Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 56 - Al-Waqiah
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Waqiah 56:1
“Chikadzachitika chochitikacho (Qiyâma)
Verse 2 — Surah Al-Waqiah 56:2
“Palibe wotsutsa za kuchitika kwake
Verse 3 — Surah Al-Waqiah 56:3
“Chidzatsitsa (oipa) ndi kutukula (abwino)
Verse 4 — Surah Al-Waqiah 56:4
“Nthaka ikadzagwedezeka kwamphamvu
Verse 5 — Surah Al-Waqiah 56:5
“Ndipo mapiri akadzaperedwaperedwa
Verse 6 — Surah Al-Waqiah 56:6
“Nkukhala fumbi longouluka
Verse 7 — Surah Al-Waqiah 56:7
“Choncho, inu mudzakhala m’magulu atatu (kulingana ndi zochita zanu)
Verse 8 — Surah Al-Waqiah 56:8
“Anthu akumanja (abwino;) taonani kukula kwa ulemelero wa anthu akumanja
Verse 9 — Surah Al-Waqiah 56:9
“Ndi anthu akumanzere (oipa;) taonani kuipa khalidwe la anthu akumanzere
Verse 10 — Surah Al-Waqiah 56:10
“Ndipo otsogola (pochita zabwino pa dziko) adzakhalanso otsogola (polandira ulemu tsiku lachimaliziro)
Verse 11 — Surah Al-Waqiah 56:11
“Iwowo ndioyandikitsidwa (kwa Allah)
Verse 12 — Surah Al-Waqiah 56:12
“M’minda yamtendere
Verse 13 — Surah Al-Waqiah 56:13
“(Iwowo oyandikitsidwawo), gulu lalikulu lochokera kumibadwo yakale
Verse 14 — Surah Al-Waqiah 56:14
“Ndipo ochepa ochokera ku mbadwo wotsirizira
Verse 15 — Surah Al-Waqiah 56:15
“Uku ali m’makama (m’mabedi) olukidwa ndi zingwe zagolide
Verse 16 — Surah Al-Waqiah 56:16
“Atatsamira m’makamawo uku akuyang’anizana (mwachikondi)
Verse 17 — Surah Al-Waqiah 56:17
“Anyamata osasintha adzakhala akuwazungulira iwo (ndi kuwatumikira)
Verse 18 — Surah Al-Waqiah 56:18
“Uku atatenga matambula ndi maketulo (odzaza ndi zakumwa za ku Jannah), ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa zochokera mu akasupe oyenda
Verse 19 — Surah Al-Waqiah 56:19
“(Zakumwa zake) zosapweteketsa mutu ndiponso zosaledzeretsa
Verse 20 — Surah Al-Waqiah 56:20
“Ndi zipatso (zamitundumitundu) zimene azikazisankha
Verse 21 — Surah Al-Waqiah 56:21
“Ndi nyama yambalame imene mitima yawo izikafuna
Verse 22 — Surah Al-Waqiah 56:22
“Ndi akazi ophanuka maso mokongola
Verse 23 — Surah Al-Waqiah 56:23
“(Kukongola kwawo) ndiye ngati ngale zosungidwa bwino mzigoba zake
Verse 24 — Surah Al-Waqiah 56:24
“Kukhala mphoto chifukwa cha zimene amachita (zabwino padziko lapansi)
Verse 25 — Surah Al-Waqiah 56:25
“M’menemo sakamva mawu achabe ngakhale (mawu a) machimo
Verse 26 — Surah Al-Waqiah 56:26
“Koma mawu oti: “Mtendere! Mtendere!”
Verse 27 — Surah Al-Waqiah 56:27
“Anthu akudzanja lamanja. Taonani kukula malipiro a anthu akudzanja lamanja
Verse 28 — Surah Al-Waqiah 56:28
“(Adzakhala m’mithunzi ya) mitengo ya masawu yopanda minga
Verse 29 — Surah Al-Waqiah 56:29
“Ndi mitengo ya nthochi yobereka kwambiri
Verse 30 — Surah Al-Waqiah 56:30
“Ndi m’mithunzi yotambasuka kwambiri, yosachoka
Verse 31 — Surah Al-Waqiah 56:31
“Ndi madzi oyenda mosalekeza
Verse 32 — Surah Al-Waqiah 56:32
“Ndi zipatso zambiri
Verse 33 — Surah Al-Waqiah 56:33
“Zopezeka mnyengo zonse, ndiponso zosaletsedwa (kwa amene akuzifuna)
Verse 34 — Surah Al-Waqiah 56:34
“Ndi zoyala zapamwamba (zawofuwofu)
Verse 35 — Surah Al-Waqiah 56:35
“Ndithu tidzawalenga (akazi okhulupirira) m’kalengedwe kapamwamba
Verse 36 — Surah Al-Waqiah 56:36
“Tidzawapanga kukhala anamwali
Verse 37 — Surah Al-Waqiah 56:37
“Okondedwa ndi amuna awo; ofanana misinkhu
Verse 38 — Surah Al-Waqiah 56:38
“A anthu akudzanja la manja
Verse 39 — Surah Al-Waqiah 56:39
“Gulu lalikulu lochokera ku m’badwo woyamba
Verse 40 — Surah Al-Waqiah 56:40
“Ndiponso gulu lalikulu lochokera ku mibadwo yotsiriza
Verse 41 — Surah Al-Waqiah 56:41
“Anthu akudzanja lakumanzere. Taonani chilango choopsa kwa anthu akudzanja lakumanzere
Verse 42 — Surah Al-Waqiah 56:42
“Adzakhala mu mvuchi wamoto ndi m’madzi owira
Verse 43 — Surah Al-Waqiah 56:43
“Ndi mumthunzi wa utsi wakuda
Verse 44 — Surah Al-Waqiah 56:44
“Siwoziziritsa ndiponso siwosangalatsa
Verse 45 — Surah Al-Waqiah 56:45
“Ndithu iwo amakhala kalelo mosangalala (samalabadira kumvera Allah)
Verse 46 — Surah Al-Waqiah 56:46
“Ndipo amapitiriza kuchita machimo aakulu (polinga kuti palibe kuuka ku imfa)
Verse 47 — Surah Al-Waqiah 56:47
“Ndipo amanena (motsutsa); “Kodi tikadzafa nkusanduka fumbi ndi mafupa ofumbwa, tidzaukitsidwanso?”
Verse 48 — Surah Al-Waqiah 56:48
““Kodi ndi makolo athu akale (adzaukitsidwanso!)”
Verse 49 — Surah Al-Waqiah 56:49
“Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo). Ndithudi, amibadwo yoyamba ndi mibadwo yomaliza (omwe inu muli m’gulu lawo)
Verse 50 — Surah Al-Waqiah 56:50
“Adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya tsiku lomwe lakhazikitsidwa
Verse 51 — Surah Al-Waqiah 56:51
“Kenako inu osokera (njira yachilungamo), otsutsa (za kuuka)
Verse 52 — Surah Al-Waqiah 56:52
“Mudzadya (ku Jahannam) mtengo wa Zakkum, (mtengo wowawa wopezeka mu Jahannam)
Verse 53 — Surah Al-Waqiah 56:53
“Mudzakhutitsa mimba zanu ndi umenewu (chifukwa cha njala yadzaoneni)
Verse 54 — Surah Al-Waqiah 56:54
“(Mkhuto wa mtengowo) adzamwera madzi owira
Verse 55 — Surah Al-Waqiah 56:55
“Adzamwa monga mmene imamwera ngamira yodwala matenda aludzu
Verse 56 — Surah Al-Waqiah 56:56
“Ili ndi phwando lawo tsiku lamalipiro
Verse 57 — Surah Al-Waqiah 56:57
“Ife tidakulengani kodi nchifukwa ninji simukukhulupirira
Verse 58 — Surah Al-Waqiah 56:58
“Tandiuzani za madzi (ambewu ya munthu) amene mumawathira m’chiberekero
Verse 59 — Surah Al-Waqiah 56:59
“Kodi inu ndiamene mumawalenga (madziwo ndi kumayang’anira mkusinthasintha kwake kuti akhale cholengedwa) kapena Ife ndiamene timawalenga
Verse 60 — Surah Al-Waqiah 56:60
“Ife tidalamula imfa pakati panu ndipo Ife sitili wolephera
Verse 61 — Surah Al-Waqiah 56:61
“Kubweretsa ena m’malo mwanu ndi kukulengani mwamaonekedwe ena omwe simumawadziwa
Verse 62 — Surah Al-Waqiah 56:62
“Ndipo ndithu mukdziwa kalengedwe koyamba; nanga bwanji simukukumbukira
Verse 63 — Surah Al-Waqiah 56:63
“Tandiuzani za zimene mukubzala
Verse 64 — Surah Al-Waqiah 56:64
“Kodi ndinu amene mukuzimeretsa kapena ndife Amene tikuzimeretsa
Verse 65 — Surah Al-Waqiah 56:65
“Tikadafuna tikadazitembenuza (mbewu zimenezo kukhala zouma isanakwane nthawi yake yozithyola) choncho mukadakhala mukudandaula
Verse 66 — Surah Al-Waqiah 56:66
“(Uku mukunena:) “Ndithu ife tangotaya chuma chathu (padera);”
Verse 67 — Surah Al-Waqiah 56:67
““Koma ife tamanidwa (phindu la khama lathu).”
Verse 68 — Surah Al-Waqiah 56:68
“Kodi mukuwaona madzi amene mukumwa
Verse 69 — Surah Al-Waqiah 56:69
“Kodi ndinu amene mudawatsitsa ku mitambo kapena ndife Amene timawatsitsa
Verse 70 — Surah Al-Waqiah 56:70
“Tikadafuna tikadawapanga kukhala amchere; nanga nchifukwa ninji simuthokoza
Verse 71 — Surah Al-Waqiah 56:71
“Kodi mukuwuona moto umene mumaukoleza
Verse 72 — Surah Al-Waqiah 56:72
“Kodi ndinu amene mudameretsa mitengo yake kapena Ndife tidaipanga
Verse 73 — Surah Al-Waqiah 56:73
“Ife taupanga kuti ukhale chikumbutso (cha Moto watsiku lachimaliziro akauona), ndikuti ukhale chothandiza kwa anthu apaulendo (amene akuyenda m’chipululu)
Verse 74 — Surah Al-Waqiah 56:74
“Choncho, pitiriza kulemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu
Verse 75 — Surah Al-Waqiah 56:75
“Ndikulumbilira motsimikiza, mmene mumatsikira nyenyezi (pomwe zikulowa)
Verse 76 — Surah Al-Waqiah 56:76
“Ndithu kulumbira uku, mukadakhala olingalira, nkwakukulu kwabasi (pazimene kukusonya)
Verse 77 — Surah Al-Waqiah 56:77
“Ndithu iyi ndi Qur’an yolemekezeka (ndipo mkati mwake muli zithandizo zambiri)
Verse 78 — Surah Al-Waqiah 56:78
“Idachokera mu buku lotetezedwa
Verse 79 — Surah Al-Waqiah 56:79
“Salikhudza kupatula okhawo oyeretsedwa (angelo)
Verse 80 — Surah Al-Waqiah 56:80
“Chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse
Verse 81 — Surah Al-Waqiah 56:81
“Kodi nkhani iyi (ya Qur’an) ndiyomwe inu mukuinyozera
Verse 82 — Surah Al-Waqiah 56:82
“Kodi mwakuchita kukanira kukhala kuthokoza kwanu pa zimene wakupatsani
Verse 83 — Surah Al-Waqiah 56:83
“Mmaona bwanji (mzimu wa mmodzi wa inu) ukafika kummero (panthawi ya imfa)
Verse 84 — Surah Al-Waqiah 56:84
“Uku inu panthawi imeneyo mukuona zimenezo
Verse 85 — Surah Al-Waqiah 56:85
“Pomwe Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu, koma inu simuona
Verse 86 — Surah Al-Waqiah 56:86
“Mukadakhala kuti simuzalipidwa (pa zomwe mukuchita)
Verse 87 — Surah Al-Waqiah 56:87
“Bwenzi mukuubweza (mzimuwo) ngati mukunena zoona
Verse 88 — Surah Al-Waqiah 56:88
“Ngati (amene yamfikira imfayo) adali mmodzi wa woyandikitsidwa (kwa Allah)
Verse 89 — Surah Al-Waqiah 56:89
“Kobwerera kwake ndi kumpumulo ndi mtendere ndi kupatsidwa zonunkhira ndiponso Munda wamtendere
Verse 90 — Surah Al-Waqiah 56:90
“Ndipo ngati adali mmodzi wa anthu akudzanja lamanja
Verse 91 — Surah Al-Waqiah 56:91
“(Kudzanenedwa kwa iye:) “Mtendere ukhale pa iwe, amene udali m’gulu la anthu akudzanja lakumanja (anthu abwino).”
Verse 92 — Surah Al-Waqiah 56:92
“Koma ngati adali mmodzi wa anthu otsutsa, osokera
Verse 93 — Surah Al-Waqiah 56:93
“Phwando lamadzi owira (ndilake)
Verse 94 — Surah Al-Waqiah 56:94
“Ndi kupsa m’moto wa Jahena
Verse 95 — Surah Al-Waqiah 56:95
“Ndithu izi ndizoona, zotsimikizika
Verse 96 — Surah Al-Waqiah 56:96
“Choncho lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu