“E inu amene mwakhulupirira! Musamatsogoze (kulamula chinthu chapachipembedzo kapena cham’dziko) patsogolo pa (mawu a) Allah ndi Mthenga Wake. Ndipo muopeni Allah, ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa
“Ndithu amene akutsitsa mawu awo pamaso pa mtumiki wa Allah, iwo ndiamene Allah wawayeretsa mitima yawo pomuopa Iye; chikhululuko ndi malipiro akulu zidzakhala pa iwo
“Ndipo iwo akadapirira ndi kuyembekeza (kuti) mpaka utuluke ndi kudza kwa iwo, zikadakhala zabwino kwa iwo; koma Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha
“Ndipo dziwani kuti ndithu mwa inu muli Mtumiki wa Allah, (mumvereni iye zimene akukuuzani) kukadakhala kuti iye akukumverani pa zinthu zambiri (zimene mukumuuza), mukadavutika. Koma Allah wachichita chikhulupiliro kukhala chokondeka kwa inu ndipo wachikometsa m’mitima mwanu ndipo wakuchitani kuti mukude kusakhulupirira ndi ufasiki (kutuluka m’malamulo a Allah) ndi kunyoza (Allah.) Iwowo ndiwo oongoka
“E inu anthu! Tidakulengani (nonse) kuchokera kwa mwamuna (m’modzi; Adam) ndi mkazi (m’modzi; Hawa), ndipo tidakuchitani kukhala a mitundu ndi mafuko (osiyanasiyana) kuti m’dziwane (basi). Ndithu wolemekezeka kwambiri mwa inu kwa Allah, ndi yemwe ali woopa. Ndithu Allah Ngodziwa, ndipo Ngodziwa kwambiri nkhani zonse
“Nena: “Kodi mukumdziwitsa Allah za chipembedzo chanu? Koma chikhalirecho Allah akudziwa zonse za kumwamba ndi za m’dziko lapansi. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse