Back to Languages

Chichewa - Chapter 54 - Al-Qamar

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Qamar 54:1

“Nthawi ya chimaliziro (Qiyâma) yayandikira ndipo mwezi wagawikana

Verse 2 — Surah Al-Qamar 54:2

“Koma akaona chozizwitsa akunyoza ndi kunena kuti: “Awa ndi matsenga womkeramkera patsogolo.”

Verse 3 — Surah Al-Qamar 54:3

“Ndipo adatsutsa (choonadi) ndi kutsatira zilakolako (zawo zoipa) koma chinthu chilichonse (cha Allah) nchokhazikika

Verse 4 — Surah Al-Qamar 54:4

“Ndipo ndithu zidawafika nkhani zomwe zili zokwanira kuwaopseza

Verse 5 — Surah Al-Qamar 54:5

“Nzeru zokwana koma machenjezo (kwa iwo) sanawathandize

Verse 6 — Surah Al-Qamar 54:6

“Choncho, apewe (iwe Mtumiki) osakhulupirira, (yembekezani) tsiku loitana woitana (wa Allah) ku chinthu chovuta kwambiri, (chodedwa ndi mitima)

Verse 7 — Surah Al-Qamar 54:7

“Maso awo ali zyoli chifukwa chakuopsa; adzatuluka m’manda uku ali ngati dzombe lobalalika (chifukwa cha kuchuluka)

Verse 8 — Surah Al-Qamar 54:8

“Akuthamangira kwa woitana (uku atatukula mitu yawo, osatha kucheukira kwina). Adzanena osakhulupirira (tsiku lachiweruziro): “Ili nditsiku lovuta kwambiri.”

Verse 9 — Surah Al-Qamar 54:9

“Patsogolo pawo (Aquraishi) anthu a Nuh nawo adatsutsa, adamtsutsa kapolo Wathu nanena kuti: “Uyu ngwamisala!” Ndipo adaopsezedwa (ndi kuzunzidwa ndi mazunzo osiyanasiyana)

Verse 10 — Surah Al-Qamar 54:10

“(Nuh) adaitana Mbuye wake (nati): “Ine ndagonjetsedwa (ndi anthu anga); choncho ndipulumutseni (kwa iwo).”

Verse 11 — Surah Al-Qamar 54:11

“Tero tidatsekula makomo akumwamba ndi madzi otsika mopitiriza, mwamphamvu

Verse 12 — Surah Al-Qamar 54:12

“Ndipo tidaing’amba nthaka kukhala ndi akasupe (ofwamphuka madzi mwamphamvu). Choncho adakumana madzi (akumwamba ndi am’nthaka kuti awaononge) pamuyeso wopimidwa ndi kulamulidwa (ndi Allah)

Verse 13 — Surah Al-Qamar 54:13

“Ndipo tidamnyamula Nuh pa chombo chamatabwa chokhomedwa ndi misomali (yamitengo)

Verse 14 — Surah Al-Qamar 54:14

“Chinkayandama pamadzi ndi kuyang’aniridwa ndi Ife. Iyi ndi mphoto ya (Nuh) yemwe adakanidwa ndi anthu ake

Verse 15 — Surah Al-Qamar 54:15

“Ndipo ndithu tidachisiya (chigumula) kukhala phunziro (pakuonongeka kwa osakhulupirira ndi kupulumuka kwa okhulupirira). Kodi alipo wolikumbukira (ndi kupeza nalo malango abwino)

Verse 16 — Surah Al-Qamar 54:16

“Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)

Verse 17 — Surah Al-Qamar 54:17

“Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

Verse 18 — Surah Al-Qamar 54:18

“Âdi adamtsutsa (mneneri wawo Hud), kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)

Verse 19 — Surah Al-Qamar 54:19

“Ndithu Ife tidawatumizira mphepo yozizira, yaphokoso, m’tsiku latsoka lopitilira

Verse 20 — Surah Al-Qamar 54:20

“Idawazula anthu (kuchoka m’malo mwawo ndi kuwaponya panthaka ali akufa) ngati matsinde a mitengo yakanjedza ozulidwa m’malo mwake

Verse 21 — Surah Al-Qamar 54:21

“Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)

Verse 22 — Surah Al-Qamar 54:22

“Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

Verse 23 — Surah Al-Qamar 54:23

“Asamudu adatsutsa machenjezo

Verse 24 — Surah Al-Qamar 54:24

“Ndipo adati: “Kodi titsatire munthu mmodzi wochokera mwa ife? Ndithu ife ngati titamtsatira ndiye kuti tili nkusokera ndiponso misala.”

Verse 25 — Surah Al-Qamar 54:25

“Kodi am’vumbulutsira iye chikumbutso pakati pathu, (pomwe tili nawo oposa iye pa ulemelero)? Koma iye ndiwabodza ndi wodzitukumu.”

