Back to Languages

Chichewa - Chapter 58 - Al-Mujadila

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Mujadila 58:1

“۞ Ndithu Allah wamva mawu a (mkazi) amene akubwezeranabwezerana nawe (mawu) pa za mwamuna wake (amene adamsala); ndipo akusuma kwa Allah. Ndipo Allah akumva kukambirana kwanu; ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya (chilichonse)

Verse 2 — Surah Al-Mujadila 58:2

“Amene akufanizira mwa inu (Asilamu) akazi awo (ndi amayi awo) iwo siamayi awo; amayi awo ndiamene adawabereka. Ndithu iwo akunena mawu oipa ndi onama. Koma ndithu Allah ali Wofafaniza (machimo) ndi Wokhululuka (kwa amene walapa)

Verse 3 — Surah Al-Mujadila 58:3

“Ndipo amene akuwafanizira akazi awo (ndi amayi awo) kenako nkubweza zimene adanena, apereke ufulu kwa kapolo asanakhale malo amodzi (ndi mkaziyo). Amenewa ndi malamulo a Allah kwa inu (amene) mukuchenjezedwa nawo. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita (zoonekera poyera ndi zosaonekera choncho sungani malamulo amene Allah wakhazikitsa pa inu)

Verse 4 — Surah Al-Mujadila 58:4

“Ndipo amene sadapeze (kapolo) asale miyezi iwiri yondondozana asadakhalirane pamodzi (ndi mkaziyo), koma amene sadathe kusala adyetse masikini makumi asanu ndi limodzi . Izi (zalamulidwa) kuti mukhulupirire mwa Allah ndi Mthenga Wake. Amenewo ndiwo malire a Allah; (malamulo okhazikitsidwa ndi Allah choncho musawalumphe). Ndipo chilango chopweteka chili pa osakhulupirira

Verse 5 — Surah Al-Mujadila 58:5

“Ndithu amene akutsutsana ndi Allah kudzanso Mthenga Wake, ayalutsidwa monga momwe adayalutsidwira amene adalipo patsogolo pawo; ndithu tavumbulutsa Ayah zolongosola, momveka (pa zololedwa ndi zoletsedwa). Ndipo chilango choyalutsa chili pa osakhulupirira

Verse 6 — Surah Al-Mujadila 58:6

“(Kumbuka) tsiku limene Allah adzaukitsa akufa onse ndi kuwafotokozera zimene adachita (pa moyo wa dziko lapansi: zoipa ndi zabwino); Allah adazisunga mozilemba koma iwo adaziiwala. Ndipo Allah ndi mboni wa zonse (palibe chingabisike kwa Iye)

Verse 7 — Surah Al-Mujadila 58:7

“Kodi sukudziwa (iwe, womvera wanzeru) kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zam’dziko lapansi? Sipakhala manong’onong’o a (anthu) atatu koma Iye Ngwachinayi wawo (ndi kudziwa kwake kosabisika chilichonse cha kumwamba ndi m’dziko), ngakhale a (anthu) asanu koma Iye Ngwachisanu ndi chimodzi wawo (mkudziwa Kwake), ngakhale ali ochepera kuposera pamenepa kapena ochulukira koma Iye ali nawo paliponse pomwe ati akhale (Allah ali nawo pamodzi mukudziwa Kwake kosabisika chilichonse), kenako adzawafotokozera pa tsiku la chiweruziro zimene adachita; ndithu Allah Ngodziwa chilichonse (mokwanira)

Verse 8 — Surah Al-Mujadila 58:8

“Kodi siudaone! Kwa amene aletsedwa kunong’onezana zoipa pakati pawo, kenako akubwereza zimene adaletsedwa? Akunong’onezana za machimo, mtopola ndi kunyoza Mtumiki. Akakudzera akukulonjera (ndi malonje achinyengo) amene Allah sadakulonjerepo nawo ndipo akunena m’mitima mwawo: “Kodi nchifukwa chiyani Allah sakutilanga ndi mawu tikunenawa (ngati iyeyu ndi Mtumikidi wa Allah?” Jahannam ikuwakwanira: adzailowa. Ndipo taonani kuipa malo (awo) wobwerera

Verse 9 — Surah Al-Mujadila 58:9

“E inu amene mwakhulupirira! Ngati mukunong’onezana, musamanong’onezane za machimo ndi mtopola ndi kunyoza Mtumiki; koma nong’onezanani za kulungama ndi kuopa Allah ndipo muopeni Allah, kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwe (ndi kuweruzidwa)

