Back to Languages

Chichewa - Chapter 48 - Al-Fath

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Fath 48:1

“Ndithu takugonjetsera (iwe Mtumiki{s.a.w}mzinda wa Makka) kugonjetsa kwakukulu koonekera poyera

Verse 2 — Surah Al-Fath 48:2

“Kuti Allah akukhululukire zolakwa zako zapatsogolo ndi zapambuyo, ndi kukukwaniritsira mtendere Wake, ndi kukuongolera kunjira yolunjika

Verse 3 — Surah Al-Fath 48:3

“Ndikuti Allah akuteteze ndi chitetezo champhamvu

Verse 4 — Surah Al-Fath 48:4

“Iye ndiamene adatsitsa chikhazikiko (kudekha) m’mitima mwa okhulupirira kuti awonjezera chikhulupiliro pachikhulupiro chawo. Makamu ankhondo akumwamba ndi pansi, nga Allah, (monga angelo, ziwanda, nyama ziphaliwali, mphepo yamkuntho ndi zivomerezi ndi zina zotero); ndipo Allah Ngodziwa chilichonse, ndiponso Wanzeru zakuya

Verse 5 — Surah Al-Fath 48:5

“(Wachita izi) kuti okhulupirira aamuna ndi aakazi akawalowetse m’minda yomwe pansi pake ikuyenda mitsinje; adzakhala nthawi yaitali mmenemo, ndi kuti awafafanizire zolakwa zawo; kumeneko, kwa Allah ndiko kupambana kwakukulu

Verse 6 — Surah Al-Fath 48:6

“Ndi kuti awalange achiphamaso aamuna ndi aakazi ndi omphatikiza Allah aamuna ndi aakazi oganizira Allah maganizo achabe. Kutembenuka koipa kuli kwa iwo ndipo Allah wawakwiyira ndiponso wawatembelera ndi kuwakonzera Jahannamu. Ndipo kumeneko nkobwerera koipa

Verse 7 — Surah Al-Fath 48:7

“Ndipo magulu ankhondo akumwamba ndi pansi nga Allah; ndipo Allah ndi Wamphamvu zoposa, Wa nzeru zakuya

Verse 8 — Surah Al-Fath 48:8

“Ndithu takutumiza kuti ukhale mboni ndi wolengeza nkhani zabwino ndiponso mchenjezi

Verse 9 — Surah Al-Fath 48:9

“Ncholinga choti mumkhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kuti mumtukule ndi kumulemekeza (Mtumiki) ndi kutinso mumtamande (Allah) m’mawa ndi madzulo

Verse 10 — Surah Al-Fath 48:10

“Ndithu amene akukulonjeza, ndiye kuti akulonjeza Allah. Dzanja la Allah lili pamwamba pa manja awo. Amene ati aswe lonjezo, ndiye kuti wadziswera yekha (mavuto ali pa iye). Koma yemwe akwaniritse zomwe adalonjeza kwa Allah, amulipira malipiro aakulu

Verse 11 — Surah Al-Fath 48:11

“Adzanena kwa iwe Arabu am’midzi otsala (ku nkhondo, amene adalibe zifukwa zomveka m’kutsala kwawo): “Chuma ndi ana athu zidatitangwanitsa; choncho tipemphereni chikhululuko.” Akunena ndi malirime awo (mawu) omwe m’mitima mwawo mulibe. Nena: “Kodi ndani angathe kukuthandizani chilichonse kwa Allah ngati atafuna kukupatsani masautso, kapena atafuna kukupatsani zabwino? Koma Allah Akudziwa zonse zimene mukuchita.”

Verse 12 — Surah Al-Fath 48:12

““Koma mudali kuganiza kuti Mtumiki ndi okhulupirira sabwereranso ku maanja awo, (akaphedwa konko); zimenezo zidakukondweretsani m’mitima mwanu, ndipo mumaganiza ganizo loipa; ndipo mudali anthu oonongeka.”

Verse 13 — Surah Al-Fath 48:13

“Ndipo amene sakhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu Ife tawakonzera okanira chilango cha Moto woyaka

Verse 14 — Surah Al-Fath 48:14

“Ndipo ufumu wakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Amakhululukira amene wamfuna (ngati atatembenukira kwa Iye) ndi kumlanga amene wamfuna (ngati sanatembenukire kwa Iye). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

Verse 15 — Surah Al-Fath 48:15

“Otsala (kunkhondo) aja, mukapita kukatenga zotola za a nkhondo, adzanena: “Tiloleni tikutsatireni.” Akufuna kuti asinthe mawu a Allah. Nena: “Simutitsatira! Umo ndimo Allah adanenera kale.” (Apo) adzanena (kuti): “Koma mukutichitira dumbo.” Iyayi, koma nzochepa zomwe adali kuzindikira

Verse 16 — Surah Al-Fath 48:16

“Nena kwa otsala (kunkhondo) mwa Arabu a m’midzi: “Mudzaitanidwa (kukamenyana) ndi anthu eni mphamvu zaukali; mudzamenyana nawo kapena adzagonja (ndi kulowa m’Chisilamu). Ngati mudzamvera, Allah adzakulipirani malipiro abwino, koma ngati mutembenuka monga mudatembenukira kale adzakulangani ndi chilango chowawa.”

