Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 43 - Az-Zukhruf
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Az-Zukhruf 43:1
“. Hâ-Mîm
Verse 2 — Surah Az-Zukhruf 43:2
“Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka
Verse 3 — Surah Az-Zukhruf 43:3
“Ndithu Ife talichita bukuli (Qur’an) kukhala chowerengedwa m’Chiarabu kuti muzindikire
Verse 4 — Surah Az-Zukhruf 43:4
“Ndipo ndithu bukuli (Qur’an) lili m’manthu wa mabuku onse (Lawhi Mahfudh) limene lili kwa Ife; (ndipo ndi buku) lotukuka, la mawu anzeru
Verse 5 — Surah Az-Zukhruf 43:5
“Kodi tisiye kukukumbutsani chifukwa chakuti ndinu anthu opyola malire (pochita zoipa)
Verse 6 — Surah Az-Zukhruf 43:6
“Ndipo tidatumiza aneneri ambiri kwa anthu akale
Verse 7 — Surah Az-Zukhruf 43:7
“Ndipo palibe mneneri aliyense amene amawadzera koma amam’chitira chipongwe
Verse 8 — Surah Az-Zukhruf 43:8
“Choncho tidawaononga amene adali amphamvu kuposa iwo (Aquraish) ndipo ladutsa fanizo la (zilango zomwe zidawapeza) anthu akale
Verse 9 — Surah Az-Zukhruf 43:9
“Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu ayankha kuti: “Adazilenga (Allah) Mwini Mphamvu, Wodziwa.”
Verse 10 — Surah Az-Zukhruf 43:10
“Amene wakupangirani nthaka kukhala choyala ndipo adakupangirani njira mmenemo kuti muongoke (ndikukafika kumene mukufuna)
Verse 11 — Surah Az-Zukhruf 43:11
“Ndiponso amene watsitsa madzi kuchokera kumwamba mwamuyeso; chifukwa cha madziwo tidaukitsa mudzi wakufa. Momwemonso inu mudzatulutsidwa (mmanda)
Verse 12 — Surah Az-Zukhruf 43:12
“Ndiponso amene walenga zinthu zonse ziwiriziwiri (chachimuna ndi chachikazi). Ndipo adakupangirani zombo ndi ziweto zimene mukukwera
Verse 13 — Surah Az-Zukhruf 43:13
“Kuti mukhazikike mwaubwino pamisana paizo, kenako mukumbukire mtendere wa Mbuye wanu mukakhazikika pamenepo, ndipo munene: “Walemekezeka Amene watifewetsera ichi; ndipo sitikadatha kuchifewetsa ndi kuchigwiritsa ntchito.”
Verse 14 — Surah Az-Zukhruf 43:14
““Ndipo ndithu ife kwa Mbuye wathu ndiko kobwerera.”
Verse 15 — Surah Az-Zukhruf 43:15
“Ndipo amuikira gawo mwa akapolo Ake. (Kuti ndi ana a Allah.) Ndithu munthu, ngwamsulizo woonekera poyera
Verse 16 — Surah Az-Zukhruf 43:16
“Kodi wadzichitira ana achikazi mzimene wazilenga ndipo wakusankhirani inu ana achimuna
Verse 17 — Surah Az-Zukhruf 43:17
“Koma akauzidwa (kuti wabereka mwana wamkazi) mmodzi wa iwo chomwe amamfanizira (Allah) Wachifundo chambiri, nkhope yake imakhala yakuda ndi kudandaula kwambiri
Verse 18 — Surah Az-Zukhruf 43:18
“Ha! Kodi amene waleredwa monga chokongoletsa, potsutsana iye sangathe kunena momveka? (Ameneyo ndiye mwampatsa Allah; omwe ndi ana aakazi)
Verse 19 — Surah Az-Zukhruf 43:19
“Ndipo angelo omwe ndi akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri akuwatcha akazi. Kodi adaona kalengedwe kawo? Umboni wawo ulembedwa ndipo adzafunsidwa (pazimenezo)
Verse 20 — Surah Az-Zukhruf 43:20
“Ndipo (otsutsa) akunena: “Akadafuna (Allah) Wachifundo chambiri (kuti tisamapembedze mafano awa), sitikadawapembedza!” Iwo alibe kudziwa pa zimenezi (zomwe akunenazi). Koma akungonena mawu opeka
Verse 21 — Surah Az-Zukhruf 43:21
“Kapena tidawapatsa buku lina tisadapereke ili, kotero kuti iwo agwiritsitsa limenelo (ndi kugwirizana nazo zili mmenemo)
Verse 22 — Surah Az-Zukhruf 43:22
“Koma akunena: “Ndithu ife tidawapeza makolo athu pa chipembedzo chimenechi, ndipo ife tikutsatira mapazi awo.”