Verse 10 — Surah Al-Mujadila 58:10

“Ndithu manong’onong’o oipa amachokera kwa satana kuti adandaulitse amene akhulupirira; koma sangawapweteke nawo chilichonse kupatula Allah atafuna ndipo okhulupirira atsamire kwa Allah Yekha, (asalabadire zonong’onezana zawo)

Verse 11 — Surah Al-Mujadila 58:11

“E inu amene mwakhulupirira! Kukapemphedwa kwa inu kuti perekani malo pabwalo (pokhala), perekani malowo (kuti anzanu apeze pokhala; mukatero) Allah akuphanulirani (chifundo Chake pano pa dziko ndi kumwamba). Ndipo kukanenedwa kuti imilirani, muimilire (musanyozere, apatseni ena malo); Allah awakwezera (ulemelero) mwa inu amene akhulupirira ndi amene apatsidwa nzeru. Ndipo Allah akudziwa bwino zimene mukuchita

Verse 12 — Surah Al-Mujadila 58:12

E inu amene mwakhulupirira! Mukafuna kuyankhula ndi Mtumiki (s.a.w) tsogozani pa zoyankhula zanuzo, sadaka: kutero ndibwino kwa inu ndiponso ndichoyeretsa (mitima yanu). Koma ngati simudapeze (sadakayo) ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni

Verse 13 — Surah Al-Mujadila 58:13

“Kodi mwaopa kutsogoza sadaka pakunena naye (Mtumiki)? Ngati simudachite zimenezi basi Allah wakukhululukirani; choncho pempherani Swala moyenera ndipo perekani Zakaat ndiponso mverani Allah pamodzi ndi Mtumiki Wake. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

Verse 14 — Surah Al-Mujadila 58:14

“Kodi sukuwaona amene apalana ubwenzi ndi anthu amene Allah wawakwiira; iwo sali mwa inu ndiponso sali mwa iwo. Ndipo akulumbira zabodza uku akudziwa (kuti limeneli ndibodza)

Verse 15 — Surah Al-Mujadila 58:15

“Allah wawakonzera chilango chaukali, ndithudi nzoipa zimene amachita

Verse 16 — Surah Al-Mujadila 58:16

“Kulumbira kwawo adakuchita kukhala chodzitetezera (iwo, ana awo ndi chuma chawo); choncho adatsekereza (anthu) ku njira ya Allah; choncho chilango choyalutsa chili pa iwo

Verse 17 — Surah Al-Mujadila 58:17

“Chuma chawo, ngakhale ana awo, sizidzawathandiza konse ku chilango cha Allah. Iwowo ndi anthu a ku Moto m’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali

Verse 18 — Surah Al-Mujadila 58:18

“(Alikumbukire) tsiku limene Allah adzawaukitsa (ku imfa) onse, adzayamba kulumbira kwa Iye (zabodza) monga akulumbira (zabodza) kwa inu. Ndipo akuganiza kuti apezapo kanthu (pakulumbira kwawo). Dziwani, ndithudi, iwo ndi abodza

Verse 19 — Surah Al-Mujadila 58:19

“Satana wawapambana ndipo wawaiwalitsa kukumbukira Allah. Iwowa ndiachipani cha satana. Dziwani kuti chipani cha satana nchotayika, (choonongeka)

Verse 20 — Surah Al-Mujadila 58:20

“Ndithudi amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, iwowo adzakhala m’gulu la onyozeka

Verse 21 — Surah Al-Mujadila 58:21

“Allah adalamula (kuti): “Ndithu ndipambana Ine ndi atumiki Anga.” Ndithu Allah ndiwanyonga zokwana, Wopambana (sapambanidwa ndi aliyense)

Verse 22 — Surah Al-Mujadila 58:22

“Supeza anthu okhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro akukonda amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, ngakhale atakhala atate awo, ana awo abale awo ndi akumtundu wawo; kwa iwo (Allah) wazika chikhulupiliro (champhamvu) m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi mphamvu zochokera kwa Iye. Ndipo adzawalowetsa m’minda yomwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Allah adzakondwera nawo ndipo (iwonso) adzakondwera Naye. Iwowa ndi chipani cha Allah. Dziwani kuti chipani cha Allah ndichopambana