Back to Languages

Chichewa - Chapter 45 - Al-Jathiyah

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Jathiyah 45:1

Verse 2 — Surah Al-Jathiyah 45:2

“Chivumbulutso cha buku (ili) chochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

Verse 3 — Surah Al-Jathiyah 45:3

“Ndithu kuthambo ndi m’nthaka muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa okhulupirira

Verse 4 — Surah Al-Jathiyah 45:4

“Ndiponso mkalengedwe kanu ndi zimene wazifalitsa mmenemo, mu zamoyo ndizisonyezo kwa anthu amene akutsimikiza

Verse 5 — Surah Al-Jathiyah 45:5

“Ndi kusinthana kwa usana ndi usiku, ndi mvula imene Allah akutsitsa kuchokera kumwamba, akuukitsa nthaka ndi mvulayo, itafa (itauma), ndi kuyendetsa mphepo mosinthasintha; (zonsezi) ndi zisonyezo kwa anthu anzeru

Verse 6 — Surah Al-Jathiyah 45:6

“Izi ndi Ayah (ndime) za Allah; tikukuwerengera iwe mwachoonadi. Kodi ndi nkhani yanji adzaikhulupirire atapanda kulabadira nkhani ya Allah ndi Ayah Zake

Verse 7 — Surah Al-Jathiyah 45:7

“Kuonongeka kuli pa aliyense wopeka zinthu, wamachimo ambiri

Verse 8 — Surah Al-Jathiyah 45:8

“Amene akumva Ayah za Allah zikuwerengedwa kwa iye kenako nkumapitiriza (zochita zake zosalungama) uku akudzikweza ngati kuti sadazimve ayazo; muuze nkhani ya chilango chowawa

Verse 9 — Surah Al-Jathiyah 45:9

“Ndipo akadziwa chinthu chochepa chochokera mma Ayah athu, amachichitira chipongwe; amenewa ndi amene adzakhala ndi chilango chosambula

Verse 10 — Surah Al-Jathiyah 45:10

“Jahannam ili (kuwayembekezera) kuseri kwawo; ndipo zimene adachita sizidzawathandiza chilichonse, ngakhale atetezi amene adadzipangira kusiya Allah (sadzawathandiza); ndipo adzapeza chilango chachikulu

Verse 11 — Surah Al-Jathiyah 45:11

“Ichi ndi chiongoko; ndipo amene adakanira Ayah za Mbuye wawo, adzakhala ndi chilango chachikulu chochokera mchilango chowawa

Verse 12 — Surah Al-Jathiyah 45:12

“Allah ndi Amene wakugonjetserani nyanja kuti zombo ziziyenda mmenemo mwa lamulo Lake; ndikuti munke mufunafuna chifundo Chake kuti muthokoze

Verse 13 — Surah Al-Jathiyah 45:13

“Ndipo wakugonjetserani za kumwamba ndi zam’nthaka, zonse zikuchokera kwa Iye. Ndithu mzimenezo muli zisonyezo kwa anthu amene amalingalira

Verse 14 — Surah Al-Jathiyah 45:14

“Nena kwa amene akhulupirira kuti awakhululukire amene sakuopa masiku a Allah (a chilango; mmasiku amenewo) kuti awalipire anthu pa zomwe amachita (zoipa)

Verse 15 — Surah Al-Jathiyah 45:15

“Amene akuchita chabwino akudzichitira yekha ndipo amene akuchita zoipa, zidzakhala paiye mwini. Kenako m’dzabwezedwa kwa Mbuye wanu

Verse 16 — Surah Al-Jathiyah 45:16

“Ndithu tidawapatsa ana a Israyeli buku, ulamuliro ndi uneneri; ndiponso tidawapatsa zina mwa zinthu zabwino ndikuwalemekeza pamwamba pa mitundu ina (ya nthawiyo)

Verse 17 — Surah Al-Jathiyah 45:17

“Ndipo tidawapatsa zisonyezo zoonekera pazinthu zachipembedzo chawo; sadapatukane mpaka pomwe kudawadzera kudziwa, chifukwa chadumbo pakati pawo. Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsemphana

Verse 18 — Surah Al-Jathiyah 45:18

“Kenako tidakuika iwe pa malamulo a zinthu za chipembedzo (Chathu). Choncho tsatira malamulo (Athu), ndipo usatsate zilakolako za amene sadziwa (njira yoona)

Verse 19 — Surah Al-Jathiyah 45:19

“Ndithu iwo (amene akutsata njira zonama) sangakuthandize chilichonse kwa Allah; ndithu achinyengo ena a iwo amatetezana wina ndi nzake; koma Allah ndi Mtetezi wa oopa (Iye potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa)

Verse 20 — Surah Al-Jathiyah 45:20

“Iyi (Qur’an imene yavumbulutsidwa kwa iwe), ndizisonyezo kwa anthu chiongoko ndi chifundo kwa anthu omwe akutsimikiza (kuti lilipo tsiku la chiweruziro)

Verse 21 — Surah Al-Jathiyah 45:21

“Kodi amene adadzichitira zoipa akuganiza kuti tingawachite monga omwe adakhulupirira ndi kuchita zabwino kuti afanane pa moyo wawo ndi pa imfa yawo? Ndi kuweruza koipa kumene iwo akuweruza

Verse 22 — Surah Al-Jathiyah 45:22

“Ndipo Allah adalenga thambo ndi nthaka moona ndi kuti mzimu uliwonse ulipidwe zimene udadzichitira, (zoipa kapena zabwino) ndipo iwo sadzaponderezedwa

Verse 23 — Surah Al-Jathiyah 45:23

“Kodi wamuona amene wachichita chilakolako chake kukhala mulungu wake wompembedza? Ndipo Allah wamlekelera kuti asokere, kupyolera mkudziwa Kwake; ndipo wamdinda (chidindo) mmakutu mwake ndi mu mtima mwake ndi kumuika chivindikiro mmaso mwake. Choncho ndani angamuongole pambuyo pa Allah? Kodi simukumbukira

Verse 24 — Surah Al-Jathiyah 45:24

“Ndipo (okanira kuuka ku imfa) adanena: “Kulibe (moyo wina) koma moyo wathu womwewu wa padziko lapansi; timafa ndi kukhala ndi moyo; palibe chikutiononga koma nthawi basi.” Koma iwo alibe kudziwa pa zimene akunenazo; akungoganizira chabe

Verse 25 — Surah Al-Jathiyah 45:25

“Ndipo Ayah Zathu zikawerengcdwa kwa iwo zolongosola chilichonse momveka, alibe mtsutso wina koma kunena kuti: “Tibweretsereni makolo Athu (aukitseni akhale ndi moyo) ngati inu muli owona!”

Verse 26 — Surah Al-Jathiyah 45:26

“Nena (kwa iwo iwe Mtumiki): “Allah amakupatsani moyo. Kenako amakupatsani imfa. Kenako adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko.” Koma anthu ambiri sakudziwa

Verse 27 — Surah Al-Jathiyah 45:27

“Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah, ndipo tsiku limene Qiyâma idzachitika, (anthu) ogwirizana ndi zonama adzaonongeka patsikulo

Verse 28 — Surah Al-Jathiyah 45:28

“Ndipo udzaliona gulu lililonse litagwada (uku nkhope zili zyoli); gulu lililonse lidzaitanidwa ku kaundula wake (kukamuwerenga): “Lero mulipidwa zimene mudali kuchita!”

Verse 29 — Surah Al-Jathiyah 45:29

““Uyu kaundula Wathu akunena zoona za inu; ndithu Ife tidali kulemba zimene mudali kuchita.”

Verse 30 — Surah Al-Jathiyah 45:30

“Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, Mbuye wawo adzawalowetsa ku chifundo Chake; kumeneko ndiko kupambana koonekera

Verse 31 — Surah Al-Jathiyah 45:31

“Ndipo amene adakanira, (adzauzidwa kuti): “Kodi Ayah Zanga sizidali kuwerengedwa kwa inu? Koma inu mudadzikweza; ndipo mudali anthu oipa.”

Verse 32 — Surah Al-Jathiyah 45:32

“Ndipo kukanenedwa kuti lonjezo la Allah ndiloona, ndikuti Qiyâma ilibe chikaiko, mudali kunena: “Sitikudziwa Qiyâma kuti nchiyani; tikungoganizira chabe, ndipo tilibe chitsimikizo (cha Kiyamayo).”

Verse 33 — Surah Al-Jathiyah 45:33

“Choncho, kuipa kwa zimene adachita kudzawaonekera, ndipo zidzawazinga zimene ankazichitira chipongwe

Verse 34 — Surah Al-Jathiyah 45:34

“Kudzanenedwanso kwa iwowa: “Lero tikuiwalani (pokusiyani mchilango) monga momwe inu mudaiwalira kukumana ndi tsiku lanu ili. Ndipo malo anu ndi ku Moto, ndipo mulibe wokupulumutsani.”

Verse 35 — Surah Al-Jathiyah 45:35

““Zimenezi nchifukwa chakuti inu mudazichitira chipongwe Ayah za Allah, ndipo moyo wa pa dziko udakunyengani.” Choncho lero satulutsidwa mmenemo ndipo madandaulo awo savomerezedwa

Verse 36 — Surah Al-Jathiyah 45:36

“Tero kutamandidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wakumwamba ndi Mbuye wa pa dziko lapansi; Mbuye wazolengedwa

Verse 37 — Surah Al-Jathiyah 45:37

“Ndipo ukulu ndi Wake, kumwamba ndi pansi; ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya