Back to Languages

Chichewa - Chapter 6 - Al-Anam

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Anam 6:1

“Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, napanga mdima ndi kuunika pamwamba pa izi, kenako amene sadakhulupirire akumfanizira Mbuye wawo ndi milungu yabodza

Verse 2 — Surah Al-Anam 6:2

“Iye ndi Yemwe adakulengani ndi dongo, kenako adaika nthawi (yothera cholengedwa chilichonse), ndi nthawi ina yodziwika kwa Iye (yomwe njoukitsira zolengedwa ku imfa). Ndipo pa izi inu (osakhulupirira) mukukaikira

Verse 3 — Surah Al-Anam 6:3

“Ndipo Iye ndi Allah (Wopembedzedwa) kumwamba ndi pansi. Akudziwa za mkati mwanu ndi zakunja kwanu, ndipo akudziwa zimene mukupeza (kuchokera mzochitachita zanu, zabwino kapena zoipa)

Verse 4 — Surah Al-Anam 6:4

“Ndipo palibe pamene chikuwadzera chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo koma akuzitembenukira kumbali

Verse 5 — Surah Al-Anam 6:5

“Ndithudi, atsutsa choonadi (Qur’an) pamene chawadzera. Posachedwapa ziwafika nkhani (za zilango) zimene adali kuzichitira chipongwe

Verse 6 — Surah Al-Anam 6:6

“Kodi saona kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Tidawapatsa mphamvu yopezera za m’dziko zomwe sitidakupatseni inu. Ndipo tidawavumbwitsira mvula yopitiriza (mwa ubwino choncho, adasangalala kopambana). Ndipo tidaipanga mitsinje kuyenda pansi pawo (pansi pa mitengo yawo ndi nyumba zawo). Kenako tidawaononga chifukwa cha machimo awo, ndipo pambuyo pawo tidalenga mibadwo ina

Verse 7 — Surah Al-Anam 6:7

“Ndipo ngati tikadakutsitsira malemba (olembedwa) m’mapepala, (monga momwe adakufunsira), nkuwakhudza ndi manja awo, amene sadakhulupirire akadati: “Ichi sichina koma ndi matsenga owoneka.”

Verse 8 — Surah Al-Anam 6:8

“Ndipo amanena: “Bwanji iye osamtsitsira mngelo (kuti aziikira umboni kwa anthu za uneneri wake)?” Tikadakutsitsira mngelo (nkusakhulupirira), ndithu chiweruzo cha kuonongeka kwawo chikadakwaniritsidwa. Ndipo sakadapatsidwanso mpata

Verse 9 — Surah Al-Anam 6:9

“Ndipo tikadampanga iyeyo kukhala mngelo, tikadamsandutsa kukhala munthu (chifukwa iwo sangathe kumuona mngelo), ndipo tikadati asakanikirane nawo monga momwe eni amasakanikirana (kotero kuti sakadamdziwa kuti mngelo ndi uyu)

Verse 10 — Surah Al-Anam 6:10

“Ndithudi, adachitidwa chipongwe atumiki patsogolo pako; koma (mapeto ake) aja mwa iwo omwe adachita chipongwe zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe

Verse 11 — Surah Al-Anam 6:11

“Nena: “Yendani pa dziko, kenako tayang’anani momwe adalili mapeto a otsutsa.”

Verse 12 — Surah Al-Anam 6:12

“Nena (mowafunsa): “Nzayani zomwe zili kumwamba ndi pansi?” Nena kwa iwo (ngati sakuyankha): “Nza Allah.” Iye wadzikakamiza kuwachitira chifundo (anthu Ake). (Pachifukwa chimenechi amawapatsa nthawi osawalanga mwachangu). Ndithudi adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko. Amene adzitaya okha, sakhulupirira (za tsikulo)

Verse 13 — Surah Al-Anam 6:13

“Nza Iye (Allah) zonse zili mu nthawi ya usiku ndi usana. Iye Ngwakumva, Ngodziwa

Verse 14 — Surah Al-Anam 6:14

“Nena: “Ndidzipangire mtetezi wanga kusiya Allah, Mlengi wa thambo ndi nthaka? Iye Njemwe amadyetsa ndipo sadyetsedwa.” Nena: “Ndalamulidwa kukhala woyamba mwa olowa m’Chisilamu.” Ndipo (ndauzidwa kuti): “Usakhale mwa ophatikiza (Allah ndi mafano)”

Verse 15 — Surah Al-Anam 6:15

“Nena (kwa iwo): “Ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.”

Verse 16 — Surah Al-Anam 6:16

“Yemwe adzapewetsedwe ku chilangocho tsiku limenelo, ndiye kuti wamchitira chifundo; kumeneko nkupambana kowonekera

Verse 17 — Surah Al-Anam 6:17

“Ngati Allah atakukhudza ndi mazunzo, palibe aliyense angathe kukuchotsera, koma Iye basi; ndipo ngati atakukhudza ndi zabwino (palibe amene angakutsekereze ku zabwinozo). Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse

Verse 18 — Surah Al-Anam 6:18

“Iye ndi Mgonjetsi pa anthu ake (onse); Iye Ngwanzeru zakuya, Wodziwa nkhani zonse

Verse 19 — Surah Al-Anam 6:19

“Nena: “Kodi nchinthu chanji chomwe umboni wake uli waukulu koposa?” Nena (ngati sakuyankha): “Ndi (umboni wa) Allah basi. (Iye) ndi Mboni pakati pa ine ndi inu. Ndipo Qur’an iyi yavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni nayo ndi amene yawafika (pali ponse pamene ali). Kodi inu mukutsimikiza ndi kuikira umboni kuti pali milungu ina pamodzi ndi Allah?” Nenanso: “Koma ine sindikuikira umboni.” Nenanso: “Iye ndi Mulungu Mmodzi Yekha. Ndithudi, ine ndili kutali ndi zomwe mukumphatikiza nazo.”

Verse 20 — Surah Al-Anam 6:20

“Omwe tidawapatsa buku akumzindikira (Muhammad {s.a.w} bwinobwino) monga momwe akuwazindikilira ana awo. Koma omwe adziononga okha, iwo sangakhulupirire

Verse 21 — Surah Al-Anam 6:21

“Kodi ndani woipitsitsa zedi woposa yemwe akum’pekera Allah bodza. Kapena kutsutsa zizindikiro Zake? Ndithudi, oipa sangapambane

Verse 22 — Surah Al-Anam 6:22

“Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse pamodzi; kenako tidzati kwa omwe adali kuphatikiza (Allah ndi mafano): “Ali kuti aphatikizi anu aja omwe munkati ngothandizana ndi Allah?”

Verse 23 — Surah Al-Anam 6:23

“Ndipo dandaulo lawo silidzakhala lina koma kunena: “Tikulumbilira Allah Mbuye wathu, sitidali ophatikiza (mafano ndi Allah).” (Uku kudzakhala kuyesera kumunamiza Allah)

Verse 24 — Surah Al-Anam 6:24

“Taona momwe akudzinamizira okha ndipo zidzawasokonekera zomwe adali kuzipeka (ponena kuti izo ndi milungu zidzawapulumutsa kwa Allah)

Verse 25 — Surah Al-Anam 6:25

“Alipo ena mwa iwo omwe akukumvetsera (ukamawerenga Qur’an), ndipo taika zitsekero pa mitima yawo kuti asazindikire (chifukwa cha machimo awo omwe akhala akuchita), ndi m’makutu mwawo kulemera kwa ugonthi; ndipo akaona chozizwitsa chilichonse, sakuchikhulupirira, kufikira akakudzera kudzakangana nawe, awo amene sadakhulupirire akuti: “Izi (zimene utilankhulazi), sikanthu koma ndi nkhani zopeka za anthu akale.”

Verse 26 — Surah Al-Anam 6:26

“Ndipo iwo akuletsa (anthu kutsatira) izi, ndipo (eniwo) akudzitalikitsa nazo. Palibe wina akumuononga koma iwo okha, ndipo sakudziwa

Verse 27 — Surah Al-Anam 6:27

“Ndipo ukadaona (tsiku la Qiyâma) pamene adzawaimitsa pa Moto nkuyamba kunena: “Ha! Tikadabwezedwa (ku dziko lapansi) ndipo sitikadatsutsanso zizindikiro za Mbuye wathu; ndipo tikadakhala mwa okhulupirira.”

Verse 28 — Surah Al-Anam 6:28

“(Sichoncho) koma zawaonekera poyera zomwe adali kubisa kale. Ndipo akadabwezedwa akadabwerezanso kuchita zimene adaletsedwa. Ndithudi iwo ngabodza basi

Verse 29 — Surah Al-Anam 6:29

“Akumanena: “Palibe moyo wina koma moyo wathu wa pa dziko lapansi basi. Ndipo ife sitidzaukitsidwanso m’manda.”

Verse 30 — Surah Al-Anam 6:30

“Ndipo ukadaona (tsiku la chiweruziro) pamene azikaimitsidwa pamaso pa Mbuye wawo nauzidwa: “Kodi ichi sichoona?” (Iwo) nati: “Inde nchoona, tikulumbira Mbuye wathu.” (Allah) adzati: “Lawani chilango chifukwa cha kusakhulupirira kwanu (aneneri a Allah).”

Verse 31 — Surah Al-Anam 6:31

“Ndithudi, ataika ndi kuonongeka amene akutsutsa zokumana ndi Allah, mpaka mwadzidzidzi nthawi ya Qiyama itawafikira, adzati: “Ho! Masautso pa ife chifukwa chakusalabadira kwathu za zimenezi, uku iwo atasenza mitolo ya machimo kumisana kwao. Taonani kuipa kwa zomwe akusenza

Verse 32 — Surah Al-Anam 6:32

“Ndipo moyo wadziko lapansi sikanthu, koma ndi masewera ndi chibwana. Koma nyumba yomaliza ndiyabwino koposa, (siyofanana ndi chisangalalo cha pa dziko lapansi) kwa omwe akuopa Allah. Bwanji simuzindikira

Verse 33 — Surah Al-Anam 6:33

“Ndithu tikudziwa kuti zikukudandaulitsa zomwe akukunenera (pokunyoza ndi kukuyesa wabodza. Ndithu iwo sakukutsutsa iwe; koma oipawa akutsutsa zizindikiro za Allah)

Verse 34 — Surah Al-Anam 6:34

“Ndithudi, atumiki onse adatsutsidwa iwe usadadze. Koma adapirira ku zomwe adatsutsidwa, ndipo adazunzidwa kufikira pamene chipulumutso Chathu chidawafika. Palibe wosintha mawu a Allah. Ndithu zakufika nkhani za atumiki (momwe muli malingaliro ndi maphunziro ambiri)

Verse 35 — Surah Al-Anam 6:35

“Ndipo ngati nkovuta kwa iwe kudzipatula kwawoku (ndi zomwe wadza nazozi pomwe iwo akukuumiriza kuti uwabweretsere chozizwitsa, nawe nkumafuna; zikadatero, pomwe Ine sindikufuna), choncho ngati uli wokhoza kufunafuna njira ya pansi penipeni m’nthaka (kukafuna zozizwitsazo), kapena (ungathe kupeza) makwelero nkukwera kumwamba nkubwera ndi chozizwitsa (chimene akufuna, chita). Allah Akadafuna akadawasonkhanitsa onse ku chiwongoko. Choncho, usakhale mwa osazindikira zinthu

Verse 36 — Surah Al-Anam 6:36

“Ndithudi amene akuvomereza, ngomwe akumva (ndipo anthu awa amene safuna kumvera chilichonse ndi akufa ngakhale ali moyo). Ndipo akufa Allah adzawaukitsa (m’manda mwawo) kenako adzabwezedwa kwa Iye

Verse 37 — Surah Al-Anam 6:37

“Ndipo akumanena: “Bwanji sichinatsitsidwe chozizwitsa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Ndithudi, Allah Ngokhoza kutsitsa chozizwitsa koma ambiri a iwo sadziwa (zomwe Allah afuna).”

Verse 38 — Surah Al-Anam 6:38

“Ndipo palibe nyama ili yonse pa nthaka, ngakhale mbalame yowuluka ndi mapiko ake awiri koma ndi magulu a zolengedwa ngati inu (zomwe Allah adazilenga). Sitinasiye chinthu chilichonse kapena kuchinyozera chilichonse m’buku (chomwe nchofunika koma tachifotokoza). Ndipo tero kwa Mbuye wawo adzasonkhanitsidwa

Verse 39 — Surah Al-Anam 6:39

“Ndipo amene atsutsa zizindikiro Zathu, ndiagonthi ndiponso abubu, ali mu m’dima (wa umbuli). Amene Allah wamfuna amamlekelera kusokera. Ndipo amene wamfuna amamuika pa njira yolunjika (yomwe ndi njira ya Chisilamu)

Verse 40 — Surah Al-Anam 6:40

“Nena: “Tandiuzani ngati mazunzo a Allah atakufikani (pompano pa dziko lapansi), kapena kukufikani nthawi (ya chilango cha tsiku lachimaliziro) kodi mudzaitana yemwe sali Allah (kuti akupulumutseni) ngati inu muli owona.”

Verse 41 — Surah Al-Anam 6:41

““Koma Iye yekha ndi Yemwe mudzampempha, ndipo Iye adzakuchotserani zomwe mukumpempha (kuti akuchotsereni) ngati atafuna. Ndipo mudzaiwala zomwe mudali kuziphatikiza (ndi Allah).”

Verse 42 — Surah Al-Anam 6:42

“Ndithu tidawatumiza (atumiki) ku mibadwo yomwe idalipo iwe usadadze. Ndipo tidaikhaulitsa (mibadwoyo) ndi mazunzo ndi masautso kuti iyo idzichepetse (pambuyo podzikuza)

Verse 43 — Surah Al-Anam 6:43

“Pamene masautso adawafika kuchokera kwa Ife, bwanji sadaphunzire kudzichepetsa? Koma mitima yawo idali youma, ndipo satana adawakometsera machimo omwe iwo adali kuchita

Verse 44 — Surah Al-Anam 6:44

“Ndipo pamene adanyozera zimene ankakumbutsidwa tidawatsekulira makomo a chinthu chilichonse (chimene adali kuchifuna) kufikira pamene adasangalala ndi zomwe adapatsidwa, tidawagwira mwadzidzidzi; pompo adataya mtima

Verse 45 — Surah Al-Anam 6:45

“Choncho mizu ya anthu oipa idadulidwa. Ndipo kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa

Verse 46 — Surah Al-Anam 6:46

“Nena: “Tandiuzani, ngati Allah atakuchotserani kumva kwanu ndi kupenya kwanu, nadinda chidindo m’mitima yanu (kuti asalowemo mawu amalangizo a mtundu uliwonse), kodi ndi mulungu uti, kupatula Allah, amene angakubwezereninso (zimenezi)?” Taona momwe tikufotokozera mwatsatanetsatane zizindikiro kenako iwo akunyozera

Verse 47 — Surah Al-Anam 6:47

“Nena: “Tandiuzani, ngati masautso a Allah atakufikani mwadzidzidzi kapena moonekera, kodi angaonongeke ndi ena osati anthu ochita zoipa?”

Verse 48 — Surah Al-Anam 6:48

“Ndipo sititumiza atumiki koma kuti akhale ouza nkhani zabwino ndi ochenjeza. Choncho amene akhulupirira nakonza zinthu, pa iwo sipadzakhala mantha ndiponso sadzadandaula

Verse 49 — Surah Al-Anam 6:49

“Ndipo amene atsutsa zizindikiro zathu, chilango chidzawakhudza chifukwa chakupandukira kwawo chilamulo

Verse 50 — Surah Al-Anam 6:50

“Nena: “Ine sindikukuuzani kuti ndili nazo nkhokwe za Allah kapena kuti ndikudziwa zamseri, ndiponso sindikukuuzani kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsata china koma zomwe zikuvumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi wakhungu ndi wopenya angafanane? Bwanji simukuganizira?”

Verse 51 — Surah Al-Anam 6:51

“Achenjeze ndi Qur’an iyi omwe akuopa kuti adzasonkhanitsidwa kwa Mbuye wawo pomwe ali opanda mtetezi ngakhale muomboli aliyense kupatula Iye, kuti iwo aope (Allah)

Verse 52 — Surah Al-Anam 6:52

“Ndipo usawathamangitse omwe akupembedza Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo pofuna chiyanjo Chake. Chiwerengero chawo sichili pa iwe ngakhale pang’ono, ndipo chiwerengero chako sichili pa iwo ngakhale pang’ono kotero kuti nkwathamangitsa. (Ngati uwapirikitsa) ukhala m’gulu la anthu ochita zoipa

Verse 53 — Surah Al-Anam 6:53

“Ndipo momwemo tawasankha ena (osauka) kukhala mayeso a ena (olemera) kuti (osauka) anene: “Kodi awa ndi omwe Allah wawasankhira ubwino mwa ife (ndikutisiya ife?)” Kodi Allah sali Wodziwa zedi amene akumthokoza

Verse 54 — Surah Al-Anam 6:54

“Ndipo (iwe Mneneri) akakudzera (awo osauka) amene akhulupirira zizindikiro zathu (atalakwa pang’ono), auze: “Mtendere ukhale pa inu. Mbuye wanu wadzikakamiza kukhala Wachifundo, kuti mwa inu amene achite choipa mwaumbuli, koma pambuyo pake nkulapa, nachita zabwino, Allah amkhululukira; Iye Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.”

Verse 55 — Surah Al-Anam 6:55

“Mmenemo ndi momwe tikufotokozera zizindikiro mwatsatanetsatane (kuti choonadi chioneke) ndi kuti njira ya oipa idziwike bwinobwino

Verse 56 — Surah Al-Anam 6:56

“Nena: “Ndithu ine ndaletsedwa kupembedza amene mukuwapembedza kusiya Allah.” Nena: “Sinditsata zilakolako zanu; ndikadatero ndikadasokera ndipo sindikadakhala mwa owongoka.”

Verse 57 — Surah Al-Anam 6:57

“Nena: “Ndithu ine ndili ndi umboni wowoneka wochokera kwa Mbuye wanga (wotsimikizira zomwe ndikunenazi), koma inu mwautsutsa. Ndilibe (chilango) chimene mukuchifulumizitsacho. Palibe kulamula koma nkwa Allah. Amakamba zoona zokhazokha; Iye Ngwabwino mwa oweruza (onse).”

Verse 58 — Surah Al-Anam 6:58

“Nena: “Ndikadakhala nacho chimene mukuchifulumizitsacho, ndiye kuti chinthucho chikadachitika pakati pa ine ndi inu (ndikadakuonongani koma ndilibe nyonga). Ndipo Allah akuwadziwa bwino anthu ochita zoipa.”

Verse 59 — Surah Al-Anam 6:59

“Ndipo Iye (Allah) ali nawo Makiyi a zobisika palibe akuwadziwa koma Iye basi. Ndipo akudziwa za pamtunda ndi za panyanja. Ndipo palibe tsamba limene limagwa koma amalidziwa. Ndipo (siigwa) njere mu mdima wa m’nthaka (koma iye akudziwa). Ndipo (sichigwa) chachiwisi ngakhale chouma, koma chili m’buku loonetsa chilichonse

Verse 60 — Surah Al-Anam 6:60

“Iye ndiyemwe amakupatsani imfa (yatulo) nthawi yausiku, ndipo amadziwa zimene mwachita masana, kenako amakudzutsani mmenemo kuti ikwane nthawi yanu yoikidwa (yofera); kenako kwa Iye ndiko kobwerera kwanu, nadzakuuzani zimene munkachita

Verse 61 — Surah Al-Anam 6:61

“Iye ndi M’gonjesi pa akapolo Ake ndipo amakutumizirani (angelo) osunga, (olemba zochita zanu); kufikira mmodzi wanu imfa ikamdzera, angelo athuwo amampatsa imfa, ndipo iwo sanyozera (ntchito yawo)

Verse 62 — Surah Al-Anam 6:62

“Kenako adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona. Dziwani kuti kuweruza Nkwake. Iye Ngwachangu powerengera kuposa owerengera (onse)

Verse 63 — Surah Al-Anam 6:63

“Nena: “Kodi ndani amakupulumutsani m’masautso a pamtunda ndi panyanja?” Mumampempha modzichepetsa ndi motsitsa mawu (kuti): “Ngati atipulumutsa m’mazunzo awa, ndithudi tidzakhala mwa othokoza.”

Verse 64 — Surah Al-Anam 6:64

“Nena: “Allah ndi Yemwe amakupulumutsani ku zimenezo ndi ku masautso a mtundu uliwonse. Kenako inu mukumphatikiza ndi mafano

Verse 65 — Surah Al-Anam 6:65

“Nena: “Iye Ngokhoza kukutumizirani chilango kuchokera pamwamba panu kapena pansi pa miyendo yanu, kapena kudzetsa chisokonezo nkukhala magulumagulu (osamvana), ndipo (akhoza) kuwalawitsa ena a inu chilango cha mtopola wa ena.” Taona momwe tikufotokozera zizindikiro kuti iwo azindikire

Verse 66 — Surah Al-Anam 6:66

“Koma anthu ako aitsutsa iyo (Qur’an) pomwe ili yoona. Nena: “Ine sindili muyang’anili pa inu.”

Verse 67 — Surah Al-Anam 6:67

“Nkhani iliyonse (yomwe yatchulidwa apa) ili ndi nthawi yake yodziwika (yofikira). Ndipo posachedwapa mudziwa (izi)

Verse 68 — Surah Al-Anam 6:68

“Ndipo (iwe Msilamu weniweni) ukawaona omwe akuchita chipongwe ndi Ayah Zathu, apatuke mpaka anene nkhani ina. Ndipo ngati satana atakuiwalitsa, (nkukhala nawo pomwe iwo akukambirana zotere), choncho, pambuyo pokumbukira usakhale pamodzi ndi anthu ochita zoipa

Verse 69 — Surah Al-Anam 6:69

“Palibe chilichonse chimene chingawapeze oopa Allah chochokera m’chiwerengero cha oipawo, koma chofunika kwa iwo (oopa Allah) ndikuwakumbutsa (oipawo) kuti aope (aleke zomwe akunenazo)

Verse 70 — Surah Al-Anam 6:70

“Asiye amene achita chipembedzo chawo kukhala masewera ndi chibwana. Ndipo wawanyenga moyo wadziko lapansi. Choncho, akumbutse ndi Qur’aniyo (kuti achenjere), kuti ungaonongedwe mtima uliwonse (ndi kuikidwa m’ndende) kupyolera mu zomwe udapata. Ndipo sukhala ndi mtetezi ngakhale muomboli posakhala Allah, ngakhale utayesera kupereka dipo lamtundu uliwonse silingavomerezedwe (kwa mzimuwo). Awo ndi omwe aonongeka ndi kunjatidwa chifukwa cha zomwe adapeza. Iwo adzakhala ndi chakumwa cha madzi a moto owira kwambiri, ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo (Allah)

Verse 71 — Surah Al-Anam 6:71

“Nena: “Kodi tipembedze omwe sali Allah, omwe sangatipatse phindu (ngati titawapembedza), ndiponso sangathe kutivutitsa (tikasiya kuwapembedza), ndetibwezedwe m’mbuyo pambuyo potitsogolera Allah? Tikhale chimodzimodzi aja omwe satana adawasokeretsa, nkukhala achewuchewu pa dziko? Ali nawo anzawo omwe akuwaitanira ku chiongoko (kuti) ‘Bwerani kwathu, (koma samva. Sitingakhale monga anthu otere).” Nena: “Utsogozi weniweni ngwa Allah, ndipo talamulidwa kuti tigonjere Mbuye wa zolengedwa zonse.”

Verse 72 — Surah Al-Anam 6:72

“Ndikuti: “Pempherani Swala, ndipo muopeni Iye, Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.”

Verse 73 — Surah Al-Anam 6:73

“Iye ndiye adalenga thambo ndi nthaka mwa choonadi. Ndipo panthawi imene akunena (kuchiuza chinthu): “Chitika,” ndipo chimachitikadi. Mawu ake ndioona. Ndipo ufumu udzakhala Wakewake tsiku limene Lipenga lidzaimbidwa. Ngodziwa zamseri ndi zooneka. Iye Ngwanzeru zakuya, Wodziwa nkhani zonse

Verse 74 — Surah Al-Anam 6:74

“Ndipo (kumbukirani) pamene Ibrahim adauza bambo ake, Azara: “Kodi mukupanga mafano kukhala milungu? Ndithu ine ndikukuonani inu ndi anthu anu kuti muli m’kusokera koonekera.”

Verse 75 — Surah Al-Anam 6:75

“Ndipo momwemo tidamuonetsa Ibrahim ufumu wa kumwamba ndi pansi (kuti ngwa Allah) kuti akhale m’modzi mwa otsimikiza

Verse 76 — Surah Al-Anam 6:76

“Ndipo pamene kunam’dera adaona nyenyezi. Adati (mwadaladala kuti abutse nzeru za opembedza mafano): “(Nyenyezi) iyi ndiye mbuye wanga.” Pamene idalowa, adati: “Sindikonda (milungu) yomalowa, (yomasowa, yakutha).”

Verse 77 — Surah Al-Anam 6:77

“Pamene adaona mwezi ukutuluka, adati: “Uyu ndiye mbuye wanga.” Koma pamene udalowa, adati: “Ngati Mbuye wanga sandiongolera, ndithudi, ndikhala m’gulu la anthu osokera.”

Verse 78 — Surah Al-Anam 6:78

“Pamene adaona dzuwa likutuluka, adati: “Uyu ndiye mbuye wanga; uyu ngwamkulu kwabasi.” Koma pamene lidalowa, adati: “E inu anthu anga! Ine ndili kutali ndi zomwe mukumphatikiza nazo (Allah)

Verse 79 — Surah Al-Anam 6:79

“Ndithu ine ndalungamitsa nkhope yanga kwa Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndapendekera kwa Iye Yekha. Ndipo ine sindili mwa om’phatikiza (Allah ndi mafano)

Verse 80 — Surah Al-Anam 6:80

“Ndipo anthu ake adakangana naye (pomuuza kuti: “Bwanji ukusiya chipembedzo chamakolo ako; uona malaulo”). (Iye) adati: “Kodi Mukukangana nane pa za Allah pomwe Iye wanditsogolera? Ndipo Sindingaope zimene mukumphatikiza Naye, kupatula Mbuye wanga akafuna chinthu, (apo chiyenera kuchitika). Mbuye wanga akudziwa chinthu chilichonse bwinobwino. Bwanji simulalikika?”

Verse 81 — Surah Al-Anam 6:81

““Ndipo ndingaope chotani zomwe mwaziphatikiza (ndi Allah) pomwe inu simuopa kuti mukumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadawatsitsire pa inu umboni (kuti muziwapembedza). Choncho ndi gulu liti m’magulu awa awiri (langa kapena lanu) loyenera koposa kupeza chitetezo? Ngati inu mudziwa (zinthu).”

Verse 82 — Surah Al-Anam 6:82

“(Palibe chikaiko kwa) amene adakhulupirira ndipo sadasakanize chikhulupiliro chawo ndi kupondereza (shirk), iwowo ali nacho chitetezo. Ndiponso iwo ndi omwe ali oongoka

Verse 83 — Surah Al-Anam 6:83

“Ndipo izi ndi zizindikiro Zathu (mitsutso Yathu), zomwe tidampatsa Ibrahim pa anthu ake. Timamtukulira ulemelero amene tamfuna. Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri

Verse 84 — Surah Al-Anam 6:84

“Ndipo tidampatsa (Ibrahim mwana wotchedwa) Ishaq ndi (mdzukulu wotchedwa) Ya’qub. Onse tidawaongola. Nayenso Nuh tidamuongola kale (asadadze Mneneri Ibrahim). Ndipo kuchokera m’mbumba yake (Nuh, tidamuongola) Daud, Sulaiman, Ayubu, Yûsuf, Mûsa, ndi Harun. Ndipo umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino

Verse 85 — Surah Al-Anam 6:85

“Tidamutsogoleranso Zakariya, Yahya, Isa (Yesu) ndi Iliyasa. Onse adali mwa anthu abwino

Verse 86 — Surah Al-Anam 6:86

“Ndi Ismail, Eliya, Yunus (Yona) ndi Luti (Loti). Onsewa tidawapatsa ubwino pa zolengedwa zonse

Verse 87 — Surah Al-Anam 6:87

“(Ndiponso tidawatsogolera) ena mwa atate awo, ana awo ndi abale awo. Ndipo tidawasankha ndi kuwaongolera ku njira yolunjika

Verse 88 — Surah Al-Anam 6:88

“Ichi ndi chiongoko cha Allah. Ndi icho akuongolera yemwe wamfuna mwa akapolo Ake. Akadakhala kuti (aneneriwo) adamphatikiza (Allah ndi zina) zikadawaonongekera zimene ankachita

Verse 89 — Surah Al-Anam 6:89

“Iwo ndi omwe tidawapatsa mabuku, chiweruzo, ndi uneneri. Choncho ngati awa (osakhulupirira) azikane izi, basi, tazipereka kale kwa anthu omwe sangazikane

Verse 90 — Surah Al-Anam 6:90

“Iwo ndi omwe Allah adawaongola choncho, tsatira chiongoko chawo. Nena: “Sindikukupemphani malipiro pa izi (zomwe ndikukuphunzitsanizi, koma ndikungotumikira Allah). Ichi sichina koma ndi ulaliki kwa zolengedwa (majini ndi anthu).”

Verse 91 — Surah Al-Anam 6:91

“Koma (Ayuda) sadamulemekeze Allah monga momwe zikufunikira pomulemekeza pomwe adati: “Allah Sadavumbulutsepo chilichonse kwa munthu aliyense.” (Adanena izi pamene mtumiki adawauza kuti Qur’an ndi buku lomwe Allah wavumbulutsa). Nena: “Kodi ndani adavumbulutsa buku lomwe lidadza ndi Mûsa? Lomwe lidali kuunika ndi chiwongoko kwa anthu, lomwe mwalipanga kukhala magawo-magawo; zimene mwafuna kuonetsa kwa anthu mukuzionetsa. Koma zambiri mukubisa (zomwe sizigwirizana ndi zofuna zanu). Ndipo mwaphunzitsidwa (ndi iyi Qur’an) zomwe simudali kuzidziwa, inu ngakhale makolo anu. Nena: “Allah (ndi Yemwe wavumbulutsa iyi Qur’an ndi mabuku ena.”) Kenako asiye azingosewera m’kubwebweta kwawo (kopanda pake)

Verse 92 — Surah Al-Anam 6:92

“Ndipo ili ndibuku limene talivumbulutsa lamadalitso ochuluka; lotsimikizira zomwe zidalitsogolera. Ndikuti uchenjeze manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mphepete mwake. Ndipo amene akukhulupirira tsiku lachimaliziro, akulikhulupirira (bukuli). Ndipo iwo Swala zawo akuzisunga bwino

Verse 93 — Surah Al-Anam 6:93

“Kodi ndani woipitsitsa koposa yemwe wampekera bodza Allah kapena wonena: “Kwavumbulutsidwa kwa ine,” pomwe sikunavumbulutsidwe kwa iye chilichonse; ndi yemwe akunena: ‘“Ndivumbulutsa monga chimene Allah wavumbulutsa.” Ukadawaona anthu ochita zoipa akuthatha ndi imfa, nawo angelo atatambasula manja awo (powamenya uku akuwauza): “Tulutsani moyo wanu; lero mulipidwa chilango chonyozetsa chifukwa cha zomwe mudali kunenera Allah popanda choonadi, ndi kudzitukumula kwanu pa zizindikiro zake.” (Ukadaona zoopsa kwabasi)

Verse 94 — Surah Al-Anam 6:94

“Ndipo (tsiku la Qiyâma tidzakuuzani): “Ndithudi, mwatidzera mmodzimmodzi (payekhapayekha popanda chuma ndi ana kuti zikupulumutseni), monga mmene tidakulengerani pachiyambi. Ndipo mwasiya kumbuyo kwanu zonse zomwe tidakupatsani. Ndipo sitikuona pamodzi nanu apulumutsi anu aja, amene munkati ngothandizana (ndi Allah; ndi kuti iwo ndi apulumutsi anu). Ndithudi mgwirizano omwe udali pakati panu waduka. Ndipo zakusokonekerani zimene munkaziganizira (kuti ndi milungu).”

Verse 95 — Surah Al-Anam 6:95

“Ndithu Allah ndi Yemwe amang’amba njere ndi mbewu ya zipatso (kuti zimere). Amatulutsa chamoyo m’chakufa. Ndiponso Ngotulutsa chakufa m’chamoyo. Ameneyu ndi Allah, nanga mukutembenuzidwa chotani

Verse 96 — Surah Al-Anam 6:96

“Iye ndi Yemwe ali Wotsekula m’bandakucha, ndipo amaupanga usiku kukhala wabata (nthawi yopumula) ndi dzuwa ndi mwezi kukhala zowerengera masiku ndi zaka (kalendala). Ichi nchikonzero cha Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri

Verse 97 — Surah Al-Anam 6:97

“Iye ndi amene anakupangirani nyenyezi kuti mulondole njira kudzera mwa izo mu m’dima wa pamtunda ndi panyanja. Ndithu talongosola mokwanira zizindikiro (zathu) kwa anthu odziwa

Verse 98 — Surah Al-Anam 6:98

“Ndipo Iye ndi yemwe adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi. (Kwa inu) alipo malo okhalapo (dziko lapansi kapena m’mimba mwa mayi) ndiponso posungirapo (mmanda kapena munsana mwa bambo). Ndithu tafotokoza zizindikiro (Zathu) kwa anthu ozindikira

Verse 99 — Surah Al-Anam 6:99

“Iye ndi Yemwe amavumbwitsa mvula kuchokera kumwamba. Ndi madzi a mvulayo timameretsa mmera wa chinthu chilichonse. Ndipo m’menemo tikuphukitsa masamba obiriwira, tikutulutsa mmenemo njere zosanjikana; ndiponso m’kanjedza m’mikoko mwake mumatuluka maphava ogoweka (ndizipatso). Ndipo amakumeretserani minda ya mphesa, mzitona ndi makomamanga, ofanana ndi osafanana. Tapenyani zipatso zake pamene zikupatsa ndi kupsa kwake. Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

Verse 100 — Surah Al-Anam 6:100

“Ndipo (pamwamba pa izi) anthu ampangira Allah ziwanda kukhala athandizi (Ake), pomwe Iye ndi Yemwe adazilenga. Ndipo akumnamizira kuti ali ndi ana aamuna ndi aakazi popanda kudziwa. Ali kutali Wolemekezekayo, ndipo watukuka kuzimene akusimbazo

Verse 101 — Surah Al-Anam 6:101

“Iye ndiye Mlengi wathambo ndi nthaka, zingatheke bwanji kukhala ndi mwana pomwe Iye alibe mkazi? Ndipo ndi Yemwe adalenga chinthu chilichonse. Ndiponso Iye Ngodziwa zedi chinthu chilichonse

Verse 102 — Surah Al-Anam 6:102

“Ameneyu ndi Allah, Mbuye wanu; palibe wina woti nkumpembedza mwa choonadi koma Iye. Mlengi wa chinthu chilichonse. Choncho, mpembedzeni. Iye ndi Muyang’aniri wa chinthu chilichonse

Verse 103 — Surah Al-Anam 6:103

“Maso samufika (kuti nkumuona); koma Iye amawafika maso (amawaona pamodzi ndi eni masowo). Iye Ngodziwa zobisika kwambiri, Ngodziwa zoonekera

Verse 104 — Surah Al-Anam 6:104

“(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu umboni otsimikizika wakufikani kuchokera kwa Mbuye wanu, choncho amene atsekule maso ake nkuyang’ana ndiye kuti (zotsatira zake zabwino) zili pa iye mwini. Ndipo amene atseke maso ake zili pa iye mwini (zotsatira zake zoipa). Ndipo ine sindili muyang’anili wanu.”

Verse 105 — Surah Al-Anam 6:105

“Motero tikulongosola mwatsatanetsatane zizindikiro, (kuti azindikire). Ndikuti anene: “Wachita kuphunzira (izi, si Allah amene wakuuza.” Ndipo tazibwerezabwereza chonchi) kuti tilongosole ndi kufotokoza momveka kwa anthu odziwa

Verse 106 — Surah Al-Anam 6:106

“Tsata zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako. Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ndipo apewe opembedza mafano

Verse 107 — Surah Al-Anam 6:107

“Ndipo Allah akadafuna sakadamphatikiza (ndi mafano), ndipo sitidakuike pa iwo kukhala muyang’aniri wawo. Ndipo iwe suli muyimiliri wawo

Verse 108 — Surah Al-Anam 6:108

“Ndipo usawatukwane amene akupembedza (mafano) kusiya Allah, kuopera kuti angamtukwane Allah mwamwano popanda kuzindikira. Motero taukometsera m’badwo ulionse ntchito zake. Potsiriza adzabwerera kwa Mbuye wawo, choncho, Iye adzawauza zonse zomwe adali kuchita

Verse 109 — Surah Al-Anam 6:109

“Ndipo (akafiri) adalumbira Allah ndi malumbiro awo amphamvu kuti ngati chitawadzera chozizwitsa ndithu adzachikhulupirira. Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah (sizili mmanja mwanga). Kodi nchinthu chanji chingakudziwitseni (inu Asilamu) kuti (ngakhale) chitaza (chozizwitsacho) iwo sangakhulupirire?”

