Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 67 - Al-Mulk
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Mulk 67:1
“۞ Watukuka ndi kudalitsika (Allah) Amene m’manja Mwake muli ufumu (wochita chilichonse pazolengedwa zonse); ndipo Iye ali ndi mphamvu yokwanira pachilichonse
Verse 2 — Surah Al-Mulk 67:2
“Amene adalenga imfa ndi moyo kuti akuyeseni (mayeso) ndani mwa inu ali wochita zabwino (kwambiri). Ndipo Iye ndiWopambana m’mphamvu (salephera kanthu) ndiponso Wokhululukira (olakwa)
Verse 3 — Surah Al-Mulk 67:3
“Amene adalenga thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikana (kapena zolingana mkalengedwe kake). Suona kusiyana m’zolenga za Wachifundo chambiri. Bwereza kuyang’ana, kodi ukuona pena pong’ambika
Verse 4 — Surah Al-Mulk 67:4
“Bwerezanso kuyang’ana kachiwiri, kuyang’anako kukubwerera wekha (uku maso) ali olobodoka ndiponso otopa. (Suona polakwika paliponse)
Verse 5 — Surah Al-Mulk 67:5
“Ndipo ndithu talikongoletsa thambo loyandikirali ndi nyali (nyenyezi) ndipo tazichita kukhala (mochokera zenje) zolasila asatana. Ndipo tawakonzera (patsiku lachimaliziro) chilango cha Moto woyaka
Verse 6 — Surah Al-Mulk 67:6
“Ndipo kwa amene sakhulupirira Mbuye wawo ali nacho chilango cha Jahannam; ndipo kuipirenji kobwerera
Verse 7 — Surah Al-Mulk 67:7
“Akadzaponyedwa m’menemo adzamva mavume ake (oipa) uku ukuwira mwaukali
Verse 8 — Surah Al-Mulk 67:8
“Udzayandikira kudukaduka chifukwa cha mkwiyo (kukwiira oipa); nthawi iliyonse gulu (la oipa) likadzaponyedwa m’menemo, Angelo oyang’anira Motowo adzawafunsa (mowadzudzula): “Kodi sadakufikeni mchenjezi (wokuchenjezani za tsikuli?).”
Verse 9 — Surah Al-Mulk 67:9
“Adzayankha “Inde, adatifika mchenjezi koma tidatsutsa, ndipo tidati: ‘Allah sadavumbulutse chilichonse (kwa iwe ngakhale kwa anzako). Koma inu muli m’kusokera kwakukulu.”
Verse 10 — Surah Al-Mulk 67:10
“Ndipo adzanena: “Tikadakhala kuti tidamvera (zimene ankatiuza) kapena kuziganizira mwanzeru sitikadakhala m’gulu la anthu a ku Moto.”
Verse 11 — Surah Al-Mulk 67:11
“Choncho adzavomereza machimo awo (koma sipadzakhala chopindula;) tero kuonongeka ndi kukhala kutali (ndi chifundo cha Allah) kuli pa anthu a ku Moto
Verse 12 — Surah Al-Mulk 67:12
“Ndithudi amene akumuopa Mbuye wawo pomwe iwo sakumuona, adzapeza chikhululuko pa machimo awo ndi malipiro aakulu (pa zabwino zomwe ankachita)
Verse 13 — Surah Al-Mulk 67:13
“Ndipo bisani mawu anu, kapena aonetseni poyera; (zonsezi nchimodzimodzi kwa Allah) ndithudi Iye Ngodziwa zobisika za m’mitima
Verse 14 — Surah Al-Mulk 67:14
“Kodi asadziwe amene adalenga (zinthu zonse)? Pomwe Iye Ngodziwa zinthu zingo’nozing’no kwambiri mmene zilili (ndiponso) Ngodziwa nkhani zonse
Verse 15 — Surah Al-Mulk 67:15
“Iye ndi Amene wakupangirani nthaka kuti ikhale yogonjera (pa chilichonse chimene mufuna). Choncho yendani mbali zake zonse; ndipo idyani rizq lake, (limene Allah akukutulutsirani). Ndipo kwa Iye Yekha ndiko kobwerera kwanu (nonse mutapatsidwa moyo wachiwiri)
Verse 16 — Surah Al-Mulk 67:16
