Back to Languages

Chichewa - Chapter 47 - Muhammad

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Muhammad 47:1

“Amene adam’kana (Allah ndi Mthenga Wake) ndi kutsekereza anthu kuyenda panjira ya Allah (powaletsa kulowa m’Chisilamu), Allah waononga zonse zabwino zimene adachita

Verse 2 — Surah Muhammad 47:2

“Ndipo amene akhulupirira nkumachita zabwino, nkuzikhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa Muhammad (s.a.w), zimene zili zoona zochokera kwa Mbuye wawo, wawafafanizira zolakwa zawo, ndipo awakonzera chikhalidwe chawo (patsiku lachimaliziro ndi padziko lapansi)

Verse 3 — Surah Muhammad 47:3

“Zimenezi nchifukwa chakuti amene sadakhulupirire adatsata chonama, ndipo amene adakhulupirira adatsatira choonadi chochokera kwa Mbuye wawo. M’menemu ndim’mene Allah akuperekera kwa anthu mafanizo awo (kuti alingalire ndi kupeza phunziro)

Verse 4 — Surah Muhammad 47:4

“Ndipo mukakumana nawo pankhondo amene sanakhulupirire amenyeni makosi awo (aduleni), mpaka mwafooketse pochuluka ophedwa mwa iwo; kenako amangeni ndi zingwe (otsalawo). Ngati mutafuna kuwamasula popanda dipo kapena kuti apereke dipo, (zili kwa inu). Kufikira nkhondo itatha. Limenelo ndi lamulo la Allah. Ndithu Allah akadafuna akadathana nawo Iye mwini powaononga onse psiti; koma (wakulamulani kuti muchite nkhondo) ncholinga choti awayese mayeso ena a inu pa ena (okhulupirira pa okanitsitsawo). Ndipo amene aphedwa panjira ya Allah, ntchito yawo sadzaipititsa pachabe

Verse 5 — Surah Muhammad 47:5

“Awaongolera (ku zimene zingawapindulitse pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro) ndi kuwakonzera zinthu zawo ndi chikhalidwe chawo

Verse 6 — Surah Muhammad 47:6

“Ndi kukawalowetsa ku Munda wamtendere umene adawadziwitsa

Verse 7 — Surah Muhammad 47:7

“E inu amene mwakhulupirira! Ngati muteteza chipembedzo cha Allah, (Iye) adzakutetezani (kwa adani anu) ndi kulimbikitsa mapazi anu (pa nkhondo)

Verse 8 — Surah Muhammad 47:8

“Koma amene akana (Allah ndi Ayah Zake) kuwonongeka nkwawo ndipo awaonongera zochita zawo

Verse 9 — Surah Muhammad 47:9

“Zimenezo nchifukwa chakuti iwo azida zomwe Allah adavumbulutsa (monga Qur’an ndi malamulo ake;) choncho waziononga zochita zawo

Verse 10 — Surah Muhammad 47:10

“Kodi sadayendeyende padziko nkuona kuti adali bwanji mapeto a amene adawatsogolera (monga Âdi ndi Samudi, ndi anthu a Luti ndi ena otero)? Allah adawaononga psiti, ndipo chilango ngati chimenecho chidzakhalanso kwa osakhulupirira

Verse 11 — Surah Muhammad 47:11

“Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, koma osakhulupirira alibe mtetezi

Verse 12 — Surah Muhammad 47:12

“Ndithu Allah adzawalowetsa ku Minda ya mtendere amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, (momwe) pansi pake ikuyenda mitsinje; koma amene sadakhulupirire akusangalala (padziko lapansi) ndi kudya momwe zidyera ziweto (popanda lingaliro lililonse kupatula lingaliro la mimba zawo ndi kukwaniritsa zilakolako za chilengedwe chawo); ndipo Moto ndiwo malo awo

Verse 13 — Surah Muhammad 47:13

“Ndi ambiri mwa eni mizinda (yakale) omwe adali amphamvu kuposa eni mzinda wakowu umene akutulutsamo (eni ake,) tidawaononga (ndi zilango zosiyanasiyana) koma padalibe wowateteza (kwa Ife)