Verse 110 — Surah Al-Anam 6:110

“Ndipo titembenuza mitima yawo ndi maso awo (kotero kuti sangathe kuchikhulupirira ngakhale atachiona chozizwitsacho) monga momwe sadaikhulupirire (Qur’an) poyamba ndipo tiwasiya akuyumbayumba m’machimo awo

Verse 111 — Surah Al-Anam 6:111

“۞ Ndipo ngati tikadawatumizira angelo (kuti adzaikire umboni za uneneri wako), ndipo akufa nkuwayankhula, (naonso nkuvomereza kuti izi nzoona; kuonjezera apo) nkuwasonkhanitsira chinthu chilichonse pamaso pawo, sakadakhulupirira pokhapokha Allah akadafuna koma ambiri a iwo sazindikira

Verse 112 — Surah Al-Anam 6:112

“Ndipo nchomwechi tidamuikira adani mneneri aliyense (omwe) ndi asatana a mu anthu ndi asatana a m’ziwanda, (omwe) amadziwitsana wina ndi mnzake mawu okometsa ncholinga chonyenga. Ndipo Mbuye wako akadafuna, sakadatha kuchita zimenezi choncho asiye ndi zimene akupeka

Verse 113 — Surah Al-Anam 6:113

“Ndi kuti ipendekere ku mawu amenewo mitima ya anthu osakhulupirira tsiku la chimaliziro, ndi kuyanjana nawo (mawuo) ndikutinso apeze (machimo) omwe amawapeza

Verse 114 — Surah Al-Anam 6:114

“(Nena:) “Kodi ndifune woweruza wina kusiya Allah, pomwe Iye ndi Yemwe adavumbulutsa buku kwa inu lofotokoza chilichonse?” Ndipo omwe tidawapatsa buku akudziwa kuti (Qur’an) yavumbulutsidwa ndi Mbuye wako mwachoonadi. Choncho, usakhale mwa okaikira

Verse 115 — Surah Al-Anam 6:115

“Ndipo mawu a Mbuye wako akwanira moona ndi mwachilungamo. Palibe amene angathe kusintha mawu Ake. Iye Ngwakumva, Ngodziwa

Verse 116 — Surah Al-Anam 6:116

“Ngati umvera ambiri amene ali pa dziko lapansi, akusokeretsa pa njira ya Allah. Satsatira koma zakungoganizira. Ndipo sali chilichonse koma akungonama

Verse 117 — Surah Al-Anam 6:117

“Ndithu Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa bwino amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye akudziwa bwino za oongoka

Verse 118 — Surah Al-Anam 6:118

“Choncho, idyani (nyama) zomwe dzina la Allah latchulidwapo (pozizinga osati zofa zokha), ngati inu mukhulupiriradi Ayah (zizindikiro) Zake

Verse 119 — Surah Al-Anam 6:119

“Mungasiirenji kudya (nyama) imene poizinga dzina la Allah latchulidwapo, pomwe wakufotokozerani momveka chomwe wachiletsa kwa inu, kupatula (mukadya choletsedwacho) mosimidwa ndi kukakamizidwa (chifukwa cha njala)? Koma ndithu ambiri akusokeretsa (ena) mwa zifuniro zawo popanda kudziwa. Ndithu Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa bwino za olumpha malire

Verse 120 — Surah Al-Anam 6:120

“Siyani machimo oonekera ndi obisika. Ndithu amene achita machimo adzalipidwa chifukwa cha zomwe adali kuchita (zoipa)

Verse 121 — Surah Al-Anam 6:121

“Ndipo musadye (nyama) imene yazingidwa popanda kutchula dzina la Allah. Kutero ndikuchimwa. Ndithudi, asatana amanong’onezera abwenzi awo kuti akangane ndi inu (m’zinthu zonga zimenezi). Ngati muwamvera, ndiye kuti mukhala opembedza mafano

Verse 122 — Surah Al-Anam 6:122

“Kodi yemwe adali wakufa, kenako nkumuukitsa ndi kumpangira kuunika; choncho ndi kuunikako nkumayenda kwa anthu, kodi angafanane ndi yemwe chikhalidwe chake chili mu mdima (wa umbuli) ndipo sakutha kutuluka m’menemo? Motero zakometsedwa kwa osakhulupirira (zoipa) zomwe akhala akuchita

Verse 123 — Surah Al-Anam 6:123

“Chomwechonso tidaika mmudzi uli wonse akuluakulu owonongamo kuti azichitamo ndale (zoletsa anthu kuyenda pa njira ya Allah). Ndipo ndale zawo sizipweteka aliyense koma iwo eni, koma sazindikira

Verse 124 — Surah Al-Anam 6:124

“Ndipo chizindikiro chikawadzera, amati: “Sitikhulupirira, mpaka tipatsidwe monga zomwe atumiki a Allah adapatsidwa.” Allah ndiamene akudziwa pamalo pomwe akuika uneneri Wake, (sikuti angapatsidwe munthu aliyense). Posachedwa kunyozeka kochokera kwa Allah ndi chilango choopsa ziwafika amene achita zoipa chifukwa cha ndale zawo zomwe akhala akuchita

Verse 125 — Surah Al-Anam 6:125

“Choncho, amene Allah akufuna kumuongola, amamtsekula chifuwa chake kuti Chisilamu chilowemo, ndipo yemwe Allah akufuna kumulekelera kusokera amachichita chifuwa chake kukhala chobanika, chovutika kwambiri (kutsata Chisilamu) ngati kuti akukwera kumwamba. Umo ndi momwe Allah akuwaunjikira uve anthu omwe sakukhulupirira

Verse 126 — Surah Al-Anam 6:126

“Ndipo iyi (chipembedzo cha Chisilamu) ndi njira ya Allah yoongoka. Ndithu tazifotokoza zizindikiro momveka kwa anthu okumbukira

Verse 127 — Surah Al-Anam 6:127

“(Anthu abwino) adzapeza Nyumba yamtendere kwa Mbuye wawo. Iye ndi Mtetezi wawo, chifukwa cha zomwe adali kuchita

Verse 128 — Surah Al-Anam 6:128

“Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawasonkhanitsa onse (nkuwauza): “E inu khamu la ziwanda! Ndithudi, mudatenga okutsatirani ambiri mwa anthu (powasokoneza).” Ndipo abwenzi awo mwa anthu adzati: “Mbuye wathu! Tidali kupindulitsana pakati pathu, ndipo tsopano taifikira nyengo yathu imene mudatiikira.” (Allah) adzati: “Malo anu ndi ku Moto. Mukakhala m’mmenemo nthawi yaitali, pokhapokha Allah akafuna.” Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri

Verse 129 — Surah Al-Anam 6:129

“Chomwechi timaika chimvano pakati pawochita zoipa chifukwa cha machimo omwe adali kupeza (kuchokera m’zochita zawo zoipa)

Verse 130 — Surah Al-Anam 6:130

“(Tsiku la Qiyâma adzafunsidwa): “E inu magulu a ziwanda ndi anthu! Kodi sadakudzereni atumiki ochokera mwa inu, amene amakufotokozerani zizindikiro zanga, nakuchenjezani zokumana ndi tsiku lanu ili?” Adzati: “Tadziikira umboni tokha.” Ndipo moyo wa dziko lapansi udawanyenga. Ndipo adzaziikira okha umboni kuti iwo adali osakhulupirira

Verse 131 — Surah Al-Anam 6:131

“Zimenezi nchifukwa choti Mbuye wako sali woononga midzi mwachinyengo pomwe eni ake ali oiwala. (Koma ankawatumizira aneneri kuti awachenjeze ndi kuwakumbutsa)

Verse 132 — Surah Al-Anam 6:132

“Ndipo onse adzakhala ndi nyota (za ulemelero) kuchokera m’zochita zawo. Ndipo Mbuye wako sali wamphwayi pa zimene akuchita

Verse 133 — Surah Al-Anam 6:133

“Ndipo Mbuye wako Ngokwanira (Wolemera), Mwini chifundo. Ngati afuna angakuchotseni ndi kuwaika m’malo mwanu amene wawafuna monga momwe adakulengerani kuchokera m’mbumba ya anthu ena

Verse 134 — Surah Al-Anam 6:134

“Ndithu (palibe chikaiko) zomwe mukulonjezedwa zifika. Ndipo simungathe kuzilepheretsa

Verse 135 — Surah Al-Anam 6:135

“Nena: “E inu anthu anga! Chitani zanu (zimene mufuna) momwe mungathere. Nanenso ndichita zanga. Choncho mudzaziwa kuti ndani mapeto ake adzakhale ndi malo abwino. Ndithudi, sangapambane anthu ochita zoipa.”

Verse 136 — Surah Al-Anam 6:136

“Ampangira Allah (amugawira) gawo m’zomera ndi ziweto zimene (Allah) adalenga. Akunena: “Gawo ili ndi la Allah.” Mkuyankhula kwawo kwachabe: “Ndipo gawo ili ndi la aja omwe tikuwaphatikiza ndi Allah.” Choncho zomwe alinga kuwapatsa aphatikizi awo, sizingafike kwa Allah. Ndipo zimene zili za Allah, ndizomwe zingafike kwa aphatikizi awo (mafano awo). Kwaipitsitsa kuweruza kwaoku

Verse 137 — Surah Al-Anam 6:137

“Momwemo milungu yawo imawakometsera ambiri mwa ophatikiza Allah ndi mafano kupha ana awo (monga nsembe ya mafanowo) kuti awaononge ndikuwabweretsera chisokonezo pa chipembedzo chawo. Ndipo ngati Allah akadafuna, sakadachita zimenezo. Choncho asiye ndi izo zomwe akupeka

Verse 138 — Surah Al-Anam 6:138

“Iwo akuti: “Ziweto izi ndi mbewu izi, nzoletsedwa; palibe angazidye koma amene tawafuna (kuti adye),” zonsezi mkuyankhula kwawo kwachabe. Ndipo (amanenanso): “Ziweto izi, misana yake njoletsedwa (kukwerapo).” Ndipo pa ziweto zina satchula dzina la Allah pozizinga; kungompekera bodza Iye. Ndipo posachedwa adzawalipira pa zomwe adali kupeka

Verse 139 — Surah Al-Anam 6:139

“Ndipo amanenanso: “Zimene zili m’mimba mwa ziweto izi, ndi za amuna okha; ndipo nzoletsedwa kwa akazi athu.” Koma ngati chili chibudu, onse adali kugawana (amuna ndi akazi). Ndithudi, adzawalipira ndi zonena zawozo. Ndithu Iye (Allah), Ngwanzeru zakuya, Wodziwa kwambiri

Verse 140 — Surah Al-Anam 6:140

“Ndithu adaluza amene adapha ana awo mwa umbuli popanda kudziwa, ndi kuletsa (chakudya) chimene Allah awapatsa, pakungompekera bodza Allah. Ndithu adasokera ndipo sadali oongoka

Verse 141 — Surah Al-Anam 6:141

“Ndipo Iye (Allah) ndi amene adapanga minda (ya mitengo) yothaza ndi yosathaza; ndipo (adapanga) mitengo yakanjedza ndi mmera wazipatso zosiyanasiyana makomedwe ake ndipo adapanganso mzitona ndi makomamanga, zofanana (mmaonekedwe) ndi zosiyana (mmakomemedwe). Idyani zipatso zake pamene zikupatsa. Ndipo perekani chopereka chake tsiku lokolola (powapatsa masikini ndi ogundizana nawo nyumba). Ndipo musaziononge pakudya mopyoza muyeso. Ndithu Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso

Verse 142 — Surah Al-Anam 6:142

“Ndipo m’gulu la nyama, (Allah adalenga) zonyamulira katundu ndi zopangira choyala (bweya bwake). Idyani zimene Allah wakupatsani ndipo musatsate mapazi a satana (ndi abwenzi ake pozichita halali kapena haramu zomwe Allah sadalamule. Satana sakufunirani zabwino); ndithu iye ndi mdani wanu woonekera

Verse 143 — Surah Al-Anam 6:143

“(Adakulengerani) mitundu isanu ndi itatu ya nyama (pophatikiza zazimuna ndi zazikazi); nkhosa (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi); mbuzi (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi Iye adakuletsani zazimuna zonse ziwiri, (mbuzi ndi nkhosa) kapena zazikazi ziwiri, (nkhosa ndi mbuzi), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Ndiuzeni mwa nzeru ngati mukunenazi nzoona (kuti Allah adatero)

Verse 144 — Surah Al-Anam 6:144

“Ndipo (adalenganso) ngamira ziwiri, (yaikazi ndi yaimuna). Ng’ombe (adalenganso) ziwiri, (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi (Iye) adakuletsani zazimuna zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zazikazi zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Kodi mudali mboni pamene Allah ankakulamulani izi? Kodi ndi ndani woipitsitsa kuposa amene akupekera bodza Allah kuti asokeretse anthu popanda kudziwa (malamulo a Allah)? Ndithu Allah saongola anthu ochita zoipa

Verse 145 — Surah Al-Anam 6:145

“Nena: “Sindikupeza m’zimene zavumbulutsidwa kwa ine choletsedwa (kudya) kwa yemwe akufuna kudya. Pokhapokha chikakhala chakufa chokha, kapena liwende lomwe limachucha, kapena nyama ya nkhumba; chifukwa chakuti zonsezi ndi uve (ndiponso kudya zotere) ndiko kutuluka m’chilamulo cha Allah. Kapena (nyama) yozingidwa popanda kutchulapo dzina la Allah. Koma amene wasimidwa (nkudya zoterezi) popanda kukonda kapena kupyoza Malire, ndithu Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha. (Wotere amamkhululukira)”

Verse 146 — Surah Al-Anam 6:146

“(Izi ndi zomwe takuletsani). Naonso Ayuda tidawaletsa kudya nyama iliyonse yokhala ndi zikhadabu, ndipo ng’ombe ndi mbuzi tidawaletsa kudya mafuta ake kupatula mafuta omwe misana yake yasenza, kapena okhala m’matumbo, kapena omwe asakanikirana ndi mafupa. Tidawalipira izi chifukwa cha machimo awo. Ndithu Ife ndioona (pa zomwe tikunenazi)

Verse 147 — Surah Al-Anam 6:147

“Ngati akukutsutsa (pa zimene zavumbulutsidwa), auze (mowachenjeza): “Mbuye wanu (Yemwe ngofunika kum’khulupirira ndi kutsatira malamulo ake) Ngwachifundo chambiri (kwa yemwe akumumvera, ndi yemwe akumunyoza pano pa dziko lapansi). Komatu chilango chake sichibwezedwa kwa anthu oipa.”

Verse 148 — Surah Al-Anam 6:148

“Amene akuphatikiza (Allah ndi mafano) anena: “Ngati Allah akadafuna, sitikadam’phatikiza, ife ngakhale makolo athu. Ndipo sitikadaletsa chilichonse. (Choncho, izi zomwe tikuchita, Allah akuziyanja). Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo kufikira adalawa chilango chathu. Nena: “Kodi muli nako kudziwa (kokutsimikizirani zimenezi), koti mungatitulutsire (umboni wake wotsimikizira kuti Allah adakulamulani zimenezi)? Inu simutsatira china, koma zongoganizira basi. Ndipo Simukunena china koma zabodza basi.”

Verse 149 — Surah Al-Anam 6:149

“Nena: “Allah ndi Yemwe ali ndi umboni wokwanira. Choncho akadafuna, akadakuongolani nonsenu.”

Verse 150 — Surah Al-Anam 6:150

“Nena: “Tabweretsani mboni zanuzo zomwe zingapereke umboni kuti Allah adaletsa izi.” Choncho ngati zitapereka umboni, (mboni zawozo) usaikire nawo umboni pamodzi ndi iwo. Ndipo usatsate zofuna za omwe atsutsa zizindikiro zathu ndi amene sakhulupirira tsiku lachimaliziro; omwenso akufanizira Mbuye wawo ndi milungu yabodza

Verse 151 — Surah Al-Anam 6:151

“Nena: “Idzani kuno, ndikuwerengereni zomwe Mbuye wanu wakuletsani. Musamphatikize ndi chilichonse, ndipo achitireni zabwino makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chakuopa umphawi; ife tikupatsani rizq inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zoyipa, zoonekera ndi zobisika; ndipo musaphe munthu yemwe Allah adaletsa (kumupha) kupatula ikapezeka njira yoyenereza (kumupha). Akukulangizani izi kuti muziike mu nzeru zanu.”

Verse 152 — Surah Al-Anam 6:152

““Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye, koma m’njira yabwino (monga kuchichulukitsa ndi malonda) mpaka afike pansinkhu wokwanira. Ndipo kwaniritsani mwachilungamo miyeso ya mbale ndi masikelo; sitikakamiza munthu koma chimene angathe; ndipo pamene mukunena, (popereka umboni), nenani mwachilungamo ngakhale (umboniwo) uli wokhudza achibale. Ndipo kwaniritsani lonjezo la Allah. Izi ndi zomwe akukulangizani kuti mukumbukire.”

Verse 153 — Surah Al-Anam 6:153

“(Auze kuti): “Ndithu iyi ndi njira yanga yoongoka. Choncho itsateni. Ndipo musatsate njira zina zambiri kuopera kuti zingakulekanitseni ndi njira Yake, (Allah) wakulangizani izi kuti mudziteteze kuzoipa.”

Verse 154 — Surah Al-Anam 6:154

“Ndipo Mûsa tidampatsa buku (kukhala) lokwaniritsa (chisomo) kwa yemwe wachita zabwino, lofotokoza chinthu chilichonse, chiongoko ndi chifundo, kuti iwo akhulupirire za kukumana ndi Mbuye wawo

Verse 155 — Surah Al-Anam 6:155

“Ndipo iyi (Qur’an) ndi buku lodalitsika lomwe talivumbulutsa (kwa inu), choncho, litsateni ndi kuopa (Allah) kuti muchitiridwe chifundo

Verse 156 — Surah Al-Anam 6:156

“Kuti musadzanene (tsiku la Qiyâma) kuti: “Mabuku adavumbulutsidwa pa magulu awiri omwe adalipo patsogolo pathu, (Ayuda ndi Akhrisitu); ndipo ife sitidadziwe chilichonse pa zomwe adali kuwerenga ndi kuphunzira.”

Verse 157 — Surah Al-Anam 6:157

“Kapena kuti musadzati: “Likadavumbulutsidwa buku kwa ife, ndithudi, tikadakhala oongoka kuposa iwo.” Choncho, chakudzerani chizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu, ndi chiongoko ndi mtendere. Kodi ndani woipitsitsa kwambiri kuposa amene watsutsa zizindikiro za Allah ndi kutembenukira kutali Nazo? Tidzawalipira amene akutembenukira kutali ndi zizindikiro zathu, chilango choipa, chifukwa cha kudziika kwawo kutali

Verse 158 — Surah Al-Anam 6:158

“Kodi chilipo chimene akudikira kuposa kuwadzera angelo (kudzawachotsa miyoyo yawo?) Kapena kudza Mbuye wako (tsiku la Qiyâma kuzaweruza)? Kapena kudza zina mwa zizindikiro za Mbuye wako (zomwe adati zidzadza)? Tsiku lakudza zina mwa zizindikiro za Mbuye wako, munthu (wosakhulupirira) chikhulupiliro chake (panthawiyo) sichidzamthandiza, yemwe sadakhulupirirepo kale, kapena (msilamu) yemwe sanapindule nacho chikhulupiliro chake. Nena: “Dikirani. Nafenso tikudikira.”

Verse 159 — Surah Al-Anam 6:159

“Ndithudi, anthu amene achigawa Chipembedzo chawo, nakhala Mipingomipingo, iwe Siuli nawo pachilichonse. Ndithu zotsatira zawo zili kwa Allah, (ndi yemwe adzawalanga. Ndipo panthawi yowalanga) adzawauza zomwe adali kuchita

Verse 160 — Surah Al-Anam 6:160

“Amene wachita chabwino alipidwa zabwino khumi zofanana ndi icho. Ndipo amene wachita choipa sadzalipidwa koma chonga icho (popanda kuonjezera). Ndipo iwo sadzaponderezedwa

Verse 161 — Surah Al-Anam 6:161

“Nena: “Ndithudi, ine Mbuye wanga wandiongolera ku njira yoongoka, kuchipembedzo cholingana, chomwe ndi chipembedzo cha Ibrahim, yemwe adali wolungama. Sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano)

Verse 162 — Surah Al-Anam 6:162

“Nena: “Ndithudi, Swala yanga, mapemphero anga onse, moyo wanga, ndi imfa yanga, (zonse) nza Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse.”

Verse 163 — Surah Al-Anam 6:163

““Alibe wothandizana naye. Izi ndi zomwe ndalamulidwa, ndipo ine ndine woyamba mwa Asilamu (ogonjera Allah).”

Verse 164 — Surah Al-Anam 6:164

“Nena: “Kodi ndifune mbuye wina kusiya Allah, pomwe Iye ndi Mbuye wa chinthu chilichonse? Ndipo mzimu uliwonse siuchita choipa koma ukudzichitira wokha. Mzimu wosenza machimo siudzasenza machimo a mzimu wina. Kenako kobwerera kwanu (nonse) ndi kwa Mbuye wanu, (Allah), ndipo adzakuuzani zomwe mudali kusiyana.”

Verse 165 — Surah Al-Anam 6:165

“Ndipo Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala am’lowam’malo pa dziko (kulowa m’malo mwa anzanu omwe adaonongeka). Ndipo wawatukula pa ulemelero (ndi pa chuma) ena a inu pamwamba pa ena kuti akuyeseni pa zomwe wakupatsani. (Amene apatsidwa chuma ndi ulemelero athandize amene sadapatsidwe. Ndipo amene sadapatsidwe apirire asalande chinthu chamwini). Ndithudi, Mbuye wako Ngwachangu pokhaulitsa. Ndiponso Iye Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha