Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 40 - Ghafir
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Ghafir 40:1
Verse 2 — Surah Ghafir 40:2
“Kuvumbulutsidwa kwa buku (ili) kwachokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri
Verse 3 — Surah Ghafir 40:3
“Wokhululuka machimo, Wolandira kulapa (kwa yemwe walapa), Wolanga mwaukali (kwa yemwe wapitiriza kunyoza Allah), Mwini kupereka mtendere. Palibe wopembedzedwa mwa choona koma Iye; kobwerera nkwa Iye
Verse 4 — Surah Ghafir 40:4
“Sangatsutsane pa zisonyezo za Allah kupatula amene akanira. Choncho kusakunyenge kuyendayenda kwawo pa dziko (kunka nachita malonda ndi kupeza phindu lalikulu ndi malondawo popanda chovuta; posachedwa tiwalanga)
Verse 5 — Surah Ghafir 40:5
“Iwo kulibe, anthu a Nuh adakaniranso pamodzi ndi makamu a anthu omwe adali kuda aneneri, m’badwo wa Nuh utatha; ndipo m’badwo uliwonse udaikira mtima kuchita choipa pa mneneri wawo kuti am’gwire (ndi kumupha). Adali kutsutsana poteteza chachabe kuti ndi uwo (mtsutso wawowo) achotse choona. Ndipo ndidawaononga kotheratu. Tayang’ana, chidali bwanji chilango Changa (pa iwo)
Verse 6 — Surah Ghafir 40:6
“Chonchonso latsimikizika liwu la chilango pa amene akanira (iwe Mtumiki {s.a.w}) chifukwa iwo ndi anthu a ku Moto (kamba kosankhakukanira ndi kusiya kukhulupirira)
Verse 7 — Surah Ghafir 40:7
“Amene akusenza Arsh (Mpando wachifumu) ndi amene ali mmphepete mwake, akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndiponso akumkhulupirira Iye; ndipo akupemphera chikhululuko amene akhulupirira (ponena kuti): “E Mbuye wathu! Chifundo ndi kudziwa kwanu kwakwanira pa chinthu chilichonse. Khululukirani amene alapa ndi kutsatira njira Yanu; ndipo apewetseni ku chilango cha Jahena!”
Verse 8 — Surah Ghafir 40:8
““E Mbuye wathu! Alowetseni ku Minda yamuyaya imene mudawalonjeza, ndi amene adachita zabwino mwa makolo awo ndi akazi awo ndi ana awo. Ndithu inu ndi Amphamvu zoposa, Anzeru zakuya.”
Verse 9 — Surah Ghafir 40:9
““Ndipo apewetseni ku zoipa; tsono amene mudzampewetsa ku zoipa tsiku limenelo, ndiye kuti mwamchitira chifundo. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.”
Verse 10 — Surah Ghafir 40:10
“Ndithu amene akanira adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Mkwiyo wa Allah pa inu udali waukulu kuposa mkwiyo wanu pa mitima yanu (yomwe yakulowetsani ku chilango) pamene mudali kuitanidwa ku chikhulupiliro, (ku Chisilamu); ndipo mudali kukanira.”
Verse 11 — Surah Ghafir 40:11
“Adzanena: “E Mbuye wathu! Mudatipatsa imfa kawiri; (imfa yoyamba tisanabadwe, ndipo imfa ya chiwiri pa dziko). Ndipo mudatipatsa moyo kawiri; (moyo woyamba wa pa dziko lapansi, ndipo moyo wachiwiri wakuuka kwa akufa). Choncho tavomereza machimo athu. Kodi pali njira yotulukira (ku chilango kuno)?”
