Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 55 - Ar-Rahman
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Ar-Rahman 55:1
“(Allah) Wachifundo chochuluka
Verse 2 — Surah Ar-Rahman 55:2
“Waphunzitsa Qur’an
Verse 3 — Surah Ar-Rahman 55:3
“Adalenga munthu
Verse 4 — Surah Ar-Rahman 55:4
“Adamphunzitsa kuyankhula
Verse 5 — Surah Ar-Rahman 55:5
“Dzuwa ndi mwezi zikuyenda mwachiwerengero
Verse 6 — Surah Ar-Rahman 55:6
“Zomera zopanda tsinde ndi mitengo, zikulambira (Allah pachilichonse chimene wafuna mwa izo)
Verse 7 — Surah Ar-Rahman 55:7
“Ndipo thambo adalitukula kumwamba ndipo adakhazikitsa sikelo (ya chilungamo)
Verse 8 — Surah Ar-Rahman 55:8
“Kuti musapyole malire ndi kuchita chinyengo poyesa
Verse 9 — Surah Ar-Rahman 55:9
“Choncho yesani sikelo mwachilungamo ndipo musapungule muyeso
Verse 10 — Surah Ar-Rahman 55:10
“Ndipo nthaka adaiyala (ndi kuikonza) kuti ikhale ya zolengedwa
Verse 11 — Surah Ar-Rahman 55:11
“M’menemo muli zipatso ndi mitengo ya kanjedza yokhala ndi mapava (a zipatso)
Verse 12 — Surah Ar-Rahman 55:12
“Ndi mbewu zamakoko (kuti chikhale chakudya cha inu ndi ziweto zanu), ndipo mulinso m’menemo mmera wafungo labwino
Verse 13 — Surah Ar-Rahman 55:13
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 14 — Surah Ar-Rahman 55:14
“Adalenga munthu kuchokera ku dongo lolira monga ziwiya zadongo
Verse 15 — Surah Ar-Rahman 55:15
“Ndipo adalenga ziwanda kuchokera ku malawi a moto (wopanda utsi)
Verse 16 — Surah Ar-Rahman 55:16
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 17 — Surah Ar-Rahman 55:17
“Mbuye wa kuvuma kuwiri ndiponso Mbuye wa kuzambwe kuwiri
Verse 18 — Surah Ar-Rahman 55:18
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 19 — Surah Ar-Rahman 55:19
“Adaika nyanja ziwiri zokumana (yamadzi amchere, ndi yamadzi ozizira)
Verse 20 — Surah Ar-Rahman 55:20
“Pakati pake pali chitsekerezo, sizilowana
Verse 21 — Surah Ar-Rahman 55:21
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 22 — Surah Ar-Rahman 55:22
“M’menemo mumatuluka ngale zing’onozing’ono ndi ngale zikuluzikulu
Verse 23 — Surah Ar-Rahman 55:23
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 24 — Surah Ar-Rahman 55:24
“Ndipo (Iye) ali nazo zombo (zimene zapangidwa ndi manja anu), zoyenda panyanja, zazikuluzikulu ngati mapiri
Verse 25 — Surah Ar-Rahman 55:25
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 26 — Surah Ar-Rahman 55:26
“Zonse zili pamenepo (pa dziko) nzakutha
Verse 27 — Surah Ar-Rahman 55:27
“Ndipo idzatsala nkhope ya Mbuye wako yaulemelero ndi mtendere
Verse 28 — Surah Ar-Rahman 55:28
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 29 — Surah Ar-Rahman 55:29
“(Onse) akumwamba ndi pansi akupempha Iye (zofuna zawo)! Tsiku lililonse Iye ali ndi zochita (monga kupatsa uyu ulemelero, ndi kutsitsa uyu)
Verse 30 — Surah Ar-Rahman 55:30
“(Inu zolengedwa zamitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 31 — Surah Ar-Rahman 55:31
“Posachedwapa (patsiku la chiweruziro), tidzaikapo mtima pa chiwerengero chanu (cha zochita zanu) inu anthu ndi ziwanda
Verse 32 — Surah Ar-Rahman 55:32
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 33 — Surah Ar-Rahman 55:33
“E inu ziwanda ndi anthu! Ngati mungathe kutuluka m’mphepete mwa thambo ndi nthaka (pothawa Allah), tulukani! Simungathe kutuluka pokhapokha ndi mphamvu. (Koma inu simungathe kutero)
Verse 34 — Surah Ar-Rahman 55:34
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 35 — Surah Ar-Rahman 55:35
“Mudzathiridwa malawi a moto ndi mtovu wa moto wosungunuka ndipo simungathe kupulumuka (ku chilango chimenechi)
Verse 36 — Surah Ar-Rahman 55:36
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 37 — Surah Ar-Rahman 55:37
“(Kumbuka) pamene thambo lidzang’ambika ndi kukhala lofiira ngati chikopa chofiira (kapena ngati mafuta oyaka)
Verse 38 — Surah Ar-Rahman 55:38
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 39 — Surah Ar-Rahman 55:39
“Ndipo patsikulo munthu ndi chiwanda, sadzafunsidwa (aliyense) za tchimo lake
Verse 40 — Surah Ar-Rahman 55:40
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 41 — Surah Ar-Rahman 55:41
“Adzadziwika oipa (pakati pa anthu ndi ziwanda) ndi zizindikiro zawo (zowazindikiritsa). Ndipo adzagwidwa maliombo awo ndi mapazi awo (ndi kuponyedwa ku Jahena)
Verse 42 — Surah Ar-Rahman 55:42
“((Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 43 — Surah Ar-Rahman 55:43
“(Kudzanenedwa mowadandaulitsa): Iyi ndi Jahannam yomwe adali kuitsutsa oipa
Verse 44 — Surah Ar-Rahman 55:44
“Adzakhala akuyenda pakati pa moto ndi pakati pa madzi owira, otentha kwambiri
Verse 45 — Surah Ar-Rahman 55:45
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 46 — Surah Ar-Rahman 55:46
“Koma amene waopa kuti adzaimitsidwa kwa Mbuye wake (pa nthawi ya chiweruziro), adzalandira minda iwiri (yaikulu yamtendere)
Verse 47 — Surah Ar-Rahman 55:47
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 48 — Surah Ar-Rahman 55:48
“(Minda ya mitengo) yanthambi zofwanthamuka
Verse 49 — Surah Ar-Rahman 55:49
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 50 — Surah Ar-Rahman 55:50
“M’menemo muli akasupe awiri, omwe akuyenda
Verse 51 — Surah Ar-Rahman 55:51
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 52 — Surah Ar-Rahman 55:52
“M’menemo muli zipatso za mtundu uliwonse, mitundu iwiri iwiri
Verse 53 — Surah Ar-Rahman 55:53
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 54 — Surah Ar-Rahman 55:54
“Atatsamira pa zoyala, mkati mwake mosokelera veleveti wochindikala; ndipo zipatso zam’minda iwiriyi nzapafupi (kuzithyola)
Verse 55 — Surah Ar-Rahman 55:55
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 56 — Surah Ar-Rahman 55:56
“M’mindamo muli akazi oyang’ana amuna awo okha basi, (mawuthu) omwe sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo
Verse 57 — Surah Ar-Rahman 55:57
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 58 — Surah Ar-Rahman 55:58
“Kukongola kwake (akaziwo) kuli ngati ngale zikuluzikulu ndi zing’onozing’ono
Verse 59 — Surah Ar-Rahman 55:59
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 60 — Surah Ar-Rahman 55:60
“Malipiro a ntchito zabwino ndikulandira zabwino basi
Verse 61 — Surah Ar-Rahman 55:61
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 62 — Surah Ar-Rahman 55:62
“Ndipo kuonjezera paminda iwiri (ija) palinso minda ina iwiri
Verse 63 — Surah Ar-Rahman 55:63
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 64 — Surah Ar-Rahman 55:64
“Yobiriwira, kwambiri
Verse 65 — Surah Ar-Rahman 55:65
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 66 — Surah Ar-Rahman 55:66
“M’menemo muli akasupe awiri ofwamphuka madzi mwaphamvu
Verse 67 — Surah Ar-Rahman 55:67
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 68 — Surah Ar-Rahman 55:68
“Mmenemo muli zipatso, mitengo yakanjedza ndi yamikangaza
Verse 69 — Surah Ar-Rahman 55:69
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 70 — Surah Ar-Rahman 55:70
“M’menemo muli akazi amakhalidwe abwino, owala nkhope
Verse 71 — Surah Ar-Rahman 55:71
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 72 — Surah Ar-Rahman 55:72
“Okongola maso, achikhalire m’mahema (m’matenti) awo
Verse 73 — Surah Ar-Rahman 55:73
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 74 — Surah Ar-Rahman 55:74
“Amene sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo
Verse 75 — Surah Ar-Rahman 55:75
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 76 — Surah Ar-Rahman 55:76
“Uku atatsamira misamiro yawofuwofu yokutidwa ndi zobiriwira; ndi zoyala zokongola, zakapangidwe kabwino
Verse 77 — Surah Ar-Rahman 55:77
“(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)
Verse 78 — Surah Ar-Rahman 55:78
“Latukuka ndi kudalitsika dzina la Mbuye wako Mwini ulemelero ndi ufulu