Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 51 - Adh-Dhariyat
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Adh-Dhariyat 51:1
“. Ndikulumbilira mphepo imene ikubalalitsa mitambo ya mvula
Verse 2 — Surah Adh-Dhariyat 51:2
“Ndi imene imasenza mitolo yolemera (ya madzi)
Verse 3 — Surah Adh-Dhariyat 51:3
“Ndi kuyenda (nawo madziwo) mwaubwino
Verse 4 — Surah Adh-Dhariyat 51:4
“Ndi awo amene amagawa rizq (limene Allah amalipereka kwa amene wamfuna)
Verse 5 — Surah Adh-Dhariyat 51:5
“Ndithu zimene mukulonjezedwa nzoonadi, (zidzachitika)
Verse 6 — Surah Adh-Dhariyat 51:6
“Ndipo, ndithu malipiro (pa zochita zanu) adzapezekadi
Verse 7 — Surah Adh-Dhariyat 51:7
“Ndikulumbilira thambo lomwe njira zake zambiri nzoikidwa mwaluso
Verse 8 — Surah Adh-Dhariyat 51:8
“Ndithu inu muli m’mau otsutsana, (pa zimene mukunena)
Verse 9 — Surah Adh-Dhariyat 51:9
“(Kupyolera m’mawu amenewa) akuchotsedwa ku icho (chikhulupiliro chalonjezo loona) amene adachotsedwa (ku chikhulupilirocho)
Verse 10 — Surah Adh-Dhariyat 51:10
“Aonongeka abodza (amene akunena za tsiku lachiweruziro mongoganizira)
Verse 11 — Surah Adh-Dhariyat 51:11
“Iwo amene akubira mu umbuli, osalabadira (za tsiku lachimaliziro)
Verse 12 — Surah Adh-Dhariyat 51:12
“Akufunsa (mwachipongwe ponena kuti) “Lidzakhala liti tsiku lamalipiro?”
Verse 13 — Surah Adh-Dhariyat 51:13
“(Limenelo ndi) tsiku lomwe iwo adzalangidwa ku Moto
Verse 14 — Surah Adh-Dhariyat 51:14
“(Adzawauza kuti): “Lawani chilango chanu ichi chimene munkachifulumizitsa (kuti chikufikeni).”
Verse 15 — Surah Adh-Dhariyat 51:15
“Ndithu oopa (Allah) adzakhala (akusangalala) m’minda ndi mu akasupe okongola
Verse 16 — Surah Adh-Dhariyat 51:16
“Uku akulandira zimene wawapatsa Mbuye wawo (malipiro aulemu); ndithu iwo ankachita zabwino asanapeze izi
Verse 17 — Surah Adh-Dhariyat 51:17
“Nthawi yausiku amagona pang’ono. (Amadzuka nachita mapemphero mochulukitsa)
Verse 18 — Surah Adh-Dhariyat 51:18
“Ndipo kum’bandakucha, iwo amapempha chikhululuko
Verse 19 — Surah Adh-Dhariyat 51:19
“Ndipo m’chuma chawo mudali gawo (lodziwika) la opempha ndi osapempha (mwa osauka)
Verse 20 — Surah Adh-Dhariyat 51:20
“M’nthaka muli zizindikiro kwa otsimikiza, (zosonyeza kuti Allah alipo)
Verse 21 — Surah Adh-Dhariyat 51:21
“Ndi mwa inu nomwe; kodi simuona
Verse 22 — Surah Adh-Dhariyat 51:22
“Ndipo kumwamba kuli zokuthandizani (pa moyo wanu), ndi zimene mukulonjezedwa
Verse 23 — Surah Adh-Dhariyat 51:23
“Ndikulumbilira Mbuye wa kumwamba ndi pansi, ndithu zimenezo ndi zoona monga kulili kuyankhula kwanu
Verse 24 — Surah Adh-Dhariyat 51:24
“Kodi yakufika nkhani ya alendo a Ibrahim; (angelo) olemekezeka
Verse 25 — Surah Adh-Dhariyat 51:25
“Pamene adalowa kwa iye ndi kunena kuti: “Salaam,” (“Mtendere”)! Iye adayankha: “Salaam,” (“Mtendere) inu ndinu anthu osadziwika (achilendo).”
Verse 26 — Surah Adh-Dhariyat 51:26
“Adatembenukira kwa akunyumba ake (mwakachetechete), ndipo adadza ndi nyama ya mwana wa ng’ombe yonona (yowotcha)
Verse 27 — Surah Adh-Dhariyat 51:27
“Naipereka kwa iwo (koma sadadye); iye adanena (modabwa): “Kodi bwanji simukudya?”
Verse 28 — Surah Adh-Dhariyat 51:28
“Mumtima mwake adadzazidwa mantha ndi iwo. Iwo adati: “Usaope,” ndipo adamuuza nkhani yabwino ya kubala mwana wodziwa
Verse 29 — Surah Adh-Dhariyat 51:29
“Adadza mkazi wake ndi mkuwe (pamene adamva nkhani yabwino ija). Adadzimenya kunkhope (ndi dzanja lake kusonyeza kudabwa ndi kusatheka). Ndipo adati: (“Ine ndine) nkhalamba (ndiponso) chumba; (ndingabereke bwanji)?”
Verse 30 — Surah Adh-Dhariyat 51:30
“Iwo adati: “Momwemo, Mbuye wako wanena. Iye Ngwanzeru zakuya (pa chilichonse chimene akulamula); Ngodziwa; (palibe chimene chingabisike kwa Iye)
Verse 31 — Surah Adh-Dhariyat 51:31
“۞ (Ibrahim) adati: “Kodi nkhani yanu ndiyotani E inu otumidwa?”
Verse 32 — Surah Adh-Dhariyat 51:32
“Iwo adati: “Tatumizidwa kwa anthu oipa.”
Verse 33 — Surah Adh-Dhariyat 51:33
““Kuti tiwagende ndi miyala yotenthedwa kuchokera kudongo.”
Verse 34 — Surah Adh-Dhariyat 51:34
““Yoikidwa chizindikiro cha aliyense wochimwa kuchokera kwa Mbuye wako.”
Verse 35 — Surah Adh-Dhariyat 51:35
“Tidawatulutsa okhulupirira omwe adali m’mudzimo
Verse 36 — Surah Adh-Dhariyat 51:36
“Sitidapeze mmenemo (okhulupirira ambiri) kupatula mnyumba imodzi ya Asilamu
Verse 37 — Surah Adh-Dhariyat 51:37
“Ndipo tidasiya pamenepo chizindikiro (chosonyeza kuonongeka kwa eni mudziwo kuti chikhale lingaliro) kwa amene akuopa chilango chopweteka
Verse 38 — Surah Adh-Dhariyat 51:38
“M’nkhani ya Mûsa (muli phunziro) pamene tidamtuma kwa Farawo uku atalimbikitsidwa ndi chisonyezo choonekera
Verse 39 — Surah Adh-Dhariyat 51:39
“Koma Farawo adanyoza (kukhulupirira Mûsa) chifukwa chotama nyonga zake, ndipo adati: “Uyu ndi wamatsenga kapena wamisala.”
Verse 40 — Surah Adh-Dhariyat 51:40
“Tidamlanga pamodzi ndi khamu lake la nkhondo ndi kuwaponya mnyanja; iye ali wodzudzulidwa
Verse 41 — Surah Adh-Dhariyat 51:41
“Ndipo m’nkhani ya Âdi (muli phunziro) pamene tidawatumizira chimphepo (chamkuntho) chopanda chabwino mkati mwake
Verse 42 — Surah Adh-Dhariyat 51:42
“Chomwe sichisiya chinthu chimene chachidutsa koma kuchichita monga chofumbwa
Verse 43 — Surah Adh-Dhariyat 51:43
“Ndipo m’nkhani ya Samudu (muli chisonyezo) pamene kudanenedwa kwa iwo kuti: “Sangalalani (mnyumba zanu) mpaka nthawi yaikika.”
Verse 44 — Surah Adh-Dhariyat 51:44
“Koma adadzikweza (ponyozera) lamulo la Mbuye wawo. Choncho chiphokoso chidawaononga uku akupenya
Verse 45 — Surah Adh-Dhariyat 51:45
“Sadathe kuimilira ndi (kuthawa) ndiponso sadali wodzipulumutsa
Verse 46 — Surah Adh-Dhariyat 51:46
“Naonso anthu a Nuh (tidawaononga) kale chifukwa iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah)
Verse 47 — Surah Adh-Dhariyat 51:47
“Thambo tidalimanga mwamphamvu (ndi luntha); ndipo tingathe kuchita zochuluka (kuposa zimenezi)
Verse 48 — Surah Adh-Dhariyat 51:48
“Ndipo nthaka tidaiyala; taonani kukonza bwino Ife amene tidakonza nthaka
Verse 49 — Surah Adh-Dhariyat 51:49
“Ndipo m’chinthu chilichonse talenga ziwiriziwiri kuti inu mulingalire (ndi kukhulupirira mphamvu Zathu)
Verse 50 — Surah Adh-Dhariyat 51:50
“Thawirani kwa Allah. Ine ndine mchenjezi woonekera kwa inu wochokera kwa Iye
Verse 51 — Surah Adh-Dhariyat 51:51
“Ndipo musadzipangire mulungu wina wompembedza ndi kumuphatikiza ndi Allah. Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera poyera kwa inu wochokera kwa Iye
Verse 52 — Surah Adh-Dhariyat 51:52
“Momwemo (ndimo idalili mibadwo yakale pamodzi ndi aneneri awo); palibe Mthenga amene adawadzera anthu akale, anthu akowa kulibe, popanda kumnena kuti: “Ndiwamatsenga kapena wamisala.”
Verse 53 — Surah Adh-Dhariyat 51:53
“Kodi adalangizana za mawuwa pakati pawo? Iyayi, koma iwo ndianthu opyola malire
Verse 54 — Surah Adh-Dhariyat 51:54
“Choncho apatukire iwo (amakani), iwe suli wodzudzulidwa (pakuleka kwawo kuyankha kuitana)
Verse 55 — Surah Adh-Dhariyat 51:55
“Kumbutsa. Ndithu kukumbutsa kumawathandiza okhulupirira
Verse 56 — Surah Adh-Dhariyat 51:56
“Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza
Verse 57 — Surah Adh-Dhariyat 51:57
“Sindifuna kwa iwo chithandizo ndiponso sindifuna kuti azindidyetsa
Verse 58 — Surah Adh-Dhariyat 51:58
“Ndithu Allah ndi Amene amapereka rizq; Iye ndi Mwini mphamvu zoposa; Wolimba, (salaphera kanthu)
Verse 59 — Surah Adh-Dhariyat 51:59
“Ndithu amene adzichitira okha chinyengo (pokana ndi kutsutsa) ali nalo gawo la chilango monga gawo la anzawo (a mibadwo yakale); choncho asandifulumizitse (kutsitsa chilango nthawi yake isanafike)
Verse 60 — Surah Adh-Dhariyat 51:60
“Kuonongeka kuli pa amene atsutsa za tsiku lawo limene alonjezedwa