Verse 17 — Surah Al-Fath 48:17

“Palibe tchimo pa wakhungu, palibenso tchimo pa olumala, palibenso tchimo pa wodwala (atasiya kupita ku nkhondo). Ndipo amene angamumvere Allah ndi Mtumiki Wake, adzam’lowetsa m’minda momwe mukuyenda mitsinje pansi pake; ndipo amene anyozere, amulanga ndi chilango chowawa

Verse 18 — Surah Al-Fath 48:18

“Ndithu Allah adawayanja okhulupirira pamene amagwirana nawe (Mtumiki) chanza pansi pa mtengo pomwe amakulonjeza (kuti adzamenya nkhondo mpaka imfa) Allah adadziwa zomwe zidali m’mitima mwawo ndipo adatsitsa pa iwo kukhazikika (ndi kudekha;) ndipo adawalipira kupambana kwapafupi

Verse 19 — Surah Al-Fath 48:19

“Ndipo zofunkha zambiri za pa nkhondo adzazitenga; ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

Verse 20 — Surah Al-Fath 48:20

“Allah wakulonjezani zofunkha zambiri zapankhondo (zomwe) mudzazitenga, ndipo wachita changu kukupatsani izi, (zinazo asanakupatseni). Ndipo watsekereza manja a anthu pa inu (kuti asakumenyeni). Ndi kuti chikhale chisonyezo cha okhulupirira (amene akudza pambuyo panu), ndi kuti akuongolereni kunjira yolunjika

Verse 21 — Surah Al-Fath 48:21

“Ndi zina zimene simudazithe (kuzipeza); Allah wazidziwa. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

Verse 22 — Surah Al-Fath 48:22

“Ndipo akadayesa kumenyana nanu amene sadakhulupirire; akadatembenuza misana kuthawa; kenako sakadapeza mthandizi kapena mtetezi

Verse 23 — Surah Al-Fath 48:23

“Iyi ndinjira ya Allah imene idapita kale, ndipo sungapeze kusintha pa njira ya Allah

Verse 24 — Surah Al-Fath 48:24

“Ndipo Iye ndi amene adatsekereza manja awo pa inu; ndi manja anu pa iwo, pa chigwa cha Makka, pambuyo pokupambanitsani pa iwo. Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita

Verse 25 — Surah Al-Fath 48:25

“Iwowo ndiamene sadakhulupirire, ndipo adakutsekerezani kulowa mu Msikiti Wopatulika pomwe nyama zansembe zidangomangika osakafika pamalo pake. Kukadakhala kuti kulibe amuna okhulupirira ndi akazi okhulupirira omwe simudawadziwe kuti mungawaponde potero inu kukanakupezani kudzudzulidwa kuchokera kwa iwo popanda kudziwa, (Allah akadakulolezani kumenyana nawo. Koma wachita izi) kuti Iye amulowetse ku mtendere Wake amene wamfuna. Akadadzipatula, tikadawalanga ndi chilango chowawa amene sadakhulupirire pakati pawo

Verse 26 — Surah Al-Fath 48:26

“Pamene omwe sadakhulupirire adaika mkwiyo m’mitima, mkwiyo waumbuli, Allah adatsitsa chikhazikiko Chake ndi kudekha pa Mtumiki Wake ndi pa okhulupirira, ndipo adawalimbikitsa ndi mawu woopa Allah; ndipo adali eni mawuwo ndi oyenerana nawo. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

Verse 27 — Surah Al-Fath 48:27

“Ndithu Allah adamtsimikizira Mtumiki Wake za maloto ake owona: “Ndithu inu mudzalowa mu Msikiti Wopatulika mwamtendere Allah akafuna; mutameta mitu yanu mpala kapena (ena) kuyepula (tsitsi lawo), simudzaopa (nthawi imeneyo); ndipo Allah amadziwa zimene simumazidziwa, ndipo zisanapezeke zimenezo, akupatsani kupambana kumene kuli pafupi

Verse 28 — Surah Al-Fath 48:28

“Iye ndi Yemwe adatumiza Mtumiki Wake ndi chiongoko ndi chipembedzo choona kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse. Ndipo Allah akukwanira kukhala mboni (yake)

Verse 29 — Surah Al-Fath 48:29

“Muhammad (s.a.w) ndi Mtumiki wa Allah; ndipo amene ali pamodzi ndi iye ngamphamvu kwa osakhulupirira (Allah), ngachifundo chambiri pakati pawo. Uwaona akugwira m’maondo ndi kugwetsa nkhope zawo pansi ncholinga chofuna zabwino za Allah ndi chikondi (Chake). Zizindikiro zawo zili pa nkhope zawo zosonyeza kulambira kwawo. Ili ndi fanizo lawo m’Chipangano chakale, Ndipo fanizo lawo m’Chipangano chatsopano nkuti iwo ali monga mmera womwe watulutsa nthambi zake; kenako (nthambizo) nkuulimbitsa ndi kukhala waukulu ndi kuima bwinobwino ndi tsinde lake, nkuwasangalatsa omwe adaubzala. (Choncho) zotsatira zake, nkuwakwiyitsa osakhulupirira chifukwa cha iwo. Allah walonjeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa) amene akhulupirira ndi kuchita zabwino mwa iwo