Verse 23 — Surah Az-Zukhruf 43:23
“Ndipo momwemo, sitidatumize mchenjezi patsogolo ku mudzi uliwonse koma olemera ammenemo adanena: “Ndithu tidawapeza makolo athu pa chipembedzochi (akuchita mmene tikuchitiramu), ndipo ife titsatira mmapazi awo.”
Verse 24 — Surah Az-Zukhruf 43:24
“Adanena (mneneri wawo): “Ngakhale ndakubweretserani chipembedzo chabwino kuposa chomwe mudawapeza nacho makolo anu (mupitirizabe kutsatira chipembedzo cha makolo anucho)?” Adanena: “Ife tikuzikana zimene mwatumidwa nazozi.”
Verse 25 — Surah Az-Zukhruf 43:25
“Choncho tidawalanga iwo. Taona m’mene adalili mapeto a otsutsa aja
Verse 26 — Surah Az-Zukhruf 43:26
“Ndipo (kumbuka) pamene Ibrahim adauza bambo wake ndi anthu ake (kuti): “Ndithu ine ndadzipatula ku zimene mukuzipembedzazi.”
Verse 27 — Surah Az-Zukhruf 43:27
““Kupatula Amene adandilenga; ndithu Iye andiongola.”
Verse 28 — Surah Az-Zukhruf 43:28
“Ndipo adalichita liwu ili kukhala losatha ku mtundu wake, kuti abwelere (ku malankhulidwe amenewa)
Verse 29 — Surah Az-Zukhruf 43:29
“Koma ndidawasangalatsa awa (Aquraish) pamodzi ndi makolo awo kufikira choonadi chawadzera ndi Mtumiki wolongosola (za choonadichi)
Verse 30 — Surah Az-Zukhruf 43:30
“Ndipo pamene choonadi (Qur’an) chidawadzera, adanena: “Awa ndi matsenga; ndithu ife tikuwakana.”
Verse 31 — Surah Az-Zukhruf 43:31
“Ndipo adatinso: “Nchifukwa ninji Qur’an iyi siidavumbulutsidwe pa munthu wamkulu mmidzi iwiriyi (Makka ndi Twaif).”
Verse 32 — Surah Az-Zukhruf 43:32
“(Choncho Allah akunena): “Kodi iwo ndi amene akugawa mtendere wa Mbuye wako (kumpatsa amene wamfuna ndi kummana amene sakumfuna? Chikhalirecho) Ife ndi Amene timagawa pakati pawo zofunika pa moyo wawo mu moyo wadziko lapansi; ndipo tawatukula ena mwa iwo pa ulemelero pamwamba pa ena, choncho ena mwa iwo akuwachita anzawo kukhala antchito awo koma mtendere wa Mbuye wako ndi wabwino kuposa zimene akusonkhanitsa.”
Verse 33 — Surah Az-Zukhruf 43:33
“Ndipo pakadapanda kuopera kuti anthu adzakhala gulu limodzi (lokanira Allah), ndithu tikadazichita nyumba za amene akumkana (Allah) Wachifundo chambiri kukhala ndi madenga a Siliva, ndi makwelero amene amakwelera (kukhalanso a Siliva)
Verse 34 — Surah Az-Zukhruf 43:34
“Ndipo nyumba zawo kukhala ndi zitseko ndi makama (mabedi) omwe amayadzamira (zonsezo kukhala za Siliva)
Verse 35 — Surah Az-Zukhruf 43:35
“Ndiponso ndi zokongoletsa za golide. Koma zonsezo sikanthu ayi, ndi chisangalalo chabe cha dziko lapansi (chosakhalira kutha); ndipo tsiku lachimaliziro lomwe lili kwa Mbuye wako ndi la oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa)
Verse 36 — Surah Az-Zukhruf 43:36
“Ndipo amene akunyozera kukumbukira (Allah) Wachifundo chambiri, timpatsa satana, kuti iye akhale bwenzi lake (lotsagana nalo)
Verse 37 — Surah Az-Zukhruf 43:37
“Ndipo iwo amawatsekereza ku njira zabwino ndi kumaganiza kuti iwo ngoongoka
Verse 38 — Surah Az-Zukhruf 43:38
“Kufikira pamene adzatidzera (tsiku la Qiyâma, uku akulowetsedwa ku Moto). Adzati (kumuuza satana): “Kalanga ine! Pakati pa ine ndi iwe pakadakhala ntunda wa pakati pa kuvuma ndi kuzambwe (kutalikirana kwathu).” Ha! Taonani kuipa kwa bwenzi
Verse 39 — Surah Az-Zukhruf 43:39
“(Allah adzawauza kuti): “Ndipo lero sikukuthandizani kukhala limodzi kwanu m’chilango pakuti mudadzichitira nokha zoipa.”
Verse 40 — Surah Az-Zukhruf 43:40
“Kodi ungathe kuwamveretsa agonthi, kapena ungathe kuwaongola akhungu ndi amene ali mkusokera koonekera
Verse 41 — Surah Az-Zukhruf 43:41
“Ngati titakuchotsa (padziko usadaone chilango chawo, usakhale ndi chikaiko), ndithu Ife tiwalanga iwo
Verse 42 — Surah Az-Zukhruf 43:42
“Kapena tikusonyeza zimene tidawalonjeza (uona ndi maso ako usadafe). Ndithu Ife tili ndi mphamvu pa iwo
Verse 43 — Surah Az-Zukhruf 43:43
“Choncho, gwiritsa zimene zavumbulutsidwa kwa iwe, ndithu iwe uli pa njira yolunjika
Verse 44 — Surah Az-Zukhruf 43:44
“Ndithu iyi (Qur’an) ndi ulemelero wako ndi anthu ako; ndipo posachedwa mufunsidwa (za ulemelero umenewu)
Verse 45 — Surah Az-Zukhruf 43:45
“Ndipo afunse atumiki Athu amene tidawatumiza iwe usadadze: “Kodi tidapanga milungu ina kuti ipembedzedwe, osati (Allah) Wachifundo chambiri?”
Verse 46 — Surah Az-Zukhruf 43:46
“Ndithu tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa Zathu kwa Farawo ndi nduna zake; ndipo adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa Mbuye wa zolengedwa.”
Verse 47 — Surah Az-Zukhruf 43:47
“Koma pamene adawadzera ndi zisonyezo zathu, basi iwo adali kuziseka
Verse 48 — Surah Az-Zukhruf 43:48
“Ndipo chisonyezo chilichonse chomwe tidawasonyeza chidali chachikulu kuposa chinzake (komabe sadakhulupirire). Ndipo tidawalanga ndi chilango kuti abwelere (kwa Ife)
Verse 49 — Surah Az-Zukhruf 43:49
“Ndipo adati (kwa Mûsa): “E iwe wamatsenga! Tipemphere kwa Mbuye wako pa chomwe adakulonjeza; ndithu ife tiongoka, (tikhulupirira).”
Verse 50 — Surah Az-Zukhruf 43:50
“Choncho, pamene tidawachotsera chilangocho, basi iwo adayamba kuswa pangano
Verse 51 — Surah Az-Zukhruf 43:51
“Ndipo Farawo adaitana anthu ake, adati: “E inu anthu anga! Kodi ulamuliro wa mu Iguputo siwanga pamodzi ndi mitsinje iyi imene ikuyenda pansi panga (pa nyumba zanga?) Kodi simukuona?”
Verse 52 — Surah Az-Zukhruf 43:52
““Kodi kapena ine sindine woposa uyu (Mûsa) wonyozeka, ndipo sangathe kuyankhula momveka?”
