Back to Languages

Chichewa - Chapter 5 - Al-Maidah

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Maidah 5:1

“E inu amene mwakhulupirira! Kwaniritsani mapangano onse (omwe ali pakati panu ndi anthu anzanu). Kwalolezedwa kwa inu (kudya nyama ya) ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi), kupatula chomwe mukuuzidwa (kuti ncholetsedwa). Koma nkosaloledwa kwa inu kuchita ulenje mutalowa m’mapemphero a Hajj, (kapena muli m’nthaka yopatulika ya ku Makka). Ndithudi, Allah akulamula chimene wafuna

Verse 2 — Surah Al-Maidah 5:2

“E inu amene mwakhulupirira! Musanyozere kupatulika kwa zizindikiro za Allah (pochiyesa chosapatulika chomwe Allah wachichita kukhala chopatulika; monga kutuluka m’mapemphero a Hajj usadakwaniritse), kapenanso (kunyozera) kupatulika kwa mwezi wopatulika (poyambitsa nkhondo mmenemo), kapena (kupatulika kwa nyama zomwe zatumizidwa ku Makka monga) nsembe, kapena (kuchotsa kupatulika kwa) makoza (omwe nyamazo zimavekedwa monga chizindikiro chosonyeza kuti ndinsembe ya ku Makka), kapena (kupatulika kwa) omwe akulinga kupita kunyumba yopatulika (ku Makka), (omwe akupita kumeneko) ndi cholinga chofunafuna ubwino wa Mbuye wawo ndi chiyanjo Chake. Ndipo ngati mutatuluka m’mapemphero anu a Hajj mukhoza kuchita ulenje (ngati mutafuna); ndipo kusakuchititseni kuwada anthu chifukwa chakuti adakutsekerezani kufika ku Msikiti Wopatulika (wa ku Makka) kuti mulumphe malire (pobwezera mtopola umene adakuchitirani). Koma thandizanani pa zabwino ndikuopa (Allah); musathandizane pa machimo ndi pa chidani. Ndipo muopeni Allah. Ndithu Allah Ngwaukali pokhaulitsa

Verse 3 — Surah Al-Maidah 5:3

“Kwaletsedwa kwa inu (kudya) chakufa chokha, liwende, nyama ya nkhumba, chomwe chazingidwa m’dzina osati la Allah, chomwe chafa ndi kubanika, chomwe chafa ndi kumenyedwa, ndi chimene chafa pakugwa kuchokera pamwamba, chimene chafa polasidwa ndi nyanga (yachinzake), chomwe chafa pakujiwa ndi chilombo (cha m’thengo) kupatula chomwe mwachipeza chili rnoyobe nkuchizinga ndi chimene chazingidwa paguwa la mafano; ndiponso (nkoletsedwa kwa inu) kufuna kudziwa zobisika pochita maula. Zonsezi ndi uchimo. Lero amene sadakhulupirire ataya mtima (za kugonjetsa) chipembedzo chanu. Choncho musawaope, koma opani Ine. Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu ndipo ndakwaniritsa pa inu chisomo changa. Ndakusankhirani Chisilamu kukhala chipembedzo chanu. Koma amene wasimidwa chifukwa chanjala, popanda kupendekera kumachimo, (nkudya zoletsedwazi, palibe kanthu). Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

Verse 4 — Surah Al-Maidah 5:4

“Akukufunsa (Asilamu) chomwe chaloledwa kwa iwo (kudya). Nena: “Chaloledwa kwa inu chilichonse chabwino. Ndi (chimene chagwidwa ndi) nyama kapena mbalame zaukali zomwe mwaziphunzitsa kusaka. Muziphunzitse zimene Allah wakuphunzitsani. Choncho idyani chimene zakugwilirani, ndipo chitchulireni dzina la Allah pochikhwirizira. Ndipo opani Allah. Ndithudi Allah Ngwachangu pakuwerengera

Verse 5 — Surah Al-Maidah 5:5

“Lero mwaloledwa zonse zabwino ndi chakudya cha omwe adapatsidwa buku nchololedwa kwa inu, ndiponso chakudya chanu nchololedwa kwa iwo, ndipo (mukuloledwa kuwakwatira) akazi abwino a mwa okhulupirira ndi akazi abwino a mwa omwe adapatsidwa ma buku kale, ngati mwawapatsa chiwongo chawo m’njira yomanga nawo ukwati, osati mochita nao chiwerewere, osatinso mochita nao zibwenzi. Ndipo amene akane kukhulupirira, ndiye kuti yaonongeka ntchito yake; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mwa oluza (otaiyika)

Verse 6 — Surah Al-Maidah 5:6

““E inu amene mwakhulupirira! Pamene mwaimilira kuti mukaswali, sambitsani nkhope zanu, ndi manja anu mpaka mmagongono; ndipo pakani madzi pa mitu panu ndi kusambitsa mapazi anu mpaka mu akakolo. Ngati muli ndi janaba dziyeretseni (sambani thupi lonse); ndipo ngati muli odwala kapena muli paulendo, kapena mmodzi wanu wachokera kokadzithandiza kapenanso mwakhalira limodzi ndi mkazi, ndiye simudapeze madzi, chitani Tayammamu ndi dothi labwino ndipo pakani ku nkhope zanu ndi mmanja mwanu. Allah sakufuna kukuvutitsani, koma akufuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa chisomo chake pa inu kuti muthokoze

Verse 7 — Surah Al-Maidah 5:7

“Ndipo kumbukirani chisomo cha Allah pa inu ndi pangano lake lomwe mudapangana Naye, pamene mudati: “Tamva, ndipo tamvera.” Muopeni Allah. Ndithudi Allah Ngodziwa za m’mitima

Verse 8 — Surah Al-Maidah 5:8

“E inu amene mwakhulupirira! Khalani olungama kwa Allah, opereka umboni mwachilungamo, ndipo chidani cha anthu pa inu chisakuchititseni kuti musachite chilungamo. Chitani chilungamo; kutero kumakuyandikitsani ku “taquwa” (kuopa Allah). Ndipo opani Allah. Ndithudi, Allah Ngodziwa nkhani zonse za (zinthu) zomwe muchita

Verse 9 — Surah Al-Maidah 5:9

“Allah walonjeza omwe akhulupirira ndi kuchita zabwino kuti adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu

Verse 10 — Surah Al-Maidah 5:10

“Ndipo amene sadakhulupirire, natsutsa zizindikiro Zathu, iwo ndi anthu a ku Moto

Verse 11 — Surah Al-Maidah 5:11

“E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani mtendere wa Allah omwe uli pa inu, pamene anthu ena adatsimikiza kukutambasulirani manja awo (pofuna kuchita nanu nkhondo) koma (Allah) adawatsekereza manja awo kukufikani inu. Choncho opani Allah. Ndipo kwa Allah Yekha, ayadzamire okhulupirira

Verse 12 — Surah Al-Maidah 5:12

“Ndipo ndithudi, Allah adamanga pangano ndi ana a Israyeli, ndipo tidawaikira Akuluakulu khumi ndi awiri mwa iwo. Ndipo Allah adati: “Ndithudi Ine ndili pamodzi ndi inu, ngati mupemphera Swala ndikupereka chopereka, ndikukhulupirira atumiki Anga, ndi kuwalemekeza ndi kumkongoza Allah Ngongole yabwino, ndithudi ndikufafanizirani zoipa zanu, ndikudzakulowetsani m’Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje. Koma amene akane mwa inu pambuyo pa (chipangano) ichi, ndithu wasochera njira yowongoka.”

Verse 13 — Surah Al-Maidah 5:13

“Choncho chifukwa chakuswa pangano lawo, tidawatembelera; ndipo tidaumitsa mitima yawo. Ankasintha mawu (a Allah omwe adali m’mabuku a Taurat ndi Injili) kuwachotsa m’malo mwake ndipo adasiya kukwaniritsa gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Ndipo ukhala ukuona (iwe Mtumiki {s.a.w}) chinyengo mwa ambiri a iwo, kupatula ochepa a iwo. Choncho akhululukire ndi kuwaleka. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino

Verse 14 — Surah Al-Maidah 5:14

“Naonso aja amene akuti: “Ife ndife Akhrisitu,” tidalandira pangano lawo koma adasiya gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Tero tidabzala pakati pawo chidani ndi kusakondana mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah adzawawuza zimene adali kuchita

Verse 15 — Surah Al-Maidah 5:15

“E inu anthu a buku! Ndithudi wakufikani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani poyera zambiri zomwe munkabisa za m’buku. Koma akusiya zambiri (posazilongosola). Ndithudi kwakudzerani kuunika kochokera kwa Allah ndi buku lomwe likufotokoza mwatchutchutchu (chinthu chilichonse)

Verse 16 — Surah Al-Maidah 5:16

“Ndi bukulo Allah akuwatsogolera kunjira zamtendere amene akutsata chiyanjano chake ndikuwatulutsa mu m’dima ndi kuwaika m’kuunika mwa lamulo Lake, ndi kuwatsogolera kunjira yoongoka

Verse 17 — Surah Al-Maidah 5:17

“Ndithudi, amukana (Allah) amene akunena kuti Mulungu ndiye Mesiya Mwana wa Mariya. Nena: “Ndani akadatha kuletsa chilichonse kwa Allah ngati Iye akadafuna kuononga Mesiya mwana wa Mariya ndi mayi wakeyo, ndi onse omwe ali m’dziko lapansi? Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake ngwa Allah. Amalenga chimene wafuna. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.”

Verse 18 — Surah Al-Maidah 5:18

“Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu akunena: “Ife ndife ana a Mulungu ndiponso okondeka ake.” Nena: (Iwe Mtumiki) “Nchifukwa ninji Allah amakukhaulitsani kamba ka machimo anu? Koma inu ndinu anthu chabe mwa omwe adawalenga. Amamkhululukira amene wamfuna; ndipo amamulanga amene wamfuna. Ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi za pakati pake ngwa Allah. Ndipo kwa Iye nkobwerera.”

Verse 19 — Surah Al-Maidah 5:19

“E inu anthu a buku! Ndithudi, wakudzerani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani inu, pa nthawi yopanda atumiki, kuti musadzanene kuti: “Sadadze kwa ife wonena nkhani zabwino ndiwochenjeza.” Choncho wakudzeranidi wonena nkhani zabwino ndi wochenjeza. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

Verse 20 — Surah Al-Maidah 5:20

“(Ndipo kumbukirani) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Inu anthu anga! Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu, pamene adawachita ena mwa inu kukhala aneneri; ndipo adakuchitani kukhala mafumu (pambuyo poti mudali onyozeka m’dziko la Iguputo m’manja mwa Farawo). Ndipo wakupatsani zomwe sadampatsepo aliyense mwa zolengedwa.”

Verse 21 — Surah Al-Maidah 5:21

““Inu anthu anga. Lowani m’dziko loyeretsedwalo limene Allah adakulemberani, ndipo musabwelere m’mbuyo kuti mungasanduke otaika.”

Verse 22 — Surah Al-Maidah 5:22

“(Iwo) adati: “Iwe Mûsa, ndithudi mmenemo muli anthu amphamvu. Ndipo ife sitikalowamo kufikira atatulukamo okha. Choncho ngati atatulukamo, pamenepo ndiye tikalowa.”

Verse 23 — Surah Al-Maidah 5:23

“Anthu awiri mwa amene ankaopa Allah, omwe awiriwo Allah adawapatsa chisomo, adati (kwa anzawo): “Alowereni pa chipata (cha dzikolo). Ngati mukalowamo ndithudi, inu mukapambana. Ndipo kwa Allah Yekha yadzamirani ngati inu mulidi okhulupirira.”

Verse 24 — Surah Al-Maidah 5:24

“(Iwo) adati: “Iwe Mûsa, ife sitikalowamo mpang’ono pomwe, pomwe iwo ali momwemo. Choncho pita iwe ndi Mbuye wako, ukamenyane nawo; ife tikhala pompano.”

Verse 25 — Surah Al-Maidah 5:25

“(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Ndithudi, ine ndilibe nyonga (yokakamizira aliyense kutsatira lamulo Lanu) koma pa ine ndekha ndi pa m’bale wanga. Choncho tisiyanitseni ndi anthu awa opandukira chilamulo.”

Verse 26 — Surah Al-Maidah 5:26

“Allah adati: “Choncho laletsedwa dzikolo kwa iwo kulilowa kwa zaka makumi anayi. Akhala akuyendayenda pa dziko. Tero, usawadandaulire anthu opandukira chilamulo.”

Verse 27 — Surah Al-Maidah 5:27

“Ndipo awerengere nkhani mwachoonadi ya ana awiri a Adam, pamene adapereka nsembe. Ndipo idalandiridwa ya mmodzi wawo, koma ya winayo siidalandiridwe. (Amene nsembe yake siidalandiridwe) adati (kwa mnzake): “Ndithudi ndikupha.” Mnzakeyo adati: “Ndithudi, Allah amalandira nsembe ya amene akuopa (Allah).”

Verse 28 — Surah Al-Maidah 5:28

““Ngati utambasula dzanja lako pa ine kuti undiphe, ine sinditambasula dzanja langa pa iwe kuti ndikuphe. Ndithudi, ine ndikuopa Allah Mbuye wa zolengedwa.”

Verse 29 — Surah Al-Maidah 5:29

““Ine ndikufuna kuti usenze machimo anga pamodzi ndi machimo ako, choncho ukakhale m’gulu la anthu a ku Moto. Ndipo awo ndio malipiro a anthu ochita zoipa.”

Verse 30 — Surah Al-Maidah 5:30

“Choncho mtima wake udamkometsera kupha m’bale wake, ndipo adamuphadi. Tero adali wotaika

Verse 31 — Surah Al-Maidah 5:31

“Pamenepo Allah adatumiza khwangwala yemwe amafukula pansi kuti amusonyeze mmene angakwililire mtembo wa m’bale wake. (Wopha mnzake) adati: “Kalanga ine! Ndalephera kuti ndifanane ndi khwangwala uyu, kuti ndikwilire mtembo wa m’bale wanga.” Choncho adali mmodzi mwa odzinena

Verse 32 — Surah Al-Maidah 5:32

“Pachifukwa chazimenezo, tidawalamula ana a Israyeli kuti amene wapha munthu popanda iye (wophedwayo) kupha munthu, kapena kuchita chisokonezo pa dziko, ali ngati wapha anthu onse. Ndipo amene wamuleka munthu ali ndi moyo, ali ngati awapatsa moyo anthu onse. Ndithudi, atumiki Athu adawadzera iwo ndi zisonyezo zoonekera. Koma ndithu ambiri a iwo, pambuyo pa zimenezo, adapitirizabe kuononga pa dziko

Verse 33 — Surah Al-Maidah 5:33

“Ndithu mphoto ya amene akulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake (pochita zomwe waletsa) ndi kudzetsa chionongeko pa dziko, aphedwe kapena apachikidwe pa mtanda, kapena adulidwe manja awo ndi miyendo yawo mosemphanitsa (dzanja lakumanja ndi phazi lakumanzere, ndipo dzanja lakumanzere ndi phazi lakumanja); kapena apirikitsidwe mdzikomo. Uku ndikuyaluka kwawo pa dziko lapansi. Ndipo iwo pa tsiku lachimaliziro adzalandira chilango chachikulu

Verse 34 — Surah Al-Maidah 5:34

“Kupatula amene alapa musanawagwire. Ndipo dziwani kuti Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

Verse 35 — Surah Al-Maidah 5:35

“E inu amene mwakhulupirira! Muopeni Allah ndipo funafunani njira zokufikitsani kwa Iye. Menyani nkhondo pa njira yake kuti mupambane

Verse 36 — Surah Al-Maidah 5:36

“Ndithudi, aja amene sadakhulupirire, akadakhala ndi zonse za m’dziko ndi zina zonga izo kuti azipereke monga dipo kuti apulumuke kuchilango cha tsiku lachimaliziro (Qiyâma) sizikadavomerezedwa kwa iwo. Ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka

Verse 37 — Surah Al-Maidah 5:37

“Adzafuna (mwanjira iliyonse) kuti atuluke ku Moto, koma sadzatulukamo. Ndipo adzakhala ndi chilango chamuyaya

Verse 38 — Surah Al-Maidah 5:38

“Ndipo wakuba wamwamuna ndi wakuba wamkazi, aduleni manja awo; kukhala mphoto ya zomwe achita ndi chilango chochokera kwa Allah. Allah Ngwanyonga zoposa, Ngwanzeru zakuya

Verse 39 — Surah Al-Maidah 5:39

“Koma amene walapa pambuyo pakuchita kwake zoipa, namachita zabwino, Allah alandira kulapa kwake. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha

Verse 40 — Surah Al-Maidah 5:40

“Kodi sukudziwa kuti Allah Ngwake ufumu wa kumwamba ndi pansi? amamulanga yemwe wamfuna (akalakwa), ndipo amamukhululukira amene wamfuna. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

Verse 41 — Surah Al-Maidah 5:41

“E iwe Mtumiki! Asakudandaulitse amene akuchita changu kukana Allah mwa omwe akunena ndi pakamwa pawo chabe: “Takhulupirira,” pomwe mitima yawo siikukhulupirira. Namonso mwa Ayuda, alipo amene amamvetsera (zimene ukunena) kuti azikanena bodza, amamvetsera mmalo mwa anthu ena amene sadadze kwa iwe (omwe ndi akuluakulu awo), amasintha mawu (a m’buku la Taurat) m’malo mwake, omwenso amanena (kuuza otsatira awo kuti): “Ngati mukapatsidwe (ndi Muhammad {s.a.w}) izi (takuuzanizi), kalandireni, koma ngati musakapatsidwe zimenezi kachenjereni.” Ndipo munthu yemwe Allah akufuna kuti amuyese mayeso sungathe kumpezera chilichonse kwa Allah. Iwowo ndiomwe Allah sadafune kuyeretsa mitima yawo. Apeza kuyaluka pa dziko lapansi. Ndipo tsiku lachimaliziro adzapeza chilango chachikulu

Verse 42 — Surah Al-Maidah 5:42

“Okonda kumvetsera zabodza; osaopa pakudya (zinthu) zoletsedwa (zaharamu). Choncho akakudzera aweruze pakati pawo, kapena uwapatukire. Ndipo ngati uwapatukira, palibe chomwe angakuvutitse nacho. Ngati uweruza pakati pawo weruza mwachilungamo. Ndithudi, Allah amakonda olungama

Verse 43 — Surah Al-Maidah 5:43

“Kodi angakuyese muweruzi chotani pomwe iwo alinayo Taurat momwe muli chiweruzo cha Allah. Pambuyo powaweruza akutembenuka (monyoza)! Ndipo iwo sali okhulupirira

Verse 44 — Surah Al-Maidah 5:44

“Ndithudi, tidaivumbulutsa Taurat yokhala ndi chiongoko ndi kuunika; aneneri (a Allah) omwe adagonjera (Allah), adali kulamulira nayo Ayuda, ndiponso Arabbaniyyuna (aphunzitsi a malamulo) ndi Ahabaru (Ansembe) omwe adapemphedwa kusunga buku la Allah ndipo iwo adali mboni pa ilo, choncho (inu Asilamu) musaope anthu, koma opani Ine. Ndipo musasinthanitse Ayah (ndime) zanga ndi (zinthu za) mtengo wochepa. Ndipo amene sakuweruza ndi chimene Allah wavumbulutsa, iwowo ndiwo osakhulupirira (okana Allah)

Verse 45 — Surah Al-Maidah 5:45

“Ndipo m’menemo (m’buku la Taurat) tidawalamula kuti: “Munthu aphedwe chifukwa chopha mnzake, ndi kuti diso kwa diso, mphuno kwa mphuno; khutu kwa khutu; dzino kwa dzino, ndiponso kubwezerana mabala.” Koma amene wakhululuka ndiye kuti dipo likhala kwa iye. Ndipo amene saweruza ndi chimene Allah wavumbulutsa iwowo ndiwo anthu ochita zoipa

Verse 46 — Surah Al-Maidah 5:46

“Ndipo tidatsatiza pa mapazi a aneneriwo, Isa (Yesu) mwana wa Mariya kudzatsimikizira zomwe zidali patsogolo pake m’buku la Taurat. Ndipo tidampatsa Injili yomwe m’kati mwake muli chiongoko ndi kuunika; ndikutsimikizira zomwe zidali patsogolo pake za m’buku la Taurat. Ndipo ndi chiongoko ndi ulaliki wabwino kwa oopa (Allah)

Verse 47 — Surah Al-Maidah 5:47

“Anthu abuku la Injili alamulire potsatira zimene Allah adavumbulutsa mmenemo. Ndipo amene asiya kulamulira ndi zomwe Allah wavumbulutsa iwo ndiwo opandukira malamulo (a Allah)

Verse 48 — Surah Al-Maidah 5:48

“Ndipo takuvumbulutsira buku mwa choonadi, lomwe likuikira umboni mabuku omwe adalipo patsogolo pake, ndi kuwateteza, (monga ponena kuti: “Lamulo ili ndiloona; ili iyayi.”) Choncho weruza pakati pawo ndi zomwe Allah wavumbulutsa, ndipo usatsate zofuna zawo kusiya choona chomwe chakufika. Ndipo m’badwo uliwonse mwa inu tidaupangira shariya (malamulo) yake ndi njira yake. Allah akadafuna, akadakuikani kukhala mpingo umodzi (wotsata chilamulo chofanana). Koma akufuna kukuyesani pa zomwe wakupatsani. Choncho pikisanani pa zinthu zabwino. Inu nonse kobwerera kwanu nkwa Allah. Naye adzakuuzani (nonsenu) mu zomwe mudali kusiyana

Verse 49 — Surah Al-Maidah 5:49

“Weruza pakati pawo ndi chimene Allah wavumbulutsa, ndipo usatsate zofuna zawo, koma chenjera nawo kuti angakusokoneze nkusiya zina mwa zimene Allah wavumbulutsa kwa iwe. Ndipo ngati anyozera dziwa kuti Allah afuna kuwapatsa chilango cha ena mwa machimo awo. Ndithudi, anthu ambiri ngopandukira (malamulo a Allah)

Verse 50 — Surah Al-Maidah 5:50

“Kodi iwo akufuna chiweruzo cha nthawi yaumbuli (chamasiku aumbuli, Chisilamu chisanadze)? Kodi ndani ali wabwino poweruza kuposa Allah kwa anthu otsimikiza (kuti Allah alipo)

Verse 51 — Surah Al-Maidah 5:51

“E inu amene mwakhulupirira! Ayuda ndi Akhrisitu musawapale ubwenzi (nkumawauza chinsinsi chanu). Iwo pakati pawo ndi abwenzi ndi atetezi kwa wina ndi mnzake. Amene awapale ubwenzi mwa inu, ndiye kuti iye ndi m’modzi wa iwo. Ndithudi, Allah satsogolera anthu ochita zoipa

Verse 52 — Surah Al-Maidah 5:52

“Uwaona omwe m’mitima mwawo muli matenda (a chinyengo) akuthamangira kwa iwo (Ayuda) uku akuti: “Tikuopa lingatigwere tsoka (ngati Asilamuwa atagwa m’tsoka), koma posachedwapa Allah abweretsa lamulo logonjetsa (midzi), kapena chinthu china chochokera kwa Iye (monga kuwaulula achinyengo zomwe akubisa m’mitima mwawo). Choncho adzasanduka odzinena chifukwa cha zomwe adabisa m’mitima mwawo

Verse 53 — Surah Al-Maidah 5:53

“Ndipo amene adakhulupirira nayamba kunena (chitaululika chinyengo cha achinyengowo): “Kodi awa si omwe adali kulumbilira dzina la Allah m’kulumbilira kwawo kwamphamvu kuti iwo ali pamodzi ndi inu?” Zochita zawo zaonongeka. Tero akhala otaika

Verse 54 — Surah Al-Maidah 5:54

“E inu amene mwakhulupirira! Amene mwa inu asiye chipembedzo chake, ndiye kuti posachedwapa Allah abweretsa anthu omwe awakonda, nawonso amkonda; odzichepetsa kwa okhulupirira (anzawo); amphamvu kwa osakhulupirira; omenyera nkhondo chipembedzo cha Allah, saopa kudzudzula kwa odzudzula. Umenewu ndi ubwino wa Allah; amaupereka kwa amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mataya; Ngodziwa kwambiri

Verse 55 — Surah Al-Maidah 5:55

“Ndithu mtetezi wanu ndi Allah ndi Mtumiki wake ndi omwe akhulupirira omwe akupemphera Swala ndi kupereka Zakaat uku ali odzichepetsa

Verse 56 — Surah Al-Maidah 5:56

“Ndipo amene achite Allah ndi Mtumiki Wake, ndi omwe akhulupirira kukhala atetezi ake, (ndithu iwo ndi a chipani cha Allah). Ndithu chipani cha Allah ndicho chopambana

Verse 57 — Surah Al-Maidah 5:57

“E inu amene mwakhulupirira! Musapalane nawo ubwenzi omwe akuchichitira chipongwe ndi masewera Chipembedzo chanu mwa omwe apatsidwa mabuku patsogolo panu, ndiponso mwa osakhulupirira, ndipo opani Allah ngati inu mulidi okhulupirira

Verse 58 — Surah Al-Maidah 5:58

“Mukaitanira kokapemphera Swala (mukachita azana) akuichitira chipongwe ndi masewera; ndithudi zimenezo nchifukwa chakuti iwo ndianthu opanda nzeru

Verse 59 — Surah Al-Maidah 5:59

“Nena: “E inu anthu a buku! Kodi mukuona cholakwika kwa ife kaamba kakuti takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwenso zidavumbulutsidwa kale? Ndithudi, ambiri mwa inu ndi opandukira chilamulo (cha Allah).”

Verse 60 — Surah Al-Maidah 5:60

“Nena: “Kodi ndikuuzeni za uja amene ali ndi malipiro oipa kwa Allah kuposa izi? Ndiomwe Allah wawatembelera ndi kuwakwiira ndi kuwasandutsa ena kukhala anyani ndi nkhumba, ndi opembeza satana. Awo ndiwo okhala ndi malo oipa, ndiponso osokera njira yowongoka.”

Verse 61 — Surah Al-Maidah 5:61

“Ndipo (achinyengo) akakudzerani, akunena: “Takhulupirira,” pamene alowa kwa inu ali osakhulupirira ndipo atulukanso ali osakhulupirira. Koma Allah Ngodziwa kwambiri zomwe akhala akubisa

Verse 62 — Surah Al-Maidah 5:62

“Uwaona ambiri a iwo akuthamangira machimo ndi mtopola ndi kudya zoletsedwa. Ndithudi, zimene akhala akuchitazo ndizoipa zedi

Verse 63 — Surah Al-Maidah 5:63

“Bwanji odziwa za malamulo ndi akuluakulu a chipembedzo sadawaletse zoyankhula za uchimo ndi kudya kwawo zinthu zoletsedwa? Ndithudi, zomwe akhala akuchitazo ndi zoipa zedi

Verse 64 — Surah Al-Maidah 5:64

“Ndipo Ayuda adati: “Dzanja la Allah lafumbatika (sitikupeza chuma ngati kale). (Koma sichoncho); manja awo ndiwo afumbatika (posachita zabwino ndi kuchenjelera anthu). Ndipo atembeleredwa chifukwa cha zomwe anena. Koma manja ake (Allah) ngotambasuka. Amapatsa mmene wafunira. Ndithudi, zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, ziwaonjezera ambiri a iwo (Ayuda) kulumpha malire ndi kusakhulupirira. Ndipo taika chidani ndi kusakondana pakati pawo mpaka tsiku la chimariziro. Nthawi iliyonse akayatsa moto wa nkhondo, Allah amauzimitsa. Ndipo amayesetsa kudzetsa chisokonezo pa dziko, (koma Allah sawathandiza). Ndipo Allah sakonda owononga

Verse 65 — Surah Al-Maidah 5:65

“Ndipo kukadakhala kuti awa anthu a buku adakhulupirira ndi kumuopa Allah, tikadawafafanizira zolakwa zawo, ndi kuwalowetsa m’minda ya mtendere

Verse 66 — Surah Al-Maidah 5:66

“Akadakhala kuti iwo adaigwiritsa ntchito Taurat ndi Injili, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwo kuchokera kwa Mbuye wawo (monga Qurani), ndithudi akanadya za kumwamba ndi za pansi pa myendo yawo. Mwa iwo alipo amene akutsatira njira yabwino. Komanso ambiri mwa iwo nzoipa zedi zomwe akuchita

Verse 67 — Surah Al-Maidah 5:67

“E iwe Mtumiki! Fikitsa (kwa anthu) zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako. Ngati suchita, ndiye kuti sudafikitse uthenga Wake. Ndipo Allah akuteteza kwa anthu; (usaope aliyense). Ndithudi, Allah satsogolera anthu osakhulupirira

Verse 68 — Surah Al-Maidah 5:68

“Nena: “E inu anthu a buku! Simuli kanthu (pa chipembedzo chanu) mpaka muimilire (kutsatira malamulo) a Taurat ndi Injili ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu, ziwaonjezera kulakwa ndi kusakhulupirira ambiri a iwo zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, choncho usadandaule za anthu osakhulupirira

Verse 69 — Surah Al-Maidah 5:69

“Ndithudi, amene akhulupirira ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi Asabayi, ndi Akhrisitu, - amene akhulupirire Allah ndi tsiku lachimaliziro, (monga momwe akulangizira Mtumiki Muhammad {s.a.w}) nachita zabwino, - palibe mantha kwa iwo ndiponso sadzadandaula

Verse 70 — Surah Al-Maidah 5:70

“Ndithudi, tidalandira pangano kwa ana a Israyeli (kuti adzamvera Allah) ndipo tidawatumizira atumiki. Nthawi iliyonse akawadzera mtumiki ndi chomwe mitima yawo siinkafuna, adawatsutsa ena (mwa atumikiwo), ndipo ena ankawapha kumene

Verse 71 — Surah Al-Maidah 5:71

“Ndipo ankaganiza kuti sipapezeka chilango; tero adali akhungu ndi agonthi. Kenako Allah adawalandira kulapa kwawo (pamene adalapa). Komabe ambiri a iwo adali akhungu, ndi ogontha. Ndipo Allah akuona zimene akuchita

Verse 72 — Surah Al-Maidah 5:72

“Ndithudi am’kana Allah amene anena kuti, Mulungu ndiye Isa (Yesu) mwana wa Mariya.” Pomwe Mesiya adati: “Inu ana a Israyeli! Pembedzani Allah Yemwe ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.” Ndithudi, amene aphatikize Allah ndi chinthu china, ndithudi Allah waletsa kwa iye kukalowa ku Munda wamtendere, ndipo malo ake ndi ku Moto. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi

Verse 73 — Surah Al-Maidah 5:73

“Ndithudi, am’kana Allah amene amanena kuti “Ndithu Allah ndi mmodzi mwa (milungu) itatu,” pomwe palibe mulungu wina koma Mulungu Mmodzi yekha. Ngati sasiya zomwe akunenazo, ndithudi, mwa iwo amene sadakhulupirire chiwakhudza chilango chopweteka

Verse 74 — Surah Al-Maidah 5:74

“Kodi salapa kwa Allah ndi kumpempha chikhululuko? Komatu Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

Verse 75 — Surah Al-Maidah 5:75

“Mesiya mwana wa Mariya sali chilichonse koma ndi Mtumiki wa Allah chabe. Ndithudi, atumiki ambiri adapita kale patsogolo pake. Nayenso mayi wake ndi mkazi wachoonadi, onse awiri adali kudya chakudya, (ndipo chotsatira chake amapita kokadzithandiza. Nanga ndi milungu yotani yopita kukadzithandiza?) Taona momwe tikufotokozera kwa iwo zizindikiro. Taonanso mmene akutembenuziridwa (kusiya choonadi)

Verse 76 — Surah Al-Maidah 5:76

“Nena: “Kodi mukupembedza chimene sichingakupatseni vuto ngakhale chabwino, kusiya Allah? Pomwe Allah ndiye Wakumva, Wodziwa.”

Verse 77 — Surah Al-Maidah 5:77

“Nena: “E inu anthu a buku! Musapyole malire pa chipembedzo chanu popanda choonadi ndipo musatsatire zofuna za anthu omwe adasokera kale, nawasokeretsanso ambiri, ndi kusokera kunjira yowongoka (yolungama).”

Verse 78 — Surah Al-Maidah 5:78

“Adatembeleredwa amene sadakhulupirire nwa ana a Israyeli kupyolera m’lirime la Daud ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Zimenezo nchifukwa chakuti adanyoza ndipo adali opyola malire

Verse 79 — Surah Al-Maidah 5:79

“Sadali kuletsana choipa chomwe adali kuchichita. Taona kuipitsitsa zomwe adali kuchita

Verse 80 — Surah Al-Maidah 5:80

“Uwaona ambiri a iwo akupalana ubwenzi ndi omwe sadakhulupirire Allah, (opembedza mafano ndi cholinga chomenya nkhondo chipembedzo cha Chisilamu). Nzoipa kwambiri zomwe adadzitsogozera okha. Tero Allah adawakwiira ndipo m’masautso adzakhalamo nthawi yaitali

Verse 81 — Surah Al-Maidah 5:81

“Ndipo akadamkhulupirira Allah (moyenera) ndi mneneriyo (Muhammad {s.a.w}) ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa iye sakadawachita abwenzi. Koma ambiri a iwo ngopandukira chilamulo cha Allah

Verse 82 — Surah Al-Maidah 5:82

“۞ Ndithudi, uwapeza anthu amene ali oyipitsitsa pa chidani ndi anthu okhulupirira (Asilamu) ndi Ayuda komanso opembedza mafano. Ndipo uwapeza oyandikira ubwenzi ndi okhulupirira (Asilamu) ndi awo akunena kuti: “Ife ndi Akhrisitu.” Zimenezo n’chifukwa chakuti mwa iwo alipo ophunzira ndi oopa Allah, ndi chifukwanso chakuti iwo (Akhirisitu) sadzitukumula

Verse 83 — Surah Al-Maidah 5:83

“Ndipo akamva zomwe zavumbulutsidwa kwa Mtumiki, uona maso awo akugwetsa misozi chifukwa cha choonadi chomwe achizindikira. Akunena: “Mbuye wathu! Takhulupirira; choncho tilembeni pamodzi ndi oikira umboni (choonadi).”

Verse 84 — Surah Al-Maidah 5:84

“(Atadzudzulidwa polowa m’Chisilamu iwo adati): “Chifukwa ninji tisamkhulupirire Allah ndi choonadi chomwe chatifika, pomwe tikuyembekezera Mbuye wathu kukatilowetsa (ku Munda wamtendere) pamodzi ndi anthu abwino?”

Verse 85 — Surah Al-Maidah 5:85

“Choncho Allah adzawalipira, pa zomwe adanena, Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino

Verse 86 — Surah Al-Maidah 5:86

“Ndipo amene sadakhulipirire, nkutsutsa zizindikiro zathu, iwowo ndiwo anthu a ku Moto

Verse 87 — Surah Al-Maidah 5:87

“E inu amene mwakhulupirira! Musazichite zabwino zomwe Allah wakulolezani kukhala zoletsedwa. Ndipo musalumphe malire, ndithudi Allah sakonda anthu olumpha malire

Verse 88 — Surah Al-Maidah 5:88

“Idyani zabwino zomwe Allah wakupatsani zomwe zili zololedwa. Ndipo opani Allah yemwe inu mukumkhulupirira

Verse 89 — Surah Al-Maidah 5:89

“Allah sangakulangeni chifukwa chakulumbira kwanu kopanda pake. Koma akulangani kamba ka malumbiro omwe mwalumbira motsimikiza. Choncho dipo lake ndikuwadyetsa osauka khumi ndi chakudya cha mlingo wapakatikati chomwe mumawadyetsa anthu anu; kapena kuwaveka, kapena kumpatsa ufulu kapolo. Koma amene sangapeze zimenezo, asale masiku atatu. Ili ndi dipo la kulumbira kwanu pamene mukulumbira. Ndipo sungani malumbilo anu, (musaswe chomwe mudalumbilira). Motero ndi momwe Allah akukufotokozerani zizindikiro Zake kuti muthokoze

Verse 90 — Surah Al-Maidah 5:90

“E inu amene mwakhulupirira! Ndithudi, mowa (kutchova) njuga, kupembedza mafano ndi kuombeza maula, (zonsezi) ndi uve, mwa ntchito za satana. Choncho zipeweni kuti mupambane

Verse 91 — Surah Al-Maidah 5:91

“Ndithudi, satana akufuna kudzetsa chidani ndi kusakondana pakati panu kudzera m’mowa ndi njuga, ndikuti akutsekerezeni kukumbukira Allah ndi kupemphera Swala. Kodi inu simusiya

Verse 92 — Surah Al-Maidah 5:92

“Mverani Allah, ndipo mverani Mtumiki ndipo chenjerani (musanyoze malamulo a Allah). Ngati munyoza, dziwani kuti udindo wa Mtumiki Wathu ndikufikitsa uthenga woonekera basi

Verse 93 — Surah Al-Maidah 5:93

“Palibe tchimo kwa amene akhulupirira ndi kuchita zabwino pazomwe adadya (zisadaletsedwe) ngati akupitiriza kuopa ndikukhulupirira ndikuchita zabwino; kenako nkuopanso (ataletsedwa zina) ndikukhulupirira; (atalamulidwa zinanso) nkuopanso ndikuchita zabwino. Ndipo Allah, amakonda ochita zabwino

Verse 94 — Surah Al-Maidah 5:94

“E inu amene mwakhulupirira! Ndithu Allah akuyesani ndi nyama zina zozichita ulenje, zomwe manja anu ndi mikondo yanu ingazifikire, kuti Allah amuwonetsere poyera amene akumuopa mwanseri. Ndipo amene alumphe malire (posaka nyamayo ndi kupha) pambuyo pa zomwe mwauzidwazo, adzapeza chilango chopweteka

Verse 95 — Surah Al-Maidah 5:95

“E inu amene mwakhulupirira! Musaphe nyama ya mtchire pomwe inu muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Ndipo mwa inu amene angaphe mwadala nyama ya mtchireyo, dipo (lake likhale kuzinga) yofanana ndi yomwe waphayo, mu mtundu wa nyama zowetedwa, (monga mmene) angaweruzire olungama awiri a mwa inu, kukhala nsembe yoperekedwa ku Ka’aba (kuti ikazingidwe kumeneko ndi kuwagawira osauka); kapena alipe dipo la chakudya kudyetsa masikini; kapena m’malo mwake asale kuti alawe kupweteka kwa chinthu chakecho. Ndipo Allah afafaniza zomwe zidapita kale. Koma amene achitenso, Allah amukhaulitsa ndi chilango chochokera kwa Iye. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wokhaulitsa koopsa

Verse 96 — Surah Al-Maidah 5:96

“Nkololezedwa kwa inu kusaka nyama za m’nyanja ndi chakudya chake (chomwe chapezeka m’nyanjamo chitafa chokha). Chimenecho ndi kamba wanu (inu amene simuli pa ulendo) ndiponso a pa ulendo. Kwaletsedwa kwa inu kusaka za pamtunda pomwe muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Opani Allah Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa

Verse 97 — Surah Al-Maidah 5:97

“Allah wapanga Ka’aba kukhala nyumba yopatulika, ndikukhala pamalo popezera zosowa za anthu. Ndipo adapanganso miyezi (inayi) yopatulika, ndi kupereka nyama zansembe ku Makka zovekedwa makoza monga zisonyezo (kusonyeza kuti zikupita ku Makka). Zonsezi nkuti mudziwe kuti Allah akudziwa za kumwamba ndi pansi, ndikuti Allah Ngodziwa chilichonse

Verse 98 — Surah Al-Maidah 5:98

“Dziwani kuti ndithudi, Allah Ngolanga mwaukali. Ndikutinso Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

Verse 99 — Surah Al-Maidah 5:99

“Pa mtumiki palibe china koma kufikitsa chabe (uthenga). Ndipo Allah akudziwa zimene mukuzionetsera poyera ndi zimene mukuzibisa

Verse 100 — Surah Al-Maidah 5:100

“Nena (kwa aliyense kuti): “Zoipa ndi zabwino sizingafanane ngakhale kutakusangalatsa kuchuluka kwa zoipazo; choncho opani Allah, E! Inu eni nzeru kuti mupambane.”

Verse 101 — Surah Al-Maidah 5:101

“E inu amene mwakhulupirira! Musamafunse za zinthu zomwe zitasonyezedwa kwa inu zikuipirani. Ndipo ngati muzifunsa pomwe Qur’an ikuvumbulutsidwa, zionetsedwa kwa inu. Allah wakhululuka zimenezo. Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza

Verse 102 — Surah Al-Maidah 5:102

“Anthu amene adalipo kale inu musanadze, adazifunsapo zotere. Ndipo pachifukwa chimenecho adasanduka osakhulupirira

Verse 103 — Surah Al-Maidah 5:103

“Allah sadaike (kuletsedwa kwamtundu uliwonse) pa nyama yotchedwa Bahira*, ngakhale Saiba**, ngakhale Wasila***, ngakhalenso Hami****. Koma amene sadakhulupirire akumpekera Allah bodza. Ndipo ambiri a iwo sagwiritsa ntchito nzeru zawo

Verse 104 — Surah Al-Maidah 5:104

“Ndipo akauzidwa: “Tadzani kuchilamulo cha zomwe Allah wavumbulutsa ndi (zomwe akunena) Mtumiki.” Akunena: “Tikukwaniritsidwa ndi zomwe tidawapeza nazo makolo athu.” Kodi ngakhale kuti makolo awowo sadali kudziwa chinthu chilichonse ndipo sadali oongoka, (awatsatirabe)

Verse 105 — Surah Al-Maidah 5:105

“E inu amene mwakhulupirira! Dziganizireni nokha. Ndipo amene asokera sangakupatseni mavuto ngati inu mutalungama. Nonsenu kobwerera kwanu nkwa Allah basi. Choncho adzakuuzani zimene mudali kuchita

Verse 106 — Surah Al-Maidah 5:106

“E inu amene mwakhulupirira! Pamene chamfikira mmodzi wa inu chisonyezo cha imfa, ndipo akufuna kusiya chilawo (wasiya) funani mboni ponena mawuwo. Aikire umboni awiri olungama mwa inu (Asilamu) kapena apadera ngati muli pa ulendo, ndipo zisonyezo za imfa zitaonekera. Ngati mutazikaikira zitsekerezeni (kuti zisachoke) mboni ziwiri pambuyo pa Swala (yomwe amasonkhana anthu ambiri), ndipo zilumbilire m’dzina la Allah kunena (kuti): “Sitikusinthanitsa malumbirowa ndi china chake ngakhale chitakhala chothandiza kwa ife kapena mmodzi mwa abale athu. Sitikubisa umboni umene Allah watilamula kuti tiupereke moona. Ife ngati titabisa umboni (kapena kuyankhula chonama), ndithudi tikhala mwa anthu ochimwa.”

Verse 107 — Surah Al-Maidah 5:107

“Koma ngati kutaoneka kuti mboni ziwiri zija zanama pa umboni wawo, kapena zabisa chinthu, apo awiri achibale a wakufayo aimiire m’malo mwa mboni ziwirizo, (pambuyo pa Swala kuti aulule za bodza lawo). Choncho alumbilire m’dzina la Allah kuti: “Ndithu kulumbira kwathu nkoyenera kuvomerezedwa kuposa kulumbira kwawo; ndipo sitinapyole malire (mukulumbira kwathu). Ndipo sitikuzipekera mbonizo bodza. Ndithudi, ngati ife titachita zotere, ndiye kuti tikhala mwa ochita zoipa, (oyenera kulandira chilango cha Allah).”

Verse 108 — Surah Al-Maidah 5:108

“Chilamulochi ndi njira yapafupi kuti mboni zikwaniritse umboni wawo mnjira yoyenera, (ndikuti zisamalire kulumbira Allah kwawo); kapena kuopa kuyaluka bodza lawo likaonekera poyera, pambuyo polumbira enawo (izi zili polumbira amlowa mmalo pokana umboni wawo). Ndipo opani Allah (mkulumbira kwanu ndi kukhulupirika kwanu), ndipo mverani malamulo Ake. Allah satsogolera anthu opandukira chilamulo Chake

Verse 109 — Surah Al-Maidah 5:109

“(Kumbukirani) tsiku lomwe Allah adzasonkhanitsa, atumiki ndikuwafunsa kuti: “Kodi mudayankhidwa chiyani?” Iwo adzati: “Ife sitidziwa. Ndithudi, Inuyo ndiye Wodziwa zamseri.”

Verse 110 — Surah Al-Maidah 5:110

“Kumbukiraninso pamene Allah adzati: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya! Kumbuka chisomo Changa pa iwe ndi pa mayi wako, pamene ndinakuthandiza ndi mzimu woyera (Gabriel), (kotero kuti) udalankhula kwa anthu (mawu omveka) pamene udali mchikuta ndiponso pamene udali wamkulu. Ndipo (kumbuka) pamene ndidakuphunzitsa kulemba, nzeru; (ndinakuzindikiritsanso buku la) Taurat ndi Injili. (Kumbukanso) pamene udaumba dongo chithunzi chambalame mwa lamulo Langa. Utatero udauziramo ndipo zidasanduka mbalame mwa lamulo Langa. Ndipamene udali kuchiza akhungu ndi achinawa, mwa lamulo Langa. Ndipamene unkawatulutsa (m’manda) ena mwa akufa mwa lamulo Langa. Ndipamene ndinawatsekereza ana a Israyeli kwa iwe (kuti asakuzunze) pamene udawadzera ndi zisonyezo zooneka, ndipo aja mwa iwo omwe sadakhulupirire, adati: “Ichi sichina, koma ndi matsenga owonekera.”

Verse 111 — Surah Al-Maidah 5:111

“Ndipo (kumbukira) pamene ndidawaululira ophunzira ako kuti: “Ndikhulupirireni Ine ndi Mtumiki Wanga (uyu Isa {Yesu}).” Iwo adati: “Takhulupirira; ndipo khalani mboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera mwa Inu).”

Verse 112 — Surah Al-Maidah 5:112

“(Kumbukira) pamene ophunzira ako adati: “E iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi Mbuye wako angathe kutitsitsira chakudya kuchokera kumwamba?” (Isa {Yesu}) adati: “Opani Allah, ngati inu mulidi okhulupirira. (Musamangopempha zozizwitsa).”

Verse 113 — Surah Al-Maidah 5:113

“(Iwo) adati: “Tikufuna kudya chimenecho, ndikuti mitima yathu ikhazikike, ndikutinso tidziwe kuti watiuza choona; tero kuti tikhale oikira umboni pa chimenecho.”

Verse 114 — Surah Al-Maidah 5:114

“Isa (Yesu) mwana wa Mariya adati: “Inu Allah Mbuye wathu! Titsitsireni chakudya kuchokera kumwamba kuti chikhale chikondwelero cha oyambilira ndi omalizira mwa ife, komanso chikhale chisonyezo chochokera kwa Inu; choncho tipatseni ndithu inu ndinu Abwino popatsa kuposa opatsa.”

Verse 115 — Surah Al-Maidah 5:115

“Allah adati: “Ndithu Ine ndikuchitsitsa kwa inu. Koma amene adzatsutse mwa inu pambuyo pa ichi, ndithu Ine ndidzamulanga ndi chilango chomwe sindidamulangepo nacho aliyense mwa zolengedwa.”

Verse 116 — Surah Al-Maidah 5:116

“Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adzanena: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi iwe udauza anthu kuti: ‘Ndiyeseni ine ndi mayi wanga monga milungu iwiri m’malo mwa Allah?” (Mneneri Isa {Yesu}) adzaati: “Ulemelero ukhale pa Inu. Sikoyenera kwa ine kunena zomwe sizili zoyenera (kwa ine mawu amenewa ngabodza). Ngati ndikadanena, ndiye kuti mukadadziwa. Inu mukudziwa zomwe zili mu mtima mwanga, pomwe ine sindidziwa zomwe zili mwa Inu. Ndithudi, Inu ndinu Wodziwa zamseri.”

Verse 117 — Surah Al-Maidah 5:117

““Sindinawauze chilichonse kupatula chimene mudandilamula kuti: ‘Pembedzani Allah, Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.’ Ndipo ndinali mboni kwa iwo pamene ndidali nawo. Koma pamene mudanditenga, Inu ndiye mudali Muyang’aniri pa iwo; ndipo Inu ndinu Mboni ya chilichonse.”

Verse 118 — Surah Al-Maidah 5:118

““Ngati muwalanga, ndithudi iwo ndi akapolo anu. Ndipo mukawakhululukira, ndithudi, Inu ndinu Mwini mphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.”

Verse 119 — Surah Al-Maidah 5:119

“Allah adzati: “Ili ndi tsiku lomwe olankhula zoona kudzawathandiza kuona kwawo. Iwo adzalandira Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. M’menemo adzakhala muyaya. Allah adzawayanja; naonso adzamuyanja. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

Verse 120 — Surah Al-Maidah 5:120

“Allah Yekha ndiye Mwini ufumu wa kumwamba ndi pansi, ndi zam’menemo. Ndipo Iye Ngokhoza chilichonse