Verse 14 — Surah Muhammad 47:14

“Kodi angafanane, (polandira mphoto,) amene ali ndi umboni wodziwika wochokera kwa Mbuye wake, (kotero kuti nkumamumvera, ndi amene wakometsedwa ndi zochita zake zoipa natsatira zilakolako zawo)

Verse 15 — Surah Muhammad 47:15

“Fanizo la Munda wamtendere (Jannah) umene alonjezedwa oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa, udzakhala chonchi): M’menemo muli mitsinje yamadzi osasintha fungo lake; ndi mitsinje yamkaka wosasasa mkakomedwe kake; ndi mitsinje yavinyo wokoma kwa akumwa ndi mitsinje ya uchi woyeretsedwa (ku phula), ndiponso iwo adzapeza m’menemo mtundu uliwonse wa zipatso ndi chikhululuko chochokera kwa Mbuye wawo. Angafanane ndi wokhala nthawi yaitali ku Moto, ndi kumwetsedwa madzi owira omwe akadula matumbo awo

Verse 16 — Surah Muhammad 47:16

“Ndipo ena mwa iwo (okana Allah) amamvetsera kwa iwe, (popanda kupindula chilichonse), ndipo akachoka pamalo pakopo, amanena kwa amene apatsidwa nzeru (mwa omtsatira ake): “Kodi (Mtumiki) wanena chiyani posachedwapa?” Iwowo ndiamene Allah wawadinda m’mitima mwawo (ndi chidindo chokana Allah), ndipo amatsatira zilakolako zawo (zachabe)

Verse 17 — Surah Muhammad 47:17

“Ndipo amene aongoka, (Allah) amawaonjezera chiongoko ndi kuwapatsa kuopa kwawo (komuopa Allah)

Verse 18 — Surah Muhammad 47:18

“Kodi pali chimene akuyembekezera posakhala tsiku lachiweruziro limene liwadzere mwadzidzidzi (uku iwo ali otanganidwa ndi zam’dziko)? Ndithu zizindikiro zake zadza kale; kodi kudzawapindulira chiyani kukumbuka kwawo likadzawadzera (tsikulo)

Verse 19 — Surah Muhammad 47:19

“Dziwa kuti palibe wompembedza m’choonadi koma Allah, ndipo pempha chikhululuko pa zolakwa zako ndi zolakwa za okhulupirira aamuna ndi aakazi; ndipo Allah akudziwa malo anu opita ndi kubwera ndi malo anu Wokhazikika

Verse 20 — Surah Muhammad 47:20

“Ndipo amene akhulupirira akunena (chifukwa cha mazunzo omwe amawapeza kuchokera kwa osakhulupirira kuti) kodi nchifukwa ninji siikuvumbulutsidwa sura (yotiloleza kumenyana ndi osakhulupirira Allah amene akutiputa)? Koma ikavumbulutsidwa Sura yokhazikika (lamulo lake), ndipo mkati mwake ndi kutchulidwa nkhani zankhondo, uwaona amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akukuyang’ana m’mayang’anidwe a yemwe akukomoka ndi imfa, (chifukwa cha kulida lamulo lomenyana ndi osakhulupirira), basi kuonongeka ndi kwawo

Verse 21 — Surah Muhammad 47:21

“(Zofunika ndi) kumvera ndi mawu abwino ndi kuti chinthu chikatsimikizika (achichite). Ngati akadamumvera Allah, ndithu zikadakhala zabwino kwa iwo

Verse 22 — Surah Muhammad 47:22

“Mwina mwake inu mukanyoza (Chisilamu), mubwerera m’mbuyo ku zomwe mudali nazo (m’nthawi ya umbuli) monga kuononga pa dziko ndi machimo) ndi kudula chibale chanu

Verse 23 — Surah Muhammad 47:23

“Oterewo ndiamene Allah wawatembelera ndi kuwagonthetsa ndi kuwachititsa khungu maso awo

Verse 24 — Surah Muhammad 47:24

“Kodi sakuilingalira Qur’an? Kapena m’mitima mwawo m’motsekedwa ndi akabali (maloko) ake

Verse 25 — Surah Muhammad 47:25

“Ndithu amene akubwerera m’mbuyo (kusiya chipembedzo chawo nkubwerera ku zosakhulupirira Allah) chiongoko chitawaonekera poyera satana ndiamene wawanyenga, ndipo Allah akuwapatsa nthawi

Verse 26 — Surah Muhammad 47:26

“Zimenezo nkaamba kakuti iwo adanena kwa omwe amada zimene Allah wavumbulutsa (kuti): “Tidzakumverani m’zinthu zina (zimene mukutsutsana ndi Mtumiki{s.a.w}).” Ndipo Allah akudziwa zobisika zawo

Verse 27 — Surah Muhammad 47:27

“Kodi adzakhala bwanji pamene angelo azidzatenga mizimu yawo uku akumenya nkhope zawo ndi misana yawo

Verse 28 — Surah Muhammad 47:28

“Zimenezi (imfa yoopsayi) nkaamba kakuti iwo adatsata zomwe zidakwiitsa Allah ndi kuda zomusangalatsa (Allah); choncho adaziwononga zochita zawo

Verse 29 — Surah Muhammad 47:29

“Kodi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akuganiza kuti Allah sangaonetsere poyera kaduka kawo

Verse 30 — Surah Muhammad 47:30

“Ndipo tikadafuna tikadakuonetsa iwo (amene akuchitira kaduka Chisilamu) ndipo ukadawadziwa ndi zizindikiro zawo. Koma ndithu uwadziwa m’kayankhulidwe (kawo) kokometsa ndipo Allah akudziwa zochita zanu zonse

Verse 31 — Surah Muhammad 47:31

“Ndipo ndithu tikuyesani mayeso mpaka tiwaonetsere poyera (adziwike) amene akumenya nkhondo mwa inu (chifukwa cha dini) ndi opirira (pamavuto); ndi kuzionetsera poyera nkhani zanu (zochita zanu)

Verse 32 — Surah Muhammad 47:32

“Ndithu amene akana (Mtumiki {s.a.w}) ndi kuwatsekereza anthu ku njira ya Allah, ndi kutsutsana ndi Mtumiki chiongoko chitadziwika kwa iwo, sangamsautse Allah ndi chilichonse, koma adzawaonongera ntchito zawo

Verse 33 — Surah Muhammad 47:33

“E inu amene mwakhulupirira! Mvereni Allah ndiponso mvereni mtumiki (Wake) ndipo musaononge ntchito zanu

Verse 34 — Surah Muhammad 47:34

“Ndithu amene sadakhulupirire ndi kwatsekereza anthu kunjira ya Allah, kenako nkufa uku ali osakhulupirira Allah sadzawakhululukira (zolakwa zawo)

Verse 35 — Surah Muhammad 47:35

“Musafooke ndi kufuna chimvano, (koma menyanani ndi adani anu); inu ndinu opambana. Ndipo Allah ali nanu (pokuthangatani ndi kukupulumutsani,) ndipo sakuchepetserani (mphoto ya) ntchito zanu

Verse 36 — Surah Muhammad 47:36

“Ndithu moyo wapadziko lapansi ndi masewera ndi chibwana. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kudzipatula kumachimo (Allah) akupatsani malipiro anu, ndipo sakukupemphani chuma chanu

Verse 37 — Surah Muhammad 47:37

“Ngati akadachifuna (kuchokera) kwa inu chumacho ndi kukuchulukitsirani (chopereka),mukadachita umbombo (ndi chumacho), ndipo akadatulutsira (poyera) kaduka kanu

Verse 38 — Surah Muhammad 47:38

“Ha! Ndinu amene mukuitanidwa kuti mupereke (chuma) mu njira ya Allah. Koma alipo ena a inu akuumira ndipo amene akuumira akuzimana yekha. Allah Ngwachikwanekwane ndipo inu ndinu amphawi. Ngati munyoza (Chisilamu) ndi kubwerera m’mbuyo posakhulupirira) Allah adzabweretsa m’malo mwanu anthu ena; iwo sadzakhala ngati inu