Verse 53 — Surah Az-Zukhruf 43:53
““Nanga bwanji sadavekedwe zibangiri zagolide kapena angelo kudza pamodzi ndi iye uku akumtsatira?”
Verse 54 — Surah Az-Zukhruf 43:54
“Adawapeputsa anthu ake. Ndipo adamvera; iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah)
Verse 55 — Surah Az-Zukhruf 43:55
“Pamene adatikwiitsa, tidawalanga ndipo tidawamiza onse mmadzi
Verse 56 — Surah Az-Zukhruf 43:56
“Tidawachita (Farawo ndi anthu ake) kukhala chitsanzo cha okanira a pambuyo pawo ndikukhala mbiri kwa anthu amene akudza
Verse 57 — Surah Az-Zukhruf 43:57
“Ndipo pamene lidaperekedwa fanizo la mwana wa Mariya, pamenepo anthu anu adali kufuula (monyoza)
Verse 58 — Surah Az-Zukhruf 43:58
“Ndipo adati: “Kodi milungu yathu ndi yabwino, kapena iye?” Sadamfanizire kwa iwe koma kufuna kutsutsana basi (kopanda kufuna choona). Koma iwo ndi anthu amtsutso
Verse 59 — Surah Az-Zukhruf 43:59
“Iye sadali kanthu koma ndi kapolo amene tidampatsa mtendere; ndipo tidamchita kukhala chitsanzo (chodabwitsa) cha ana a Israyeli
Verse 60 — Surah Az-Zukhruf 43:60
“Ndipo tikadafuna tikadawachita angelo kukhala pa dziko mmalo mwa inu ndi kumasiirana iwo kwa iwo (kuti mudziwe kuti angelo akugonjera malamulo a Allah. Iwo siAllah)
Verse 61 — Surah Az-Zukhruf 43:61
“Ndipo iye (Isa (Yesu) adzakhala chizindikiro cha Qiyâma (kuti yayandikira). Choncho musaikaikire, koma nditsatireni. Imeneyi ndi njira yolunjika
Verse 62 — Surah Az-Zukhruf 43:62
“Asakutsekerezeni satana; iye kwa inu ndi mdani woonekera
Verse 63 — Surah Az-Zukhruf 43:63
“Ndipo pamene Isa (Yesu) adadza ndi zisonyezo zoonekera poyera, adati: “Ndakudzerani ndi nzeru (yopindulitsa), ndikuti ndikulongosolereni zina zimene mudali kusiyana mu izo; choncho, muopeni Allah ndiponso ndimvereni.”
Verse 64 — Surah Az-Zukhruf 43:64
““Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndi Mbuye wanunso; choncho mupembedzeni; imeneyi ndiyo njira yolunjika.”
Verse 65 — Surah Az-Zukhruf 43:65
“Koma magulu adasemphana pakati pawo. Ndipo kuonongeka kuchokera mu chilango cha tsiku lowawa kudzakhala pa amene adzichitira okha zoipa
Verse 66 — Surah Az-Zukhruf 43:66
“Palibe chimene akuyembekeza, koma Qiyâma basi yomwe iwadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira (ali otanganidwa ndi za m’dziko)
Verse 67 — Surah Az-Zukhruf 43:67
“Abwenzi tsiku limenelo adzakhala odana, wina ndi mnzake, (chifukwa chakuti adali kuthandizana pa zinthu zosalungama ndi zamachimo) kupatula oopa Allah (amene adachita chibwenzi mwa Allah, pothandizana kukwaniritsa malamulo a Allah ndi kusiya zimene Allah waletsa)
Verse 68 — Surah Az-Zukhruf 43:68
“(Allah adzati): E inu akapolo Anga (abwino)! Palibe kuopa kwa inu lerolino ndiponso simudandaula
Verse 69 — Surah Az-Zukhruf 43:69
“Amene adakhulupirira zisonyezo Zathu ndipo adali Asilamu (ogonjera Allah)
Verse 70 — Surah Az-Zukhruf 43:70
“Lowani ku Munda wamtendere, inu ndi akazi anu musangalatsidwa
Verse 71 — Surah Az-Zukhruf 43:71
