Back to Languages

Chichewa - Chapter 62 - Al-Jumuah

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Jumuah 62:1

“Zonse zakumwamba ndi dziko lapansi zikulemekeza Allah; Mfumu, Woyera, Wamphamvu zopambana ndi nzeru zakuya (ndi kumyeretsa ku makhalidwe osayenerana ndi ulemelero Wake)

Verse 2 — Surah Al-Jumuah 62:2

“Iye ndiAmene adatumiza kwa Ummiyyina (osadziwa kulemba ndi kuwerenga), Mtumiki wochokera mwa iwo kuti awawerengere ndime Zake ndi kuti awayeretse (ku uchimo ndi kumakhalidwe oipa) ndi kuwaphunzitsa Qur’an ndi mawu anzeru (a mtumiki) ndithu kale adali osokera kowonekera (Mtumiki {s.a.w} asadadze kwa iwo

Verse 3 — Surah Al-Jumuah 62:3

“Ndipo (adamtumizanso) kwa ena mwa iwo, omwe sadakumane nawo, ndipo Iye (Allah) Ngopambana (pa chinthu chilichonse ndi Wamphamvu zoposa ndiponso) Ngwanzeru zakuya

Verse 4 — Surah Al-Jumuah 62:4

“Umenewo ndiwo ubwino wa Allah akuupereka kwa amene wamfuna (mwa akapolo Ake); ndipo Allah yekha ndi Mwini ubwino waukulu

Verse 5 — Surah Al-Jumuah 62:5

“Fanizo la (Ayuda) amene adawasenzetsa Taurat (pokakamizidwa kuti atsatire zophunzitsa za bukulo, koma osatsatira), ali ngati bulu amene akusenza mabuku akuluakulu anzeru, (koma osathandizika nawo). Taonani kuipa fanizo la anthu amene atsutsa zisonyezo za Allah. Ndipo Allah saongola anthu achinyengo

Verse 6 — Surah Al-Jumuah 62:6

“Nena: “E inu Ayuda! Ngati mwadziganizira kuti ndithu ndinu okondedwa a Allah kuposa (mitundu ina ya) anthu, ilakelakeni imfa (kuti mukalowe ku mtendere wa Allah) ngati mukunena zoona

Verse 7 — Surah Al-Jumuah 62:7

“Ndipo sangailakelake mpang’ono pomwe chifukwa cha (zoipa) zimene manja awo atsogoza! Ndipo Allah akudziwa bwino za (anthu) osalungama

Verse 8 — Surah Al-Jumuah 62:8

“Nena (kuti): “Ndithu imfa imene mukuithawa (palibe chipeneko) ikumana nanu; kenako muzabwezedwa kwa wodziwa zobisika ndi zooneka; ndipo adzakuuzani zimene mudali kuchita

Verse 9 — Surah Al-Jumuah 62:9

“E inu amene mwakhulupirira! Kukaitanidwa ku Swala (pemphero la Ijuma) tsiku la Ijuma, pitani mwachangu kukamtamanda Allah. Ndipo siyani malonda; zimenezo (mwalamulidwazo) nzabwino kwa inu ngati mukudziwa

Verse 10 — Surah Al-Jumuah 62:10

“Choncho Swala (ya Ijumayo) ikatha, balalikanani pa dziko, ndipo funani ubwino wa Allah; ndipo mtamandeni Allah kwambiri kuti mupambane (pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro)

Verse 11 — Surah Al-Jumuah 62:11

“Ndipo akaona malonda kapena masewero, akubalalika kunka ku zimenezo ndi kukusiya uli chiimire (ukuchita khutuba ndi anthu ochepa). Nena (kwa iwo): “Zimene zili kwa Allah nzabwino kwa inu kuposa masewero ndi malonda. Ndipo Allah Ngwabwino kwambiri kuposa opatsa onse.”