“Ndithu inu muli ndi chitsanzo chabwino cha (mtumiki) Ibrahim ndi amene adali naye pamene adawauza anzawo (osakhulupirira kuti): “Ndithu ife tapatukana nanu pamodzi ndi milungu yanu imene mukuipembedza kusiya Allah; takukanani, ndipo chidani ndi kusakondana zaonekera poyera pakati pa inu ndi ife mpaka muyaya, kufikira, mutakhulupirira mwa Allah mmodzi (inunso chitani chimodzimodzi, muwakane abale anu amene ali akafiri), kupatula mawu a Ibrahim pamene adamuuza tate wake (kuti): “Ndithu ndikupempherani chikhululuko. Palibe chimene ndingakutetezereni nacho kwa Allah (ngati mutamuphatikiza Allah ndi zina.”) E Mbuye wathu! Kwa Inu tatsamira. Ndipo kwa Inu tatembenukira ndiponso kobwerera nkwa Inu
“Ndithu muli nacho inu kwa iwo (Ibrahim ndi omtsatira) chitsanzo chabwino kwa amene akuyembekezera kukumana ndi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene anyozere ndithu Allah Ngolemera (ndiponso) Ngotamandika
“Mwina Allah angaike chikondi pakati panu ndi ena mwa amene mumawada (poiongolera mitima yawo kukhulupirira mwa Allah), ndipo Allah Ngokhoza chilichonse ndiponso Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni chosatha
“Allah sakukuletsani kuwachitira zabwino ndi chilungamo amene sadakumenyeni ndi kukutulutsani m’nyumba zanu chifukwa cha chipembedzo. Ndithu Allah amakonda achilungamo
“E iwe Mtumiki! Akakudzera akazi okhulupirira kudzakulonjeza kuti samphatikiza Allah ndi chilichonse ndi kuti saziba, sazichita chiwerewere, sazipha ana awo ndi kuti sazinena bodza lamkunkhuniza, lomwe akulipeka pakati pa manja awo ndi miyendo yawo (pompachika mwana kwa wina amene sali tate wake), ndi kutinso sadzakunyoza pa chinthu chabwino (chimene ukuwaitanira), landira lonjezo lawolo, ndipo apemphere chikhululuko kwa Allah. Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni