Back to Languages

Chichewa - Chapter 53 - An-Najm

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah An-Najm 53:1

“Ndikulumbira nyenyezi pamene zikulowa

Verse 2 — Surah An-Najm 53:2

“Sadasokere m’bale wanu (Mtumiki panjira ya choonadi) ndipo sadakhulupirire zonama

Verse 3 — Surah An-Najm 53:3

“Ndipo sayankhula zofuna za mtima wake

Verse 4 — Surah An-Najm 53:4

“Iyoyi (Qur’an imene akuinena), sichina, koma ndichivumbulutso chovumbulutsidwa

Verse 5 — Surah An-Najm 53:5

“Adamphunzitsa (chivumbulutsochi) (Jibril) wanyonga zambiri

Verse 6 — Surah An-Najm 53:6

“Wanzeru zakuya; ndipo adakhazikika (m’maonekedwe ake)

Verse 7 — Surah An-Najm 53:7

“Ali m’chizimezime kumwamba

Verse 8 — Surah An-Najm 53:8

“Kenako (Jibril) adamuyandikira (Mtumiki {s.a.w}) ndikuonjezera kumuyandikira

Verse 9 — Surah An-Najm 53:9

“(Kumuyandikira kwake) kudali ngati (mpata wa) nsonga ziwiri za uta, kapena kuyandikira kuposa apo

Verse 10 — Surah An-Najm 53:10

“(Choncho Jibril) adavumbulutsira kapolo wake (wa Allah) zimene adazivumbulutsa

Verse 11 — Surah An-Najm 53:11

“Sudaname mtima (wa Mtumiki) pazimene adaziona

Verse 12 — Surah An-Najm 53:12

“Kodi mukutsutsana naye (Mthenga wa Allah) pazimene adaziona

Verse 13 — Surah An-Najm 53:13

“Ndipo ndithu adamuona (Jibril) m’kuona kachiwiri mkaonekedwe kake

Verse 14 — Surah An-Najm 53:14

“Pa ‘Sidratil Muntaha’ (mtengo wamasawu pothera zinthu zonse)

Verse 15 — Surah An-Najm 53:15

“Pafupi pake pali Janatu Ma’awa, (munda wokhalamo)

Verse 16 — Surah An-Najm 53:16

“Pomwe chophimba chidaphimba msawuwo

Verse 17 — Surah An-Najm 53:17

“Maso ake sadaphonye kapena kupyola malire (oikidwa)

Verse 18 — Surah An-Najm 53:18

“Ndithu (Mneneri Muhammad {s.a.w}) adaona zina mwa zizindikiro zikuluzikulu za Mbuye wake (zosonyeza mphamvu Zake)

Verse 19 — Surah An-Najm 53:19

“Kodi mwamuona Laat ndi Uzza

Verse 20 — Surah An-Najm 53:20

“Ndi Manata; (fano lanu) lina lachitatu, (kuti iwowa ndi milungu)

Verse 21 — Surah An-Najm 53:21

“Kodi mwadzisankhira ana aamuna (kukhala anu), ndi aakazi nkukhala a Iye (Allah)

Verse 22 — Surah An-Najm 53:22

“Choncho kugawa kumeneko nkopanda chilungamo (pompatsa Allah zimene mumazida)

Verse 23 — Surah An-Najm 53:23

“Sali (mafanowo) chilichonse koma ndi maina basi omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, (molingana ndi zilakolako zanu zachabe); Allah sadatsitse umboni pazimenezo (wotsimikiza pamawu anuwo). Sakutsatira koma zoganizira basi ndi zimene ikufuna mitima (yawo yopotoka). Ndithu chidawadzera chiongoko kuchokera kwa Mbuye wawo (chomwe m’kati mwake mudali kuongoka kwawo akadachitsatira)

Verse 24 — Surah An-Najm 53:24

“Kodi munthu akuganiza kuti adzapeza chilichonse chimene akuchilakalaka

Verse 25 — Surah An-Najm 53:25

“Moyo wa tsiku lachimaliziro ndi wadziko lapansi ngwa Allah Yekha

Verse 26 — Surah An-Najm 53:26

“Ndipo kuli angelo ambiri kumwamba omwe kuchondelera kwawo sikungathandize china chilichonse pokhapokha Allah ataloleza kwa amene wamfuna ndi kumuyanja

Verse 27 — Surah An-Najm 53:27

“Ndithu amene sakhulupirira za (Moyo wa) tsiku lachimaliziro, amawatcha angelo kuti ndiakazi

Verse 28 — Surah An-Najm 53:28

“Ndipo alibe kudziwa kulikonse pa zimenezo sakutsata china koma maganizo. Ndipo ndithu kuganizira sikuthandiza chilichonse pofuna kupeza choonadi

Verse 29 — Surah An-Najm 53:29

“Choncho apewe (osakhulupirirawa) amene anyozera chikumbutso Chathu (Qur’an); ndipo palibe chimene akufuna koma moyo wa padziko lapansi basi

Verse 30 — Surah An-Najm 53:30

“Zimenezo ndiwo mapeto a kudziwa kwawo. Ndithu Mbuye wako Ngodziwa kwambiri za amene akusokera njira Yake ndiponso akudziwa bwino za yemwe wawongoka

Verse 31 — Surah An-Najm 53:31

“Ndipo zonse za kumwamba ndi zadziko lapansi nza Allah Yekha, (pozilenga ndi kuziyang’anira), kuti adzawalipire amene adaipitsa pa zimene adachita ndi kutinso adzawalipire zabwino amene adachita zabwino

Verse 32 — Surah An-Najm 53:32

“Amene akuwapewa machimo akuluakulu ndi zadama, kupatula timachimo tating’onoting’ono (timene Allah amatikhululuka); ndithu Mbuye wako ndiwokhululuka kwakukulu. Iye akudziwa chikhalidwe chanu kuyambira pomwe adakulengani kuchokera m’nthaka ndi pamene inu mudali makanda m’mimba mwa amayi anu (mosinthasintha; mosiyanasiyana). Choncho musadzitame nokha kuyera mtima; Iye Ngodziwa kwambiri za yemwe akumuopa (Allah)

Verse 33 — Surah An-Najm 53:33

“Kodi wamuona yemwe wadzipatula (pakusiya kutsatira choonadi)

Verse 34 — Surah An-Najm 53:34

“Ndipo wapereka (chuma) chochepa nasiyanso kuperekako

Verse 35 — Surah An-Najm 53:35

“Kodi akudziwa zamseri, kotero kuti akuziwona (zomwe wadza nazo (Mtumiki {s.a.w) kuti sizoona

Verse 36 — Surah An-Najm 53:36

“Kapena sadauzidwe zomwe zidali m’mabuku a Mûsa

Verse 37 — Surah An-Najm 53:37

“Ndi Ibrahim amene adakwaniritsa (lonjezo la Allah)

Verse 38 — Surah An-Najm 53:38

“Kuti mzimu wamachimo sungasenze machimo a mzimu wina

Verse 39 — Surah An-Najm 53:39

“Ndi kutinso munthu sakalipidwa koma zimene adachita

Verse 40 — Surah An-Najm 53:40

“Ndipo ndithu ntchito zake zidzaonekera

Verse 41 — Surah An-Najm 53:41

“Kenako (munthu) adzalipidwa malipiro okwanira (pa ntchito zake zimene amachita)

Verse 42 — Surah An-Najm 53:42

“Ndipo ndithu kwa Mbuye wako yekha ndiwo malekezero (a chilichonse)

Verse 43 — Surah An-Najm 53:43

“Ndithu Iye ndiAmene amapereka chisangalalo ndi zoliritsa

Verse 44 — Surah An-Najm 53:44

“Ndipo Iye yekha ndi Amene amapereka imfa ndi moyo

Verse 45 — Surah An-Najm 53:45

“Ndipo Iye ndiAmene adalenga mitundu iwiri: chachimuna ndi chachikazi, (anthu ndi zamoyo zina)

Verse 46 — Surah An-Najm 53:46

“Kuchokera m’mbewu ya moyo pamene imafwamphukira (m’chiberekero)

Verse 47 — Surah An-Najm 53:47

“Ndipo ndithu ndi udindo Wake kuukitsa kwina (pambuyo pa imfa)

Verse 48 — Surah An-Najm 53:48

“Ndipo Iye ndiAmene amapatsa chokwanira ndipo ndi amene amapatsa chosunga

Verse 49 — Surah An-Najm 53:49

“Ndipo ndithu Iye ndi Mbuye wa nyenyezi yotchedwa Shiira

Verse 50 — Surah An-Najm 53:50

“Ndipo Iye ndi amene adaononga Âdi oyamba; (anthu a Mneneri Hûd)

Verse 51 — Surah An-Najm 53:51

“Ndi Samudu; (anthu a Mneneri Swaleh;) choncho sadasiye (ndi mmodzi yemwe wa iwo)

Verse 52 — Surah An-Najm 53:52

“Ndipo (adawaononganso) anthu a Nuh, kale (asadaononge Âdi ndi Samudu). Ndithu iwo adali osalungama ndi olumpha malire kwambiri (kuposa Âdi ndi Samudu)

Verse 53 — Surah An-Najm 53:53

“Ndi midzi yotembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, (ya anthu a Luti) adaigwetsa

Verse 54 — Surah An-Najm 53:54

“Tero chidaivindikira (midziyo) chomwe chidaivindikira (chilango)

Verse 55 — Surah An-Najm 53:55

“Kodi ndimtendere uti (mumtendere) wa Mbuye wako umene ukuukaikira

Verse 56 — Surah An-Najm 53:56

“Uyu (Mtumiki) ndimchenjezi mwa achenjezi oyamba (amene adachenjezedwa nawo anthu a mibadwo yakale)

Verse 57 — Surah An-Najm 53:57

“Chayandikira choyandikira (Qiyâma)

Verse 58 — Surah An-Najm 53:58

“Palibe amene angachionetse koma Allah Yekha

Verse 59 — Surah An-Najm 53:59

“Kodi mukuidabwa nkhaniyi (ya Qur’an moikana)

Verse 60 — Surah An-Najm 53:60

“Mungoseka (mwachipongwe) ndipo simukulira (pamene mukuimva monga momwe akuchitira okhulupirira)

Verse 61 — Surah An-Najm 53:61

“Ndipo mukunyozera

Verse 62 — Surah An-Najm 53:62

“Mlambireni ndi kumpembedza Allah (amene wavumbulutsa Qur’an kuti ikhale chiongoko cha anthu)