Verse 12 — Surah Ghafir 40:12
“Zimenezi nchifukwa chakuti akapemphedwa Allah Yekha, mudali kutsutsa. Koma akaphatikizidwa (ndi milungu yabodza) mudali kukhulupirira. Choncho chiweruzo ncha Allah, Wotukuka, Wamkulu
Verse 13 — Surah Ghafir 40:13
“Iye ndi Yemwe akukuonetsani zisonyezo Zake (zosonyeza mphamvu Yake yoposa), ndipo akukutsitsirani madzi kumwamba chifukwa cha inu kuti abweretse zokupatsani moyo (monga chakudya ndi zina). Koma palibe amene akukumbukira kwenikweni kupatula amene watembenukira (kwa Allah)
Verse 14 — Surah Ghafir 40:14
“Choncho mpempheni Allah pomuyeretsera mapemphero Ake ngakhale (kumuyeretsera kwanu kwa mapempheroko) kuwaipire okanira
Verse 15 — Surah Ghafir 40:15
“Iye Ngotukuka ulemelero, Mwini Arsh (Mpando wachifumu); amapereka chivumbulutso (Chake) mwa lamulo lake kwa yemwe wamfuna mwa akapolo Ake kuti achenjeze (anthu za) tsiku lokumana (anthu onse)
Verse 16 — Surah Ghafir 40:16
“Tsiku lomwe iwo adzaonekera poyera (kwa Allah). Ndipo palibe chilichonse chidzabisidwa kwa Allah (mzinthu zawo). (Ndipo adzamva kufunsa koopsa ndi yankho loopsa): “Kodi ufumu ngwayani lero? Ngwa Allah, Mmodzi yekha, Wogonjetsa, (woweruza mmene akufunira kwa anthu Ake).”
Verse 17 — Surah Ghafir 40:17
“Mzimu uliwonse lero, ulipidwa zimene udachita; palibe kupondereza lero (pochepetsa mphoto kapena kuonjeza chilango). Ndithu Allah Ngwachangu (pa) chiwerengero Chake
Verse 18 — Surah Ghafir 40:18
“Achenjeze (iwe Mtumiki {s.a.w}) za tsiku lomwe lili pafupi (Qiyâma), pamene mitima idzakhala ku mmero (chifukwa cha mantha oopsa) atadzadzidwa ndi nkhawa. Wodzichitira chinyengo sazakhala ndi bwenzi ngakhale mpulumutsi womveredwa (powateteza iwo)
Verse 19 — Surah Ghafir 40:19
“Iye (Allah ) akudziwa kuyang’ana kwa maso a chinyengo ndi zimene zifuwa zikubisa (mzobisika zonse)
Verse 20 — Surah Ghafir 40:20
“Ndipo Allah amaweruza mwa chilungamo. Koma omwe akuwapembedza kusiya Allah, saweruza chilichonse (chifukwa cha kufooka ndi kulephera kwawo). Ndithu Allah Yekha ndiye Wakumva, Woona (chilichonse)
Verse 21 — Surah Ghafir 40:21
“Kodi sadayende padziko ndikuona momwe mathero a anthu akale adalili? Adali opambana panyonga ndi mzochitachita zawo za mdziko kuposa iwo, (monga kumanga nyumba zikuluzikulu). Koma Allah adawaononga, psiti! chifukwa cha machimo awo, ndipo adalibe mtetezi ku chilango cha Allah
Verse 22 — Surah Ghafir 40:22
“Zimenezo nchifukwa chakuti ankawadzera aneneri awo ndi zizizwa zoonekera poyera, koma adazikanira. Choncho Allah adawaononga motheratu. Iye Ngwanyonga zambiri, Wolanga mokhwima
Verse 23 — Surah Ghafir 40:23
“Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa ndi zizizwa zathu ndi zisonyezo zamphamvu zoonekera poyera
Verse 24 — Surah Ghafir 40:24
“Kwa Farawo ndi Haamana ndi Kaaruna. Ndipo adati: “(Uyu) ndi wamatsenga, wabodza.”
Verse 25 — Surah Ghafir 40:25
“Ndipo pamene (Mûsa) adawadzera ndi choona chochokera kwa Ife, (Farawo pamodzi ndi omtsatira) adati: “Iphani ana achimuna a amene akhulupirira naye limodzi; ndipo siyani ana awo achikazi.” Koma ndale za okanira sizakanthu, nzotaika
Verse 26 — Surah Ghafir 40:26
“Ndipo Farawo adati: “Ndilekeni ndimuphe Mûsa; ampemphe Mbuye wakeyo (kuti ampulumutse kwa ine). Ine ndikuopera kuti angasinthe chipembedzo chanu, kapena kufalitsa chisokonezo pa dziko.”
