenezo
“Ndipo tidatukula phiri la Al-Tur pamwamba pawo (Ayudawo) polandira pangano lawo; tidati kwa iwo: “Lowani pachipata (cha dziko ili la Sham) mutawerama.” Tidatinso kwa iwo: “Musalumphe malire pa nkhani ya Sabata.” Ndipo tidalandira kwa iwo pangano lokhwima
“Choncho (tidawalanga) chifukwa chakuswa mapangano awo, ndi kukana kwawo zisonyezo za Allah, ndi kupha kwawo aneneri popanda choonadi, ndi kunena kwawo kwakuti: “Mitima yathu yakutidwa (siingathe kuzindikira zomwe ukunena iwe Muhammad {s.a.w}).” (Ai, Siinakutidwe ndi chilichonse), koma Allah waidinda zidindo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo; tero sakhulupirira koma pang’ono pokha
“Ndikuyankhula kwawo (kwakuti): “Ife tamupha Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, Mtumiki wa Allah; pomwe sadamuphe ndipo sadampachike pa mtanda. Koma adasokonezedwa (ndi munthu wina namuganizira kuti ndi Isa (Yesu). Ndithudi, amene akutsutsana pankhaniyi (Ayuda ndi Akhrisitu) ali m’chikaiko pa iyo; alibe kudziwa kotsimikizika, koma akungotsatira zongoganizira. Ndipo, sadamuphe mosimikiza (kuti ndi iye)
“Palibe aliyense mwa anthu omwe adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) koma kuti azamkhulupirira iye (Yesu kuti sadali mulungu) imfa yake (Yesuyo) isadadze (izi zizachitika pamene Yesuyo azabwerenso padziko lapansi kumapeto kwa dziko). Nayenso (Yesu) pa siku la chiweruziro adzaikira umboni pa iwo (kuti iye adali chabe kapolo wa Allah)
“Koma mwa iwo amene azama pa maphunziro, ndi okhulupirira (onsewo) akukhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zimene zidavumbulutsidwa patsogolo pako. Ndipo omwe akupitiriza kupemphera Swala, ndi kupereka Zakaati, ndi kukhulupirira Allah komanso tsiku lachimaliziro, iwo tidzawapatsa malipiro aakulu
“Ndipo (tidavumbulutsanso chivumbulutso) kwa atumiki omwe takusimbira kale nkhani zawo komanso kwa atumiki ena omwe sitinakusimbire (nkhani zawo); ndipo Allah adayankhula ndi Mûsa mwachindunji
“E inu anthu! Ndithu Mtumiki wakudzerani ndi choonadi chochokera kwa Mbuye wanu. Choncho khulupirirani; ndi bwino kwa inu kutero. Koma ngati mukana, (dziwani kuti) zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri Ngwanzeru zakuya
“E inu anthu a buku! Musamalumphe malire pa chipembedzo chanu. Ndipo musamamnenere Allah koma zowona (zokhazokha). Ndithu Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, ndi mtumiki wa Allah (ndiponso ndi munthu wolengedwa) ndi liwu Lake lomwe adaliyika mwa Mariya ndiponso (ali) ndi mzimu (moyo) wochokera kwa Iye (Allah, monga mizimu ina yonse imachokera kwa Iye). Choncho Khulupirirani Allah ndi atumiki Ake. Musamanene: “Utatu wa Mulungu;” siyani, (zikhululupiliro za utatu wa Mulungu), kutero ndibwino kwa inu. Ndithudi, Allah ndi Mulungu m’modzi (basi). Ulemelero wake ngotukuka kutali ndi kukhala ndi mwana. Nzake zonse za kumwamba ndi pansi. Ndipo Allah ndiMtetezi Wokwanira
“Mesiya (Mneneri Isa {Yesu}) sangaone kunyozeka kukhala kapolo wa Allah, ngakhalenso angelo oyandikitsidwa (kwa Allah). Ndipo amene angaone kunyozeka pa ukapolo wake kwa Allah nadzitukumula, onse adzawasonkhanitsa kwa Iye (ndipo kenako nkuwalonga kung’anjo ya Moto)
“Koma amene adamkhulupirira (Yesuyo) ndi kuchita zabwino adzawapatsa malipiro ao mokwanira ndi kuwaonjezera mu zabwino Zake. Koma amene adaona kunyozeka (pokhala kapolo wa Allah) nadzitukumula, adzawalanga chilango chowawa; ndipo sadzapeza bwenzi ngakhale mtetezi kupatula Allah
“Tsono amene akhulupirira Allah ndi kudziphatika kwa Iye, iwo adzawalowetsa ku chifundo ndi kuzabwino zochokera kwa Iye, ndikuwatsogolera kwa Iye njira yoongoka