Verse 26 — Surah Al-Qamar 54:26

“Mawa lino adzadziwa (tsiku lakuwatsikira chilango,) kuti ndiyani wabodza wodzitukumula (iwo kapena Swaleh)

Verse 27 — Surah Al-Qamar 54:27

“(Tidamuuza mneneriyo kuti) ndithu Ife titumiza ngamira yaikazi kuti ikhale mayeso kwa iwo. Choncho adikire, ndipo pirira

Verse 28 — Surah Al-Qamar 54:28

“Ndipo auze kuti madzi agawidwa pakati pawo (ndi ngamira). Aliyense ali ndi tsiku lopita kukatunga

Verse 29 — Surah Al-Qamar 54:29

“Koma adaitana mnzawo (wa mphulupulu). Choncho adakonzeka kupha ngamirayo ndipo adaipha

Verse 30 — Surah Al-Qamar 54:30

“Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa anthu otsutsa)

Verse 31 — Surah Al-Qamar 54:31

“Ndithu tidawatumizira nkuwe umodzi choncho adakhala ngati udzu ndi mitengo youma yaomanga khola

Verse 32 — Surah Al-Qamar 54:32

“Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

Verse 33 — Surah Al-Qamar 54:33

“Anthu a Luti adatsutsa machenjezo (a mneneri wawo)

Verse 34 — Surah Al-Qamar 54:34

“Ndithu Ife tidawatumizira chimphepo champhamvu choulutsa miyala (ndi kuwagenda), kupatula akubanja la Luti; tidawapulumutsa (ku chilangocho) m’bandakucha

Verse 35 — Surah Al-Qamar 54:35

“(Choncho kupulumukako kudali) chisomo chochokera kwa Ife (pa iwo). Momwemo ndimo timamlipirira wothokoza

Verse 36 — Surah Al-Qamar 54:36

“Ndipo ndithu (Luti) adawachenjeza anthu ake za kulanga Kwathu koopsa. Koma adakaikira machenjezo (ake ndi kumtsutsa)

Verse 37 — Surah Al-Qamar 54:37

“Ndipo ndithu adafuna kwa iye kuti awapatse alendo ake (kuti achite nawo zauve), koma tidafafaniza maso awo (kuti ikhale mphoto pa zimene adafunazo). (Ndipo tidawauza): “Choncho lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.”

Verse 38 — Surah Al-Qamar 54:38

“Ndipo ndithu chidawadzera mwadzidzidzi chilango chokhazikika, nthawi yam’mamawa

Verse 39 — Surah Al-Qamar 54:39

“Choncho (kudanenedwa kwa iwo) “Lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.”

Verse 40 — Surah Al-Qamar 54:40

“Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an (kuti ikhale chikumbutso). Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

Verse 41 — Surah Al-Qamar 54:41

“Ndipo ndithu machenjezo (ondondozana) adawadzera anthu a Farawo (ndi iye mwini)

Verse 42 — Surah Al-Qamar 54:42

“Adatsutsa zozizwitsa Zathu zonse (zimene zidadza kupyolera m’manja mwa aneneri Athu). Choncho tidawalanga, kulanga kwa Wamphamvu (Wosapambanidwa), Wokhoza

Verse 43 — Surah Al-Qamar 54:43

“Kodi osakhulupirira anuwa ndi abwino kuposa iwo (kotero kuti sadzaonongedwa)? Kapena zalembedwa m’mabuku kuti inu mdzasiyidwa (sadzakuonongani monga momwe adawaonongera akale)

Verse 44 — Surah Al-Qamar 54:44

“Kapena akunena kuti: “Ife ndiochuluka titha kudziteteza (palibe angatipambane)?”

Verse 45 — Surah Al-Qamar 54:45

“(Auze): Gululo ligonjetsedwa ndipo athawa ndi kutembenuza misana

Verse 46 — Surah Al-Qamar 54:46

“Koma lonjezo la chilango chawo ndi tsiku la chiweruziro, ndipo tsiku la chiweruziro ndi latsoka lalikulu, lowawa kwabasi (kwa osakhulupirira)

Verse 47 — Surah Al-Qamar 54:47

“Ndithu oipa (mwa awa ndi aja) ali nkusokera ndi misala

Verse 48 — Surah Al-Qamar 54:48

“Tsiku limene adzakokedwera ku Moto ndi nkhope zawo, (kudzanenedwa kwa iwo:) “Lawani zowawa za Jahena (ndi kutentha kwake)

Verse 49 — Surah Al-Qamar 54:49

“Ndithu Ife tachilenga chinthu chilichonse ndi muyeso (kulingana ndi zolinga)

Verse 50 — Surah Al-Qamar 54:50

“Ndipo silili lamulo Lathu (pa chinthu tikachifuna) koma liwu limodzi, (timangoti kwa chinthucho: “Chitika.” Ndipo chimachitika mwachangu) ngati kuphethira kwa diso

Verse 51 — Surah Al-Qamar 54:51

“Ndipo ndithu tidawaononga anzanu (onga inu osakhulupirira): Kodi alipo wokumbuka

Verse 52 — Surah Al-Qamar 54:52

“Ndipo chinthu chilichonse adachichita iwowo (pa dziko lapansi) chili mkaundula

Verse 53 — Surah Al-Qamar 54:53

“Ndipo ntchito iliyonse, yaing’ono kapena yaikulu, idalembedwa; (palibe chimene chingamsowe)

Verse 54 — Surah Al-Qamar 54:54

“Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda ya ulemelero waukulu ndi Mitsinje (yosiyanasiyana)

Verse 55 — Surah Al-Qamar 54:55

“Pokhala pabwino pachoonadi, (popanda mawu achabe ndi machimo), kwa Mfumu yokhoza chilichonse