“Kodi muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakukwilireni m’nthaka (ndikukudzidzimutsani) pamene nthaka ikugwedezeka molimba
Verse 17 — Surah Al-Mulk 67:17
“Kapena muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakutumizireni mphepo yamkuntho ya miyala (ndi kukuonongani ndi miyalayo?) Choncho mdzadziwa mmene lilili chenjezo Langa (pa inu)
Verse 18 — Surah Al-Mulk 67:18
“Ndithudi amene adalipo kale iwo asanabadwe adakana mithenga yawo. Nanga udali bwanji mkwiyo Wanga pa iwo (pakuwaononga onse)
Verse 19 — Surah Al-Mulk 67:19
“Kodi, sadaone mbalame pamwamba pawo mmene zikutambasulira (mapiko ake) ndi kuwafumbata. Palibe amene akuzigwira kuti zisagwe koma (Allah) Wachifundo chambiri; ndithudi Iye pachilichonse Ngopenya
Verse 20 — Surah Al-Mulk 67:20
“Kodi ndani amene ali asilikali anu okutetezani kuchilango posakhala (Allah) Wachifimdo chambiri? Ndithudi osakhulupirira ali mkunyengeka (pa zimene akuganizira)
Verse 21 — Surah Al-Mulk 67:21
“Kodi ndani uyo amene angakupatseni rizq (limene mungakhalire ndi moyo ndi kupezera mtendere) ngati Iye atatsekereza rizq Lake (kwa inu)? Koma Akafiri akupitiriza kudzikweza kwawo, ndi kudziika kutali ndi choonadi
Verse 22 — Surah Al-Mulk 67:22
“Kodi amene akuyenda mozyolika ndi nkhope yake angakhale wolungama kapena amene akuyenda moongoka panjira yosakhota
Verse 23 — Surah Al-Mulk 67:23
“Nena: “Iye ndi Amene adakulengani (pomwe simudali kanthu) ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima, (zimene mukhoza kupeza nazo mtendere). Koma kuyamika kwanu (kwa Yemwe adakupatsani zimenezi) nkochepa kwambiri
Verse 24 — Surah Al-Mulk 67:24
“Nena: “Iye ndi amene adakuchulukitsani pa dziko ndipo kwa Iye (Yekha) ndiko mudzasonkhanitsidwa (kuti adzakuwerengereni ndi kukulipirani)
Verse 25 — Surah Al-Mulk 67:25
“Akunena (monyada osakhulupirira za kuuka): “Ndiliti (lidzakwaniritsidwa) lonjezo ili ngati inu muli owona?”
Verse 26 — Surah Al-Mulk 67:26
“Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}): “Ndithu kudziwa (kwa izi) nkwa Allah yekha, ndipo ndithudi ine, ndine mchenjezi wowonekera.”
Verse 27 — Surah Al-Mulk 67:27
“Koma akadzaziona (zimene akulonjezedwazo) zili pafupi (ndi iwo), nkhope za amene sadakhulupirire zidzakhumudwa ndikuyaluka kwambiri, ndipo kudzanenedwa (mowadzudzula): “Izi ndi zija mudali kuzipempha (kuti zidze, zadza tsopano)
Verse 28 — Surah Al-Mulk 67:28
“Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}): “Tandiuzani ngati Allah atandiononga pamodzi ndi amene ndili nawo (monga momwe mukufunira) kapena kutichitira chifundo (ndikutalikitsa nthawi ya moyo wathu). Nanga ndani amene adzawateteza wosakhulupirira ku chilango chowawa?”
Verse 29 — Surah Al-Mulk 67:29
“Nena: “Iye ndiye (Allah) Wachifundo chambiri, takhulupirira mwa Iye ndiponso kwa Iye ndikumene tatsamira. Choncho posachedwapa mudziwa (chilango chikatsika kuti) ndani (m’magulu awiriwa) yemwe ali m’kusokera koonekera.”
Verse 30 — Surah Al-Mulk 67:30
“Nena: “Tandiuzani ngati madzi anuwa ataphwa (kulowelera pansi penipeni); choncho ndani amene angakubweretsereni madzi oyenda (ochokera mkati mwanthaka)