“Adzakhala akupititsidwa mbale zagolide ndi matambula (agolide); zonse zokomera moyo zidzakhala mmenemo ndi zokomera maso, ndipo inu mudzakhala mmenemo nthawi yaitali
Verse 72 — Surah Az-Zukhruf 43:72
“Ndipo umeneo ndi munda umene mwapatsidwa chifukwa cha (zabwino) zimene munkachita
Verse 73 — Surah Az-Zukhruf 43:73
“Inu mupeza mmenemo zipatso zambiri zomwe muzidya
Verse 74 — Surah Az-Zukhruf 43:74
“Ndithu ochimwa (okanira) adzakhala m’chilango cha Jahannam nthawi yaitali
Verse 75 — Surah Az-Zukhruf 43:75
“Sadzapatsidwa nthawi yopumula, ndipo mmenemo iwo akataya mtima (zakupeza moyo wabwino)
Verse 76 — Surah Az-Zukhruf 43:76
“Ndipo sitidawapondereze koma adali kudzipondereza okha
Verse 77 — Surah Az-Zukhruf 43:77
“Ndipo (okanira) adzaitana E iwe Malik! (yemwe ndi mngelo woyang’anira moto): ‘‘Mbuye wako atipatse imfa (kuti tipumule kuchilangochi!)” Adzanena (Malik): “Ndithu inu mukhala momwemo!”
Verse 78 — Surah Az-Zukhruf 43:78
“Ndithu tidakubweretserani choona; koma ambiri a inu mudali kuchida choona
Verse 79 — Surah Az-Zukhruf 43:79
“Kodi akonza bwino chikonzero (chawocho chomwe ndi chiwembu chofuna kumupha Mtumiki {s.a.w})? Ndithu nafenso ndife okonza chikonzero chabwino (cholepheretsa chiwembu chawocho)
Verse 80 — Surah Az-Zukhruf 43:80
“Kodi akuganiza kuti sitikumva zobisa zawo ndi zonong’oneza zawo? Iyayi, (tikuzimva zonse), ndipo atumiki Athu (angelo) ali nawo pamodzi; akulemba
Verse 81 — Surah Az-Zukhruf 43:81
“Nena (kwa omphatikiza Allah ndi mafano): “Zikadakhala kuti (Allah) Wachifundo chambiri ali ndi mwana, ndiye kuti ine ndikadakhala woyamba kumpembedza (mwanayo).”
Verse 82 — Surah Az-Zukhruf 43:82
“Mbuye wa kumwamba ndi pansi, Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu), Wapatukana ndi mbiri zimene akum’nenerazo (zoti Allah ali ndi mwana)
Verse 83 — Surah Az-Zukhruf 43:83
“Asiye azingonena zachabezo ndi kusewera kufikira adzakumana ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa
Verse 84 — Surah Az-Zukhruf 43:84
“Ndipo Iye ndiamene akupembedzedwa kumwamba, ndiponso ndi Iye Amene akupembedzedwa pansi. Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa kwambiri
Verse 85 — Surah Az-Zukhruf 43:85
“Ndipo watukuka kwambiri Yemwe ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi pakati pa zimenezi ndi Wake. Ndiponso kwa Iye ndiko kuli kudziwa kudza kwa tsiku la Qiyâma; ndipo kwa Iye Yekha ndi kumene m’dzabwezedwa
Verse 86 — Surah Az-Zukhruf 43:86
“Ndipo omwe akuwapembedzawo kusiya Iye (Allah), sangathe kupulumutsa (aliyense) kupatula amene akuikira umboni choonachi, pomwe iwo akuchidziwa bwino
Verse 87 — Surah Az-Zukhruf 43:87
“Ndipo ngati utawafunsa: “Ndani adawalenga?” Anena motsimikiza kuti: “Ndi Allah.” Nanga akutembenuzidwa bwanji (kusiya choona)
Verse 88 — Surah Az-Zukhruf 43:88
“Ndipo zonena zake (Mneneri Muhammad{s.a.w} nthawi zonse): “E Mbuye Wanga! Ndithu awa ndi anthu osakhulupirira (nditani nao)?”
Verse 89 — Surah Az-Zukhruf 43:89
“Choncho, akhululukire, ndipo auze mawu a mtendere. Posachedwa adzadziwa