Back to Languages

Chichewa - Chapter 61 - As-Saf

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah As-Saf 61:1

“Zonse zakumwamba ndi zapansi zimalemekeza Allah (ndi kumuyeretsa kumakhalidwe osayenera ndi ulemelero Wake). Ndipo Iye Yekha Ngopambana pa chilichonse; Wanzeru zakuya

Verse 2 — Surah As-Saf 61:2

“E inu amene mwakhulupirira! Bwanji mukunena zimene simuchita

Verse 3 — Surah As-Saf 61:3

“Nzomuipira zedi Allah kunena zinthu zimene simuchita

Verse 4 — Surah As-Saf 61:4

“Ndithu Allah amakonda amene akumenya nkhondo pa njira Yake (yofalitsa chipembedzo Chake), ali pa mzere (umodzi) uku ali monga chomanga, chomangika mwamphamvu

Verse 5 — Surah As-Saf 61:5

“Ndipo kumbuka (iwe Mneneri{s.a.w}) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti: “Ndichifukwa ninji mukundivutitsa ine pomwe mukudziwa kuti ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu?” Ndipo pamene adapitiriza kupandukira choonadi, Allah adaipinda mitima yawo (kuti isalandire chiongoko); ndipo Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo Chake

Verse 6 — Surah As-Saf 61:6

“Ndiponso (kumbuka) pamene adanena (Mtumiki) Isa (Yesu) mwana wa Mariya, kuti: “E inu ana a Israelil! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu, amene ndikuchitira umboni zimene zidadza patsogolo panga za buku la Chipangano chakale (Torah) ndipo ndikuuzani nkhani yabwino ya mthenga amene adzadze pambuyo panga, dzina lake Ahamad (Muhammad{s.a.w}).” Koma pamene adawadzera (Mtumiki wolonjedzedwayo) ndi zisonyezo zowonekera poyera (kuti iye ndi Mtumiki wa Allah). Adati: “Awa ndi matsenga owonekera.”

Verse 7 — Surah As-Saf 61:7

“Kodi ndani oipitsitsa kuposa yemwe wapekera Allah bodza, pomwe iye akuitanidwira ku Chisilamu (chipembedzo choona ndi chabwino)? Ndipo Allah saongola anthu achinyengo

Verse 8 — Surah As-Saf 61:8

“Akufuna kuti azimitse dangalira la Allah ndi pakamwa pawo ndipo Allah Ngokwaniritsa dangalira Lake ngakhale ziwaipire osakhulupirira

Verse 9 — Surah As-Saf 61:9

“Iye ndi amene adatuma Mtumiki Wake (Muhammad{s.a.w}) ndi chiongoko ndi chipembedzo choona, kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse, ngakhale kuti ophatikiza Allah ndi mafano zikuwaipira

Verse 10 — Surah As-Saf 61:10

“E inu amene mwakhulupirira! Kodi ndikudziwitseni malonda amene angakupulumutseni ku chilango chowawa

Verse 11 — Surah As-Saf 61:11

“Muzimkhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake; ndipo muzichita Jihâd pa njira ya Allah ndi chuma chanu, ndi matupi anu. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati muli odziwa

Verse 12 — Surah As-Saf 61:12

“Akukhululukirani machimo anu ndipo akulowetsani m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake, ndiponso (adzakupatsani) mokhala mwabwino ku minda yamuyaya. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

Verse 13 — Surah As-Saf 61:13

“Ndizina zomwe mukuzifuna. Thandizo (lonse) lichokera kwa Allah ndi kugonjetsa kumene kuli pafupi; ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira

Verse 14 — Surah As-Saf 61:14

“E inu amene mwakhulupirira! Khalani othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah (pamene Mtumiki akukuitanani kuti mumthangate) monga momwe adanenera Isa (Yesu) mwana wa Mariya powauza otsatira ake: “Ndani adzandithangata pa ntchito ya Allah (yofalitsa chipembedzo Chake)? Otsatira ake adanena: “Ife ndife othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah.” Choncho gulu lina la ana a Israyeli lidakhululupirira, ndipo gulu lina silidakhululupirire, tero tidawapatsa mphamvu amene adakhulupirira pa adani awo, ndipo adali opambana