Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 44 - Ad-Dukhan
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Ad-Dukhan 44:1
Verse 2 — Surah Ad-Dukhan 44:2
“Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka
Verse 3 — Surah Ad-Dukhan 44:3
“Ndithu tidaivumbulutsa (Qur’an) mu usiku wodala. Ife ndithu Ndiachenjezi
Verse 4 — Surah Ad-Dukhan 44:4
“Mu (usiku) umenewu chinthu chilichonse chanzeru chimaweruzidwa ndi kulongosoledwa
Verse 5 — Surah Ad-Dukhan 44:5
“Mwa chilamulo chochokera kwa Ife. Ndithu Ife ndife otumiza atumiki (kuti achenjeze anthu)
Verse 6 — Surah Ad-Dukhan 44:6
“(Chifukwa cha) chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Wodziwa kwabasi
Verse 7 — Surah Ad-Dukhan 44:7
“Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli otsimikiza
Verse 8 — Surah Ad-Dukhan 44:8
“Palibe wopembedzedwa moona koma Iye basi. Amapereka moyo ndikupereka imfa, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu oyamba
Verse 9 — Surah Ad-Dukhan 44:9
“Koma iwo (okanira) ali mchikaiko akungosewera, (potsatira zilakolako zawo zoipa)
Verse 10 — Surah Ad-Dukhan 44:10
“Basi, yembekezera tsiku limene thambo lidzadze ndi utsi woonekera (konsekonse)
Verse 11 — Surah Ad-Dukhan 44:11
“Udzawaphimba anthu onse (ndipo adzakhala akunena:) “Ichi ndi chilango chowawa
Verse 12 — Surah Ad-Dukhan 44:12
“E Mbuye wathu! Tichotsereni chilangochi, ndithu ife tikhulupirira.”
Verse 13 — Surah Ad-Dukhan 44:13
“(Kodi lero) kukumbukira kuwapindulira chiyani iwo? Chikhalirecho mtumiki wolongosola chilichonse adawadzera
Verse 14 — Surah Ad-Dukhan 44:14
“Koma sadamlabadire uku akumnena kuti: “Waphunzitsidwa (ndi anthu), ndiponso wopenga.”
Verse 15 — Surah Ad-Dukhan 44:15
“Ndithu Ife tichotsa chilangocho pang’ono (koma) inu mubwerezanso (machimo anu)
Verse 16 — Surah Ad-Dukhan 44:16
“(Kumbuka, iwe Mtumiki), tsiku limene tidzawalanga chilango chachikulu; ndithu Ife ndife olanga
Verse 17 — Surah Ad-Dukhan 44:17
“Ndipo ndithu iwo asadadze, tidawayesa anthu a Farawo. Ndiponso adawadzera mtumiki wolemekezeka
Verse 18 — Surah Ad-Dukhan 44:18
“Kuti: “Ndipatseni akapolo a Allah. Ndithu ine kwa inu ndi Mtumiki wokhulupirika.”
Verse 19 — Surah Ad-Dukhan 44:19
““Ndipo musadzikweze kwa Allah. Ndithu ine ndikubweretserani chisonyezo choonekera.”
Verse 20 — Surah Ad-Dukhan 44:20
““Ndipo Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye Wanga ndiponso Mbuye wanu (ku chiwembu chofuna kundipha) pondigenda (ndi miyala).”
Verse 21 — Surah Ad-Dukhan 44:21
““Ndipo ngati simundikhulupirira, ndipatukeni (musandivutitse).”
Verse 22 — Surah Ad-Dukhan 44:22
““(Koma adamchitira mtopola). Ndipo iye adaitana Mbuye wake kuti: “Awa ndithu ndi anthu oipa.”
Verse 23 — Surah Ad-Dukhan 44:23
“(Allah adamuuza kuti): “Pita ndi akapolo Anga usiku; ndithu inu mulondoledwa.”
Verse 24 — Surah Ad-Dukhan 44:24
““Ndipo isiye nyanja ili momwemo, zii. ndithu iwo ndikhamu (lankhondo) limene limizidwa.”
Verse 25 — Surah Ad-Dukhan 44:25
“Kodi ndi minda ingati ndi akasupe zomwe adazisiya atamizidwa
Verse 26 — Surah Ad-Dukhan 44:26
“Ndiponso mmera ndi malo abwino
Verse 27 — Surah Ad-Dukhan 44:27
“Ndi mtendere (waukulu) umene adali kusangalala nawo mmenemo
Verse 28 — Surah Ad-Dukhan 44:28
“Umo ndi mmene zidalili. Ndipo tidawapatsa anthu ena zimenezo
Verse 29 — Surah Ad-Dukhan 44:29
“Thambo ndi nthaka sizidawalilire ndipo sadapatsidwe mpata (wobwereranso pa dziko)
Verse 30 — Surah Ad-Dukhan 44:30
“Ndipo ndithu tidapulumutsa ana a Israyeli ku chilango choyalutsa
Verse 31 — Surah Ad-Dukhan 44:31
“Chochokera kwa Farawo; ndithu iye adali wodzikweza ndiponso mmodzi wa opyola malire
Verse 32 — Surah Ad-Dukhan 44:32
“Ndipo ndithu tidawasankha (Ayuda nthawi imeneyo) pa mitundu ina m’kudziwa Kwathu
Verse 33 — Surah Ad-Dukhan 44:33
“Ndipo tidawapatsa zisonyezo (kupyolera m’dzanja la Mûsa) momwe mudali mayeso oonekera poyera kwa iwo
Verse 34 — Surah Ad-Dukhan 44:34
“Ndithu awa (Aquraish) akunena (kuti)
Verse 35 — Surah Ad-Dukhan 44:35
““Palibe china choposera pa imfa yathu yoyambayi, ndipo ife sitidzaukitsidwa.”
Verse 36 — Surah Ad-Dukhan 44:36
““Choncho tibweretsereni makolo athu (amene adafa), ngati mukunena zoona (kuti kuli kuuka).”
Verse 37 — Surah Ad-Dukhan 44:37
“Kodi iwo ndi abwino (ndi kupambana pa nyonga), kapena anthu a Tubba (mafumu a kudziko la Yemen) ndi amene adalipo kale iwo asadadze? Tidawaononga. Ndithu iwo adali oipa
Verse 38 — Surah Ad-Dukhan 44:38
“Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zimene zili pakati paizo, mwachibwana
Verse 39 — Surah Ad-Dukhan 44:39
“Sitidalenge ziwirizi koma mwachoonadi; koma anthu ambiri sakudziwa
Verse 40 — Surah Ad-Dukhan 44:40
“Ndithu tsiku lachiweruziro ndiyo nthawi yawo onse (imene alonjezedwa)
Verse 41 — Surah Ad-Dukhan 44:41
“Tsiku limene m’bale sadzathandiza m’bale wake pa chilichonse (ku chilango cha Allah), ngakhale iwo sadzapulumutsidwa
Verse 42 — Surah Ad-Dukhan 44:42
“Kupatula amene Allah adzawachitira chifundo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwachisoni chosatha
Verse 43 — Surah Ad-Dukhan 44:43
“Ndithu mtengo wa Zakkumi
Verse 44 — Surah Ad-Dukhan 44:44
“Ndi chakudya cha ochimwa
Verse 45 — Surah Ad-Dukhan 44:45
“(Kutentha kwake) ngati mtovu wosungunulidwa, (wotentha kwambiri;) udzakhala ukuwira mmimba
Verse 46 — Surah Ad-Dukhan 44:46
“Monga kuwira kwa madzi otentha kwambiri
Verse 47 — Surah Ad-Dukhan 44:47
“(Kudzanenedwa): “Mgwireni; mkokereni (ndi kumponya) pakatikati pa Jahena!”
Verse 48 — Surah Ad-Dukhan 44:48
““Kenako mthireni pamwamba pamutu wake chilango chamadzi otentha!”
Verse 49 — Surah Ad-Dukhan 44:49
“(Adzauzidwa mwachipongwe): “Lawa! Ndithu iwe ndiwe wamphamvu zambiri, wolemekezeka, (monga momwe udali kudzitamira muja).”
Verse 50 — Surah Ad-Dukhan 44:50
““Ndithu izi ndi zimene mudali kuzikaikira zija!”
Verse 51 — Surah Ad-Dukhan 44:51
“Ndithu oopa Allah adzakhala pa malo a chitetezo
Verse 52 — Surah Ad-Dukhan 44:52
“Mminda ndi mu akasupe
Verse 53 — Surah Ad-Dukhan 44:53
“Adzavala (nsalu) za silika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atayang’anizana (nkhope)
Verse 54 — Surah Ad-Dukhan 44:54
“Umo ndi mmene zidzakhalire; ndipo tidzawakwatitsa ndi akazi okongola amaso aakulu
Verse 55 — Surah Ad-Dukhan 44:55
“Mmenemo adzakhala akuitanitsa mtundu uliwonse wa zipatso, mwamtendere
Verse 56 — Surah Ad-Dukhan 44:56
“Sadzalawa imfa mmenemo, kupatula imfa yoyamba ija; ndipo adzawateteza kuchilango cha Jahena
Verse 57 — Surah Ad-Dukhan 44:57
“Chifundo chochokera kwa Mbuye wako! Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu
Verse 58 — Surah Ad-Dukhan 44:58
“Ndithu taifewetsa (Qur’an) mchiyankhulo chako (cha Chiarabu) kuti akumbukire
Verse 59 — Surah Ad-Dukhan 44:59
“Choncho yembekeza; iwonso akuyembekezera, (kodi ndani chimtsikire chilango pakati panu)