Verse 27 — Surah Ghafir 40:27
“Ndipo Mûsa adati (kwa Farawo pa modzi ndi anthu ake): “Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye wanga amenenso ali Mbuye wanu (ku chiwembu) chochokera kwa aliyense wodzikweza, wosakhulupirira za tsiku la chiwerengero
Verse 28 — Surah Ghafir 40:28
“Ndipo munthu wokhulupirira, wochokera kubanja la Farawo yemwe adali kubisa chikhulupiliro chake, adawalankhula (anthu ake): “Kodi muphe munthu chifukwa chakuti iye akunena kuti: ‘Mbuye wanga ndi Allah,’ chikhalirecho wakubweretserani zisonyezo zoonekera poyera, zochokera kwa Mbuye wanu? Ndipo ngati ali wabodza pa zomwe akunena ndiye kuti kuipa kwa bodzalo kum’bwerera yekha. Koma ngati ali woona (pazomwe akukulonjezani), ndiye kuti gawo lina la zomwe (chilango) akukulonjezani likupezani; ndithu Allah saongola munthu wopyola malire, wabodza la mkunkhuniza!”
Verse 29 — Surah Ghafir 40:29
““E inu anthu anga! Ufumu walero ngwanu: mwagonjetsa dziko (la Iguputo). Ndani amene angatipulumutse ku chilango cha Allah ngati chitatidzera?” Farawo adati: “Sindikukupatsani maganizo koma okhawo ndikuwaona (kuti ndi abwino) ndiponso sindikukuwongolerani koma kunjira yoongoka.”
Verse 30 — Surah Ghafir 40:30
“Ndipo munthu wokhulupirira uja adanena: “E inu anthu anga! Ine ndikukuoperani (za tsiku la masautso) monga tsiku la magulu (omwe adaukira aneneri awo).”
Verse 31 — Surah Ghafir 40:31
““Monga chikhalidwe cha anthu a Nuh, Âdi, Samudi ndi anthu omwe adadza pambuyo pawo. Koma Allah safuna kupondereza akapolo Ake.”
Verse 32 — Surah Ghafir 40:32
““Ndiponso anthu anga! Ine ndikukuoperani tsiku la kuitanizana (anthu).”
Verse 33 — Surah Ghafir 40:33
““Tsiku limene mudzathawa ndi kutembenuza misana yanu; pomwe simudzakhala ndi mtetezi ku chilango cha Allah; ndipo amene Allah wamulekelera kusokera (chifukwa cha zochita zake zoipa), ndiye kuti sangapeze muongoli.”
Verse 34 — Surah Ghafir 40:34
“Ndithu adakudzerani kale Yûsuf ndi zisonyezo zoonekera poyera (Mûsa asadadze). Koma simudaleke kuzikaikira zimene adadza nazo kwa inu, kufikira pamene adamwalira, mudati: “Allah sadzatumiza mneneri wina pambuyo pake.” Motero Allah amamulekelera kusokera yemwe ali opyola malire poononga, wokaikira kwambiri
Verse 35 — Surah Ghafir 40:35
“Amene akutsutsana za zisonyezo za Allah popanda umboni uliwonse umene wawadzera. (Kutsutsa zisonyezo za Allah) nchokwiitsa Allah kwakukulu ndi kwa amene akhulupirira (mwa Allah). Momwemo ndi momwe Allah amadindira pamtima wa aliyense wodzikuza, wodzitukumula
Verse 36 — Surah Ghafir 40:36
“Ndipo Farawo adati: “E iwe Haamana! Ndimangire chipilala kuti ndikafike kunjira,”
Verse 37 — Surah Ghafir 40:37
““Njira za kumwamba kuti ndikamuone Mulungu wa Mûsa. Koma ndithu ine ndikudziwa kuti ameneyu ngonama.” Umo ndi momwe zochita zoipa za Farawo zidakongoletsedwera kwa iye, ndipo adatsekeretsedwa ku njira yoona, ndipo chiwembu cha Farawo sichakanthu, koma choonongeka
Verse 38 — Surah Ghafir 40:38
“Ndipo uja adakhulupirira adati: “E inu anthu anga! Nditsatireni; ndikuongolerani ku njira yoongoka.”
Verse 39 — Surah Ghafir 40:39
““E inu anthu anga! Ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndichisangalalo (chakutha). Ndithu tsiku lachimaliziro ndiye nyumba yokhazikikamo.”
Verse 40 — Surah Ghafir 40:40
““Amene akuchita choipa sadzalipidwa chinachake koma chofanana ndi chomwe adachita. Ndipo yemwe akuchita zabwino, mwamuna kapena mkazi, uku iye ali okhulupirira, iwowo adzalowa ku Minda ya mtendere. Adzapatsidwa zopatsidwa mmenemo zopanda chiwerengero.”
Verse 41 — Surah Ghafir 40:41
““E inu anthu anga! Chifukwa ninji, ine ndikukuitanirani ku chipulumutso ndipo inu mukundiitanira ku Moto?”
Verse 42 — Surah Ghafir 40:42
““Mukundiitanira kuti ndimkane Allah, ndi kuphatikiza ndi milungu yonama yomwe ine sindikuidziwa, pomwe ine ndikukuitanirani kwa Mwini mphamvu zoposa, Wokhululuka kwambiri?”
Verse 43 — Surah Ghafir 40:43
““Palibe chikaiko, ndithu zomwe mukundiitanirazo (kuti ndizipembedze) zilibe (kuyankha) pempho lililonse pano pa dziko lapansi ngakhale tsiku lachimaliziro. Ndipo kobwerera kwathu nkwa Allah basi. Ndipo, wopyola malire (a Allah) iwowo ndiwo anthu a ku Moto.”
Verse 44 — Surah Ghafir 40:44
““Choncho posachedwa, mudzakumbukira zimene ndikukuuzanizi. Ndipo ine ndikutula zinthu zanga kwa Allah, ndithu Allah akuona za anthu Ake.”
Verse 45 — Surah Ghafir 40:45
“Choncho Allah adam’teteza ku zoipa zomwe adam’tchera. Ndipo chilango choipa chidawazungulira anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini)
Verse 46 — Surah Ghafir 40:46
“Zilango za kumoto zikusonyezedwa kwa iwo mmawa ndi madzulo. Ndipo tsiku lomwe Qiyâma idzafika (kudzanenedwa): “Alowetseni anthu a Farawo ku chilango cha ukali kwambiri (choposa chomwe adalandira mmanda mwawo).”
Verse 47 — Surah Ghafir 40:47
“Ndipo (akumbutse) pamene azidzatsutsana m’Moto! Pamene ofooka (amene amatsatira) adzanena kwa omwe adali kudzikweza: “Ndithu ife tidali otsatira anu; kodi simungathe kutichotsera gawo lina la chilango cha Moto?”
Verse 48 — Surah Ghafir 40:48
“Awo amene adadzikweza adzati: “Ndithu ife tonse tili mommuno. Ndithu Allah waweruza kale pakati pa akapolo (Ake). (Choncho palibe chilichonse chimene tingaphulepo).”
Verse 49 — Surah Ghafir 40:49
“Ndipo a ku Moto adzayankhula kwa (angelo) olondera Jahannam: “Mpempheni Mbuye wanu, atipeputsire chilangochi tsiku limodzi.”
Verse 50 — Surah Ghafir 40:50
“(Alonda aja) adzati: “Kodi sadakudzereni aneneri anu ndi umboni oonekera poyera?” Iwo adzati: “Inde, (adatidzera. Koma ife tidanyoza).” (Ndipo) adzawauza: “Choncho pemphani nokha. Koma pempho la okanira silili la kanthu, ndi lotaika basi.”
Verse 51 — Surah Ghafir 40:51
“Ndithu Ife timapulumutsa aneneri Athu ndi amene akhulupirira pa moyo wa dziko lapansi ndi tsiku limene zidzaimilira mboni (kupereka umboni)
Verse 52 — Surah Ghafir 40:52
“Tsiku limene achinyengo sadzawathandiza madandaulo awo, ndipo matembelero adzakhala pa iwo, ndipo pokhala pawo padzakhala poipa kwambiri
Verse 53 — Surah Ghafir 40:53
“Ndithu Mûsa tidampatsa chiongoko, ndipo tidawasiira buku ana a Israyeli
Verse 54 — Surah Ghafir 40:54
“(Lomwe lidali) chiongoko ndi chikumbutso kwa eni nzeru
Verse 55 — Surah Ghafir 40:55
“Choncho pirira, ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Ndipo pempha chikhululuko cha machimo ako (ukachimwa), ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda madzulo ndi m’mawa
Verse 56 — Surah Ghafir 40:56
“Ndithu amene akutsutsana pa zisonyezo za Allah popanda umboni umene udawadzera, mmitima mwawo mulibe chilichonse koma kudzitukumula (ndikufuna ukulu), koma saufikira. Dzitchinjirize mwa Allah, ndithu Iye Ngwakumva, Ngopenya
Verse 57 — Surah Ghafir 40:57
“Ndithu kulenga kwa thambo ndi nthaka nkwakukulu kuposa kulenga kwa anthu. Koma anthu ambiri sakudziwa
Verse 58 — Surah Ghafir 40:58
“Ndipo sali wolingana wakhungu ndi wopenya ndiponso amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi wochita zoipa. Zimene inu mukumbukira nzochepa, ndithu
Verse 59 — Surah Ghafir 40:59
“Ndithu Qiyâma idza; ndipo za iyo palibe chikaiko. Koma anthu ambiri sakhulupirira
Verse 60 — Surah Ghafir 40:60
“Ndipo Mbuye wanu wanena: “Ndipempheni, ndikuyankhani; koma amene akudzikweza posiya kundipembedza, adzalowa ku Jahannam ali oyaluka.”
Verse 61 — Surah Ghafir 40:61
“Allah ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti mupumule mmenemo, ndi usana kukhala wounika (kuti muthe kuchita ntchito zanu). Ndithu Allah ndi Mwini kupereka ufulu kwa anthu. Koma anthu ambiri sathokoza
Verse 62 — Surah Ghafir 40:62
“Iyeyo ndiye Allah, Mbuye wanu; Mlengi wa chilichonse palibe wina wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Nanga kodi mukutembenuzidwa chotani (kuchoka ku zoona)
Verse 63 — Surah Ghafir 40:63
“Momwemo ndi mmene adatembenuziridwa amene adali kutsutsa zisonyezo za Allah
Verse 64 — Surah Ghafir 40:64
“Allah ndi Amene adakupangirani nthaka kukhala pamalo anu okhalapo, ndi thambo kukhala ngati denga (losagwa); ndipo adakujambulani maonekedwe ndikukongoletsa maonekedwe anu; ndipo adakupatsani zinthu zabwino. Ameneyo ndiye Allah, Mbuye wanu. Choncho walemekezeka Allah, Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 65 — Surah Ghafir 40:65
“Iye Ngwamoyo Wamuyaya; palibe wopembedzedwa wina, koma Iye. Choncho mpembedzeni momuyeretsera chipembedzo. (Musapembedze milungu ina mophatikiza ndi Iye). Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa
Verse 66 — Surah Ghafir 40:66
“Nena: “Ine ndaletsedwa kupembedza amene mukuwapembedza kusiya Allah, pamene zidandidzera zisonyezo zoonekera kuchokera kwa Mbuye wanga; ndipo ndalamulidwa kugonjera Mbuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 67 — Surah Ghafir 40:67
“Iye ndi Amene adakulengani kuchokera ku dothi, kenako kuchokera ku dontho la umuna, kenako kuchokera mmagazi; kenako ndikukutulutsani muli khanda; ndipo kenako (adakusiyani) kuti mufike nthawi yanyonga zanu. Ndipo kenako (adakulekani) kuti mukhale nkhalamba. Ndipo ena a inu amapatsidwa imfa asadaifike (nthawi ya ukalamba) nkuti muifikire nthawi imene yaikidwa; (zoterezi nkuti inu) mukhale ndi nzeru
Verse 68 — Surah Ghafir 40:68
“Iye ndi Yemwe amapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo akafuna kuchita chinthu ndithu amanena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo chimachitika
Verse 69 — Surah Ghafir 40:69
“Kodi sukuona amene akutsutsana za zisonyezo za Allah? Kodi nchotani akutembenuzidwa (kusiya choonadi)
Verse 70 — Surah Ghafir 40:70
“Amene alitsutsa buku ndi zomwe tidawatuma nazo atumiki athu; koma posachedwa adziwa
Verse 71 — Surah Ghafir 40:71
“Pamene magoli ali m’makosi mwawo ndi unyolo (uli mmiyendo) akukokedwa
Verse 72 — Surah Ghafir 40:72
“M’madzi otentha, kenako m’moto akuotchedwa
Verse 73 — Surah Ghafir 40:73
“Kenako adzauzidwa: “Ili kuti (milungu) imene mudali kuiphatikiza (ndi Allah),”
Verse 74 — Surah Ghafir 40:74
““Mmalo mopembedza Allah?” Adzanena: “Yatisowa, koma chiyambire kale sitidali kupembedza chilichonse (kupatula Inu).” Umo ndi momwe Allah akuwalekelera kusokera okanira
Verse 75 — Surah Ghafir 40:75
““Izi, (zimene zakupezani ku Moto kuno), nchifukwa chakuti mudali kudzikweza pa dziko mosayenera. Ndiponso chifukwa chakuti mudali kunyada
Verse 76 — Surah Ghafir 40:76
“Lowani m’makomo a Jahannam; mukhala mmenemo nthawi yaitali. Taonani kuipa malo a odzikweza!”
Verse 77 — Surah Ghafir 40:77
“Chonco pirira, ndithu lonjezo la Allah ndiloona. Mwina tikusonyeza zina mwa zomwe tawalonjeza, kapena tikupatsa imfa (usadazione. Basi, palibe chikaiko, zichitika chifukwa chakuti onse) adzabwezedwa kwa Ife
Verse 78 — Surah Ghafir 40:78
“Ndithu tidawatuma atumiki patsogolo pako; ena mwa iwo tidakusimbira (nkhani zawo ndi maina awo). Ena mwa iwo sitidakusimbire. Sikudali kotheka kwa mtumiki aliyense kudzetsa chozizwitsa mwa yekha, koma ndi chifuniro cha Allah. Ndipo lamulo la Allah likadzadza, kudzaweruzidwa mwa choonadi. Ndipo ochita zachabe panthawi imeneyo adzataika; (adzaluza)
Verse 79 — Surah Ghafir 40:79
“Allah ndi Yemwe wakupangirani nyama kuti mudzizikwera zina mwa izo, ndipo zina mwa izo kuti muzidya
Verse 80 — Surah Ghafir 40:80
“Ndipo mmenemo mulinazo zokuthandizani zambiri; ndipo kupyolera mzimenezo mukupeza zokhumba za mitima yanu; pa izo, ndi pa zombo, mukunyamulidwa
Verse 81 — Surah Ghafir 40:81
“Ndipo (Iye) amakuonetsani zisonyezo Zake. Kodi ndi ziti m’zisonyezo za Allah zimene mukuzikana
Verse 82 — Surah Ghafir 40:82
“Kodi sadayende padziko ndikuona momwe adalili mathero a omwe adali patsogolo pawo? Adali ochuluka kwambiri kuposa iwo; ndiponso adali anyonga kwambiri ndi ochulukitsa zomangamanga mdziko. Koma sizidawathandize zimene adali kuchita
Verse 83 — Surah Ghafir 40:83
“Koma pamene atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera, adakondwera ndi kudziwa komwe adali nako, (ndipo sadalabadire zomwe atumiki adadza nazo). Choncho zidawazinga zimene adali kuzichitira chipongwe
Verse 84 — Surah Ghafir 40:84
“Ndipo pamene adachiona chilango Chathu, adanena (kuti): “Takhulupirira mwa Allah Yekha, ndipo tikuzikana zimene tidali kumphatikiza nazo.”
Verse 85 — Surah Ghafir 40:85
“Koma chikhulupiliro chawo sichidali chowathandiza panthawi imeneyo, pomwe adali atachiona kale chilango Chathu. Ichi ndi chizolowezi cha Allah chomwe chidapita pa akapolo (Ake onse kuti chilango chikadza, kulapa sikuvomerezedwa). Choncho pamenepo, okanira adaluza