Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 50 - Qaf
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Qaf 50:1
“Qaf. Ndikulumbira Qur’an yolemekezeka
Verse 2 — Surah Qaf 50:2
“Koma akudabwa chifukwa chowadzera Mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adanena: “Ichi nchinthu chodabwitsa.”
Verse 3 — Surah Qaf 50:3
“Kodi tikadzafa ndi kukhala fumbi (tidzaukanso?) Kubwerera kumeneko nkwakutali kwambiri, (nkosatheka).”
Verse 4 — Surah Qaf 50:4
“Ndithu tikudziwa chimene nthaka ikuchepetsa m’matupi mwawo (akalowa m’manda). Ndipo kwa Ife kuli kaundula wosungidwa
Verse 5 — Surah Qaf 50:5
“Koma adatsutsa choona pamene chidawadzera. Ndipo iwo ali m’chinthu chosokonezeka
Verse 6 — Surah Qaf 50:6
“Kodi sawona thambo pamwamba pawo m’mene tidalimangira ndi kulikongoletsa? Ndipo lilibe ming’alu
Verse 7 — Surah Qaf 50:7
“Ndipo nthaka tidaiyala; ndi kuika mapiri m’menemo ndi kumeretsamo m’mera Wokongola wamtundu uliwonse
Verse 8 — Surah Qaf 50:8
“(Kuti zimenezi zikhale) chotsekula maso ndi chikumbutso kwa munthu aliyense wotembenukira (kwa Allah)
Verse 9 — Surah Qaf 50:9
“Ndipo tatsitsa madzi odalitsidwa kuchokera ku mitambo, ndipo kupyolera m’madziwo, tameretsa (mmera) m’minda ndi mbewu zokololedwa
Verse 10 — Surah Qaf 50:10
“Ndi mitengo italiitali ya kanjedza yokhala ndi mikoko yazipatso zothothana
Verse 11 — Surah Qaf 50:11
“(Kuti chikhale) chakudya cha akapolo (a Allah); ndi madziwo taukitsa dziko lakufa (louma). Momwemo ndimmene kudzakhalira kutuluka m’manda (muli moyo)
Verse 12 — Surah Qaf 50:12
“Kale, iwo kulibe, adatsutsa anthu a Nuh ndi eni chitsime ndi Asamudu
Verse 13 — Surah Qaf 50:13
“Ndi Âdi, ndi Farawo ndi Abale a Luti
Verse 14 — Surah Qaf 50:14
“Ndi anthu a m’mitengo (ya Aika), ndi anthu a Tubba; onsewo adatsutsa Aneneri; choncho chenjezo Langa lidatsimikizika (pa iwo)
Verse 15 — Surah Qaf 50:15
“Kodi tidatopa nkulenga koyamba? Koma iwo ali m’maganizo osokonezeka m’zakalengedwe katsopano
Verse 16 — Surah Qaf 50:16
“Ndithu tidamulenga munthu, ndipo Ife tikudziwa zimene mtima wake ukumunong’oneza; ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wam’khosi mwake (wolumikizana ndi mtima)
Verse 17 — Surah Qaf 50:17
“Ndipo pamene amalandira olandira awiri (angelo), wina amakhala kudzanja lamanja, wina kudzanja lamanzere
Verse 18 — Surah Qaf 50:18
“Palibe chilichonse chimene amayankhula koma pafupi ndi iye pali mlonda amene wakonzekera (kulemba)
Verse 19 — Surah Qaf 50:19
“Ndipo kuledzera kwa imfa kukam’dzera mwa choona, (pamenepo adzauzidwa): “Ichi ndi chomwe mumachithawa chija.”
Verse 20 — Surah Qaf 50:20
“Ndipo lipenga lidzaimbidwa; limenelo ndilo tsiku lamavuto (tsiku lachiweruziro)
Verse 21 — Surah Qaf 50:21
“Ndipo udzadza mzimu uliwonse pamodzi ndi m’busa (wake) ndi mboni (yake)
Verse 22 — Surah Qaf 50:22
“(Adzauzidwa): “Ndithu udali wosalabadira zinthu izi; basi takuvundukulira (chomwe) chimakuphimba, ndipo kuyang’ana kwako lero nkwakuthwa!”
Verse 23 — Surah Qaf 50:23
“Ndipo (Mngelo) yemwe adali naye (pamodzi ndikumalemba zochita zake) adzanena (kwa Mngelo wachilango): “Izi ndizimene zidakonzedwa ndi ine.”
Verse 24 — Surah Qaf 50:24
“Mponyeni ku Moto aliyense wokanira, wamakani,”
Verse 25 — Surah Qaf 50:25
““Wotsekereza zabwino, wolumpha malire, wokaika.”
Verse 26 — Surah Qaf 50:26
““Amene adampangira Allah mulungu wina. Chomwecho mponyeni ku chilango chaukali.”
Verse 27 — Surah Qaf 50:27
“Mnzake (satana) adzanena: “E Mbuye wathu! Sindidamsokeretse, koma iye mwini adali wosokera kutali kwambiri ndi choonadi”
Verse 28 — Surah Qaf 50:28
“(Allah) adzanena: “Musakangane kwa Ine; ndidakutsogozerani kale chenjezo (Langa).”
Verse 29 — Surah Qaf 50:29
“Liwu Langa silisinthidwa kwa Ine, ndipo Ine siwopondereza akapolo (Anga)
Verse 30 — Surah Qaf 50:30
“Tsiku limene tidzaifunsa Jahannam: “Kodi wadzaza?” Iyo idzanena: “Kodi kuli zoonjezera?”
Verse 31 — Surah Qaf 50:31
“Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa pafupi kwa oopa (Allah)
Verse 32 — Surah Qaf 50:32
““Izi ndizimene mumalonjezedwa, za aliyense wotembenukira kwa Allah, Wosunga (malamulo Ake)
Verse 33 — Surah Qaf 50:33
“Amene adaopa (Allah), Wachifundo chambiri, pomwe samamuona ndi maso, ndipo adadza ndi mtima wotembenukira (kwa Iye).”
Verse 34 — Surah Qaf 50:34
“(Adzauzidwa): “Uloweni mwamtendere.” Limeneli ndi tsiku lokhazikika mpaka muyaya
Verse 35 — Surah Qaf 50:35
“M’menemo adzapeza chilichonse (chimene) adzafune, ndipo kwa Ife kuli zoonjezera
Verse 36 — Surah Qaf 50:36
“Ndipo kodi ndi mibadwo ingati tidainonga kale iwo kulibe, yamphamvu kuposa iwo? Adayendayenda padziko. Kodi padalipo pothawira
Verse 37 — Surah Qaf 50:37
“Ndithu m’zimenezi muli chikumbutso kwa yemwe ali ndi mtima ndi yemwe akutchelera khutu (uku) iye ali pompo (ndi maganizo ake)
Verse 38 — Surah Qaf 50:38
“Ndithu tidalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo sikudatikhuze kutopa kulikonse
Verse 39 — Surah Qaf 50:39
“Choncho, pirira nazo zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako pomutamanda dzuwa lisadatuluke, (Swala ya Subh), ndi (dzuwa) lisadalowe, (Swala ya Asr)
Verse 40 — Surah Qaf 50:40
“Ndi gawo lausiku, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso (mulemekeze) pambuyo pa mapemphero (popemphera Swala za Sunna)
Verse 41 — Surah Qaf 50:41
“Ndipo mvetsera (za) tsiku limene woitana adzaitana kuchokera pamalo apafupi
Verse 42 — Surah Qaf 50:42
“Tsiku limene adzamva phokoso mwa choonadi: limenelo ndilo tsiku lodzatuluka (m’manda)
Verse 43 — Surah Qaf 50:43
“Ndithu Ife ndi amene timapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo kobwerera Nkwathu
Verse 44 — Surah Qaf 50:44
“(Akumbutse za) tsiku limene nthaka idzang’ambike kwa iwo mwachangu; kusonkhanitsa kumeneko nkosavuta kwa Ife
Verse 45 — Surah Qaf 50:45
“Ife tikudziwa bwino zimene akunena; iwe siuli wowakakamiza. Choncho mukumbutse ndi Qur’an yemwe akuopa chilango Changa