“Amenewa ndiwo omwe akunena kwa Answari; (Asilamu aku Madina, kuti): “Musawapatse chuma (chanu) amene ali ndi Mtumiki wa Allah kuti abalalikane.” Pomwe nkhokwe zonse (zachuma) za kumwamba ndi dziko lapansi zili m’manja mwa Allah (ndipo amachipereka kwa amene wamfuna); koma achiphamaso sakuzindikira (zimenezo)
“Akunena kuti: “Ngati tibwerera ku Madina wolemekezeka adzatulutsa wonyozeka m’menemo. “Pomwe ulemelero ngwa Allah ndi Mthenga Wake ndi okhulupirira; koma achinyengo sakudziwa (zimenezo).”
“E inu amene mwakhulupirira! Chuma chanu ngakhalenso ana anu zisakutangwanitseni ndi kusiya kukumbukira Allah (ndi kukwaniritsa zimene wakulamulani). Ndipo amene achite zimenezo iwo ndi otaika
“Ndipo Allah sangauchedwetse mzimu (ngakhale ndi mphindi imodzi) ukaidzera nthawi yake ya imfa; ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita, (ndipo adzakulipirani pa zimenezo)